Mgwirizano Wodzipereka Wamgwiro

15/11/1991

Ambuye Yesu, ndinu mphunzitsi ndi maonetseredwe athu. Ndipemphero lahtu pamene tisonkhana kuti mbewu ya mawu anu yodzipereka kwa wina ndi mzache ikomze miyoyo yathu ndi maganizo athu ndi zochita zathu. Kukhumba kwathu ndiye kuti ntchito yanu ikhale kuti yakwanilitsidwa munjira yanu, mumtendere ndi muchikondi ndi modzichepetsa, mukulimbika ndi muofunikira zonse tilinazo. Tikufuna kukutsani munjira mmene munagwiritsira anthu ntchito. Chonde tithandizeni. Tikhulipirira inu kuti mudzatero. Singatisiye ife opanda mbusa, koma ndinu mbusa ndi mphunzitsi wathu

Ndife okondwa kuti zobvala zathu sititengera paphewa tokha monga kuzindikilika amene zkahalira. Potero tidzatsata mwana wa nkhosa kulikonse adzapitako. Ife tidzatsata inu Yesu. Tithandizeni ife. Chonde lolani mau anu achuluke ndikulamurila mumtima yathu ndi malingaliro athu, tiphunzitseni kudzipereka kwa inu. Mzimu wanu, ndi umuyaya wathu ndi mau angwiro Ameni. (zikhale choncho)

ZOWAWA ZAKUBELEKA KWA WINA NDI MZAKE

Paulo adati kwa Akristu a ku Galatiya ndili mu ululu wa ubeleka mpaka Kristu ataumbika mwa inu’ “ndipo kwa Akolose anati ndifuna kuti ndidzaze mthupi langa pokamba za Kristu monganso kwa inu mpingo thupi lake” uku ndiko chifundo chenicheni komanso anati, “ali ndi kulimbana popeleka aliyense waphumphu mwa Kristu.”

Ndipo mtudu wa kuzipeleka kotero kumaposa moyo wongokhala phwii pamando, kuimba makolasi ndikudikilinso nsonkhano wina ukadzakonzedwanso, zochititsa manyazi ngati moyo wanu supyola pazimenezi! Ndipo mukulakwitsa kwambili mwatsoka zoterezi zakhala zikuchitika ndi mibadwo yonse yokhalaso mudziko lonse lapansi pano mudzina la khristu, komama ndi zosayenela ndiponso ndi kulakwa, ndiye potelo ndikulangizani kuti muzdzambule khalidwe lotelo! Kutsata ndi kusintha miyoyo ya anthu mu njila yeniyeni.

Aliyese amene awelenga mawu awa ndi wa Msembe wa Mulungu. Ngati iyeyo mwamuna kapena mkazi ali okhulupirila weniweni. Ndipo kuitanidwa kumeneko sikugokhala munsokhano ayi kawiri-kawiri—ameneyo sindiye kuti ndi wa Msembe. Wa Msembe monga mwa mawu a Mulungu ndi mtumiki wa Mulungu ndikupatsidwa ntchito kubweletsa mulungu kwa anthu, ndi athu kwa mulungu. Udindo umewu sindiye kuti mudzapulumutsa aliyese! Pali m’modzi yekha amene ali kuimilila pakati pa mulunngu ndi mtumwi ‘Yesu.’’sitikutathauza kuti tili ngati Yesu wawina aliyense. Koma tingachite monga Paulo adachita polimbikira kupereka aliyense kwa Yesu. Monga iye, mungakhale omva zowawa pobeleka mpaka Nkristu aumbike mwa anthu amene ali okhlupirila. Munganene pamodzi ndi ine, ndili ndi ululu obeleka mpaka odzozedwa aumbike mwa ine—mpaka mukhale muchithnzi ndi muuthuthu ndi chisomo ndi ufulu wa mwana wa Mulungu. Sindingasiye ndekha ndikufa tsiku ndi tsiku mpaka ndione moyo wa Yesu mwa iwe”

Ngati tsopano muli ndi chithunzi polandira mawu awa ndiye kuti mukulakwitsa. Sikuti aliyense angakhale ndi ululu wakubeleka kwainu. Ngati mukuganiza choncho, ndiyekuti mukyenda munchipangano chakale osati chatsopano. Muchipango chakale mumakhala ndi okulakhulilani ambiri pamawu amodzi-monga aneneri, asembe ndi mafumu-mumawazungulira namakutumikilani. Koma iyi sinjira ya Mulungu muchipangano chatsopano, pamene tikumanga ufumu wa a nsembe (1 Pt 2: 4-10, Chivu. 1:6) pokhala nonse ansembe a Mulungu ichi ndiye chifuniro chake cha Mulungu.

Simudzadziwa kutanthauza kukhala mfulu mmoyo mwanu mpaka mutazipeleka pothandiza ena podziwa Mulungu. Simudzadziwanso kukhala mwa Yesu ngati simukhala muchifuniro chake. Zoona ngati mukuganiza kuti muli pachiyanjano ndi Mulungu koma simukubweretsa anthu ena kwa iye, ndiye kuti mukudzinamiza nokha. Paulamulira wamawu a Mulungu, simungakhale ndi ubale ndiye ngati mulibe mtima wothandiza ena monga Yesu anali nawo.

Monga Yesu mwini wake ananena “ngati mukhala mwa ine ndi mawu anga mwaine muzabeleka zipatso zambiri, mudzaonetsera kuti munali ophunzira anga”. Moyo odzipeleka kuntchito ya Mulungu mudziko limene muli ndi chipatso chosefukira mukukhala mwa kristu. Simukhahthe kukhalebe mozama mwa iye mumtima mwanu kufikira mumatsiriziro. Simuzakhala ndi moyo wa Mulungu weniweni ngati simusamala anzanu moona mtima nthawi ya pemphero lanu iokhale yopita kwa Mulungu wa Bukhu lopatulika! Mukhale ndi nthawi yochuluka popemphera, koma monga mwa Yesu, kukhala mwa Mulungu wa Bukhu lopatulika muzakhal ndi zotsatira zabwino, ndikukhala nawo moyo othandiza ena powabweretsa pamwamba munjira yake. “Ndiye kukhala ndi zipatso a ulemerelo wa atate—chipatso chamuyaya.”

Choncho kuokhetsa zonse pamodzi: kukhala ndi moyo wa chifundo, kuhtandiza ena mozama, ndikukhala okhudzika mmoyo mwawo ndiye kumva zowawa.tisangokhala, kuganizira kuti ndife ongolandira mtundu wa kukoma mtima. Tiyenera tikhale opitirira munchikhulupirilo ndikudzichepetsa—titenge zonse. Kukhulupirira mulungu ndi kutaya moyo wathu kwa ena ndichithu chofunika, kuchokera mu chikristu cha bukhu loyera.

Bukhu la Machitidwe Atumwi limati akristu oyambirira amapita ‘kukalalikira’ mawu a Mulungu. Mawu a chigiliki oti ‘kulakhula’ amatathauza kuti ‘Kulalikila’ kugawa mawu ndi chikondi chake ndiye unali mtima wawo ndi chikhumbombo chawo. Amakhala muzinezo choncho mukane, kukhala pansi kunyumba kwanu ndi malemba kungokhazika chabe olembedwa kutsogolo la khomo lanyumba yanu, kukhala ndi mapemphero aphamvu kumawa, pomvetsera nyimbo za potamanda ndi zothokoza tsiku lonse ndikuonekera mmisokhano nthawi ndi nthawi, ndikumati uku ndiye kutathauza kwa chikristu. Zoona zake, simungathe kukhala ndi pemphero laphamvu ngati simunachilitse mabala a osweka mtima ndi kumasula maunyolo amene ali munsinga la tchimo. Umenewo ndiye moyo wa Yesu wa kunazerene, ndiyenso moyo wanu olumikiza kumutu zodziwikiratu.

Chonho zitambasuleni nokha. Sunafunani mozama kuchotsa chilichonse mkati mwamtima wanu. Pachikani mantha kuzikonda ndi makhalidwe amoyo wanu zoyembekezera ndi kutanganidwa kumene dziko ndi satana angakwanitse kuchita kwa inu. Kanani kudzilungamitsa mwainu nokha kapena ulesi umene ungakhale oima patsogolo panu. Chotsani kudzikhulukira nokha. ‘yambani ndipo galamukani’. Ndiye yambani kuchotsa kuzophuthwa mmoyo wnau zimene zimapangitsa kukuchotsani kuti mugwire ntchito ya Mulungu.

Yesu adzakhala mmoyo mwanu ngati muli obadwa pochokera kumwamba, ndipo mtima wanu ndiokhudzika ndi ntchito ya nyumba ya atate. Ndimoto onyeketsa —osati chipembedzo chongoyang’ana kumwamba mmawa uli onse ndikutsatila mawu abodza munsokhano kapena kuonetsera munzeru amaonekedwe a chipembedzo. Mmalo mwake ,ponyani moyo wanu ndi kusintha zinthu, angakhale kuti ndiyoneka motani.Ichi ndiye mayambidwe a chikhrisitu.

Tiyenera ife kukhala muntchito ya atate, kwenikweni, mmiyoyo yathu, payekha payekha—osati mbali ya gulu chabe sitiyakhula za gulu tiyakhula za moyo wa liyense. Musabisare ponena kuti ndine mayi kapena wakutiwakuti, ndiye sindikwanitse zonsezi tayesetsa kuchita. Koma potsiliza ndi Yesu yekha amene akhala mwa ine amene agonjetsa satana mpaka kumapeto. Ndikulimbikitsani kuti mukhale munthu wagwiro, mwachisomo cha ambuye. Ndi moyo otseguka mwa iye, tichotse choipa chili patsogolo pathu.

Osamuyasa Ambuye

Tatsiliza mbali imeneyi ndipo tionenso mbali ina. Pamene muyenda motsogozedwa ndikukoma mtima mosamalira miyoyo ya uzimu ya ena, ndiposavuta pochita zithu molakwika. Kukhala ndi ulamuliro kwa miyoyo kwa anthu ena sizimene tikamba pano ayi. Ndizolakwika kukhala ndi mtima otere kuti munthu aumbike mwa kristu. Kukhala ndi ulamuliro kumiyoyo ya anthu ndimoyo wachifatso. Kwa anthu onse, Yesu sanakhale ndiulamuliro otero ndipo ife sibwino kuti titero ayi mkounika kuti timvetsetse bwino pamutu umenewu.

Mwachitsanzo, tinene kuti ndikufuna kugawana kanthu ndi m’bale wina, chifukwa choti ndili ndi kanthu kamene kamuvuta. Tsopano ngati ndili ndekha ndizamukakamiza kuti amvere ine. Koma ngati zili choncho sindisamala ngati kamva kapena kuzilandila pazimene ndikalakhulezo. Ineyo ndisapindule kanthu, chimene ndifuna ndikuona Mulungu akutamandidwa mumoyo wa m’baleyo. Tinene kuti zaka makumi zapitazo ndinamuthandiza munjira ina. Lero ngakhale anandikhululukira kotheratu leronso akakhala akundimvera pazimene ndikayakhule. Pamenapa pali kusamvetsetsana bwino. Pamenapa ndiye kuti ayenera kundimvomera ine pachomwe ndinganene ine zokhudzana ndi moyo wake. Munthuyyu sikuti ndi oumilizidwa kuti kuchita zinthu kwa ine ayi. Kuumilizidwa kwake ndikumvera mawu amulungu ndikuwachita poyenda nao. Ngati wina wamuthandiza kusintha kotere pobweleta mau ochokera kumwamba amene alandilidwa , ndiye tingoto ,halleluyaah, ndilibe bvuto ndi zoterezo, chifukwa sindikufuna kuti akhale ngati ali kundtdzimikizira ine.Chimene ndifuna ndichoti atsimikizire Yesu yekha.

Nthawi zina Mulungu amatseka dala kuthekera kwathu kuti tisakhudze moyo wa mbale wina kuti potere tizichepetse tokha.Timuthokoze iye kuti ndimdalitso chifukwa sitili ife a ife tokha .Tili Poona kuti Mulungu adzachita mu moyo wa aliyense. Ngati ine sindinathe kulankhula kanthu kwa mbale wina aliyense chifukwa zimene zili motere , chomco zili bwino .Ndiyenera kuti ndikhale oyankhanira nkhope yake. Ngati Mulungu watipatsa undindo wa iye, koma safuna kumva zimene ndinena kwa iye , ndiye ndiyenera kuti ndipemphere ndikusala—kapenanso kungosiya , ngati ndi kotheka .Ngati zafika potere ,ndingosiya ,kusiyana kuononga zonse chifukwa cha kukhala pakati pa zinthu zotere.

Tsopano, Yesu watipatsa machitidwe pochita ndi zinthu zokhudzana ndi chimo mu moyo wa munthu. Sanati kuti ndikaona chimo la mbale wanga, ndiye kuti ndipite ndipitenso…Ndikupitanso kwa iye, mmalo mwake, Yesu anati ndikabweleta kanthu kwa iye ndiye pazifukwa zina sanalandire, ndiye kenako ndibwelese anthu ena. Mateyi 18 amatero, “ngati amvera iwe ndiye kuti wamupambanitsa mbalewo. Koma ngati samvera, tengani mmodzi kapena awiri kuti pazonse pakhale umboni wa anthu awiri kapena atatu , ngati akananso osamvera, muuze mpingo wonse.”

Sikuti Mulungu wandipatsa undindo wa munthu ndiye kuti ndimuzunze ndi kumuika akhale kapolo zikhale kuti ndizinthu zomvetsetseka kwa iye kuti alandire uphungu osati zochita kukonza, Mulungu safuna kuti ubake wathu ukhae wowoneka motero ai. Iye wandiitana kuti ndimubweze ndimawu a chilimbikitso monganso anenera mu 1 Akorinto 5 ndi Mateyu 18. Ngati samvera ine, ndiye kuti Yesu amati mutenge awiri kapena atatu chifukwa choti mmodzi waine angathe kuunikira bwino koposa mmene ine ndingachitire, Ngati mmodzi wa ife angakwaniritse, kuti mpingo wonse udziwe—kenako Yesu anati tengani ena kuti zikhale poyera.

Choncho zili bwino chifukwa sindipindula ndekha sindifuna kuti ndizindikilidwe. Sindifuna kuti ndikondedwe, ndikuti ndiyamikilidwe. Sindifuna kuti ndilemekezedwe. Sindifunso kuti akhale bwenzi lapamtima panga pazofuna zanga. Ndikufuna kuona m’baleyu akuperekedwa kwa kristu mwathunthu. Potero muzochika zonse ndiye kuti zili bwino, zimene zindichepetse ine kapenanso kubweretsa kapenanso kubweretsa mgwirizano weniweni, monga ziyenera kukhalira. Mulizilizonse zochika muzopempha kwa Mulungu ndiye mnjira yache akhale monga mulungu afunira.

Siubale ongoonekera chabe.mfundo ndiyoti ulemerero wa Mulungu ukaonekere mmoyo mwa wina aliyense. Potero Mulungu amanga ubalewo “ngati Mulungu samanga ubalewo umangika chabe.” “Tikuopetsera mulumikizo ochokera pamachitidwe a Ishemael wooneka ngati ubale. Ndizofunika kuti maubale athu amangidwe osati mukufuna abwenzi kapenanso machitidwe mukudzikonda chabe. Tingokhala okoma mtima Poona chifuniro cha Mulungu chilikuchika mmiyoyo ya anthu ena”.

Mumchipanganochakale timamva kuti pomanga kachisi mnyala yolimba yokha ndiye imene imagwiritsidwa ntchito, osati nyundo, kasemasema kapena ndi chitsulo china chili chonse chisamveke pamalo pomangidwa kachisi (1 Mafumu 6: 7), samafuna kuononga kachisi ndizomveka mveka pamene amakonza miyala yoyenerela kumangira nyumbayo. Kachisi wa chipangano chatsopano inali mthunzi wa Mpingo umene kufikira tsopano lino ndikulakhula. Sintchito yahtu kuphoma kachisi poika miyala monga tifunira sitikunena kuti kosafunika kukhala okhudzika mumoyo wa m’bale wina aliyense. Koma pokhudzidwa ndi kachisi wa Mulungu kuti ndiwabwino motani koma chofunika ndichoti mumange chikhulupiriro chawina aliyense osati mokakamiza koma muubale wakufuna kwanu. Izi ndizofunika kwambiri chifukwa monga taona mbali yoyamba ija—kuyesetsa potenga zovuta zomwe zimzmuumbitsa munthu mwa kristu-zikhoza kukhala zosinthidwa

Ngati mungabwere nyumba mwanga ndikuti ndipatseni ine 50-dollar kapena tipeze zithu zonse mofanafana? Chabwino, zilibwino ndilibe mvuto pakupereka 50 dollars chifukwa malemba amatero ngati tipereka kwa Yesu, ndalama yathu siyathu. Koma ngati wina abwera pakhomo ndikuti ndipatseni 50 dollars chifukwa ndife ofanafana muzonse ndikudziwa kuti tili pamavuto mbukhu loyera kuliwerenga munzeru, mwina izi ndi zabwino koma ngati munthu wina agwiritsa malemba molakwika kuti wina apereka, ndiye kuti akutembenuza zinthu. Musapereke 50dollar ngati atabwera modzikonda, modzikweza, ndiye kuti mudzachita molakwitsa. Umu simmene malemba atathauzira ponena kuti zithu zonse ndi zathu. Sizimene mzimu oyera amatathauza kuti anthu mukhale mbuye wwa munthu wina pamene tiyenda ndi Mulungu. Ngati munthu akufuna kukupatsa 5o dollar zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu, osati chifukwa chotchula malemba.

Izi ndizimene ndikulakhula za ubale monga mwa lemba tiyenera kulumikizitsana wina ndi nzake ndi mitsepha yonse koma zisakhale kuti choonadi chikuopseza moyo wamunthu chikwa choti pali mgwirizano ndi ine. Sichoncho zimeme malemba amaphunzitsa. Ngati pali tchimo mmoyo wa munthu, apepherereni. Ngati mufuna kulakhula mmoyo mwawo ndi chabwino. Koma ngati savera inu musakakamize, musakakamize, ndiponso musakakamize.

Ngati muli ndi chitsimikizo choti mwaonadi tchimo ndipo muli kufuna kuti muchitepo kathu ndipo mukufuna kuti mboni ziwiri kapena zitatu, ndipo pitilizani ndi zimene Yesu anaphunzitsa. Koma mukhale osamalitsa pachimene mukfuna kuti anthu achidziwe chifukwa mudzapezekanso kuti ndinu amene mukulakwa. Ndipo ngati ndi choncho ndiye kuli bwino mudziwiretu.

Nthawi zina zaka zapitazo munthu wina ati kwa ine “muyenera kuti muchite izi ndithu ndikuona uchimo painu”

Ndinayankha kuti ndizoona kuti ndi ntchimo?

Ndizoonza kuti ndi ntchimo anatero.

Chabwino chonde bweretsani anthu awiri kapena atatu chifukwa ine ndikuona ngati sintchimo.

Munthuyo anati, chabwino mwina sintchimo koma maganizo opitilira oitana mboni zingapo sanachitike. Ndifukwa chake kuti Yesu anapereka zithu izi kuti zikhale mwadngosolo lotero. Aliynse akhale ndi mwayi odziwa mmene zili pamene mwadweletsa awiri kapena atatu.

Choncho kukoma mtima kwa anthu ena ndikofunika komabe pamene mupitiliza musapoteze machitidwe akudzipereka kwanu, monga ngati uja anabwera ndi kufuna mumpatse 50 dola chifukwa choti tonse ndife ofanana. Ngati mudzatero ndiye kuti mudzakhala mukulaakwitsa kuti anthu ena ayende bwino ndi Mulungu, ndipo adzalephera kuti azipereke ndipo azakhala okhumudwa ndipo adzonetsa kukhumudwa kwao mmalo moonesa chikondi chawo kwa Mulungu.

Ndinamva wina wake posachedwa kuti anali omanga chikhulupiriro, osakhala nyundo. Izi ndizabwino sichoncho? Nditero ine ngati ndikulemba pakalata ndi chisankho choti ndizagwilitsa bukhu loyera Encyclopedia Britannica kapenanso kuchokera mu Today Show (ili ndi bukhu) kapenanso computer almanac zimenezi ndizopezekazo kuti zitithandize. Sizithu zimene zikundiumiliza ine koma kuti ndili ndikuthekera kuti ndizipeze koma osati ndiliomilizidwa kuti ndipeze zimenezo. Poteronso tiyeneranso kuti tikhale otero obweretsa machitachita kwa anthu ena koma osati kukhala nyundo mngakhalenso ndi nyundo zabwino! Muonetsetse kuti mukhale otseguka pokhulupilika ndipoona mtima kuti musakhale mwazikundikira zithu nokha. iyi ndiye mbali yolimbana kuti ena aperekedwe athuthu kwa akristu. Zimene takhala tili kulakhulazi motero khalani omva zowawa mululu wakubeleka mpaka kristu aumbike kwa ena koma muchite ichi mwa machitidwe okoma. Musaononge munjira ina iliyonse monga ndafotokozera muja.

Kudzipereka Kugwirizano Wangwiro

Kumbukirani nyimbo ya ana uyu ndiye mpingo ndiyonso nsanja yake tsegulani chitseko ndipo awa ndiwo anthu onse? Awa ndiwo maganizo akuya ndiinso zimene zakhala zikuganilizidwa monga momwe zilili lero lino monga maonekedwe ampingo. Iyi ndiye njira yake wuunso ndiwo nsokhano wake. Awa ndiwo ndondomeko yake ndipo iyi ndiyo zochitika zonse zampingo okozeratu zihtu.

Tsopano kwaife amene tili ndi nzeru zakuya za zochitika za chipaembedzo tingati inde ndi anthu. Mpingo simalo amene anthu amapita. Yesu anati suli uko kapena kuno ufumu uli mwa inu. Mpingo sinyumba yomangidwa simunsokhanonso kapena muzochitika ndi anthu ndithu.

Koma ndikufunseni kuti mudziwa mozamilapo ndipo sizikhala nkhani chabe kwa aliyense komanso tigoikapo mawu oti si nsanja kapenanso anthu. Mpingo ndi mgwirizano. Mungakhale ndi anthu chikwi kapenanso ochulukirapo pachifukwa chimechi kunena kuti mpingo ndi anthu. Ndikunena kuti sindingapite kumpingo chifukwa ndine mpingo, koma muchita bwino chifukwa anthu ambiri amane amatero amapitabe kumpingoko. Mungawamve la Mulungu mmawa kota to 9.00 akuti tiyeni tikonzekere kupita kumpingo, sara zimanenedwa pakwamwa pawo chifukwa choti ndi choonadi kuti ali kupitilizabe ndichita china chake kungakhale kuti amadziwa zina zopitiliza pamenepo. Sanaonenso umo mmene mpingo umangwirira ntchito.

Martin Luther amane anakhala oyambirira kuchita usembe wa okhulupirira chiphunzitso chake chinakhala chodzazidwa ndichoonadi kuti panalibe usembe wina chifukwa pali usembe wa okhulupirira okha. Koma sanachite izi ndi mmene anakhudzikira. Ndipo asembe ambiri amene amatembenuka kuchoka kukatolika amayamba kukwatira masisiteri koma zochita ndizoti amapitiliza kumachita zausembe amene lero amatchedwa alaliki kapenanso azibusa. Anapitilizanso zonse zimene amachita kale, zaukwati, zoika maliro ndi zamdalitso. Anayamba kuwalamulira anthu zomwe zinali kuusembe wa chi roma omwe unasandulika usembe wa mapolositanti (otsutsa chikatolika) omwe lerolino amatchedwa azitumiki. Ngakhale kuti pali kusintha kotero izi ndizosiyana ndimene bukhu loyera linaikira zithu. Ngati mutaonetsetsa bwino bukhu la machite a tumwi pali kusafanana ndi anthu awa amene amakhala (ma polositanti) amene amansija anthu ndimakhalidwe awo. Koma Martin Luther amadziwa kuti paunsembe okhulupilika ndipo ndichoonadi chimenechi chimene chinagwedeza dziko lonse koma ngakhale kuti sanadziwa kuchita kwake monga tidziwira ife koma iye analephera munthawi ya moyo wake.

Koma mukuunikira kwathu kulikonetsera zomwe zikupitilizidwabe kuti mpingo ndi anthu ndi nsanja yake ndi imeneyi, ndithu mpingo ndi anthu. Anthu amene amanena zimenezo mwatsoka sakhala mmoyo umeneu. Zoona zake ndizoti amapitabe kumpingo. Ndipo mpingowo wakhazikika pazochita ndi zokonzedweratu.

Pofuna kuti tiononge maganizo oterewa ndikupereka kuti zimveke bwino paizi. Ngati ufumu suli kuno kapena uko koma mwainu (Luka 17:20-21) ndiye kuti njira yake yopezekera muufumu wayesu ndiye kuti ukhale mwainu, chifukwa ndi mmene ufumuwo umapezeka. Ufumuwo kti upezeke mwa inu payenera kukhala mawu ochita chita amane amaonetsera zamtima (Aheberi 4:12) pakuti mawu amulungu ndi ochita chita ndipo tiyenera kusamalirana wina ndi mnzache tsiku ndi tsiku kuti pasapeke wina kuumitsidwa kutchimo (Aheberi 3:12-13) tiyenera kulukana kumitempha pamodzi (Aefeso 4:16) ziyenera kukhala zenizeni koyenera kukhala mgwirizano osati zochitika chabe, osatinso anthu koma ndithu mgwirizano sinsanja, kapenanso anthu, koma mgwirizano ndiye nkhani yake.

Mgwirizano ndiye njira imene ingakhale mbali ya mpingo otchedwa “oyitanidwa ndi Mulungu” sindilakhula ndi Mpingo odziwika ndi dziko kuno kuti ndizindikile kuti munthuyo anaomboledwadi. Ndikuti kukhala mucholinga cha Mulungu monga mzinda oikidwa pamwamwa pa phiri umene sungabisike umene wafalikira ponse ponse ndipo ndiochita mwa mulumikizo pamodzi monga Aefenso 4 anena ndi cholinga cha Mulungu kwa ife .Mtima wake uli ndi thupi lolumikiziwa pamodzi osati ndi thupi thupi lonse laikiwa palokha kulankhula zinthu zabwino ,koma kukhala opanda umboni .

Umu ndi mmene anthu onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga —osati adzadziwa ndi njira imodzi yokha, koma ndi njira yodziwika. Mgwilizano sizokomedzera pa mwamba pa keke koma ndi zinthu zofunika kwambira .Umu ndi mmwne anthu adzadziwa kuti ophunzira anga pa kukondana kopanda chinyengo chimene chidzaonedzedwa. Ndizofunika kuti miyoyo ikhale yolumikizika kuti miyoyo ikhale yolumikitsidwa. Ndipo dziko lapansi lili kudikira kuona izi

Nthawi Yotsiriza

Posachedwapa mbusa wa mpingo waukulu kuno ku America wakumwera analannkhula ndi ine ndipo anabvomeleza kuti mpingo umadziwika ndi mgwilizano. Anatinso ngati sangakhale ochita motera ndiye kuti akuchita zotani pamene kukolora kuti kudzachitike ku masiku otsiliza anthu azaonongeka zedi ndi mdaniyo satana. Okhulupilila makanda nthawi imeneyo sadzakwanilitsa chifukwa matumba sadzatha kutenga zotutu,

Nkhani yomwe ndimalankhula ndi mbusa ameneyu ndi yoti akulu mnsikhu munyengo ino Sali kuuzidwa kuti apita mbali zonse za mzinda, muzipinda za pamwamba kapenanso malo okomanilako. Funso ndiloti ngati tili ndi kuunika kochokera mu mgwilizano omwe ndi oyonetsera moyo weniweni monganso anenera 1 Yohane 1,kuti maziko a chiyanjano chathu ndi atate chilinso chotere ndi wina ndi mdake kuti tiyende mukuwala pamodzi ngati tifuna chiyanjano ndi Mulungu ndi munthu.

Pamene nthawi yotsiliza ili pafupi, Yesu ananenera pamodzi ndi amene anadzazidwa ndi mzimu oyera, kuti padzakhale kutsutsa kwakukulu ku ntchito ya Mulungu. Mulungu wakhala akutsinjiliza zotere kwakanthawi tsopano ndipo sipanakhale kutsutsa kwenikweni kuchokera kwa satana. Satana ali ndi zambiri zoti achite ndipo kawarikawiri kwa anthu amene akhala ali mbali yake ndi amene ali opulumitsidwa koma anafa kuuphawi wa usiwa wauzimu. Ochepa chabe ndi amene asintha zithu mudziko lomwe tikhamo. Anthu akhoza kukamba za choonadi ichi akhozanso kuyimba koma ndiochepa okha amene angabwerere kuchipulumutso chake koma ayenera abweretse ulemerero mlembi wa Aheberi analemba motere kubweretsa ana ambiri ku ulemerero (Aheberi 2:10) ulemero ndiye kuti kudzazidwa ndi moyenerera ndiponso ndi ulamuliro wa Kristu, ndiye choonadi chifundo ndi kukhululukira komanso kuonjezera ulendo wa Kavale ndi ulendo wa ku Pentekositi. Ikani zithu zonsezi pamodzi ndipo mudzkhala ndi moyo wa Yesu woonekeredwa mwainu. Mulungu akufuna kuti abale ana ambiri amane anapulumutsidwa, ndiye musangokhala osuta chabe koma kugwira ntchito mopitirira koposera umo timachitira. Mulungu afuna kuona ulemerero wake kudzera mwa anthu ake.

Kufunitsitsa kumeneko kuzakwaniritsika pamane Yesu akubweranso kachiwiri koma akufuna kupeza mkazi amene wazikozeletsa kubwera kwa mwamuna wake. Popanda banga, chilema, wowala ndiponso ndioyenera ndi Yesu—pamenepo ndiye palimtima wake pamene lipenga lidzaimbidwa ndipo kudzamveka “taonani mkwatidwi! Chifukwa choti mbiri yakale yatha ndipo moyo osatha wayambika pamene padzakhala mkwati wa mwana wa nkhosa” (Chibv. 19:1-10) izi ndizimene Mulungu ali kudikira

Tsopano nkhani iyi ya mkwatidwi yodziwikiratu. Azibusa amachita ndi matumba atsopano ndimachitidwe ena pomaitanitsa minsokhano mumilaga ndimalo ena odziwika ndikukumana la Mulungu kummawa pamakhala kupembedza. Izi ziyenera kuchitika ngati pali mgwirizano.

Ziyeneranso kuti zoterezi zikhalenso pa moyo wathu. Ndikufuna kukulimbikitsani kuti mavuto amane akudza ndi mayesero angoyambika pa moyo wanu ndi ofunika pachithu chimodzi pamene tivutika pamenepo tili kukolola chimene tinadzala. Ndipo tangolandira kumene pmbali pazimenezo. Mulungu ndiye ali mphamvu yoongolera, chifukwa ambiri tinali tulo, mwina tinali kusangalatsidwa ndi chiphunzitso ichi kapena ndichiphumzitso china. Poganizira kuti ntchito iyi kapena iyo tidzagwira, koma osazama kwenikweni muchikondi chayesu kumulambira iye pamene ena onse sakukuonani chifukwa choti mumamukonda iyeyo Yesu? Mukuona bwanji kukhala ndi kulimbika mtima panthawi ya kutsutsika pakuima panthawi ya zovuta zimene mwakumana nazo zimene zimaonekera pa ulendo umeneu. Ndikupepesa ndikumena kuti Mulungu sadzasiya zithu kuti zioneke motero ayi. Panthawi yotsiliza, masiku otsiriza enieni satana mwini wake azadza ndi nkhondo ndipo tidzakolola chomwe tinafesa. Ngati zinabwera chifukwa chaife tokha, mwinanso ndichifukwa choti tinasankha kuti tifanane ndi Yesu, ndipotero satana amadana ndikutsutsa chisankho chotero chifukwa iye akuona kuti nthawi ikupita kotsiriza.

Chibvumbulutso 12:10-12-limalakhula-za-satana kuti odzazits ndi mkwiyo chifukwa akudziwa kuti nthawi yamuthera. Mwatsokadi nthawi yake yathadi kufikira tsopano. Palibe umboni wowonekeka muthupi la kristu omwe mungakhulupirire kuti Yesu akubwera posachedwa, zochepa pa zochita za satana zatsutsidwa, kuwonongedwa, kubwezedwa, kudza kwa iye. Zochepa pa tchito ya satana zawonongedwa pansi pa mapazi athu (Aroma 16:20) thawi yochepa chabe imeme yakhala yomwe yachitika kuti satana wawonongedwa. Koma zomwe mulungu akufuna n di umboni wa mphamvu, ulamuliro, bata, kulimbikika kuzuzidwa, mtendere, kusangalala ndi kulimbikira-pamene mwatero zonse, poimapo (Aefenso 6:13) kumwamba ndi dziko lapansi lili lodikira kuona mtundu wa mtima ndi moyo kuoneletsedwa.

Tikunena kuti, musadabwe kuti muli kumva zowawa kapena zobvuta kapenanso mayesero mu mgwirizano inu mungogwira ntchito kumalo amane mukhalawo izi zonse zidzachitika ndipo mudzapereka kuti muli zowawa, pansi pa ululu ndi mayesero-poyamba pazochita zanu, mwinanso osakhala kuti ndi zimene inu mwachita. Zidzachitika chifukwa choti satana akuona kuti inu mwakonzekera kumva zowawa pakukwapulidwa ndi ndodo ya Mulungu.

Mulungu “amalanga ana amene amawakonda” Aheberi 12:6 ndipo muli kumva zowawa zotere chifukwa mwakonzeka kuti mudzakolore chilungamo ndi mtendere (Aheberi 12:11) mumoyo wanu uli mkudza. Mwakonzekera kukolora zimene inu munadzala. Ndipo mulikukomana ndi izi zowawa zotere. Ndipo mwazichepetsa nokha ndi kunena kuti; onani ndakhala olephera mudera ili “ndipo mwakonzekera kuti malangidwe ndikuti kutambasula dzanja lanu ndi kuti misomali ya pamtanda mwaibvomera: ndipo simulu kukana kuti izi zisachitike.ndipo mukufuna kuti muwengedwe ndi Mulungu ndi kumanga chikhulupiriro choyera chopambana. Mukufuna kuphunzira kupephera mu mzimu muzonse zokumana nazo ndipo mwatenga lupanga la mzimu kulimbana kuti mupulumutse abale ndi alongo mukufuna kuti zikhale choncho koposera koposa mmene mukufunira kuti mumve bwino koposanso umo kudziwika kwanu mukufuna kapenanso kuti umo banja lanu angakuyamikileni amene akudziwa kuti ochepetsedwa koma safuna kuima nanu limodzi

Chabwino nthawi zimenezi zili mkudza. Anthu adzaima motsutsana nanu ndipo padzakhala zowawa, maphokoso ambiri ndani, ngakhalenso maina kupatsidwa ndiponso kusinjilira, koposera zimene inu munaganizira mu moyo wanu. Ngati izi zili zotere ndi kumva chisoni mwainu nokha pa bvuto ili kapena ilo, ndipo ngati mungakhale a ulesi mmalo mwakuloza nkhope yanu kwa Mulungu ngati inu mupitilizabe kukhala ochita motere ndiye kuti mudzakhala ogonjetsedwa. Mulungu ali kukukomera kukukonzekerani kudzera njira yophweka yomwe ndi yooneka yoipa koma ndi yachipambano. Mulungu ali woogolera zinthu zonsezi. Iye ali odikilira kuona kuti mudzachita chiyani ndi mayesero onsewo.

Zinali motero ndi Aburahamu, amene ali dziko lalikulu la mtogolo lomwe lili mkudza —

ndiponso ndi tsogolo lathu pa dziko limeneli amene adika mwana wake pa nkhuni chifukwa chomwe Mulungu anauza Aburahamu anati “ndidzakudalitsa iwe ndi kuchulukitsa mtundu wako ndipo udzachuluka ngati mchenga w kunyanja. Ndipo mtundu wako udzakuda mizinda ya adani awo ndipo kudzera mwa mbeu yako maiko onse adziko lapansi adzadalitsika chifukwa choti wandimvera ine (Gen.22:17-18)

Mulngu adzaika maeselo amenewampatsogolo pathu poposera pa zimene simunaganizilepokoposela pa zimene simunaganizilepo koposela zimene anthu amati ndi mamembala ampingo uwo kapena winawo, kumangolimba kosalekeza kulakhulaso zithu zowoneka bwino, ndipo ngati ena sazifuna zimenezi amagopita ndi chipembedzo china.izi zonse zachitika chifukwa choti zina zake zabvuta zachitika zomwe zabalalitsa anthu.

Tsopano, ngati tazipeleka kuzinthu izi zochepetsazi zamakanda ndiye kuti sitidzakhala wothekela kugonjetsa mu nthawi yotsiliza ili ndikutsimikizilani inu kuti padzakhala kungonja ndithu. Ndikutsimikizilaniso, kuti padzakkalaso anthu ena amene adzakhala okozekela za izi koma njila yothekela kuti. Ndikupambana zithu izi molimbika ndi kuchitilana ulemu wina ndi mzake ndi chikondi, ndi mtendele wa mumtima, ndi chimwemwe , ndi kulambila ndi chilugamo zimene zinasiyanitsa Yesu ndi anzake ndiye kuti anaconda chilungamo ndikuda uchimo. (Aheberi 1:9) chabwino ,izi ndizimeneso zidzakusiyanitseni inu ndi azanu ena ngatitu mukonda chabwino ndikudana ndi chimene chili chimo sionse amene amatha zimenezi koma kuthekela kotela kuti kudza ndiye mukhale anthu amene muli okozekela, ndipo muyambe kuziphuzitsanso pano.

Muthawi yamayeselo imeneyi, mudzakhala muli while and moan ndi kudandaula komaso kutaika mudzazibisa nokha nyumba kwa masiku angapo? Kodi mudzakana kulakhula ndi awa ndi awo komaso mudzakhala otalikana ndi zithu mu mtima wanu angakhale kuti muli kusekelela kunja? Ngatmutasewela notelo tsopano ndiye kuti mudzakhala pa mabvuto odzadza. Nkhondo ya uzimu idzakhala yokukupambani podza ndi mphavu kwambili mwamkokomo. Ndipo zukunenelani zidzakhala zozunguza (end of page 13) zomwe zidzapangitse kuti mudzaika chikhulupililro ndipo chidzakhala chongotetha mongaso wina aliyese. zoona ndiye kuti osati onse adzakhala wongotetha chabe koma kuti ndi m’mene zithu zidzakhalire polandila zowawa zimenezi

Pamene zithu zochepa zidza patsogolo pathu—zokhudza chuma koma tidziwe kuti ndi zofunika pamene tikozekela motere pamene zazikulu zidza, ndiye zidzamenya mopambana kwambili muyenela kukozekela moyele pamene zazikulu zidza kuti mukhale ogojetsa ndikulembelani, anyamata inu chifukwa ndinu aphabvu ndipo mawu a mulungu akhala mwainu ndipo mwamupambana oyipayo (1 Yohane 2:14) kwa iye opambana ndidzawapatsa kuti adye kuchokela kumtengo wa moyo umene uli paladaizo wa mulungu (Chibvumbulutso 2:7) ali opambana ndipo zodza kwa iwo zidzabwela ndipo ndipofunika khukhala okozekeratu ndikudziwa kuti popanda manja oyela ndi mtima wa ngwiro popandanso kutsutsika, mtima woyera ndi chipiliro changwiro—ndiye kuti ndidzakhala osakwanilitsa ndipo ndidzaphonya .

Tsopanoso ndikofunika kotani kuti mpingo usangokhala mmipando palamulungu mmawa angakhalenso kuti uthenga ndi wa bwino ndiponso wa mubukhu la oyera? Chifukwa monga mwa Aheberi 3, njira imene tinga kwanilitse kupambana pa izi zimene zili patsogolo pathu osati kukhala oumitsidwa ndi kunamizidwa, ndiye kukhala ndi kuyesetsa kuthekera mu umoyo wa mzathu mu tsiku ndi tsiku.

Taonani kuti wina wa inu ngati wagwa mu uchimo osakhulupilira umene wachoka kwa mulungu, chabwino mudzakwanilitsa kumvera malangizo asmenewa ngati simukhala mu mgwirizano? Onani kuti pasakhale wina wa inu amene ali mu uchimo osakhulupilira`` mulungu ali kutiitana ife kukhala mu kuzama mu mugwilizano.

Ndipo mlembi yemweyi wa Aheberi analembanso mwina patapita ka nthawi maminitsi makumi awiri ndi asanu (25) ndipo analemba. Onetsani kuti pasakhale wina wa inu angakhale ndi khalidwe losafuna kusonkhana monga ena amachitira (Aheberi 10:25) Kodi mukudziwa kuti ananenadi zimenezo? Kuti mukonzekera pamene masiku alimkudza. Pamene masiku ali kudza ku chimaliziro ndipofunika kuti matumba woyenera akhale chiriri. Osatinso chifukwa cha kukolora kumene tikuyembekezera komanso osatiso ndi makanda omwe amene mulungu watitsutsa kuchokera mu kupembedza kosalugnama dziko lino. Komanso osati tidzakwanitsa kuchokera muzowawa zimene abale abanja ndi otida ndi onyada amene dziko apereka pamene atinyengerera ndi zinthu za dziko la pansizomwe timafuna kukhutitsa mimba zathu. Zowawa zidzakhaladi potero ndiye kuti chotengera vinyo chikhale chitasintha osati chifukwa kuoklora kokha, komanso chifukwa cha mtundu wa kutsutsa kumene mdaniyo aponyera pamene aona mkwatibwi ali kukonzekera. Khalani odikira tsopano motsimikizika.

Kuuza anthu zochita? Kapena miyoyo yawo poyera?

Pali chinthu chimodzi mu mgwirizano wa mgwiro, kotero ndikupatsani chimodzi mwa icho.

Simaganizo a Yesu kuti anthu adziyenda awiri-awiri kukachita ntchito ya Mulungu? Inde, anali maganizo a Yesu. Ndiye kuti anthu atatu sangathe kuyenda? Sindikutero ayi. Kodi Paulo samayenda yekha? Chabwino Paulotu anali munthu wamgwiro ndi oima mumoyo. Anakwanitsa kuukitsa anthu akufa, ndipo ndi moyo anakwanitsa kuuika anthu akufa, ndipo ndibvumbulutso loposera, munjira zambiri ngakhalenso ndi Petulo ndi Yohane, anthu amene anayenda ndi Ambuye ndikubvomelezeka mu Aefenso 3 ndi Petulo ananenanso mu 2 Peulo 3, Paulo anali munthu wa bvumbulutso amene adapita ku miyamba ya chitatu. Ngati mungatsate bwino mu mbiri ya moyo wake mu Machitidwe atumwi ndi zolemba mmakalata ake ndipo mudzapeza kuti anali ndi anthu oposa makumi asanu (50) amane anali ndi iye pa nthawi imodzi pa ulendo umodzi okha. Sikuti iye anthu onsewa anali ndi iye nthawi imodzi koma kuti anali ndi anthu awiri, atatu, anai kapenanso asanu ndo mmodzi poyenda mzindz ndi mzinda.monga mmenendidziwira panali nthawiimodzi yokha mmbiri imene mzimu woyera, unalemba kuti anali yekha muzaka makumi awiri ndi asanu (25). Anayenda pansi pa mtunda pazifukwa zodziwa iyeyo ndi Mulungu, ndipo abwenzi ena amene anali yakha pa nthawi yonse ya zaka 25 utumiki wake.

Choncho ndi chabwino kuti tikhale pamodzi? Chotero ndi chabwino ndithu. Pamene awiri kapena atatu asonkhana mudzina langa kumeneko ine ndili komweko. Bwanji sanati kuli konse konse amene ali ndi mzimu woyera ine ndili komweko anakatha kuakhula chomwecho, chifukwa mwina ndi zoonadi koma bwanji anati awiri kapena atatu akhale pamodzi? Ndinenanso kuti chomwe chamangidwa ndi anthu pano padziko lapansi chmwe mudzapepha, kudzaloledwa ndi Atate kumwamba. Potero pamene awiri kapena atatu abwera pamodzi mudzina langa pamenepo ine ndidzakhala ndi Iwo. (Mateyu 18:19-20) chifukwa chiyani anatero? Chifukwa Yesu akuti ife pamodzi tikhala okhulupilirana ndi kumvelana. Anadziwa kuti kudzakhala kuchimwirana wina ndi nzake kuti tiphunzilenso nira ya mtamda. Ndichifukwa chache amatinyengerela ife kuti tikhale pamodzi Yesu anawatumiza awiri awiri pachifukwa chomveka: kuti aliyense akhale odziwitsika bwino ndi mzake, kutinso kuti angathe kupemphera mmodzi kutinso adzutsane pamene mdani abwera. Angakhale kuti Yesu mwini nayenda yakha. Angakhale munthawi ya zowawa, anali ndithu ndi abale atatu pamtunda woponyedwa mwala sanapitilire mapazi atatu aja angakhale munthawi yazowawa. Iye anayendabe pamodzi ndi Iwo.

Iye amathanso kupemphera payekha. Anatiphunzitsanso kuti pali kufunika kokhala wekha mumchipinda ndi kupemphera. Pamalo amene wina sangathe kukumva ndi kukuona. Inde izi ndi chonho ndipo sitikuchotsapo ai.

Koma pali zina zimene ndikufuna kuti mudziwa mmene ife kwa zaka zambiri kumalo amene timakhala. T aona mmene zimakhalira kuti mmalo mwa munthu mmodzi kupita yekha ku mpingo ku mzinda wina, asanu ndi mmodzi kapenanso asanu ndi atatu a abale ndi alongo amapita nawo. Ndipo taona zikuchitika modabwitsa ntchito imeneyi.ndi zimene maikidwe ake a mu buku loyera, ndipo ndi maganizo abwino. Pali malamulo ndinso malonjezo ake okhudza zimenezi. Onsewa ndi zipatso zomwe tapeza a zonsezi. Pamene wina muchipinda afuna kuthanziza ukwati limene lili pafupi kutha ndiye kuti pali kale abale anai kapena asanu amene akuthandiza mu chipinda, kuthandizira ndi kulambira onse Pamodzi.palinso kuchita zinthu poyera palibe kung’ung’udza ku mbali ina ndinso kudandaula kosweka moyo. Palibe mayesero akulu ochitika Kwa abale chifukwa choti mwina bale kapena mulongo akuyenda yekha ndipo kenako mumapambana pamaene pali kufunikira. Machitedwe a Mulungu ndiooneka. Ndiye malonjezo ake alipo ndipo zipatso zake zochita njira ya Mulungu ndiimeneyi.

Ndikuuzeninso abale za zovuta zina. Mgwirizano wamgwiro wabwino ndi wamphamvu. Kuyenda awiri-awiri ndi kwamphamvu. Koma ngati munena kuti muyenera kumayenda awiri-awiri, ndipo ngati sizitero ndi chimo ndiyeku mwalakwitsanso. Chifukwa kuyenda awiri awiri ndikofunikadi? Kodi siphatso yochokera kwa Mulungu. Sizopambana? Pali nalonjezo akhudzana ndi zimenezi? Kodi pali malamulo ake? Zoonadi. Koma pamene tiyakhula kwaena tiyenera kudziona mtima wa Mulungu pa iwo—kwina aliense amene mulakhula naye amene akudzikhalira mwa iye yekha ndikufuna kuchita mwaiwokha okha. Mwachoncho ndiye kuti akuphunzitsidwa ndi satana pamoyo wawo onse chifukwa moyo onse wa America umaoneka otsogola ndipo aliyense amachita zimene akufuna ndichifukwa chake pali zoyakhulidwa zambiri zimene zimayankhula chinthu chimodzi? Ambiri akhala muchikhalidwe ichi ndikulowetsa kukumana kwa la mulungu mmawa ndikumati ndi machitidwe a mpingo umene umalora wina aliyense kuchita zofuna zamoyo wake umo afunira. Amakana mzeru yoperekedwa yomwe amalemba imanena kufunika kwa kuzipereka wina ndi mnzake, pokondana wina ndi mnzake kutengerana zothobwetsa ndi kukwaniritsa lamula la Kristu.

Pali zambiri zoikidwa zokhudzana ndi maganizo awa mumalemba “kulapitsana tchimo wina ndi mzake, ndikupemphererana wina ndi mnzake kuti muchilitsidwe” mungamukonde bwanji Mulungu amane simunamuone—pamene mukhala ndi moyo wainu nokha. nthawi yopemphera yochepa—“pamene simukonda m’bale wanu amene mumamuona?” “musanyengedwe!” onani, zonsezi ndizochokera mmawu oyera.

Yesu mwini amane anaonekera mthupi mudziko lino lapansi anationetsera njira imeneyi. “anali pakati pawo monga otumukira”, “anabwera nakhala pakati pawo”. Anakhala ndi ife monga “Mulungu pakati pathu.” Anakhala pakati pa opunzira ake anakhala kuti awatumize Iwo. Njira ya moyo pamodzi inaonekera pa mawu amoyo ndi ophunzitsa mumalemba olembedwa. “Tiyeni tichite tonse pamodzi”.

Koma zonse tanenazi ziyenera kukhala zokhudza mtima wa munthu. Chifukwa chiyani akufuna kukhala pawokha, “chabwino, ndikunena kuti sindifuna munthu wina. Ndikufuna kupita ku msika ndekha, ndipo usandiuze china chili chonse”.

Kuyanha kwathu ndikuti “palibe wina aliyense payekha muyenera kuyenda wina ndi mnzache” ziyenera kukhal choncho chabwino kupita kumsika nokha. Tapempherani chifukwa chiani mukupita kumsika nokha? Chabwino chitani chomwcho tengani galimoto yanga chifukwa chake ndi chiani? Bwanji mukuchita motero?

Chabwino, “mukuyamba kuyankha funso limenelo, ndipo ngati muli ndiokhulupika naye mwina mukongofuna kutaya nthawi ndi zinthu zadziko”.

Mwina muli ainu nokha ndipo simuli okhudzika ndi otumikira anzanu ndikuwakonda iwo kapena mukufuna kukhala mudziko. Kapenanso ndinu odzitukumula nokha kuti mudzipelekera umboni wa zimene mudachita ndikuonjezera nkhani mmene inu muli wa uzimu. Mwinanso muwauze anzanu kuti muli kupita kokapemphera, sindipemphero nthawi ya mphindi zisanu, ndiye kenako tidzipita kudzera mmalo ogulitsira zinthu kwa ola limodzi ndi theka. Chifukwa chake ndi chiyani, zoona? Kodi cheni cheni chimene chikuchitika m’mtima wa munthu ndi chiyani?

Ndi zimene mau amoyo ndi amphamvu amachita. “amasiya opanda kanthu zolinga za mtima”. Siumauza anthu zoyenera kuchita, Moyo wathanzi, maubwenzi okhulupirika siumauza anthu choyenera kuchita, kapena. Ngati mau a Mulungu, nawonso, amasiya zolinga mtima opanda kanthu.

Ngati wina aliyense akufuna kuti mumuuze choyenera kuchita, musachite, chifukwa zimezi sizidzawathandiza konse. Ngati mutawapatsa mayankho makumi asanu ndi mphambu mphambu zisanu ndi zitatu (58) pa mutu wa zoyenera kuchita, mwina akhoza kutuluka m’mavuto, koma sadzakhala mu ubale wina uliwonse ndi Mulungu. Kodi cholinga chake ndi chiyani pamapeto? Anthu zikwi zisanu kutuluka mmavuto, kapena anthu zikwi zisanu amene amakonda ndi kupembedza Mulungu ndikumkhulupirira mtima wawo onse, kumvera Iye kwathunthu ngakhale wina akuona kapena ayi? Ikubwera nthawi imene mudzazisiya kuti zipite. Zoona, nthawi yamasautso, koma ngakhale zili chonchi, chenjerani kuti musabwere ndi zikhulupiriro “zokhala mbali ndi mbali”. Zoona, eya, umodzi ndi mtima wa Mulungu. Koma bwanji sindinapite kunjira imeneyi? Imeneyi ndiye nkhani yeniyeni. Koma ngati ndikudziwa choonadi, ndipo ndikuona icho, ndipo ndili ofatsa pamaso pa Mulungu ndikufuna kumvera Iye, koma ndikufunabe kupita kumalo ogulitsira zinthu ndekha chifukwa Mulungu ali ndi cholinga ndi zimenezi, chabwino, eya, zoona; pitirani chimenechi. Ndipo tikhulupirirana wina ndi mnzache, kukonda wina ndi mnzake, ndkupempherera. Palibe chimene zingapange ndi “kuchita chinthu chabwino” kutsutsana ndi “zoipa zyenera kuchita”. Zikuyenera kuchita ndi zinthu za mtima pakuthandizana kupeza Mulungu ndi njira zake.

Matumba atsopano sindikufuna wina kusokoneza zinthu, chifukwa cha maubale-maubale okhlupirika—ndiwo matumba a tsopano . Palibe funso pachoona chimenechi . Zonse zidzera Muchipangano Chatsopano ndi mtima woonekeratu wa Mulungu. Dzanja silikuyenera kunena kwa diso, “ndilibe nawe ntchito.” Mbali ina ikadwala, thupi lonse—osati m’bale wako yekha—ayenera kukhumudwa. Mu 1 Petro 2 timawerenga kuti Yesu ndimwala wa mtengo wapatali wapangodya umene Mulungu anauika ku Zion, ngakhale ambiri sanamusamale Iye. Ndi mwala opondapo, mwala umene unaphunthwitsa anthu. Tsopano ife, ngati miyala ya moyo, tikhala, tidzakhala muuzimu kapena “odzazidwa-ndi mzimu”nyumba, anthu osankhidwa, unsembe wa chifumu, anthu woyera, anthu a Mulungu, sitili anthu ake, koma pano tili ake”—anthu, anthu, anthu ake. Ndi mtima wa Mulungu, kuti pamene andiona ine, awona inu; pamene aona inu, awonanso ine’ kuti ndife amodzi, ngati Yesu ndi Atate ali m’modzi. “ Umu ndi m’mene dziko lidzatidziwira,’ ili ndi pemphero la Yesu mu Yohane 17.

Uwu ndi uthenga wa mphamvu simaganizo chabe owonjezera. Uwu ndi mtima wa Mulungu mu nthawi yotsiriza ino. Ngati sitingayende mu izi, monga tanena kale zonse mbuyomo ngati sitingakhale pamodzi, ndiye kuti tidzakhala ogawikana. Lembani zimenezi. Ndizoona zimenezi, ndipo ndithu zimene taziphunzira mumachitidwe a Mulungu.

Mgwirizano Wa Mgwiro

Mulungu ali kufuna mngwilizano wangwiro, Amafunanso mgwilizano wamphamvu. Kusamala mozama miyoyo ndi mitima, ndi moyo wa ena mtsogolo muno. Atetezani anzanu kuchokera kwa mdaniyo. Gwilani ntchito kuti adziwe machenjerero a oipayo. Koma onani kuti mu njira ina ili yonse pochita izi pasakhale kuti muli owaumiliza ndi kuphangira ndi kuti mudzawauza zoti achite ai. Ngakhale kuti mwateteza kuchokera ku choipa china chili chonse,musaumilize kuti adzimvera za inu nokha.Ayenera kuti akhale ndi mngwilizano okha ndi Mulungu—ndikupitilizanso mngwilizano ndi inunso.Palibe chobvuta chili chonse.Mungathe kukhala ndi zonse .Simungathe kukhala ndi mngwilizano ndi wina ali yense chifukwa choti pali zina zimene simuchita kapena mumabvomelezana, ndi chikondi kukhulukilana ndi mtendere pamene tili paulendo, ngati muli ndi mgwilizano umene ulibe ungwiro monga kunena kuti udzichita izo kapena izi . Kumbukilani zonze zimene ndanenazi ndipo mudzakhala mkristu wabwino.

Zonse zimene tanenazi nizofunika kwa ife tonse Mawu a mulungu analembedwa kuti tiphunzire kuti tikhulupilire ndikuti tikhale ndi moyo odzaza. Ndi mmene mbewu ya yosaola ya mulungu kuti ndiyolembedwa mu moyo wathu. Tiyenera kuthandiza kuti tidziwe kubyala mbeu imeneyi. Tiyereranso kuti tithandizane wina ndi mzake ndi mau a Mulungukuti pasakhale ena amene angaumitsidwe mitima ndi chimo. Koma musachititse kuti zikhale zopanda pake pothandizana wina ndi mzake pouza anthu “zoti adzichita Kumeneku ndiye ndi ungwiro wa mgwilizano wangwiro. Uku ndiye siungwiro wabwino, ndi ukhristu wa ukhanda umene suli wa mphamvu.”

Musachite manyazi pokondana ndi kusamalilana. Ndipo mukhale otchinga munyhu ngati pali wina amene afuna kuzitchinga yokha pa moyo wa uzimu. Koma onani kuti imani moongoka, ndipo lankhulani ndi Iwo pa mau a Mulungu, ndiponso muwaonetse mtima wa Yesu omwe inu munapeza ndipo mulore kuti akhale ndi chisankho kuti mawu amene muli kuyankhula ndi a Mulungu. Afunseni, “kodi izi ndizimene Mulungu ayakhula? Kodi ndipitilize? Kodi ndiganizirebe? Kodi ndiyambe ndasala?” aloreni kuti akumane ndi Mulungu mwini ndipo apange chisankho pamene inu mwayesetsa kuthandiza.

Mawu a Mulungu ndiopindula kuchiphunzitso ndi kukonza ndi kudzudzula ndi kuphunzitsa chilungamo kuti munthu wa Mulungu akhale okonzekadi. Potero gwiritsani mau a Mulungu munjira yotere. Koma komaliza, lolani ena akumane ndi Mulungu ndi kusankha. Aloleni akumane ndi Mulungu ndi kusankha. Asakhale oyadzamila painu ndi kulephera kukumana ndi Ambuye.

Mgwirizano odzipereka wa mgwiro-uzatikonzeretsa ndi kukhala olimabana ndi zokumana nazo, zowawa, zaululu, zolephera, zoyesedwa pamagawo, komanso ndi chiopsezo chochokera kwa mdani pakhwerelo lina “tikufuna mgwirizano umenewo. Koma osakhala mgwirizano chabe, koma wamgwiro, mgwirizano odzipeleka ngati tikufuna kuononga satana. Tikufuna ife mgwilizano wa pa kavare ,ndikupita pa mtanda chifukwa cha anzathu, posawauza anzathu zoti achite.

Sindikuti kuti palibe mgwilizano wabwino tsopano .Koma ndikutheka kuti pangakhale wina wa ife amene angaononge zinthu ,Ndikudziwa kuti pali kufunika kuti asaononge ena ndikuti pasakhale mpanipani.

Kuyankha kwa bwino sikungakhale, lolani mzimu woyera utenge gawo pa zimenezi, Pamene nthawi yino zili motero pamene ena akhala pansi,ana ena a kanzi mu magawo awo a zochita apatsidwa mimba ndi anzawo a zaka khumi ndi zisanu, mwinanso ali mu mabvuto amenewonso angapangitse kukhala ndi mimba .Satana wawononga chikristu pamena anthu akuti ,Lolani mzimu woyera achite ,chabwino pamene bukhu lopatulika limene mzimu woyera linalemba limati.

“Chengatalanani wina ndi mzake tsiku ndi tsiku kuti wina asaumitsedwe ndi kunamizidwa ku uchimo.” (Aheberi 3:13)

“Anthu angakhale bwanji ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti apulumutsidwe ngati sanamve zaiye? Adzamva bwanji ngati palibe wa kuwauza iwo?” (Aroma 10:14)

“Koma tilinawo zoikira za dothi zapamwamba zoonetsera mphamvu ya Mulungu osati yochokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7)

“Pakuti mumzeru ya Mulungu dziko la pansi kudzera munzeru yake silinadziwe iye, kunamukomera Mulungu kudzera chopusa cholalikidwa chopulumutsa kwa iwo okhulupirira.” (2 Akorinto 1:21)

Choncho mgwirirzano ndiofunika kwenikweni, kokhudzana ndi mawu a Mulungu. Koma nthawi yomweyo onetsetsani kuti musadutse gawo olpitilira ndi kuwabera mwayi okumana ndi Mulungu ndi kupanga chiganizo paiwokha. Ndipo mukhale akuwakonda iwo ndi kuwathandiza iwo poti ayimenso. Ndipo muchite izi modzipereka, koma musawapanikize iwo kuti alakwitse ndi kuwaera mwai okuma ndi Mulungu ndi kukhala ndi chinsankho chawochawo.

Pali nthawi ina imene ikufunika okhala ndi moyo limodzi ndi iwo, tidzati mukuchita mawu a Mulungu kuti abale ena tinakhala nawo ndi yabwino pamodzi-mumoyo wa bwino mumawu a Mulungu. Ena ambiri mwaife tazichita munyengo ina. Ndipo ndi zabwino. Koma komaliza muyenera kuti aponyedwe kwa Mulungu pamenepo atakhala kuti ‘azikonzeletsa kuntchito’ kufikira mkuthekera kwao. Akumane ndi Mulungu ndikukhala ndi chiganizo chawo. Chosinthitsa mtima ndicho choonekera kwaiye ndi kuwalitsidwa kwenikweni kwa ulemerelo wa Ambuye, amene ali mzimu. Mbewu ya mulungu ndi mawu, ndipo tiyenera kuti timulore iye kuti achulutse. Zamveka?

Mgwirizano wodzipereka wa mgwiro—ndiofunika kwambiri pa phunziro ili. Ndipo lingalirani za kudza, zowawa zomwe zidzapungulidwe kwa anthu a Mulungu mwina kutha kwa mbado uno, kapenanso pakati pamdado uno. Tiyenera kukhala okomzekera kuichi. Kotero khalani ndi mgwirizano wodzipereka, komanso wa mgwiro, osati oyelekeza chabe kapena opsinja kapenso olamulira mgwirizano.

Pemphero.

Atate kufikira tsopano ndikufunsani kuchuulikitsidwa kwa mawu anu lolani mbewu yanu ibale zipatso pa moyo wathu. Tipatseni mzeru, tisaope kuit tikhalenso okhudzika ndimoyo wa anthu ena-wamphamvu, wamgwiro, mzeru zamhamvu zoonera munthu amene tiyakhula naye, tikweza manja athu kwa inu ndikuti tafunsanso iwo atero chimodzomodzi. Ambuye Yesu, ndinu mphunzitsi. Munati phunzitsa ife kuti tikhale otere. Mwina sitinaone bwino nthawi yapitayo koma nyengo iyi tifuna kuona bwino ndipo tadziwa kuti pali anthu amene akonzekeratu. Kumalo kwina nthawi ina muzochita zina pali munthu wina amene ali kupungulidwa zoipa amene mdani akufuna kumulikhwira. Sitikufuna kuthawa chinkho chimenechi. Tikufuna kukhala ogonjetsa pakati pa zowawa. Zimene zimabweretsa matamando kwainu. Chikhumbo chathu sikuchoka muzowawa za Malawi a moto, koma kukumana ndi inu amene mwamanga nyumba yoyera. Sitikfuna kumanga malo okhalitsa a ife, koma malo inu, okhalamo inu mwa mzimu. Tifukuna kukhala anthu otero. Achangu pa nyumba yanu, osati zochitira ubwino ife tokha. Atate tinyeketseni ife. Atate tithandizeni ife, tilimbikitseni ife, ndikutipatsa mphamvu yothekera patsogolo pahtu. Timange ife mumzeru. Tikufuna zimenezi, chifukwa nyunba yanu imangidwa ndi nzeru. Ameen.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon