Nyumba Ya Mulungu

4/8/2003

Komba, Malawi, Africa 1996

Banja La “Thanzi”—Mkwatibwi Wokonzeka

Posachedwa, Yesu abwera chifukwa cha mkwatibwi wake. Bayibulo likuti Yesu adzabwelera mkwatibwi yemwe wadzikhonzekeletsa yekha. Kodi tingayikidzike bwanji miyoyo yathu kukhala yokonzekera? Chabwino, lingalirani chithunzithunzi ichi ndi ine.

Pamene zipembedzo zathu kapena uzimu ukachitika pamalo patsiku limodzi musabata, ndiye dzili ngati kudya chakudya chimodzi sabata iliyonse. Umu simomwe atate anati tikhale. Tayenera kudyetsa matupi athu tsiku lililonse kuti tikhale. Anapangisanso mizimu yathu kudya nthawi zambiri musabata—kudya mkate wochokera kumwamba ndi kukondana wina ndi nzake tsiku, ndi tsiku , ndi tsiku. Anatipanga kukhala mu ufumu wa ansembe pamodzi ndiku bweletsa mkate wamoyo kwa aliyense pamene tikudzukira m’mwamba, pamene tikukhala pansi ndi pamene tikuyenda munjira.

Kupembedza kwa Yesu kuli ngati kudula nkhuni ndiponso ngati tichapa Malaya pamodzi. Timaphunzisana mau a Mulungu mumalo a miyoyo yathu. Pamene tiyenda mu misika pamodzi. Ngati tiona munthu amene ali wovutitsa mkazi wake, timamubweretsela mawu a Mulungu ndikuyamba kumuthandiza kuona Yesu. Pamene tiona mwamuna kapena mkazi amene ali wozikonda ndi zimene alinazo. Timawakonda ndi mau a Mulungu tsiku lililonse. Sitidikila wina ku “lalikira uthenga” okhunzana ndi izo la Mulungu, koma timawapatsa mau a Mulungu chifukwa tonse ndife a nsembe.

Mwana wang’ono amene amadya chakudya chimodzi sabata iliyonse akhodza kudwala ndi kufowoka. Izi ndi zowona za mkwatibwi wa Yesu. Tayenera kudzidyetsa tsiku ndi tsiku ndi utsiku, tsiku ndi usiku—kuti tikule a mphamvu. Timadyetsana mau a Mulungu. Timapembeza limodzi tsiku lililonse. Timamufunsa Mulungu kuti atithandize tsiku lililonse.

Anthu ambiri atha kuganiza kuti banja la thupi lingadwale kwambiri ngati lingamasonkhane la Mulungu ndi la chitatu lokha lokha. Mu bayibulo, tikuwerenga dza banja la Mulungu ku Machitidwe 2. Akunena bwino bwino kuti adali pamodzi tsiku lililonse ndipo amadzipereka tsiku lililonse kudziphunzitsa za atumwi, kutumikirana m’modzi ndi nzake. Ndikupemphera limodzi. Tsiku lililonse, usiku uliwonse. Samadzitengela zomwe alinazo ngati zawo. Adanyema mkate ndi kudya limodzi mumanyumba awo tsiku lililonse.

Tidanzidwa zaka zambiri kuti chikhristu ndi mpingo ndi chinthu chimene tingochionerela ndikubwereranso ku moyo wa kale linja. Tili ndi mayiko awiri kapena atatu osiyana. Tili ndi dziko la kunyumba kwathu ndi banja, dziko la ku ntchito ndi kukhala, ndi dziko la “mpingo” wathu. Yesu wathu adatiphunzitsa kuti mayiko onsewa ali pamodzi ndiponso ali chimodzi. Aliyense amene wapereka miyoyo yawo kwa Yesu ali ndi dzana (100) la atate, azimayi, abale, alongo, malo ndi zinthu—osati dzana la anthu. Oyandikana nawo ndi okuwadziwapo ena, koma dzana la amayi ndi abambo. Izi ndi zomwe Yesu adatimphunzitsa. Ichi ndi chomwe mpingo ukuthandauza. Tsimalo opitako, koma chomwe tili tsiku lililonse. Mpingo uli ngati kukhala pamodzi ndi pafupi ndi wina ndi mzache ngati mayi ndi mwana wongobadwa kumene. Awa ndi mau eni eni a Yesu.

Zotsinga

Sono chimatipangasa kuti tidzitsiye zinthunzi ndi chiyani?

Chotsinga choyamba ndi chiphunzitso chotsamalizika chomwe tidaphunzitsika dzaka zapita zambiri. Koma chomwe tikazindikira ziphunzitso za Yesu zokhudza zinthuzi. Pali zotsekereza kapena zotsinga zotipangitsa kutsiya njira yomwe Yesu afuna kuti tikhale ngati mpingo. Ngati tikhala odzikonda kapena aulesi. Sitikufuna kukhala mpingo womwe Yesu afuna kuti tikakhale. Tikufuna kukhala moyo wathu m’mene tafunira kukhalira. Ngati wina abwera kwa inu kapena kwa ine ndi kubweretsela uthenga wa Yesu za momwe tikukhalira ndi akazi athu kapena amuna athu. Munthu wozikonda amati, “dziwa zako. Pitani kutali ndi ine.

Koma iyi sinjira ya Yesu akuti, “Aliyense amene andidziwa ndi kundikonda ine akonda dziphunzitso zomwe ndi phunzitsa.” Wokond Yesu adzanena “Dzikomo kwambiri chifukwa chondithandiza.” Ndikufuna kumudziwa Yesu kwambiri. Ndinali wosaona koma mwandithandiza kuonanso pang’ono, ndikuthokoza pa ichi.” Umu ndi momwe banja la Mulungu layenera kukhalira pamodzi tsiku lililonse. Timathandizana kudziwa bwino Yesu pothandizzana kusiya tchimo, kondanani wina ndi nzake, ndi kusamalira monga tidzisamala ife eni. Izi ndi ziphunzitso za Yesu. Umu ndi momwe adakhala moyo wake ndi ife, ndi momwe watiyitanila kukhala moyo uwu ndi wina ndi mzache. Umu ndi momwe mkwatibwi wayenela kukhonzekera kubweranso kwa mkwati Yesu.

Ichi ndi chifunilo cha Atate kuti “tisakhuze mkwatibwi” koma kukhala mkwatibwi. Titha kupanga ichi ngati tikondana ndi kusinthana miyoyo ndi wina ndi mzache tsiku ndi tsiku. Izi zipotsa kuti “Hi!” ndi kuti “ndimakukonda!” ndi kamayenda. M’malo mwake. Nditsekula mtima wanga kwa iwe ndikukufunsa kuti undithandize. Ngati muona tchimo m’moyo mwanga, simupita njira yina ndi kuyisala. Inu ndinu a kazembe ake a Yesu monga momwe Mulungu amandiuzila kudzera mwa inu.

Uwu ndi mpingo—kukhala moyo uwu tsiku lililonse, osati kupita ku nyumba ya Mulungu, koma kukhala malo omwe Mulungu amakhala. Ndiye manyumba athu, m’malo ogwilira ntchito athu ndi mipingo yathu yonse ili limodzi, ndi yayikulu. Palibenso zotsekereza kumtima wanga ndi wanu komanso dzotsekereza kunyumba kwanga ndi kwanu. Ndikutchosa kudzikonda kwanga ndi kudzikuza, ndikuchotsa ulesi wanga ndi kusakhulupirila ndipo ndikukonda ena ngati momwe Yesu adandikondera. Ngati wina aliyense achita izi, kuchokera ang’ono mpaka aakulu, Yesu adzathira mafuta amachiritso ndipo ife ndife mpingo ndi mkwatibwi wokongola. Ngati sitidzafuna kukhala nawo m’mawa wa tsiku la sabata, ife tidzasemphana ndi mtima womwe uitana za Mulungu, ndipo tisakhale zipembezo zomwe zili zopanda phindu.

Utsogoleri M’nyumba Ya Mulungu

Kumachitidwe 20, Paulo amalankhula kwa atsogoleri ena ndikuti, “ndali Mzimu Woyela womwe adakupangitsani kukhala wamkulu woyang’anira.” Izi ndi zotsiyana ndi njira ya munthu. M’mayiko ambiri omwe takhala tikupitako, njira yomwe munthu amakhalira mtsogoleri m’nyumba ya Mulungu ndi pokha pokha apita ku sukulu ya dza bayibulo kapena ku seminare, kapena awerenge kupotsa momw anthu ena amgathe, koma zonsezi ndi zifukwa zosayenera. Izi si njira zomwe Mulungu amapangira atsogoleri.

Padali nthawi zomwe takhala tikuyenda mumipingo yosiyana siyana muma tauni ndipo tidafunsidwa kulankhula ndi atsogoleri. Panthawiyo, padali njira ziwiri zomwe tidaganiza omwe ali tsogoleri. Njira yapafupi ndiyoganiza kuti, “Kodi amene ali mu utsogoleri ndi ndani, kapena kodi ndi ati amene adatsankhidwa ndi anthu kukhala atsogoleri?” chabwino atsogoleri ndi okhawo amene amakhala ndi a maudindo awo, mwa chisanzo “Abusa kapena abusa aakulu”.

Koma umu ndi momwe Mulungu amasankhira atsogoleri ake. Sadasankhe anthu chifukwa cha sukulu ya baibulo kapena seminare. Adasankha anthu momwe adaona mumitima yawo ndi kuona kuti adali okonzeka kusiya machimo awo ndi dzikhumbo khumbo pa moyo wa munthu ndi kumtsata pokhapokha iye kuwapulumutsa iwo dzingavute maka. Sono, ngati tafunsidwa kulankhula ndi atsogoleri muma tauni kapena mumayiko osiyana siyana. M’malo moyitana aliyense amene ali ndi udindo kapena m’maina kuti abwere, talankhula kuti, aliyense amene apita kukagona napempherela anthu oyela mtima, amene masana amasamala oyera mtima ena ndi ena osakhulupirira, amene ali ndi mtima womusata cholinga cha Mulungu mu dziko, amuna kapena akazi, ang’ono kapena akulu, ngati musamalira mizimu ya anthu ena osati pa inu nokha, ndiye kuti ndinu mtsogoleri. Bwerani tiyeni tilankhule umu ndi momwe mzimu woyera umapangira oyang’anira aakulu. Izi dzikusiyana kusankha mtsogoleri kamba ka udindo kapena maphunziro.

Machitidwe 6, padali ntchito yaikulu yochita ku Yerusalemu. Sadanene kuti sankhani anthu awiri amene ali ndi seminare yamaphunziro ndi kutsogolera bwino kapena kulankhula bwino kusiyana ndi ena.” Iwo anati, “sankhani anthu asanu ndi awiri mwa inu amene ali odzazidwa ndi mzimu woyera ndi nzeru.” Mukuona anthu achikondi ndi anthu othandiza moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Awa ndi amuna ndi akazi amene Mzimu Oyera ukuwadzutsa. Sidzitengera pepala lamaphunziro lomwe aliyika pakhoma ndi chizindikiro cha golide. Dzimatengela mtima wosweka ndi chizindiki cha Mzimu woyera. Sono izi ndi ziphunzitso zina za utsogoleri, chifukwa Mulungu akufuna kusankha adzitsogoleri pa anthu onse.

Zomwe munthu amaganiza kuti ndi zofunikira, Mulungu saganiza choncho. Pamene Samueli amafuna kusankha munthu wokhala mfumu, ambiri adzibale a Davide adaoneka kuti adzakhala atsogoleri abwino. Koma wang’ono, kanyamata kabusa nkhosa kadali komwe Mulungu adasankha, tsalabada za mkati mwa mbale kapena mlongo. Amaona za bwino ndi ukulu wa mtima wa munthu ameneyo. Davide amafunitsitsa kuteteza moyo wake ndi wa nkhosa zake ku mkango ndi dzi mbalangondo. Davide ali wang’ono adapha mkango ndi chimbalangondo kuti apulumutse kankhosa kamodzi ka Mulungu. Davide adamuuza Sauli “ndapha mkango” ndapha chimbalangondo ndithanso kupha Goliyati.” Chifukw aDavide adali wodzipereka kupulumutsa nkhosa, Mulungu adaona kuti Davide athanso kupereka moyo wake pa ana ake. Ichi ndi chizindikiro cha mwamuna ndi mkazi chomwe Mulungu adzutse kukhala mtsogoleri, osati mwamuna kapena mkazi omwe adachita bwino mumaphunziro, koma munthu yemwe adzazipereka moyo wake pa nkhosa za Mulungu.

Bukhu la Machitidwe likulankhulanso za Davide kuti adali wakufuna kwa Mulungu chifukwa amachita zonse zomwe Mulungu amafuna. Davide adalakwa m’moyo wake, tikudziwa zimenezi. Koma mtima wake udali woti akachite zonse zomwe Mulungu anena. Pa chifukwa chimenechi Mulungu amapungulira mafuta an’dalitso pa iye ndi kumuvomereza Davide kukhala mtsogoleri pa anthu ake—chifukwa amdzipereka moyo wake pa nkhosa za Mulungu ndi kuchita zonse zomwe mbuye wafuna kuti akachite. Ichi ndi chikondi cha Mulungu: Amuna, Akazi ndi ana amene adzapereka miyoyo yawo pa nkhosa za Mulungu, ndi omwe adzachite zonse zomwe Mulungu adzanena, omwe adzachite zonse zomwe Mulungu adzafunse—iwo ali amuna, akazi ndi ana omwe ali akumtima wake wa Mulungu. Ameni?

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon