KUKHUDZIKA

24/10/1995

KUSOWA CHOTI NDITSATIRE

Ndimafuna kutsogozedwa ndi “Mzimu Woyera” (ichi ndichofunika kuposa kungokhala ndi chiyanjano ndi chibale ndi Yesu?!) komanso ndinazindikira kuti ndi “mpingo” (osati” mayendedwe anga okha”) Izi zimatheka chipilala komanso Maziko Choonadi” kuti zinthu zonse “zikhazikitsidwa pamaso pa mboni ziwiri kapena zitatu” Diso silinganenekwa dzanja, ‘ine sindikufuna iwe!’ ndipo chimodzimodzinso mutu siunganene kwa mwendo, ‘ine sindikufuna iwe!’ “Pali nzeru pakuchuluka kwa uphungu.” Limbikitsanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa lero, “ kuopa wina ndi wa inu angaunitsidwe mtima machenjerero oipa auchimo.” Ndinso, ndinso, ….. Malo mwake, ndingakhale bwanji ndi chiyanjano ndi Mulungu komanso “ kuzindikira thupi” komanso ndikukhala nawo moyo womwe Mulungu, wauika mmpingo wa ku malo koma ine ndikupezeka nthawi imodzimodzi?! Kodi munthu wina sangathe kuona kuti anthu ena ndi wosafunika popanga zinthu zosokoneza?

Kodi ndikhonza kukhala munthu okhudzika, komanso kutha kugwira ntchito mumodzi mukukhulupirira anthu ena? Kodi zingakhale bwanji ngati ndingapezeke ndiri ndi kukhudzika kwakukulu ndithu. Pa zinthu zina, ndipo m’malo mwake ndayenera kufunsapo anthu ena ali ndi mbiri yabwino ya mayendedwe awo ndi Mulungu, koma kukhudzika kwawo kukusiyana ndi kwanga? Koma kukhudzika kwanga ndi kwakukulu ndithu, pomwe kukhudzika kwa ogwira ntchito a Mulungu kuli kosiyana kotheratu ndi kwanga.

Kodi njira yanga yolakwitsa iyenera kukhala chonchi, pamaso pa mboni ziwiri zitatu omwe akuona mosiyana ndi m’mene ine ndikuonera, kodi ndidzayenera kukhulupirira kukhudzika kwawo kusiyana ndi kukhudzika komwe ine ndirinako? Ndibwino kuoneka ngati munthu olakwa. Posafuna kusiya zomwe ndikuganiza kuopa kuti mathero ake ndingadzilakwire ine ndekha?

ZINTHU ZOYENERA MAKANGANO

Pali magulu a zinthu zomwe buku la Aroma Mutu wa 14 akuzifotokoza ngati za malekano. Pali zinthu zina zomwe ndi zosafunikira kuzifotokoza ngati kodi ndigule galimoto yofiira kapena lobiriwira. Nthawi zambiri sizinthu zomwe zowopseza moyo wathu ngati moyo kapena imfa. Nthawi zina zikhoza kutheka kuti mungathe kulota maloto usiku wathawu ndikupanga chiganizo kuchokera pa malotowo, ngati zinthu zofunika kwambiri (ngati imfa ndi moyo).

Chingachitike chiyani ngati anthu awiri kapena atatu angadze ndi kunena, “ife tikuona ngati ndi zoopsa kwambiri, chifukwa cha ___________.” Chinthu chofunika kuchizindikira kufunika kwa mpingo” sizitathauza kuti kodi kapena tigwirizane kapena ayi, tigwirizane kapena ayi kuti tigwirire ntchito limodzi ndi kupita chamtsogolo pamodzi ndikuthandizana wina ndi mzake olo zingafute bwanji tsogolo lathu m’mene liliri.

Kodi nthawi zina timatha kuona kuti nkhani yomwe tili nayo ndiyosayenera kukangana, koma kuti tili ndi kukhudzika konena kuti tili nacho chhikhulupiriro kuti chinthu tikunena chachokera kwa Mulungu? Tiyenera kuona bwinobwino m’mene tingatchulire zinthu zathu mosamala kwambiri. Chinthu chomwe ndingachisankhe ngati “chokhudzika changa” chiyenera kusakhala chaching’ono, choutsa makangano. Chiyenera chikhale chinthu chomwe chingakhale nacho chidaliro chochokera m’mawu a Mulungu kuti “anthu omwe akubwera kumene” ayenera kuti adzathandizike nacho.

Komanso chikhalidwe cha zolengedwa ndi Mulungu zimene ziyenera kufunika kosatha, osati miyambo ndi zosangalatsa za ana anthu mwa chotchinga chonena kuti “chokhudzika changa.” Tiyenera kumvera kwa anzathu ena. Ndemanga yomwe Ambuye Yesu adanena yokhudzana ndi kumvera kwa munthu wina mubuku la (Mateyu 8:9 —10) pamapeto pake chinali chinthu chodalilika. Ndiyenera kukhala munthu wosamalitsa kwambiri ndikufuna kunena za “kukhudzika kwanga.” Kapena kuti kutsogozedwa kwanga ndi “Mzimu woyera” kuti zikhale zinthu zenizeni, posatengera kufuna kwake kwa thupi. Ndiye near kukhala ndi malingaliro pa zinthu zina. Komanso ndiyenera kuteteza zinthu zomwe ndikunena ngati chokhudzika changa kuti chikhodza kukhala ndi zotsatira zake kumwamba. Chokhudzika changa chiyenera kukhala chomwe ine nthawi zonse ndiyenera kuimapo ngakhale zitavuta motani. Ndiyenera m’malo mwake kukhala okonzekera zotsatira ndikuperekera mtengo wake pa chimenechi. Zonse nthawi zambiri chimakhala champhamvu kwambiri, pochokera m’maganizo, chinthu champhamvu chimene chingakhazikidwe pa anthu ena, komanso ngati (chonyadira) chodzitamandira (‘Ndili ndi chiyanjano ndi Mulungu!” “Ine ndimangomvera Mzimu Woyera”)

KUKHUDZIKA SIKUKHALA KONSE KOFANANA

Pali, komanso ndi chachidziwikire kuti, pali “kukhudzika kosiyanasiyana” mwachitsanzo, mchimene othekera atapita kudziko lina ndikulankhula m’mchipinda chodzala ndi anthu kuti mwezi udapangidwa ndi cheese, chifukwa izi adamuuza ndi agogo ake akazi omwe nthawi zambiri sadamunamizepo, ndiye m’malo mwake ndi zoonadi mwezi umapangidwa kuchokera ku cheese. Komanso ine ndikhonza kukhala kukhulupirira kwakukulu kuti Yesu adapereka magazi ake kuti tisadelerane wina ndi mzake, kuti tonse ndikuthekera konse tilimbikitse umodzi mumzimu ndi muchilungamo. Chikhulupiriro ichi ndi chapamwamba kuposa chokhulupirira pamwamba pa mwezi. M’malo mwake ine ndiyenera kusunga chikhulupiriro cha kupangidwa kwa mwezi posafuna kuchititsa manyazi mbaleyo. Sichinthu chofuna ngakhale chilli “chikhulupiriro.” Ngakhale kuti izi zikhoza kuonetsa m’mene zinthu ziliri ndi mbaleyu muchiyanjano chake ndi Mulungu, mpingo ndi banja lake izi ziyenera kukhala ndi kukambirana kofunika, tisakambirane zinthu zopanda pake ngati zamwezi chikhulupiriro chopanda pake. Ndikukhulupirira ngati mudawerengapo za “Kamnyamata kena komwe kadalilira chimbalangondo.’”

Pamene tikuyesetsa kuti tisakhale ndi kukhudzika kuonjeza kuposa komwe kuyenera kukhalapo “Chikhulupiriro changa,” chiyenera kukhala, osati chaulesi potsatira Mulungu. Ngati zinthu zilipo.” Ndikuyenera kutipula chiyanjano changa ndi Mulungu chimene sichiyenera kukhala chakale koma chatsopano nthawi zonse. Ndiyenera kumvera Mulungu ndikukhala paubwenzi ndi iye (Yohane 15:14-15; Aroma 8:13-14; Yohane 17:3). Kungotengera zinthu monga momwe zikuyenera ngati kukhudzika sikothandiza popanda kutsatira Mulungu mwini wake ndi njira yosayenera komanso yosazama komanso yosakwaniritsa zinthu. Tiyenera kusamalitsa posafuna kudziika tokha pamwamba pa moyo wa Yesu m’mpingo wake “pochita zinthu zokondweretsa ife tokha” kumeneku ndiko timati kumusautsa Yesu komanso kumukana Yesu. Uku ndiko timakutcha kugwira njakata (dilemma!) koma m’malo mwake ndi chinthu chosavuta ndi chokondweretsa kuchita zinthu munjira yomwe Mulungu amasangalala nayo. Tiyeni tione mozamirapo pankhaniyi.

PAULO SAKADACHITIRA MWINA!

Chitsanzo ndi ichi. Paulo adali kukhudzika kuti adayenera kupita ku Yerusalemu. Ifenso nthawi zina tikhoza kupezeka mumachitidwe ngati amenewa omwe mbale wathu adapezana nawo pamene abale ngati Luka ndi Agabus (omwe adali aneneri ndi abale ena adanena ayi, “Paulo usapite ku Yerusalemu. Ndidayenera kuchita izi monga iwe ukadachitira. Usachite ichi.” Umu ndi momwe Mzimu wa umodzi umene Atate amafunira munthawi ngati iyi: Paulo adanena, “Pepani abale, ndiyenera kuchita ichi. Ndiyenera kupita ku Yerusalemu.

Ndikadatha kuchita mnjira yanu. Mukundidziwa ine abale. Ine sindine odzikonda kapena gonthi kapenanso onyozera posalemekeza mawu anu abale. Ndimakukondani kwambiri inu abale. Ndikukhulupirira ndi mtima wanga wonse kuti ndiyenera kupita ku Yerusalemu. Kodi inu mundithangatira pachinthuchi? Ndikufuna inu muyime limodzi ndi ine m’chinthuchi.”

Apa sitikumva kuti Paulo sadafune kutuluka m’chipindacho ukamadzipereka kwathunthu kwa abale omwe adamuuza “kuti usapite, usapite.” Malingaliro mwake mudalibe zinthu ngati izi: Tiona m’mene zikhalire, ndikuganiza kuti ndikulondola pa zimene ndikuchita……. Ndiwaonetsa iwo ….. ndawauza choncho ….. ndiyenera kupita ndikuchita chinthu ichi ….. “ kungotuluka m’chipinda ndi malingaliro otere kukadaonetsa uchimo pamaso pa Mulungu. Iye adakayenera kumveranso kwa kachiwiri kuchokera kwa Yesu wouka kuchokera kwa akufa, “Saulo, chifukwa ukundilondalonda ine?”

Mwanjira ina, ngati abale ena akadatha kutuluka mchipinda nkuganiza, “Paulo ndi wosamva komanso wa Mzimu wosaweruzika…. Malamulo sadali kugwira ntchito pa iye…….. kunena kuti iye adali bwino kuposa anthu ena onse ………….. tidamuuza kuti mbale usapite, koma m’malo mwake iye adapitabe…………. Anthu asanu kulimbana ndi munthu m’modzi, koma iye adalimbikira kuchita chinthucho…………” Ngati pakadapezeka munthu wina yemwe akadatuluka m’chipinda ndi maganizo oterewa iyeyo akadapezeka ochimwa pamaso pa Mulungu posaona kufunika kwa thupi la Ambuye.

Pa nthawi yomwe iwo akadatuluka mchipindamp, Paulo kapena abale enanso akadatha kutuluka ndi cholinga chofuna kuthandiza abale ena pochita zinthuzi m’njira ya iwo wokha. Kapenanso ntahwi zina sakadatha kuchita kanthu kamtundu wina pofuna kudikira pa Yehova kuti awatsogolere chomwe iwo adayenera kuchitsatira. Kupatula kuti pakhoza kukhala kulimbika kwa paderadera kuti chilli chonse chomwe chiti chichitike, chitifikire limodzi. Awa ndiwo timati malingaliro a Mulungu wokhudzana ndi chinthuchi. Ichi ndi chomwe iwo adachita.

Mzimu wa Yesu utalankhula pokhudzana nthawi yovuta monga yomwe Paulo adali nayo (yosiyana kukhudzika) udakaoneka ngati wabodza: “Abale, ndikumva zomwe mukulankhula ndiponso ndikudziwa komwe mukuchokera. Ndikuthokoza kwambiri, ndinakulemekezani koposa. Moyo mwanga sindidapange chiganizo china chilli chonse chochita zinthu zosiyana ndi zimene inu mudakonza kuti zichitike. Koma pa chinthu ichi ndiloleni ine abale ndimuke ndipo ndikukupemphani kuti mundilole muchinthu kuti ndichichite.

Ngati ndili olakwa, ndiloleni ndi chite zimenezi nthawi ina ngati pali chinthu china choyenera kutenga. Ndiyenera kuchita chinthuchi tsopano ndipo m’malo mwake ndikupempha inu abale mundithangatire kuti nditero. “M’zokumana nazo zomwe Paulo adakumana nazo iwo adamuthandiza pomufunira mafuno abwino. Palibe ndi m’modzi yomwe amene adakwanitsa kutuluka mchipinda, pomuganizira Paulo ngati mbale osaweruzika, ofuna uphungu wa iye yekha. Kwa iwo kuzindikira thupi kumathandauza kudzipereka kugwirira ntchito pamodzi.

Koma ngati idali nkhani yoyenera makangano, Paulo akadayenera kukhala wamanyazi kapenanso maganizo ake adamulola kuti iye asamvera anthu onse otchedwa abale! Manyazi adayenera akhale pa iye. Koma, mukufufuza mbiri ya kutembenuka kwa patatha zaka 20 mbuyomu, iye adali ndi masophenya kuti adayenera kuima pamaso pa anthu amitundu ndi mafumu. Iye ankadziwa kuti adali ndi zaka 20 zoyembekezera kuima pamaso pa mafumu. Koma tsopano iwo ankanena kuti, “Paulo ngati upita ku Yerusalemu akamangidwa. Iwe ukayenera kukaima pamaso pa mafumu.” Ndipo iye adayankha kuti “ndikudziwa. Ndiyenera kutero. Ndidauzidwa kuti ndikuyenera kukulankhula ndi anthu amitundu ndinso mafumu awo. M’mene zinthuzi zilili zikuoneka kuti ndi mbali ina ya moyo wanga. Inenso abale ndikudana nacho chinthuchi. Koma palibe kuchitira mwina ndikuyenera kutero. Uku ndiko kukhudzika.” Sinali nkhani yoyenera makangano. Iye adali umboni onse kuti adayenera kuyenda muchitsogozo chotero.

Pali zinthu zina zoyenera makangano koma izi ayi, ine ndimafuna kumvera ngati nkotheka kwa anthu onse omwe ali ndi kukhudzika. Ndikufuna kunena monenetsa kuti, ndi kukhudzika kwawo komwe ine ndingamvere osati maganizo awo ayi. Ine sindimafuna kuti maganizo awo ndiwo akhazikitsidwe pa ine. Ngati zinthu za uzimu omva za iwe wekha. Koma ngati pali kukhudzika ine ndikuyenera kuthandizapo pa chinthuchi. Ngati kuli kotheka ndikuyenera kutero. Koma ngati ndili ndi kukhudzika kosiyana, sindidzangokana zomwe iwo ali nazo. Ndinayenera kuwapempha abalewo kuti agwirire limodzi ndi ine ntchitoyo. “ndithangateni ine pa chinthu ichi, ndipo tidzayenda limodzi. Ndikufuna chithandizo chanu abale ngati nkotheka choonde ndithandizeni kuchita chinthu ichi. Ichi ndicho chokhudzika changa ndili nacho ndiyenera kuyenda nacho.

ABRAHAMU SAKADACHITIRA MWINA!

Pali chinthu chomwe chikuchitika mu nkhani ya Abrahamu pamene Abrahamu akuphunzitsa mwana wake Isaki m’mene angamaponyere muvi ndi uta wake. Ndipokudachitika kuti mnzake adabwera ndikumulankhula, “bwera kuno Abrahamu, tiye tidzipita kunyumba. Banja lako likukufuna kuti ukachite mdulidwe.” Koma m’malo mwake Abrahamu akuyankha kuti, “ndidakhumudwitsapo Mulungu m’buyomu, sindidzachitanso chinthuchi. Ndidzamuphunzitsa Isaki kuti sadzasunthike ndi chinthu chilli chonse, munjira iliyonse, ngakhale mu zinthu zabwino. Ichi ndikuchita.” Munkhaniyi, Abrahamu akunena, “Ndikukhulupirira mudalankhura ndi Sarah, sichoncho? “Iye sadagwirizane nazo, ndipo sadatithandize Sarayo adalankhula mwatseri ndi anthu ena za malingaliro ake. Izi zikuoneka ngati m’mene Miriamu ndi Aroni amakambirana malingaliro awo okhudza za malingaliro a Mose mu buku la Numeri Mutu wa 12, Kodi simenemo? Werenga Mulungu sadadabwe ndi zimene zidachitikazo. Kusakhulupirira zimene wina aliyense angakhale osamvetsa kumawerenga ngati uchimo omwe ukupezeka mubukhu la Yuda. Sarah, m’malo mwake adakaikira m’mutu wake. Paichinso Mulungu sadazizwe nacho.

Tsopano ndikutha kuzindikira kuti ngakhale sewero la Abrahamu sidali yowona koma iye adali ndi kukhudzika koma mkazi wake Sarah sanafune kumuthandiza. Kunena zoona, iwo adali kumunena miseche Abrahamuyo akachokapo. “Eya, ndinalankhulanso ndi Sarah koma m’mene zikuonekera iyenso sakuchimvetsa chinthuchi.” Seweroyi m’eme ilili zikuoneka kuti panali chioneongeko chachikulu. Abrahamu adali ndi kukhudzika kooneka bwino bwino iye adatsimikiza mtima kuti sadzakukhumudwitsanso Mulungu. Iye adakhumudwitsapo Mulungu zaka za mbuyomu koma tsopano sakufuna kuchitanso chinthuchi. Iwo adayenera kumulimbikitsa pa kukhudzika komwe Abrahamuyo adali nako kosafuna kuchitanso mdulidwe omwe iye ndi kale “lonse amachita” pokhala iwo ndi mafunso pa chinthuchi. Iye anayambapo kutsatira kuunika kwa Mulungu pa moyo wake, Iyo m’malo mwake amaganiza kuti Abrahamuyo adayenera kuchitapo kanthu kena. Iwo sadakhale pansi nayo Abrahamu ndi kulankhula nayo zokhudzana ndi m’mene akuchitira tsopano! Izi ndi chitsanzo chabe chomwe ife tiyenera kupewa m’nthawi ngati imeneyi pomwe chinthu china chachilendo chikuchitika ndi mbale kapena mlongo pamene tili ndi “kukhudzika” nkuganiza kuti mbaleyo akuyenda molakwika posatsata chitsogozo cha Mulungu.

Nthawi zina zikhoza kutheka kuti mbaleyo akulakwitsa koma tiyenera kukhala nayo pansi ndikukambirana! Munthu wa mitima iwiri anakhala osinkhasinkha pa njira zake ziwiri nthawi zonse.” Koma ngati chomwe chamuchitisa kukhala ndi khalidwe la chilendo ndi uchimo, izinso zidzadziwika pamene nthawi ikupitapo m’moyo. (izi zikufuna kuti patsautso (lamulo) mfundo ina yoyenera kuitsata pokhala kunja kwa ulamuliro) pa Aheberi 3:12-14, Nthawi zonse tsiku ndi tsiku tiyenera kukhala ndi Abale ndi Alongo anthu omwe timasonkhana nawo kuti tithe kugwira ntchito yomwe Mulungu adatitanira ife. Chonde tadziikani nokha m’nyengo ngati iyi, malo mwa yesu—kapena kuti mukufuna kudziwa tsogolo lanu m’mene iyenera kukhalira! Tiyenera kukambirana pangono za zinthuzi, patsogolo pake, tidzakhala wodziwika zoonadi za nkhaniyi.

Ngati lamulo, pankhani zovuta zoyenera makangano, tiyenera kuthandiza aliyense alingalire m’mene angachitire ndi mnyengo yake ngati iyi (zonse ziyenera kuchitidwa kuchokera pa chiphunzitso cha Mulungu ndi mfundo zake zochokera mawu a Mulungu) tiyenera tichite kuthekera konse kuti tithe kuchita bwino pa mnyengo ngati iyi. Koma pali zinthu zina zomwe sizoyenera kuutsa makangano. Izi zimatengera chikumbumtima ndi chikhudziko chako, chomwe chiyenera kuchitika potengera pa zinthu zochitika zeni zeni. Nthawi zambiri kumaoneka kuti anthu ambiri amachimwira chikumbumtima ndi kukhudzika kwao.

Tiyenera m’malo mwake kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kuti athe kukwaniritsa zomwe akulinga komanso ngati zili zolakwika athe kuzindikira cholakwikacho). Tiyenera kuwaunikira motheratu ngati kungatheke, tiyenera kuwalimbikitsa, ngati tingachitire ndi zomwe Paulo adakumana pofuna kupita ku Yerusalemu.

“INU NDINU AUZIMU”

Pano pali kanthu kena komwe tiyenera kukhala osamala kwambiri pamachitiro ake, ngakhale zili choncho. Chingachitike chiani ngati pakati pathu tingakhale pamodzi ndi anthu omwe maganizo awo sakukhala monga mwa mawu a Mulungu, amene machitidwe awo onse satenga mawu a Mulungu n’kuwaika mu zochitika za moyo watsiku ndi tsiku? (Mat. 7) Anthu omwe sadasinthike amakhala ndi malingaliro osiyanasiyana pa zinthu zambiri. Izi zimatha kuchitika m’malo mwake anthuwo amatha kuombetsana mitu ndi zochitika! “munthu wina akhoza kunena kuti iye ali nako kukhudzika ndipo Mulungu amuyankhula mwakuti mwakuti,” pamene wina amene moyo wake ndiwosokonezeka akhoza kunenapo, ndi zovuta kuzikhulupirira. Ine ndiribe chiyembekezo kuti Mulungu akulankhula china chilichonse. Ndiri ndi umboni kuchokera m’mene moyo wako, chikhalidwe chako cha panyumba. Komanso moyo wako m’mene ulili waku ntchito kwa ine ndi zokaikitsa, ngati ungakwanitse kumvera bwino lomwe zomwe Mulungu wati akulankhula ngati izi.

Moyo wabwino umachokera muzasewero. “mtengo umadziwika ndi zipatso zake, “ choncho mzeru imadziwika bwino ndi ana ake” “Ana ako, ndi opepesa kunena kuti, ali olumala. Ine ndakhala ndikuona chikhalidwe chako komanso kumva lilime lako. Ndikudziwanso pang’ono za mbiri yamoyo wako wakale. Ndimadziwa malingaliro ako ukachokera kuntchito. Ndikudziwa za kusowa kwako kwa njala ya mawu, ndinso kunyada kwako. Sindikukhulupirira za nzeru yomwe uli nayo ngakhale ndili nako kufuna kumvera pa zomwe ukufuna kulankhulazi. Komanso ndikudziwa kuti M ulungu angachite kanthu kena kuchokera pa zimene ukunenazi, koma zipatso zako, monga iwenso ukudziwira, siziri bwino ndi m’mene ukayendera Mulungu moyo wako ndizodzutsa mafunso mwa anthu ambiri. “Nthawi zina zinthuzi zimachokera mzinthu zomwe zimaoneka ngati za masewero kuchokera m’zokambirana (m’zocheza) ndi munthu wina yemwe amene ali ndi “kukhudzika” pa chinthu china. Nthawi zina zikhoza kutheka kuti iye nayenso akhoza kufuna kufunsa mafunso pa zomwe zikuchitikira pofuna kukhala olungama pa zipatso zake.

Koma m’malo mwake ndi zinthu zovuta ukamanena za zimene ndi anthu omwe mayendedwe awo ndi Mulungu ali abwino m’moyo mwawo. Zimene amachita m’moyo mwawo zamangidwa pa thanthwe, amaika mawu a Mulungu muzochitika zawo. Iwo ndiwo anthu okhazikika osagwedezeka ndi mphepo ya mtundu uli wonse ndi olimba mwa Yesu. Moyo wawo ndiwodalilika pakati “pa gulu lonse amene amakumana ndi abale nyumba ndi nyumba.” Moyo wawo ndi umboni kwa anthu onse, oyenda nkuunika pamaso pa okhulupirira okhala nayo “mbiri yabwino.” Anthu a mtundu uwu pamakhala povuta akakhala ndi kukhudzika kuti uwatsutse, pamene ine ndapezeka kuti ndili osiyana nawo pa kukhudzika komwe kuliko, ife tonse m’mene tingathandizanire pofuna kuzindikira thupi la Kristu, pogwirira ntchito limodzi ndiponso pokhalira limodzi. Uku ndiko timakutcha chionetsero cha kudzipereka kwathu pozindikira kufunika kwa thupi la Yesu. Kusunga chiweruzo chathu kuchokera pa mtima osakhulupirira kudzakhala chionongeko. Tiyenera kusalora zinthu za mtundu ngati umenewu m’mitima mwathu. Uku kumakhala kuchititsa manyazi Yesu, kumakhala kusowa umboni, komanso umodzi umene umafunika pokhala ndi zipatso za kumvera ndi kudzichepetsa konse.

MWANAYO NDI IFE MUNG’ANJO YA MOYO

Tiyeni tiganizirepo pang’ono za mavuto omwe amachitika pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Taganizirani inuyo muli ndi mfundo mu chifu mwanu, koma m’malo mwake sinukutha kuzindikira bwino za chinthuchi. Kupatikiza apo mukulephera kufotokoza m’mene mukumverera za chimenechi. Ngati kungapezeke kuti munthu wina atakufunsani kuti, Kodi zili bwanji, “Inuyo n’kumuyankha sindikudziwa.” Chodziwika n’chakuti inuyo muli ndi chinthu chokumangani m’mimba mwanu. Ngati mungakwanitse kunena kuti simukudziwa, mungonena kuti ndimaganizo chabe muli nayo osati ngati chokhudzika. Komanso nthawi zina chimatha kukhala chinthu chomwe chingakhale chosiyana ndi zomwe inu eni ake mukuganiza kuti muchite. Anzanunso angafuna kuchitanso mosiyana ndi inu, koma iwe ungafune kuchitanso mosiyana ndi iwowo. Inu mwina makhoza kudabwa bwanji zinthuzi zikuchitika dero?

Nthawi zina ndikhoza kunena ngati izi. “Abale, ngati mungathe, ine ndikufuna chithandizo chanu pa chinthu chomwe ndili nacho. Ine ndikutha kumva bwino lomwe zomwe mukunena ndipo zikumveka zabwino ndithu, koma ndili ndi chonjata m’chifu mwanga chifukwa cha chinthu chi ndikufuna nditachita mosiyana ndi inu munjira ya ine ndekha. Kodi abale simungathe kundithandizapo pa chinthuchi? “pochita dero sizikuonetsa kuti simukuwalabadira iwo. Koma kuti mukuwalabadira anzawo ngati ziwalo za Khristu. Osangofulumira kukwiya ayi, abale zimene kuchita mukufuna kuti ine ndileke kuchita zomwe chikumbumtima changa chikundiuza. Ine ndili ndi chomanga m’chifu mwanga m’malo mwake inu mukundiletsa kutero.”

Nthawi zina zikhoza kuchitika kuti inu panokha makhoza kukhala ndi kudedela m’moyo mwanu ndi kusakhazikika chifukwa cha chinthu chomwe chilli m’moyo mwanu. Komanso nthawi zina makhoza kubwera mukugonjera konse ku “Thupi la Khristu.” Ndikumva zomwe munena komanso ndili oyamikira kwambiri. Komanso zikuonetsa kuti inuyo mukhoza pa chinthuchi. Kome ine kunena zoona ndili ndi mfundo yonjata m’kati mwanga. Kodi abale mungandithandize pa chinthuchi? Ndikufuna chilimbikitso chanu. Ineyo pandekha sindingathe kuchita chinthuchi m’njira ya ine ndekha. Sindikutha kudziwa kuti chifukwa chake chenicheni n’chiani. kodi abale ngati kungatheke kodi simungachite nane kafukufuku pa chinthuchi kuti chichitike? Mukatha kuchita chimenechi pambuyo pake mutha kudzaseka kuti ndinakuuzani mochedwa.

Pamenepo makhoza kudzasangalala zinthuzi zitakhala kunja kwa zofuna kwanu. M’malo mwake ine ndizatha kutengerapo phunziro mnjira yovuta. Koma inu kodi mungathe kukhala nane pachinthuchi?.

Pochita motero, kudzaonetsa kuti inuyo muli ogonjera kuti ulamuliro wa thupi la Khristu, inuyo muyenera kuti musawawidwe mtima chifukwa chokupangitsa kuchita chomwe inu simunafuna kuchita. Kodi inuyo—simuyenera chita ngati khoswe wakufa: chabwino, chabwino, ine ndili ndi kukhudzika pa chinthuchi, koma iwo alankhula mosiyana ndi ine, m’malo mwake ndi ngokhala chete.’ Chimene chiyenera kuchitika n’chakuti inuyo simuyenera kupitiliza kunenanena za chinthucho pokha pokha mutatha kuona pakati panu pali kumvetsetsana.

Pamenepo, kudzathandauza kuti ndinu ogonjera pozindikira kufunikira kwa Thupi la Khristu, zosiyana ndi kuwawidwa mtima komwe kumapangitsa kuti muchita chinthu china chosiyana ndi chomwe inu mumafuna kuchita poyamba.

Nthawi zina, zimatha kuchitika kuti muli ndi malingaliro chabe ofuna kuchita kanthu pa nthawi ngati iyi—siyani chinthuchi. Mvetserani, pali nzeru “pakuchuluka kwa Aphungu.” Mvetserani koma ngati zili zinthu zochokera maganizo anu okha, chonde musapitirire kuchita chinthu chomwe inu mukumva. Chilekeni musachite. Khalani nawo limodzi iwo amene ali akulu mwa Ambuye ndi inu. Ngati muli ndi “kukhudzika” kudzipereka kwanu kukhale powapempha anzawo kuti abale ndithandizeni kuti ndikwaniritse chinthu chomwe ndili nacho. Koma izi zizakhala zotheka ngati chinthu mukufuna kuchichitacho chilli chofunika kwambiri mu uzimu iwo adzagwira nawe ntchito limodzi.

Iwo adzapeza njira yoti achitire chinthuco. Kapenanso zikhoza kutheka ku Agabus adzayenera kuyenda limodzi ndi Paulo ku Yerusalemu—zinthu zina zake ngati zimenezi.” Ine ndikumva bwino pa zinthu izi. ine ndikutha kumva kuti inuyo zimuyenera kupita. Koma ngati Agabus ali ndi inu ndidzakhala ndi chinthuchi mosavuta.

Kunena mwamtundu wina, izi zikhoza kutanthauza kuti payenera kuti pali mayankho ena amene ife sitinawalingalirepo, amenewo ndiwo amene Mulungu watipatsa, pamene ife tonse pamodzi tapilira. Iye adatilonjeza kuti adzakhala nafe ife tikakhala a mtima umodzi (Mateyu 18). Izi zizachitika ngati ife tingadzipereka ndikuchita zinthu zimodzi, m’malo mongolekerera ena posawathandiza pa zomwe akukhudzika nazo, Yesu adzagwira nafe ntchito mopanda vuto lina lililonse, monga adachitira ndi anthu ena “Ng’anjo ya Moto” ndi abale athu atatu, Shadreki, ndi anzake. Ife (tikhala) tikadziika tokha m’njira ya Yehova pofuna kumvera iye, pamenepo padzakhala kulemera kwa Nzeru ya Mulungu kudzavumbulutsidwa kwa ife.

KUFUNAFUNA MAWU

Tsopano makhoza kudabwa kuona kuti zinthu zina zomwe inu mukuzitcha kukhudzika simungathe kuzifotokoza ine zimandichitira. Pamachitidwe ngati amenewa amangofuna kuti lumikiza ife ndi Mulungu pamene tikukula muzinthu zimenezi? Kodi ife tiyenerabe kukhumudwa ndi kunyinyirika ngati opusa mpakana titapeza chomwe tikufuna.

Chomwe ndikufuna kunena pano n’chakuti ndikudziwa anthu omwe akuchita bwino kwambiri kuposa zaka zisanu ndi chimodzi kapenanso zisanu ndi zitatu zapitazo pakuvetsetsa zauzimu “pofotokoza zomwe timamva” makamaka pomvetsa za mawu a Mulungu amene amatha kuyankhapo pa zomwe kale lonse sitimazimvetsa. Anthu ngati amene ndawatchula pamwambapa amatha kuika mawu a Mulungu muntchito koposa kungomva mawu a Mulungu. Izi zimachitika ndi kupita kwa nthawi. Komanso izi zizitanthauza kuti nthawi zonse ungathe kumva ndi kudziwa chifukwa chiani. chifukwa chiani Abrahamu adasiya makolo ake, dziko la makolo ake, ndikupita m’chipululu?. Isadafufuze m’mene amapita izi sizitanthauza kuti iye sadali wauzimu kwambiri. Iye sakadatha kukhala wauzimu m’dziko la Ur kuti akadziwe chomwe chidzachitike. Atate sadamuuze kuti ndi kwakuti kwakuti. Iye adangonena “upite, osafotokoza kwakuti kwakuti, ine sindikuuza chifukwa chakuti koma iwe upite.” Iye adali ndi chiphinjo cha Uzimu chomwe chidamupangitsa kuti apite.

Nthawi zambiri, ngakhale Mulungu sakhala malingaliro omveka bwino. Koma Yesu adanenapo kuti, ine ndikuuzani chifukwa ndinu abwezi anga” (Yohane 15). Pamene ife tidzakhale pa chiyanjano chabwino ndi Yesu, ndi pamene iye adzayambe kutiuza ife za zolinga zake (mapulani ake) osati iye angachite chabe, iye adzatiuza chifukwa chomwe akuchitira chinthucho. Pamene chiyanjano chathu chikadzakula, tidzatha kudziwa nthawi zambiri zomwe chotikhudzacho chilili ndi chifukwa chake. Nthawi zambiri osati nthawi zonse.

Ndipo kukachitika kuti tonse tagwirira ntchito limodzi ndipo kulakwitsa kwapezeka ndikugwa pansi nkhope zathu, zili bwino. Nthawi zambiri Mulungu amasangalatsidwa ndi mtima wathu. Iye amafuna ife kuti tifanane ndi chifanizidwe cha mwana wake Yesu.

*Zinthu izi ndizofunika kwambiri. Kunena zoona, anthu ambiri omwe zimawakhudza amakhala ndi kudziwa kuchulukira kwa zomwe zimachitika pa mpingo pa dziko lonse lapansi ndi pazomwe anthu ambiri amakonda kuchita zomwe zimadabwitsa anthu ndikukhala ndi mafunso. Iwo amachita zomwe amafuna munthawi yomwe akufuna, pachifukwa chomwe akufunira chinthuchi. Palibe munthu amakwanitsa kuwafunsa iwo mafunso pa zomwe iwo akuchitira izo. Nthawi zambiri kumaoneka kuti kumakhala kovuta pamene munthu ali ndi kukhudzika kulankhula za chinthuchi kw ana, apamoyo wathu, pachisankho chathu, pa zinthu zomwe tilinazo. Ndi anthu owerengeka okha omwe amatha kulankhula za muzu wa moyowawo chomwe chilli madalitso omwe ali a mtengo wapatali omwe ali nawo anthu owerengeka okha. Thokoza Mulungu ngati uli nawo mdalitso umenewu. Pamenepo padzakhala “kuunika” kochuluka. (Yohane 3, 1 Yohane 1).

Chinthu ichi chimakhala chovuta ngati anthu okuzungulira ali osamalira moyo wanu mwa Yesu. (2 Timoteo 3: 16-17), koma njira ina yake yomwe ingakhalepo ikhoza kukhala yoopsa ndi yopanda pake.(Aheberi 3:12—14).

Komabe, m’dalitso wapaderawu umachita zinthunso zachilendo. Mwachitsanzo, funso lomwe tikukambirana m’bukuli limagwira ntchito kwa anthu ochepa okha padziko lapansi lino. Anthu ambiri zakhala ndi kukhudzika kwa chinthu china chake pamoyo wawo. Ndipo akakhala ndi kukhudzika ndi anthu ochepa chabe omwe angawafotokozere za kukhudzika kwawo ndi anthuwo omwe angakhale ndi kukhudzidwa kosiyana ndi kwawo. Anthu ambiri monga ndikunenera amakhala omvetsa chisoni mtima wanga chifukwa sakhala ndi kukhudzika koma malingaliro chabe a mumtima mwawo, anthu amtundu ngati umenewu amakhala osamangika m’mawu a Mulungu pachiyambi chawo cha moyo wawo.

ZINTHU ZOFUNIKA PAMENE TIKUMVERA MULUNGU PAMODZI

Inu muyenera kudziwa, kuti pali zinthu zambiri zofunika kuti izi tikukambirana zikhale zofunika. Muyenera kuonetsetsa kuti moyo wanu wamangika pa mawu a Mulungu koposa pa malingaliro anu okha ndi zokhumba—izi zimakhala zosowa. Muyeneranso kumangika pamodzi ndi anthu ena tsiku ndi tsiku pamene patchedwa lero—izinso nzosowa.

Inu muyenera kumangika mwakuti moyo wanu uyenera kukhala buku lotseguka kwa anthu otizungulira ife. Muyenera kufuna ndi mtima wanu onse, kuti Yesu akakwezedwe m’moyo mwanu komanso pa mpingo wake, posaopa zomwe zinthuzo zidzatikhalire mtengo tsiku lina. Zinthu zonsezi ziyenera kuchitika pofuna kudziwa bwino za kukhudzika komwe tili nako kuti kukhale komveka bwino nthawi zonse.

KODI NDI MAWU AYANI OMWE INE NDI KUMVETSERA?

Nthawi zina zimatha kutheka kuti “kukhudzika” komwe inu mukunena kuti Mulungu ndiye wabweretsa pa moyo wanu mwina kwachokera m’thupi chabe osati kwa Mulungu. Kufuna kudziwa zoona zenizeni za zimenezi kumatheka ife tikapitiriza kukula mu umunthu wa Yesu Khristu! Taganizirani inuyo mutakhala ndi chinthu chomwe mungachitche kukhudzika m’malo mwake. Ine ndingathe kukufunsani kuti kodi kukhudzika komwe inu muli nako kwachokera kwa Mulungu kapena kwa Thupi lanu. Inu n’kuyankha kuti muli otseguka kwa zotsatira zake za chinthu chomwe mukuchita kuti kukhudzikako, koma simukuganiza choncho.”

Nthawi zina zikhoza kuoneka kuti ine ndili ndi machenjerero omwe sindifuna anzanga adziwe chifukwa ndikhala kuti akhoza kukhala chotchinga kuposa monga momwe umadziwira, uku ndiko timakutcha umunthu osati uzimu weniweni ayi. Komanso kupitirira apo kusamvetsa m’mene zinthu zili koma ngati ndingazipereke kwanthunthu kwa wina ndi mmnzake poopa kuti ndingaphwanye ufulu wa chomwe inuyo mukuchita chokukhudzani (kapena chomwe mukuchitcha mukuganiza kuti ndi chokhudzika chanu) koma ine ndiyenera kuti ndisakutsutseni paka patsogolo pake mudzathe kuzindikira za kukhudzika kwanu komanso mudzathe kuona kuipa kwa zipatso zake.

Chinthu chomwe mumachitcha kale lonse kuti chokhudzika chanu chikafika pamenepa mumatha kuzindikirz kuti inali thupi lokha basi. Pamapeto pake anzako amakuuza kuti ife timakuuzatu koma iwe siumatimvera wawona izi zachitika. “chabwino, tsopano uyenera kuphunzira kuchokera pa zakuchitikirazi” patsogolo pake ndi pamene umathano kumvetsera Mulungu moyenera.

Kumbukirani zomwe Yesu adalankhula kwa Petulo, “Kodi inu mumanditcha yani ine?” Petulo adayankha, inu ndinu Khristu, mwana wa Mulungu wa moyo.” Yesu adayankha, Simoni Petulo, Atate wanga wa kumwamba ndiye wakuululira ichi iwe. Anthu sanakuvumbulutsire ichi ayi—koma Atate ndiye.”

Taganizirani chinthu chosokoneza mutu ngati ichi/ atangolankhula izi, Petulo adamutengera pambali Yesu kuti akamdzudzule chifukwa cholankhula za imfa yake. Yesu adamuyankha, “Pita kumbuyo kwanga, Satana!” zitangochitika izi, Petulo adasokoneza poganiza kuti akumvera mawu a Mulungu pomwe amamvera mawu a Satana, iye amaganiza kuti akupitirira kumvera Mulungu! Sadathe kudziwa kuti chimene ayenera kuchitsatira ndichiti?

Iyinso inali nthawi yomwe ife ambiri tili makamaka munthawi yathu yoyambirira ndi Mulungu. Uyu adali mbale yemwe adamva liwu la Atate. Yesu adali asananenepo ndi kale lonse kuti ife timazindikira chinthuchi. “munamva Atate ali kulankhula ndiwe Petulo. Ntchito yabwino kwambiri.” Izi sikuti amamumva Mulungu akulankhula momveka ayi koma m’mitima mwake. Komanso Petuloyi samangoganiza chabe koma zenizeni zochitika. Yesu adanena kuti Petulo adamvadi mawu ochokera kwa Atate! Koma patangopita nthawi pang’ono chabe munthu yemwe yemweyo adapezeka akumvera Satana. Yesu adayenera kumuuza iye, “kupita kumbuyo kwa Satana.” Ndizotheka kuti nthawi zina pomwe tikulandira kanthu n’kutheka timalandira ndi waya wa minga yemwe amatikwalula ndikutitulutsa magazi nthawi zina kwa wina ndi mnzake. Zili ngati kuona zinthu ziwiri zikuchitika nthawi imodzi ndiye pamakhala povuta kuti utsatira chiti.

KUGWIRITSA NTCHITO ZINTHU ZA ZOVOMEREZEKA ZA DZIKO LONSE

Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiyenera kuchita mawu a Umulungu. Pomaliza pa buku la Aheberi mutu 5 timawerenga “chakudya cholimba ndi cha okula msinkhu omwe, pakuchitachita kwawo adazolowera ndipo amatha kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Zinthuzi zimachitika ndi Kuzolowera kuchita chinthu Chokhachoka. Kunena kwina, nthawi zina, ngati chisali zinthu choopsa, ine ndikadakonda kuti inu mukadathamanga makaniwo, ngakhale lili umunthu wanu, kuti inunso mukaphunzire, “pochita zinthu zomwe mudazolowera kuzichita nthawi zonse.” Kapenanso ndingofuna kuti muthamange makaniyo, ine ndidzakhala nanu pamodzi pamene inu mudzayambe kupita. Ine ndidzakhala odzipereka kupita ku Yerusalemu” ndi inu, ngakhale ndikudziwiratu kuti mukulakwitsa. Ine ndidakhalapo ndikuonetsa kuti ndikuthandizeni kuti tisanthule chinthuchi chomwe inu muli nacho mumtima mwanu ngati chokukhudzani pamene chinthu china choipa chikachitika, kuti m’malo mwake inu mukaphunzire phunziro zinthu zikalakwika.

“Chabwino, tsopano ndikutha kuona kuipa kwa chiganizo changa. Koma m’mene chimayamba ndindichitira ndimayesa kuti chinali chabwino koma tsopano ayi ndithu ndikutha kuona kuipa kwake.

NGATI SITINGAIME PAMODZI PACHIKHULUPIRIRO TINGATHE KUMWAZIKANA

Kupyolera muchirititsa kwathu kwa kawirikawiri kwa zinthu kungathe kupangitsa ife kuti tidzitha kumva kulankhula kwa Mulungu komanso kulankhula kosachokera kwa Mulungu.

Tiyenera kuzichita izi. izi makamaka zimatheka ukazolowera kuchita zinthuzo. Ine ndi inu timakula bwino mwa Ambuye tikamamvaimva mawu a Mulungu komanso pomwe ine ndatha kuwanitsa kutsutsapo ngati zinthu zili zotero pa zomwe mbale wina anganene kuti ndi chokhudzika chake pomwe ine ndikuti ayi sizili choncho m’malo mwake iwe ngati ulumbikirebe ndiyekuti uthamanga wekha mpikisanowo, ine ayi. Koma ngati ine ndingakuthaweni kukusiyani inu nokha ponena kuti sindikuthandizani chikakuphulikireni nokha, muthamange nokha maknaiwo! “ ine sindidzakhalapo kukuthandizani kuti inu muphunzire pachinthuchi. M’malo mwake inu mudzavutika ndi zotsatira zake komanso nthawi zina makhoza kudzanyengedwa kuti palibe zovuta. Inu simudza phunzira mumayenera kuti muphunzire.

Nthawi zina “umunthu” omwe uli woipa kwambiri, pamene iwe chonsecho umaganiza kuti “utsogozedwa ndi mzimu wa kukhudzika” ngakhale zili choncho, nyengo zina tiuyenera kulingalirapo m’mene tingadziwire komanso m’mene titchotse malingaliro amenewo ngati sitiokhutitsidwa nawo, pamene taona kuti tikulakwitsa.

Koma ngati muli okhutitsidwa ndi kukudzidwa kwanu, kudzayengedwa ndi mawu a Mulungu, osati ndi maganizo athu okha, ine ndikufuna kulemekeza anthu amtundu wotere. Iyi inali nthawi yomwe Paulo adangochoka kwa anthu osakhulupirira pamene amalankhula za kukhudzidwa kwake. Appolo amanyoza kukhudzika kwa Paulo m’ 1 Akorinto 16:12.

Tangolingalirani za zimene mwakanthawi: Paulo adali otsimikiza mtima kuti Appolo adalidi kulondola kuti iye adalidi kuyenera kuchitapo kanthu ndithu. Kodi Paulo adachitapo chiani pa kusiyana kwa kukhudzika kwake ndi Appolo? Ngakhale Paulo adalimbikira kukana komabe kulolerana kunalipobe ndi abale ake pamene iwo amafuna kudziwa m’mene angachitire mwa Yesu. Machitidwe amenewa ndipo timawatcha kuti umodzi. Umodziwu umatithandiza ife kuti tithe kugwirira ntchito pamodzi pophunzira pa zomwe tidazizolowera kuzichita kumvera mawu ake a Mulungu.

Ngati kukhudzika kwanga kungakhale koona pamene kwa ndingokunyalanyaza ndikukuuzani, “ndinakuuzani ine.”

Ine sindikuyenera kuchita motero, ndikuyenera kukuthandizani kuti muone ndi kuphunzira pa zomwe adachita. Ndiyenera kufotokoza kuti chifukwa chiani ine ndinachita motero sichinthu cha munthu modzi yekha koma cha pagulu kuchitira limodzi. Izi sizililira kuti ayi aliyense m’mene angayendere ndi Mulungu payekha ayi. Koma tonse pamodzi kumvera kukulankhula kwa Mulungu—iwe uchite zako ine ndichite zanga.

Pamodzi tonse tiyenera kumva kulankhula kwa Mulungu. Pamodzi tonse ngati gulu tiyenera kukhala odzipereka tonse pamodzi ngati tikufuna kumvera kulankhula kwa Mulungu momveka bwino.

“Ndidzamanga MPINGO wanga omwe makolo a ku gahena sadzaulaka .”

“MPINGO umene uli Mzati ndi maziko a choonadi.”

“Pamene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndili pomwepo”.

“Pamodzi, ndi oyera mtima onse……”

“Yesu mwa inu —chiyembekezo ya ulemerelo.”

M’KALASI NDI M’MALO OMWE AMAFUFUZIRAPO ZINTHU ZOSIYANASIYANA ZA SAYANSI: LABORATORY)

Nthawi zina ziyenera kukhaladi choncho kuti Mulungu ayenera kutenga maphunziro owoneka ngati akulakwisa. Mwina mwake abale okondedwa inunso mudali m’njira imeneyi. Ndipo mudaone zomwe zimabwera kutsogoloko, koma simudalankhule kanthu. Mumangoona ndi kupemphera, mudangolimba mtima kuti ngati anthu omwe amachita maphunziro amene inuyo mumatenga akagwa mayesero inunso mugwanawo limodzi. Nthawi zina zimachitika kuti mbale kapena mlongo amatha kukhala ndi machitidwe achinsinsi pa zochita zake izi zimakhala zoopsa iwo satha kuona zotsatira zake. Zinthu zikakhala choncho inuyo ponyani thupi lanu kutsogolo kwanjira ndikuwaitana kuti aganizire. Ndi zinthu zina zotsatira zake sizikhala zabwino, choncho mungawaphunzitse kupyolera mnjira yovuta. Koma inu abale onetsetsani kuti muli pafupi nawo abale amtundu wotere pofuna kuwathandiza kuti achite bwino pakukhudzika kwao komwe

Koma abale izi sizitanthauza kuti pali njira imodzi yokha yomwe munthu angaphunzirire makhalidwe abwino a Yesu Khristu, kapenanso njira ina. Mulungu, m’nzeru zake amagwiritsa zinthu zosiyasiyana zolumikizika pamodzi kuphunzitsa komanso kutiyeretsa ife. Ukamaphunzira zokhudzana ndi kapangidwe ka makhwala, mwachitsanzo, kuphunzira kwambiri kumachokera kumaphunziro amene timaphunzira komano tikafika mu Laboratories, ndi pamene munthu amayamba kugwira zinthu zosiyanasiyana monga Bunsen burners ndi pipettes. Apa ndi pomwe munthu umayamba kuona zinthu zija umaphunzira m’kalasi. Zimakhalano zinthu zochitiks zenizeni.

Kodi izi sizimatanthauza kuto sipafunikanso “maphunziro kaya chidzudzulo ayi?” Chabwino, tikabweranso pachifaniziro chathu cha phunziro lopanda mankhwala (chemistry) siungathe munthu kulimvetsa thandauzo la (chemistry) ngati ungakhale chabe osachitapo kanthu. Ifeyo sitikuyenera kuopa kuphunzitsa munthu wina wake zomwe Yesu adaphunzitsa kukhudzana ndi zinthu zina, koma muyenera kudziwika kuti pali “Laboraties.”

Izi sizitanthauza kuti tiyenera kukhazikitsa laboratory. Koma kuti zoonadi zake ndi zakuti aliyense ayenera agwire ntchito yake kupyolera m’laboratory ngati tikufuna zoonadi pamoyo wathu. Pamene tikuphunzira kwambiri, pomweponso moyo wathu umakhala ukukonzeka, pomwepo tidzakhala osamala kuti chitini chomwe tikugwiritsira ntchito m’labmo chitsaotche. Sichinthu choyenera kuti aliyense aphunzire chimene akuchimva ngati chokhudzika chake m’njira yowawa. Koma zonsezi chifukwa choti ine sindinafune kumufotokozera mbaleyo. Chonsecho ndikanatha kutero.

KUKHULUPIRIRANA KOCHOKERA MUCHIYANJANO CHAWO

Izi zikutibweretsanso pang’ono kunkhani ya Luka ndi Agabus. Iwo adali ndi kukhudzika kuti Paulo asapite ku yerusalemu. Ngakhale zinali choncho, m’malo mwake iwo sakadalora kuti kukhudzika kwao kupose kukhudzika kwa Paulo. Kodi izi zikuchokera kuti? “Kodi zinali zamphamvu kwambiri” uthenga wawo unali wakuti, ? Woona maonekedwe ake a munthu, kapena amayimba nyimbo, kapena owumiriza? Ayi ndithu!!! Mphamvu yawo poyenda ndi iye sadamvetse kapena kugwirizana nazo pamene akakwera nakulira limodzi pomudziwa iye osati pongotengera mphekesera ya kuyenda kwake kwa Paulo ndi Mulungu. Iye adakhala pakati pawo ngati Tate, mbale, mayi wawo—usiku ndi usana ndi kulira ndi misozi.”

Izi zikusiyiraniratu ndi zomwe zikumachitika masiku ano pomwe azibusa ali mabwana, odzikudza. Iye adalidi munthu wa Mulungu, “pakati pawo ngati mtumiki.” Iwo adamudziwa iye. (1 Atesalomika 1:2—12).

Ngakhale tidamva zowawa koma timalimbika mtima kulankhula uthenga wabwino wa Mulungu, vs3, pakuti kudandaula kwathu sikuchokera kukusochera, kapena kuchidetso, kapena m’chinyengo, tikufuna kusangalatsa Mulungu osti anthu chifukwa Mulungu amayesa mitima yathu. Pakuti sitinayenda nawo mawu a Mulungu osyasyalika nthawi zonse monga mudziwa, kapena kupsyinjira msiriro, mboni ndi Mulungu. Ngati atumwi ake a Yesu Khristu sitinakhale chipsinjo pakati pano, koma tinaonetsera kufatsa konse ngati muja achitira mayi akamafukata mwana wache, kotero ife poliralira inu, tinavomereza mokondwera kupereka kwa inu si uthenga wabwino wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife. Kumbukirani abale chigwiritso chathu ndi chivuto chathu, pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu. Inu abale ndinu mboni za zimenezi komanso Mulungu ndi mboni. Ife tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira.”

Abale pankhani yomwe ija ya Luka ndi Agabus akadalimbikira nkunena kuti “ayi nzotheka! Ine sindisamala kuti kaya ine Paulo ndiwe wamkulu kapena ayi koma chomwe tingakuuze n’chakuti ndiwe olakwa! Izi zikadasonyezeratu poyera kuti iwo akanakhala odzikonda pa kukhudzika kwawo kuposa kukhudzika kwa Paulo chifukwa cha moyo wache ndi Mulungu. Chimene mumachidziwa ndi moyo wake wa munthu ndi kuyenda kwache ndi Mulungu ndizo zimasonyeza kutsimikizika kwa munthuyo anu. Inuyo makhoza kuwafotokozera anzanu za kukhudzika kwanu makamaka iwo amam’dziwa Yesu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi, koma pamene pali chiyanjano pali kudalirana. Ngati mungawakonde anzanu ndiye kuti mumawadziwanso mayendedwe awo ndi Mulungu, nthawi zina ukhoza kudalira anthu ngati awa kuti akadali olimba mwa Mulungu koma chonsecho adagwa kale pamaso pa Mulungu. Komanso chomwe ndikufuna kukuuzani abale ndi chakuti musalore kuti kukhudzika kwa kuoneka ngati zinthu zosafunikira poyerekeza ndi anzanu ayi.

Apanso, pakuoneka kuti panali amai ndi abale omwe adakanika kumufotokozera Paulo zoti asapite ku Yerusalemu, anthu ngati amenewa lero lino akhoza kutengera mwayi pa mipingo yomwe ilipo.

Chingachitike chiyani ngati Luka kapenanso Agabus angakane kuti, “Ayi, ife sitisamala kuti iwe ndiwe wamphamvu ayi m’malo mwake tikuti, ukachita chinthchi ukhala olakwa!”? Izi zikanationetsa kuti iwo akadadzikonda posafuna kumvera ndi kulemekeza kukhudzika kwa mnzawo Paulo pofuna kuchita zokondweretsa kukhudzika kwawo monganso Paulo pokhala mbale komanso moyo ndi chiyanjano ndi Mulungu.

Chimene umachiziwa pa moyo wake wa munthu ndi kuyenda kwache ndi Mulungu ndizo zomwe zimakupangitsa iwe kutha bwino lomwe m’mene ungayezera kukhudzika kwa munthuyo kupatikizapo malingaliro awo. Komanso inuyo mutha kugawana ndi anzanu zokhudzana ndi zomwe mukumva kuti Mulungu akukulankhulani kuti muzichite, koma chomwe muyenera kuchidziwa ndi ichi pamene pali chiyanjano, pali kudalira. Zikachita kuti ngati munthu / kapena anthu mumawakonda komanso mumadziwa moyo wawo m’mene amayendera ndi Ambuye, mumakhulupirira kuti ali m’manja abwino a Mulungu, ngakhalenso nthawi zina zimachitika kuti munthu yemwe mukumukhulupirirayo adagwa kale m’manja mwa Yehova.

Ndikupemphani abale ndi alongo mwa Ambuye kuti chonde musalore kunyada kapenanso ukhanda ukusokonezeni ndi chikondi pa mnzanu olora nyumba ya Mulungu kuti maganizo anu akhale osafunikira kuposa kukhudzika kwa mnzayo.

Nthawi zina, kutengwa kwa abale ndi alongo omwe adamulankhulapo Paulo n’kulephera kuti asapite ku Yerusalemu, akhoza kutengerapo mwayi ngati m’mene angadzachitire ambiri ife akhristu amakono.

Iwo adakhala nthawi yaitali pamodzi ndi Paulo. (ine ngati ndikuyenda ndi mbale yemwe ali munthawi yoyesedwa koma ndi mbale okhulupirika mwa Ambuye, ndiye kuti iye ali mayesero a moto pachiyanjano chake ndi Mulungu ndiye ine ndiyenera kusamudziwa munthuyo monga mwa umunthu, koma zomwe ndiyenera kudziwa ndiko kukhulupirira iye amene sindimudziwa monga mwa umunthu) komanso m’mene zili zinthu m’mipingo yathu masiku ano anthu samadziwana wina ndi mnzake. Iwo akalemba zolankhula zake, kugula makaseti ake a nyimbo, ulaliki, kapenanso akawerenga Buku lake la munthuyo kapenanso kupemphera naye limodzi m’mipingo umodzi tsiku la Mulungu m’mawa. Izi ndi zina zomwe Mulungu akufuna inu ngati mukufuna kukhala omvera iye ndi Mulungu akufuna inu ngati mukufuna kukhala omvera iye ndi kumudziwa mnzanu yemwe mumapemphera nayo:

“Limbikitsanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku pamene patchedwa lero kuti wina angaumitsidwe ndi machenjerero a choipa (uchimo).”

Chinthu tangochitchulachi pamwambapa sichichitika m’mpingo yambiri m’dziko lino, masiku ano. Chifukwa cha zimenezi pamakhala povuta kwambiri kudziwa choti achite, m’malo mwake pamakhala povuta kuchita mawu a Mulungu pamoyo wawo moyenera! Tangoyerekezani kuti ine ndakufotokozani kuti mupite “mupite kupyola nyamba zitatu cha kum’mawa ndi kutembenukira kumanja, pitani kubzolani nyumba zingapo motsetsereka chakumusi pang’ono, ndipo mukaime mukafika pamalo pomwe amaimitsira magalimoto (car park)”—koma m’malo mwake inu mwayambira mbali yosiyana ndi komwe ine ndimafumira kuti muyambe m’malo mwake wayamba mbali ina, chilangizo changa sichingakhale cha thandauzo kwenikweni, kodi chikhoza kumveka bwino bwino? N’chifukwa chake zimakhala chimodzimodzi ngati munthu / anthu kamakhala moyo wa uzimu osiyana ndi zomwe “Bible” lifotokozera za chikhristu mu machalitchi ambiri omwe akupezeka mdziko lino, akhristu ambiri satsatira zofunika za chikhristu ndi kuzilumikiza kwao ndi moyo wa anzathu omwe akupezeka m’buku la Machitidwe atumwi mutu 2: 42—47. Ndipo tiyenera kubwerera ku moyo woyambirira wa chikhristu wa m’mene tiyenera kukhalira! Muyenera kudziwa abale kuti mpingo wanu uyenera kuchita chiyanjano chimenechi ndi Yesu komanso wina ndi mnzake mbali zonse za moyo wathu apo bii, tidzafa tikadayesabe kutsatira moyo umenewu.

(Akolose 1:24—2:4) “Tsopano ndili okondwa chifukwa chiphinjo chomwe inu mumachiyesa, ndipo ndikwanitsa zoperewera za chitsautso cha Yesu Khristu m’thupi langa chifukwa cha thupi lache, ndilo Eklesiayo; amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwanitsa mawu a Mulungu, ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ache, kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene ciri chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero; amene timalalikira ife ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense wamphumphu mwa Yesu Khristu: kuchita ichi ndidzivuta monga mwa machitidwe ache akuchita mwa ine ndi mphamvu. Ichi ndinena, kuti munthu asakusocheretseni ndi mawu okopakopa.”

(Agalatiya 4:19) “Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu kufikira khristu aumnika mwa inu. Koma bwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mawu anga; chifukwa ndisikhasinkha nanu.”

Ndi zoonadi kuti abalewo ankamudziwa kwambiri moyo wake Paulo. Iye adali kutengapo mbali (yambiri) yaikulu m’’moyo mwawo. Iye amapezeka mnyumba zawo nthawi zambiri. Iye adali mbali ya banja lawo la uzimu. Werengani Aroma mutu 16: “Mayi uyu anali ngati mayi wanga kwa ine.” Pali anthu ambiri omwe inuyo simunawamve akuutchulidwa m’buku la Machitidwe Atumwi. “Munthu uyu adagwira ntchito zolimba ndi ine ngati ogwira ntgchito limodfzi ndi ine.” Iye adafuna kutaya moyo wake chifukwa cha ine.” Mn’thawi ngati iye n’kuti buku la Aroma idali itangolembedwa kumene pafupifupi theka lokha pa mfundo munkhaniyi ndi iyi: Paulo adali osalakwa pamoyo wake, makamaka tikamanena ngati munthu yemwe amatunikira. “pamene abalewo amanena kuti akuuziwa moyo wake Paulo iwo amatathauza zenizeni za zimenezo amaudziwadi moyo wake! iwo adali ndi mwayi omwe uli osowa mako anu chifukwa zomwe zimachitika nthawi zambiri ingakhale anthu omwe aliyense amawadziwa bwino lomwe kuti moyo wawo ndi oongoka pamaso pa Mulungu pamakhala povuta kukhulupirira zomwe Mulungu akuti akuwalanhkulazo.” Ayi tayesani kuchita monga iwo adachitira, anthu masiku ano akhoza kunena, Aah, anthu awa ndi opanda pache amangokhulupirira zomwe wina aliyense anganene.” Chabwino, nthawi zina zikhoza kutheka kuti chifukwa ulibe chiyanjano ndi munthu aliyense, apa ndichachidziwikire kuti mfundo yanu ikhoza kukhala yonena kuti anthu awa ndi opanda uzimu amangokhulupirira zili zonse zomwe munthu anena kuchokera paguwa, chifukwa unganere zonsezi chikhoza kukhala kuti iweyo ulibe chiyanjano cholumikizika pamodzi ndi anthuwo cvhomwe chimabwera chifukwa chakuyanjana kwao kwa tsiku ndi tsiku pomwe patchedwa lero. “Kudandaulirana wina ndi mnzake pomwe patchedwa lero.” Monga m’mene Mulungu adanenera. Inu mukakhala ndi chiyanjano, dziko lonse limasinthika ndipo zinthu zonse tafotokoza pamwambapa zidzayamba kukhala zomveka kwa inu!

MULUNGU NDIWOPAMBANA NTHAWI ZONSE!

Pambali pomukhulupirira Paulo, iwo amakhulupiriranso Mulungu. Iwo adaona kuti moyo wake wa paulo Mulungu adausankha kuti agwire nawo ntchito.

Iwo adadziwa kuti ngakhale Paulo adachita kusokonezeka ngati uku koma zidzakhalabe bwino. Apa abale pakhoza kutiuzanso kuti kapena Paulo adali ndi chinsinsi chofuna kudzakhala m’modzi mwa anthu ophedwa chifukwa cha dzina la Yesu koma iye ponena chilungamo sadathe kuona zimenezi.

Koma anzakewo adatha kuona mtima wake wa Paulo kuti unali wangwiro, pachifukwa chimenechi, iwo adadalira Mulungu. Izi sizikuthandauza kuti iwo adali kukhulupirira Paulo ngati munthu opanda chilema ayi koma (iye adali ndi mbiri yabwino pa zinthu zambiri). Koma zomwe adachita zidapitirira malankhulidwe amenewa.

Iwo adapitirira kunena kuti, “mukudziwa abale inu, ngakhale kuti chinthuchi chikuoneka kuti Paulo akulakwitsa ndiye kuti akulakwitsa patatha za 25), ine ndikukhulupirira kuti mtima wake ndi wangwiro ndipo ndikukhulupirira Mulungu pachinthuchi.” Izi sizikunena kuti iwo adamudalira Paulo kotheratu ayi m’malo mwake adadalira Mulungu, koma amamudziwa Paulo makamaka mtima wake kuti udali wangwiro. Choncho, ngakhale kuti zikanakhala kulakwitsa kwakukulu iwo wonse pamodzi adaphunzurirapo pamenepa. Kudalira Mulungu ndiko kudachulukira kuposa kudalira Paulo, ngakhale adachita chinthuchi chifukwa moyo wake wa Paulo.

Tsopano, ngati zingachitike kuti simukudalira munthu chifukwa cha mbiri yache yabwino izi zikadakhala zovutirapo. Ngati tsiku lina mudamuonapo munthuyo akupitirira kulakwira Yesu, kumupereka Mulungu ndi munthu kawiri kawiri pakadakhala povuta kukhulupirira.

Inu abale mukadatha bwanji kukhulupirira Mulungu ngati mbaleyo mayendedwe ake adali osalungama pamaso pa Mulungu, pochita machimo ndi kudzikonda? Izi zikadakhala zovutirapo kwambiri. “Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” Iwo adadziwa kuti Paulo amamukonda Mulungu ndi moyo wake wonse udali pa chifuno chake cha iye ( Mulungu). Ngakhale izi zimaoneka ngati kulakwitsa, Mulungu akadatha kuzipangitsa kuti zikhale bwino. Pokha pokha zinthu ziwiri tazitchula pamwambapa zilipo (kudalira Mulungu, kudalira Paulo chifukwa cha Moyo wake wangwiro). Koma kuti zikachitka kuti moyo wake wa mbale yemwe inuyo mumamudziwa uli wokaikitsa komanso palibe umbino wina uli wonse kuti amakonda Mulungu komanso adaitanidwa ndi cholinga cha Mulungu, zimakhala zovuta kuti Mulungu angazisinthe zinthu za mtundu ngati uwu kukhala zabwino.

YEMBEKEZA KULIMBANA KWA UZIMU

“Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife; koma kudatero kuti kudziwike kuti Sali onse a ife.” Nthawi zambiri padzakhala “munga m’thupi,” Iwo akunyoza kuunika (1 Yohane 1, Yohane 3). Iwo odana ndi kuunika? Iwo amene anakhala ndi mafunso pa zonse zotchedwa chipembedzo komanso iwo amene amapembedza monga mwa dziko lapansi namakonda zinthu za dziko lapansi kuposera apo anthu ofunda, opeza phindu ndi dzina.

Iwo angathe kudya mwansangala pamaphwando anu koma mapeto ake angathe kukubaya kumbuyo ngati mpata ungapezeke wakutero. Zonsezi n’chifukwa chakuti sadapereke moyo wawo mwatunthu kwa Yesu komanso kwa anthu ena (zinthu zofanirapo ndi zimenezi,—1 Yohane 4:20), Iwo adamanga maziko awo pamchenga. Iwo sakadatha kufotokoza za chikondi ndi mphamvu yomwe Agabus ndi Luka adali nayo yomwe adaonetsa kwa Paulo. Iwo sakadatha kugwirira limodzi ntchito ngati mbale ndi mbale ayi.

Koma anzathuwa sadalozana zala (koma adapitirira ndi kulolerana pautumiki wawo”) kunena mwauzimu. Padasowekera mphamvu ina yowapangitsa kuti athe kuzindikira thupi la Yesu” n’chifukwa chake amamuweruza Paulo kuti zomwe adamuchenjeza Paulozo zidzachitika.

Shimei adali munthu yemwe zimamutengerapo nthawi kuti ayambe kukhulupirira (Mulungu nthawi zambiri amafuna kulola zinthu zina zomwe zili zovuta kuti zichitike, komanso kulora anthu ngati Yane ndi Yambule kuchita “zodabwitsa” pa nthawi yochepa mosiyana ndi dongosolo la Yehova ndicholinga kuti ayeretse chikhalidwe chathu!). koma pamapeto pa zonse, adzayeneras kuyala gome yodyera kwa okhulupirika ake, pamaso pa adani awo. Khalani ndi Yesu ndi njira zake, posadera kwawa za anthu komanso ziwanda za kugahena, iye adzakutetezani m’nthawi yake.

KUMUFUNA MULUNGU PAZOVUTA:

Monga mbuyomu yikambirana zokhudza abale omwe amayesetsa kuti apeze mayankho kuchokera kumtima wa Mulungu pakakhala zovuta pakati pawo. Mukuona kuti chikanachitika n’chiyani ngati chonsecho chomwe Agabus ndi anzake akanachita kudali kukana posafuna kumuthandiza Paulo pa chisankho chake? Kodi Paulo akadapitadi ku Yerusalemu, kuchokera pa kukhudzika kwake, posafuna kumvera zomwe anzake adamuuza? Ine ndikuganiza kuti Pauloyo adatha kudikira kwa masiku angapo kusala kudya ndi kupemphera pamodzi ndi anzakewo chisanachitike chomwe chimayembekezeredwa. Iye akadatha ngakhale kusiya kumene ulendeowo ndi cholinga chofuna nkhope ya Mulungu pa zinthu zovutazo.

Ngakhale zinthu zitakhala zokoma bwanji, inuyo abale mukuyenera kudzafika pa zinthu zomwe timazitcha zovuta ngakhale kuti mutamangwirira limodzi ntchito ndi ophunzira oona a Yesu ngati kalipentara. Nthawi zonse padzayenera kupezeka njira zomwe mudzathetsere zovuta zanuzo zokhudza ndi “zomwe mukumva kuti Mulungu akukuuzani.” Mulungu adatipatsa ife zipangizo zosiyanasiyana zogwirira ntchito yothesera kusamvana kumeneku. Ngakhale kuti Agabus ndi gulu lake akadanena kuti sitikulola kupita ku Yerusalemu” pakadapezekabe yankho lothetsera vutoli.

Nthawi zina zimatheka kuti Mulungu amatha kuchita chinthu china chovuta kuchivetsetsa kuti ife m’malo mwake tifanizidwe ku cholinga chake. Izi nthawi zina zimangotengera nthawi ngati ine ndingakwanitse kukhala masiku awiri kusala kudya ndi abale ndidzaphonyana ndi boti ndsipo mapeto ake chinthuchi chidzanditengera mwezi watunthu kuti ndimuke. Kapena tikhoza kunena kuti mwina Mulungu amafuna kuti Paulo adikire mwezi wina asanapite ku Yerusalemu kuti achite ntchito ina yomwe adayenera kuti ayichite. Choncho zovutazo zidathandizira kuti nthawi izipita mofulumira kuti chinthucho chichitike. Ichi chikhoza kukhala chinthu chomwe chingapangitse kuti nthawi ikwaniritsidwe.

Ine nthawi zina ndikhoza kukhala ndi kukhudzika kumene kungachokere “pa kalirole.” “Ine NDIKUDZIWA dzuwa limaoneka lalikulu kwambiri likamalowa kuyerekeza masana. Ine ndikhoza kuona ndi maso angawa! Kodi iwe ungandiuze bwanji kuti ndikhulupirire mosiyana ndi m’mene ndimadziwira?!” Nthawi zina, zinthu sizikhala monga m’mene zimaonekera malinga ndi malamulo a Mulungu. Tiyenera kupitirira ndi kusamala konse, ngakhale kuti pamene tikudziwa kumene kuti zinthu zili choncho. Nthawi zina zimakhala kuti Mulungu akufuna kuchita kanthu kena katsopano, posokoneze m’mene timazionera zinthu pofuna kukwaniritsa cholinga chake ndinso nthawi yake. Tiyenera timupatse m’malo ochitira zinthuzi. Ichi ndi chilimbikitso chopangitsa kuti umodzi wa Uzimu usungike, komanso kulumikizika kwa mtendere kukhalepo” pamene tiyesayesa njira zopezera mayankho pa zinthu zosiyanasiyana zomwe Mulungu akutilanhkula ngati zotikhudza,

Ngati ife “tidzalindira pa Ambuye,” padzapezeka yankho izi sizidzangotengera kuti kukhudzika kwakukulu ndikudzapambane poyerekeza ndi kukhudzika kocheperako. Ine ndili nako kukhulupirira konse kuti Nzeru ya Mulungu idzatsegula makomo ena amene sadaganiziridwepo m’buyomu. N “chabwino Paulo, ife titsagana nawe.” Pamenepa padayenera kukhala mayankho omwe kuchokera m’mitima wake wa Mulungu kuti abale ndi alongo akutitsidwe ndi kulumikizidwa ku mutuwo umodziwo. Izi tikukambazi tidzadzifanizira ndi gule wa Cindrella, amene povinidwa mwana wa mfumu wamkazi amayenera kuyenda khomo ndi khomo kufunafuna mwendo m’ufumu onse umene glass loterera lidakayenera kukwana. Izinso zimachitika m’uzimu, pamene ife tifunafuna kupeza chifano cha Mulungu. Paulo adafuna atapita ku Yerusalemu koma sizidakhale bwino ndi anzakewo. Iwo adafuna iye atakhala komanso izi zizidatheke. Kuchokera mukusala kudya ndi kupemphera, polingalira mawu a Mulungu, Agabus ndi Luka ndi Sila ndinso Phillipo, adayankha,” ife tidzapita nawe pamodzi, “Galasi lotereta lija lagweramo m’malo mwake. Tsopano Paulo ayenera kumuka ku Yerusalemu, ndipo abalewo adatsala ali okhutira ndi chidachitikacho.

Kuchokera pa zinthu zomwe ndakhala ndikuzidziwa ndikhoza kunena kuti, ine ndidakhalapo ndi nthawi yovuta yokhulupirira kuti nthawi zina Mulungu amatha kuvutitsa anthu nmgakhale okhulupirika kumene kuti m’malo mwake ayende motsogozedwa ndi Mzimu wa mwana wake. Sizimachitika nthawi zambiri kuti pamakhala paliberetu njira yomwe “galasi loterera” lingakwanire ayi—pamene aliyense angathe kukhutira kuti chifuno cha Mulungu chikuchitika komanso anthuwo sakulimbana ndi Mulungu. Izi sizimatengera ndi gulu liti lomwe lidaganiza moyambirira ayi. Pamapezeka mayankho ena omwe amatibweretsa kumalo a mtendere ndi m’zimu. Tiyenera kulimbikira pachinthuchi nkutheka kuti tikabwera ife muchipinda chosonkhaniramo ife m’menemo tisadaganiziretu kanthu kochita. Koma kutsutsa kwanu pa kukhudzika kwanga ndi kutdutsa kwanga pa kukhudzika ndizo zingatipangitse ife kufunafuna nkhope ya Yehova ndi mtima wake pamodzi.

MAYENDEDWE ACHITIKE POTSOGOZEDWA NDI CHIKONDI

Chinthu chomwe Mulungu akuchichita pa ife “pa kukhudzika kwathu kosokonezeka.” Iye amatisokoneza komanso kutichitsa manyazi kumene kuti ife tifatse (ngati tili omvera)…. Kuti tithe kukhala nako kuona kwabwino pa iye (Mulungu), komanso pa mpingo wake, komanso pa ife tokha.

Ngati mphamvu yathu za uzimu zili zochokera pa maganizo athu okha, komanso zokhumba zathu ngakhaleno umunthu wathu, Mulungu adzapeza njira yofuna kukonzera mitima yathu. Iye chimene adzafune chidzakhala kuti choyamba cha munthu chiyenera kugwa. Koma m’malo mwake ngati zonse tikuchita zikuchokera pa chikondi chomwe tili nacho pa iye (Mulungu) komanso pa chikondi chathu pa wina ndi mnzake, posadzikonda ife tokha, kuyenda kwathu ndi Mulungu kudzapita mtsogolo pochoka ku ulemerero wina kupita ku ulemerero wina.

Tiyenera kukhala anthu omwe nthawi zonse tiyenera kukhala oyika maso athu pa Mulungu ndi kudabwitsa kwache kuti iye akathe kuchotsa kunyada kopezeka mwa ife ngati khalidwe lathu lachibadwidwe—pochokera m’kusiyana kwa kukhudzika pakati pa abale ndi alongo mwa Ambuye.

Inuyo abale ena komanso Mulungu kuti khalidwe la bwino kukumvera abale ena komanso Mulungu kuti khalidwe lamulo likaonetsedwe munzeru ndi m’chidziwitso kuti Mulungu akathe kugwiritsa ntchito kukhudzika kwanu kuti akaphunzitse inu komanso ndikukuyenerezani pa ntchito yake.

ZA ULAMULIRO ZIKUTI BWANJI?

Ichi n’chachidzikire kuti, tonse tiyenera kugwirizana, komanso payenera kukhala zokambirana za m’mene tingachitire ndi “ulamuliro” m’mpingo wa Yesu. Ena amaona ngati chinthchi ndichosafunikira kwenikweni! Uwu ndiwo timautcha Mzimu wa Kola, umene unaloseredwa ndi Yuda m’chipangano chatsopano, ndipo Mzimu umenewu ulipobe pakati pa anthu okhulupirira mpingo ya dziko lino lapansi.

(Yuda 1:10—12) “ Koma zimene samadziwa anazichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi ztzyika. Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m’njira ya Kaini, ndipo

anadziononga m’chisochero cha Balamu chifukwa cha kulipiridwa, natayika m’chitsutsano cha Kore. Iwo ndiwo okhala mawanga pa pamaphwando anu a chikondano pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofa kawiri, yozuka mizu:”

iwo amanena kuti (ngati momwe Paulo ananenera za iwo omwe samaona kufunikira kwa thupi la Yesu” oyenda ngati makanda), “Ine ndine wa Yesu! —sindikufunanso munthu wina koma yesu yekha.” “Tonse tili nawo Mzimu!” adanena choncho Kora wa make dzana, masiku ano.” Awa ndi maganizo oipa. Izi sizingakhalire bwino munthu yemwe ali ndi malingaliro oipa oterewa, izi zidzaonetsa kuunika mtima komanso moyo wa Mesaya.

Zikuoneka kuti anthu ambiri akhala akuopa komanso kuphimbika kumaso ndi zinthu zokhala ngati za uzimu zoopseza za anthu omwe amazitcha okha anthu a Mulungu omwe nthawi zambiri amangoopseza akhristu awo powauza kuti, “usakhudze odzodzedwa wake wa Mulungu!” Amalephera kupeza Mulungu okha ndiye mmalo mwake amangoloweza zinthu zimene mu mpingo ya anthu. Koma ndili ndi chiyembekezo ndipo chilipo. Tiyamike Mulungu wathu pali machitidwe amene anatimasula ife kuti tipeze Yesu mu thupi lake monga pakati pa Yesu ndi anthu wamba.

Zina mwa zinthu izi zimene tingapezere Mulungu zili mu bukhu lotchedwa ulamuliro wa uzimu lolembedwa ndi W. Nee angakhale kuti sindinakhale kumbali ya zolembedwa mu bukhuli, ndili kudziwa kuti pali otsatira ambiri a Ambuye amene anawelenga ndi kunena kuti ndi labwino kuti zimatsegula maso ku zinthu izi. onani ndipo mupeze malo ngati mukufuna kuti zimene ndikunenazi zikhale za kuya.

Mu kalata yotsatilayi ndikhulupililanso kuti kubweletsani inu kuzama mukudziwa moyo wa yesu limene ndinene mu “ulamuliro” linalembedwa ndi munthu kulembera anyamata achichepele amene anali pamodzi kufuna kupeza Yesu mu gulu anthu apembedza amene amamenya khoma ndipo anali kufuna kudziwa za tsogolo lawo pamene amapeza mayankho ku mafunso pamodzi. Kodi ulamuliro ndi chiani? ndipo ndi kutumiza kalata iyi kuchokera kwa munthu kupita kw abale monganso zokulimbikitsa pa ulendo wautali umenewu.

. . . . . . . . . .

January 14,1995

Kwa abale, anzanga, okondedwa, ndi alongo apamtima wanga omwe kuchokera kwa iwo zokhudzana ndi Yesu zidabwera pamoyo wanga.

Ine ndili nacho chikhulupiriro kuti malingaliro awa akudalitsani ndithu. Ndipemphero langa lakukhutira konse kwa mtima wanga. Inu mwakhala dalitso kwa ine zomwe ndikulephera kufotokoza ndi (kulankhula) Mulungu yekha akudziwa m’mene inu abale mwathandizira moyo wanga, ndipo pamene ndalephera kubwezera motere kwapang’ono kwa mseri, adzakwanitsa kupeleka mphoto kwa inu yochuluka, kukudzumuka, pansi ndikuyendela ponse kudzadza mumanja anu—ndipo zidzandisangalatsa inenso kwambiri!

Posachedwapa ambiri aife tinalemetsedwa ndi mafunso a ulamuliro wa uzimu ndi kudzipeleka, ndiponso lina lokhudza malingaliro ndi kukhudzidwa kwa pagulu mu mau ena, ndi nthawi yanji pamene ine pandekha ndimasiya malingaliro anga ndi kutsatira kukhudzika kwa munthu wina kuti ndi kofunika? Ndingatani ndi kuchengeta kumene Paulo amanena kumvelana wina ndi mzake mwa Kristo. Ndipati pamene izi zimanenera pa Aroma 14 zinthu zina zimene zili zofunika kudziwika ine ndi Mulungu?

Iwo amachiona chinthuchi chovuta kwambiri kupeza Yesu yekha pakati pa anthu odzitcha okha anthu a Mulungu omwe nthawi zambiri amakonza ziphunzitso m’mipingo yomwe ikupezeka m’dziko lino lapansi. Kunena zoona pali chiyembekezo! Ndipo chiyembekezo chilipobe. Pa chinthu ichi tiyenera kumtamanda Mulungu. Pali chiyembekezo choti masula ife tonse kuti timupeze Yesu mu thupi lake, monga m’mene amafunira, koposa kotani kuti ife tikhale osinkhasinkha za m’mene tingasankhire pakati pa yesu ndi gulu la anthu wamba.

Zina zokhudzana za m’mene mungamvetsetsere za Mulungu ndi njira zake zikupezeka m’buku lina lotchedwa “ulamuliro wa Uzimu” yolembedwa ndi W. Nee. Ngakhale kuti ine ndemwe ndiribe kudziwa kwenikweni chifukwa sindinawelengapo koma ndiri nacho chikhulupiriro kuti bukhuli likhoza kukuthandizani kwambiri. Komanso ndikudziwa kuti otsatira okhulupirira a Ambuye omwe adawerengapo bukhuli adaliyamikira kuti ndi buku lopatsa nzeru pofuna kuona zinthu zonsezi zomwe tikufotokoza pamwambapa. Komanso ngati mungalipeze mnthakuphunzira za zomwe takhala tikukambirana m’bukhumu mozamirapo.

Ndili kubvomeleza kuti muli kudziwa kale ine ndilibe mayankho onse komanso ndi mafunso yonse. Koma ndingofuna kuti tigawe zofunika kuti tipeze choonadi cha Mulungu ndi nzeru ndi ufulu ndi Mtendere yochuluka. Ngati tingachite motero tonse ndidzakuwelengani kuti mudzandithandiza, kamodzi kuti ndidziwe m’mene ndingatsatire zinthu zofunikanzo.

Singozi kuti tili kupeleka mafunso otero panopa zili za thupi ndithu mpaka tsopano takhala okhudzika ndi ife tokha ndi mutuyo. Tiyenera kuti tikhale ndi tcheru pafunso limeneli nthawi zonse. Koma ngati mwana wabadwa pano, mwana wang’ono wa Khristu. Tiyenera kuti tiganizire za kuyang’anira ndikuyankha kulunjika kwa gulu kuchokera kwa mutu.

Ili ndi mtundu wa thupi limene Yesu afuna kuyang’anitsitsa ndi kuyang’anira bwino matupi athu atenga zinthu kuchokera ku bongo ndipo nthawi yomweyo limachita. Nthawi zonse bongo umafuna kukwaniritsa zimene zili zogulitsidwa kuchokera kukuyetsetsa kuchokera ku ziwalo zina. Koma nthawi zina ndimafunitsitsa kuti thupi lonse kuti likwanilitse monga pamodzi. Ngati ndiswera ndi kuyimba nyimbo pa Piano, zimatengera thupi lonse kuti lichite pamodzi. Kodi muli kukhulupirira kuti Yesu anakwanitsa kuchita zodwabwitsa kupumira mphweya kwa mpingo wake.

Musandilweluze ine ai chifukwatu ili ndi funso lofunika kwambiri ngati Yesu Sali kumanga mpingo mwa ife tilibe kanthu kochita monga iye zidzangokhala zosapeleka chiyembekezo chenicheni ndi kungokhumudwitsa ena ngakhalenso kusachitirana bwino wina ndi mzake. Koma ngati Yesu mwini ali kutiitanira kuti tichite ntchito monga thupi ndiye kuti tingachite zina zimene zingabwere.

Mwa zina mwa izi ndi zoti Atate atilengera ife kulunjika mwa kuchita pagulu. Zoona ndi choti amatipatsa ife kuzindikira ena a ife ochepa pa nthawi yake. Koma kuti ena a ife tibvomeleze ndithu kwa anthu ena amapeleka mwai wamphamvu nthawi ndi nthawi. Koma zimatere kwakuchokera kochepa. Mu chipangano chakale Tsraeli linali dziko osati kungokhala anthu payekha—yekha. Pamene iwo amachita aliyense pamene amakwanitsa monga mu bukhu la Oweluza. Chisokonezo chinachitika. Pamene anthu anabvomeleza kwa aneneri a Mulungu panane chitsitsimutso ndi kupeza bwino kwa uzimu. Ndipo mu chipangano chatsopano, ife monga aliyense payekha anali ndi kupeza bwino kopambana podziwa Mulungu ndi kumva Mzimu wake. ndiye nthawi ya Yesu. Aneneri ndi Atumwi oyera amene timawadziwa kuti ali omva motere ndipo tingawelenge kuti anali kutsogozedwa ndi anthu ochepa. Pa nthawi ndi nthawi monga ku Antiokeya. Mzimu onaika padera Paulo ndi Barnaba ku ntchito yapadera dera inali chinthu chimene chinakhudza anthu ambiri—anthu amenewa ali atsogoleri ndiponso aphunzitsi—ndipo mpingo onse pamodzi unawabvomeleza koma kuti zinachokera pamene anthu asanu anali kusala ndi kupemphera. Paulendo wina Mzimu unamusonyeza Paulo mum maloto kuti apite ku makedoniya ndipo anthu onse amene anali naye anatsinikiza kuti Mulungu ali kuwaitanila kuti apite ndi mmene Mulungu amagwilira ntchito.

Pa mau apansiwa ali kundiopsa monganso mmene angakuopseleni inunso. Ndili kukucenjezani kuti sisatiopseze ife ai. Koma kuti tikumane nazo tidzapeleka zitsanzo za atsogoleri ena amene anali osati aumulungu amene sanali kusamala nkhosa zawo ndi kumachita mumachitidwe athu. Muyenera kumaopa atsogoleri anu. Ndipo mumvere ku olamulira wawo komanso kuti musakhudze anthu odzozedwa a Mulungu ndipo tamva nkhani zawo. Ndipo zambiri ndi zoipa ndithu, sindikukaika kuti zina ndi zoona) ndi zoipitsitsa zonsezi ndi kuti Mulungu apelike njira kwa ine ndi banja kuti wina angakwanitse kuyendamo ku kuwala kumeneku.

Thupi la mphamvu limayenera kugwira ntchito kwa wina aliyense kuchokera ku ziwalo zina sikuti tili kunyalanyaza zolembedwa pa Aefenso 4, 1 Akorinto 12 ndi malembo ena. Zochitika, pa moyo tonse pamodzi ndi kuti wina aliyense wa ife kuti tikhale thupi lake la Yesu ndipo kunena kuti dzanja kwa diso sindili kukufuna iwe ndipo sitikukhulupira kuti Yesu angalemekeze Mzimu wa pa yekha kweni kweni. Tidzakhala ndi mphatso ziwili kapena zitatu, kuti tithandize mpingo wonse ndipo ngati sindili olola kulandira mphatso ya ena imene ine ndilibe (ndipo kuti zidzandithandiza ine monga ana anga) ndipo zidzakhala bwino.

Ndikukhulupilira kuti tachita bwino ndithu pokhulupilira ena ndiponso ndi kukonzeka kulandira zobvala wina ndi mzake. Pazaka zapitazi ndakhala ndili pansi ndithu kuti ndi khulupirire wina ndi kumulandira mmoyo mwanga. Koma ndiyenera kusintha dzulo lomweli wina wa inu anapeleka chinthu chosakhala bwino pa nkhani ina zokhudza ana anga pa makhalidwe awo. Ndikukondani pa chimenechi—mopitilira angakhale pamenenso anaimba foni, sindine ndekha amene ndikulandira chisamaliro chotere mokhala msinkhu zikuoneka kuti ndi ife tonse.

Panthawi ino pamene tili kukumana ndi zotere zikuthandiza kuti Yesu ali kutikumbatira mtima wake kukuya koposa kale. Ndiye kuti ali mulengi ndi otisamalira, mtsogoleri ndinso oweluza wadziko lapansi ndipo ali kutisamalira ife tonse kwenikweni poonetsa chikondi chake ali kutiitana ife kupita pa ulemerero wina izi sizochititsa mantha ai, Yesu ali ndi matupi amene amamvera iye pamene ali kuchita zinthu, pamene timafukiza. Chiphunzitso chonama ndi mizimu imene imatisocheletsa ife kuchoka mu chifuniro chake. Tingafike mu mulingo ofika mu muyezo woyesa zinthu zonse ndikugwira zabwinozo, ndikukana zina zonse zoipa podziwa kuti zamangidwa kumwamba ndi kumasulidwa. Zilinso tero pansi pano sikuti ndi zoti ndi zololedwa chabe ai.

Ngati pafunso la kuzindikira pagulu ndi kubvomeleza ku thupi ndi nkhani, ndiye kuti zingabweletse thupi la mphamvu polandira. Ndikupeleka kuchokera mwa Kristu zingamubweletse iye matamando. Pali malembo awa Akolose 3:16-17) amene amakamba za moyo pa gulu.

Ndipo Mtendere wa Khristu uchite ufumu mu mitima yanu kulingakonso munaitanidwa mthupi limodzi ndipo khalani akuyamika mau akhristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse ndi kuphunzitsa ndi kuyambililana eni nokha ndi masalimo ndi mayamiko ndi nyimbo za uzimu ndi kuiyimbira ndi chisomo mu mtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachitila mu mau kapena muntchito, chitani zones mdzina la Ambuye Yesu ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.

Ili ndilo thupi limene ndi kulifuna. Mtendere ukhale kuyamika kuchokera pansi pa mtima wamoyo, wochita mau amphamvu ochokera mu kasupe wa moyo amene amalumikizidwa kudzera mu chiphunzitso ndi kuchengetana kuchita mu ulamuliro wa dzina lake. Mbali ya thupi lotere liyenera lolukimikiza mu “Lolani mau a Kristu adzaze mu kuchuluka monga pamene tiphunzitsa ndi kumangililana wina ndi mzake ndi nzeru zakuya. Ziyenela kuchitika kuti tilankhule mau a Yesu mu moyo wa laiyense, kupangitsa kuti akwanilitsidwe molongosoka. Mwa izo ndi zoti m’modzi kapena achepa amalankhula mu moyo wa wina ndi mzake mmodzi kapena ochepa. Koma nthawi zina zimakhudza ochepa kulankhula kwa anthu onse.

Kumbali ya moyo wa thupi, ambiri aife takhala olephera kwenikweni kumbali yoti tigwile ntchito yotere ndipo popitiliza malembo a mu Akolose 2 amanena chifukwa chake. Pambuyo pa abale okhulupirira asamakhale mu malembo a ndime 13—15 ayenera kuti adutsa kudzera mu ndime 1-121 iyi ndi mmene lili.

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu funani zakumwamba kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja la manja la Mulungu lingalilani za kumwamba osati za padziko ai. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu pamene Kristu adzaonelera ndiye moyo wathu pamenepo inunso mudzawonekera pamodzi ndi iye mu ulemerero chifukwa chake fetsani ziwalo zili dziko, dama chidetso chifuniro cha manyazi. Chilakolako, choipa ndi chisiliro chimene chili kupembedza mafano chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana akusamvera zimene munayendamo inunso kale pamene tayani inunso zonsezi mkwiyo, kupsya mtima, dumbo, mwano, zonyasa zotuluka mkamwa mwanu. Musamanamizana wina ndi mzake popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake ndipo munabvala watsopano amene alikukonzeka watsopano kuti akhale nacho chizindikilitso monga mwa chifaniziro cha iye amene anamulenga iye.

Pano pali chinthuci cha mayambidwe a moyo wa ophunzira. Anafa ndi kuuka pamodzi ndi Kristu ndipo analandira watsopano amene al okonzedwanso mu chidziwitso mu chidzalo cha mwini mulengi. Ndipo tsopano pali tsopano kuchoka mu ifa ndikuchoka mu ukapolo wa chimo.

Payenera kuti ophunzira aliyense pagulu wayenda mu maziko amenewa. Kuukitsidwanso kwa mtima ndi kulora chitsimikizo cha ophunzira amenewa palibe aliyense amene angachite monga thupi Sali thupi ungalero kuti ali osakanizilana mgwilizano ndi chiyanjano cha mtima ndi kuunika pamene pali chotupitsa ndipo ndi mtanda wonse.

Funso lonse la Yesu limatengera gulu lonse kuzilakolako monga thupi la anthu osamva ndi obvuta. Ambirir a iwo ali monga atsogoleri ndipo salinso mmanja ndi chitsogozo chake cha Mulungu okhawo amene anaika moyo wawo pansi la gome lansembe kw aYesu. Kutaya machitidwe adziko lapansi ndiyo amene angasese chifuniro chake cha Mulungu mwamva? (Aroma 12) ndipo machitidwe otero monga gulu ndi ngozi yaikulu ngati utsogoleri uli otekeseka anakumana muzitseko zomata ndi kusankha nkhani. Ndikuzipeleka kwa anthu polonjeza zinthu ndi zakuwaopsyeza. Kuwanyengelera ndi kuchita zones mozikondi chisokonezo. Ngati utsogoleri uli wangwiro wotero ndikukhala ndi zokwanilitsidwa za mumtima ndiye kuti adzawamanga anthu ndi malamulo. Zoonetsetsa anzanga ambiri a ife takhalapo mu magulu otere ndi kukhalanso mu utsogoleri otere. Ndipo ndi ife mboni kuti uzimu wokhala osokonekera mu machitidwe otere. Sichifukwa chake kodi kuti zones za uzimu zakhala zosayenda bwino pa ulamuliro ndi kugonjera?

Koma sitiyenera kutero ai, ku moyo wathu wakale ndikulandira watsopano ndikupilira kuphunzira kuyenda moyo obisika wa Yesu mwa Mulungu. Simungathe kuchita chinyengo padzanja la mphamvu ndi kupsinja anthu ena?

Ndiye pali malembo ena mu Akolose 3 pamene palibe Mheleni ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa watchedwa wakunja, mskuti kapolo, mfulu, komati Kristu ndiye zonse ndi zonse.

Pano pakati pa anthu opachikidwa ndi kuuka ndi potheka kuti Kristu achite zones kuti athane ndi zosiyana kuti zither ndi kuchitidwa. Nkhani ya umodzi, kapenanso kulumikizidwa pamodzi pokhala miyala yamoyo ndipo yoikidwa kukhala kachisi woyera mw aAmbuye ndi izinso ndi zofunika kwabasi ngati muli anthu chabe amene magwilidwe ake ndi osalumikizidwa bwino ndiye kuti ndi zobvuta izi ndi zoona pakuonetsedwa ndi kumvera kwa Kristu. Izi ndiye zoyembekezedwa koma nthawi zina sitili otero mungwilizano wathu kwa amene Sali pa umodzi ndi ife. Tili ndi ufulu otero ndi udindo popeleka malangizo kwa ana athu, koma sitingaterenso popeleka ufulu otero kwa iwo amene tangokumana nawo kukogula katundu.

Zanditengela ine nthawi ndidziwe zinthu ngati izi chifukwatu sindinali otero kwa nthawi yaitali zaka zitatu kapena zinai zapitanso ndinali kuwatchula molakwa kuti anali mpingo. Timafuna kuti tikhale amodzi ndipo ndinali okhala odandaula ngati sizingatero Mike Petyers anandiuza ine nthawi ina siya kuti ubweletse anthu pamodzi ndi kuwatcha mkati mwa mpingo ndikuwauza kuti adzikhala moyo wina kweza Yesu ndipo muloleni kuti abweletse anthu kw aiye yekha. Ndipo musalore kuti adandaule ndi kuzungulidwa. Linali langizo labwino koma lobvuta kuti ndilikwanilitse.

Panthawi imeneyo ena ainu mukumbukira banja lina pokhala pamodzi ndi banja lina kuno pamenepo amene anapita ku tauni kwa mwezi umodzi kusiyana ndi ife ndiye tinayetsetsa kuti tithetse chimo lomwe linalipo mu banjamo. Kunali zamwano ndinso malingaliro oipa pamenepo. Kenako mzimayiyo anapita kwawo kwa makolo ake ndiye ndinafunitsitsa kuti aliyense adziwike bwino monga manena mu Mayetu 18 zinthu zotere pa zobvuta zotero. Koma kenanso Mike mbale, anaganiza mwina munthu uyu musamuwelengere ngati mbale pa gulu limeneli simuli ngati mpingo. Choikilapo nyali monga nonse pamodzi ndi moyo zoona ali owerengedwa uchimo kwa Yesu ndinso kwa ena omwewo analakwira, koma ndi oti ayenera kuti aweluzidwe ndi inu monga gulu.

Amakhoza ndithu

Gulu la anthu okhulupilira angakhale kuti ali oyetsetsa kukhala monga Yesu akhonza kusakhala moyo wabwinondikuyetsetsa kupeza Mulungu pa mugwilizano umene ndipo koma ngati pali anthu ena muno mu mzinda mw aife amene alunikizidwa mu dziko la uzimu ndiye kuti moyo wamphamvu udzawonelera. Tidzachita mokongola ngati ana ongobadwa kumene ndiye kkuti tidzafunika chithandizo, koma mwana ndi odabwitsa ndithu pogwira ntchito yotere sichoncho?

Koma zilipo zina

Choncho, monga osankhidwa a Mulungu, woyera ndi wokondedwa, bvalani monga osankhidwa a Mulungu oyera mtima ndi wokondedwa, mtima wachifundo kukoma mtima kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima kulolerana wina ndi mzake ndi kukhulukilana eni okha, ngati wina ali nako chifukwa cha mzake monganso Ambuye anakukhulukilani inu teroni inunso koma koposa izi zones khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

Angakhale mu gulu lomwe laikidwa pamodzi monga mkate payenera ndithu kukhala thupi lamphamvu. Chikondi, popanda palibe kuti tingalumikizike kumgwilizano weniweni umene ungathe kuchita mofunikira kaya ndi nkhani ya mgwilizano ndi kuzindikira pa nkhani ya moyo ndiye kuti tidzakhala ndi mabvuto ambiri.

Masiku apitawo ndinafunsa Mulungu kuti bwanji sindinakhale dalitso kwa ena pa zinthu zimene ndimaona kuti zichitike yankho, mwina ndi lakuti kwa nthawi yaitali ndakhala ndi sakukonda abale angakhale kuti taona chinthu ndimafuna kuti zichitike mu mtima wonyada ndi kuzikonda ndipo sizithandiza wina ali yense.

Koma sichoncho mmene ndikuonera mtima wako! Ndikuona kuchuluka kwa chifundo kukoma mtima kuleza, kuchita ubwino, kudekha, kupilira ndi kukhulukira. Mau amenewa abweletsa moyo wina chifukwa cha kubvomeleza ndiponso kusamalidwa nalandira mu dzanja la chifundo. Ndiyembekeza kuti mwaona mtima wanga uli kusungunuka sichoncho?

Sindingathe kuthandiza koma ndikhulupirira kuti miyoyo yathu yabisika mwa Kristu mwa Mulungu ngati akutimanga ife pamodzi mu dziko la uzimu. Ndipo ngati tikondana wina ndi mzake ndiye kuti tingathe kutenga nkhani iyi ya kulandira ndi kubvomeleza ku chitsogozo cha ife tonse mu njira ya mphamvu.

Kulata iyi ndi yaitali kuposa momwe ndimaganizira koma pali funso linanso limene ndifuna kufunsanso pa nkhani ya utsogoleri wa uzimu ndi kuzipeleka.

Mbali yoti ndi yothekera kukulu mu mutu ndi kufikira muchidzalo pamodzi monga thupi liyenera limangilidwe Aefeso 4 Amati ndi Kristu amene anapatsa ena kukhala Atumwi Alaliki, Abusa ndi ena Aphunzitsi kukonzeletsa anthu a Mulungu ku ntchito kuti thupi la Kristu limangike pamodzi ndipo ntchito ya onsewa ndiye kuti ndi yofunikira. Pali unsembe wa okhulupilira palibe wina wa wamkulu kuposa wina monga mwa chipembedzo.

Koma nsizoona kuti onse ali kugwira ntchito yofanana. Sipali unsembe wa anthu ochita motere. Panthawi ina moyo wa Mulungu kwa ena ndi kubweletsa kupambana kwa onse koma onse akhale mmene zimafunikira ndi chifukwa chake kuti mphatso zinayi kapena zisanu zatchulidwa kupangitsa kuti mphatso zomangilira zimene zili mu mphatso wa Krsitu ku moyo wake.

Pankhani ya utsogoleri wa uzimu ndi pamene zimaonekera mphatso ya mtumwi, kapena mneneri kapena mlaliki kapenanso mbusa / mphunzitsi ndi zoti munthu uyu ali ndi maziko eni—eni. Kapenanso mau ochokera kwa Mulungu, kapenanso polengeza uthenga. Kapenanso kudyetsa gulu, kuti gulu lonse liyenera kulandira ndi kubvomeleza. Opanda atsogoleri anu ndi kuwangonjera ku ulamuliro wawo, zili ndi mu malembo sikuti kuti mumangilidwe pa kulemekeza kwa iwo amene agwira ntchito mwa inu amene ali pamutu panu mwa Ambuye ndiponso amene amakuchengetani asamaleni iwo ndi ulemu wawo mu chikondi ndi ntchito yawo. Mtumiki wa Mulungu sadzakakamiza kuti anthu atsatire iye mu njira yotere koma thupi la Kristu silidzapindula kuchokera kwa iye pokha pokha atalandira mu mtima yotere.

Kupezeka kwa atimtenawo mu thupi la Kristu sizitengela wina kuzofuna ndi udindo kuti ayese zones, kugwilitsa chabwino, ndikukana khalidwe lilonse loipa. “Pakuti awa ndi aneneri onyenga amene ayenera kuyesedwa ndi kukanidwa. Chibvumbulutso 2:2 Awa ndi aneneri onyenga (Mateyu 7:15-23-24:10) amene afuna kuti onyenga ndi alaliki onyenga ndikulalika uthenga wina (Agalatiya 1:6-9) amene ali adani athu. Abusa onama amenewa amene ali ankhalidwe olusa amene afuna kuwononga nkhosa ndikubweletsa ophunzira kwa iwo yokha. (Machitidwe 20:29-30) ndinso aphunzitsi onama (1 Timoteo 5-35 2 Timoteo 4:3-4, 2 Yohane 9, Chibvumbulutso 2:14-26) amene sayenera kupatsidwa malo ndiye tiyenera kuti tiyanganitsitse bwino koma osati motelena kukaikilana komanso mtima wozikonda. Chifukwatu mwina tidzakana opembedza woona ndikhala ndi onama ndikusiya mphatso ya Kristu. Tingathe kugwila ntchito popanda zida zotere. Koma tili ndi mau a Mulungu amene amati sitingafikire ku kukula msinkhu mu chikhulupiriro popanda mndondomeko yotere.

Kuyan’ganitsitsa kwathu sindingoona maonekedwe chabe ai. Tiyenera kuyenda mwachikhulupiriro osati mukuyan’gana. Paulo sanali munthu wabwino konse pamaonekedwe a dziko lapansi. Ndipo atumwi enawo otchukawo; amene iye adanena za iwo ambiri anali athupi ndipo maganizo awo anakana Paulo ndi kubvomeleza amene sanali onekera—ndipo zotsatira zake ndiye kuti chotupitsa chinayamba kukhala mu mpingo wa Akorinto.

Tiyenera kupeza zinthu mu mzimu chikonzero cha Mulungu kwa ife chimene chimabwera kudzera kuthupi mwina zingakhale zosamvetseka ndi popanda nzeru kw aife monga tidzimira moaka tiyang’anire pa mapewa athu ndi kudziwa kuti zili chonchi bwanji. Tiyenera kudziwa kuganiza za moyo wa Kristu kwa wina aliyense pa zimene akulankhula. Tiyenera kukhala ndi funso lokoma la Kristu pakuti ulamuliro kumwamba ndi pansi pano pa Kristu palibenso kwina

Ndikubweletsano kanthu kena kooneka mu machitidwe ndisanamalize. Kodi mudzaudziwa bwanji utsogoleri mu moyo wanu? Tiyenera kuganiza za zimenezi kodi mukufuna kuti akhale wa chuma? Bwenzi othandiza msanga ? wina amene watambasula manja ndikutionetsa moyera koma kuti sitikumudziwa kapena kwa ena amene akhalapo amene tanganizira mneneri ndipo tidzalandira mphatso ya uneneri. Ngati mudzamulandira ngati adziwana chabe ndipo mudzalandira mphatso ya ubwenzi chabe. Ngati mumulandira ngati ubweletsa uthenga ndipo uthenganso mudzalandira, osati kupatsana moyo. Tiyeni tonse tipemphere zamveka?

Ndimaliza pompha kukhala mukristu nthawi zina zinthu zimakhala zobvutilapo. Ndi chikondi chapamwamba chimene Atate aikiza kwa ife tonse kuti titchedwe ana a Mulungu ndiye ndi mmene ife tili.

Kodi sichikondi chodabwitsa, Dan (mbale wochokera ku Ohio)

Tikhale tonse mu pemphero pa zimene zanenedwazi.

Atate, Anthu ndithu ndi osazama monga wa lamulo, ndipo ndikukhulupilira kuti ife tidzakhoza mu gawo limene lili komanso tinalengedwa ochepelala pansi pa angelo koma mukafunitsitsa kupeleka moyo wanu ndi mtima ndi mzimu ndi nzeru kw aife. Mukuchita izi kuti tikakhale olamula pamodzi nanu ngakhalenso kuweluza angelo amene tinalengedwa osafanana nawo. Tikudziwa kuti pali ulendo wautali umene mwatilengelako zinthu izi ndi zofunika kwambiri kuti ife tiphunzire kuti tiyende tonse pamodzi ndi kufikira mu mulingo wina. Sitikufuna kuti pakhale chisokonezo kuti pasakhale ubale weniweni ndi inu ndi kuzindikilanso thupi lanu nthawi yomweyo zinthu zonsezi zidzayendera limodzi mu mtima wathu ndi maganizo athu. Palibe funso loti adzagwira bwanji ntchito ngati ndi osiyana ndi wina. Tithandizeni kuti zinthu izi zitheke pamodzi kuti tingakwanitse kuthandiza ena kuti akayende mu zimenezi.

Atate, musalore kuti ife tikhale osadziwa ndi apamwamba —mwamba. Mumalonjeza kuti mudzatitenga ife malo amene tili woyenerera kuti tikakhale pa mpando wanu wa chifumu ndi inu ndikulamulira mayiko onse sindikumva kukwanitsidwa kuti takwana kale tsopano ai, koma tikhulupirira inu monga mphunzitsi wa mkulu kuti mudzatipatsa ife, kwa wina aliyense wa ife mu mphatso mu njira imene tikudziwa kuti tidzayenda ndi inu mu zinthu zotere mu dziko la uzimu. Ndi mmene ziliri tionetseleni mmene tingagwilire ndi mu mgwilizano ndi inu ndi wina ndi mzake osati mopikisana ai koma aliyense kugwilira ntchito pamodzi ku ulemerero wanu popilira pa zimene mufuna kuti muchite mwa ife. Mwa kufuna kwa mwana wanu ndi ufumu wake.

Ine mwa iye

Mike

Marichi 10, 1999

Monga mwa nthawi zones ngati mufuna thandizo lililonse Lemberani ku mpingo kuno ku Box 68309 Indianapolis Indiana 46268.

© losindikizidwa ndi Kingdom Publishing

Mu chaka cha 1995.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon