Zochitika Mu Dziko La Chipembedzo

2003

October 2, 1999, Salima, Malawi, Africa

Ndifuna kulankhula nanu kwa kanthawi yochepayi za anthu a Mulungu amene anakhala zaka zikwi zitatu zapitazo. Amenewa anali Aisrael, adali ndi kachisi ku Yerusalem pa phiri lotchedwa Wazion. Linali nyumba yomangidwa. Idali yokutidwa ndi Golidi ndi kukutidwa ndi matabwa okongola. Nthawi zambiri pa chaka anthu amabwera kunyumbayi. Anali ndi masiku opatulika. Anali ndi nthawi yopuma imene ali kukumanako. Anali kupeleka nsembe kwa Mulungu. Anali kufuna kubwera pafupi ndi Mulungu. Ansembe anali kuthandiza anthu ku Kachisi. Ansembe anali kuthandiza anthu kufika pafupi ndi Mulungu, Ansembe amapeleka nsembe za nyama. Ansembe anali kupha nyama ndi kuwaza mwazi pa guwa kuti machimo a anthu akhululukidwe ndi kufika kwa Mulungu pafupi.

Izi inali zaka zikwi zitatu zapitazo, tiyeni tilankhule za anthu alero. TIlankhure za Israel woona. Abale ndi alongo ngati munapereka moyo wanu kwa Yesu ndinu Israel woona wa Mulungu, Amen ngati munapeleka moyo wanu kwa Yesu. Ali mfumu yanu ndinu Israel wa Mulungu.

Ndinali kukhala pano ndipo ndinaona munthu alimkututsa, pamene ali kudutsa panali chithunzi kumbuyo kwake. Pamene munthuyo amayenda, chithizichonso chimayenda pamene anakweza dzanja lake. Chithunzichoso chimakwezanso dzanja, chithunzicho chinali ndi miendo. Chithunzicho chinali ndi mutu. Kodi chithunzicho chinali munthu? Ai, chithunzicho sichinali cichinali cheni-cheni. Chimaoneka ngati munthu. Chimayenda monga munthu koma mafanizidwe a munthu. Abale ndi alongo ana a Mulungu mu zaka zikwi zapitazo anali mthunzi wa ana a Mulungu. Lero tilankhule za chithunzi chimenechi.

Kale, kunali kasichi, lero tilibe kachisi omangidwa ndi manda. Lero inu ndinu kachisi wa Mulungu. Mulungu sakhalanso mu nyumba zomangidwa ndi manja. Lero, inu ndinu Kachisis wa Mulungu. Mulungu sakhala munyumba. Yesu amakhala mu mitima ya amene anamusankha iye monga Mfumu. Simufunikanso kupita ku malo opatulika. Ngati muli woyera ndiye kuti ano ndi malo wopatulika. Simufunikanso kupita kwina kuti mupeze pafupi Mulungu mungadziwe MUlungu mu mtima yanu. Ndinu Kachisi.

Abale ndi Alongo simufunikanso masiku apadera dera. Lero ndi tsiku la chipulumutso, LInena, “Lero musaumitse mitima yanu. Samalanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku. Sitidikira tsiku la Mulungu, sitidikira nthawi yolambira. Masiku asanu pasabata ndi maora makumi awiri ndi anai pa tsiku tingakhale pafupi ndi Mulungu ndiye sitifunikanso kukhala ndi malo apadera kapena nthawi yapadera.

Nanga za ansembe? Ntchito yawo inali yoyandikitsa anthu kwa Mulungu. Tsopano tilibe chithunzi, tili ndi choonadi. Lero ansembe a Mulungu ndi INU. Ntchito yanu ndi kuziyandikitsa nokha kwa Mulungu mu mitima yanu ndi anthu ena pafupi ndi Mulungu. Potero simufunikanso munthu kubvala zobvala zapadera kapena kuzitcha ndi maina ena chifukwa mutha kukhala wansembe wa Mulungu.

Lero Ufumu wa Mulungu suli mu malo. Suli mu nthawi, suli mu nyimbo zapadera. Uli mwa anthu amene akhala mwa iye. Anthu amene angatumukire Yesu kasanu ndi kawiri pa Sabata, makumi awiri ndi anai pa tsiku. Anthu amene amakonda iye ndi mtima wawo wonse. Maganizo, umunthu ndi mphamvu zonse pamene Yesu anali kuyenda pa dziko lapansi pano, adalankhula ndi mzimayi. Adamfunsa funso; Tingalambire kuti Mulungu? Kodi ndi mphiri ili? Kapena linali? Yesu anayankha, “Osati malo ano” Ufumu wa Mulungu suli pano kapena uko “Ufumu wa Mulungu uli mwa inu.”

Opembedza otere amene Atate afuna kuti ampembedze iye mu mzimu ndi mchoonadi. Amen Anthu a Mulungu ndi amene amapembedza Mulungu kasanu ndi kawiri pa Sabata. Makumi awiri ndi anai patsiku pakukonda ndi miyoyo yawo palinso zambiri za kachisi. Munthu m’modzi sangakhale kachisi, Inde, Mulungu angakhale mu mtima wa munthu m’modzi. Koma ali yense ndi mwala omangidwa pamodzi ndi miyala ina kukhala kachisi. Tiyenera kufunana wina ndi mnzake. Ndingapembedza Mulungu motani tsiku lili lonse? Kolingana ndi mau a Mulungu pokhapo nditalimbikitsidwa kuchokera kwa abale ndi alongo tsiku ndi tsiku. Mtima wanga udzauma kwa Mulungu moyo wanga udzadzaza ndi chimo. Ndidzaumilitsidwa ndi chimo. Ndiyenera kupeza abale ndi alongo kundilimbikitsa ndi kutonthoza ine, ziyenera kuchitika tsiku ndi tsiku. Mnjira imeneyi tidzakhala kachisi wa Mulungu munjira imeneyi opembedza oona a Mulungu adzapelekedwa mu mitima yathu.

Tilankhure za kulambira mwa kamphindi chabe, lero sitifunanso kukhala ndi nsembe yanyama. Kodi ndi nsembe yotani yopelekedwa kwa Mulungu? Monga mwa baibulo, nsembe yopelekedwa ndi mtima yathu. Ife sindife nsembe ya kufa ndi nsembe ya mvyo. Maganizo athu sali ngati maganizo adziko lapansi, tiyenera kuganiza ndi maganizo a Kristu. Tiyenera kudzipereka tokha kwa Mulungu. Tidzakhala nsembe za moyo. Kumeneko ndiye kupembedza Mulungu, ngakhale sitikuimba kapena kupemphera. Tingapembedze Mulungu pamene tili kugwira ncthito. Tingapembedze Mulungu pamene tikuphika kapena kuchapa zobvala kapena kukhala pansi ndi anzathu.

Ngati tili ndi maganizo amene amalamulidwa ndi Yesu ndipo tizipeleka tokha monga nsembe tikupembedza Mulungu. Abale ndi alongo amenewa ndiye Ufumu wa Mulunguosati malo, osati nthawi, koma anthu. Anthu amene ali monga ansembe a Mulungu nthawi zonse tsiku lonse kulimbikitsana ndi kuthandizana wina ndi mnzake kuti akonde Mulungu ndi mtima wawo wonse maganizo, umunthu ndi mphamvu, choncho kuti apeleke miyoyo kwa Iye tsiku lili lonse. Ichi ndi cholowa chathu monga anthu ake. Tingakhale munjira imeneyi sitifunikanso kukhala monga chithunzi chija. Tingakhale munthu weni weni. Izi ndi zinthu zimene Mulungu afuna kwa ife lero. ndizimene mufunanso? Chabwino, tiyeni tiphunzire kukhala monga choncho pamodzi.

Kumanga Molingana Ndi Makonzedwe

Ndikudziwa kuti zambiri zimene mwamva lero, zingakhale pang’ono zobvuta. Koma taona dziko lonse lapansi kuti ndi uthenga wabwino. Tabwera Unifu kwa tili osangalala kukuuzani njira imene Mulungu akhala akufuna kumanga nyumba yake. Takumana ndi anthu ambiri amene ali abwino. Ena ndi Achi pentekosti, ena ndi bapatisti, ndi ena ndi azipembedzo zina. Akhala akusiyanasiyana miyoyo yawo yogawidwa kuchokera kwa wina. Akhala ndi miyoyo yawo yosweka ndi chimo. Choncho anthu ambiri ataya miyoyo yawo nd zokhumidwitsa ndi mgwirizano mu banja. Zokhumudwitsa zambiri zawoneka osati ngati Yesu. Ngakhalenso zokhumudwisa mwa ife tokha, zinthu zimene tikudziwa tiyenera kuchitira Yesu ngati sitichita. Chimo limene likufunika kuchotsa ndiye timapezeka tokha ofooka kuti lichoke.

Baibulo limati mu Yohane 3:8 kuti mwana wa munthu anabwera ku dziko kuononga chimo. Sanangobwera kudzakhululukira chimo lokha. Si choncho? Amen. Komanso akufuna tigonjetse chimo. Akufuna kutenga satana ndi kumugonjetsa pansi pa mapanzi ake. Ichi ndi cholowa cha ana a Mulungu, kuononga satana osati kungopulumuka, koma kuononga ntchito ya Mdyerekezi. Mwazina zimene sitinawone Mulungu akuonekera kuchilitsa mitima yosweka ndi kuwononga chimo, si chifukwa palibe anthu odabwitsa—alipo, sikuti palibe mphatso zabwino mu thupi la Khristo—zilipo mphatso zambiri. Zambiri zotere zachitika chifukwa zikhumbo za mitima zalephera kukondweretsa Mulungu chifukwa chosamanga mu njira ya Mulungu.

Chithunzi chimene takamba za nyumba za Mulungu. Kachisi ya Mulungu mu chipangano chakale chinayenera kumangidwa ndi maonekedwe. Mulungu anawauza m’mene angamangire kachisiyo, ndi kumanga munjira ya Mulungu imene adanena. Zinakhala zotani ngati anakatenga miyala yonse ndi Golide wa kachisi ndi kuchita m’mene amafunira? Mulungu sanakakondwa ndipo nyumba bwezni itagwa pansi.

Tikufuna kulankhula m’mene anthu angafikire kothekera kotere tsopano. Tingalore mphatso mu thupi la Kristo kumangidwa pamodzi kukhala mokhalirapo Mulungu, kudzazidwa ndi ulemerero wa Mulungu. Ilipo njira imene Mulungu akufuna kuti timange kuti mphamvu ya machimo siphwasulidwe mu moyo osati waukaporo ku zofooka zathu. Lingaliro la Mulungu ndi kumanga ife mu kulumikizana osati kukhala ndi mabvuto nthawi zonse. Mulungu ali ndi njira yodabwitsa pomanga nyumba yake ndi anthu ake odabwitsa chipembedzo mu dziko, mphaka tsopano, zakhala zomangidwa mu zolakwika, ndi anthu ena monga mabwana ndi anthu woyera ndi kuchita misonkhano ndi kumasulira kwawo kuti “Mpingo”.

Mu dziko lowonekali, taphunzira kwa zaka ndithu m’mene tingamangire ndi zolimba. pali muyezo wa mchenga ndi kupita mu (Konterete) ndi madzinso pang’ono. Ngati mukathira simenti kapena mchenga wambiri koncrete silimba. taphunzira kuzungulira dziko lapansi kuti tipange koncrete wamphamvu muyenera kuika zitsulo zolimba mu izo kuti pasakhale ming’alu pamene pakhala kutentha ndi kuzizira. Tikudziwa kuti ngati tipanga njerwa kapena zidina, pali njira zina zimene timamangira nyumba ndi m’mene tingaikire njerwa mu ng’anjo. Pali zinthu zambiri taphunzira pazomanga mu dziko lino. Sitinadziwe m’mene tingamangire koma tsopano tiyenera kudziwa kumanga. Mulungu anati tiyenera kusamala m’mene tikumangira

Choncho, mwachiyembekezo mu chisomo cha Mulungu tidzalankhula zambiri pa kanthawi inai. M’mene anzathu amisiri Engineers anaphunzilira m’mene angagwiritsire ntchito konkerete mmene angakhalire wabwino kuti akhale wa mphamvu, momwemonso anthu a Mulungu ayenera kudziwa m’mene kumanga kwabwino kuti ikhale yolimba. Anthu abwino wokhala ndi mphatso zabwino amamanga bwino amamanga nyumba yotamandika ndi zimene timafuna kulankhulapo. m’mene tingamangire nyumba ya Mulungu bwino ndi anthu abwino omwewo. sikuti tikunyoza zakale, sitikudanana ndi machitidwe akaleyo, ndi mtima odzichepetsa tikungofuna kunena ndi nthawi yoi tipirire mstogolo tsopano. kale ndi kale tiyeni tikule msinkhu tsopano mu chikondi ndi kudekha mtima ndi kukoma mtima. Tiyeni tiyende pastogolo tsopano taonong zaka zambiri kukhala ana a chaka chimodzi. Ndi nthawi yoti tiyende tsopano, ndi manja athu otseguka.

Mzimu woyera watipatsa ise zoti tiganize ndingofuna kuwonjezera ndi mau achilimbikitso kanthawi kena tinayimba ndi nyimbo zina zinali za muchingelezi ndipo ndimadziwa m’modzi mwa nyimboyi inali “Ambuye ndinu olemekezeka, ndikudziwa kuti ndinu olemekezeka” ndi nyimbo yoona. Yesu ndi olemekezeka. Ndikuganiza malembo mu 1 Petro 2:9 koma ndinu mbadwa zasankhidwa, Ansembe a chifumu, mtundu woyera, anthu mwini wake Mulungu kuti mukalalikire zolemekezedwa za iye amene akuitanani inu kuchoka mu mtima ndi kulowa mu kuwala kodabwitsa” Ambuye athu Yesu watiitana ife kuchokera mu mdima ndi kulowa mu kuwala, ndipo ndife othokoza. Muli othokoza inunso? Amen. Mukufuna kuti mulengeze kuti ali olemekezeka? Alipo anthu ambiri otizungulira amene akufuna kumva kuti Ambuye Yesu ndi olemekezedwa. M’mawa uno tinadutsana ndi achisilamu, kodi mukufuna kuti adziwe kuti Yesu ndi olemekezeka? Ndikufuna kuti adziwe zazimenezi.

Kuzungulira dziko lapansi pano tapeza anthu amene amapembedza anthu akufa kapena mafano ndi enanso amene sapembedza chili chonse. Akufunika kuti adziwe kuti Yesu ndi olemekezeka, ndi ntchito yathu kukawawonetsa. Koma nkhani iyi yoonetsa Yesu kuti ndi olemekezeka ndi zotengera m’mene ife tili osati kulankhula chabe, m’mene Peturo anati pano. Anati ife ndi “Ansembe a talankhula zimenezi kum’mawaku kuti sikuti pali wansembe m’modzi yekha koma ansembe ambiri ndi kunenanso kuti ndife mtundu wapadera, anthu ake a Mulungu. Kunenanso kuti pakati pa Akristo Ambuye Yesu ndi mfumu ndipo timamumvera iye mu iey tidzalengeza matamando.

Ine ndimakhala ku Amerika, pa ulendo wathu ndabweretsa chitupa cha Amerika. Koma sindine, mukuona kwenikweni ndine mbadwa ya America. Ine ndine mbadwa ya ufumu wa Mulungu. Inu ndinu mbadwa za Malawi, koma a ufumu wa Mulungu, mwa choncho mbwadwa za ufumu wa Mulungu ali mbadwa zabwino mu dziko lawo chifukwa amamvera malamulo osati kuchokera mu mantha koma kufuna kumvera basi. Koma ngati dziko lawo linena kuti asamvere Mulungu amati “Ai sitidza tidzamvera Mulungu osati munthu” Ndizimene zimathandauza kukhala mbadwa zosankhidwa. Munjira imeneyi sitidzalora chikhalidwe chathu kutiuza ife zochita. Tidzalora Mulungu kutiuza zochita. Ndikuchokera ku dziko lomwe chikhalidwe chake ndi cha uchimo chikhalidwe cha Amerika chaiwala kuchita manyazi ndi chimo. Sindidzamvera chikhalidwe changa. Ndidzamvera Mulungu Amen.

Ine sindidziwa chikhalidwe chachi Malawi komanso inunso muyenera Mulungu, osati chikhalidwe chanu. M’menemo ndiye mbali yokhala mu ufumu wa Mulungu. Chomwechonso ndi zoona ndi chipembedzo. Lero m’mawa tadutsa nyumba yolembedwa “Mpingo wa Nazarene” Ndikudutsanso malo ena otchedwa Luzarene” Tinadutsanso pena analemba “Mpingo wa Khristu” onsewa akukumana lero. Onsenso ali kustatira miyambo yawo. Mbali ina ya Ufumu wa Mulungu ndi kumvera Mulungu koposa miyambo chabe Amen? Miambo sali mfumu yathu, Yesu Khristu ndiye mfumu yathu. Tili mtundo wapaderadera, tidzaimba ndi kulengeza olemekezeka Yesu Kristo. Ndife mtundu woyera. Zolengeza zahu ndi zomverka bwino, sizosokoneza, ndipo amuna onse adzafunsidwa ngati adzapinde mabondo awo ndi kumvera iye. M’mawa uno sitinabweretse chipembedzo china chatsopano. Tabweretsa ufumu wa Mulungu, tiyeni tikhale munjira imeneyi tonse, AMEN.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon