Chiyembekezo Choona Cha mu Zaka Za Zikwi (1000)

Mtima wa zofuna za Mulungu Kwa Anthu ake

17/12/1999

Mu Disemba 1999, Bungwe lina la mpingo lodziwika bwino anatulutsa ndi kugawa kwa anthu opitilira 300,000 opembetsa kanema yochenjeza ndi kudziwitsa okhulupilira Yesu ndi kuwadziwitsa kuti alimbike ndikuyenda ndi Mulungu. Pamene amagawa kanema amenewu amachita ndi cholinga chabwino. Ndipo anaonetsera kwakukulu zinthu zimene zili zoipa. Ndipo zolembedwazo ndinatulutsidwa pamene kanema ameneyu anali kuonetsedwa ndi cholinga chothandiza onse amene amabvala dzina la Yesu kuti apilire ndi kukhudzidwa ndi kuzikonzeretsa ndi kusintha.

Munthu wina ali yense woona mtima amene waloledwa kuyang’ana kuseri kwa nsaru ya chipembedzo chamakono ndi kubwelera mbuyo, akhoza kuyang’ana. Tingaone mabvuto. Koma ndingakozeke kupita malo apamwamba mu zinthu zeni zeni zotere? Kapena tikhathe ife monga mnyamata wa mng’ono wa chi Dachi, kungoika zala zathu mu mpika monga tachitira kwa mbando wathu yonsewu? Tiyeni tipite kwathu popeza yankho! Zili mu mtima wa Yesu ndi njira zake Mesaya. Njira imene anakhala ndi choonadi chimene anaphunzitsa ndi kupeleka ndi aphunzira ake. Zamveka?

Mu tsamba akubwelawa pali mau ena kuchokera kuno ku Amerika ndi atsogoleri a chipembedzo cha makono mau amenewa analengedwa pa video nagawidwa posachedwepa kwa anthu 300,000 achipembedzo muno mu Amerika. Chiyembekezo chinali choti pa 1January 1999 mu Amerika yense. Ngati atamveledwa bwino ndiye idzakhala kutsegula kwa maso kwa anthu ambiri. Ngati wina angapewe zimene zoipa ndipo pomaliza pa kanemawu kuyesetsa kumene kwakhalapo mu mbadwo uno koma osakwanilitsa—mwina ndikutheka kuti miyoyo ina idzatsegulidwa mu dziko lonse ndidzakhala okonzeka tonse pamodzi, popanda kuopa munthu kapena kulodzerabe pa zimene timachitabe ndi kupeza yankho lenileni. Izi zachita ndi kuononga kw anthawi yaitali. Tikudziwa ndikuonetsera kwa zipatso zake.

Chodabwitsa pa zinthu izi ndi mau amene ali mu munsiwa ndi zimene atsogoleri a chipembedzo anabvomekeza za anthu amene amapemphera nawo. Kuchokera kwa Jack Hayford, Tony Evans kwa Crawford Loritts, kwa Henry Blacka by kwa Annie Graham, Lotz, Kwa Kay Arthur. Kwa Bill Mc Cartney munthu wina ndi wina kukwaniritsa koyenera kwa Khristu. Koma kapena kuli kulephera kwenikweni kuonetsera Yesu bwino ndi kusintha miyoyo yathu. Anthu ochuluka ambiri amene amaonerera chipembedzo cha makono ndi kusonkhano kw apa Mulungu. Zokozeratu mamangidwe anjira ubusa ali kugwa ndi kukanuka. Opembedza amaoneka abwino kunja koma njira yamamangidwe ndi yosagwira ntchito. Monga mwa zolankhura atsogoleri amenewa zoona ndi izi kuti sizinatheke ndipo ndi zopanga ntchito chifukwa sinjira ya Mulungu pa mamangidwe palibe njira ya nyama mu malembo monga mu njira ya makono kuti mpingo ukhale wotere ndi zodziwikiratu pa maumboni a atsogoleriwa odziwika bwino kuti makomo andendeali kugonjetsa dziko la chipembetso zodziwikiratu, choncho, ili singakhale mtundu wa mpingo umene Yesu ananena kuti adzamanga—angakhale kuti uli ndi anthu abwino momwemo.

Ndichifukwa cha anthu abwino amenewa ndi ana awo ndi amene tingaganizire mmene tingamangire mipingo pamene tikhalako. Ndi chifukwa chofuna kupulumuts miyoyo—anthu osapulumutsidwa amene amalakwitsa kuti ndi mamembala a mpingo, ndiponso ndi osakhulupilira amene amangokhala—ndi kwa anthu amenewa amene tingawaganizirebe pa chinthu ichi chotchedwa mpingo. Tiyenera kuganizira pa zimene tathandauzira utsogoleri, mmene tathanthauzira mpingo ndi mmene tadziwira ma membala a mpingo ndi akristu. Pali mayankho, Abale ndi alongo ngati tili ndi kulimbika kuti mwachengete amenewa. Sizingakhale mapologalamu ambiri, mautumiki, amalankhulidwe abwino. Magulu a nyumba gulu la mbiri polalikira kapena pemphero kapenenso kupembedza ndi zina zonse zotere. Zambiri zimaoneka zabwino ndi kumveka bwino ndipo mumachitidwe angakhale ndi zothandiza koma zachita zoononga poonetsa chipatso zimene zili pansipa. Zinthu zabwino ndi zochepa 5% chifukwa zimachitika mu mpingo womangidwa ndi anthu.

Fufunzani mbiri yakale ndipo mudzapeza kuti takhala mmwamba ndi pansi mu njira ya chipembedzo chotero “kulewerana” kwa zaka zambiri dzenje ndi lakuya koposa Grand Canyon. Ndipo tsopano zaipilatu, osati pang’ono pokha, monga mwa omanga okha, akunenera ndi mamangidwe otele. Tadikira, koma popanda kanthu, kumenya mwala kena ndi kena, monga Mose anachitira. Mukuganiza kwina, tikuganiza kuti Mulungu angasinthe maganizo ake ndi kuchitanso zonse bwino, angakhale tikusamvera malamulo ake ndi njira zake.

Mu njira ina ya moyo tidzayembekeza kusintha kwa zinthu mumachitidwe amene sanabare kanthu mbuyomu? Ngati muli sukulu yapamwamba ndipo muli ndi kulemera kokwana 150 pa sikelo, koma ndikumalephera zonse zolembedwa kodi mungaganize zosintha? Ndi zopusa ndithu kotero mungasinthe zonse polankhula za zimenezi. Kapenanso kukhudzidwa ndi zolankhura? Mukudziwa zoonatu. Mukudziwa mmene mungapelekere malipiro pochiya za zinthu izi. Davide sanagonjetse Goliati chifukwa choti anakonza msonkhano waukulu pa mutu wa kupha Goliati.

Pansipa mudzapeze mau ena ochokera mu kanema ndipo werengani bwino ndipo pemphererani dziwani mmene mabvutowa alili ndiponso dziwani kuti 150 kulemera kwache ndi kulephera. Sikungochoka pa zimene timapanga mbuyomu mauthenga ochepa ndi mapulogalamu ndi zinthu zina zabwino. Sizingathe kuchotsa zinthu izi mmene timangira ndi zimene zimayenera kukhalira kwa nthawi yaitali pochilika misonkhano wa anthu ambiri ndi mapologalamu ndi mabungwe a chipembedzo ndi mapemphero ndi misonkhano semina, zinthu sizili bwino, sizili mwabwino, mapologalamu ndi machitidwe ndi zoyerekeza zonse ndi zoonoka zazikulu sizikutumikira Mulungu bwino ai monga tamvera ndi atsogoleri aja. Maukwati ndi ana mu dziko lonse ali kulipira dipo chifukwa cha mamangidwe a anthu ndi mamangidwe olakwika. Pamene timanga ndi njerwa mmalo mwa miala ndiye timaika zakunja ndi malankhulidwe ndipo kusonkhana kw atsiku ndi tsiku mu ufumu wa unsembe. Satana amatengerapo mwai pa mamangidwe oipa otere ndi kufuna kugwetsa nyumbayo.

Izi ndi zina mwa zimene atsogoleri ananena posachedwapa zokhudza mipingo yawo.

“America ikuchoka mu machitidwe anthu a Mulungu mu mipingo”

“mukafukufuku woposachedwapa pa anthu 66 mwa anthu 100 aliwonse mu makhalidwe awo akhristu sali osiyana mu

zochita zawo ndi amene Sali akristu mwa gawo a anthu 66 aja.”

“Akristu Sali ndi kulankhula mwa machitidwe okoma mu dziko lino.”

“Kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya dziko lino ku maiko azungu kusiyana mabanja kwachuluka mu mpingo kwambiri,

kusiyana ndi amene Sali opemphera.”

“Mulungu akuyang’ana mu mipingo yathu ndipo akupeza kusiyana kwa mabanja kwa anthu a Mulungu monganso achitira anthu a dziko lapansi. Mulungu akuyang’ana mu mpingo ndipo ali kupeza kutaya mamba mwa anthu a Mulungu monganso achitira anthu a dziko lapansi. Alinso kuyang’ana mu mpingo ndi kupeza kuba kwa ana a Mulungu. Kafukufuku anati kusiyana pakati pa mipingo ndi anthu adziko lapansi ndi kosabvuta kusiyanitsa mu maonekedwe.”

“Ndikabwera ku nkhani ya mabanja ndi maukwati sitinachite bwino konse.”

“Mwa ana 80 mwa aliyense amene alolodwa mu mpingo ndipo ndikumakhulupilika kupita ku mpingo 80 mwa iwowa aiya mpingo pamene achoka ku manyumba a makolo awo.”

“Tachotsa zochitika pa pemphero, ndipo taikapo zina za uzimu ndipo kusinthana ndi kumvera kwatunthu, ndipo ndikuwapatsa ukulu abusa anthu ndi Ansembe ndili mu nyengo ya chinyengo. Mulungu ayenera kuchita chatsopano mu mpingo.”

“Tafika pa mphambano ndipo tiyenera kusintha kwenikweni mu mipingo. Taima mu nthawi yobvuta pa chiweluziro ndi chitsitsimutso. Tiyenera kusankha ngati tidzamvere.”

“Kuchokera mu mbiri za mmbuyomu ndi zokaikitsa kuti dziko lino lidzakhalanso ndi chitsitsimutso, mpingo uyenera kukhala ndi chitsitsimutso. Talowelelani moyo wathu ndi zinthu za dziko lapansi ndipo taika chikhristu monga chiwonetsero.”

Monga ndi masankhidwe a mfumu kulowa mmalo a utsogoleri wochokera kwa Mulungu ndipo mtengo ndi waukulu ndi mamangidwe a njira ya anthu (1Samueli 8:4-20) Maonekedwe anthu amene ali kutali ndi malemba ndi kusinthana ndi ukulu wa Yesu ndi mautumiki ndi anthu otchedwa ma missionaries ndipo mipingo yaing’ono ing’ono ndi mautumiki ndi malongosoledwe a anthu ndipo ngozochita za mabungwe. Angakhale atsogoleri a nyengo ino aona kuti zinthu zones zalephereka. Ndipo Mulungu ali kulengeza kuti mudzadiwa mtengo ndi zipatso zake.

Ndipo pa matero a Kanema ameneyu ndipo ambiri Sali kuzindikirabe kuti tili kupitilabe kuyetsetsa kupeza njira pobweletsabe zinthu zakale zija mu mbando ndi mbado wina.

Bwanji usati kuti posaganizira za mtengo wopelekedwa kuti tipitenso kumbuyo kumene kuli ndondomeko zimene Yesu ndi Atumwi anaika kuti mpingo ndi wamaonekedwe otere Machitidwe 2:42—47 sikuti zidali monga mwa chikhalidwe chawo koma kuti anthu zikwi zitztu 3000 akristu atsopano anayamba kuyenda mu njira ya Mulungu kupeza “mpingo” posunga ziphunzitso zophweka za Ambuye zinali zotani zofunika zawo zoyambilira pa moyo wawo? Kodi anali kuonjezera chi kristu pa zochita zawo pokhala, kuyenda ndi zimene amakhala mwa Kristu aliyense anali kufunitsitsa ufumu poyamba tsiku ndi tsiku ndipo mudziwa yankho yakeokhulupirira onse anali pamodzi ndipo anali ndi zinthu zofanana.

Anali kuululana machismo awo kwa wina ndi mzake ndipo anali kupemphelerana wina ndi mzake kuti achilitsike.

Uku sikungokhala pagulu chabe koma kuti osakhala mwa iwe wekha ndi wina pa moyo wa chifundo. Kulimbikira kupeleka aliyense kwa chiyeletso mwa Kristu anali kuchita bwanji wina ndi mzake kodi ndi anthu opezeka la sabata ndi zochitika ndi zolemetsa mu sabata yonseyo? Kapena tsiku ndi tsiku monganso ansembe a okhulupilira. Kodi msonkhano yawo inali yofanana ndi mmene ilili nthawi yino imene ndi yotsogolezedwa ndi munthu? Kapena kuti pamene bvumbulutso ibwera kwa wina okhalapo ndipo wina oyambayo akhale pansi? Chifukwa ndi chiyani? Chifukwa Ambuye anati inu ndinu nonse abale.

Banja pali zambiri zolankhulidwa mmene Yesu ndi ophunzira ophunzitsidwa bwino Atumwi anali kumangira mpingo mmene Ambuye amafunira. Monga Mtumwi Paulo analankhulira tiyenera kuti tidziwe tonse. Chuma chobisika cha Kristu ndi machitidwe ake ndi mmene zimayendera pa chuma chobisika chimenechi kuti, mmalo mwake, tsopano kudzera mu mpingo, nzeru yakuya ya Mulungu ikadziwike kwa maukulu ndi zimphamvu za nyengo ino (Aefeso 3) tingathe kudzimitsa Mzimu ndi mmene tili kuchitira zinthu kapenanso tingachitenso pamodzi ndi iye mu ufumu wake wosatha.

Tadziwani pa zimene zaoneka mu kanema uja ndi ngozi ndithu ndipo angaonongeke. Ulemerero ukhale kumatamando ake. Mitima wosweka ndi moyo wosweka ingathe kuchilitsika ngati titamanga mu maziko ake ngati tonse pamodzi tingazule kugwetsa kuwononga ndi kutchotselani (zones zimene zili zomangidwa ndi anthu) kuti iye angathe kumanga ndi kubyala. (Yer 1:10) pomalizira penipeni tikuonetselani kuchokera mu maganizo zaka zapitazo ali kulankhula umu tingapezere Yesu.

Ufulu ndi Opezeka

Ndinaona zopelekedwa pankhani madzulo ano pamene Mphunzitsi wamkulu amene anali ofufuza za sayansi anapeleka zamalonda kulengeza mu Newapaper ina kufunsa ophunzira. Anapeleka $15 pa tsiku ngati adzachite sewero. Gawo lina likhale akaidi mu ndende. Ndipo enawo akhale asilikali a ndende, ndipo pasakhale kumenyana ndi zankhaza, koma kusewela basi koma zotsatira zake zinali zoipa ndithu mu masiku asanu okha onse amene anali Asilikali anakhala oipitsitsa mu zochita zawo anali kuwachitira zoipa akaidi aja. Ndipo akaidi aja amene anali amphamvu, angwiro, anzeru, ndiponso ana asukulu a ku college) anali kupeza kuphinjika ndi zina zija zosaneneka pa moyo wawo mmodzi ndi mmodzi anali tsopano kuipitstsa mu malingaliro awo ndi mu bongo wawo ndipo anayamba kuiwala kuti anali onse ophunzira) onse asilikali ndi akaidiyo anali kungochita masewelo chabe. Kwa masiku asanu okha anakhala oipa chifukwa cha zimene anali kuchita ndipo ndi makolala oyera ulamuliro zimene zinalimbikitsa pa zimene zimachitikazo ndipo anachoka muzimene anali ndi kukhala mmene samayembekezera mu masiku asanu okha.

Uthenga wa ufumu ungakhale osamveka bwino, koma ndinena motero kuti pali anthu abwino ambiri kunjaku amene ali kufunitsitsa kuti azipeleke kwa Yesu ndi kukula mu chikondi chake ndi mukukula msinkhu ndi kuzipeleka nsembe ndi iye. Kuti tisalephere ai, anakhala anthu amene sanali kuwaganizira kukhala anakhala olephera mu moyo wawo wonse komanso kumamva bwino ndi chinyengo dziko lapansi ngakahlenso miyambo ya chinyengo komanso kusakhudzidwa kapena ndi kukhala mu moyo womvetsa chisoni chifukwa ninji? Siziyenera kukhala choncho ai Mulungu anakonza njira ndi machitidwe amene angathandize angakhale munthu amene ali ofooka kuti amudziwe iye, komanso kugonjetsa uchimo. Ndidzamanga mpingo umene makomo a anthu akufa sudzatha kuwogonjetsa. Yesu, podziwa kuti ndife ofooka anapumira mpingo wake kuti akristu wamba, amuna ndi akazi akhale ogonjeza ndipo pamene tikuti mau oti mpingo sindikunena zimene zimafanizilidwa ndi kungokhala oyang’anira chipembedzo ndipo ndikuthandauza zimene malembo amanena mmene amauwa ayenera kuthandauzidwa,.

Ndikunena monga mmene Yesu mwini amagwilitsira ntchito mauwa ndikunena za chiyanjano chenicheni (chimene sichongokumana chabe) kumene mau a Mulungu ali ndi kugwilitsidwa ntchito kwa munthu wina aliyense mwamuna kapenanso mkazi ndi mwana yemwe tsiku lili lonse (Aheberi 3:12-14) Machitidwe 2:42—47) ndikunena za mpingo umene Yesu ananena kuti adzamanga pamene bamboo, mai ndi ana omwe ali ndi amai ambiri, abale ndi alongo, malo, katundu mazunzo, ndipo pamapeto ake, moyo wosatha pambali pa izi palibe mpingo ai, ngati uli mpingo weniweni uyenera kukhala kuti aliyense akukonda Yesu ndiponso kumudziwa komanso kutengeka zothombitsa ndi kukwaniritsa lamulo la Kristu” kuwululana machimo wina ndi mzake. Kuthandizana wina ndi mnzake. Kukondana wina ndi mzake ndi zina zooneka mwa mphamvu wa mpingo woona china chake ndiye kuti ndi chotaika kapena chidzataika, choikilapo nyali) ndiye kuti sitinganene kuti mpingo wa Yesu, kristu ndi mutu.

Ngati uli mpingo mwa kuthandiza kwa Mulungu ndiye kuti makomo a ndende sadzakwanitsa kuti aononge. Sitidzaluza ana athu ku dziko lapansi ndi mzimu wa dziko lino. Sitidzaluza maganizo a muna athu monga kupelekedwa kuzopanda pake ndi zalutha. Ndipo mali zambiri zopsyola apa. Ndipo ngati mpingo uli mpingo weniweni osati ndi chongochita pa lasabata lokha ndiye kuti sudzakhala choncho, pamene tikufuna kubweletsa chikondwelero kwa Yesu. Kungosewera chabe ndi zongochitika pamene tikupitiliza kuwonetsera pa lamulungu monga zongocheza chabe. Ndipo ndikuika zinthu zomzngilira kuti asachoke ai umenewu si mpingo ai. Mudziwe zimenezi angakhale kuti nyimbo ndi zamphamvu ndikuti ulaliki ndi wauzimu ndi othandiza sizingathandauze kuti ndiye mpingo chifukwa pali kuchitika zotere mpingo uyenera kukhala monga mmene Mulungu amaudziwira (Mat 16:18) aliyense amene ali ndi mphamvu ya Mulungu imene thupi ndi mgwilizano siwolumizidwa ndi kuwonera kapena kudya pa chipembedzo koma ndi kuti kuyenda mu kuunika pamodzi ngati monganso iye ali kuunika. Ngati sitikulora ena kudza mkati mwathu sitidzadziwa ufumu wakumwamba ndi zipatso zake. Zoona ndi zoti sikuti uli uko kapena uko, koma mwa ife.

Ngati tikumanga munjira ya Mulungu osati ndi miyambo ya anthu imene imakana mau a Mulungu ndipo ngati tili thupi lake Kristu ndipo likugwira ntchito tsiku ndi tsiku monga kufunikira. Sizitenganso nthawi yaitali kuti ife tikhale mu machitidwe otere monganso tawonera ophunzira aja. Posalengera kuti ndife ndani kapenanso tili kuti Yesu amadziwa kuti padzafunika njiya ya Mulungu. Moyo wa tsiku ndi tsiku kupeleka moyo ndi kuwonetsera ndi chiphunzitso mu mpingo makhalidwe ndi magulu oipa awononga ndipo ali kuwonekera ndipo sakuthetsedwa ku chikristu nthawi ino.

Iyo ndi mbali yathu pamene pa malo amene kukhala pa moyo wowonetsera moyo wa Kristu koma kukhala pa msonkhano umene ndi yongotenthetsa kuti mabvuto amene tawapeza mu nkhani ya Akaidi ndi asilikali andende ndidzalikonza ndipo pomaliza anthu wamba amene akufuna kukhala mu moyo wa Yesu osati mwa iwo okha adzayamba kuwona mabvuto awo kuchotsedwa ndiponso adzaona kuthekera kwawo. Mulungu amadziwa kulephera kwathu ndiponso mmene timagonjera kubvuto ya asilikali a ndende ndi akaidi monga mmene talankhulira mmwambamu. Anthu okhala nawo ulamuliro mu malo antchito. Mu boma ndiponso mu chipembedzo) mu masukulu nthawi ndi nthawi muli zachinyengo zimene zimatibweletsera zauchimo.

Magulu oipa amawononga (ngakhalenso) amakhalidwe abwino! MALO AMENE TILI AMALANKHULA.

Munthu wapakati (mkazi) pa ntchito ndi ananso mu masukulu aboma ndi muzipembedzo ngakhalenso azimai kunyumba onsewa ali ndi mgwilizano ochepa chitsogozo alikulephera kuthandiza kukula mu kuzama mu zenizeni ndi Yesu ndi enanso.

Akhala ali kudziko lamanyado umbombo mantha, chilakolako, kusilira, ulesi, kukhumudwa ndinso uzimu umene suli wabwino mu machitidwe ake ali mu zonama za dziko lapansi monga Asilikali/ ndi akaidi aja zimene dziko lapansi laika ndipo palibe kuziteteza, popanda Yesu ndi mpingo wake kuti makomo andende sangaime. Pamasiku asanu okha ndi mulingo okwanira kuti pakhale bvuto lalikulu kukhala monga chotupitsa ndipo zachinyengo zimene timakhalanso ndi chifukwa chake Mulungu anati chengetelani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku monga patchedwa tsiku kuti wina osamumitse mtima wake.

Zoona ndi kuti pangakhale zofooka ndi zolakwitsa angakhale kuti cili mu mpingo wodabwitsa otani koma pali malo amodzi amene Mulungu amene apeleka chuma kuti chikule kufikira kuchidzalo cha muyezo mu utundu wa kristu.

Osakhalanso makanda otengedwa ndi mafunde uku ndi uko ai ndiye kuti tsiku nfi tsiku kuwonetsera mgwilizano mu choona cha kristu umene umaonetsera mu bvumbulutso la Kristu. Kwa munthu wina aliyense (Mat 16) ndi kulumikiza mu zenizeni) 1 Akor 12) ku thupi la Kristu tsiku ndi tsiku. Ndipo tidzazindikira kuchokera zimene mdani amatenga kwa ife pamene tilakwitsa kuchokera mu kusadziwa kwathupi lathu, ndiye mu mpingo, makomo a ndende sadzatha kupambana.

Ndiye Tingatani Pamene Sizili Mu Njira Yotere Pamene Takumana Ndi Zotere?

Ndikubwelelanso moyo wathu wakale wa dziko la pansi osalumikizidwa kuchokera mu moyo wolumikizika pakuyenda mu kuwumika ndi kuzipeleka, kutengelana zothondetsa zimene zimakhala mu mpingo sindingabwelelenso ku machitidwe otere.

(1) Pempherani kosalekeza ndi kusala kudya kwa Ambuye okolora kuti antchito ndi zokolora kwa ife kudzawonekera bwino ngati tichita khalani opembedza mu chipinda mseri ndi kukhala wantchito ku mabondo anu.

(2) Chotsani zipinga zones ndi kuika moyo wanu kwa anthu ena tsopano, tsiku ndi tsiku usiku kugwira ntchito ndi kuwulula machismo anu kwa wina ndi mzake ndi kuchita zones zamu kuunika monga iye ali kuwunika kuti muchite izi masiku ndi madzulo onse ndiye kwinako musiileni iyeyo,.

Ndiye kuti tili okhudzidwa kuti takwanira mu muyezo yopitilira aliyense wadziwa kuphatikiza ndi atsogoleri kuti pali kufunika kuti tisinthe makhalidwe a chipembedzo adziko lino. Angakhale kuli malo abwino adzadza ndi chotupitsa kupeputsa lamulo la Ambuye. Tsopano tiyeni tidziwe kuti mabvutowa amafunika kuwathetsa ndi mabvuto enanso tidziwe kuti sibvuto la Mulungu ai kuti makutu athu mutuluke usoso, ndiye tiyenera kudziwa kuti zipatso zoipazi ndi udindo wathu chifukwa cha kusamvera kwathu ku chowonadi cha chiyambi mmene mpingo uyenera kukhalira. Tsopano pachifuniro cha mwana wa nkhosa wa Mulungu ndi ang’ono ena ndikutinso dziko lidziwe mmene tingakondelana tiyeni tiyende mu kumvera mu chisomo chake. Simuli ainu nokha, munagulidwa ndi mtengo wake ndi mphatso wodabwitsa ndi mai lero ndi masiku onse mu nthawi yonse ya moyo wanu posasotsera, kwa inu banja lanu, mpingo wanu, ndi ena amene mumawadziwa amene amati ndi ake aiye ndi zabwino ndithu.

Timalize tonse monga tinayambira?

Aliyense oipa mtima, mu chipembedzo amene waloledwa kuona kuseri kwa chipembedzo cha makomo ndi kubwelera mbuyo angaone, tingaone mabvuto, koma takonzeka kupita pamwamba kuti tithetse mabvuto amenewa kapena tidzakhala ngati mwana wang’ono uja wa ku Holland kugwilizitsa manja monganso tachitira mu mibadwo yonseyi? Tiyeni tipitenso kwathu kumudzi kuti tipeze yankho, zili mu mtima ndi njira ya Messaya—njira imene anakhala ndi choonadi chimene anaonetsera ndi kuphunzitsa kwa onse amene ali ake chabwino?

<<<
jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon