Kufunduka Kwa Gulugufe

4/8/2003

October 1999, Africa.

Funso: Pamene tikugawana ndi anthu choonadi cha Yesu ndipo anthu akufuna kulapa ndi kufuna kutuluka mu zipembedzo zawo, Tingawauze chiani?

Ngakhale kuti anthu akufuna kuchoka muzipembedzo, ndizabwino kusakana ngati kungatheke chifukwa chache ndi ichi; ngati atadziwa, kapena apeza choonadi chi cha Mulungu monga kulapa machimo kwa wina ndimn’zake, kutengelana zo thobwetsa, kuchengetana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku, ndi kuchotsa chotupitsa pakati pa abale. (Choonadi ichi chakhala chili mu Baibulo kwa nthawi zonse, koma chaiwalidwa kapena kuiwalidwa kapenanso kutchutsidwa) ndiye ayenera kugawa zinthu izi kwaanzawo apafupi. Tiyenera kukankha anthu kuti atenge choonadi ichi chimene aona kuchokera kwa Mulungu ndi kugawiranso kwa anthu ena amuchipembedzo.

Ali ndi abwenzi ndi apabanja amene ali m’bali ya chipembedzo. baibulo limati amene wapatsidwa kukhulupilidwa ayenera kusonyeza kukhulupirlika pa chinthucho. Ngati munthu amene takumana nayeyo ali ndi mphatso yochokera kwa Mulungu kudzera mu mau a Mulungu, atenera kukhala okhulupilika ndi omvera ndi mgwilizano umene ulipo kale pamene anthu ali omvera ndi okhulupirika ndi mgwirizano umene ulipo, ndiye kuti zinthu chimodzai kapena ziwiri zidzachitika. Miyoyo ya ambiri kapena monga Yeremiay, munthu amene akuyesa mukukhala mu choonadi cha Mulungu adzachotsedwanso nawo pamodzi, ndi kuthamangitsidwa kuchokera mu chipembedzo.

Koma amene walapa potulukira kunja kwa chisteko sakukhala okhulupirika ndi choonadi chimene Mulungu wapatsa iwo. Ngati muli mu Hotela ndikuthawa fugo la usti ndikuona kuti muli moto ngati mungothawira kutulukira kumbuyo kwa chitseko mudzakhala ndi dzanja pa anthu amene afawo. Ngati wina wadziwa kuti chipembedzo chili kupsya usangowasiya kuti atulukire ku mbuyo ya chitseko. Timawaphunzitsa anthu kufuura pamwamba pa nyumba, “Dziwani njira za Mulungu! mvelani Mulungu! Ndili ndi uthenga wabwino—zilipo zambiri zimene angakhale tsopano sitinadziwe pa choonadichi! Tingamasulidwe kuchoka kudziwe pa choonadichi! Tingamasulidwe kuchoka kuchimo! Tingakhale anthu amodzi m’malo mwake kapena otayanatayana aliyense! Tingakhale mpingo woona umene makomo andende akufa sangathe kupambana. Choncho timawapempha anthu kuti akhalebe mu chipembedzo ndi kukhala okhulupirika ndi mabanja awo ndi abwenzi awo ndiye mirakulu idzaoneka kapena adzathamangitsidwa koma sitimalora kutuluka ku mbuyo kwa chitseko pamene fungo la moto lawoneka.

Ngati aliyense ndi omvera munjira imeneyi ndi kuitana wina ali yense kukhala okhulupirika mu njirayi, ndiye kuti siife amene akumanga mpingo wake. Sitikupeza anthu anthu amene amaganiza monga ife timaganizira. Tikufuna kuti wina ali yense amvere njira ya Mulungu. Kuti konse kumene ali ndipo pamene Yesu agwedeza mtengo zipatso zabwino zimagwa. Akhonza kukhala anthu khumi abwino mu chipembedzocho. Angakhalanse anthu zana limodzi mu chipembedzocho. Koma ngati wina athawira kukhomo la kunja ndi kusiya chipembedzo kachete chete, ndiye kuti pali anthu khumi kapena zana amene anakatha kusinthika miyoyo yawo ndipo sadzadziwa.

Ngati muli ndi khungwa lagulugube ndipo mutenga reza ndikutsegula mkati mwa Gulugufe, sadzauluka. Ndi ndondomeko yomenyera Gulugufe imene Gulugufe amakhala ndi mphamvu wowulukira!

Afunseni anthu amene ayamba kale kuwoona choonadi ichi cha Mulungu kukhala ndi kukhulupirika ndi anansi awo ndi mabanja awo asanyengelere ayi komanso kukhotera mu kusamvera. Afunseni kuti aime ndi kulimbika muchoonadi chimene apeza kuchokera kwa Mulungu. Ngati adzakhala okhulupirika, omvera, olimbika, ndi kulola kupeleka dipo posawelengera kukanidwa, ndipo adzakhala monga MBOZI imene ikusandulika Gulugufe ndi kuchoka mu chikhombe chake.

Anthu ambiri adzaphunzira njira ya Mulungu pakukanidwa kumene kwachitidwa ndi moyo wawo. Ndiye sitiba kukula kuchokera mudula poyera chikhungwa ndi kutenga Gulugufeyo. Timayetsetsa kuti njira yotulukira ipezeke—choncho kuti AKHONZA KUWULUKA.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon