Mapelekedwe A Ndalama Mu Ufumu Wa Mulungu
2003
October 6, 1999 Lilongwe, Malawi Africa
Ku mpingo umene ine ndimakhala kulibe aliyense amene amalipidwa ndalama palibe aliyense amene amatenga ndalama kwa iwo wokha palibenso amene amaphunzitsa kuti apeze ndalama. Koma aliyense ali otanganidwa kupereka monga takhaliramo sitiyendetsa nsengwa koma koma wina aliyense amathandizidwa ku nchito ya Mulungu mu chuma. Pali anthu ambiri amene amapatsidwa udindo mu nyumba mwawo mwa nseri umene abale ndi alongo amapereka pochita zimenezi timafuna kuti dzanja lamanja lisadziwe zimene la manzere likuchita. Sapita kutsogolo kukapereka ndi kuona anthu onse koma amapereka kuchokera pa mtima pawo.
Pali zinthu zambiri zimene anthu ayenera kupereka. Abale ena amaika mu enevolope ndi kujlemba kuseri kuti zigwire nchito yoti. Akhoza kuti kwa “osauka” kuti amene ali osowa pakati pathu kapena mu malo amene timakhalamo angalembenso “zosindikizira mabuku” Monga mwa mabuku amene mwalandorawa ambiri oyera mtima anapereka zopeza zawo chifukwa linali pemphero lawo ndi mtima kugawa choonadi chimene chinali chopambana kwa iwo. Ena angathe kupereka kwa mbale amene akutumikira Ambuye kwambiri, mwina ali ndi ulendo wopita kwina. Sali pa ntchito yomwe amagwira koma chifukwa akufuna kuti akakhale ndi okhulupilira ena kwina amapereka mbali ya zopereka zawo pa chifukwa chimenechi.
Kulemba kuseri kwa enivolopu kumathandiza kulumikiza miyoyo yawo pa zimene zikuchitika. Osangopereka ndalama mosawonetsetsa mu nsengwa ai. Koma ndalamazo zikuimira nchito ya Mulungu. Pamenepo ayenera kulumikiza ntchito imene ili yofunika ku maganizo awo. Sangadziwe kuti sabata ino akapereka kwa ndani ndiye angaike kuti atsogoleri pali zambiri zochitika ndithu.
Mu zaka zoyambilira Chikhristu nthawi zina anthu amaguritsa nyumba ndi kuika ndalama pa mapazi a tumwi ndi kutumizidwa monga kufunikira ndiye nthawi zina zimatero. Kwa nthawi amapereka kwa zinthu zodziwika bwino chifukwa palibe amene ali kuona zingakhalenso ndi ulesi chifukwa dzanja la manzere silikuona la manja. Mungakhale aulesi mukupereka kwanu. Aliyense ayenera kukhala osamala kuti asalore izi kutero. Anthu ambiri ku Amerika amalandira pa ssabata iliyonse uku ndi chabwino kukumbutsa kuti atenga ndalama ku ntchito ya Mulungu. Kodi zayankha funso lanu? Palinso lina? Kodi ndasiya zina zimene zikanathandiza.
Nanga Za Chakhumi?
Chiphunzitso cha chakhumi sichili mu Chipangano chatsopano ngati mukufuna kupereka chakhumi ndiye kuti muyanera kupereka nsembe ya nyama. Ndi chiphunzitso cha Chipangano Chakale. Chipangano Chakalelinali kumvera pa zimene Mulungu ananena kwa anthu ake mu Chipangano Chakale. Chakhumi sichilinso mbali ya nsembe za nyama kapena munthu woyera kapwna wa nsembe kapena kupembedza kwa kuasinsi zinali mbali ya phangano la mwazi wa Yesu, Sali chakhumi mulibenso. Palibe kupereka chakhumi mu mgwilizano watsopano. Anthu amapeza ndalama kwa nkhosa za Mulungu pazogula (zomanga za chipembedzo) ndikulipira malipiro kwa anthu. Potenga malamulo akale ndi malembo kuti anthu a Mulungu apereke, motero anthuomwewa sanenanso za loweruka monga (sabata) kupembedza ku Yerusalemu mkansinsi) kapenanso nsembe za nyama zimene zili mu gawo limeneli. Ndi kusakhulupilika kuchotsa zinthu zina ndi kusakhulupilika kuchotsa zinthu zina ndi kulowetsa zina ndi kuti zinthu zidzikhala motero.
Paulo aanaphunzitsa ndithu kuti tinafa ndi machismo athu ndi mwazi wa Yesu ndi osakwanira kwa ife ngati tikhale mu pangano la kuumbala ndi kusunga sabata ndi kupereka Chakhumi. Palibe gawo lina kupita kwa mbusa mu Baibolo. Iyi sinjira ya Mulungu.
Mu pagano ili Mulungu amafuna ndipo alikufuna kuchokera mu mtima ndi kuti zichokera mu Mzimu. Yesu anati ngati mungapambane chilungamo cha Afarisi simungathe kulowa mu ufumu. Mu pagano limeneli liyenera kukhala mu UBWENZI mu moyo, chikondi chalero ndi Messiah. Kupereka kwathu mu pangano la tsopanoli liyenera kukhala kudzipereka monga mwa kulamula kwake ndi kumvera kwa Mzimu wa Mulungu tsiku ndi tsiku.
Pamene Yesu anaima pa kasinsi mkati anaona mzimayi amane anapereka kwambirimu choperekera ndalama sizidali zochuluka ai monga mwa myezo. Yesu sanati anapereka gawo khumi. Sanaperekanso chakhumi koma anapereka anapereka ndalama zake zogulira chakudya. Mulungu anali opambana kwa iye koposa chakudya. Anakonda Mulungu wake ndi mtima wake wonse moyo, Maganizo ndi mphamvu zake zonse. Sanali fkufuna njira yoperekera mbali ya gawo. Amafuna kupereka Mphatso imene inalipo ndipo Yesu anati Taonani mzimayi uyu Angelo ali kuimba nthungululu ndi kuomba mmanja kwa iye chifukwa sanaganize za chakhumi anapereka mtima wake wonse, maganizo, moyo ndi mphamvu zake zonse. Uwu ndi uthenga wa Chipangano Chatsopano ndipo Chipangano chakale ndi chofooka monga mmene chilili.
Popanda Cholowa
Pamene Paulo amalemba kwa mipingo anati, “sitifuna phindu ku mawu a Mulungu.” Paulo samaona ku Mphatso yake ngati chinthu choti amangire anthu osati kuti apeze ndalama kuchokera kwa anthu. Iye anayesetsa kupereka monga tanena kale ena anazipereka kuti mabukhu amene tabwera nawo asindikizidwe. Sitikugulitsa mabukhuwa tikupereka mabukhuwa kwa inu ndi kwa ena onse. Ziphunzitso za mabukhuwa ndi a Yesu osati Iye Yesu anagawa zinthu zimenezi kwa ife mwaulere ndiye ndithu tifunanso kugawa kwa inu ulere
Ndikujyembekeza kuti sipakhala wina ogulitsa limodzi la mabakhu kwa aliyense. Ndi Mphatso imene Yesu wapereka kwa inu, ngati ndi chiphunnzitso ngati ndi nzeru ngati ndi chidziwitso ngati ndi kuimba kapena kusewera ndi choimbira ngati ndi kuthekera kwa kulankhula bwino ndi zinthu zimene zaikidwa ndi Ambuye kuti muzisalire ndipomphatso imeneyi ndi ya Yesu koma waizeza kwa inu kuti zipindulire anthu ena tsiku lina Yesu analankhula ndi Afarisi ngati mungapemphere kuti ena akuyamikireni ndiye kuti mwalandiratu phindu lake izinso ndi zoona mu nkhani ya ndalama. Ngati mungaphunzitse kapena kuelmba nyimbo kuti ena akulipireni ndiye kuti ndalama imeneyo ndiye malipiro anu. Koma ngati mukufuna kupereka mwaufulu pa zimene Yesu wapereka kwa inu ndipo malipiro ndi akulu. Madalitso ake ndi ochuluka mu miyoyo yokuzungulirani ndipo uzdakhala kulemekeza Mulungu.
Mu zochitika zinanso, aliyense anachita chiganizo kwa Mulungu mu sabata inailiyonse monga angakhalire opereka mmene angaperekere zinthu zawo pakati pa iwo ndi Mulungu amapanga cholinga chifukwa choti amamukonda ndi mtima wawo wonse. Amachita chisankho ndiye amaganiza kuti angapereke ndalama zimenezo. Pali okhala nawo pafupi amane abale oyera mtima amakhala nawo pamodzi. Timaika box kumodzi kwa nyumba zotere ndiye abale amene amakhala mu zinyumbazi za kumeneko amapita mwakachetechete ndiye amapempha Mulungu kuti alandire Mphatso yawo. Analemba kalata ndi Mphatso ndi nchito yake imene yaperekedwera ndiye amaika mu choikira ndi kuchoka.
Ndiye tili ndi abale awiri kapena atatu amene amapita ku zinyumba zimenezo (midzi yaing’onondiye amatenga ndalama kuika malo amodzi ndiye abale osankhidwawa, okhulupilika amagwira ntchito pamodzi amatenga ndalama zimene zalembedwa kwa osauka ndi kutumiza kwa osauka mokhala mwathu. Ndalama zimene zaikidwa kusindikiza mabuku odzafika ndalama zonse pamalo amodzi ndi kupereka kwa iwo amene amasindikiza, ngati pali mbale kapena mlongo amene moyo wawo easintha mabanja awo asintha pa Mphatso ya anthuwo angathenso kulemba dzina angathenso kulemba dzina la munthuyo ndiye abale okhulupilidwa amagwira ntchito pamodzi amapereka kwa iwo amene maina awo analembedwa pa envolopu kuti alandire moyenera. Monga Paulo abale enawo ndi alongo oyenera kupanga ma tenti kapena nchito ina chifukwa Paulo anakhuzidwa ndi miyoyo ya anthu ku Filipi ndi Atosolonika, amatumizira Mphatso pa ntchito kumeneko ndiponso amawasamira ena osowa ndi Mphatso. Amathandizanso abale ena monga Timoteyo ndi Taitasi ndiye kuti sanali kumanga tenti nthawi ndi nthawi mu kalata yak u Afilipi. Paulo anati timalandira nthawi zina ai. Nthawi zina analuka matenti nthawi zina ai. Ngati Mulungu amawathandiza pa zosowa zawo mu njira ina ndiye kuti zinali zabwino ngati ai. Anali kumanga matenti ndi kuthandizanso anthu ena. Popanda vuto choncho abale amene amatolore ndalama anagawa kwa amene dzina lake lalembedwa pa envolopu ndiye satenga kanthu paiwo wokha kodi zikumveka zimenezi.
Pamene wina akupereka ndalama kwa mzake amene wasintha moyo palibe amene amati alandire ndalama chifukwa kuti moyo wake wasinthika. Palibe amene amati ndilandire ndalama. Aliyense amafuna kutumikira Yesu pa Mphatso ili yonse ali nayo. Aliyense osati abusa ndi anthu ena onse. Aliyense mphatsozina ndi zothandiza. Pamene Mphatso zimenezi zikuthandiza inu timafuna kuthandiza mwaulere kuti Mphatso ithandize enachoncho nthawi zina zimachitika koma osati chifukwa wina akuchita malonda mau a Mulungu ku phindu. Cholinga chawo ndi kuthandiza ndi kutumikira sakufuna kupeza ndalama susunthuka kwa iwo kumanga kwa nthawi zaka zisanu kapenanso amasulidwa kwa nthawi amatumikira Ambuye ndi moyo wawo nthawi zonse. Izi ndi zosiyana mmene dziko la chipembedzo limachitira. Anthu amaona mau a Mulungu monga ntchiyo. Sintchito monga umisiri wa matabwa zimenezi mulibe mu Baibolo.
Ndi Bwino Kupereka
Tiwonjezenso Yesu amati tikudalitsika kupereka koposa kulandira ndi kwabwino kulandira koma kwabwino kupereka koma sikwabwino kufuna kupatsidwa osati ana anga akandiuze abambo, abambo tipatseni kanthu ine ndi kumapitiriza ndikulira. Chimene ndingapereke ndi monyinyirika koma ndikuona ana anga ali kugawa ndi ena ndi kukonda anthu ena . Ndidzakhuzidwa ndi kumudodometsa ndi Mphatso. Izi ndi zoona mu banja la Yesu pasaoneke wina amene ali kuumiliza kuti alandire ndalama palibe amene anene mau anati, tili ndi zonse mofanana muyenera kundipatsa ndalama wina asadziyerekeze kunena kuti malemba amati, “ngati uli ndi Malaya awiri pereka limodzi kwa mbale, muli ndi Malaya awiri linalo ndi langa kumeneku ndi kuchimwira kumeneko ndiye kudzikonda choncho ngati wina ali kuumiliza ndalama kapena kena kali konse mpingo usamupatse kwambino kuti awawitsidwe mtima ngati zoonadi kuti ofunikadi kuthandizidwa ndipo abale aonadi kufunika ndi mu chikondi ndi kufnika kugwira nchito ya Yesu amapereka ndi zabwino ndipo ndi zobvamerezeka.
Aliyense Amagwirira Nchito Mulungu Kwa Nthawi Yonse
Pamene Paulo anayenda kuchokera mu mkzinda ndi mdziko kuphunzitsa ena, Paulo sananene inde ndine mtumwi wa Mulungu wapamvandu! Sindingadzitsitse ndekha kupanga matenti. Ndine mtumwi wa Mulungu wamoyo. Paulo anali kupanga matenti pamene amafuna ndalama ngati Mulungu amampatsa mu njira ina zinali bwino koma sanali odandaula kuti ali kumanga matenti. Ngati amamanga matenti ndiye kuti amakuna ndi anthu amenenso amachita chomwecho amene amafuna nsaru zopangira matenti anthu amene amadzagula ,matenti amene amawamanga ndi zimene iye amachita. Iye samasamala kuti anthu apeza ku msika kapenanso musunagogi, moyo wake wonse unali kukonda Mulungu ndi anthu ndi kwa anthu onse mu nthawi ina iliyonse ngati anali ku ndende amayenera kumusandutsa wa ndende ngati anali pa maso a mfumu kudikira mulandu amayesa kusandutsa mfumu ngati akupanga tenti amayesa kusandulitsa omugulawo mmene amapezera moyo wake sizinasinthe kanthu kali konse. Ngati Mulungu apereka zosowa kuchokera kwa abale ndi alongo amene akonda Iye ndipo ali oyamika ndipo anali omasulidwa kumanga tenti kwa kanthawi ndiye anali ndi mpata woyenda nkdi sailasi ndi abale ena kupita ku mizinda ina ngati analibe ndalama monga mmene ananenera mu kalata ya Afilipi monga amachitira. Amapanga matenti kwa kanthawi popanda bvuto.
Miyambo ya anthu zatiphunzitsa ife zoipa pa kunena kuti ndife azitumiki a Mulungu. Paulo anali wamtumiki wa mphamvu koposa anthu ang’ono otenga ndalama kapena osatenga ndalama. Paulo amagwira nchito molimbika ndi manja ake usiku nsi usana ndi kulipira chakudya changa pamene ndinali ndi inu. Mukandipezera chakudya koma ndinalipira ndekha ndimagwira nchito molimbika ndimanja potero kuti tikwaniritse zosowa zanga ndi ena.
Ngati ndizoona mu Mphatso yaikulu monga Paulo bwanji Mphatso zazing’ono zinaganiza kuti ndizosafunika kuti asamagwire nchito ndi manja awo? Ngati Mulungu angatithandize mu njira zina ndabwino koma tisayembekezere kapena kuwumiliza. Ngati anthu a Mulungu ali ndi mtima opereka ndi kutimasula kuti tisamange matenti ndi zabwino. Ngati titumikire tiyenera kupanga matenti ndiye tidzapanga matenti ndi kutumiza kwa zosowa za anthu ena.
Choncho zimenezi ndi zimene takhala tikuchita kwa zaka khumi ndi zisanu(15) kwa iwo ambiri anali a Zimbusa kapenaso atsogoleri anasiya malipilo awo ndi zolandira zawo ndipo Mulungu wakhala okhulupilika ndipo palibe mwayiwo ali ndi njala ndipo ali kutumikira Mulungu nthawi zonse. Oyera mtima onse ndi ana alikutumikira Mulungu nthawi zonse, satumikira Mulungu polandira ndalama amatumikira chifukwa cha chikondi ndipo Mulungu amawapatsa njira zosiyanasiyana. Ichi ndiye choonadi changwiro koma ndichochititsa mantha nthawi zina kuti tisiye miyambo ya anthu. Pamene ndalama sizikhalanso mumatumba athu palibe amene anatumikira Ambuye munjira imeneyi, Mulungu ndikulephera. Ambuye ndiokhulupilika ndipo amasamala akhwangwala ake, amasamalanso mbalame zamulengalenga, amasamalanso iwo amene akonda iye. Palibe opambana anzawo muchikristu.
Palibe muchikhristu pamene anthu amagulitsa mphatso zawo, pamene ena alibiletu mphatso. Palibe amene agulitsa mphatso yake mumpingo ndipo Mulungu amaona aliyese monga kufunika kwake, ndipo Mulungu ndiye amafuna kuti kuchitike ndi zofunika zathu. Ndiye atumiki ake Amulungu nthawi zonse amatumikira kaya ndi kusika, kapena ku ndende,kunyumba kwathu zonsezi ndi choonadi chofunikira. Tiyenera kugwedeza mtengo wa miyambo ya anthu ndikuyigwetsa pansi. Mulungu ndiokhulupilika ndipo azatiteteza ife ngati tichita chomwecho.
Mwachitsanzo ambale ena ndi alongo anafunitsitsa kuti ife tibwere kuno sikuti tidangoganiza choncho kapena kuti ndife odziwika, kotero kuti tingapite kwina kulikonse. Sitili monga choncho, ndife akapolo chabe monganso inunso muli. Kunali kufuna kwao osati kwathu aziperekanso kulipila zithu zina, pamene ife tili kuno.
Sitinawafuse kuti atero . Anthu amulungu amamva Mulungu ndikuganiza pamodzi kuti tibwere, ndimmene zinakhalira.
Mayeso amene Yesu anawapeza pakati mkachisi ndi amene ali ofanafana ndiamene ifenso nthawi zina timakhala nawo, sichoncho?
Kodi tikhulupilira zimenezi?
Funso (La Msiska) Pamene tafuna kupereka uthenga wa mfumu ndi umfumu wake ndi abale amene ali kuchipembedzo pokhudzana ndi ndalama zimene iwo amalandira tingawauze chiyani pokhudzana ndi ndalama zimene amalandira? pamene iwo adalira ndalamazo pa moyo wawo.
Ngati munthu afuna kukhala kuchipembedzo chifukwa cha ndalama Mulungu adzamuweruza kwambiri. Ngati munthu akana choonadi cha Mulungu chifukwa cha ndalama, ndiye kuti ndiwopembedza wa Satana. Tikulankhulazi siza ndalama! Izi ndi za Mulungu, amene ali wamkulu koposa ndalama! Tiyenera kunkhulupilira Mulungu ndikumumvera iye muzowawa zonse. Ngati ndizowawa za m´banja kaya ndi nyumba, kaya ndi ntchito, kaya ndalama zathu zonse-zimenezi ndizithu za Yesu zomuyenera muzilizonse zokumana nazo.
Petulo ndi Yohane adati, “siliva ndi golide NDILIBE. Koma ndili ndi Yesu ameneyo ndikupatsa iwe”.Ngati chipembedzo chimwaza ndalama kwa wanthu ndiye kudalira kwawo, ndipo anthu amenewo akayamba kumvera Yesu polandira zowawa zilizonse, chithu chimodzi kapena ziwiri zidzachitika choyamba kuchitika, ndiye choonadi cha Mulungu chidzabwera chipembedzocho ndikusintha chipembedzo chonsecho. Anthu adzayamba kupeleka ndalama chifukwa miyoyo yawo yasinthika. Chinanso chidzachitika kuti chipembedzocho chidzasiya kupeleka ndalama. Ndipo ngati asiya kupeleka ndalama……. Ndiye kuti “ZIDZAKHALA CHONCHO!” Ambuye adzapereka kwa omvera ndiokhulupilika.
Kodi timankhulupilira kuti Mulungu ali ndi ng’ombe m’mapiri? Kodi timakhulupilira kuti tikafunsa iye m’dzina la Yesu adzatipatsa? Kodi timankhulupilira kuti amatikonda kwambiri koposa khungumbwi ndi maluwa ammunda? Kodi chingakhale kuti ndi chipembedzo chabe chofuna kupeza zithu mwa ife tokha? Ngati mutsata njira ya Mulungu potsata ndalama, kapena ngati munyengelera ndikusiya choonadi cha Mulungu chifukwa cha ndalama ndiye ndikuuzani chithu chimodzi monga Paulo adati kwa Simoni wa nyanga. “Iwe ndi ndalama yako utaika nayo ku Jehena” Tisakhudzidwe ndi ndalama. Tinkhulupilire Mulungu ndikumvera Mulungu muzowawa zili zonse iye ndiye atate odabwitsa amene akonda kupeleka mphatso zabwino kwa ana ake.
Ganizirani zimenezi……..
Pamene Ethiopia lidali dziko la chikristu ndipo anthu ndikumaopa Mulungu,Ethiopia adatchedwa mkate mundengu la Afrika.
Chabwino ndi Mulungu amene amamvubwitsa mvula, kuti mela ukule ndi ziweto kusangalala ndiponso dziko kutukuka. Pamene Ethiopia anakhala dziko la chisilamu ndipo chihristu chinapeputsidwa, Mulungu anaweruza dzikolo ndipo mvula inasiya kugwa. Ethiopia lero ndichipululu osati mkate odzadza.
Siyani ndi kuganizira zimenezi chifukwa chimene ndikulankhulachi ndi chimene chimabwezeletsa choona mmbuyo. Ngati tidzamanga nyumba ya Mulungu osati mmamangidwe athu ndipo ngati tidzapeleka tokha poteteza chuma chathu ndiye kuti Mulungu adzakulitsa mbeu yathu. Adzagwetsa mvula, ndipo ma bizinezi athu adzatukuka, ndipo adzapeza njira yotisamala pa zofuna zathu
Ngati Njira ina tiziteteza tokha ndi kunyengelera pakusamvera choonadichi chifukwa cha mantha pa zimene zingatigwere, ndiye Mulungu adzatilanga. Kotero kuti matumba athu adzakhala obowoka . Ndalama zomwe timaganizira zizizakhalanso motero. Mbeu zomwe tizabzala mmunda zizakula moyenera koma ngati tikulupilira Mulungu adzatisamala ife tonse choncho ngati sitimvera adzatiweluza ife monga anena( Haggai Chaputala Choyamba)
Ndiliti Mulungu adzakhala ndi athu amene amukhulupilira iye kotheratu ndi kumvera iye mu zowawa zirizonse? Kodi mudzakhala muli inuyo? Ngati sichoncho mudzaola . Mudzakhala opambana mu ULEMELERO WA MULUNGU
Ambuye Mulungu wamphamvu , choonde mvetselani pemphero lathu tsopano, Tikupemphani inu tsopano kuti mutsegule ku mwamba. Choonde pitilizani kuthila bvumbulutso kwa abale ndi alongo okhulupilikawa, pitilizani kuthila mafuta a chikonwelero kwa iwo amene amvera. Pitilizani kumanga mpingo wanu ndi nzeru za kuya Chikondi ndi kudzipeleka kwaiwo onvera inu mudipo lilonse tikupemphaninso Atate Mulungu monga mwa malonjezo anu mubuku la Detolonome kuti mudzabweretsa matembelero ndi ma weluzo kwa iwo osamvera inu tikufunsaninso kuti mukhale Atate athu ngati tikonda ndi kumvera inu tikufunsani kuti mukhale oweruza ngati sitimvera inu tikudziwa kuti simufuna kubweletsa zoipa koma tidziwa kuti tiyenera kumva zowawa pokonzaso mizimu yathu tikupemphaninso kuti mukonze mitima youmitsa ngati tili nayo tikupemphaninso kuti mutikumbatire ndi kuthandiza kufowoka kwathu. Chonde chotsani kuukila kwathu ndipo mutithandize pa kufowoka kwathu . Tikukuitanani tambasulani nkono wanu kuti muchite zonse munjira ya Umulungu. Tidziwa kuti inu mulipo wamoyo ndi waulemelero. Awa simasewera chabe sikuti tikungokusankhani inu kukhala Mulungu wathu.
INU NDINU MULUNGU, Ndipo tiyenera kugwadira inu. Ndife opusa ndi ofowoka nthawi zonse, koma tikuitanani kuti tikhale abambo ndi amayi a Mulungu, onongani kuwukira kwathu. Tipeleka ullemero kwainu Oyamba ndi Mlengi okonda miyoyo yathu ndi mmisiri wa mpingo wanu,lilemekezeke dzina lanu AMEN