MIYAMBO YA ANTHU M’MIPINGO YAO (YA ANTHU.)
24/10/1989
Chowona ndichoti miyambo imeneyi, ife tayilemekedza kwambiri yabweretsa chiwonongeko chachikulu mthupi la Yesu Khristu. Miyamboyi yachotsa utsogoleri ndi umbuye wa Yesu mpingo wake mopanda chisoni.
Ndipo iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yao, koma andilambira ine kwacabe. Ndikuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu. Marko 7:6 —7”
Yesu yekha anapwanya nthawi yose mowoneka miyambo yao yodzidzira ndi mfundo zao podziwa kuti zitha kudzetsa chitsokonedzo kwa atsogoleri ake. Chitsanzo chimodzi:
Ndipo pakulankhula iye, anamuitana mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya. Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe. Koma Ambuye anati kwa iye, cikho ndi mbale, koma mkati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Opusa inu, kodi iye wopanga kunja kwace sanapangeso mkati mwace? Koma patsani mphatso yachifundo za mkatimo; ndipo onani zonse ziri zoyera kwa inu. Koma tsoka inu, Afarisi! Cifukwa muperekalimodzi lamagawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa cakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka ciweruzo ndi chikondi ca Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo. Tsoka inu! Afarisi cifukwa mukonda mipando yaulemu m’masunagongi ndi kulankhulidwa m’misika. Tsoka inu Cifukwa muli ngat manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa. Ndipo m’modzi wa cilamulo anayankha, nanena kwa iye, Mphunzitsi, ndikunena izi, mutitonza ifenso Luka 11:37—45.
Zindikilani tsono kuti sikundi kovuta kusamba m’manja monga momwe ankafunila afirtisiwo. Kodi kuwonetsa chikondi comwe akhristu, ubwino ndi kuleza mtima sikungathe kusuntha moyo mlingo umodzi? Cikawapweteka motani? Tiyenera kuwapedza anthu kumene ali, ndiponso tikhale zonse kwa anthu one. Timachita zimenezi?
Mwina simudziwa, Yesu ndi wodzadza ndi cikondi—iye ndiponso IYE YEKHA ndiye tanthauzo la cikondi cacikhristu, kuleza mtima ndi m’mene uli bwino. Zinthu zonse kwa anthu onse? Yesu yekha ndi amene angafotokoze m’mene zinthu zonse zingafikile anthu onse mtanthauzala Atate. Ndipo Yesu adachita zinthu zambili monga kukuwonekam’mwano ndi atsogoleri acipembedzo ponkanyoza zocitika pacakudya ca madzulo. Nthawi zina Yesu ndi akuphunzira ake ankapita munda wa tirigu pa tsiku la sabata ndi colinga pamene amutsutsa ankamuwona natanthauzira mwina naletsa coyambika kalekale ndi Mulungu. Anthu odzikhulupilira muchilamulowa ankadzika okha pa mtsutso ndi amaulungu m’mene iwo ankatanthauzira malemba. Ndipo Yesu anali kuwalongosolera zonse bwino bwino osaphatikiza ndi maganizo aumunthu. Chifukwa chiyani? Tikukhulupirira kupeza yankho pamene tipemphera
Ndikupitiliza ndime imeneyi. Muyeso wazokometsera dzimene Yesu adadzikhazikitsa pamene ankayenda midzinda ndi ophunzira ake khumi ndi awiri dziyenera kumachitika ndi muyeso womwewo ndi otsatira ake lero. Khumi ndi awiriwo,naphunzitsidwa bwino m’mene zikhristu cidaliri ndi amene anali kutsogolera gulu la anthu 3108 kuphatikizapo otembenuka oyamba m’moyo wa yesu mkhristu patapita tsiku la pentekositi nadzadzitsa moyo wawo ndi Yesu. Zimene ankabweletsa kwa gulu lalikulu la amene adazipereka kwa Yesu ndi muyeso woyenera wadzokometserazo ndi ndondomeko zacipembedzo kuti ife anthu tidzigwiritse ntchito mpaka lero. Ndipo cowonadi ciyenera kudziwika kwa anthu mazana mazana otsonkhana pamodzi a mpingo wakhristu wa m’bayibulo kumene kulibe nkhani yiliyonse yokhuza mapulogilamu, zokometsera kapena nthano. Kunalibe comangidwa ndi gulu lililonse, monga momwe timacitila ife kuti ichi cikutchedwa IBM kapena AMWAY zitalembedwa. Kunalibe kucotsa mavesi ena naikapo maganizo akucenjera kwao. Ndikubwerezenso kunena kuti zowonjezera zathu kumipingo ya Mulungu kawirikawiri zikuoneka ngati miyambo yopanda ntchito yatsekeleza ciyero, cikhulupiriro ceniceni kuti ciwoneke monga momwe Mulungu ankafunila zinthu zikhalire padziko lace zisanakwana zaka cikwi cimodzi (100) atamwalira Yesu.
Ngakhale tanthawira kutali kucoka kunjira za yesu, ndondomeko ndi nthano zathu ndi kudzipweteka zakhala zinthu zimene mibadwo yambiri yapadziko pano ngati zenizeni. Ena atha kutsutsa kuti zonse za zipatso zimene zinalipo mwathu zabadwa kucoka kunja, kudzipweteka ndi ndondomeko zathu zoona ndithu. Monga ana amafuna malangizo ndi zipangizo cooneka kuti atengeleko. Anthu olumala amafuna ndodo ndi mipando yoyenda. Kungatani ngati mwana uja atakula? Kungakhalenso bwanji ngati ziwalo zopuwala ndi thupi lobvutika linacila? Ndiponso kuli bwanji ngati mpingo wokula msinkhu wa Yesu?
CHAKUDYA CA MAGANIZO NDI LINGALIRO
Ena mau acipembedzo amene sakupezeka mu Bayibulo, (kutanthauzira molakwika kumaphunzitsa mosamveka kapena mfundo zolakwika.)
“Mpingo”, “Utumiki” “Ubatizo”
“Cipembedzo” “M’busa, “Pemphero”
“Khristu, “Mtumwi” “Cipulumutso”
Ngakhale mau amenewa amapezeka paliponse masiku ano mcikhristu monga Bayibulo limene timatha kuwerenga mcilankhulo cathu limatiwonetsa zoona ndikupemphani kuti muganize amodzi ndi ine mwakamphindi kocepa. Cifukwa ninji mau amene Yesu ananena kwa khwimbi la anthu, ndiponso mau amaene mtumwi Paulo adalembakumipingo tanthawi yimeneyo akutsiyana matanthauzo ndi mau amene timamva ndikuwerenga lero? Mwacitsanzo mau oti “gay”, sakutanthauzidwa m’mene ankatauzilidwa kale? Akufunana ngati?
Ukunena kuti gay mu zaka zapitazo mwavevetsa bwino chipembezo chamakon zili ndizotengera zambiri zimene zili zabodza zotengedwa kuchoka mu mawu a chipembedzo atathauzidwa molakwika ndi kulembedwa munzeru zina, kusiyana ndi Bayibulo.
Zodandauitsa kuti mau amenewa sayimila zimene zonse Yesu ali, mwinanso Paulo ngakhaleso ena aliyense amene tingathe kumkumbukila. Pamene muwerenga Bayibulo napitiliza yetsetsani kumva zimene anamva koposa kumva m’mene zili mubadwo wosatembenuka ndi katanthauzidwe kalero. Thetsani, samalani ndichotsekesa ndi chobvuta kupeza coonadi.
Ena madziko okhazikika matsiku ano mdziko lonse—amene sakupezeka mpingo wa bayibulo ndi awa: mapemphero akapembezedwe, ulaliki, maphunzilo ala Mulungu, masukulu akolenji achikhristu, makwaya, kuyitanitsa adzilaliki amoto—makaleta ofunsira ntchito, kuyetsa, kuyetsedwa polowa ntchito, kukhazikitsa tsiku la Mulungu ngati tsiku lapadera, kusankhidwa kwa anthu kuti adzipempherera msonkhano wa cikhristu. Nthawi isanakwane kulalikira, kapena kutsogolera mayimbidwe ndi zina zotere.
Kugwira kwa mbiri yakale—Paulo sankanyamula Bayibulo, kulalikira ndi kusukulu za Bayibulo.
KUKONZEKERA ULALIKI
Kumanga Makachisi …………….. Chiyambi ca mizu ya makachisi achikhristu kukuwoneka kuti kuyamba posachedwa mzaka zikwi zitatu ndi makumi awiri atamwalira Yesu Khristu (AD) pamene mfumu (Emperor) constantine anawona kuti onse adzipembezo zonyenga adali ndi makachisi ndiye nayenso anaganiza kuti Mulungu wake watsopano Yesu Khristu naye adzimangilidwa makachisi. Akaswiri ofufuza zakale sakupeza chotsalira chilichose cimene chikubvomerezana ndi chipembedzo chachikhristu munthawi ya Yesu kapena kwa khumi ndi awiri, kapenanso patadutsa zaka mazana awiri atapita. Ichi nchachidzikire kuti gulu lokwana zikwi khumi lotembenuka mtima linkapita ena kukachisi wa Mulungu, mwina masunagoge achiyuda ndi makachisi ao, mwinanso kumakachisi azipembezo zina. Chikadamveka kwambiri ndiponso chosakanika nthawi yimeneyo kwa akhristu kumanga makachisi akulukulu monga anthu achitira lero nakhala ndi mapemphero momwemo. Koma sanatero mwa nyengo ziwiri, sanatero, cifukwa ninji? Chifukwa cilamulo comapita kumakachisi patsiku limodzi lopatulika, ndi mwa malo amodzi chitsutsana kwambiri ndi zolinga ndi zifukwa za Yesu ndi mpingo wam’bayibulo umene adaufera po ukhazikitsa. Tengani nthawi zpchepa, pemphelerani maganizo amenewa pamodzi nane amene ali enieni ndithu mwa zimene Yesu anabweletsa kudzakhazikitsa kucoka kumwamba kufika pansi pano—m zimene Yesu anabweletsa kudzakhadzikitsa kucoka kumwamba kufika pansi pano—mchiyanjano cha umulungu m’mpingo wace. Chithakukusinthani nthawi yose. Ndipo nchotsangalatsadi,:”
Komatu wamwamba mwambayo sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja monga m’neneri anena. Thambo la kumwamba ndilo mpando wacifumu wanga. Ndi dziko lapansi copondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani? Ati Ambuye kapena malo ampumulo wanga ndi otani? Machitidwe 7:48—49”
“Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri, citseko ciri cose pa cokha ca ngale imodzi. Ndipo kwalala la mzinda nilagolidi woyengeka, ngati mandala openyekera, ndipo sindiona kacisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu wamphamvu yonse, ndi mwanankhosa ndiwo kacisi wace. Cibvumbulutso 21:21-22”
Pali mtima wa Mulungu ndipo mpingo uyenera kukhala citsanzo camayendetsedwe ace pansi pano. Mpingo wa moyo, wawo na wa okhulupilira nautenga ngati wawo naumangira zipupa nayikako malata yimene sinkhani kwenikweni pansi pano. Izozo zilibe ntchito poyelekeza ndi zimene tikulingalira pano. Timangofuna kuwona ndithu chikhristu cimene cili ndimawonekedwe a chikhristu, koma nayikana ca icho mu umodzi ngakhalenso, payenkha payekha.
Kawiri kawiri mau a Mulungu akuchitira umboni wa ulemerero wa njira yatsopano. M[ingo watsopano wa ku Aefeso mwacitsanzo unkakumana ndi mabvuto oopsya kwambiri. Mzinda umene uja unacita citsomo ndi zamphamvu za cimodzi za zozizwa za mdziko lonse lapansi kachisi wa mfunu Diana.
Kukulirakulira kwa mipingo yotsiyanasiyana mumzinda wao / yimene motsakayika kuti ambiri anatembenukira kwa yesu) anali ndi kachisi wokongola kwambiri mdziko lapansi lonse. Kodi akhristu adatha kupitiliza bwanji ndi izo? Pauli ankalemba makalata ambiri nawongolera maso amitima yao kuti awone masomphenya a ufumu ndi ndi a mpingo wakacisi nati zimenezi zitha kuwoneka ndi maso auzimu okhaka. (Yohane 3:3-8, 1 Korinto 2:8-16, mateyu 11:25-27) Ndipo njira yamoyo watsopanoyi yikuposela kwakukulu poyelekeza ndi zimene zimapezeka m`manyumba omangidwa ndi anthu wamba. Mulungu akukupangilani inu mokhalamo m`nyumba ya ulemelero wache. Simungo sangalala ndi kamangidwe ka anthu pamene inuyo ndinu miyala yamoyo-natengedwa kuchoka m`mwala weniweni umene ali yesu mwini. “ndipo anatiukitsa pamodzi natikhazikitsa pamodzi, mzamwamba mwa khristu yesu, Aefeso 2:6” pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera , komatu muli amudzi womwewo wa oyera mtima ndi abanja la Mulungu. Omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali khristu yesu mwini, mwala wapangodya; mwa iye chimango chonse, cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale kachisi wopatulika mwa Ambuye, Aefeso 2:19-21!
(Werenganinso: Mateyo 21:1-2; Marko 14:58; Yohane 2:18; 14:1-3-3; 14:15-21, 1 Akorinto 3:9-10; 1petro2:1-12; Yesaya 51:1-2.)
IFE NDIFE KACHISI WACE!!! Ndife malo ake! Ndife nyumba yachristu yomangika yimene yiposela zonse, anthu osati malo kapena nthawi. Tizakhaladi m’malo, panthawi, m’nthawi zina koma tikamadzizungulira zimenezo, china chake ndithu citsoweka si mpingo wace, ufumu wace sukufotokozedwa kuti ndi wapamalo mwanthawiso yina.
Ndipo pamene Afarisi. Anamfunsa iye kuti ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe; ndipo sadzanena, taonani uwu, kapena uwo; pakuti, taonani Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu, Luke 17:20 —21.
Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa, ndipo musakaike mtima, pakuti izi zonse amitundu ya anthu yapadziko lapansi amazifunafuna, koma Atate adziwa kuti musowa zimenezi. Komatu tafunafunani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.
Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu. Gulitsani zinthu muli nazo nimupatse mphatso zacifundo mudzikonzere matumba andarama amene sakutha, Cuma cosatha m’mwamba kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli Cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu. Luka 12: 29—34.”
Yesu ananena naye, Tamvera ine, mkazi iwe kuti ikudza nthawi imene simudzalambira Atate kapena mphiri ili kapena m’Yerusalemu. Inu mulambira cimene simucudziwa ife tilambira cimene ticidziwa pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda. Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’coonadi pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace; Mulungu ndiye Mzimu ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi mcoonadi Yohane 4:21-24.
Koma tsopano podziwa Mulungu inu, koma makamakapodziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofoka ndi ya umphawi imene mufuna kubwerezanso kuicitira ukapolo? Musunga masiku, ndi miyezi ndi nyengo, ndi zaka, ndiopera inu kuti kapena ndadzibvutitsa ndi inu cabe (Agalatiya 4:9 —11!)
Ndicamtengo wace ndicotsangalatsa kuwona zimene Mulungu watichitira ife ndiponso mwa ife nakhala mwacizalo. Kukhazikika mukukonzeratu malo ndi nthawi ndiponso mfuupa za anthu, m’malo momulola mutu wa Eklesia Yesu mwini kutsogolera miyoyo ndi misonkhano yathu ndikusemphane ndi ulemerero wa mulungu wacolowa. Panopa tikumaganiza kudziteteza tokha ndi mapembezedwe abwino, titakonzelatu mocenjera malankhulidwe (nkutheka kuti akucoka mbayibulo) nakhazikitsa matsiku, masabata, ngakhalenso zaka ndi nyimbo zonse kuphatikizapo cina ciliconse cofunika mapemphero patsikulo.
Sicinali cikonzero ca Mulungu kukhala ndi cikhristu cimene cikudziwika ndi maganizo a anthu, ndondomeko pasabata nakhala ndi anthu obvala bwino, nawauza bweretsani mzanu patsabata, nakhala ndi gulu lotchedwa komitiyi, akatakwe amene alembedwa ntchito ndi mpingo kukhala mtsogoleri wawo zinthu ngati zimenezo. Kuyambira kale tawona zotsatira za zinthuzi zimene zilikutali kwenikweni kuchoka kunjira ya Yesu Khristu, ndi khumi ndi awiri ngakhalenso mpingo umene udawadziwa.
Miyoyo amuna ndi adzimayi, atsikana ndi anyamata yakhala yosabvuta kupezeka m’masewero apansi pano ngakhalenso kugwiritsidwa ntchito ndi satana. Zoonadi ali pamabvuto. Koma mpingo weniweni ndi umene Yesu Khristu adaunena kuti makomo adziko la akufa sadzaulaka uwo. Ndondomeko ndi miyambo zalephera. Yekha Yesu alimkutchulidwa mwa anthu ace—mpingo umene m’coonadi walumikizana naphatikizana pamodzi nalandira cithandizo la Ufumu wa ansembe, banja logwirira ntchito mnjira yace, osati munthu amene sangathe kucotsa mphamvu zakumdima.
Tikayang’anitsitsa kumbuyo timapeza mbiri za cipembedzo nawona m’mene tinafikila pamene tilikupeza kuti kacisi womangidwa zinayamba kukhala mbali yacikhristu mzaka zana limodzi ndi zikwi zisanu zambirimbiri. Gulu limene linkasusana ndi mau a Mulungu (protestants) linapitiliza kugwiritsa ntchito makacisi aciroma itantha nthawi yakukonzanso ndi mtumiki wotchedwa Martin Luther, ndipo anayamba kudzindikilitsa okha nga nawonso ndi aciroma. Monga timamvera mtumwi Paulo ndi cimodzimodzi lero. Kwina kusinthika kofunika kwambiri kunali kuwonjezekeredwa nthawi ya Luther. Izi nzotsacita kufunsa ndipo tiyenera kutsangalala kuti munthu monga Martin Luther ankafuna kutaya moyo wace polimbana ndi zipembedzo zophuka mnsanje naphatikizana ndi nyumba za manja a anthu anthawiyo komabe muyeso wakanidzilidwe kakakulu kamene kakutsogolera zipembedzo zambiri mpaka pano kanatengedwa pamodzi kucoka m’masiku a Luther ngati cinthu copembedzedwa.
Mpingo umene Yesu anaumanga (ndipo akuumangabe) si uli pano, kapena apo. Panthawi, sukugwirizana ndi malo a mfumu monga momwe zipembedzo zones za padziko lonse ndi zaciyunda zinkacitira.
Kodi zimenezo zikutanthauza kucepa kwacocitika, cipatso ngakhalenso mwina kucepa kwa msonkhano mumpingo? Iyayi, makamaka Mulungu adalora kusokonezeka kwa chipembedzo chake ndikukweza zoyamba zace ndimaganizo a anthu chifukwa chakulimba kwa mitima yao. Koma sidzinali choncho paciyambi; Mulungu anawapatsa ana ace loweluka tsiku loyera. Anatipatsa ife Yesu kukhala sabata yopumila (Ahebri 4:1—11; Mateyo 11:25—30)Tsiku lililonse kaya patokha kaya pamene titsonkhana pamodzi, nkofunikilathu ngati tikhaladi ndi Khristu m’malo a ufumu nakhala ndikukhala nazo zonse mwa iye. Ngati tikhaladi mwa iye kusokonezeka ndi cikhalidwe, kupandilathu masiku ndi nthawi ndi mfundo zongopeka zimatchinga poyelekeza ndi zimene zikanacitika kopanda zimenezo pakati unsembe wacifumu. Anthu a Mulungu ndi odzindikira pamene anamasulidwa kukhala moyo wace pamodzi kusiyana ndikungowelenga mawuwo ndikungowayimba.
Kukada khala choncho m’badwo wosatembenuka ndi wosadzipereka wa amuna ndi azimayi ndi umene ukadakhala ukufuna ufumu wao ndi nthawi ndi malo, pakalendara ndi dongosolo la dzimene zizachitike pamene tizafika kumwamba.cifukwa ninji akanayika kufuna kwao mdzkometsela ndi zikhalidwe kapenanso cikonzekero. Cifukwa kufuna ufumu wa Mulungu ndi canthawi yose, zowona kutsatira moyo wa Mulungu ndikusonkhana cifukwa ca iye kawirikawiri poyela ngakhalenso kupita nyumba ndi nyumba sikoyenera ndithu kusunga chilichonse cha mzaka makumi awiri makezana mnthawi ya mafano.
Iyitu ndi njira ya Mulungu, dziko loyela nafuna chiyamba ufumu wake, ndi Yesu akukhala mkati mwao:
Ndipo anali cikhalire mciphunzitso ca atumwi ndi m chiyanjano, m’kunyema mukate ndi mapemphero, koma panadza mantha pa anthu onse, ndipo zozizwa ndi zindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.. Ndipo zimene anali nazo ndi Cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga, momwe yense anasowera. Ndipo tsiku ndi tsiku anali cikhalire ndi mtima umodzi mkacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona. Nalemekeza Mulungu ndi kukhala naco cisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwa. Machitidwe Atumwi 2:4 2—47”
Chikhalidwe chapa ndime yapamwambayi cimacitika ndi anthu osatembenuka, akunja okhalamo, alendo amene anatembenuka kucoka ku umbombo kulowa mu ufumu wa mwana wace wokondeka zoona ndi zosabvuta kwa anthu amene ali Yesu mwini nakhala mkati mwao, amayenda monga iye anayendela, nazaza ndi changu ca mnyumba ya Atate. Mukangacotsa Luka 6:1, 14:35 ndipo muzatsilidzira ndikanthu kena monga Machitidwe 2, Kodi mungaganize zifukwa zina zabwino zimene zingakuletseni kukhalira iye amene anakuferani inu? Ine palibe, tose pamodzi tilibe.
MBIRI ZINA ZOTSANGALATSA
Panopa timamva citsoni kukhala ndi mpingo wopanda maphunziro aza Mulungu (Sunday school) ena akunena kuti akazakula ndi pamene adzakhala ndi mpingo weniweni wofanana ngati umene Petro ndi Yohane ankautsogolera umene unali ndi maphunziro ala Mulungu angopangidwa posachedwapa ndi anthu nakulitsa dzimene Yesu ndi atumwi nazicotsa m’makalasi zitakhazikika pakati pa ayuda ndi agiliki.
Tawonani izi: zokhomakhoma zinakhazikika mnthawi ya kusadziwa Mulungu Kalekale ndi Aroma
Guwa—Zinakhazikika atamwalira Yesu (AD) mzaka zikwi zisanu ndi chimodzi ndi Aroma nthawi ya (1520 AD) mnthawi Martin Luther.
Zowaza mkapu—mnthawi ya 800 AD.
Maphunziro azitsogoleri (seminaries)—1300 AD
Kuphunzitsa anthu (atsogoleri) ndi cacilendo kwambiri powona macitidwe ndi maphunziro a Yesu ndiponso cipangano catsopano. Mu ufumu wa Yesu anthu ankakula mmoyo wakuya osati mocita kuwapopa ngati tchubu kapena tili kuwaphunzitsira makalasi utsogoleri.
Makolenji acikhristu—anayamba nthawi ya 1640 AD kupereka maphunziro acikhristu.
Kubvala kwa tsiku lasabata—Nthawi yakusadziwa (Dark ages).
Matayi apakhosi—anayamba ndi anthu pofuna kupikisana kuwona amene wabvala capamwamba kwambiri pacakudya camadzulo.
Zobvala zazitendene zazitali—Zinayamba kunena kuti amene amafufuza zamakezana ndi ena oyesa dziko kucoka ku Iguputo sankafuna kupanda zosala zatsiyidwa! Dziwani kuti palibe colakwika ndi izi wazokha monga malaya abwino, tayi wapakhosi ngakhale zitendene. Koma kudalira zobvala zokongola patsiku lasabata m’mamawa, mndimvetse kuti zimatsutsana ndi ciphunzitso ndi moyo wa yemwe ali mutu wa mpingo Yesu Khristu. Cabwino ngati munabvala bwino popita kumaliro am’bale wanu, mulekelenji kubvsls cimodzimodzi popita kutchalichi?
Ngakhale cikamveka coyenera kale mnthawi ya 20th Century, m’mayiko monga America ndI Ulaya sidzinali m’mene Yesu ankafunila kapena kuti mpingo unatero kuti anthu azibvala choncho kupita kutchalichi. Yesu sanacitepo, ndiponso nafe sikofunika. Ndikudziwa kuti zonse izi zabveka zacilendo kwambiri kwa omwe anakulira muziphunzitso osati za Khristu. Kumbukilani kuti sitikuwonananso zotsatira za mpingo tikuwuwelenga m’bayibulo tikuwonanso ngati? Ichi sicinthu cocepetsedwa. Tinawongedwa ndi cikhalidwe ca anthu ndipo panopa nthawi yakwana yoti tiyikile njira za chibwanazi kumbuyo, (Marko 7:13, 12:38—40) Monga Mtumwi Paulo analemba kuti tisaweruzidwe ndi wina aliyense pamene muli nkukhala mu ufulu wa uthenga wa Yesu (ndipo tisatsiyane ndithu koma tiwone zinthu m’njira imene Mulungu amayiwonela.
Apatso Pali Zina Zodabwitsa—Tikanena za Alaliki, Abusa (mlaliki wamphamvu, wotsogelara zocitika mwina titi (Master of Ceremony MC) ngakhalenso atsogoleri apa mpingo, zimenezi zinayamba mnthawi ya 1520 AD. Martin Luther ankagwiritsa ntchito ansembe akale, ongotembenuka kupitiliza kuika maliro, kuyendetsa kapena titi kumangitsa maukwati, ndipo mnthawi yace ya utsogoleri wace anthuwo a mkayendetsa zonse zapatsiku la Mulungu, kupereka mau, kapena ulaliki. Mukuwona kufanana kwace kwa zanga, zanga.
Tiwonetso za makola oyela apadela obvala mkhosi atsogoleri —indedi Yesu anadzudzula cizolowezi comabvala zinthu zapadela ndi colinga cakumukopa wina mu cipembedzo cake kapena kudziyeneretsa, tiyeni tibwelelele nthawi yamasiku amenewa. Posachedwapa ena akunena kuti tili ndi mangawa ndi mpingo wa methodist cifukwa coyambitsa zimenezi mnthawi ya ulaliki wao. Makamaka pamene ankayenda kucoka ku malo ena kupita kwina nayenda pa akavalo, nafikanso pomatha kubvala zotseka kukamwa ndi mfuno zao. Ankamasulira pansi malamba agho kuchoka mu makosi agho atamaliza kulalikira.
Mnthawi ndi pamene kumkabadwa cisumo comabvala makolala autsogoleri zacabecabe siconcho kodi?
Tibwele pa nkhani yamapini, mabelo, maguwa, cigulu coyimila utumiki, dongosolo la ngati zimenezo, ngakhalenso izi “Joe Schmoe Ministries, Inc Tipitilize za zimenezi zinkawonetsa cikhristu mnthawi yimeneyi zoona anayika zatchinga mnjira kutitsekeleza kuti tidzadziwe za moyo wa okhulupilira oyamba nga ansembe a cifumu ndi kufuna kunena mobwelezabweleza mfundo yimene ena atha kukuwa kunena Allelluah natulutsa mau amene sanalikudziwika kuti ali mkamwa mwao, kuyankhula ndikupanganso ena zinkhonono nalephera kupuma atayambitsa nthenda ya mtima.
Ambiri amene amadzitcha okha akhristu lero alandidwa ndi amene amawatenga nakhadzikika mcisoceletso caciroma nadziwa pang’ono kwambiri mawu am’bayibulo ndi m’mene angakhalire olandilidwa nacitira pamodzi ndondomeko nawayika mu utsogoleri wamipando yazipembedzo. Ngati mlengi wazonse zokhazikikazi ankapezeka m’magulu athu, sicikanathandiza, koma kukhala kutali kwenikweni kuposela apa. Eni a mpingowa amene tawatchula pamwambapo antha kuwoneka ngati ndi abwino, poyetsetsetsa njira yowonetsera mipingo yao kuti sidzingayende kopanda m’modzi wa iwo. Ukaganizira zimenezo kuti ndi m’mene ukupeza kodi nkuganiza ngati ndi m’modzi mpingo wa mphamvu wa m’buku lamacitidwe (pakuti iwo sanali concho) kapena ukuwona kusapha tikidzidwa kwakulu? Kodi ngati titacotsa amene akudzitenga ngati ndi eni ainu kodi pangatsale munthu mumpingo wanu? Ngati mpingo wanu sunakhazikike ndi kuwonjezapo umodzi ndi mphamvu ya Mulungu koma umangokhazikika pa zofuna za eni, kukonza kayendetsedwe, kumanga, kuyimitsa azitumiki amphamvu, Gulu loyendetsa Gulu loyendetsa mpingo, ndi kukonza zokumana kumana kawirikawiri ndiye kuti mwamanga pa polakwika. Pamene kayendetsedwe aka ndi zophatukiza zace ndi kapangidwe ndi cilendo kumpingo wa m’bayibulo (ngakhale mpingo utakula mpaka anthu 15000 kuwonjezerapo mamembala ena am’mpingo momwemo) ici ndi cilamulo cokomatsela akhristu amunthawi zamakezana (20th Century) abale sidziyenera kutero. Kunena zoona zonse zimene tikangamilakozi ndi zofunika kamba koti tikutsoweka ubale ndi Mulungu weniweni wa zonse. Zimene iye ankafuna inu mucicite m’mpingo wace, Ahebri 8:1; 10:25, Akolose 2:16—17).
Ngati timuziwa iye mcoonadi, citetezo cathu canthawi ndi nthawi citsogozedwa mwa ubale osati mwa cilamulo. Zoyamba zamaciridwe a mphamvu ya Uzimu m’mipingo umene tikuwutchula m’buku la Machitidwe mutu 1:1 m’mene tipeza zoti Theo—philus—kutanthauza okoma Mulungu osati Theo—Logians, amaphunziro a pamwamba. Mbiri ya macitidwe aulemelero pakati pa anthu wamba sizinalembedwa kwa anthu odzikweza pamaso a Mulungu. Pafunika kuganizira kwambiri pamenepo, kuti umasukilethu moona mwa Yesu. Mucikhristu canu, muyenera kukhala ndi ubale mwacikondi osati mwacilamulo. Ndikhulupilira kuti zonsezi zikutitengela ife sono kukonzanso siconcho? Zimenezi sidzikuthandauza kuti sono tiyamba kuphunzira ciphunzitso zacilendo copanda zokometsera (ngakhale zokometsera ziyenera kuwonongeka moti tiphunzire kudlira Mulungu, nacita zonse pansi pa utsogoleri watsopano wa Ambuye wa mpingo? Makamaka tisowekadi kucilitsidwa kusoyamba zamakezana (20th century) zamafano nadalira nyumba sokumanamo, kayendetsedwe ka anthu, madipuloma, ulesi mawayilesi akanema, zitsangalaro zopanda pace kapena zaucimo za matupi athu, nathamangira zotengeza, nathamangira zotonthoza, ndi mafano osiyanasiyana tosawoneka miyoyo yathu. Pamenepa tithakusiyanitsa pakati pa mpingo ndi dziko osati mthupi, pamene mafano aswekela pansi amene atitchunga ife kucoonadi (Ezekiel 14:3).
Ndipo tidzatha kutsangalala ndi Yesu nakhala ni moyo watunthu wa ulemerero umene anauyang’anila natisiyila ife, Ahebri 3:1; 12:1-2; Yohane 17:5, 22, Luka 12:32; Mateyo 16:19, 13:43; 13:52.
Siyanitsani mau amenewa ndi zimene Yesu anasiyila amene adzayenda m’mawonekedwe osati mwa iye. Mateyu21:43; 23:13; 23:38; sibwino nditsilize ndi ndime yazolemba zina. Izi nzafupi ndipo nzothandiza makamaka popitiliza mapephero ndi kuganizira. Kumbukila kuti pamene mudzilandira kopanda maganizo atsopano citsiliziro chake cikhala coyipa kuposa coyamba. Pokhapokha tidzichotsa mukukula kwathu ndi pamene tidzabvala za umwana wa Mulungu nadzindikila cifuniro cake. Tikangotembelera ndi kucotsa cobvala ca umwana tidzakhala ndi mwana wamaliseche, wobvutika. Munthu wolumala akusoweka comuthandiza kuyenda (wheel chair) nyala zakunjinga yoyendapo, malo apadera wosungako, ndi malo ake ake osambako. Kungakhale bwino bwanji kucilitsa munthu ameneyu malo momukonzera zinthu zomuthandiza zapamwamba momputsitsa (ndondomeko, nthano, zolinga zopanda pace)
Mose anatumikila molakwitsa, m’malo ndi zinthu, ndi nthawi, ndi zopanga cifukwa cakuuma mitima yathu, koma kuyambila paciyambi isinali concho. Tiyeni tisinthe tithetse zimenezo. Tipilize.
PALI CIYEMBEKEZO
Kodi ufumu wamulungu ukuwoneka bwanji? Kodi mpingo unene ukuyenda pamodzi ndi Mulungu ndi mcisomo conse ukuwoneka bwanji? Kodi ngingazindikile bwanji Mzimu wa khristu ndi njira yake yabwino ya anthu ace ndi ine ndemwe?
Yesu mkwati, mpingo wace. Ali mkazi wamtengo wace wapamwamba mkazi wokonzekera kubweranso kwa mkwati, Mfumu ya ulemerero, ali mkazi wa mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena makwinya, ngakhalenso kacilema kena kalikonse. Mkwatiyu ndi gori lofanana ndi Yesu—wacifundo, koma nazaza ndi ukali kwa cinyengo, wotsamalitsa natsatira ntchito ya Atate ace mosabwezako. Uyu ndi mpingo umene Yesu anaugula ndi mwazi wa iye mwini.
Uzakhala mpingo umene siukumangidwa ndi nthawi kapena malo, koma nthawi yose paliponse poyela nayendanso kupita nyumba ndi nyumba. Udzakhala pamodzi naphatikizana ndi thandizo lathupi lace, nakhalidwe wina ndi mnzake, navomelezana macimo wina ndi mzace, nalimbisana wina ndi mzace nthawi zonse ndipo popanda wina wolimba mtima kamba kacinyengo caucimo,nthawi zonse nakondana, natumikilana, nasenzelana zowawa wina ndi mzace mwa cimwemwe ndi ciyamiko. Nakhalanso ndikucepa kwa misozi. Kupezeka kwace kuzaphatikizana ndi kasonkhanidwe kamizinda ndi m’manyumba kwa anthu ake onse. Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wamtima umodzi kuti kanthu kacuma anali naco ndi kace ka iye yekha.
Mpingo uzazindikilidwa ndi mphamvu yace ndi cisomo cace. Tchimo lizawonekera ndi kucotsedwa ndi mphamvu ya ulemerero wace wosatha m’miyoyo anthu ali mumpingomo. Amusinga azamasulidwa, kuyimbira nyimbo za Mulungu sikudzakhala kwa colemba mbuku nthawi isanakwane koma kudzakhala kwa kutsika kwa zimene Mulungu akucita nthawi imeneyo pakati pa anthu. Yang’anilani amene azazidwa ndi cimwemwe, cikhulupiriro, oyera mtima ace atha kuzaza ndi nyimbo pena paliponse ngakhale pamene mpingo uli m’nyumba yodyela. Cimene cili ceniceni pamalo amodzi ciyenera kukhala ceniceni paliponse. Vinyo ndi madzi a moyo ali ndi tanthauzo latsopano mwakudziwa izi. Ndiza m’bayibulo, zabwino bwino nazaza ndi cikhristu ca Yesu.
Tonse ndi ubale weniweni tizakhala monga Ambuye anacitira. Yesu mkhristu wa Mulungu tsono akhala mwa ife payekha payekha ngati anthu ace, Akolose 1; 26—27; 3:4; Gal 2:20; Macitidwe 17: 28; Aefeso 5:18; 1 Yohane 2:6; Aroma 8:9.
Ndime imeneyi ndi citsanzo cosatha campingo umene Yesu anaukhazikitsa, ndipo cilica m’badwo uliwonse umene udzayenda ndi iye, mwa mzmu wace.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, pakuti Yehova wandidzodza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa, iye wanditumiza ndikamnge osweka mtima, ndikalalikira kwa amusinga amasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende, ndikasikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu. Ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro, ndikakonzere iwo amene akulira maliro mziyoni ndi kupatsa cobvala kokometsa m’malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m’malo mwa maliro, cobvala ca matamando m’malo mwa mzimu wopsinjika kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuloka Yehova, kuti iye alemekezeke.
Ndipo iwo adzamanga mabwinja amibadwo yambiri, ndipo alendo adzaimilira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako ndi kukukonzera minda ya mphesa,
Koma inu mudzachedwa ansembe a Yehova, anthu adzoyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya Cuma ca amitundu m’mudzalowa mu ulemerero wao ( Yesaya 61:1-7; Luka 4:18—19).
Panopa tinene kuti zonena za Mulungu nzabwino koposa tsiku lamunthu, siconcho kodi? Ndipo mipingo yotereyi yilipo yimene matsatira zonena za Mulungu. Ngati ufuna ukalowe ndikutsimikidzileni kuti kudzela mudzowawa zambiri tikalowe mu ufumu wa Mulungu. Mutha mudzonsezi monga wina aliyense akucitira?
Mungathe kulipa mtengo wace koculuka koposa m’mene tingapemphere kapena kuganizira, mwa mphamvu ya iye amene agwira ntchito mwa ife, kwa iye yekha kukhale ulemerero mpingo, kunzera mwa Yesu Khristu kupitilira mzaka nzonse, dziko lonse kosatha, Ameni; Aefeso 3:20 Amen.
MAU OMALIZA
Cakhala ciyembekezo ca mtima wosweka uliwonse, munthu wokonda Mulungu mwamuna ndi mkazi kuti mwina ulaliki wina wabwino, wina watsopano ndi kuwonjezekela mphamvu, ndondomeko, kacisi womangidwa watsopano ungathe kucilitsa zilonda ndi zikhumudwitso za mipingo yao. Mowona, ophumzira a Yesu, owopa Mulungu ndi wothedwa mphamvu, cifukwa cakusathandizidwa nawona kutha kwa mabank kukukulirakulira mipingo yao muwelengela anthu apadziko osayanganila zimene Mulungu akuletsa. Akuyanganila moopsya muja, kuti ana oposa 60% alinkulowa banja nthawi isanakwane mochepa zaka khumi ndi zisanu. Ngakhale pali citsimikizo cosakhazikika, kuyi mpingo ya ophunzirayi ndi mabungwe ena, sakukhala mucizalo cha mphamvu ndi chikondi ndi ciyero ca Mulungu wathu, ena molekelera ndi mwacifundo nazitchinga okha. Cifukwa zokakamila kuzikhalidwe za anthu, zimakhala mantha akukanidwa, mantha akulephera, mantha akucotsedwa ntchito yao ya utsogoleri. Nalekerela zokometsetsa zao ndi ziphatikizo cifukwa cakudzikonda ngakhale colowa ca m’banja. Yanganilani zifukwa zobisikadi mwa iwo amene akwiyitsidwa ndi maganizo ena apelekedwe apo. Pamene muphulitsa chubu wakunyengelera ndi muzu wacipembedzo kotheka kukumana ndi musutso umenewu monga Ambuye Yesu adakumanilana nazo. Khala okonzekera izo, nawayamba ndi nzeru ndi cikondi. Koma matsiku oyelekeza anapita.
Tiyenera kupitila pamodzi patsogolo ndi Mulungu wathu mnzaonse iye watikonzera ife. Mneneri Yesaya adanena kuti mau a Mulungu sazabwerela chabe. Yesu analongosola mopitiliza ndi kulamulira mwa mphamvu. Ambuye wathu anatiphunzitsa kuti pali cinthu cimodzi cimene cithetse ndi kuwononga mau a Mulungu m’miyoyo yathu.
Muyese cabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu umene munapereka ndi zinthu zotere zambiri mucita. Marko 7:13.
Pomaliza…
koma okondedwa takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhura, pakuti Mulungu Sali wosalungama kuti adzaiwale ntchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera kudzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe, koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere cangu comweci colinga ku ciyembekezo cokwanila kufikira citsiriziro, kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa cikhulupiriro ndi kuleza mtima Ahebri 6:9—12”
DZIKO LOPANDA MIZINDA
(Fanizo)
Ganizirani kwa kaphindi kamodzi mizinda kulibe amene payenkha azatha kudzindikira kapena kunena kuti mzinda ndiwantchito yanji. Moyo wakhala wa mizinda, mwa cigulu ndi m’maphunziro,
m’badwo uno, mbiri yikunena kuti mizinda yinali ya amuna amene akadzitcha okha amunadi, ndipo anthu ndi mabanja anali ciculukire koposa malo okhalamo.
Imani, ndipo ganizirani ndi ine mwakamphindi kuti kungakhale bwanji kukhala m’dziko lapansi pano popanda mizinda. Tangonjetserani kuti gulu la anthu m’badwo umene uja waganiza zosintha zinthu ndikuzipanga m’mene ziyenera kukhalira. Ataganiza kubwezelanso mizinda, nakhadzikitsa mizinda ngati malo ogwirirako zonse pamoyo wao. Ikanatchedwa mizinda waliyense kungokhala mizinda wogwiritsira ntchito. Coyamba kucita cikanakhala, mwacilengedwe kupita kunena akusungilako mabuku kapena malamulo kuwerenga, kuwerenga, kuphunzira chilichose ca mzinda.
Pokhazikika mukufufuza kwao, anagwirizana pamodzi kuti adzabwezeletsa moyo wamizinda mibadwo wao. Pamodzi akamanga nasuntha mizinda ndi matabwa, namalizira ndi malo amalonda, odyelamo, mahotelo, nyumba, mabanki, masukulu, misika, ngakhalenso kokhala acitetezo (police station).
Anthu adziperekawa amuna ndi akazi anantha ntchito yobweletsaso mzinda weniweni ndi moyo wace kudziko losowa lopanda mizinda. Anagwirizana kuti mwa ora limodzi tsiku lililonse adziphunzira moyo wamizinda. Munthu amene ankasewera masewero ena ngakhale sanal wacitauni weniweni anayamba kuzala timasamba kukayika mkasitolo kake. Wogwirira ntchito yopereka ndalama m’banki ndi amayi ace ndi adadi ace nthawi yonse ankaganiza kuti iye azakhala ndi ndalama zambiri masiku ena anapeza timadola tocepa kutsogolera gulu nafunafuna kutero anapeza mabuku ocepa kuti akapatsa ana ake ndi kugwiritsa ntchito kusukulu.
Ndipo wapolisi amene ankasamalira ofesi yace kudzera m’mabuku anapeza mabvuto cifukwa mabwana ake kawiri kawiri ankacotsa mabukuwa mukabatiyo. Monga tauni mfuti sidzinakhalekonso, cimenecho chinali cosabvuta. Kumene kunali zocepa mu nthawi ya makezana mzaka za makumi awriri ndi mphambu ziwiri, zosakhazikika konse.
Napanga kafukufuku mucilankhulidwe ndikupeza njira popanda njira. Nasunga buku limene linali ndi mfumbi limene linali ndi nkhani yoti kumangalande mzaka za muma 1980 apolisi adziwika kuti (Bobbies) sankagwiritsira mfuti, m’malo mwace ankagwiritsira zophulitsa utsi. Ndipo mukamvekedwe kace cina bwino kwa iye kuti wa polisi akufunika mfuti yokha mnthawi zoyambilira pamene ankazikhadzikitsa monga anthu adindo. Patapita izo anaganiza kuganiza, kuti anthu apita patsogolo, concho sikunali kofunikanso mfuti kutsimikiza maudindo aakulu akulu. Mzaka zina zamuma 1980 anthu ankagwiritsilabe mfuti zinali zacizolowezi ngakhale zinali zamakezana ndiponso zimaonetsa kutsazindikira muzimenezi. Ndipo nthenda yimeneyi mathedwa. Mfuti sinali yosayenera mcikhalidwe cao. Sidzimamulola kucita ntchito m’mene yiyenera kukhalira.
Monga mbali yopindula anayamba kupangitsa maphunziro ndi misonkhano ndi apolisi, kamba koti maphunziro onse azoyamba zao.
Mwaconcho anthu ambiri amayi ndi abambo okhulupirika ankapita tsiku lililonse, mwacipembedzo kuzinyumba zao zamatabwa kukaphunzira moyo wacitauni. Monga anthu amutauni anagula zakudimba, masamba ndipo mwini dimba nathamangila ku banki ndi ndalama zimene anazipeza mzogulitsa. Ndipo wapolisi anayimilira namuteteza mwini munda uja kuti acifwamba angamulande Cuma.
Mphunzitsi wamkulu analikukangalika naphunzitsa. Ndipo mwa ora limodzi tauni imeneyo inkakhala ndi zokambilana tsiku lililonse ndipo aliyense anayetsetsa (kamba ka zolinga) kugwiritsa kayankhulidwe ka makezana kam’matauni masikuwo. Concho ntchito zao za m’matauni zinali kuwakwanila.
Iyi yinabvomerezedwa kuti inali nthawi yoziwika ya chete kwa anthu a ambirimbiri. Indedi nthawi zina kunkawoneka mabvuto poti dzimenezi ndizoyembekezereka. Ena atha kunena kuti zonse zatsopano ndi zapamwamba zomangidwa m’matauni zimene zinkakulirakulira zinacoka kumagawamo kapena kudziwonetsa. Ambiri anamva bwino kwambiri ndi maganizo wotsatira cowonadi, kukula ndi kumadzalanso m’mataunimo.
Tsiku lina munthu wina wakale wocokera mtauni yeniyeni anabwera. Anawona pamene anthu m’tauni ya mwiniyi ankayendetsera malonda awo. Ankathamanga apo ndi apa ngati kuti zotsatira zamalondawo zinali kudalira iwowo. Pamwamba pazonse nkhaniyi yakubwezeletsa moyo wamutauni ndi yofunikadi kwambiri. Mkulu wocoka kumudzi wakaleyo adasweka mtima natsokonezeka, nazizwa, ndipo nakwiyitsa onse nthawi yomweyo. Kodi zonsezi zinali za nthcito yanji? Atikubwezeletsa moyo wamutauni—zimenezi?
Anadela nkhawa kwambiri ndi kusangalala kuwaphunzitsa iwo amene analikuwonetsa kwambiri moyo wamutauni koposa zimodzi ndi za mtauni. Mabuku onse ophunzira anali nawo mnthawi yao anawathandiza kucotsa cymene cinkawoneka cokwanira moyo uliwonse wam’tauni, kaciduswa pakaciduswa koma kopanda moyo uliwonse kumbuyo kwao.
Mkulu wongobwelayo ankabvutika kwambiri kufafana ndi miyoyo ya anthu amutauni. Koma zimenezi zinali bwino bwino. Anthu ngati banja ili. Zoonadi, pali mabvuto koma sankacotsedwa zisawawa, m’malo mwace ankadzikweza kukhala oyera kuposa inu. Ananena monong’oneza kwa wina ndimnzake pamene ankadutsa m’mizinda. Tikudziwa zoona kuti ife tili amutauni. Anali ndizibvomelezo ciliconse ankacifuna.
Pali colikwika kodi kukhala ndi ndalama ku banki?
Kodi simuli mabuku okwanila musukulu?
Pamene ankawonetsetsa zotsatira za mkulu wacilendo uja ndi mabvuto ace pamene sankatonthozedwa mafunso awo ankakulirakulira.
Yetsani kutenga ndalama ku banki muwona ngati gulu la apolisi silikugwira ntchito anakuwa.
Mvetsera ngati sufuna m’mene tikumangira apamu tangoyamba nyumba yako pano wekha. Takoleza moto wowotha ngati ukufuna. Ukudziwa kumene malo osangulilako zinthu ali. M’malo mongonenanenana kwambiri bwanji osamamanga limodzi ndi ife? Kodi iwe ubwino kwambiri koposa wina aliyense?
Nkosafuna kunena kuti mkulu wacilendo ufa anacoka modzidzimutsidwa ndi kukhumuditsidwa. Ndipo anthu amutauni ankapitabe mokhulupilika mutauni tsiku lililonse panthawi yoyenera pena paliponse mpata unkapezeka ndipo pamene makomo ankatseguka khala okhulupilika mpaka imfa.
Modzilemekeza ndi mwadongosolo mukuwona moyo wamantha ndi kudzikudza, simawalore iwo kuti atsiyanitse pakati pakupita kutauni ndi kukhala wa mtaunimo.
Tikupempha kuti anthu mutauni atiphunzitse kuti tisasokoneze ceniceni ndi kadziwidwe ka kalekale. Tikupempha kuti tikhazikike pang’ono koposa m’mene kumakhalira, mkati ndi kunja ndi kuti tisangowonjezera ubwino wa muyeso wa sikelo kapangidwe. Maphunziro awasukulu akusunga ntchito ya eni ace.
Sidzikupangidwa osati ndi tauni kapena mpingo. Ndiponso kunena za matauni kapena kuwerenga za mtauni sikungafanizidwe ndi cidziwitso ndi cimwemwe ndi phindu lace la moyo wamutauni. Ngakhalenso moyo mu ufumu wa Mulungu. Phindu ndi mphamvu ya moyo wamutauni sidzidzakhalako pamene matauni, ndi mipingo yikhalira yapamwamba muzochitika za eni ake. Musakhutire kuyenda m’malo osungilamo uchi. Lowani mcimeneci ndi moyo wamtima wonse. Khazikika osati cifukwa cilamulo cinaciliconse, kapena kukhala ofatsa mzaka zoonjezera khumi kapena kupyola.
Mayankhulidwe amphamvu mutayima kumbuyo kwa guwa kusacotse coonadi ca Mulungu, cocoka mtima wace pa anthu ace, masiku ano. (Aefeso 3:10) Ambuye atidalitse nchikutithandiza pamene tonse tifunafuna kukhala anthu ace, mkwati amene wadzikonsekera kubwelanso kwa mkwatibwi, “ Ufumu ya ulemerero Ambuye, Yesu Khristu. Dzina lace lilemekezedwe.