Mabvalidwe: Kuitana kwa Yesu

Kwa Mkwatibwi wake—Kwa ife Tonse!

5/10/1998

Kudzera mu kulemba kwa bukhuli lidzatiunikira ku nkhani imene timaitcha :mabvalidwe”. Ndiyofunika ku zofuna zathu kwa Mulungu ndi kufunikanso kutiyeretsa ku moyo wathu ndi chifundo ku miyoyo yathu yathu chifukwa chanji? Chifukwa ndi choti kupatula kukhudza kwake ndi kuikidwa kwa masomphenya kwa ife, sitingathe kudziwa zambiri za moyo wake kudziko ili lapansi. Izi sizobvomelezedwa kapena zokaniza kuchita pa mabvalidwe. Ndi ulendo ofuna kupeza mtima wa Mulungu. Mwalamulo ndi imfa, monganso yomwe sizachilamulo kapena zololedwa. Tikulankhura za iye. Tizabwera pafupi mu mtima wa Mulungu ndi kupeza mitima ndi maganizo kusinthika kuchokera mkati.

Ndizomukonda mwakuya ndikumalingaliro mmene timabvalira matupi athu kunja kwa matupi athu.

Gawo Loyamba

Kusintha kwa Kuwona Kwathu.

Ndichofunika kutikumbutsa kuti mbali yathu monga otsatira a Yesu. Kuthandauza kuti amatidalira, amaika zonse zochitika pa okonza mbiya ndipo ife tonse ndi dongo. Iye ndi mlengi ndife olengedwa ake. Izi ndi zofunika kuika momveka bwino mu mitima yathu ndi mmalingaliro ku ntahwi zonse kuti tingonjere ku zotere kumvera, ndi kukondadi kwenikweni malamulo ake. Malamulo ndi malangizo ai. Choncho, Mulungu koma…. sitifuna zonga zimenezo “sindikuganiza kuti ndi zofunika palibe njira mwana wa Mulungu angakhale ndi kuzikonda machitidwe onyada ndikupeza kuti wapambana ndi kukula mu uzimu. Mulungu anakonzeratu nthawi zonse kuti tizikwaniritse “moyo woyesedwa” kuti tione mmene timazipelekera kwa Yesu. Chiyembekezo chathu ndi choti mupeze mu mwayi wina uwu kuti muike zonse pansi pa mapazi ake ndi maganizo ndi kufunitsa kumvera iye, pa mtengo wina uliwonse. Zikhonza kukhala kwa inu kuti ndi nkhani imene yapereka mwayi. Chonde muchitenge ichi mwa kuya, ngati mwasiya zinthu zonse potsata Yesu. Monga anthu a mu nthawi yake—ngati uku ndi kulingalira ndi mtima, ndiye kuti musatope tsopano! Musalore umunthu wanu kapena zofuna zanu. Kapena kunyada kapena zakutha kukhala Mulungu ali woyenereka kuposa mmene muganizira. Kodi simudziwa kuti simuli a inu nokha munagulidwa ndi mtengo wapatali? Chonde lemekezani Mulungu ndi matupi anu (1 Akorinto 6:19-20)

Ndi zofunika pamene tikubwera kwa Mulungu ndi mau ake a mabvalidwe ngati tikutha kuzindikira kuti ndi chiani chimene tikuphunzitsa ndi kuonetsera ku miyoyo yathu. Ngati takulira ku Amerika kapenanso dziko, timakakamizidwa kudya chakudya cha zonyansa. Kusabvala bwino, zachiwelewere ndi zathupi, maganizo athu ndi kulingalira kumakhala ndi kuganiza kumene dziko liwonera osati mmene Mulungu awonera zinthu. Monga mwana wa Mulungu (mfumu) maziko zthu onse ndi zochita ziyenera kusinthidwa mmene dziko liliri! Choonde mvetsani bwino kuti tiri ndi kuona kwa dziko lapansi tisanakhale kwa dziko lapansi tisanakhale kwa Mulungu.

Chifukwa chake tikupempha inu, abale mwa chifundo za Mulungu kuti mupeleke matupi anu nsembe yamoyo yopatulika yokondweletsa Mulungu ndiko kupembedza kwanu. Koyenera ndipo musafanidwe ndi makhalidwe a pansi pano. Koma mukhale osandulika mwa kukonzanso mwa kwa mtima wanu kuti mukazindikire chimene chiri chifundo cha Mulungu, chabwino ndi chokondweletsa ndi chagwiro. Aroma 12:1-2

Pamenepo ndinena ichi, ndipo tichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, mchitsiru cha mtima wawo. Kuti mumbvule kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za chinyengo koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu. Mubvale munthu wa tsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu. Mchilungamo, ndi mchiyero cha choonadi. Aefeso 4:17,22-24

Kusintha mitima yathu ndi kukonzanso munthu watsopano ndi maganizo a tsopano. Paulo ali kunena kufunika kwa kusinthika kwa malingaliro ndi kutaya zonse za machitidwe a dziko lapansi.

Maganizo athu ayenera kusinthidwa ndi Mulungu. Ndipo mbali ina pamafunika kuzindikira ndi kulapa kuzoikidwa mu dziko lapansi. Takhala ndi maganizo amene anakhala mu zimene dziko lapansi amati ndi “ofunika” kukhudzana ndi matupi athu kubvala zinthu zothina. Mmaonekedwe kugwira thupi ndi zoonekera, zobvala zopsyapsala zimene zimakoka amuna ndi akazi. Mdani ali nthawi zonse kunama kwa ife kuti maonekedwe ali mu zonse ndi kuthandauza za zimene ife tili. Dziko limapitiliza kufuula kuti maonekedwe ndi ofunika ndi kunong’oneza kutiitanira kukumwa ndi kuonetsera zotere kuchokera ku chikwangwani zazikulu mu misewu, mumanews paper, zolengezedwa, mmasitolo a nsaru, mmacinema ndi ngakhalenso ma kanema. Dziko limati ndi zabwino ndi zofunika kuti tikhale mthupi totere la mabvalidwe onyasa. Zili bwino! Sangalalani! Teloni maso athu ndi makutu akhala okwapulidwa ndi sizaumulungu. Makhalidwe otere amene ife takhala mu zimenezo atipangitsa kumuyezo kutichotsa ku malingaliro a Mulungu. Ndi zinthu ngati izi za moyo wa uzimu mwa Mulungu ndi kumvera mwana wakw Yesu kuti ngati tidyetsedwa ndi dziko lapansi pamaganizidwe ndi kupuma mphewa wake wa dziko ndi kulandira mabodza ake ndi muyenso wa makhalidwe ndi pobvuta kuona bwino ndi kudziwa ndi kumva mtima wa Mulungu kwa nkhani zina.

Choonde, tengani undindo, pitani mu chipinda chanu ndi kutseka chitseko ndi kukumana ndi Mulungu pa nkhani imeneyi. Mwakuona mtima funseni, iye kuti tsegule maro anu ndi kuonetsera zonse kwa inu, kuthandiza inu kuona zinthu zenizeni sizidzakuonetsani inu ubwino uli wonse pakuwerenga izi ngati simufunsa maganizo pa mmene mubvalira, ndipo ngati simufunsa Mulungu adzakwanilitsa kuyeletsa ndi kukonzanso malingaliro pa nkhani imeneyi ndipo pakuyankha kwina pongochita chabe izi. sinthani mabvalidwe chifukwa ndi bwino ndi chipembedzo kutero—kuteleko sikuti ndiye choncho ai. Kusankha kwithu pozichepetsa ku maganizo ndi mitima yathu kwa Mulungu ndi kusintha njira zathu ziyenera chifukwa choti taona Yesu ndipo tavomeleza kw aiye monga munthu. Sitifuna kuti tidziwe zonse kuti tizipeleke kwa Ambuye. Mtendere wathu udzapezeka mu kupezeka kwa kufuna kwa moyo ndi kukonzeka ku kumvera kwa Mulungu wa moyo amene ali ndi maganizo abwino tsopano a izi funani iye. Itanani kw a iye. Funani popezeka iye pa nkhani imeneyi ndi mtima wanu wonse. Akufuna kulemetsa ndi kudalitsa inu ndi kukuitanani ku mbali ndi kudzaza inu ndi ulemerero ndi ubwino wa mau ake oyera. Ndiye lonjezo limene anapanga ndi ife monga mwa mau ake.

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife kachisi wa Mulungu wa moyo monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo ndipo ndidzayenda yenda mwa iwo, ndipo adzakhala Mulungu wawo ndi iwo adzakhala anthu anga chifukwa chake tulukani pakati pao ndipo patukani, ati Ambuye ndipo musakhudze kanthu kosalandira kwa Atate. Ndi inu mudzakhala kwa ana Amuna ndi Akazi anena Ambuye wamphamvu yonse. Pokhala nawo tsono malonjezano amenewa. Okondedwa tidzikonzere tokha kuleka choletsa chonse cha thupi ndi cha uzimu ndi kutsiriza chiyero mkuopa Mulungu. 2 Akorinto 6:18—7:1

Yang’anilani pa zimene Mulungu anaikika kwa anthu. Anthu aiye mwani wake Mulungu. Tiyenera kuti tichoke kwa iwo adziko ndi kuziyeletsa tokha pazimene zimadetsa thupi ndi mzimu. Iye wanena, ndi kuti, tichoke ife kudziko, Dziko ndi maganizo ake ndi malingaliro ndi zikhumbo zake ndi zofuna za dziko lapansi. Sindife omangidwanso, ndi dziko, ngati tili eni eni ake ndiye kuti tili alendo ogonera chabe mu dziko lino sitili mu zochitika za dziko lapansi osatinso wowonongedwa ndi ilo. Mulungu anati tichoke kuchokera kwa iwo ndi kutiuza kuti tikakamire pa zimene anena za moyo wathu.

Ndife ndani otsutsana naye Mulungu wathu? Tiyenera kusinthika kwa maganizo athu? osatinso okuzidwa ndi machita-chita adziko lapansi. Ife taomboledwa kuchokera ku mpahmvu ya mumdima ndi kubwera mu ufumu wa mwana wake Yesu otikondawo sitifenso makhanda ndi akaporo a uchimo umene watimanga nawo. Njira za dziko lapansi ndi olamulira wa mwamba. Mzimu umene tsopano ugwira ntchito kwa iwo osamvera. Tonse, amene tinali monga iwo nthawi ija. Mzilakolako zathupi ndi maganizo. Aefeso 2:2-3

Monga ifenso amene tinachita zofuna za thupi kuonjezera Nsanje, ndi anzathu mu mawonekedwe, kufanizira mawonekdwe athu ndi ena muthupi, kupikisana ndi mawonekedwe athu ndi kufunitsitsapo tengeka ndi chilakolako choti tiwoneke bwino. Zakutha zamitundu mitundu. Ichinso ndili chimo lalikulu limene latengera anthu ambiri kwa Mulungu ndi makhalidwe athu kaya modziwa kapena mosadziwa ambiri aife mu nthawi zina takhala ochimwa popangitsa anthu ena kuphundwa. Kulowa mu chilakolako ndi mu uchimo wina chifukwa tinali ozikonda tokha ndi kubvala tokha zobvala za kunja kuti tikope ena ndi kuonekanso bwino pamaso awo.

Izi ndi zotsatira zopezeka mu chakudya cha dziko lapansi mu kuganiza kwa dziko lapansi pokhunzana ndi mabvalidwe ndi maonekedwe. Ichinso chiyenera kupangitsa ife kuti tithawe ku chilli chonse. Chobwera mu mtima wa dziko ndi satana. Iye ali mdani wathu ndipo adzagwira ntchito mu njira ina iliyonse kuononga ndi kutipatsa kumva zowawa za imfa ndi kudetsa maganizo athu kusiyana ndi umulungu ndi moyo obisika mw aKristu ndi Mulungu sizosadabwitsa kuti wapangitsa athu kuti amizidwe mu zathupi ndi zachiwelewere ndi kusabvala bwino kudzera mu njira ya mmaso athu ndi makutu athu ndi malingaliro. Choonde lolani ndi kubvomeleza pa izi. kugwilizana ndi Mulungu pa izi sizothera pompa kwa otsatira wa Yesu.

Mwa choncho ndi zofunikanso kutchula zina pano kuti sikuti zili bwino mu kuyenda ndi Mulungu ngati mabvalidwe ali abwino koma moyo wanu uli ku dzikobe. Machitidwe anu achilungamo adzakhala sanza pa Mulungu ngati simubvomereza ku chifukwa cha mtima wa Mulungu. Anthu ambiri chifukwa amabvala bwino, akhonzanso kukhala oziyeletsa okha, mu kuganiza kwawo. Koma sizithandauza kanthu n gati sabvomeleza Yesu, amene ali mutu wawo, ndiye choonde osangokhala obvala bwino amene alibe kufunitsitsa kuti apeze mtima wa Yesu pa chobvala chanu. Kusintha kabvalidwe kayenera kukhala malo abwino poyambira koma ndi zapamtundu ndi kuba ngati mulekera pompo!

Pano pali chitsanzo cha zinthu zina zopezeka mu kusunga zinthu zakunja kwa thupi mu dzina la mabvalidwe zimene zimakhala zobvuta ndi zotsatira munthu akapanda kupeza chikondi cha Mulungu ndi mtima wako. Posachedwa, mlongo anaona wa chisilamu mzimayi ali kuyenda ndi mwana wake. mmene mlongoyu amapenyetsetsa mchisilamu amene mwana wa ng’ono anathamanga patsogolo ndi kumapita kumene galimoto limabwera. Mukufulumira kuti apeze mwanayo ndipo nsaru za nduwira zinayamba kugwa pansi pa ichi mau aja ali pakati kati pa zinthu ziwiri kuti achite. Anayenera kuika mpango wake kumutu! Nanga mwana wake uja? Zimene zinaoneka pamenepo ndi zolilitsa kuti tinganene zinali zotere chifukwa cha chipembedzo chimene anali kusunga? Nsalu ya kumutu inakhal yofunika koposa moyo wa mwana. Sizinali mu maganizo a Yesu pazimene ife timaziona ndi zimene zilipo malamulo a moyo oyera kusiya kufunika kwa moyo oyera kusiya kufunika kwa moyo mmalo mwake.

Kumbukilani mau ake amene anati anthu anthawi yake anali kusungira sabata ndi kusunga miambo ya makolo ndi kusasamala chikondi cha Mulungu ena? Sikuti tikuti ndi kufunitsitsa kwithu pokondweletsa Atate athu ndi kubvala kwithu tiyenera kubvomeleza iye mu chikondi monga munthu osati ku malamulo olembedwa ndi kusindikiza umene ungazimitse moyo wathu wa mwa Yesu ndi inu moyo wathu kwa anzathu ena mukhale auzimu mu kuzama popeza kukunmbatira mtima wa Mulungu mu nkhani imeneyi. Choonde musangokumbatira kubvala bwino kokha KUMBATIRANI MULUNGU. Kenako mupitilire kuthandiza abale ndi alongo kuti awone ndi kusinthaka mkati mwa moyo wamkati.

Mu mzimu ndi chisomo cha Mulungu tonse pamodzi tiyenera kuthokonza Mulungu kuti chifukwa cha chikondi chake kwa ife. Mulungu amene ali olemera mu chifundo adzatipanga ife kukhala ndi Kristu ndi chisomo chake tinapulumutsidwa ndipo Mulungu anatiukitsa ndi Kristu pamodzi ndi kutikhazika ndi iye ku zamwamba mwamba mwa Yesu Kristo kuti mukudza adzaonetsera chuma chosaola cha chisomo choonetsedwa mu kukoma mtima kwa ife mwa Kristu Kristu. Aefeso (2:4—7)

Tiyeni tonse pamodzi tipeze Mulungu

Gawo Lachiwiri

Zinayambira Mu Munda…

“Mwamuna ndi mkazi wonse anali wa maliseche, ndipo analibe manyazi” Genesis 2:22-25

Panali nthawi mu munda, pamene mwamuna ndi mkazi anali woyera, abwino opanda chidetso, chilema kapenanso uchimo, umu ndimo njira imene Mulungu anawalengera iwo popanda uchimo kapenanso chilema. Choncho, sanali kuona maliseche ngati chamanyazi. Anali onse ndi Mulungu ndi wina ndi mzake ndipo matupi awo anali opanda chidetso ndi woyera. Zoona za zimenezi zinaonetsera pamodzi pamene anali onse amaliseche, koma analibe manyazi.

Potero…

Pamene anaona kodi chipatso chinali cholakika mmaso ndi kudya ndi chodziwitsa nzeru. Anatenga nadyz ndipo zina anapatsa mwamuna wake ndiponso iye anadyanso. Ndipo maso awo. Anatseguka ndipo anadziwa kuti anali wamaliseche, ndipo anatenga masamba a mkuyu nawasoka ndi kubisa maliseche. Ndipo mwamuna ndi mkazi anamva kuyenda kwa Mulungu kuti anali kuyenda mmundamo pakati kati pa dzuwa. Ndipo anabisala pakati pa mitengo ya mmundamo. Ndipo Ambuye Mulungu anaitana kwa mwamunayo uli kuti kodi?

Anayankha ndinakumvani kuti muli mmunda ndipo ndinali kuopa CHIFUKWA NDINALI WA MALISECHE, ndiye ndinabisala. Genesis 3:6-7

Taonani chinthu choyamba chimene Adam anazindikira. Anali wamaliseke. Pa zonse… wamaliseche, onse anali, mwamuna ndi mkazi, onse mu munda. Sitidakhala chinthu chachikulu . anali wamaliseche. Anali okwatira ndi wina ndi mzake! Pazomwe Adam adazindikira kapena kulankhula atachimwa anali okhunzidwa ndi umaliseche ake. Anali atalakwira Mulungu wake wamoyo, mulengi wake. Anali ataswa kukoma kwa ubwenzi ndi Mulungu mwini. Anali ataphwetela moyo wa Mulungu. Koma motero thupi lake lamaliseche ndilo patsogolo mu maganizo ake ndi mantha. Mwamuna kapena mkazi mu chizolowezi choyenda ndi Mulungu, koma kukhala mu dziko lolephera ayenera kusamala ndi mabvalidwe, monganso Adamu adachitira.

Izi ndi kuyamba kwa mtundu mbiri yake munthu olephera ayenera kubisa maliseche ake ndi kukhala ndi moyo woyera ndi mantha akulu ndi chilungamo ndi Mulungu olungama.

Pamene anaononga lamulo la Mulungu ndipo anthu onse anakhudzidwa ndi uchimo, kudza ndi mkati ndipo maliseche awo amakhala chinthu chofunika kubisika. Angakhale anazibisa okha ndi masamba a mkuyu. Adamu anali kubisalabe kuchokera kwa Mulungu chifukwa anali ndi mantha. Chifukwa anali wamaliseke. Ngakhale kuti anazibisa yekha ku muyezo wina mu maganizo ake anali kuziganizira yekha wamaliseche ndipo amafuna kuti abisale chifukwa cha mantha. Mwani Adamu adadziwa kuti masamba sanali okwanira kubisa maliseche kapena kubisanso manyazi. Kukhetsedwa kwa mwazi wa nyama kunali kofunika kukwanira kubisa maliseche ake monga Ambuye Mulungu anapanga chobvala cha chikopa kumpatsa Adamu ndi mkazi wake ndi kubvala onse. (Genesis 3:21) kuwabveka kunali kofunika kwa Mulungu kuti iye mwini anawapangira zobvala. Kudzera mu mwazi (kuwonetsera chinthuzi za kufunika kwa mwazi wa mwana wa Mulungu. Kuchotsa chimo ndi malamulo kwa ali yense amene adzaitana pa dzina la Ambuye) ndiye pali yeni yeni yofunika? Mulungu mwani wake anawamveka onse. Mulungu anafuna kuti abvale.

Kodi sitili ofanana ndi Adamu kukhala ndi kulingalira ku maliseche athu. Sipali mizera imene nthumazi yanu imakuunzani? Sizoona kuti tili ndi lingo la manyazi cha kudzera ku umanyazi athu? Mwa chitsanzo, Brauzi limodzi ndi Malaya kuti lili losamangidwa bwino malo ambiri. Kodi mungakhudzidwe mu mzimu wanu kuti simunamange bwino mabatani ndiye kupita kwa anthu muli choncho? Ngati tili ozindikira kuti tili ndi mizere imene sitingadutse ndiye tingadziwe kuti ndi mizere imene inaikidwa ndi Mulungu. Siza aliyense payekha kuganiza chisankho cha zimene zili za bwino mu maso ake. Pakuika muyenso wa ife tokha. Tiyenera kuti tiike mitima yathu kwa Mulungu ndi kupeza kuti amafuna chiani za kubvala bwino ndiye tingalore maso kuti aone kapena kulandira. Ngati kuli kofunika kwa Mulungu kubveka Adamu ndi Eva, ndiye kuti alinso osamalira mmene timabvalira leronso. Tiyenera kukonda zimene iye amakonda ndi kudana nazo ndi zimene amadana nazo kumbali ya moyo wathu.

Kumbukilani kuti tisanadziwe Kristo ndi mphamvu yokukitsa ndi moyo, tinali anthu akufa ku zofuna zathu kuyeretsa ndi kukhululukidwa mu moyo wa uchimo tinali akufa akhale tinali ndi moyo. Pamene taukitsidwa ndi iye ndi kukhalanso anthu olengedwa atsopano. Tili ndi machitidwe koma osatinso auchimo kukhala monga thupi lifuna. Chifukwa ngati tikhala kukhudzana ndi uchimo, tidzafa koma ngati ndi mzimu timapha zofuna zonse za thupi ndipo tidzakhala ndi moyo (Aroma 8:12—13) kodi simudziwa kuti zofuna za uchimo zili pa nkhondo ndi mzimu, mzimu ndi nkhondo ndi zofuna za thupi, zili nkhondo wina ndi mzake, choncho musachite pa zimene mufuna ali koma ngati mutsogozedwa ndi mzimu simuli a lamulo’ (Agalatiya 17:18)

Tiyenera kupeza Mulungu ndi kukhala a nzeru ndikudziwa kuti zolephera za dziko limene lili thupi lili pa nkhondo ndi zilakolako za Mzimu wa Mulungu mwa ife. Uchimo wathu ungafune kukhazikidwa mw aife mu njira yoipa. Pamene mzimu umatipatsa chiyeletso cha thupi, moyo ndi maganizo mwa choncho mwa mzimu tili kuthandauza kukwanitsa thupi kulibweretsa ku kuzipeleka kwa Kristo.

Pamene panali nthawi imene Adamu, Analibe manyazi, tsopano timabisa manyazi athu. Mwina mwa izi ndi zolowana kuti chobvala ndi chobvalidwanso kudziko la uzimu monga malembo anenera mu nthawi zosasambika. Ngati chobvala ndi chobvalidwa mu dziko la uzimu kumene okhulupirira ali pamodzi ndi Yesu Kristo kotani kotani tsono, mu dziko lino lakugwa kumene kuonekera ndi mthunzi wa zenizeni za kumwamba chodziwilatu ndi kuti ndi zosamveka ndi kulakwitsa kupititsa patsogolo zolingalira chabe popanda ndi chitsimikizo cha malembo, kuti maliseche ali bwino pamene tili akristo ndiye tembelero linachotsedwa kubvala kwathu, pa thupi zimaonetsera pa zimene zili kumwambako. Pamene tsiku la ukwati lidzafika ndi pamene temberero lidzaphwanyidwa chobvala chabwino ndi chithu chokongola!

Tiyeni tikondwere ndi kusekera kwa kukuru ndi kumupatsa ulemelero pakuti tsiku la ukwati wa mwana wa nkhosa wakonzeka yekha mkwati chobvala chabwino chowala ndi chaunkhondo, chinapatsidwa kwa iye kuti abvale. Chibvumbulutso 19: 7-8

Gawo Lachitatu

Zitsanzo za zochititsa Manyazi za Maliseche.

Nikulamulira iwe kuti ugule kuchokera kwa ine nsalu ya ombedwa bwino mu golide wodzera mmoto kuti ukhale wa chuma ndi chobvala choyera ubvale kuti ubise manyazi a maliseche ako. Chibvumbulutso 3:18.

Yerusalem walakwa koposa ndipo waikidwa monga nsanza kutali ndithu. Amene ali kumutamanda iye tsopano ali kumupeputsa chifukwa aona chamanyazi ake ndi kuyalutsidwa chimene angachite ndi kubvala ndi kubisa nkhope yake. Maliro 1:8 NLT

Noah munthu wa nthaka anapita nabvala vinyo mmunda ndipo anamwa mowa wina nakhuta, ndi kugona maliseche mkati mwa nyumba yake Ham. Atate a Cannan anaone Atate awo maliseche ndi kuuza abale ake kunja koma Semu ndi Japeta anatenga chobvala ndi kuika pa mapewa awo ndiye anayenda cha mbuyo ndibisa maliseche a Atate awo maso awo anaona kumbali kwina kuti asaone maliseke a atate awo.

Pamene Noah anauka kuchokera ku mowa wake ndi kuona zimene mwana wake wang’ono anachita anati kwa iye. Atembeleledwe Cannan! Adzakhala ochepetsedwa kapolo wa abale ake. Anatinso madalitso kwa Ambuye Mulungu wa SHEM ayenera Cannan kukhala kaporo wa SHEM zikuoneka kuti Noah popanda chidziwitso pa zomera zimene zimapanga mowa zinamutengera ku ngozi yoipa.Genesis 9 :20—26

Noah sanatenge posintha zobvala za usiku pamene iye anali mtulo motero taonani zimene SHEM ndi Japheta anachita pamene anabisa umaliseche wa Atate awo popanda kuwaonerera. Cholungama chopelekedwa ku thupi la maliseche. Ham anatemberedwa poonerera umaliseche wa Atate ake ndipo enawo anadalitsidwa. Mulungu anamerelatu kuti maliseche ndi chinthu chobisika. Amenewa anali abale eni eni a thupi ndi mwazi. Taganizirani za zimene zili choncho moteremo sikwabwino kwa ife kutsutsa Mulungu pa zimene anatiuza ife zokhudza mabvalidwe. Angakhale ndi abanja athu. Ndizosadabwitsa kuti satana akuyeretsa kuti maliseche osati asabvekedwe komanso atamandidwe! Dziko limakonda thupi lopanda chobvala ndi maliseche mu maonekedwe ena ndi ena. Sitinakhale ndi manyazi kapena ndithumazi kapenanso chisoni ndi makhalidwe a ife lero lino? Monganso Shem ndi Japheta tiyenera kukhala ndi mantha akulu za umaliseche ndi mizera ya njira ya Mulungu.

Mulungu anati tulukani pakati pano khalani woyeretsa kwa Mulungu. Mungaone mmene satana walionongera dziko kudzera ku zolengedwa pa wailesi ndi mieso ya thupi kutizungulira ife? Ngati anthu “abvomera” ndi zathu zothina kapena zoonetsa thupi kapenanso chobvala chosokedwa ndi masokeledwa oipa zoona tizitsatiura mu khungu ndikulowa mu dzenje? Muyezo wa dziko lapansi ndi olowa pansi monganso makabutura ndi masiketi alili ntahwi zonse. Kukhalira mu nyengo ndi chikhalidwe kulowa pansi, pansi kuli kukulira kulirabe kwa oyera mtima wa Mulungu ndi kwa mwana wa Nkhosa tiyenera kuti tione! Taonani ndi muganizire chipangano chakale malemba ake a Atumiki oyera a Mulungu.

Upange nsaru ya mkati yophimba thupi lonse kufikira mchiuno mpaka mu mtchafu. Aaroni ndi ana ake ayenera kubvala pamene ali kupita ku chigona chokomanirana kapena kulowa ku gulu la nsembe kutumikira mu malo woyera kuti asalakwe ndi kufa. Ekisodo 28:42

Mulungu anali kunena mwachindunji za nsaru ya mkati mwawo! Ndipo anali pachiopsyozo cha imfa ngati osabvala chobvala cha mkati mu njira imeneyi kuchokera mchiuno mpaka mu maondo imfa! Zinali zofunika kwa iye Mulungu ndipo talingalilani pangono za maganizo awa. Pamene Mulungu ananena za chobvala cha mkati kuchokera mchiuno mpaka mchafu. Zimene tizitchura ife kabudula. Ndiye kuti kabundula ndi woyenera mu maso a Mulungu? Tinene moona kuti sitikudziwa yankho lenileni la funsoli. Mwina kapena ai. Nthawi zonse Mulungu amaika zinthu pa mitima yathu ngati taslumikizika ndi iye (osati ndi malamulo okha) mantha ndi kunyada, kapenanso kusasamala mukukhala osati mu umulungu) koma tiike mutu wathu patosogolo ndi kukhala ndi maganizo okonda pa zimene Mulungu akonda ndi kudana ndi zimene adana nazo munthu wamkati kukhudzidwa kuyenera kumangidwa kulingana ndi maganizo a Mulungu osati ndi zochita za maganizo a dziko.

Apanso pali malemba a bukhu la chipangano cha kale

Musapite kumwamba kwa guwa la nsembe mwamba, kuti maliseche anu angaonekere. Ekisodo 20:26

Mulungu sanali kulora kuti pakhale chokweza popitako kuguwa lansembe kuti maliseche a mtumiki a Mulungu asaonekere pamene ali kukwera pa mwamba taganizilani zimenezi. Anthu amenewa mmene tinganenere anali ndi mikanjo yawo yobvalidwa kuwonjezera ku zobvalidwa mkazi mwa thupi lawo kubvalidwa kuchokera mchiuno mpaka mtchafu. Kodi panali mwawi wowona maliseche awo panalibe? Zikuoneka kuti Mulungu sasamala zakuti thupi lidzioneka.

Kodi tikupeza upambana ndi zokhudza nkhani yonseyi? Mwina ai. Ali ndi maganizo ndi malingaliro za mmene timabisira ndi mmene timabvalira ife tokha. Lankhulani ndi Atate za izi pamene muli kuwelenga. Pamene tikutenga maganizo a Mulungu ndi modeka zimatilora ife kuganiza pa zimene timaganiza za kabvalidwe.

Apa palinso malemba ena amene amasonyeza kuti Mulungu amasamala malingaliro a mtima ndi mmene anthu angazisamalire okha.

Komanso Yehova ati chifukwa kuti ana akazi a ziyoni angozikuza adakweza makosi ao, ndi maso ao a dama nayenda nayang’ana pofunda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao, chifukwa chake Ambuye adzachita nkhanambo paliwombo la ana akazi a ziyoni, ndipo Yehova adzabvundukula mchiuno mwawo. Tsiku limenelo Ambuye adzachita zigwinjiri zao zokoma ndi zitunga ndi mphande mbera ndi makoza ndi nsaru za pankhope ndi zisada ndi maunyolo a kumwendo ndi mipango ndi nsupa zonukhira, ndi mphinjiri mphete, zipini, Malaya a paphwando ndi zopfunda ndi zimbwi, ndi nduwira, zophimba ndipo padzakhala mmalo mwa zotsekemera mudzakhala zobvunda ndi mmalo mwa tsitsi labwino dazi, mmalo mwa cobvala chapa chifuwa mpango wachiguduli zipsera mmalo mwa ukoma. Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako mnkhondo, ndipo zipata zache zidzalira Maliro ndipo iye adzakhala bwinja nadzakhala pansi. Yesaya 3:16—26 NLT

Azimayi a ku Israel anali okhudzidwa ndi kukongola kwawo ndipo linali chobvunda pamaso a Mulungu tazungulidwa ndi anthu amene azimayi aikidwa ndi maganizo oitana maso a amuna ndi kukopa poononga maso awo chidwi ndi makongoledwe awo. Uchimo uwu uli kuchitika moyonekera ndithu, ndipo ngati kuti pali chobvuta malingana ndi malingaliro a dziko lapansi. Koma tiyenera kudziwa mu mtima yathu ndi chibvunde ndi chosaloledwa kwa Mulungu zikhalenso choncho kwa iwo amene anagulidwa ndi mwazi was mwana wa nkhosa kuti akhale opanda chilema ndi banga.

Oyera a Mulungu kumbukilani kuti ife ndithu mkwatibwi wake. Tiyenera kutitithetse tokha ndi dziko ndi kubvala tokha ndi mwinjiro ya chilungamo cha Mulungu (onani Yesaya 61:10) tizipatule ife tokha ku zinthu pa zimene dziko laphunzitsa ndi zinthu zimene thupi pa zimene tzphunzitsidwa kuti ndi zaphindu Kanani zowonadi za inu nokha monga kuganiza zoti ndinu wooneka bwino ndiye kumamva bwino kwambiri kukhala mbali ya kumidima. Ambuye, tithandizeni kuti tiphwanye kuzindikira tokha ndi kulowa kuti njira ya kubvala kuti ikhale yabwino kwa anthu ena. Tikutamandeni Ambuye mu kukongola kwa chiyero (1 Mbiri 16: 29)

Chinanso chionetsera cha maganizo a Mulungu pokhudzana ndi maliseche amapezeka mu bukhu la Ezekiel 16. Pano Yerusalem akufanizilidwa ndi mkazi:

Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadule nofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi sanakuthira mchere konse, kapena kukukulunga msaru ai, panalibe diso lina kuchitira chifundo, kukuchitira chimodzi chonse cha izi, kukuchitira iwe nsoni, koma unatayidwa kuyere pakuti ananyasidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwako. Ndipo popita ine panali iwepo ndinakuona uli kubvinizidwa mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe mwazi wako, khala ndi moyo inde ndinati kwa iwe mwazi mwako, khala ndi moyo. Ndinakuchulukitsa ngati mphindu za kumunda ndipo popita ine panali iwepo ndi kukupenya taona nyengo yako ndiyo yakukonda, pamenepo ndinakupfunda chofunda changa ndi kuphimba umaliseche wako, inde ndinakulumbira ndi kukupanga nawe ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.Ezekeil 16:4-8

Ichi ndi chinthunzi chabwino ndi cholera mu njira imene Mulungu amaonera ife thupi lathu ndi mmene ali ndi chifundo ndi moyo wathu otaika. Anatipeza ife kumbali kwa iye monga athu amene tili mu mwazi okha okha ndi maliseche (tsiku lobadwa) mu zamanyazi ndithu. Kuchokera mu kukoma mtima kwake ndio chikondi kwa ife. Anatisambitsa ndi kutifunditsa umaliseche wathu.

Mulungu anapereka mwana wake Yesu kuchokera mu chikondi chozama kwa ife kuti apelekedwe monga ku uchimo mmalo mwathu. Nsembe ya Kristu ndi kukhetsa kwa mwazi wake mmalo mwathu ndi chifundo cha Mulungu ndi kutisambitsa kwa miyoyo yathu ndi mmene njira mmene anatiphimba umaliseche wathu ndi kuchotselatu chosalungama chathu ndi manyazi athu. Chinthuzi cha Ezekiel ndi choonekera motero. Onenetsani kuti Mulungu anati zofuna zathu zili ngati umaliseche ndi zopanda pache. Kupatula iye ndi chikondi chake. Alemekezeke Mulungu wathu potichitira chokoma, kutisamala kutisambitsa ndi kutimveka ife ndi mwazi wa mwana wake amene anamutumiza!

Mwachoncho pa nthawi zina, pa zaka zopitilira 6000 zapitazo Mulungu poswa zimene zinali kutsatilidwa pa chiyero chake monga zakhuzidwira ku mabvalidwe (monga ndi Yesaya ndi Hosea) anali kuonetsera chiweluzo chake! Mwa zonsezi, anali kufunabe mkala pakati (Kazembe) mu mbadwo umenewo kuti aphwanye tembelero monga Yesu anachita. Tembelero ndi limene lidamuphetsa iye pa mtengo (mtanda) kuonetsera chake kwa munthu wa uchimo, umaliseche wa Issaih sunali kuyesera pa kuchita. Tembelero limene linali kwa munthu koma kuonetsera mkwiyo wa woyera umene anali nawo.

Gawo Lachinai

Ndi lero?

Ndi zonse zimene taona mu malembo woyera zokhudzana ndi zamaliseche, zikukudza bwanji moyo wathu, munjira yooneka? Tiyeni tiganizire za zinthu zina zimene choona cha umaliseche utifikira ife pafupi ku nyumba zathu lero lino.

Kusambira Kunyanya

Sizoti ndi zololedwa, koma zimanenedwa ndi machitidwe a dziko lapansi kuti kubvala kofafana ndi kabudula wang’ono wamkati, ndi kumayenda, kusambira, kukhala, ndi kutambalala patsogolo pa anthu onse amene ali kufuna kuti akuonere. Timaonetse latu thupi lathu lonse pa mtunda lonse ndi kuonetsa thupi lathu kwa anthu onse kwa alendo angakhalenso kwa abwenzi. Ndipo takhulupirika popatsira zinthu zotere kw aana athu ndi kuwaphunzitsa kuti zili bwino kuti kusabvala bwino ndi kubvala kotere ngati ndi padziwe kapenanso mbali mwa nyanja zonsezi zikuchitika mu dzina la kusangalala (kupumula) ndi kulimbikitsa matupi.

Ganizilani za izi zaka makumi asanu apitawo (50) zinali zobvuta kuonetsa matupi athu mu njira yotere ndi anthu osazindikira chabe amene amaganiza zotere motero kuyambilira kwa zaka zapitazo. Amayi ndi zobvala zosambira zowoneka kuyambira pakhosi ndi mchafu. Mabvalidwe otchedwa (Victorian) koma pang’ono ndi pang’ono kubyola mu nyumba zowulutsira mau ndi zamalonda. (satana ndiye ochita zimenezi) nthumazi yathu ndiye zamizidwa ndi kusakhala ndi umulungu.

Bvalani motero pitani patsogolo ndipo bvulani angakhale ndi kabudula wa mkati wanu. Yendani, thamangani zungulirani poonetsera kwa anthu onse amene afuna kuti akuwoneni kuti maso akhute ndi zotere. Ndi zoipa kodi? “chabwino,” Mdani amati Mulungu sakudzidwa ndi izi ndi zabwino ndithu zongocheza, chonde taganizaninso kachiwiri tagula bodza ili kuchokera kwa mdani wa Mulungu kuti tikhoza kukhala osabvala ngati ndi kusambira chabe kunyanja, ndiye chipatso cha kukumbatira ndi kusasamala ndiye zotsatira za chilakolako cha maso nsanje, zakutha ndi mpikisano wa thupi ndi kuonongeka kwa umunthu, kwa ongoyamba uku ndi mayeso abwino kuti inu muganize zimene timati sikulakwa kuti mungaganize bwanji kuti muone kuti muli ndi munthu mu chobvala cha mkati ndi kapisholo pa gome la chakudya chanu. Pafupi ndi ine mu Restaurant kapena kuti onse olandira ndalama mu sitolo onse ali mu panti ndi makasitomala ndikuganiza kuti mukhumudwa ndi kuganiza kuti sizili bwino pamabvalidwe otere. Koma mumuike munthu wa mkati ndiye kenako ndi kumabvomeleza kuti ndi zabwino ndi zobvomeleza chifukwa? Bwanji ndi maganizo awiri otere. Mwina zili bwino ndi malo otero osati choncho ai? Ngati ndi bwino kuti anthu akuone uli mphempete mwa nyanja ndi chobvala cha mkati koma osati zabwino mu shopu kapena mu Restaurant ali maliseche, nanga chabwino mu nyumba ya charichi? Kodi mungakhale ndi ana anu muli bwino pa bwalo lochezera ndi alendo onse pamodzi ndi kukhala ndi mabvalidwe otere mu kabudula wa mkati? moteremo sichoncho ai. Chasintha chiani? ndi maganizo athu chabe amene asinthidwa.

Mdani watinamiza potiuza kuti zili bwino ku zinthu zina powonetsa thupi lathu pa maso pa anthu ndi kuti maso athu okopeke kwa amuna kapena mkazi amenewa kufuna kuona zonse. Kodi ndi zabwino zimenezi. Tinene zoona, zoona ndi izi palibe mwana wa Mulungu ali ndi kubvomelezedwa kubvala chobvala chimene chili chobvala cha mkati ndi kupita kumalo owonekera anthu. Choonde musalore ana anu kuti akule ndi kuti kusabvala bwino ndi zabvomelezeka pokhapo kuli munadzi pa mtunda pa nyanja. Ndizoonadi po zimapangitsa Yesu kukhala okwiya Luka 17, 1-2.

Zolengeza

Mbali ina ya maliseche ndi imene ili kumbali ya zolengeza malonda pawailesi mapepala monga zolengedwa za opanga zinthu zamalonda. Kuonetsa azimayi ali mu kabudula wamkati (chino-chino) zikwangwani zoonetsa maliseche. Zobvala zowonekera mkati kuika pathupi zothina zogwira thupi zopezeka mu masitolo apamwamba. Ana okuwona ndi abambo wonse kuona zotero: zathupi zimene tinapangitsa kukopa chilakolako cha amuna ndi kudzazitsa maso ana pazimene sanakayenera kuona. Panonso ndi chitsanzo cha zimene dziko labvomeleza kuti ndi zololedwa kudzera njira ya makono mu zolengedwa malonda) kuonetsa mitundu yowoneka bwino. Luso lapatali ndi kusindikiza pa mapepala ndi kuonetsa zamaliseche. Chabwino kodi ndi zabwino kuona mu News pepala. Zolengeza malonda kapena zamaliseche zolengeza. Mapepala okhomedwa mu gawo la zogulitsa zobvala. Kodi ndi zoona kuti zolaula zikhale zoikidwa kwa ulere ndi kuti zili bwino. Ndikuganiza kuti sichoncho wina onditsutsa angati ndi zolengeza chabe basi, taisiyani ndi choncho? Tikubvala mbeu ya mtundu wanji kwa ana athu mu maganizo awo ndi mmalingaliro awo? Kukwelezera mafuta amene amachita nkhondo ndi maganizo ndi malingaliro ndi mitima ya woyera mtima a Mulungu zisamachitike motero!

Nthawi Zina Zapadela

Chifukwa chiani nthawi yapadera? Zimene zimaloledwa kuti munthu abvale kabudula wa mkati kapenanso zopanda zomangira kumbuyo monga zobvala zonse zili. Paukwati, kapenanso pa mgonero ndikumachitika motero. Koma mwana wa mtsikana ukhale ndi T-Shirt yotegula kumbuyo kuwonetsa msana yonse ndi kumabwera ku charichi kwanu.

Mukuganiza bwanji pa zoonetsa matupi mu machitidwe otere osati monga zikamayenera kukhalira? Kodi tikubvomereza kusabvala bwino (kusamvera 1Tim 2) chifukwa cha chikhalidwe choikidwa ndi kukhakitsidwa ndi zopezekapo? Kodi siuchimo?

ZAKU CHIPATALA

Talingalirani za ntchito ya chipatala kutibvula zobvala za mkati, kapenanso kukwiya chobvala. Kodi sizinabweletse mabvuto kwa anzathu amene ali madotoro, madotolo ndi anamwino pamene ali ife. Hmmm chifukwa ali ndi chikalata chowabvomeleza pa chipupa ndiye kumaswa mtima wa Mulungu ndi kutibvula maliseche athu mu machitidwe otere. Pafupinso ndi alendo? Kodi tinagamiza kawiri za zimene kw aife tokha ndi kwa ana athu? Chifukwa chiani ________________________ tikuchita chotero kwa ena kwa munthu chifukwa cha udindo patsogolo pa dotoro kapena namwino ndi kumaloledwa kubvula pamaso pa Dotoro? Kodi tikuona kunama kumene ife talowamu.

Sitikuti tiwasale ma Dotoro koma ndi nzeru ndi kuganiza kuti ndikwabwino kupeza amene ali ofanana nawe? Ngakhalenso kukhala ndi zobvala ngati kungatheke kutero? Sichisankho chanu chotere, ntchito ya chipatala ndi ya anthu amene tinaitana kuti atithandize. Sikuti iwo ndi mabwana athu, kuti tingakhale patsogolo pawo pachili chonse chimene alankhula kapenanso abweletsa angoitanidwa kuti atithandize pa zinthu zina. Osabvula pamenepo Mulungu ndi Mulungu iwo simulungu ai zinthu zina ndi zotheka kuzipatutsa, monga kumalo kutumbulira munthu kumene sikuloledwa chobvala china chimene munthu amabvala. Koma kodi sitiyenera kudziwa kuti tisagule bodza limene limati maliseche ndi abwino limene lili mu ntchito ya zipatala? Sitingathe kukana bodza limene sitifuna kuti tifunse zamanyazi mu office ya Dotoro chifukwa kuti zonse zowonetsedwa kuti ndi za ntchito basi ndipo zili motero. Tiyeni tikhale ndi Mzimu ozindikira ndi tcheru pa zinthu zimenezi. Akunja ndi a kunja. Kaya amabvala motani mu machitidwe ai koma mau a Mulungu ali chikhalire owona. Kodi timadziwa kuti ophunzira aku chipatala kuti amabvulidwa pamene ali kuphumzira za chipatala? Mu kuphunzira kwa zachipatala ophunzira amafunsidwa kuti ayese anzake ophunzira ali maliseche! Ndizokanidwa zimenezi. Ndikwabwino kupita ku maphunziro otere ndi kukana mau a Mulungu? Kuyang’ana maliseche ndi cha manyazi ndipo ndi choipa chokanizidwa. Kulembedwa ntchito kwa madotoro ndi anamwino kumafunika kuti ayang’ane maliseche athu ena) kusambitsa odwala, (giving shots) kuwatumbura, kuwayesa ndi zina zotero) tingatani kwa ife amene tagulidwa ndi mwazi wa mtengo wapatali wa Mulungu? Kodi chofunika kwa ife ndi chotani? Zosamalira zathu… ndi ulemu uli pa ife monga ansembe a Mulungu?

Chisunzo

Palinso chitsanzo china chimene kusabvala bwino kukuchitika tsiku ndi tsiku mu dziko la chisunzo. Mu dzina la chisudzo kaya ndi zolemba lemba zosema kaya ndi zoumba timalora zochititsa manyazi ndi zolaura kuti ndi zabwino ndi kubvomelezedwa. Timati ndizoyelekeza chabe. Dziko limati ndi zinthu zimene zimayeneredwa kutamandika. Kwa zaka zambiri azisunzo otchuka akala kukweza zolzura kuti ndi zabwino ndipo dziko limati zili bwino. Koma sizakhale choncho kwa na a Mulungu. Tatengedwa kuchokera ku ufumu wa mumtima ndi ulamuliro wa Satana ndi mabodza ake onama tiyeni tisinthike pokonzanso malingaliro athu. Zoumba zamaliseche ndi zololedwa kuonetsedwa angakhalenso mu malo a chipembedzo. Ndizoipa kuti zili kuloledwa mu maikidwe otere poterenso kwa anthu a Mulungu. Kodi sanati Mulungu kuti maliseche ndi chamanyazi.

Gawo Lachisanu

Kukongola Kofanana Ndi Mulungu

Monga Yerusalem, Mulungu kawiri kawiri amamunena iye ngati mfumukazi, mukazi, mukazi wokodzedwa kukwatiwa kwa mwamuna wake. iye ndiye mkazi wokongola wa Mulungu. Mkazi wokodzedwa kufikila Kristuyo. Ife ndife mkaziyo, anthu amene Mulungu akuwakaza. Ndi chinthu chofunikira kwambiri kuwona ulemelero wache. Ndipo kulemekeza kutenga chinthunzi thunzi chakuti ife ndife ayani.

Ndipo chifukwa chiyani ife tiyenera kukhala ndi mtima woyera kwa iye.

Estere ndi chinthunzi thunzi cha mkaziyo, kapena mpingo.

Ndipo iye adalera Hadasa, Ndiye Estere, mwana wamkazi wa Atate wace wang’ono, popeza iye analibe Atate kapena amai ndi namwaliyo anali ndi maonekedwe okoma, ndi wokongola. Ndipo atamwalira Atate wace ndi mai wace,Moredekai anamtenga akhale mwana wace.

Pofika tsono kulowa kwace kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wang’ono wa Moredekai amene adadzitengera akhale mwana wace, kuti alowe kwa mfumu, sanafuna kanthu koma zonena Hege mdindo wa mfumu wosunga mkazi ndizo.

Ndipo mfumu yidamkonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye ku ndi chifundo pamaso pace , koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pace, namuyesa mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti. Estere 2:7,15,17

Uneneri wokhuzana ndi Kristu ndipo Ukwatibwi wace:

Mwa omveka anu muli ana akazi a mafumu. Ku dzanja la manja lanu aima mkazi wa mfumu wobvala golide wa ku ofira. Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tachera khutu lako. Uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako. Potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako: pakuti ndiye Mbuye wako: ndipo iwe ungwadire iye. Ndipo mwana wamkazi wa turo adzafika nayo mphatso.

Acuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu. Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse mkati mwa nyumba: zobvala zace zopangidwa ndi golide. Adzamtsogolera kw amfumu wobvala zamawanga mawanga:—anamwali azace omtsata adzafika nao kwa inu. Adzawasogorela ndi chimwemwe ndi kusekerera: Adzalowa m’nyumba ya mfumu. Masalmo 45:9-15

Uneneri okhunzana ndi mkazi wa Mulungu, Anthu ake

Chifukw acha Ziyoni sindidzakhala chete ndi chifukwa cha Yerusalemu. Sindidzatuluka kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera ndi chipulumutso chache monga nyali yoyaka ndipo amitundu adzaona chilungamo chako ndipo udzachedwa dzina latsopano limene mkamwa mwa Yehova mudzatchura. Iwe udzakhalanso limene mkamwa mwa Yehova mudzatchura. Iwe udzakhalanso korona wokongola mdzanja la Yehova, korona wachifumu mudzanja la Mulungu wako. Iwe sudzachedwanso wosiyidwa dziko lako silidzachedwanso bwinja koma iwe udzachedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula. Pakuti Yehova akondwera mwa iwe ndipo dziko lako lidzakwatiwa. Pakuti monga mnyamata akwatira nambali momwemo ana ako amuna adzakwatira iwe ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.Yesaya 62: 1-5

Chifundo cha Paulo:

Pakuti ndichita Nsanje pa inu ndi Nsanje ya Mulungu. Pakuti ndinapatsani ubwenzi mwamuna mmodzi kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Kristu. 2 Akorinto 11:2

Bvumbulutso la Yohane:

Ndipo ndinamva ngati mau khamu lalikulu ngati mkokomo wa madzi ambiri ngati mau a mabingu olimba nizinena Aleluya: pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu wamphamvu zonse. Tikondwere tisekere ndipo tipatse ulemelero kwa iye pakuti wadza ukwati wa mwana wa nkhosa ndipo mkazi wake wadzikonzera ndipo anapatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu, pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima. Nsaru za bafuta ndi makhalidwe olungama a woyera mtima. Chibvumbulutso 19:6-8

Ndipo ndinaona mzinda woyerawo Yerusalem watsopano uli kutsika kumwamba kwa Mulungu wokonzeka ngati mkwati wokometsedwa mwamuna wache ndipo ndinamva mau akuru ochokera ku mpando wa chifumu pa anthu ake ndipo adzakhala ndi iwo pamodzi. Adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwani adzakhala ndi anthu ake ndikukhala Mulungu wawo. Chibvumbulutso 21:2-3

Uneneri wa Ezekiel ukudzana ndi Mzinda woyera:

Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinasuka, kukucotsera mwazi wako ndikukudzodza mafuta, ndinakubvekanso ndi nsaru zophikapika ndi kukumveka nsapato za chikopa ca katumbu ndinakuzenenga nsaru ya bafuta ndi kukuphimba ndi nsaru yasilika. Ndinakukomeseraso zokometsera ndi kuika zigwinjiri mmanja mwako, ndi unyolo mkhosi mwako. Momwemo ndinaika zipini m’phuno mwako ndi maperere m’makutu mwako ndi korona wokongola pamutu pako, ndipo ndinadzikometsera ndi golidi ndi silica ndi yopika pika: unadya ufa wosalala ndi uchi ndi mafuta: ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindula pindula kufikira unasanduka mfumu. Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu chifukwa cha kukongola kwako. Pakuti ndiko kwangwiro mwa ulemelero wanga ndinaika pa iwe ati Ambuye Yehova. Ezekiel 16:9-14

Mulungu amapereka kukongola pa anthu ake, ndipo ife tikhale anthu otere, obvekadwa ndipo opangidwa kukhodzedwa kufikira kwake kwa mukwatibwi. Ngati Mulungu ndi kukodzedwa kwa okondedwa zoperekedwa za mtengo ndi zobvala zokongola. Iye wakunena ndi chifundo, iye wapereka pa anthu ake kuti ayenda muchilungamo. Monga ife tachipereka kwa Mzimu wake mwa ife. Ife tili ndi ulemu wa kuziwonera kukongola kwathu ndi kalirole lache ndi moyo. Ife tinalibe ndi mwai wokhala ndi kukongola kotere mwa ife tokha, koma Mulungu wathu wa m’kulu. Ndipo opulumutsa atipasa ife colowacho kuti ife tikhale “owala ngati nyenyezi kucdziko lonse la pansi, ngati tikugwira mawu a moyo.” (Afilipu 2:4-16) Iye atipasa ife kukongola kuti timangidwe. (Yesaya 61:3) kukongola kwathu kwa mukati wa moyo, umene wofanana ndi chipatso ca Mzimu oyera; “chikondi kusangalala cimwemwe Mtendere, kudekha, kukoma mtima. Chiletso Agalatiya 5:22 23. izi ndi zipatso za mkwatibwi monga takwatiwa, ndalonjeza ife tokha kukhala opanda chilema, usakhala mu za dziko lapansi ndi mdima wake.

Paulo analemba

Amuna inu kondani akazi anu, monganso Kristu anaconda Eklesia nazipeleka yekha mmalo mwache kuti akampatule atamuyelesa ndi kusambitsa madzi ndi mau kuti iye akadzindikire yekha Eklesia wa ulemelero, wopanda banga kapena khwiya, kapena kanthu kotero komatu kuti akhale woyera ndi opanda chirema” Aefeso 5: 25-27

Tingakhale okondwa motani pokhala ndi kulandira masiku athu padziko kukonzekera opanda banga mkwatibwi okongola! ndi mdalitso waukulu ndi kudala polandira ndi kugwira ntchito ya Atate mmalo mwa mwana wake Yesu.

Zingakhale zotani zonsezi ndi mabvalidwe. Ndi chiyembekezo tikupeza kuyamika kuti ndi chiyero, opanda banga ndi kuima mu miyoyo yathu pakufunika Mulungu. Tikukhala ndi chuma cha mtengo wake mu zotengera za dziko lapansi lotchedwa matupi. Tili ndi mzimu wa Mulungu ngati tibadwa kuchokera kwa iye. Timasunga Mulungu wa kumwamba, mlengi padziko lapansi pamene tili mtupi lathu. Taonani zoterezi! Kodi izi sizingatsitsimutse mitima yathu pokhala ndi udindo ndi kanthu ndi chiyero! Pakuti matupi athu sali aife tokha koma ogulidwa ndi dipo sitingakhale ndi maganizo kuzisamalira tokha. Ndi tcheru pa nkhani ya kubvala? Osati pa zimene timabvala koma limenenso timabvalira?

Monganso mkwatibwi yakonzekera kukongola opanda banga kwa mwamuna wake yekha. Anapangidwa chifukwa cha iye 1Akorinto11:9) osati wa dziko lapansi kapena kwa zakutha. Pakuti talamulidwa kuti ukwati uyenera kulemekezedwa ndipo.

Ndipo pakama la ukwati payenera kukhala poyera (Ahebri 13:4) sizingakhale zabwino kuti matupi ndi maonekedwe kuti aonekedwe ndi munthu, mmodzi yekha amene ali mkazi wathu? Kodi simiyoyo ndi matupi athu ali mphatso yopelekedwa mu mkati mwa miyoyo yathu?

Pamene nkhani ya mabvalidwe ibwera ena ngati, kodi sizabwino kuti mzimayi adzioneka bwino? Sizimene Mulungu anapeleka, inde Mulungu anapereka koma ndi kwa mwamuna yekha kwa iye yekha. Ngati mphatso ya iye yekha basi iye thupi la mkazi silili kwa iye yekha komanso kwa mwamuna 1 Akorinto 7:4 sili la dziko lapansi la abale ena ngakhalenso kwa iwe wekha kuti ungakhale ndi kutamanda wina ndi zopita.

Izi ndi zitsanzo za kuyera ndi kukongola kwa kuyankha kwa mkazi wokongola kwa okondedwa wake ngati mungaimilire nokha mu moyo umene Mulungu anaonetsa mu chithunzichi moyo wanu udzaimba ndi kumwetulira kapenanso kulira pakukongola kwache.

Ndipo anauka Rabeka ndi anamwali ake nakwera pa ngamira natsata munthuyo mnyamata ndipo anamtenga Rabeka namuka.

Ndipo Isake anadzera njira ya Beerelahai-roi chifukwa kuti anakhala iye mdziko la kuwera. Ndipo Isake anaturuka kulingalira m’munda madzulo, ndipo anaturuka maso ake nayangana taona, ngamira zinali kudza. Ndipo Rabeka anatukula maso ake anatsika pa ngamira. Ndipo anati kwa mnyamata, munthuyo ndani amene ayenda mmunda kukomana ndi ife?

Mnyamatayo ndipo anati, uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake nadziphimba.

Mnyamatayo ndipo anamuuza Isake zonse anazichita ndipo Isake anamlowetsa mkaziwo mhema wa amake Sara, natenga Rabeka nakhala iye mkazi wake, ndipo anamkonda iye ndipo Isake anatonthozedwa mtima atafa amake. Genesis 24:61-66.

Mu Genesis 24. Abrahamu anatumikiza wantchito wake kupita kwawo kukapeza mkazi wa mwana wake Isake. Wantchitoyo anapita ku malo otchedwa Nahor ndipo anampeza Rabecca. Namwali, bunthu okongola.” (Vesi 16) wantchito analankhura ndi Atate ndi alongo ake Betula ndi Laban ndikufunsa kuti Rabecca akhale mkazi wa Isake. Anati, uyu ndi Rabecca mutengeni ndi kupita lorani iye akhale mkazi wa mwana wa bwana wanga, monga Ambuye walankhulira. Rabecca anabvomereza kupita ndi watchitoyo pamodzi ndi one.

Onetsetsa pa zimene Rabecca anachita anachita atamva kuti mwamuna wake anali mmunda. Pamene anamva izi anatsika pa bulu ndipo anatibveka yekha. Anali namwali wokongola ndipo pamene anamva kuti ndi Isake mwamuna wake watsogolo amene sanamuonepo adachita chiani? anabisa ulemlero wake kukongola kwake. Kudikilira nthawi ndi malo kumene kukabvulidwe. Kuyankha kwake sikunali kukonza tsitsi lake ndi kuyamba kuseka. Ai, anazibveka yekha mukuzichepetsa ndi mwaubwino ndi ulemu.

Onani tsopano machitidwe amene mzimayiyu anayankha pokhala ndi maonekedwe abwino, kukongola ndi ulemerero unapatsidwa, kwa iye. Mu Ezekiel analemba za mkazi ameneyu Yerusalemu.

Ndipo anadzikometsera ndi golidi, ndi siliva ndi chobvala chake ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika. Unadza ufa usalala ndi uchi ndi mafuta ndipo unali wokongola woposa ndithu. Ndipo unapinndula—pindula kufikira unasanduka ufumu. Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu chifukwa cha kukongola kwako pakuti ndiko kwangwiro mwa ulemelero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova. Ezekiel 16:13-14

Kukongola kwake kunali chifukwa kuti Mulungu anachita chonchochi kwa iye. Mulungu anampatsa kwa iye kukongola kwake kunali kwabwino chifukwa kunachokera ndi kudalitsa kwa Mulungu. Koma kuyankha ku dziko lapansi kunali koipitsa kukongola kwake ndipo anakhala wa chiwerewere yekha ndi anthu ena kuononga kuyera kwa iye ndi kwa mwamuna wake yekha osati kwa ena ai. Werengani pa zimene zimaoneka zinakhala pakukongola ndi maonekedwe abwino kuti ena awone.

Koma unatama kukongola kwako ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako ndi kutsamulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo unali wache! Ezekiel 16:15-16

Anatenga kukongola kumene Mulungu anapeleka ndi zobvala ndi kuzitambasula kwa abwenzi ena. Kwa ena onse odutsapo ndipo kukongola kwake kunakhala kwa iwo monga zinaliri, koma kuchokera kwa Mulungu ndi kwa iye yekha. Ndipo anapitiliza kukongola kwake kwa anthu ena aliyense amene anafuna. Zimenezi siziyenera kuchitika zisamachitike ai.

Kukongola kwathu ndi matupi athu anapelekedwa kwa amuna athu okha. Akazi ali ndi maonekedwe abwino powapenya, ndipo timadziwa mmene tingaonetsere zimenezi pamene tifuna kutero koma ndi uchimo. Ngati tionetsa mosakhala ndi chiyero ndipo ndi mphatso yosadetsedwa kw amwamuna. Sitikunena kuti tisamaonekedwe bwino kwa amuna athu ai. Koma ngati tisamala zotere ndiye kuti mzimu wathu udzatsika chifukwa cha mabvalidwe athu. Ngati tang’amba kuti tidzionetsa makandatchembere musamachite ai. Ndipo ngati mukubisa thupi lanu ndi zopisa zopepera zongochokera pa khosi ndi mchiuno ndipo kuti mukadutsa malire otere. Ndi zotheka kubisa maliseche koma osati ulemelero.

Ndi ndani amene akufuna kubisa zosokedwa bwino ndi bwino kubvala zomangidwa bwino ndi lamba? Sidziko limene limatiuza zokhudzana kuonetsa mbali ina ya matupi athu. Tikayamba kusunga chuma chimene tapatsidwachi ndi chimodzi chokhachi chapelekedwa ndi cholinga chotere. Ndidzapeza mtendere ndithu. Tikapeza mtima wathu pamodzi ndi mosungilamo katundu wathu. Mulungu adzatitsogolera ndi mzimu wake pa zimene zili zabwino ndi kubvomelezedwa ndi mabvalidwe abwino ndi kumasulira kwache ndi kuti tikhale tcheru posakhumudwitsa ena chifukwa cha matupi athu amene ali kwa Kristu ndi amuna athu okha.

Pamene tikuyesa mitma yathu tizifunsenso kuti tikubvala ichi pa chifukwa chotani? Kodi pali gawo lonyada kuchokera mu malaya amene tabvalayo. Kodi tikufuna kuti paonekere pali ponse kwa anthu? Ngati ndife amuna kodi pali kunyada ndi kukula kwa thupi lathu.

Timakonda kuwonetsa kwa miyendo yathu ndi kukwezera kabudula, muwamba kuti tionetse miendo. Tili ndi zofuna kuonetsa, phazi lokha kuti tiyende popanda nsapato mu njira yotere? Ndikumaoneka bwino? Ganizani za zimenezi.

Ngati zina zabwino zimene zili za ife eni zimene ndizabwino chifukwa timazikonda ife eni tamukhumudwitsa Mulungu mtima wake ndi kuika Yesu pambali ndi yekhayo amene ali oyenera ndi kupambana ndi kuganizidwa bwino.

Tilore kuti zonse izi zitakase mozama potidziwitsa pa zofuna zathu kwa iye.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon