Maziko A Yesu

4/8/2003

Chisitu, Africa 1996

Anthu—-—osati zomanga

Baibulo limatiphunzitsa kuti Mulungu sagona nyumba zomangidwa ndi manja anthu. Efeso 2 ndi malemba ena otere amati ndife malo okhalamo Mulungu mu Mzimu Oyera—mpingo.

Timadziwa mmene mpingo wumaonekera ndiye ngati nyumba ya Mulungu ndi anthu osati nyumba, Nanga imaoneka bwanji?

Pamene muyenda muyenda mu msewu ndiye mumaona zomangidwa ndi zipembedzo ndiye poti mpingo ndi opangidwa ndi anthu osati nyumba zomangidwa. Ndiye zimaoneka motani. Tingasiyanitse motani ndi mpingowo ona ndi osaona? Awa ndi maonokedwe a mpingo umene umamangidwa ndi anthu osati miyala.

Pamene Yesu ayenda uko ndi uko kufuna mpingo woona adzaudzidwa bwanji? Mpingo woona omangidwa ndi miala ya moyo umene Yesu anaukonda uyenera kukhala ndi zida zabwino. Ngati nyumba imangidwa ndi zida zoola ndiye kuti idzagwa. Ngati matabwa yogwilizana kumwamba ndi woola idzagwa pansi. Njerwa zofewa zosaumbidwa bwino kapena kuchokera ku zolakwika sizingathe kuthandiza, ndipo idzagwa. Mpingo woona umene umangidwa ndi Mulungu, osati manja anthu, ndi umene upangidwa ndi miala ya moyo—Akristo woona osati akufa. Njerwa kapena zidina ngati ndi nyumba ya Mulungu kuchokera kwa amai ndi abambo kuti ikhale yothekera. Siyenera kukhala miyala woipa (1 Akorinto 3-5)

Kuchokera Ang’ono mpaka Akulu Onse Sadziwa Mulungu

Uneneri wa chipangano chatsopano umati mpingo wa Mulungu umene ali kumanga (Jer 31, Aher8, Ahebri 10) ndiwo mpingo woona umene kuyambira ang’ono mpaka akulu onse adzadziwa Mulungu wamoyo.

Mu mpingo wakale umakhala membara chifukwa kuti makolo ako ndi Ayuda ndiye ngati ukhulupilira chinthu chabwino ndi kuti makolo ali kumeneko ndinso iweyo umapita kawiri kawiri ndi kumapeleka chakhumi ndiye kuti membara wa mpingo umenewo. Mu chipangano chatsopanomu mpingo wa Yesu izi sizoona ai. Uyenera kupeleka mtima wako kwa Mulungu ………… Uneneri wa chipangano chatsopano chinali mpingo umene Mulungu akumanga Jer 3, Ahebri 10) ndiye mpingo woona ndiye kuti wang’ono mpaka wamkulu ONSE adzadziwa Mulungu wa moyo. Ngati munthu sadziwa Mulungu sangathe kukhala membala wa Yesu. Udzakhala monga zomangidwa zimene zili zofewa kapena kuwola—Nyumba imene Yesu akumanga ndi nyumba yopambana ndipo Yesu adzagwilitsa ntchito zida zabwino zokha pomanga nyumba imeneyi.

Osanyengelera

Machitidwe 3 imati Yesu anali Mneneri ndipo anamanga nyumba yake (Mpingo) ndipo ali yense amene samvera iye adzachotsedwa pakati pa anthu. Izi ni zimene Yesu analankhula mu Mateyu 18 kuti ngati munthu apitirira kuda mnzake. Kuuma mtima kuzikonda ndikupitilira kumwa moyo, kukalipira mkazi kapena ana ndikuchita zakuba mu malonda awo, kunama kapena ulesi ndiye tipita kwa iwo ndikuwatandiza, mwachoncho ngati sasamala pakumvera chiphunzitso cha Yesu ndiye tiyenera kubweretsa awiri kapena atatu ena ndi kulankhura ndi munthuyo. Ngati sakumevlanso pazimene Yesu anena ndikuti sakusintha, ndiye tilankhure ndi mpingo wonse ndi kumufunsa kuti achoke.

1 Akorinto 5 limati tiyenera kuchotsa isiti kuchokera pa chakudya. Yesu anatilamulira osadya kapena kukhala pamodzi ndi munthu amene sadzasintha moyo wawo ku chiphunzisto cha Yesu. Pasakhale chigwilizano ndi iwo, ndikuti achotsedwe pakati pathu. Baibulo limatero “Yesu ndi omanga wamkulu. Iye sadzamanga ndi zofewa ndi zowola akufuna kumanga nyumba yapamwamba kuti akhalemo—imene ili yoyenera Mfumu monga iye.

Kusankha Zida Zomangira

Choncho zida zomangira mu nyumba ya Mulungu ziyenera zapamwamba, izi sizoti munthu ali yense ndi wabwino ai. Sizoti munthu ali yense ndi wabwino ai. Koma, zithandauza munthu, akonde ndi kumvera Yesu ndipo sanyosera kuthandiza kwa ena, amene afuna kuthandiza iwo kukonda ndi kumvera Yesu, afuna kuthandizika zomangila zabwino za nyumba ya Mulungu ndi pamene munthu amene safuna chithandizo iye amati, “osandiweluza ine” “samala zako amaziteteza,” “chotsa choipa m’maso mwako” zimenezo ndi zomangila zoipa, zimene Mulungu salora mnyumba yake. Yesu sadzamanga nyumba yake motelo. Iyi ndi mitengo wowola ndipo udzadulidwa pakati pa anthu. (Machitidwe 3:23, Mat 18, 1 Akorinto 5) Mu mpingo woona amene atelo saloledwa. Ngakhale atakhala ndi ndalama zochuluka, kapena amadziwa Baibulo motani angakhalenso mtsogoleri” koma ngati sabvomeleza mpingo wa Yesu mofewa ku chiphunzitso cha Yesu, ndiye sangakhale ku mbali ya mpingo woona umene uchitika mu mzimu. Ngati akana, chikondi ndi kupepsa nzeru, kuthandiza ndi kudekha mtima, ndi kuwalola kukhala pakati pa abale ndiye tikutsutsa Yesu ngakhale malamulo ake.

Yesu adzamanga ndi zida zomangira zabwino, ngati tili ndi mitima wofewa, kukonda chiphunzitso chake, kwenikweni tifuna kusintha zinthu mu moyo wathu umene ufunika kusintha, ndikubwera ndi nkhope zathu kwa iye munthawi ya zobvuta kapena kuyesedwa. Kumufuna iye ndi abale athu kuthandiza ifeyo. Ndiye kuti mwala yamoyo yokongola kumangira yomangidwa ndi nzeru.

Nyumba Yomangidwa Ndi Nzeru

Nyumba, tikutenga zomangira zonse zimene zili zoyenelera kumangira nyumba. Miyala yonse ndi matabwa onse ndi zida zonse zimene Yesu wazisankha pa nyumba yake. Tsopano zonse tiziike malo amodzi—ndiye kuti tilibe nyumba. Nyumba ya Mulungu imafunika kuposa mitengo wabwino yokha. Simungathe kugona mnyumba imene zida zake zangoikidwa pamalo amodzi sizidzakupulumutsani ku mphepo ya mkuntho, angakhale ndi zomangira zapamwamba.

Palinso njira imene tingamangire nyumba ndi zida zabwino—njira imeneYesu afuna pogwilitsa miyala ya moyo. Monga mmene achipembedzo chomwecho mpingo woona umakhalir sumangidwa ndi miyala, koma anthu, miyala ya moyo. Ndipo iyenera kuoneka ndi maonekedwe ena kuti ikhale nyumba ya bwino yoyenera kukhala Yesu.

Palinso njira ina yomangira nyumba kuti yosabvuta kukhala komanso mphepo osaigwetsa. Yesu ndi omanga wa nzeru ndipo amanga nyumba motere; Ndikuuzani maonekedwe anyumbayo chifukwa ngati sitingamange motere nyumba idzagwa pamene mphepo idzabwera ndi mmene tingamangire nyumbayo ndi zomangira zapamwamba ndithu zida zoipa ndi zosaloledwa mu nyumba imeneyi pokhapo pali kusinthika ndi kukhala zida zabwino monga Yesu afunira.

Mnyamata olemera anauzidwa kuti anali wabwino. Koma sanali ololedwa pa nthawiyo chifukwa anali ndi umbombo mu mtima mwake. Anali kudalira ndalama zake koposa Mulungu, anali wa chisoni kupeleka ndalama ndiye Yesu anati, “Sungakhale ku mbali ya Mpingo munjira yotere mpaka mutasintha moyo wanu. Simuli ololedwa kukhala miyala ya moyo mu nyumba yake, umu ndi mmene Yesu ali kumangira nyumba yake. Amationa ife ndi kutikonda ife monga adachitira ndi munthu uja komanso akatiuza kuti tisinthe. Ngati sitingasinthe, potipabe ife chikondi ndi malonjezo onse anatipatsa sadzakwanitsa kutigwiritsira ife ntchito monga mwala wa moyo. Adzatiika pambali mpaka nditafewetsa mtima yathu.

Kusendeza Pamodzi Monga Amodzi

Ndipamene miala ikhala pamodzi ndi kulumikiza ndi moyo wa tsiku mu chikondi ndi kupezana ndi kumanga ndi makonzedwe a Mulungu. Mulungu akhalidzamo

Ndipamene miala yonse ikhala pamodzi ndi mamangidwe ndi makonzedwe amene tonse tingakhale ngati kwathu. Zimenezi ndi zoona kwa Yesu. Nyumba ya Yesu imangidwa ndi mamangidwe ake ndithu osati athu. mamangidwe ake ndi oti abambo zana, Amayi, Abale ndi alongo. Makonzedwe ake ndi kuti tichitsilike. Makonzedwe ake ndi oti titengeleni zobvuta ndi kukwanilista lamulo la Kristo. makonzedwe ake ndi oti tikhale pamodzi monga iye ndi Atate ali—Amodzi monga tikaona Timu, mwaonanso David mukaona mwana mwaonanso atate. Yesu anati tidzakhala amodzi monganso iwo ali tiyenelanso kukhalanso otere osati myala yosiyanasiyana ndi kubwera pamodzi la Mulungu, koma banja lomangidwa pamodzi tsiku ndi tsiku.

Uku ndi kumanga kwa Yesu Mphepo idzabwera ndipo nyumbayi yidzaimabe. Yesu adzabwera ndi kukhala pa nyumbayi ndipo idzabweretsa iye kukondwera ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa anthu ake mu dziko lili lonse, ndipo tikuitanani ku zinthu izi mwa changu.

Atate Chikwi, Amayi, Abale, Alongo

Atate chikwi, Amayi, Abale, Alongo Yesu anati ngati mundimvera ine mudzakhaladi atate chikwi Amayi, Abale, Alongo osati chikwi cha okhala pafupi koma chikwi cha abale apa banja. Ichi ndi chifuniro cha Mulungu. Ichi ndi chiphunzitso cha Yesu kuti amange ndi zida zabwino. Zida zoipa sizololedwa ngati sizisintha. Nyumba ya Yesu ndi yomangidwa ndi mamangidwe ake osati athu ndipo mamangidwe ake ndi Atate chikwi Amayi, Abale, ndi Alongo mamangidwe ake ndi oti tiyenera kuwulura machimo kwa wina ndi mzake kuti tichiridziwe manangidwe ake ndi yoti titengelane zothobwitsa ndi kukwaniritsa lamulo la ambuye. Manangidwe ake ndi oti tiyenera kukhala amodzi woti ukaona Timu wawonanso Devedi. Ukaona mwana wawonanso Atate. Yesu anati tiyenera kukhala amodzi monga iwo ali ifenso tikhalenso munjira yotereyo osati miyala yosiyana imene imabwela la Mulungu koma banja lomangidwa pamodzi tsiku ndi tsiku.

Kubweretsa Chokoma Kwa Yesu

Ngati pali zosintha zina zimene zili zofunika kuchitika. Yesu anati “Ngati undikonda ine” mudzasunga malamulo anga” ndiye chonde sinthani pazimene Yesu akuitamilani. Musaope ai, Ambiri safuna kukonda chikondi ndi choonadi ndipo adzakhala okwiya ndi zinthu izi chifukwa ali ndi zinthu zobisika mu moyo wawo, njira yoona ya Mulungu imakhala yokanidwa ndi Satana, Mdani.

Ndiye limbikani, pililani ndi kudekha mu zinthu zonse izi, wonetsani chikodni kwa Yesu pakuchita chili chonse chimene pa chiphunzitso cha Yesu. Pepani abale ndi alongo amene kungathe kukhala nawo, pemphelani ndi iwo lankhulani ndi iwo. Onongani zopinga pakati pa abale ndi alongo, zopinga za mantha ndi kunyada, zopinga za ulesi kapenda zochititsa manyazi, zopinga za ulesi kapena zochititsa manyazi, zopinga za manyazi, zopinga za chiweruzo, tengani zonsezi ndi kuchapa zonse pachifuniro cha Yesu. Phunzilani kukondana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku. Izi sizidzangobweretsa Yesu chimwene chokha, chifukwa choti ndi mamangidwa a mpingo wake, koma sizidzasintha moyo wanu kopambana muyeseni Ambuye lero, zinthu izi ndi zoona.

Kwa inu a Kristo woonadi, amene muli ndi mzimu woyera wamoyo inu, tsiku lina, sitidzakhala ndi chilankhulidwe chosiyanasiyana. Matembelero a Babelo adzaonongedwa, miyala yonse ya moyo idzakhala ndi kuthekera pokhala ndi kulankhula ndi mgwirizano odzaza wina ndi mnzake.

 

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon