Madziko Anayi A Choonadi

4/8/2003

Salima, Malawi, Africa, October 3, 1999

(Izi zidayankhulidwa ndi abale atatu pamene adayima pamudzi wina ku Malawi ku africa, pakuonetsera zokhudza mpingo ya chipentekositi. MUTSIKU LIMODZI “Mpingo” wonse udatembenukira kwa Yesu ndipo siwunayang’anepo m’mbuyo. Polipilira mtengo waukulu, munthu ali yense payekha, zosintha zambiri zidapangidwa kwamuyaya, kusintha anthu ambiri, ndikhalenso gawo lawo laza chuma m’mudzi wawo kumagulu ena achipembedzokuti china chake chodabwitsa chikuchitika pakati pawo. Ndikufunitsitsa kukadakhala kotheka tikadajambula zinthu zomwe zidanenedwa ndi abale ochokera m’mudzi umenewu ku Africa muolu lotsatira patatha nthawi imene maganizo awa adayikidwa ndi oyera mtima kumeneko. Ichi chidali ndipo ndichodabwitsa ndi …………, ndithudi, kuwona kulimbika mtima kwao ndi “changu chao pa nyumba ya Atate” zowonetseredwa ndi “chikondi cha choonadi” ndi machitachita munthawi kuchokera pa tsiku limenelo.)

Chuma chamtengo wapatali ndi kudzutsa ndi kuchangamutsa anthu a Mulungu padziko lapansi munthawi yino. Chilimo chilungamo chapadera chomwe chakhala chili m’Baibulo lanu nthawi yonseyi chimene chidzasintha moyo wanu ndikusinthanso njira imene mpingo umaonetseredwa, kuti koposaposa tikakweze Mfumu Yesu ndikuwona loto lake likukwaniritsidwa. Ndichiyembekezo chathu, mwa mzimu oyera, kuti maso athu onse akatseguke ndikuwona choonadi chokongola ichi. Mulungu akufuna kumanga nyumba yake kuti tonse tikhale amphamvu pamodzi. Iye akufuna kumanga nyumba yake kuti makomo a ndende asadzailakenso konse. Iye akufuna kumanga nyumba yake kuti ubale ukhonze kuchilitsidwa. Iy akufuna kumanga nyumba yake kuti iye akhale omasuka kuchiza matupi athu, malingaliro athu ndinso moyo yathu. Iye akufuna kumanga nyumba yake kuti ife tikhale amphamu ndi nzeru, ndi kuti uthenga wabwino wa Yesu upite patsogolo, mwamphamvu kuposa kale.

Kodi muli nako kulimbika mtima pakumva zinthu izi? Kodi mumvera mau a Mulungu pamene mukumva zinthu izi? Kodi mwasintha miyoyo yanu posawerengera mtengo wake? Ngati muli nako kulimbika mtima kuti mumvera ndi kudzipereka, ndiye chonde werenganibe.

Pali choonadi chinayi chimene ife tiyenera kumangapo. Popanda chimenechi, nyumba ya Mulungu sidzakhala yamphamvu, ndipo makomo a ndende adzapitiliza kudzetsa chisokonezo pa nyumbayi. Komabe, ngati ife timvetsetsa zinthu zinayi izi ndikuzimvera izo, ndipo ngati ife tifunitsitsa kudzipereka, ngakhale chowawa chidze, pa choonadi cha Mulungu chinayi chimenechi, kenako Mulungu adzalemekezedwa ichi ndipo iye adzatumidza mphamvu yake mumiyoyo yake. Osauka adzachita bwino ndipo ofooka adzapeza mphamvu. Uwu wakhala uli mtima wa Mulungu ndi cholinga chake. Komabe, chuma ichi chokhala chitabedwa kuchokera kwa ife kuchokera mzaka zoyamba mpaka tsono. Ife talandidwa ndi miyambo ya anthu yachabechabe.

Choonadi Choyamba: Kodi Mkhristu Ndi Ndani?

Choonadi chamadziko choyamba ndi kufotokoza moyenera chimene mkhristu ali. Ife takhala tili otayirira padziko lonse lapansi ndi mumiyambo yonse pazokhudza ichi. Chifukwa takhala osadziwa mwachindunji zokhudzana ndi chimene Mkhristu ali, tamanga kwambiri kwa nyumba ya Mulungu pa mchenga. Ifeyo tafotokozera ndi kutanthauzira zimene zimampangitsa munthu kukhala Mkhristu kudzera mu zinthu zomwe sizenizeni, kapena mamvedwe a matupi athu kapena mmene timalerera banja. tatanthauzira chimene Mkhristu kudzera mkati ngati wina amayimba bwino, kapena amakhala nawo m’misonkhano kwambiri, kapena amapereka chakhumi bwino. Umo sim’mene Yesu adatanthauzira Mkhristu.

Yesu adati, “Pokhapokha inu mutataya zonse, simungakhale ophunzira anga.” Yesu adati “pokhapokha inu mutasenza mtanda wanu tsiku ndi tsiku, simunganditsate ine.” Mubukhu la Machitidwe, Baibuo limati, “Ophunzira adatchedwa ‘akhristu’ koyamba ku Antiyokea. Tsono pamene muona liu loti ‘ophunzira’ muziphunzitso za Yesu, ganizirani mumalingaliro anu zaliu loti, “Mkhristu” pamene Yesu ananena kuti, “pokhapokha mutataya zonse, simungakhale ophunzira anga” Iye amatanthauza kuti simungakhale a Khristu ngati inu simutaya kapena kupereka moyo wau. Iye sadanene kuti, “pokhapokha mutakhala nawo mumisonkhano, simungakhale a Khristu” Iye adanena kuti , “pokhapokha mutafa kwa inu nokha, simungakhale a Khristu.

Yesu akuyitana kwa anthu amene adafa kwa iwo okha. Iwo adzataya chili chonse nkumutsatira iye. Iwo adzataya kunyada kwawo ndi chuma chawo kuti amutsatire iye. Iwo adzatembenuka kumachimo awo ndi kudzikonda. Iwe adzakonda ena koposa m’mene amadzikondera eni. Ubale umenewu wapakati pa iwo ndi Yesu udzasintha m’mene amachitira zinthu zawo tsiku liri lonse.

Pokhapokha ife titanthauzira liu loti “Mkhristu” munjira yomwe Yesu atanthauzira, nyumbayi idzatitimira mumchenga ndikukokoledwa. Leli ndi chimene Yesu Mfumu adalonjedza kuti chidzachitika tikamanga pa mchenga wa kumva, kuyimba ndi kuyankhula, koma osamvera. Nyumba imene timanga idzakhala, mwina chinthu chimene chili chongosangalatsa ife,koma sochidzatanthauza kanthu kwa Yesu. Nyumba imene timanga ikonza kutisangalatsa ife chifukwa tikuyimba ndi kukhala pamodzi, koma siyitanthauza kali konse ngati Mulungu siali okondwa nayo. Sichitanthauza kali konse ngati satana akadagonjetsabe pa nkhondoyi m’miyoyo yathu. Ngati ife sitimanga moyo ndi Mpingo zomwe zibweretsa kusangalala kwa Yesu, ndiye kuti ife tikungotaya nthawi yathu ndi nthawi ya Mulungu.

Mkwingwirima yake

Mwala wa madziko oyamba pakumanga nyumba ya Mulungu ndi kufotokoza chimene Mkhristu ali munjira yomwe Baibulo limafotokozera chimene Mkhristu ali. Ife tiyenera kupanga chisankho mwakulingana ndi amene Mulungu amamutcha Khristu. Kodi munthu nkutheka kukhala membala wa Mpingo wa Mulungu koma osakhala Mkhristu? Nzosatheka! Koma pa dziko lapansi anthu akuphunzitsidwa kuti ndi zabwino bwino kuti Mkhristu ndi amene siali Mkhristu kukhala gawo la Mpingo. Baibulo limati ichi sichoona! Mu Akorinto oyamba 5, Baibulo limati “chotsani dzotupitsa mumkate” chotsani tchimo mu Mpingo. Ichi ndi chofunikira kumvetsetsa, chifukwa Mulungu adati, “chotupitsa pang’ono chimatupitsa mkate onse”

Kodi inu mukukumbuka pamene malinga a Yeriko anagwa pansi? Anthu a Mulungu adali a mphamvu munjira yodabwitsa. Komabe, patangotha kugwa kwa malinga a Yeriko, Israel idagonjetsedwa pankhondo. Iwo adamenyedwa! Nchifukwa chiyani, Israel idagonjetsedwa pa nkhondoyo? Chifukwa choti munthu mwa Israel adachimwa mu hema yake. Mulungu adakwiya chifukwamunthu m’modzi mu Mpingo wonse adachimwa mumoyo wake umene udabisika. Munthu ameneyu, Akani, adali ndi fanizo (mulungu osema) litakwiliridwa pansi pa hema yake. Mulungu adapangitsa a Israel onse kuvutika ndi chigonjetsocho chifukwa cha tchimolo. Mulungu ali yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse. Sichoncho? Mulungu akadali osakondwa pamene anthu mu Mpingo wake abisa tchimo miyoyo yawo. Ichi chimaswa mtima wake. Baibulo linena kuti Mulungu amabweretsa chiweruzo pa ichi.

Kodi ndi chabwinobwino kwaife kunena kuti wina wake amene sadapereke moyo wake kwatunthu kwenikweni kwa Yesu akhonza kubwera ndikukhala mbali ya Mpingo? Ayi! Ichi ndi chibwana kwambiri. Mulungu amabweretsa chiweruzo pa nyumba yonse chifukwa cha munthu m’modzi amene akunamizira kukhala Mkhristu, koma sanapereke moyo kwatunthu kwenikweni kwa Yesu. Tsono, ngati ife tikufuna kuona Nyumba ya Ulemerero imene imagwira ntchito ya Mulungu, chinthu choyamba chimene tingachite ndikutanthauzira liu loti “Mkhristu” munjira yomweyo yomwe Yesu anenera. malemba anena “pokhapokha mutataya zonse, simungakhale ophunzira anga” “Ngati mukonda abambo, amai ndi ana anu koposa ine, simungakhale ophunzira anga, ngati mukonda dziko lapansi ndi zinthu zamdzikoli, mwasanduka mdani wanga, Mulungu amadana ndi odzitamandira ndipo amapereka chisomo kwa odzichepetsa”.

Ife tiyenera molondola, kutanthauzira chimene Mkhristu membala wa Mpingo—ali chenicheni! Inuyo simunganamizire kusambitsidwa mu mwazi wa Yesu, ndi kukhala chiwalo cha thupi la Yesu ndi kuyesedzera kuti Mkhristu ngati mtima wanu siuli kwa Yesu pamene muli kunyumba, kapena kuntchito, kapena m’minda. Ngati ubale wanu siuli ubale oyera, muyenera kulapa ndi kupereka moyo wanu kwa Yesu.

Choonadi Chachiwiri: Kodi Utsogoleri Nchiyani?

Chinthu chachiwiri chimene tiyenera kutanthauzira, mwala wachiwiri wa madziko pakumanga Nyumba ya Mulungu, zikhudzana ndi chimene utsogoleri mu Nyumba ya Mulungu. Ichi ndicho choonadi chodabwitsa kwambiri! ichi chidzabweretsa chimwemwe pa inu ndi kusintha moyo wanu. Mu maiko padziko lonse lapansi, tapanga chibwana chachikulu kwambiri pankhani yokhudza utsogoleri mu Mpingo. Mumalo ambiri munthu amene adaphunzira Baibulo ku seminale kapena kusukulu ya Baibulo, kapena odziwa zamalonda kapena odziwa kuyankhula amapatsidwa “ubusa”. Ife taona ku India ndi maiko ena kuti nthawi zambiri, munthu amene ndi njinga amenenso angathe kuwerenga amasankhidwa kukhala mtsogoleri. Ichi sinjira ya Mulungu! utsogoleri wa Mulungu siugona pa iwo amene angathe kuyankhula bwino, kapena amene ali ndi luso pa malonda, kapena amene ali ndi chuma kapena maphunziro kapena mankhwala kapena maonekedwe abwino kapena njinga.

Kukhala monga Yesu

Ine ndikupatsani chitsanzo kuchokera mumalemba. Machitidwe 6, padali azimayi amasiye achi Greek amene amakhala anjala kwambiri kwa nthawi zambiri chifukwa choti amayiwalidwa. Pamene chakudya chimagawidwa iwo amasiyidwa ndi kusasalidwa bwino. Mpingo mu Yerusalemu adayenera kupanga ganizo la m’mene akadathetsera vuto ili. iwo adaganiza kuti asankhe anthu ena kuti athetse vutoli. Ngati mungawerenge Baibulo lanu, mupeza kuti padali njira ina yosankhila anthu amenewo. Kodi Baibulo likunena kuti, “sankhani kuchokera pakati pa anthu asanu ndi awiriwa amene amadziwa ma Baibulo awo? Ayi. “Sankhani kuchokera pakati pa anthu asanu ndi awiri amene angayimbe bwino?” Ayi, sankhani kuchokera pakati pa anthuwa amene ali ndi luso pa malonda, kapena pa malonda a zakudya? Ayi, “Sankhani kuchokera pakati pa anthuwa amene akhonza kuyankhula bwino?” Ayi. Njira yothetsera vutoli idali, “zisakhalire kuchokera pakati panu anthu asanu ndi awiri amene ali ozadzidwa ndi Mzimu oyera ndi ozadzidwa ndi nzeru.

Awa adali anthu amene amayesedwa tsiku liri lonse. Awa sadali anthu amene adapita kusukulu kuti akhale auzimu, kapena amene amangoyankhula bwino chabe. Awa adali anthu amene adali abwenzi a Mulungu ndiposno abwenzi akuya abale ndi alongo apakti pawo tsiku liri lonse. Stefano ndi Filipi ndi anthu asanu ndi awiri awa amapezeka mnyumba za anthu tsiku liri lonse, kuyetsetsa kuthandiza anthuwo. iwo amakhonza kugwira manja a ana a anzawo ndikuyankhula nawo ndi kuwaphunzitsa. iwo amakhonza kutungira madzi okhulupirira ena ndi kuwathandiza iwo. Iwo amakhonza kupita kunyumba za anthu pamene iwo akutaya mtima. Iwo amakhonza kupita m’malo ogwira ntchito a anthu mkati mwa tsiku ndikukawalimbikitsa iwo. Ndi iwo sadali ngakhale kutchedwa atsogoleri! iwo adali abale chabe amene amakhala umoyo wa Yesu tsiku liri lonse. “Zisankhileni nokha kuchokera pakati panu anthu asanu ndi awiri amene awoneka ngati Yesu, asanu ndi awiri amene angathe kuona Mulungu ndi kumva Mulungu.” Sankhani anthu asanu ndi awiri amene akutsuka mapazi a oyera mtima tsiku liri lonse”. “Abale asanu ndi awiri amene ali abale chabe tsiku lirilons amene amakodna Mulungu mozama kuchokera pansi pa mtima ndi kuonetsera kulumikizika kodabwitsa kwa Messiah.”

Chifukwa anthu amenewa awoneka ngati Yesu, tsiku liri lonse munyumba za anthu, ndiye kuti ife timadziwa kuti iwo ali odzadzidwa ndi mzimu oyera. Iwo siali odzadzidwa ndi mzimu oyera chifukwa choti iwo amayankhula mokweza kapena kuyimba bwino kapena amayankhula zinthu zambiri. Iwo ali ozdadzidwa ndi mzimu oyera chifukwa choti iwo amayankhula mokweza kapena kuyimba bwino kapena amayankhula zinthu zambiri. Iwo ali ozadzidwa ndi mzimu oyera wa Yesu chifukwa choti iwo amaoneka ngati Yesu ndi moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Uwu ndi mtundu okhawo wa utsogoleri m’Baibulo. Mu chipangano cha tsopano, Yesu adauza atumwi khumi ndi awiri aja kuti asatchule munthu kuti mphunzitsi, tate, mtsogoleri, mbuye, rabbi, m’busa, pakuti onse ndi abale! Tsopano ife tili ndi maganizo odabwitsa, osiyana a utsogoleri.

Zosiyana ndi zadziko lapansi

Kuphunzira ichi chidali chovuta kwambiri kwa ine pandekha. Muzaka zambiri zapitazo ndidali “m’busa” kufikira nditazindikira zimene Baibulo lidanena, zoti ndimayenera kungokhala m’bale pakati pa abale. Ndimayenera kugwiritsa ntchito mphatso ili yonse ndingakhale nayo “pakati pa abale, monga m’modzi amene atumikira”—osati monga bwana kapena wina wake oti adzionereredwa panthawi zonse. Ngati chimenechi chidali choona kwa Petro, Yohane, Yakobo ndi atumwi ena, chiyenera kukhalanso choona kwa wina ali yense wa ife, opanda kuchotserapo! “Muli nonse abale chabe.”

Ndidatuluka kuchokera ku ndalama zambiri zomwe ndimapanga mudziko lamalonda pakukhala “m’busa”. Ndipo tsopano ndidayenera kusiyana nazo ndalama ndi mipando yakukhala osati monga mwa Baibulo imene anthu amaitcha “M’busa” wa mpingo. Ndidayenera kupanga chisankho kuti ndiyenera kukhala m’bale pakati pa abale. Chili chonse chimene Yesu wapanga m’moyo wanga chikaonekera munyumba ndi m’miyoyo ina pamene ndigwirana manja ndi ana. Ine sindimayeneranso kukhala chipolopolo chachikulu ayi. Sindimayenerera kukhala munthu wamkulu ayi. Ndikadangopanga zimene Paulo adanena kuti adapanga ndi Atesalonika, ndi Afilipi, ndi okhulupirira mu mzinda wa Korinto ndipo chimenechi ndiko kukonda anthu monga tate ndi m’bwenzi, ndiponso monga m’bale kuchokera nyumba ina kufikira nyumba ina.

Paulo adati, “Ndidapita kuchokera nyumba kufikira ina ndi misonzi” Iye adakonda anthu monga tate, kapena monga m’bale. Iye analera m’moyo yawo monga mai angalerere mwana okhulupirira ena adamichitiranso iye chimodzimodzi, uwi ndiye utsogoleri woona mu Mpingo Owona wa Chipangano Chatsopano.

Yesu adati kwa atumwi, “Amitundu ali ndi njira ina yokhalira ndi utsogoleri, koma izi siziri choncho ndi inu.” Mu mpingo woonadi, Mpingo umene makomo a ndende sangaulake, utsogoleri wake ndi wosiyana kwambiri ndi njira ya dziko lapansi. Utsogoleri umabwera kuchokera mkati kati, osati “kuwupatsa mphamvu” kuchokera pamwamba.

Mphatso ndi ulamuliro wa Yesu

Ndiloleni ndikupangireni chithunzi inu. Baibulo limanena ku Aefeso 4 kuti pamene Yesu adakwera kumwamba, iye adapereka mphatso kwa anthu. Yesu adatenga mphatso zonse zimene anali nazo (ndipo Yesu anali ndi mphatso zauzimu zambiri, sochoncho kodi?) ndipo iye adapereka mphatsozi kwa anthu ake onse. Iye sadatenga mphatso zonse zimene adali nazo ndikuziyika pa “m’busa” kapena pa “munthu m’modzi wa Mulungu” Malembo akunena kuti iye adatenga zonse mwa mphatso zake ndipo adazipereka izo kwa thupi lake lonse. Baibulo linena kuti mzimu uyikidwa ndi kuperekedwa ngati mphatso, monga mwa amene Mzimu ufunira, pa Mpingo wake onse. Ngati inu muli Mkhristu oona, ngati mwatayadi moyo wanu chifukwa cha Yesu, ndiye kuti Mzimu oyera ukupatsani inu mphatso yapadera uoposa. Mphatso yanu ndi gawo kapena kuti chiwalo cha Yesu.

Yesu asadapite kubwerera kumwamba, adati, “ulamuliro onse ku Mwamba ndi padziko zapatsidwa kwa ine” Kodi mukukumbuka kuti Yesu adanena zimenezi? Ulamuliro onse uli kwa Yesu ndipo osati wina ali yense! Tsono ngati Yesu anapereka gawo la iye yekha kwa inu, gawo lina kwa munthu uyu ndi gawo lina kwa munthu uyo, ndiye kuti mphatso yauzimu ina ili yonse adapereka kwa wina ali yense wa inu, pali ulamuliro mu mphatso imeneyo. Yesu adapereka mphatso ndipo iye ali ndi ulamuliro onse.

Pali mphatso zamitundu yambiri zomwe zidalembedwa m’Baibulo. Mzimu Oyera, mwachitsanzo, umapereka chifundo ngati mphatso. Mphatso ya chifundo ndi gawo la Yesu limene iye adapereka kwa anthu ena. Ndi mphatso yodabwitsa. Tonse a ife tiyenera kukhala ndi chifundo, sichoncho? Koma pali chifundo chodabwitsa chimene chili mphatso ya Mzimu Oyera. Tsono, ngati iye adapereka kwa inu mphatso yapadera ya chifundoyi, inu mwapatsidwa ulamuliro kumbali ya chifundo. Ngati inu muli ndi mphatso yodabwitsa ya chifundoyi ndipo ine ndilibe, ndipo ngati ulamuliro onse uli kwa Yesu ndi inu muli ndi mbali ya Yesu, ndiye kuti ine ndilemekeze mphatso imeneyi mwa inu. Muli ndi ulamuliro kumbali imeneyo. Kodi mukumvetsetsa? Ichi ndi chimene utsogoleri uli!

Ulamuliro onse uli kwa Yesu ndipo ife tonse tili nayo mphatso zathu zapadera. Mwachitsanzo, pali mphatso ya uphunzitsi. Ahebri 5 imati, “tonse tayenera kukhala aphunzitsi tsopano” Komanso ku Aefeso 4 ndi Aroma 12 limati pali mphatso zauzimu za uphunzitsi zimene Yesu amapereka. Ichi chitanthauza kuti pali ulamuliro mu mphatso imeneyi chifukwa Yesu amapereka mphatsoyi ndipo Iye ali ndi ulamuliro onse. Ife tidzipereke kwa wina ndi mnzake mu ichi. Koma kuphunzitsa ndi gawo limodzi lokha ndi mphatso imodzi yokha ya Yesu. Palinso mphatso zina zambiri. Pakuti ulamuliro onse uli kwa ali yense wa ife ndi gawo la Yesu, ndiye tikuyenera kudzipereka ku mphatso zomwe zili mwa wina ali yense wa ife chifukwa Yesu ndi amene waikamo mwa ife mphatsozi.

Palibe ulamuliro wina wake umene uli mwa “munthu wa Mulungu” m’modzi ndipo wina ali yense angokhala chabe ndikuonerera. Chifukwa chanjira zimene anthu amangira Mpingo zaka zodutsa 1800 zapitazo, ife takhala ndi machitidwe onga ngati pali mphatso imodzi yokha basi—mphatso ya “ubusa”. (Kapena mwina wina ali yense ali ololedwa kukhala ndi mphatso yopereka ndalama yokha!”) Koma m’busa / ubusa ndiye mphatso yokha basi! Ngati ife timanga molakwika, tonse tiluza. Ngati, munthu m’modzi akankhilidwa kutsogolo kukhala “m’busa” ndipo wina ali yense kungokhala pansi ndi kumvetsera nthawi zonse, ndiye kuti wina ali yense sakugawana nawo mphatso yanuyo. Iwo amangotenga mphatso “ya ubusayo”. Ichi ndi chochepa kwambiri ndi chachinyengo! Ngati tikufuna kuti tione ukulu wa Mulungu, ndipo ngati tikufuna kuona miyoyo yathu yonse ikusintha ndipo miyoyo ya ana athu ikusintha, apa ife pafunika zigawo za Yesu, Amen? Ife sitiyenera kukhazikika pa gawo chabe la Yesu. Amen?

Kulimbika mtima kukusintha ndi kulimbika mtima kukuthamanga

Kodi mukuona chifukwa chimene tikunenera kuti tiyenera kulimbikira mtima? Zinthu ziyenera kusintha! Simungapitirire kuchita zomwe mwakhala mukuchita. Mupanga chisankho kugwiritsa ntchito mphatso yanu kwambiri ndiponso kulandira enanso kuti nawonso atero. Mupanga chisankho kukhala omvera ndipo kukhala ndi kulimbika mtima. Ngati mupitirira kukhala pa mpando wanu kapena pansi nthawi zonse ndiponso osagwiritsa ntchito yanu kwambiri ngati mmene zimayenera kukhalira, mphatso yanu idzapitirira kulowa pansi. “Iye amene wapatsidwa mphatso akuyenera kuonetsa kukhulupirika.” Kodi mukukumbuka zimene zidachitika kwa munthu amene adakwirira talente yake? Yesu adati, “Iwe oipa, wantchito waulesi.” Icho ndi chimene Yesu amanena kwa ife pamene ife sitipanga zomwe tiyenera kuchita. Ngati ine sindigwiritsa ntchito mphatso yanga kapena inu kugwiritsa ntchito mphatso yanu, ife tili “oipa ndi aulesi”.

Kodi mukuona m’mene miyambo ya anthu ikubela ndi kulanda mau a Mulungu? Bwanji inu mutakhala othamanga wa Olympic mwagona pa bedi ndi wina wake watenga chingwe ndipo wamanga kuzungulira inu pamodzi ndi bedi? Ngakhale mutakhala opambana pamasewero olimbitsa thupi, ngati inu mwamangidwa pamenepo pamodzi ndi bedi minofu yanu ikulungala ndipo kenako inu mufa. Mphamvu ndi kuthekera kwanu konse kupita pachabe chifukwa mwamangidwa kubedi kwa miyezi kapena zaka. Kodi inu mukuona m’mene miyambo ya anthu imabela ndi kulanda Mau a Mulungu? Njira imene tamangira mzaka zoposa 1800 mu Nyumba ya Mulungu zamanga anthu a Mulungu ambiri kumodzi ndi bedi. Iwo akhala opanda kuthekera koima ndi kothamanga ndi kokwaniritsa masomphenya awo chifukwa anthu amanga molakwika, mosatsatira mau a Mulungu. Ngati ife tamanga kapena kukonza Mpingo munjira imene makweza munthu m’modzi kapena “waudindo” ndi kuzima mphatso zaena, ife tili zigawenga mu Bwalo la milandu la kumwamba chifukwa cha zowongeka ndi zowawa zimene ena awawidwa nazo chifukwa cha “chotupitsa mu mkate” ndiponso mphatso zosagwiritsidwa! Sikuti ndi chifukwa choti anthu ndi “oipa” chimene ife tamangira molakwika. Kwenikweni ndi chifukwa choti ife sitikudziwa kumanga Nyumba ya Mulungu ndi Mapangidwe ake.

Tsono kumbukirani kuti mwala omangira oyamba wa madziko oonadi ndi akuti okhawo ali Akhristu oonadi okhonza kuzitcha okha mamembala a Mpingo. Mwala wa madziko wachiwiri umene ungamange Nyumba ya Mulungu ndi kuti tiyenera kumvetsetsa utsogoleri bwinobwino. Ife tayika munthu m’modzi kukhala olamulira kwa zaka 1800. Ife tatenga mphatso imodzi, mphatso ya “mbusa” (kapena ubusa, kutanthauzira kwabwino) ndipo tayipanga kukhala mphatso yoyambirira. Ichi ndi kutali ndi choonadi mu Mpingo mu Baibulo!

Ndipo sichiyenera kukhala chilungamo ngakhale pano. Ichi chamangirira ambiri mwa anthu a Mulungu ku bedi kuti iwo asakhalenso m’mene Mulungu adawaitanira iwo kuti akhale. Utsogoleri uli mwa anthu onse a Mulungu. Baibulo limatcha ife Ufumu wa ansembe. Baibulo silinanene kuti Ufumu okhala ndi ansembe, koma Ufumu wa ansembe. Palibe gulu lapadera monga ngati ansembe achilevi aku Chipangano chakale. Muchipangano chatsopano onse a anthu a Mulungu ali oyenera kukhala ansembe jwawina ndi mnzake. MULUNGU adati, “pemene bvumbulutso lidza kwachiwiri, siyani oyambayo akhale pansi!!!!!!

Ngati inu muli odzadzidwa ndi mzimu oyera ndi odzadzidwa ndi nzeru, ndiye kuti ndinu mtsogoleri.

Sikuti ndingoti unapita kusukulu, kapena ngati umayankhula bwino. Sikuti ndingati uli wam’muna kapena wamkazi, kapena wamng’ono kapena wamkulu. Utsogoleri ndi munthu amene ali ndi mphatso ya Yesu ndi ubale ndi Yesu, adzadzidwa ndi Mzimu Oyera ndi nzeru. Utsogoleri ndi kugwirana manja ndi ana tsiku liri lonse. Utsogoleri ndi kuchiza mabala a anthu a Mulungu kuchokera nyumba ina kufukira nyumba ina tsiku liri losne. Utsogoleri ndi kuthandiza kuthetsa mavuto a tchimo mu miyoyo ya abale ndi kusambitsa mapazi awo tsiku liri lonse. Ichi ndi chimene utsogoleri uli ndipo ndi mtundu okha wa utsogoleri umene baibulo limankhula, kugwiritsa ntchito gawo la Yesu limene Mzimu Oyera udayikamo mwa wina ndi mnzake wa ife. Ichi ndi mbali ya utsogoleri ndi ulamuliro. Ichi chitanthauza kuti ife tiyenera kusintha m’mene timachitira tsopano. Ife tiyenera kusintha m’mene timaonera utsogoleri ndi m’mene ife timachitira pa ndondomeko ya utsogoleri.

Ichi ndi chosintha kwambiri. Ichi chisintha m’mene timachitira mu misonkhano yathu, m’mene ife timachitira mu moyo wathu wa tsiku liri lonse. pali mtengo omwe tiyenera kulipira pa ichi. Koma Mulungu amapereka mphoto kwa ife kokwana zana limodzi pa chili chonse timapereka, monga mwa lonjezano la Yesu.

Pamene ine ndidali “m’busa” ndidaganiza kuti ndikhale mosiyana ndi poyamba. Ine ndidaganiza kuti ndikhulupirire ndi kumvera malembo pazokhudza utsogoleri. Ndidasankha kukhala m’bale pakati pa abale koposa kukhala kutsogolo kwa abale. Kunena moona, ndidaopa. Ndidaopa za m’mene ndidzasamlira banja langa. Ndidaopanso kuti mwina ndidzataya ubale wanga ndi Mulungu mwinamwake ndi kuti anthu sadzandilemekeza inenso ayi. Ndidali ndi mantha pa zinthu zambiri. Koma ndidadziwa kuti Mulungu adanena mu Baibulo. Iye amafuna ine kuti ndikhale m’bale pakati pa abale. Mu moyo wanga wa tsiku ndi tsiku, sindidzakhalanso bwana ayi. Ndidzangokhala chabe m’modzi mwa abale, ndipo ndidzapitilira kugwiritsa ntchito mphatso yanga kuchokera kwa Yesu monga “m’bale pakati pa abale” amene mofanana agwiritsa ntchito mphatso zao. Izi zidasintha chili chonse pa ine, koma Mulungu adali okhulupirika kwambiri. Iye adalonjeza kuti palibe amene adasuya chili chonse amene adzalephera kulandira koposa zana limodzi kapena kuposa zomwe adataya. Mulungu amasunga lonjezano lake! Amen?

Kuchokera pa zintchito, ndikufuna ndiyikepo maganizo anga pa inu akuti ngati tifunitsadi kuti tilemekze mphatso zimene ziri mwa wina ali yense mwa ife, ndikutulutsa poyera mphatso zimene zili mwa anthu onse a Mulungu, ndiye tifunika kusintha zinthu zambiri. Monga mopusa m’mene chikumvekeramu, chimodzi mwa zinthu zimenezo chikhonza kukhala mmene timakhalira pamene tisonkhana pamodzi. Pamene Yesu anali pano, Iye adali ndi anthu omuzungulira Iye—awa ndiwo amayi anga, abale anga, ndi alongo anga” (Mariko 3) Kukhala mwabwalo omuzungulira Iye! Ichi sichinthu chachizolowezi kupanga, pamen ife tasonkha pamodzi kuti timumve IYE, ndipo osati munthu chabe wa mphatso zowerengeka. Ichi chikhonza kumveka ngati chopepuka kwambiri kwa inu, ndi chikhonza kusamveka ngati cha phindu ndi chofunikira, koma ndikufuna ndikutsimikizireni inu kuti ichi ndi chofunikira. Ndamva kuti mau ayimira “Gome” ndi “mnofu” amanenedwa munjira imodzimodzi. chi Faransa.

Ngati wina wake kumalo ogwirira ntchito kapena kumsika anena chinthu china kwa inu, kodi chili ndi kanthu mmene achinenera? Zoona chili ndi kanthu! Ngati iwe akutsamira, kapena kukhala motsamira kumwala ndi kunena china chake motsitsa kwanaku akuyatsamula, chimenechi chikhala chosiyana koposa ngati iwo akadanena chinthu chomwecho ndi nkhope yao yoima moyang’anizana ndi yanu ndipo akuyang’ana m’maso anu ndi moto. M’MENE chili chonse chinenedwa chili ndi kanthu kwakukulu.

Pamene tikhala ndi wina ali yense akuyang’ana kutsogolo, chimabweranso kumvetsera konse kwa munthu m’modzi. Ife sitilinso ofananana pakati pa ofanananso ayi. Ine ndili odzipereka kwa ali yense amene watenga mpando olamulira kustogolo kwa ine monga mbuye wanga, kapena kondakitara kapena wapolisi wamagalimoto kapena kadaulo wa china chake. Koma dziwani ichi bwino lomwe! Wantchito oona wa Mulungu sakhumbira kufuna kumveredwa pa iye yekha. Yohane mbatizi, amene adali munthu wa mphamvu obadwa mwa mzimayi adati, “Yesu ayenera akulire, ine ndiyenera ndichepere. Ine sindifuna anthu adziyang’ana pa ine nthawi zonse monga munthu amene ali ndi mayankho onse. Ine ndikungofuna kukonda ndi kutumikira Yesu, ndi kuthandiza ali yense kupanga ichinso. Yesu ayenera kukwezeka, ine ndiyenera kuchepera.

Munthu wa Mulungu awona ali yense amafuna kudzibwenza kuti Yesu adzitengere ulamuliro koposa iye mwini. Ndiponso, ena adzanena kuti ichi ndi chopanda tanthauzo, koma mukukhala mkuyenda kwanga m’mayiko ambiri ndi m’mizinda ndikutsimikizani inu, sikuti ndichosafunika. Ichi ndi chofunika kwambiri, m’mene tinganenere chinthu china chake. Pamene ife tiyika mipando m’mizere malo mwa mabwalo, ichi chikukhala ngati kuyatsa nyali pamunthu m’modzi. Ali yense amangokhala ngati odzangoonerera ndipo munthu m’modzi ndiye ali wachikoka. Icho ndi chinthu cholakwika chifukwa pali mphatso zambiri pakati pathu, ndipo pali zigawo zonse za Yesu. Ngati ife tiyika aliyense mwakuyang’ana kustogolo ndiye kuti likukwezga mphatso imodzi yokha basi. Kodi ndikunyada kwanji komwe munthu angakhale nako pakuzivomereza yekha nthawi zonse kukhala “mpando wa ufumu” kapena nyali younikira.

Tsono, bwanji ngati m’malo mwake mphatso zonse zitakhala ndi malo ofanana? Mwina pali wina wake ndi mphatso ya ubusa atakhala mwa bwalo. Mwina wina wake ndi mphatso ya uphunzitsi atakhala pamenepa ndipo wa mphatso ya chifundo atakhala pamenepa. Mphatso ya kuthandiza itakhala pamenepa ndipo mphatso ya uneneri itakhala pamenepa. Zonse mwa mphatso zili ndi malo ofanana chifukwa zonse ndi za Yesu! Kodi ichi chikupereka nzeru? (Ngati muli ndi makina a Kompuyuta, onani pa iwo. Aii at his feet.com / Jesus as Head kuti muone “chithunzi” cha ichi.

Tsopano, ngati mzimayi ali mubwalomu ali m’misonzi pa zakaleredwe ka ana ake, mphatso ya uphunzitsi ikhonza kuyankhula naye ndi kumuphunzitsa zokhudzana ndi zimene Paulo adanena mubuku la Tilo zokhudza azimayi. Mphatso ya chifundo ikhonza kupereka lingaliro la chifundo, mwina iye ali ndi ana a ang’ono kupereka panthawi imodzi ndipo akhonza kugawa zakuwawa za ichi. Mphatso imene ili ndi chidziwitso chauneneri ikhonza kuona mu mtima za chifukwa chimene mlongo uyu ali ndi mavuto ndi ana ake, ndi choncho. Tsopano, pomaliza, likhonza kumveradi moona lamulo lochokera kwa Mulungu, “pamene bvumbulutso libwera kwawachiwiri, siyani oyamba akhale pansi”. Allelluya!!!!!!! (Mikuwo, ibwerenza)

Ali yense, ndiofunikira mofanana

Mu Akorinto oyamba 14, Mulungu adanenanso “pamene mubwera pamodzi, abale, ndipo Mpingo uli pamodzi, lekani chili chonse chichitike mwakumanga kwa thupi la Khristu. Ali yense wa inu ali ndi inu la chilangizo salimo, bvumbulutso” Palibe bwana koma Yesu yekha! “Musaitane munthu mtsogoleri, mbuye, mphunzitsi kapena m’busa. Nonse ndinu abale”. Inu nonse muli ndi Yesu ndipo Iye ali chimodzi chimodzi mwa wina ali yense wa inu.

Mwachidziwikire pali kusiyana m’makhwimidwe, ndipo mphatso zina zili za “pachigulu” pamene mphatso zina zili zachete kapena zosaonekera onekera pa gulu. Koma, zonse zilipo ndipo zili ndi mwayi. Nthawi zina timafuna chifundo cha Yesu ndi nthawi zina timafuna chiphunzitso cha Yesu. Nthawi zina timafuna nyimbo za Yesu ndipo nthawi zina timafuna thandizo la Yesu kuti tithetse vuto. Koma zonse ndi za Yesu mofanana. Chonde werengani Akorinto oyamba 14:26-40.

Kodi mukhonza kuona kuti zimafunika kulimba mtima? Kodi mukhonza kuona kuti zimatengera chikhulupiriro ndi kumvera? Kodi mukhonza kuona kuti ichi chisintha moyo wanu ngati muyamba kukhala mu ichi? Kodi inu simungadzamangidwanso kumodzi ndi bedi! Mphatso yanu ndiyosiyana ndi yanga, koma yanu ndi chimodzimodzi ndi yanga. Ine ndikufuna mphatso yanu kwambiri monga inusno mufunitsa yanga.

Zinthu zina zofunika zimene zachitika mmoyo wanga zachitika chifukwa cha mwana wa zaka khumi ndi ziwiri ndi mphatso yake kukhudza moyo wanga. Azimayi kukhudza moyo wanga ndi ana kukhudza moyo wanga. Anthu okalamba kukhudza moyo wanga ndipo osati pa m’mawa, Lamulungu lokha ayi, koma tsiku liri lonse.

Ife tiri Ufumu wa ansembe tsiku liri lonse. Misonkhano ndi zongoonjezerapo ndithu. Mbali yokwana makumi asanu ndi anayi akukula kwathu imachokera mukukhala pamodzi, ndipo mwina mbali yokwana khumi limodzi chabe ndi m’mene imachokera mmisonkha. Ichi chitanthauza kuti muyenera kutuluka mnyumba zanu ndipo mulowe mnyumba za anthu ena. Inu munyamule madzi, kapena chakudya, kapena zovala popita kunyumba zawo. Pamene inu muona kuti ali ndi njala pamodzi ndi mwana, muyenera kuwatengera pambali ndikuyankhula nawo ndi kuyenda nawo. Pamene inu muona kuti ali ndi njala pamodzi ndi mwana, muyenera kuwatengera pambali ndikuyankhula nawo ndi kuyenda nawo. Pamene muona kudzitukumura mmoyo wawo, muyike dzanja lanu kuzungulira iwo ndi kuwafunsa iwo kuti sayenera kukhala oditukumura. Pamene inu muona kudzikonda mwa m’bale, inu muyenera kuyika dzanja lanu mozungulira iye ndipo nati, “Chonde usakhalenso odzikonda ayi”. Ife sitimangotseka maso athu kufikira msonkhano wina. Ife timakhala pakati pa moyo wa wina ndi mnzake tsiku liri lonse monga ansembe akuchita ntchito ya Mulungu, ndipo monga “zana la amai, abale ndi alongo” Ichinso ndi lamulo kuchokera kwa Mulungu mu Ahebri 3 ndiponso m’malemba ambiri.

Mwala wa madziko oyamba ndi “Kodi mkhristu ndi ndani? Kodi umembala wa Mpingo uti? Ngati inu muli ndi anthu amene siali otembenukira moona kwa Yesu mu Mpingo, ndiye kuti inu mudzakhala mapafupi pafupi ndi nkhondo ndi ndewu imene simuyenera kukhala nayo. baibulo linena, “kuchokera kwa ang’ono kufikira kwa akulu, onse adzamudziwa iye.” Pamene wina ali yense amene amadzitcha yekha membala moonadi ali m’chikondi ndi Yesu, pamakhala mtendere kwambiri—popanda ndeu, popanda mijedo. Ndipo pamakhala chikondi chakuya pa wina ndi mnzake tsiku liri lonse. Inu simungakhale membala woona wa Mpingo wa Yesu pokhapokha inu mutataya moyo wanu. Ndi Mkhristu yekha angakhale membala wa Mpingo. Ali yense ndi alendo chabe, koma iwo sakhala mamembala a Mpingo wa Yesu.

Ichi ndicho chenicheni cha zimene Baibulo linena. Ndipo “chotupitsa” chiyenera kuchotsedwa mu mktae, kapena ife sitimukonda Yesu monga m’mene tinenera. “Ngati mundikonda Ine, mudzamvera malamulo anga.” Mpingo uli kulumikiza ndi kulimbikitsa ndi kuphunzitsa ndiponso kuteteza kwa amene adasambitsidwa mu Mwazi wa Yesu, atasankha kufa kwa iwo okha kuti akwatiwe ndi Mbuye, Yesu kwamuyaya. Ali yense amene sanapange chisankho, wakuyikiridwa umboni ndi moyo wawo ndi chosankha chawo, ndipo ndikuti ngati kapena ayi, “akonda kuwala” (Yoh 3, 1 Yoh 1), sayenera kudziyesa yekha Mkhristu kapena membala wa Thupi la Mkhristu. ichi ndi chimene Mulungu adanena.

Tanthauzo liri losne la “mpingo” ndi lopangidwa ndi munthu, ndipo “makomo a ndende” adzalaka chifanifani chotere. tayang’anani, inu mudzaona ichi mu mseu uli wonse mu mzinda ndi mzinda, fuko ndi fuko. Ichi simalingaliro a Mulungu, koma china chake chomwe chimangokwaniritsa mamvedwe a anthu, pamene akugwiritsa ntchito dzina la Yesu kuti achotsere nthumadzi zawo. Koma palibe kuchiritsidwa apo! Messiah yekha ndi amene amazungulira pamene Iye angasiyepo nyali!

Mwala wa madziko wachiwiri uli ndi chochita ndi mtsogoleri. Mzimu ndi Moyo wapano wa Khristu Owukistidwa, ndiye mtsogoleri yekha wathu. Dziko silidzandiona ine, koma inu mudzandiona! Mulingo wa Mzimu umene munthu ali nao, mphatso imene wina ali nayo, kukula ndi kuya kwenikweni kumene ubale wa moyo ndi Yesu wa Moyo umene ali nawo—icho ndiye matanthauziro a Baibulo a “Utsogoleri.”

Choonadi chachitatu: moyo wa tsiku ndi tsiku

Mwala wa madziko wa chitatu uli ndi chochita ndi moy wathu wa tsiku ndi tsiku pamodzi ndipo ife tayankhulapo mochepa pa zaichi. Moyo wa tsiku ndi tsiku ulibe chochita ndi misonkhano imene timakhala nayo, koma koposa m’mene timakhalirana, ife timakhala tsiku liri lonse monga ansembe mumabanja ndipo ndi ana athu amene atizungulira ife, ndipo ndi magwiridwe ntchito ndi makhalidwe ofanana ndi anthu amene atizungulira ife? Kodi ife tikukhala tsiku liri losne pa muyeso wa pa mtima ndi abale ndi alongo? Kodi ife “timasenzerana wina ndi mnzake chipsyinjo ndi kukwaniritsa Lamulo la Khristu? Kodi ife “timavomereza ndi kuululirana machimo athu wina ndi mnzake ndi kuti tichiritsidwe? Kodi ife “timakhala monga munthu m’modzi pa chikhulupiriro,” “molumikizana ndi kulukana pamodzi ndi munyewa yothandizira”, ndipo osavomereza chili chonse kupatula “Mpingo woona ndi “Thupi la Khristu”? Pamene pokha ndipamene mudzapeza chimene Yesu amatanthauza pakuti, Ndidzamanga Mpingo Wanga kuti makomo a ndende sadzaugonjetsa kapena kuyima!” Chinthu chili chonse ndi “nyumba yomangidwa pa mchenga” wa kunyalanyaza, kufunda, kusamvera, kusalumikizana. Ndipo udzabereka chipatso choyenerera, mwatsoka. Mulungu adati chili ndi kanthu kapena tanthauzo m’mene timangira!

Ine ndikuonetsani Malembo, amodzi ndipo asintha moyo wanu onse ngati mungamvere. Ngati inu mungachite malembo awa amodzi, inu mudzadabwitsidwa zam’mene zinthu zina izi zikuperekera tanthauzo. Ichi ndi lamulo kuchokera kwa Yesu. Kodi mupanga ichi? Kodi mutero? Kodi inu mumukonda Iye? ichi chidzasintha moyo wanu onse kuti MUPANGE chimene Iye anena koposa kungogwirizana nacho kapena kungochiphunzira chabe kapena kungoyimba za icho kapena kungokumnana pa zaichi. Tiyeni tiyang’ane pa ichi limodzi. malembowo ndi Ahebri 3:12-14

Penyani abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu, mtima woipa wosakhulupirika wakulekana ndi Mulungu wamoyo komatu ndikudandaulilani nokha tsiku ndi tsiku pamen pachedwa lero, kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjelero la uchimo pakuti takhala ife olandilana ndi Kristu ngatitu tigwiritsa chiyambi chakutama kwathu kuchigwira kufikira chitsirizilo.

Dziwani chimene malembo awa akunena—ichi ndi chochokera kwa Mulungu. Mulungu wamphamvu zonse akunena kwa inu ndi ine kuti tiyenera tsiku liri lonse kuchenjezana wina ndi mnzake ndi kuthandizana wina ndi mnzake tsiku liri lonse. Mzimu Oyera udasankha kuti unene kuti “tsiku liri lonse”. Iwo siudanene kuti Lamulungu ndi la Chitatu liri lonse ayi. Iwo siudanene ngakhale kuti misonkhano mokha, iwo adati tikhale pa muyeso wa choonadi mo moyo wa wina ndi mnzake tsiku liri lonse. Ngati ena ali opezeka kapena akhonza kupezeka, ndipo inu simufuna kukhala nao kapena kukhudzidwa chifukwa cha moyo wanu, kapena kunyada, kapena kudzikonda, kapena chisankho chimene mungakhalire, Mulungu adati monga iye amvera. Inu mudzapusisidwa mu kuganiza kuti mumadzi. Chimene chili choona pamene inu simudziwa. Icho ndi chimene malembo akunena mwatchuchutchu! Iye adangoti kuchipanga ichi, iye adati ngati simupanga ichi, chidzakuvulazani kwambiri. Ngati ine ndilibe m’bale ondiyankhula ine tsiku liri lonse zokhudza moyo wanga. Tsiku liri lonse ine ndidzasanduka olimba. Ine ndidzapusitsidwa. Inu mukhonza kunena kuti, “Koma ndimawerenga Baibulo tsiku liri lonse!” “Koma ndimapemphera tsiku liri lonse! “Mkazi wanga ndi Mkhristu ndipo ndimamuona iye tsiku liri lonse!” Icho sichimene Mulungu akunena, mukhonza kuwerenga baibulo ndi kupemphera tsiku liri lonse, koma ngati simufuna kukhala mu moyo wa wina ndi mnzake tsiku lili lonse, inu mudzakhala mukuwumila umilabe ndi kupusitsidwa pusitsidwabe. Mulungu adanena ichi mu Ahebri 3:12-14. Kodi mumakhulupirira baibulo? Kodi mumakhulupirira Mulungu?

Kodi adalemba baibulo ndani? Mulungu! Mulungu adanena kuti ife tiyenera kukhala mo moyo wa wina ndi mnzake tsiku liri lonse. Ngati muwona ine ndikudzikonda, mufunika kumbwera kwa ine ndi kunena, “m’bale, osakhala odzikonda. Ichi chipangitsa Yesu kukhumudwa.” Inu mukandiona ine ndikunyada, chonde bwerani ndi kundikumbutsa ine kuti Mulungu amatsutsana ndi onyada. Ine sindifuna kuti Mulungu adane nane! Inu muyenera kuthandiza ine, chifukwa ine singingaone ichi nthawi zonse. Palibe amene angahe. “Dandaulilani wina ndi mnzake, tsiku ndi tsiku kuti ali yense wa inu asadzimitsidwe mtim kapena kupisitsidwa” Ichi ndi mbali yofunikira (ndipo siyimveredwa pafupi pafupi dziko lonse. Iyi ndi njira ya chifungulo imodzi yokhalira ansembe pogwirista ntchito mphatso, ndiponso “akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu amabweretsa chofuna chake kudzera mwa inu.”

Choonadi Chachinayi: Misonkhano

Kwa zaka 1700, mudziko la chikristu mudali chosokonezo pa nkhani yokhudza kuti Mkhristu ndi ndani …… mtsogoleri ndi ndani ……… kodi moyo wa tsiku ndi tsiku uyenera kuoneka bwanji, maziko achinayi amakhudzana ndi misonkhano ya chikristu chakhala chosamveka kuchokera mu zaka 1700 ndipo kodi misonkhano iyenera kuoneka bwanji? Atate athu akufuna kubwezeretsa zinthu izi kwa inu mu moyo wanu tsopano. Monga ngati mau a Mulungu adatayidwira mu matsiku a Mfumu Yosiya, ndipo choonandi chinakwiliridwa mu makhalidwe a ufumu ndi miyambo ya anthu, chonchonso lero Choonadi cha Mulungu, chakanidwa (koma chikadalibe mu Baibulo) koma chikhonza kumasula anthu mu ufulu. Mulungu adzasintha moyo wanu modabwitsa ndi kusinthanso ali yense ozungulira inu motsatira mwake. Ichi ndi choonadi champhamvu ndi cha mtengo wapadera. kaya muli anthu ambiri kapena ochepa m’mudzi wanuwo, monga Yonatani, bwenzi la pafupi la davide adanenera, “Mulungu siali okanizidwa kupulumutsa kudzera mu ambiri kapena ochepa.” “Iye amene wagwirizitsidwa oyenera kuonetsa kukhulupirika” Ife tiyenera kukhala ndi kulimbika mtima kuti tipangepo china chake chokhudza ndi chilungamo chomwe chanyalanyazidwa kapena kusamveredwa ku mbuyo kwapitaku. Ndi iye mwini wake adzakhala m’busa wanu, linga lanu ndiponso mulonda wanu ngati mukhala molimba mwa Iye.

Ife tiyenera kukhala ndi kulimbika mtima, kukhala ndi misonkhano monga mafotokozedwe a Baibulo mu Akorinto Oyamba 14, “pamene mubwera pamodzo, abale, wina aliyense ali ndi mau achilangizo, salimo, bvumbulutso” Palibe wina olamulira kupatula Yesu yekha. Ife timasonkha pamodzi poganizira m’mene “tingasulirane win andi mnzake ku chikondi ndi ntchito zabwino” (Ahebri 10:24-26). Ife tiyenera kuganizira ndi kupempherera pamene tingathandizirane wina ndi mnzake pamene tibwera pamodzi, ndipo wina ali yense wa ife atengepo udindo kukhala chonyamulira cha Mau a Mulungu ndi chikondi cha Mulungu. Ife tili ndi ali yense” kuganizira m’mene tingasulirane wina ndi mnzake ku chikondi ndi ntchito zabwino.” Ichi ndi icho chili mu Ahebri 10, chonde khalani otsimikizika ndipo yang’anani pa malemba amenewa! ichi ndi cha tonse a ife, ngakhale “mumisonkhano!”

Akorinto Oyamba 14 akunena kuti, “pamene bvumbulutso libwera kwa wachiwiri, siyani oyambayo akhale pansi.” Ichi ndi chimene baibulo linena. Nchifukwa chiyani sitichita chimene Baibulo limanena? Pasakhale “munthu wapadera” amene “mwachidziwikire” adziyembekezera kupanga chili chonse kupatula kumvetsera ndi kuyankha kwa Mulungu monga wina ali yense. Ngati wina wake abweretsa chiphunzitso kuchokera kwa Yesu ndipo ena abwera ndi mau a chilangizo kapena salimo kapena bvumbulutso; ngati m’bale ameneyu kapena mlongo ameneyu akugawana nafe chinthu china, chomwe Yesu waonetsa kwa iye ndipo bvumbulutso labwera kwa wachiwiriyo, oyambayo akhale pansi—ngati tikumvera lamulo la Mulungu, koposa miyambo ya anthu. MOnga m’mene baibulo limanenera nthawi zonse.

Nchifukwa chiyani sitichita izi? Ndi chifukwa choti ife tatengera katundu olemetsa wa miyambo wochokera ku katolika ndi kuchokera ku “maprotestant” ndiponso ku “dzipembedzo” ndi makolo athu opembedza mafano. “Ansembe” kapena “abusa” kapena “audindo” ena onse ali kutsogolo, kuyankhula kwa wofunikira “pang’ono”, anthu osauka onse , anthu owonerera onse—atangokhala ndi kumamvera chabe. Ichi mwachidziwikire ndi machitidwe ndi miyambo imene Yesu adati amadana nayo, miyambo ya “Antikolatia” (kutanthauziridwa monga anthu amene ‘agonjetsa anthu ake’) Koma Mulungu eti adanena kale kuti zonse izi ziyenera kusintha chifukwa cha Iye ndi cha ife.

M’malo mwake Yesu adanena kwa “bwalo lokhalo momuzungulira Iye” kuti ali yense ali ndi liu la chilangizo, salimo, bvumbulutso. Ife tonse tili abale ndi alongo ndi zogowa zosiyana siyana othiridwa mwa Yesu ngati mwa m’modzi ndim’modzi pa chabwino chimodzi. Ndi chodabwitsa ndi chozizwitsa bwanji ichi! Iye AKUTIMASULA ife kuchokera ku “miyambo yopanda kanthu yomwe tidalandila kuchokera ku makolo athu” pamodzi ndi utsogoleri wa mpingo ndi miyambo. Iye akutimasulira ife ku dziko “loopsya” la kumukhulupirira ndi kumukonda IYE monga zonse mu zonse wathu! Ndipo sikukhala chiwawa kumeneko, chifukwa Iye amadzitcha yekha, “Mulungu wa Mtendere” ndi “dongosolo” Ili ndi dongosolo lake chabe, osati kutengerapo mwai kwa Iye.

Madziko a kusintha

Ichi ndi chosiyana kuchokera pazimene tidazolowera kodi? Kodi tili nako kulimbika mtima kumanga m’njira ya Mulungu? Kodi ndizopatsa mantha? Kodi zikumveka mosekesa: Kodi ndi chosangalatsa? Anthu ena amene tili gawo la Mpingo tidali mbali ya amene adakhala ali a Khristu kwa zaka makumi awiri koma akadalidi makanda. Koma pamene adadziwa njira izi ndi kuyamba kugwira ntchito ngati ansembe! Adakula kukula kofunika zaa khumi pa chaka chimodzi. Alleluya! Ena adakhala “atsogoleri” m’mipingo imene idali ndi anthu mazana ndi zikwi. Iwo adapeza kuti mu uzimu akadali makanda! Iwo amaganiza kuti ndi atsogoleri, koma adapeza kuti ana ndi amai ambiri adali a uzimu koposa iwe. Iwo amayenera kukula kuchokera kukhala khanda, ndipo adakula! Zonse izi ndi zopatsa mantha kwambiri, komanso ndo zosangalatsa kwambiri.

Ngati muika choonadi ichi chimene chakhala mu Baibulo nthawi zonse mudzakhala odabwa mmene mudzakhalire pafupi ndi Yesu zaka ziwiri kuchokera pano. “Khalani limodzi tsiku ndi tsiku”. Monga pamodzi ndi ana anu, mabanja anu ndi kuntchito kwanu tsiku lililonse. Pitani kumeneko! Ndipo chokani kumalo kumene muli ndikuchita zimene simunachitepo inde ndikulankhulala ndi inu, chitani izi kwa Yesu. Lankhulani mau ake monga mau a Mulungu kwa miyoyo yanu mwachitsanzo kundanani munzeru yabwino tsiku lonse. Pamene mubwera limodzi abale wina ali ndi kanthu nyimbo kapena vumbulutso. Pamene vumbulutso libwera kwa wachiwiri, woyambayo akhale pansi. Mukachita izi mudzapeza kuti ena sakukonda Yesu ngati mmene mumaganizira. Ndipo ena amene mumawaganizira kuti ndiwofooka adzakhala amphamvu ndi a nzeru kusiyana ndi mmene mumaganizira. Njira ya Mulungu imaonetsera zinthu zopanda pake ndikukhazikitsa zofooka kukhala zamphamvu. Atamandike Mulungu!

Chuma ichi chapatsidwa kwa inu muchigwiritse ntchito mokomera Yesu miyala imeneyi ndiye maziko mueyenera kuonetsera kuti Khristu ndi ndani monga Yesu ananenera. Mueyenera kudziwa utsogoleri umakhala otani, khalani miyoyo yanu tsiku lonse, pamodzi limbikitsanani wina ndi mnzake manganani wina ndi mnzake, thandizanani kukula kukula ndi kukonda Yesu kopitirira masana ano ndi madzaulo ano. Bwerani ndikukumanana pamodzi mozungulira Mfumu Yesu.

Ngati mukondaYesu ndikumanga njira yoeyenera, malinga andende sadzapambana ayi, uchimo udzawonongedwa, kufooka ndi matenda kudzachiritsidwa. Uchimo udzakhululukidwa. Kukoma mtima kudzatitengera kukulapa. Ubale udzamangindwanso ndi kukonzedwanso mopitirira mmene mumaganizira mumaloto anu abwino. Muzakhala owala monga nyenyezi zakumwamba kuonetsera ubwino wa Mulungu. Ndi mkwatibwi, mpingo wake adzadzikonzekeretsa ndipo konzekerani pamene mkwati abwera. Amen

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon