Mtima, Moyo, Maganizo Ndi Mphamvu

2003

October 1999, AFRICA

POSACHEDWA, ndinalankhula ndi atate zatathauzo lakukonda iye. Kukambirana kwithu kunali kukhuza ine. Kulingana ndi mutu wakukonda iye kuchoka pa mtima wabwera kulingana ndi nyimbo imene mbale anayamba kale. Ndikumva ngati ndinene zimene iye anayamba kuphunzitsa ine posachedwapa. Ngati ziri choncho, ndifuna ndigawane nanu zimene Mulungu wawonesela ine zokhuza kumukonda iye.

Ndidziwa tonsefe lamulo lalikulu zikupanga nzeru kwa ine kuti ngati sitimvera lamulo lirilonse tisayambe ndikusamvera lamulo lalikulu. Inde popeza sitifuna kusamvera malamulowa ingakhale limodzi la iwo; koma limene anena Yesu ndi lalikulu pa onsewa ndilofunika kuliona ndi chidwi chachikulu. Nditafunsa atate tanthauzo lake lakukonda iye, anandikumbutsa za lamulo lalikulu, anandifunsa kuti ndigwirizane naye zatanthauzo la lamulo lake.

Mulungu anati timukonde ndi mtima wathu wonse, timukonde ndi moyo wathu wonse, timukonde ndi maganizo athu onse, timukondenso ndi mphamvu zathu zonse. Tikaganiza tonse pamodzi za tanthauzo la zimenezi, ndinaganiza ndikulemba za izo; ndinapanga izi mwa ine ndekha, ndi chiyanjano changa ndi iye; ngati mufuna tikhoza kugawana zomwe tidakamba.

Mtima Wathu Wonse

Pamene iye anati timukonde ndi mtima wathu onse. Panali zinthu zapadera zimene iye anali kutanthauza. Kutanthauza kuti tizipeleke kwa iye mwatunthu. Safuna mpikisano pakudzipeleka kwa mtima wathu; ngati ndi mvera lamulo lakukonda iye ndi mtima wanga wonse; ndisamalize ndi mtima wanga wonse. Ndipange chisankho cha mtima wanga. Tonsefe timasamira pakuzipereka za zinthu zosiyanasiyana.

Anthu ena amazipeleka pakudya zinthu. Mumayoko ena, kuzipeleka pa chakudya chiri chinthu chofunika kwambiri. M’dziko la itale, mwa chisanzo amanunkha chakudya ndi kuti ziri bwino amachipatsa ulemu chakudyacho ndikuchikonda zedi; ndi kukonda kununkhila kwa chakudya.

Mulungu anati sindizakonda kuti ukhale osusukira chakudya mu mtima mwako (mtundu wa chakudya chotere) ndi kuti kodi ichi sichodabwitsa chakudyachi ndi chingwiro, chikumukhila bwino, ndi chodyeka bwino. Chakudyachi chiri chokongola m’maonekedwe. Mulungu wati iyayi usazipeleke pa zinthu zopirira, anthu akutayika za zimenezi Mbuye anati, ndifuna uzipeleke kwa ine, osati pachakudya, chakudya m’chabwino koma usazipeleke mwatunthu ku icho.

M’maiko ena, mdzikhalidwe, zathu mpingo saunvetsa, ndipo kuti mpingo si banja leni-leni. Anthu anapeleka mtima wawo ku mabanja a thupi. Taonani, ili ndi banja langa, mmalo mopeleka mtima wanga kuzimene Yesu ananena kukhuza athu a Mulungu ngati banja lake, amakhala ndi chidwi chapadera dera anakhalanso ndi Nsanje ya banja anthu awa ati ndidzina langa lotsiliza la ine.

Anthu awa awoneka ngati ine—Abambo anga, Amayi anga ndi Ana anga. Amalora chakudya, mwazi, chinyengo, chikhale chosusa mzimu wa choonadi wa khristu ndikutiuza tanthauzo leni leni la banja pamene ife tabadwa mwatsopano. Yesu amati chiani za ichi? Azimayi zana abale ndi alongo, amayi anga ndani? Abale kapena alongo? Amene achita cholinga cha Mulungu basi.

Anthu ena a chipembedzo a ali ndi mtima wokonda banja lawo la thupi basi munjira yopusisa athu kuti asaziwe m’mene tiyenera kukhalira moyo wosangalasa Yehova.

Ngati ziri m’mene tionere ife zokhuza banja tisamale banja lathu la thupi; ndife oipisisa kuposa anthu osapemphera. Mawu amati, ndithu tikonde akazi athu, amuna athu ndi ana athu. Koma mtima wanga akazipereka pa ichi ndikupatsa khungu anthu ena ndiye zingokhala kuti ine, ine, ine! Uku ndikulakwitsa kwakukuru. Mtumwi Paulo anati kwa ife ndi Mzimu amane anali ndi akazi akhale ngati alibe, umu ndi m’mene mawu anenera. Mawu sakuti, musawakonde akazi anu ndikuwasamala chimodzi amuna anu ndi ana anu. Mulungu anati, ndiri ndi nsanje ndi kudzipereka kwa mtima wako. Mulungu akuti uzipeleke mwatunthu kwa ife. Kenako ndisazigawa kwa anthu ena tisakhale eni ma banja ndilatengedwa ndi iwo monga a khungu.

Mitima yathu ili ya kwa Mulungu, mitima yathu yonse.

Ndaonapo anthu akuzipeleka kuzinthu zopusa; amangoyenda mtunda wopanda chirichonse.

Akhoza kuyima pa nyanja ndikuyang’ana mafunde chifukwa amakonda kuona madzi. Muganiza za ine ndi chilengedwe changa. Musataye chikondi chanu ndi kuzipeleka kwanu pa zinthu zonse ndinalenga.

Anthu ena amazipeleka ku zinthu za dziko. Amakhala ndi nsanje pa dziko lawo. Mukaonera mpira, kapena kanema, pamakhala mpira wa dziko lonse, dziko ndi dziko kusewera mpira. M’malo amenewa anthu amaima chifukwa timu yawo yalephera. Ambiri amakhala ndi chimwemwe pamene timu yawo yapambana.

Mulungu anati, iyayi mtima wanu ukhale kwa ine basi. Usapeleke mtima wako ku zinthu popanda pake. Ukhoza kuonera moira, ukhoza kukondwera pamene timu yako ipambana, koma kulira ndi kukondwa usiyire ine atero Mulungu.

Mulungu wati afuna, mtima wathu wonse, ndikaona zimenezi kubwera mtima wanga, kaya ndi pachakudya kapena pa banja, kapena pamasewera a mpira, ndiope Mulungu basi, ndisazipereka pang’ono ku zinthu za iye.

Iye anati, ndifuna mtima wako wonse, ndifuna kuzipereka kwako konse kwa ine. Ili ndi lamulo, choncho ndichite chimenechi ndikaona mtima wanga ukufuna zina ndi bweze kuti ulowele kwa ambuye basi. Ndilamulo choncho, chisankho chimene ndingapange chikhale chotere. Ndiziperekeletu kwa iye basi osati ku zinthu zina ayi.

Moyo Wathu Wonse

Chinthu chinanso ndi chakuti “Moyo wanga wonse” ichi chitanthauza zinthu zambiri. Zikuchitachita ndi mawu woti (kuzikuza) zichitechite ndi zinthu zimene muli chizindikiro changa. Ine ndine ndani? Kapena ndiganiza kuti ndine ndani? Uwu ndi moyo wanga. Ndakangalika pozilora ndekha kunyadira pa zinthu zimene ndakwanilitsa. Ndachita zazikulu mu malonda ndipo ndikumva bwino pa zimenezi. Ndikuchimva kuti ndine odala ndikumva bwino ndikuzimverera ndekha kuti zanga ziri bwino. Ndine waukhondo ndipo zanga ziri bwino. Ndine wochenjera ndipo zanga ziri bwino. Ndikhonza kupangisa anthu kuseka.

Ndikhonza kunena nthano kapena nkhani ndikumva bwino pazimenezi. Ana anga ndimawasamalira, kuposa anthu ena ndimamva bwino pazimenezi. Ndiri ndikusunga kwa zinthu kuposa mmene eana achitira, choncho ndimamvanso bwino. Sindigonja, ena amataya mtima, koma ine ndine wamphamvu, ndipo ine sindigonja.

Uwu ndi “moyo wanga” ndipo uku ndikulakwa kwakulu pamaso pa Mulungu kukhuza zinthu zotelezi makhoza kulingalira zambiri. Kumbukirani m’mene satana anachotsedwa kumwamba. Satana anali ndi mzimu woti ine, ine, ine nthawi zambiri. Sanaphe mngelo kumwamba. Iyeyu sanaze katundu wa mngelo aliyense. Koma anali ndi maganizo oyipa. Anaganiza za yekha osati Mulungu.

Iye anati, ndine wokongola, ndizakwera nakhala ngati wamkulu kulu. Ndili nayo mphatso yakuyimba, ndipo ndinawala kuposa miyala yamtengo wake, ndiri nawo ufulu woonedwa kuti ndilipo komanso wofunika.

Ndiri nawo ufulu woti anthu aziziwa kuti ndilipo, komanso kutcheleza kwa ine chifukwa ndine wofunika, ndiwapadera ndili ndi uzimu kuposa angelo onsewa.

Mulungu anati, ndakuchosa pakupezeka kwanga Mulungu akuti, undikonde ine ndi mtima wako wonse, uchengetere mtima wako ndi moyo wako, kuti undipembeze ine ndikundikonda ndi moyo wako wonse.

Mtumwi Paulo anati, ndiri nazo zoti ndikhoza kunyadira, koma ndiyenera kuti ndinyadire mwa Yesu ndi iye wopachikidwayo. Ndapachikidwa ku dziko ndipo dziko—lapachikidwa kwa ine.

Iye anati, ine ndine wamkulu wawo chimwa ndine woipitsisa ndi wochepetsetsa mwa iwo wokhulupira Mulungu. Ndinyadire muzopeka zanga, uyu anali Paulo Mtumwi amene anli munthu wabwino. Koma anapanga chisankho chokonda ambuye, ndi mtima wache wonse anakondanso Mulungu wache ndi moyo wache wonse. Sananyade chifukwa chazimene iye anachita kapena m’mene iye anakhalira muzochita zache.

Munthu ameneyu (Paulo) anapita mmwamba nthawi yina kumene Mulungu anakhala. Koma sanafune kunena za zonsezi, iye anati, ndiziwa munthu amane zaka zambiri zapitazo sananyade, ine ndine Paulo mtumwi, ine ndinapitako kumwamba. Anali wozichepesa kuti alankhule zimenezi sanafune kuzisangalasa yekha. Sanafune kukhala wozindikira yekha, sanafune kuti azikwezedwa monga Yohane mbatizi, anazichepesa kuti Yesu mwa iye akwezeke.

Nthawi zonse timakonda kuzilabadira tokha pakuganiza za ife tokha, tikuzipatula tonse kwa Mulungu. Nthawi zonse timapanga zisankho zokondweresa tokha; kuposa monga momwe tiriri, tikuzipatula tokha kwa Mulungu wathu. Nthawi zonse tikamaweluza anzathu timayesa kuti ndife apamwamba kuposa ena; tikuzipatula tokha ndi Mulungu wathu. Mulungu anati undikonde ndi mtima wako wonse. Iwe yense ukonde Mulungu ndi zinthu zonse zimene ziri zofunika kwa iwe zikonde ine ndikutumikila ine upezeke mwa Yesu ndi chizindikiro chako chonse. Undikonde ndi moyo wako wonse, upeze chizindikiro chako mwa Yesu ndi mwazi wake; zida zonse uli nazo zikuthandize kutumikira ine. Palibe mwini wa zinthu zonsezi ndi Mulungu basi. Tisanyade chifukwa cha zomwe Mulungu wachita ndi zake, ndipo ndizaiye yekha. Pamene timanga nyumba ndi manja athu tikabwera kunyumba imeneyi tisayende ndikuti, ee! Ntchito yabwino ndayichita; kapena kuti ndamanga nyumba yabwino; ndamanga ndi manja anga, ndagwira ntchito yabwino pokuza ana anga tisazipatse mphamvu tokha.

Moyo wathu uli wa Yesu ndi atate Mulungu akuti undikonde ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse.

Malingaliro Athu Onse

Ndinafunsa atate tanthauzo la zimenezi, ndifuna iwe undikonde ndi maganizo ako onse. Nthawi zina zinthu izi zimasokoneza. Koma chinthu chimodzi anandionetsa chokhuza kukonda iye ndimaganizo wonse maganizo amane amabwera aziyimilira chisankho chimene ndimapanga. Ngati ndimkonda iye ndi malingaliro anga onse, ndiye pafunika ndizipanga chisankho pa lingaliro lililonse lobwera kwa ine. Mawu amati, mwa Paulo mtumwi tirimange lingaliro lililonse. Tizilisusa lingaliro lililonse loyipa lomwe lichite chilungamo.

Mulungu amati chiri chonse chabwino chokoma, chiri chonse choyera, choyenera matamando, ganizani za zinthu zimenezi. Paulo amati, timasinthika pamene takonza malingaliro athu.

Aroma 8 amati malingaliro amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu ali moyo Mtendere.

Kodi ena mwa inu mumakhalapo ndi mkwiyo wam’maganizo? Kapena lingaliro la Nsanje? Kapena la ukali? Kapena la chilakolako? Kapena la kunyada? Awa ndi malingaliro amene amzionetsela okha mwa iwe. Zili ngati munthu wa chichepela walowa m’malingaliro anu ndikuti, ndifuna ndikuonetseni kulingalira.

Mphamvu Zathu Zonse

Tonsefe tiri ndi zisankho zathu, tsiku lililonse, tizasankha kapena kuti maonekedwe athu apita kapena ayi pamene timkonda Mulungu ndi mtima wathu wonse. Tizasankha zimene moyo wathu watilora kuchita kapena ayi. Moyo wanga wandilora kupeza chizindikiro changa mu zinthu zina, kupatula mwa Yesu. Paulo anati, ndapachikidwa ndi Yesu akhala wa moyo mwa ine. Paulo anaconda Mulungu ndi moyo wake wonse. Chizindikiro chake chinali, mwazi wa Yesu basi.

Anathandauza Yesu basi osati chinanso. Ngati timakonda Yesu ndi moyo wathu wonse, tizalora mawu a Mulungu ndi malingaliro ake m’maganizo athu.

Sitizalora, kuphingika, kapena chilakolako kapena mantha ayi tizawachotsa m’malingaliro athu. Sitizalora malangizo a mkwiyo, kapena kusakhululuka, kapena Nsanje, kutilamulira ife tizachotsa m’malingaliro athu—sitizakhala ngati anthu a chikunja m’malingaliro koma anthu osinthika ndi otsimikika.

Tizakonda Mulungu ndi malingaliro athu onse. Tizaganiza za iye yekha basi.

Atate amandionetsa kuti mphamvu zathu zimatengera zinthu zambiri. Tikamkonda ndi mphamvu zathu zonse ndiye aziwe kuti nthawi yathu ili ya kwa iye. Nkhani yathu ili gawo la mphamvu yathu timulore Yesu, chikondi cha moyo wathu atiphunzitse m’mene tingapelekele nthawi yathu kwa iye. Sitizalowa zinthu zoononga mphamvu yathu kutiononga ife, tizalora chikondi cha Mulungu pasi kuyenda mmoyo wathu, chakudya chathu chikhale gawo la mphamvu yathu.

Mfumu Davide mtundu wa Yesu, Ambuye akutionetsa chinthu china chofunika pankhani yakukonda Mulungu ndi mphamvu zathu zonse. Anthu ake akhondo anayenera kuziyiwala pamene iwo anali kumenya nkhondo (1 Samueli 21:5)

Kuti tichite zazikulu za Mulungu zitengela mmene timagwiritsila ntchito mphamvu zathu. Tikagwiritsa ntchito mphamvu zathu pa china chilichonse, ndikunena kuti ndatopa sundingatumikire Mulungu, pamenepo ndiye kuti sitikonda Mulungu. Tizipanga chisankho chimene chingatipatse mphamvu zotumikira Mulungu mu nyengo zonse.

Ndalama zathu ziri gawo la mphamvu zathu. Ndalama zimachokera ku ntchito ya manja athu. Gawo la chisankho chimene timapanga pogwiritsa ntchito ndalama timatengera mphamvu zathu. Mtumwi Paulo anati, pamene iye anayenda mzinda ndi mzinda dziko ndi dziko. Anati, chifukwa ndasintha moyo wanu ndakupatsani choonadi chauzimu; ndiri ndi ufulu kukuuzani kuti mundipatse ndalama pa zonzezi.

Munkhozanso kudnipatsa mkate, koma iye anati, iyayi, ndikupatsani chisanzo cha momwe ndimagwirira ntchito ndi manja anga; usana ndi usiku kuti ndikhale wakuthekera kukupatsani ngakhale moyo wanu ndifuna chifukwa cha zinthu za uzimu. Ndakuphunzitsani, sindifuna kukuuzani, kapena zovala zanu, ingakhalenso ndalama. Ndinena njira ya momwe ndingachitire. Ambuye wati, kupatsa kumadaritsa kuposa kupeleka; kotero ndizeza ntchito ya momwe ndingachitire nanu.

Paulo anati azera njira imene angathandizike nayo kuti atumikire Mulungu.

Mawu akuti tizipeleke matupi athu ngati nsembe ya moyo, ndi gawo la thupi lathu ngati zida za chilungamo. Paulo ndi atumwi ena a Mulungu anapachika matupi awo chifukwa cha kusagona tulo ndi kutopa. Amapachika thupi lake pena akakhala ndi njala, kapena kulumidwa ndi zigawenga.

Pamene amaenyedwa nakhala tayile wakufa mu mzinda, chifukwa chakuti anaconda Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Analalikilabe mawu osatopa ingakhale anaganiza kuti iye wafa. Petro ndi Yohane anali ndi mabala a zowawa zomwe anamva chifukwa chotumikira Yesu. Analalikirabe za nkhani ya bwino ya Yesu Khristu.

Stefano, Yakobo, Yohane mbatizi—anazipeleka kwa anthu potumikira Yesu ndi mphamvu zawo zonse. Ifenso tisakonde moyo wathu okha koma Mulungu, ngakhale mpaka imfa itipeze tikutumikira Yesu, tiyeni tidalire Yesu nthawi zonse.

Kulowetsa Kwa Kuya

Nditamfunsa Mulungu za ichi kuti chitanthauzanji? Ndinadabwa yankho lomwe iye anandipatsa akundifuna kuti ndimukonde iye ndi mtima wanga wonse. Chifukwa iye ndi Mulungu wa Nsanje afuna ndimukonde ndi moyo wanga wonse, chifukwa iye ndiwa sanje. Afuna ndimukonde ndi malingaliro anga onse. Ndikalimbana nazo zimeneyi ndikuona kuti moyo wanga ukuyandikira ku zimenezi, ndiona kuti iye akunditengela kw aYesu mozama. Akundipanga ine wanzeru, ndiwokonda komanso womasuka. Akhonza kupangitsa mitsinje ya madzi kuchoka mwa ine monga Yesu analonjeza, akhonza kuzika zinthu zodabwitsa mwa ine ndi mphamvu yake, akhoza kuyika zida za chilungamo kudzanja langa la mazere ndi lamanja.

Eliya munthu ngati ife analamula mitambo isavumbitse mvula, amalamulanso kuti mvula igwe ndipo inagwa. Mawu akuti, Eliya anali ngati ife, palibe chovuta ndi ife ngati tiri ndi Yesu, ndikukonda Mulungu ndi moyo wathu mtima wathu ndi mphamvu zathu zonse. Anthu ambiri sakonda Mulungu ndi chiri chonse chawo. Mukondeni Mulungu ndi mtima, moyo ndi mphamvu zanu zonse.

Ndikuthandizana Wina Ndi Mzake

Gawo liomdzi lakukonda iye limachita chita pamene ife tikonda anzathu amene tikhala nawo limodzi. Kuwakonda ndi zonse zomwe tiri nazo mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, komanso mphamvu zathu—zonse. Akaona wina pafupi ndi iwe akhoza kukhala mbale kapena mlongo, sakonda Mulungu ndi mtima wawo, moyo wawo, kapena mphamvu zawo, Mulungu akuti tiwathandize kuti azitero.

Akuzitora okha komanso panthawi yomweyo abela Mulungu, tikatero, mpingo uzakhala chinthu chaku

Koma zimenezi zimayenda ndi ife ngati munthu m’modzi. Mawu akuti mkondeni iye ndi mtima, moyo komanso ndi mphamvu zanu zonse.

Ichi chinali chakwa ine pakatipa ine ndi Mulungu, koma ngati ndizothandiza kwa inu, pamenepo ndingati ndinali nawo mwayi woti tikambirane.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon