Kulondolera Kwa Mtumwi Paulo Podzudzula Akhristu Osokekera

15/4/1986

Palibe angatsutse “kusakhulupirirka” kwa icho. Pakuyesa kubweretsa kukhwima mwa Khristu ngati gulu la anthu ochokera ku Korinto. M’zosatheka. Mzinda uja kunsi kwa Mtsinje wa Anthens umene ndi wodziwika ndi kuledzera kwambiri padziko lonse lapansi. Ndi mpingo wakumeneko. Chabwino……pali kupambana kwakukulu,1 komabe pali zinthu zimene zikusoweka. Tingachite Chiyani?. Nanga Paulo angayankhe bwanji ku nkhani zaku Chloe pakuti zinthu sizinali bwino mumpingo waku Korinto.

Mungamuyankhe bwanji kwa m’bale kapena mlongo amene wakhala mkhristu kwa zaka zochulukirapo-koma adakali ndi vuto la kusakhala pamodzi ndi kudzikonda? Bwanji abale amene akulimbana ndi alongo ndi abale awo, khulupirirani izi kapena ayi kuwatengera ku bwalo lamilandu. Tikuganiza bwanji za iwo amene ali omangidwa mu chiwerewere amene amangokhala osalabadira konse. Mungamuyankhe bwanji m’bale kapena mlongo woteroyo. Osamusamala, kumuthamgitsa, kumubweza ndi kusataya nthawi yanu pachabe.

Paulo, mosakayika, adabwera ndikukhazikika muzothekera zomwezo.

Ndizopindulitsa kumvetsetsa zoona zilizonse zimene Paulo anachita…zinatheka! M’miyezi isanu ndi umodzi ndi isanu ndi inayi atathana ndi vutolo, anawalembera iwo anati, ‘mwanjira iliyonse mwaonetsa kuti ndinu osalakwa, “munali omvera” ndikukunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi” ndipo ndili okondwa kuti ndikhoza kukhala ndi chikhulupiriro chonse mwa inu. (2 Akor.7:11-16). Kumeneko ndikupambana kwakukulu!

Tiyeni tiganizire mopambana utumwi wa Yesu, abambo ndi amayi amene adakali ofooka ndi a miyoyo yopanda mulungu. Komabe, pamene muwerenga ndi kupemphera kudzera mu maganizo kuchokera mu moyo wa mtumwi Paulo, dziwani kuti chinsinsi cha kupambana kwa Paulo sizinali mu “zimene amachita” koma “chimene anali iye” Ndipamene, mupeza kuti muyenera kusintha mmoyo wanu ngati mufuna kukhala chida choyenera kuti Mulungu akachite nanu pakubweretsa chozizwa mmoyo wa munthu wina.

Palibe chilinganizo, koma mphamvu ya Mulungu yokha yotha kulenga kuchokera popanda kanthu, pakubwezeretsa, moyo kuchokera ku imfa. Mnthawi zambiri Mulungu adzalekelera amene mukumupempherera “ndikukuphunzitsani kumvera” Khristu alamula “Lazaro” wanu, kukhala mu fungo loipa laimfa kwa nthawi yaitali-kuonetsera kwakukulu kulephera kwamunthu kuikitsa aliyense kuchokera kumanda. Mulungu akondwa kulemekeza dzina lake pakubwezeretsa mbuyo mwala kutsogolo kwa magalasi othimbilira a m’manda ndi kukwaniritsa zosatheka m’miyoyo yathu. Palibe chilinganizo chamatsenga koma INE NDEKHA. Ntchito yanu ngati mutasankha kuvomera, kuti mtima wanu ukhale njira ya kwa Mulungu wa muyaya ndiponso wa mphamvu.

Ndiye, Kodi ndi otani mtima wa Mtumwi Paulo polimbana abale ndi alongo a liuma?

Chotsani M’Futi Zazikuluzikulu, Chabwino? AlankhuleniI Ndi Mau Amphamvu.

Ndizoonadi kuti Paulo adalimbana kwambiri ndi “aliyense wodzitcha m’bale koma ndiwachiwerewere kapena wadyera, wafano (ntchito, umwini, wamakokondwerero kapena (kapena wopembedza banja), kapena wotonza (“kuchitira zabwino Mulungu pa pakuleka kudzudzula ndi kudandaula). Woledzera kapena woononga chuma “(1Akor. 5:11). Anali ndi khama ndi kudzipereka mu chilungamo cha Mulungu kuti anayenera kuchita molimba mtima: “misonkhano yanu ipanga zoipa koposa zabwino!” (1Akor. 11:17). Inu “Abale, sindinayenera kukuyankhulani ngati mwauzimu koma mwa mau—ana chabe mwa Khristu” (1 Akor.3:1). Iye anali wolimba mtima kutengapo gawo ndikuyankhula motsutsana mkukhala wosamvera ndiponso kukhazikika muumwana. Kufunikira kwanu kwa Mulungu kudzayesedwa ngati muli kapena simuli ofuna kupereka mphotho pakupita patsogolo ndipo osalola abambo ndi amayi kutsitsa dzina la Mulungu La Ulemu, mosalabadira Kuyera kwache ndikungoganiza mwaungwiro. Ngati Paulo m’bale wathu, “munthu ngati ife,” tikhale ndi chikhumbokhumbo chochita nawo. Tsopano tisanalowe kwenikweni mu “za Mzimu Woyera” ” kukweza,” chenjezo”, pakusamala” m’modzim’modzi tsiku ndi tsiku kuti pasakhale kunyengedwa ndi tchimo.” (Heb.3:13,12:15), tikuyenera kusamala poyesa mtima wa Paulo umene anali nawo ku banja lake kwa Akorinto.

Kumbukirani, “inu amene muli mzimu muyenera kubwezeretsa wogwidwa mu uchimo mosamala.” (Gal. 6:1). “Muuzimu” sizikutanthauza kuti ndinu oyenera kuphunzira za Baibulo, kapena kuti anthu anakusankhana kukhala otumikira, kapena kuti mumalalika m’misonkhano (kapena mmisewu), “ndizabwino”. Zikutanthauza kuti mwapita patsogolo munjira zosadutsika pakukhala “pakumangika mubanja lokhala ngati la Mwana)” (Rom. 8:29; 1Cor.2:16). Ndinu ofanana ndi Yesu mu umunthu, kuganiza moyo, pakukhala odekha, moyo wamapemphero, kutumikira kwa abale ndi alongo ndi khalidwe lokonda zinthu. “Ndi m’mene timadziwira kuti tiri mwa Iye: Aliyense amene amakhala mwa Iye ayenera kuyenda ngati m’mene amachitira Yesu” (1John 2:5-6).

Mzimu Woyera ukuti: “Inu amene muli oyera (odzazidwa ndi Mzimu wa Yesu) pakuubwezeretsa.” Mfundo ndiyakuti sikuti mukhale angwiro kuti mukhale ophunzira mwa Yesu. Ndikofunika kuyamba mwayesa mtima wanu, “yambani mwachotsa chitsotso m’maso mwanu” ndipo khalani ndi mtima wakuti Mulungu akhoza kuugwiritsa ntchito pakuchita zozizwitsa kudzera mwa iwo.

Mtima Wa Mtumwi/ Mlangizi

Nawu mtima wa Yesu mu umunthu wotchedwa Paulo, mtima umene Mulungu anaugwiritsa ntchito pakuchita zosatheka.

1) Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni. Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndamnvetsa chisoni? Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndikukhulupirira mwa inu nonse kuti chimwemwe changa ndi cha inu nonse. Pakuti mchisautso chambiri ndikuwawa mtima ndinalembera inu ndi misonzi yambiri; sikuti ndikumvetseni chisoni koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu chimene ndili nacho koposa.” (2Akor.2: 1-4)

“Koma pamene ndinadza ku Trowa kudzalalikira uthenga wabwino wa Khristu,ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo,mwa Ambuye,ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga,posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nawo ndinanka ku Makedoniya.” (2Cor.2:12-13)

Pakutinso pakudza ife m’Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, mkatimo mantha koma iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu anatitonthotoza ife ndikufika kwacha kwa Tito; koma sikufika kwache kokha, komanso ndichitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwan, kulira kwanu,change chanu kwa ine, kotero kuti ndinakondwera koposa. Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndikalata uja sindiwawapo mtima ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani chisoni ngakhale kwa nthawi yokhayo. (2Cor.7:5-8)

Dziwani izi za munthu kuti Mulungu akhoza kumugwiritsa ntchito osangoti pazintchito zakunja kokha komanso mitima-Inde zinayenera kukumanizana nawo, koma anadana nazo! Silinapange tsiku lake, ndipo ndikumpatsa iye cholinga cha ulendo. Inde, anawakana momveka. Ndikuwerengako mbali zina za kalata yake, tikhoza kumuweruza mwankhanza ndi mosamukonda. Koma chenicheni ndi ichi kugwira ana ako akusewera pamsewu popanda lamba ndi chitsimikizo chakuti siwuwakonda. (Aheb. 12:5-11). Ngakhalebe kholo lokonda (kapena kukhala m’busa mwa Yesu, kapena Mkhristu mzathu). Adzadana ndi mphindi iliyonse ya nkhani ya kudzudzula. Sadzalota zakudzitamandira za mmene anagwirira ntchito yodabwitsa yothana ndi oukirayo. Zadzakhalabe zachinsinsi zawo. Ndicho chikondi. (1Akor. 13:4-7).

Paulo anali pafupi kukhumudwa ndi zochita zimenezi pamodzi ndi Akorinto. Ngakhale zimaoneka kuti zimawayenera nkhanza zimenezi. Ngakhale anayenera kuzichita pakukhala mu Ubale ndi Mulungu ndi Oyera (1Jon 1:3-7), mwamuna kapena mkazi wa Mulungu adzadana ndi maganizo oika chidzudzulo pakhomo pa m’bale woyenda-ngakhalebe kusaganizira kuchuluka pazimene angafune. Paulo anati kulembedwa kwa kalatayi kunali “kowawa’ kwa iye. Zinabweretsa “kukhumudwa kwambiri” ndipo analira “misonzi yambiri” pamene amayesa kulemba kalatayi ya chidzudzulo ndi malangizo.

Paulo, ngati ukumbukira, anapatsidwa “kutsekula chitseko” kulalika uthenga wa bwino ku Troas (2Akor.2:12). Pamene anali odandaula ndi mantha kuti banja laku Korinto adzakana mau ake ochokera kwa Mulungu, Iye, “masomphenya a Mulungu” m’kalata yake. (1Peter 4:11), sanayang’anenso pa (kutsekula chitseko) ndikupita kukampeza Tito kukaona mmene chidzudzulo chake anachirandirira. Analibe “mtendere mumtima”, “opanda mpumulo,” “kukangana kwa kunja, mantha mwa iye” ndiponso kudzitsutsa ku anaperekeranji chidzudzulo. Kupweteka konseku sikunathe mpakana, pamapeto, Tito anauza Paulo kuti amamukondabe ndikukhala “odzipereka ndi okhudzidwa”kwa iye. Zabwino mwa izo, chisoni chachikulukuti chidzudzulo chake chabweretsa kwa Akhristu ku Korinto kuwalondoloza iwo kulapa kozizwitsa ndi “kusalakwa panjira iliyonse” m’miyezi isanu ndi umodzi kufikira mwezi wa chisanu chi chinayi atatha kuwalembera iwo zokhudza moyo wa dziko lapansi.

Nayi mfundo: Mzoona tilibe ufulu kungokhala chete pamene ena akuononga ubale wawo ndi Mulungu ndiponso, kugulitsa Tsogolo lawo mwa Iye. Pamene, tikhoza kuononga mosaganizira wina, ngakhale kuganizira machimo odziwika, osalira ndi kuzunzika, sitili oyenera kuyankhula liwu Kwa iwo. Yesani mtima mosamala. Ngati mulibe pang’ono chikhumbokhumbo kukhala okhudzidwa, ndiye mulibe chilolezo kuchokera kwa Mulungu choyankhula, ngakhale “muli okhoza” kapena ayi. “Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndinzeru zonse, ndipo ndingakhale ndirinacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndiri chabe.” (1Akor.13:2) Amen?!

2) “Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pamoyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.” (2Akor.1:23)

“Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha ndisadzenso kwa inu ndi chisoni” (2Akor. 2:1)

Paulo, ndi mamuna kapena mkazi aliyense amene Mulungu adzera mwa iye, adziwa nthawi yokhala ndi nzeru ndi kubwezera mbuyo. Paulo anadziwa kuti pali zambiri zoyenera kuchita mumzinda woipa uwu ndiponso mdzikoli, mugulu la Akhritsu ochita zoipa.2 Anadziwanso nthawi yakuluma lilime lake. Inabwera nthawi imene Paulo anadziwa kuti sayenera “kukhumudwitsa ana ake”. Anasankha kusabwerera ndikupanga ulendo “wina wowawa” ku mpingo wakumeneko, ngakhalebe panthawi imeneyi analibe uthenga wina uliwonse kuti alapa pamadera oipa amene anamangidwa nawo.

Ubwino wa nkhaniyi ndikuti pakhoza kukhala zinthu zina zakuti tikhoza kunena, kuzipenya ndikupanga nazo m’bale kapena mlongo wina-zinthu zoona, zinthu zokhoza-ngakhale zikhoza kukhala zochimwa kunena mau amodzi kwa iwo za izo. Paulo anadziwa ngati mmene Yesu anadziwira, tikhoza kuphunzira, kuti pamene tiri amodzu ndi Atate mwa Yesu, sitidzayankhula liwu limodzi mwa ife tokha. (Yohane 14:10-11,24; 8:28-29; 17:21; Agal. 2:20; Aef 6:19-20; Akol 1:9; 1Pet4:11). Mpakampaka. Zinthu zimene zili zoona sizili zoona kapena zabwino kuti zikhoza kuyankhulidwa panthawi imeneyo. Inuyo dzigonjetsereni kwa Mulungu kuti mukufuna kuchita zomwe Iye akufuna: wachikondi kukonza mavutowo kapena kupanga pang’ono pang’ono mpaka patatha miyezi isanu ndi umodzi, kapena sakufuna kukumana nazo mpang’ono pomwe ingopempherani mosalekeza kuti Mulungu agwiritse ntchito njira zina kuwathandiza iwo kusiya tchimo limemelo. Siinu wolondera wa Polisi waMulungu. Mulungu wathu alingati bambo wabwino aliyense-sadzakhala ndi ena mosintha sintha kutumikira Ana ake. (Oba.1:12; Miy. 50:21). Pali nthawi yakudzudzula—mwakuthekera pamaso pa abale onse (Agal. 2:11-14; 1 Tim.5:20; Machitidwe 5: 1-11). Palinso nthawi yakutsuka mapazi mwakachetechete ambala yodziwika monga Yudasi, ngati m’mene Yesu anachitira, kumusiya kupitiriza ngati msungichuma mpakana nthawi yomaliza. Mkukhalabe wa chilungamo kwa mau a Mulungu ndi kudzipereka kuimirira Mulungu waboma la muyaya, chonde khalani a chikondi ndi omvetsetsa ndi opereka (Arom.2:4 ; 2Tim. 2:25-26; 1Ates. 5-14; Luka 6:37-38). Phunzirani ngati Paulo, kuluma lilime panthawi.

3) Koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu. (2Akor. 1:24)

“Koma za Apollo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi. (1Akor. 16:12)

Onani chozwizwa champhamvu chikugwira ntchito mwa Mtumwi amene waona Khristu muzaka zapitazo amene anatumizidwa ku mbali ina ya m’mwamba mwayokha. (Machitidwe 9; 22;26; 1Akor. 15:8; 2Akor. 12:2). Ngakhale Mtumwi Paulo mwiniwake anakana kuika mau mkamwa mwa aliyense, anawapanga anthu kupanga zinthu mmene akufunira. Kenaka ndondomeko za Mulungu sizinasokonekere (Gal. 2:14; Tito 3:10; 1Akor. 5: 9-13), ndipo okonza ndi “otha kukonza” sanauzidwe. Izi zikufotokozeredwa ndi kukana kwa Apolo utsogoleri wa Paulo (1Akor. 16:12).

Kumbukiraninso kudzudzula kwamphamvu ndi kupempha kudziwitsidwa mneneri wa Mulungu wotchedwa Agabus pamodzi ndi sing’anga (chimene analembera Uthenga) wotchedwa Luka-amene anakanizidwa ndi Paulo (Machitidwe 21:10-15).

Lamulo ndi ili, zoona, sitikufuna kunena malamulo opangidwa ndi munthu pazauzimu (“tsiku lokumana,” kufupi, maphunziro a Baibulo achipufi, ndi zina zotero)—ngakhale zikhale zovuta motani. Yesu, Mwiniwake, sangakhale “muweruzi) kwa akunja (Luka 12:14). Paulo anati: Malamulo “asowa mphamvu restraining self indulgence’’ zimabweretsa ‘’imfa ‘’ zilibe mphamvu kusintha mtima wa munthu koma chabe kukonzako zina mwa zintchito ndi chikhalidwe chawo.(Akor. 2:23; 2Akor. 3:6)

Chifukwa Mulungu ndi Muweruzi wa zolinga za mtima, ngakhale zochita zili za bwino (Mat 5:27-28), ndi zopanda pake kuchita chiti pa kukometsa khalidwe. Paulo analira mokweza ndi chisoni kwa Akhristu aku Galatiya: “Ndinu opusa kodi?! Nditayamba mzimu, mukuyesa kupeza zolinga zanu mwamphamvu ya umunthu?” (Agal.3:3).

Paulo anawakumbutsa Akorinto momveka bwino kuti sanali ndipo sangathe “lord it over” chikhulupiriro chawo, komano anadzipereka yense ngati chida kwa iwo chosangalira ndi kugwiritsira ntchito pakuzamitsa chikhulupiriro chawo mwa Khristu ndi kuwonjezera modzadza kuyenda mwa iye. (2 Akor. 1:24). Mosakaika “ulamuliro” sinzeru yosachokera m’baibulo pakukulitsa china chilichonse m’maganizo (Aheb. 13:17,7; 1 Akor. 16:15-16; 2 Akor.13 10; 1 Ates. 5:12-13), koma cholinga cha aliyense pakuika miyoyo yawo mwa ena mwa uzimu ndikuti akhale chida cha iwo chopeza pa iwo okha chikhulupiriro, osati chomenyera kuwapanga iwo kutatha kukondwedwa kwawo ngati mmene Afarisi anachitira (Mat. 23:15). Mwanjira zonse, patsani onse kuyera mowonekera chitsanzo choti mkukopera. (1 Ates. 1:6; 2: 10, 14; 1 Akor 11:1; Afil. 3:17, 4:9; 1Tim. 4:11-16), koma kumbukirani mawu a Yesu, “Simuyenera kudzilola nokha kutchedwa mphunzitsi, bambo (mtumwi?, ndi zina zotero) pakuti muli MMODZI-NONSE MULI ABALE” (Mat. 23:5-12).

4) Ndipo ndinalemba ichi chomwe kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndikukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse. Pakuti m’chisautso chambiri ndikuwawa mtima ndinalembera inu ndi misonzi yambiri sikuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndiri nacho koposa. (2Akor.2:3-4)

Tipatseni malo; sinamchitira munthu chosalungama, sitinaipsa munthu, sitinachenjerera munthu. Sindinanena ichi kuti ndikutsutseni pakuti ndanena kale kuti muli mumitima yathu kuti tife limodzi ndikukhala ndi moyo limodzi ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu kwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe mchisautso chathu chonse. (2Akor. 7:2-4)

Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwaiye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga timayankhula zonse ndi inu choonadi, koteronso kudzitamadira kwathu kumene kwa Tito kunakhala choonadi. Nidkondwera kuti mzonse ndirimbika mtima za inu. (2Akor. 7:14,16)

Kodi mungaganizire kukhala “m’chikhulupiriro chonse,” “kukhutitsidwa kwakukulu”, “kulimbikitsidwa kwakukulu” komanso “chakumwa” mwa munthu amene waledzera pa mgonero wa Ambuye ndinso kudzandira m’kudzikonda, kudzikweza ndi kudziunjikira? Bwanji kwa kwa mpingo umene ukuwoneka ndizodabwitsa za uzimu ngati zimenezi? Kodi mungaufute? Kodi inuyo “mungasase fumbi kumapazi anu?”

Kapena, kodi mungakhale ndichikhlupiriro chonse mwa iwo pawakutembenuza ndikuwonetsera iwo kwa ena ngakhale musanamve kapena mutamva kuti asiya zinthuzo? (2Akor. 7:14-16). Ngati muli ndi mtima wa Paulo, amene nthawi zonse anali ndi mtima wa Khristu simungatsutse ndikudandaula zaena’ pakulephera-koma kudzionetsera kwenikweni za banja lako kapena za ena. Ndinso ndiye kukhala ndi chikhulupiriro chonse chatsogolo. Mulungu amachita ntchito zabwino!. Mukupanga bwanji? Kodi ena adzaona ubwino mwa inu? Ndiri “ndi chikhulupiriro chonse kuti adzakhala. (!).

5) “Komai iye wakukhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu; ndiye Mulungu anatisindikiza cizindikiro, natipatsa chikole ca mzimu mumitima yathu”. (2Akor. 1: 21-22)

“Amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimariziro, kuti mukhale opanda chifukwa m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu. (1Akor. 1:8)

Panali munthu uyu wotchedwa Paulo amene anali wamaphunziro amalamulo mbiri yake anadziwa mawu pambuyo ndi patsogolo pomwe, analandira malangizo a umunthu kuchokera kwa Yesu Woukitsidwa, amene anakhudzidwa mozizwa zambiri, ndipo anabweretsa zikwi zamuna ndi akazi kwa Khristu (Afil. 3:5, Mach 26:24; 23:6, Agal.1:14; Arom. 15:18-19; Mach. 20:35). Zonsezi, anafulumira kuzilandira kuti pa iye yekha sangathe kukwaniritsa chilichonse mu moyo wamunthu aliyense.

Ndi Mulungu yekha angalenge ndinso kuyeretsa komanso kupereka mphamvu. Paulo anawerengera kwa Mulungu kubweza mau ake a mwala kukhala mkate wa moyokwa abale ndi alongo ake. Paulo anadziwa kuti ndi Khristu Yekha amene angaulule za Atate ndi Mulungu yemweyo amene anampatsa nyonga akhozanso kuwapatsa nyonga (Mat. 11:24, 27; Afil. 3:15, 2Tim 2:7; Akor. 1:9-11; Aef 1:17-19; 3:16-19, Machit. 20: 30-32; 1Yoh. 5:20). Anakhulupirira abale ndi alongo kwathunthu kwa M’modzi yekha amene “akhoza kuwasunga kukhala olimba mpakana kumampeto ndinso kumaliza zimene adaziyamba mwa iwo.” (Aheb. 12:2, 11; 13:20; 1Ates. 5:23-24; 2Ates. 3:3; Yoh. 3:21). Ntchito ya Paulo inali yokhulupirirka kudzala mbewu ndikuthirira ndinso mosapeneka kuchita zonse zimene akanatha kupanga mmoyo wake kwa iwo (1Ates. 2:8), Koma mwaulemu anazindikira kuti zophunzitsa zaMulungu, kutsutsa, kukopa kapena kuyankhula ndi lilime lakuthwa sizingapange chilichonse kusintha mzimu kapena mzimu wokhwima. (Yoh. 1: 1-12; Rom.12:3). Zonse zimene akadatha kuchita zinali kubweretsa mbeu ya chilungamo munjira yosweka ndi moyo wosaipa. (2Akor, 4:6-7, 2Tim. 2:20-21 ndikupemphera kuti Mulungu of Zokolola achulukitse m’mitima yotseguka.

Kwa inu ndi Ine”Zingakhale zosiyana bwanji? Tiyeni tikhale okhalupirkika, odzazidwa ndi chikhulupiriro, olimba, osatekeseka, oyera ngati mwana wa nkhosa wopatulika-ndikupemphera kutula mavuto anthu ena pamapazi a”M’busa mwamkulu wa Nkhosa” Adzapeleka zida ndi zabwino zonse pakuchita kufuna kwake ndi ntchito mwa iwo zimene zimukondweletsa iye. (Aheb 13:20-21)

6) “Komatu pano pafunika za adindo kuti munthu akhale wokhulupirika.” (1 Akor. 4:2)

“Tiri opusa ife chifukwa ca Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tiri ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka. Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tiri amaliseche, tikhomedwa, tiribe, pokhazikika; ndipo tigwiritsa nchito ndikuchita ndi manja athua ife tokha; polalatidwa tidalitsa; ponzunzidwa, tipitirira; ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano. (1Akor. 4:10-13)

“ Pakuti ife ndife pfungo labwino laKhristu, Kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo lamoyo ku moyo. Ndipo azikwanira ndani izi? (2Akor. 2:15-16)

Palibe funso kuti kudzipeleka molimba Mtima moyo wa ena Mwa uzimu ndi odula koposa. Palibe funso lililonse pachilichonse za mphotho ya kukhala yofunika kwa Mulungu asanabwere mwina adzatisiya atazunzidwa, kukhumudwa ponyozedwa kapena pakukhala ndi njala ndi ludzu. (Luka 6:24-26). Palibenso funso kuti ngati tili “opusa chifukwa cha Yesu” kusiyana ndi kuima kapena “kukonzekera” kapena chilolezo cha chogwiritsidwa ntchito mwauzimu …… pakuti tidzapereka dipo lalikulu.

Ndi zovomelezeka ndi zochitika mmoyo wanu kuti muli kufunitsitsa “Mudzipange wopanda kanthu” “mukhale chopondapo dziko”? Ngati mutayesera kukhudzidwa ndi kugwira ntchito ya moyo ndi Chilungamo cha Mulungu, ndithudi mudzakhala ndi okoma ndi onunkhira kwa iwo okoma mtima. Ndi zooona, ngati muli okhudzidwa mu ntchito ya Mulungu ndipo mudzakhala fungo loipa laimfa kwa amene ali ndi mitima yosalapa. Zimene mudzazilipira ngati mmene anachitira mwana wamunthu. Ngati mmene mpotsoli wamphamvu anachirira “Ndi ndani ali ofanana ndi ntchito imeneyi”?! Iye Sanapange, ndipo ifenso,sitinapange, chitengeni mopepuka.

Ndi chinthu chonyaditsa kukhala okhudzidwa muubwino “mphamvu za mdima za dziko lino lapansi kupikisana ndi mphamvu za mzimu woipa mufumu wakumwamba”. (2Akor. 10:3-4; Aef.6:10-12)

Tsopano moona, mukawerenga mutu wa bukuili, mukhala ndi chinthu mumtima kuti mupeza chilinganizo chimene chidzamasula ntchito iyi yosatheka yakulangiza Akhristu osochokera kwa Khristu. Zoona? Ndi pempero langa kuti muzindikire kwathunthu kuti “chinsinsi” chagona mu chinthu chimodzi chokha: Kuti mtima wanu ndiwobisika mwa Khristu ndipo kuti mukufunitsitsa ngakhale kufera “ngakhalebe izi” —“ pamene iwo ndiwochimwa”. Mtima wanu uli ngati Yesu’: pakugula anthu a Mulungu, ngakhalenso ndimoyo wanu omwe ngati kutafunikira kutero. Pali chinsinsi pangani izi pakuyang’anitsitsa kwakukulu, funani Mulungu wa Mau. “wamoyo ndi wamphamvu” Mau a Mulungu, ndipo anthu a Mulungu, mudzakhala opanda mavuto kuposa Paulo anachitira pakulangiza Akhristu osochera. Konzani mitima yanu.

Pamene mukuyang’ana patsogolo pokonza moyo wanu kwa Mbuye wanu ndiponso abale ndi alongo anu, zosatheka ziikeni pachiopsezo ndi zosatchuka ndipo ziyankhulidwe za inu kumwamba, ngati zimene zinaliri za munthu wamba: (Machit. 13:36)…

“ICHI CHINAGWIRA NTCHITO YA CHOLINGA CHA MULUNGU MU M’BADO WAKE OMWE.”

1985, 1989

1 (1 Akor. 6:9-11)

2 Luka. 14:33, Luka. 9:57-62; Mat. 10:32-39; Mach. 3:22-23 sakutsutsana ndi 1Akor.3:1. Akorinto luyankha kwawo ku choona ndi makiyi. Onani 2 Akor.7:8-16. Ili ndiyankho lenileni la Mtumwi pakuyankha chilungamo-opanda kutsutsa, zaka zitatu zoonjezera za kuphunzira mau a chi Giriki, ndikuzama. Chonde werengani ndimezi mosamala ndipo mudzavumbulutsa kuti ndithu ndi zosatheka kuti amene amadzitcha iye mwini Mkhristu akhoza kukhala wosasinthika panthawi yakumana ndi mau a Mulungu.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon