Mulungu Wa Dongosolo Ndi Aefenso 4
4/8/2006
Malemia, Malawi, Africa 1996
Mfumu Yogonjetsa Ndi Mphatso Kwa Anthu
Mulungu wathu odabwitsa sanalephere kutipatsa zapamtima wake ku Mpingo wake ngati mungaone bwino ndi tcheru ku malemba, mungaone kupambana ndi zopambana za Yesu Kristo ndi ufumu wake.
Yesu anali ogonjetsa wamphamvu. Mu Efeso 4:8 imati: “Anatsogolera ogwidwa ukaporo anapeleka mphatso kwa anthu” (NIT) kuonetsera m’mene mfumu wogonjetsa imabwelera kuchokera ku dziko lachilendo atapeza Golidi, Siliva ndi zinthu zina zodula kuchokera kwa ogwidwawo. Yesu wagonjedwa adaniwo ndi kubwelerako pachionetsera cha chigonjetso atapeleka mphatso kwa anthu ake. Mphatso zimene zaikidwa mu Afeso 4:11—Atumwi, Aneneri, Alaliki, Abusa ndi Aphunzitsi—ali mbali ya mtunduwa Yesu pamene Yesu anakwera kumwamba mu mitambo ndi kutumiza mzimu wake woyera. Sanangoika mzimu wake kukhala mkati mwa ife amene takhulupilira. Koma anatenganso mbali ya iye mwini ndikupeleka kwa anthu osiyanasiyana amene akhulupilira iye. Yesu anali wansembe wa mkulu ndi okhulupirika mnyumba ya Mulungu yosne. Anali mtumwi, mneneli. Mbusa wabwino ndi mphunzitsi wa mkulu. Anali uthenga wabwino kuonekera mu thupi.
Thupi limafuna mphatso zonse
Baibulo limati pamene Yesu anapita kumwamba ndi kutumiza mzimu wake, anatenga mbali ya iye ndikutumiza zonse pathupi la Khristo, mpingo zidziwika kwa ife ndizoti ziwalo zosiyanasiyana za mbali ya matupi athu amapanga zinthu zosiyasiyana. Mungathe kuona ndi maso anu ndipo mungathe kumva ndi makutu anu. Koma simungathe kumva ndi mphuno, ndi kuona ndi pakamwa) ziwalo zonsezi sizili zofanana, mwachoncho, ziyenera kudalirana china ndi mnzake kwambiri.
Tisanapitilire ndi Aefeso 4:11, muyenera kudziwa m’mene mukufunira thupi lonse la Kristo. Timafuna tonse thupi la Kristo. 1 Akorinto 12 amati sitinganene kwa anzathu kodi “sindili kukufuna” m’malo mwake tiyenera “Ndili kukufuna iwe” “Ndili kukufuna iwe” uwu ndi mtima otere umene umakondweretsa Yesu kwambiri. Yesu anali ndi mphatso mwa iye yekha ndipo zina zazimenezi zili mu Aefeso 4. Mu mpingo wa Mulungu, thupi la Kristo liyenera kufuna mphatso zonsezi mwachoncho, mpingo wina uli wonse pawokha sungathe kukhala ndi mphatso zonse. payenera kukhala mlumikizo weniweni pakati pa amidzi ndi amu mzindawo mulumikizowo ndi wabwino ndi ofunika.
Galimoto lili ndi ziwalo zambiri, zitsulo, galasi ndi rabala. Ilinso ndi injini, chiongolero, nyali, hutala ndi matayala. Ngati tingaike zida zonsezi za galimoto mu chipinda ndiye kuti sitidzakwanitsa kuyendetsa galimotowo, Angakhale kuti zidazo ndizabwino, sumulowa mu galimoto ndi kuyendetsa mphaka zida zonse pamodzi zitakhala m’malo mwake. Munjira ina idzakhala kuunjika zitsulo, osakhala ndi zochita zabwino. Izi zimaonetsera kufunika kwa mphatso ya mtumwi.
Mbali iyi ya Yesu—mphatso ya mtumwi, ndi mphatso imene imaona uika zinthu zonse pamodzi ndi kupangitsa “galimoto” kuyenda. Palibe Atumwi ambiri mu dziko lapansi komanso m’mene zinalili ndi zaka zambiri za chikristo.
Baibulo linasindikiza atumwi osapitilira makumi awiri ndi asanu ndi m’modzi 26 mu nyengo zonse za zaka 100. Poyambirira 12 kenako 14 atumwi ena , angakhale enawo anali ndi mtima woona ndi kukonda ntchito ya Mulungu sanali ndi mphatso yoika zinthu pamodzi mu Galimoto. Enanso popanda mphatso za atumwi, sangathe kuwona m’mene angatengere zida zina mu mpingo ndikuziika pamodzi ndikukhala mpingo wamphamvu—okhala ndi mtima umodzi, maganizo amodzi, ndi cholinga chimodzi.
Mphatso Ya Mneneri
Mphatso ya chiwiri kuikidwa mu Aefeso 4 ndi mphatso ya uneneri. Mneneri ali othekera kuona ndi kumva fungo loipa kapena labwino. Iye sadalira pazimene maso ake ndi makutu ake a dziko lapansi. Iye amakwanitsa kumva fungo limene lili la Yesu kapena ai. Munjira imeneyi, mneneri amathandiza kupeleka milimo yabwino yoyenera kumamangidwa kuti Mtumwi amange. Mphatso zonse zinayi kapena zisanu zimene zatchulidwazi zili ndi malo ake ake mu thupi la Kristo, ndipo ngati mulibe mphatso zimenezi pa msonkhano pano, muyenera kugwira ntchito molimbika kumanga ubale ndi mphatso zinazo ndi anthu a mizinda ina. Mukawerenga mubukhu la Machitidwe, mudzaona kuti zimachitika pafupi—pafupi. Mphatso zimene zalembedwa mu Aefeso 4 zimayenda kuchokera mu mzinda wina kupita kwina ndikuthandiza polimbikitsa ndi kumanga, woyera mtima onse pamodzi.
Pofuna kukwaniritsa izi, mphatso ya Atumwi ndi Mneneri ndi yofunika mu mbali zisanu ndi zitatu kapena zisanu ndi zinayi mu zonse pamodzi. Popanda mphatsozi anthu a Mulungu adzakhala ndi umphawi weniweni. Ayenera kukhala amtima ofunitsitsa kukonda Mulungu kwambiri, ndikukhumudwa ndi zobvuta zina. Koma ndi kuthandizidwa ndi mphatso zobvuta zidzachotsedwa.
Kusoka Thupi La Kristo
Mphatso yamu Aefeso 4:12 ndi zofunika kukonzeketsera anthu a Mulungu ku ntchito yotumikira. Mau oti kukonzeketsera limathandauza kuti “Kulumikiza kapena kuphatikiza pamodzi” muchigiriki ndi mau amene anasankha kuthandauza kwa mphatso zisanu zimene zinali kugwirira ntchito—kuthandiza kuika fupa pa malo ake, ngati dzanja ndi losweka. Sing’anga amaika fupalo pamalo ake nthawi zina zimawawa kuika fupa pa malo ake. Koma ndizofunika kapena thupi kukhala lopunduka ndi lopanda pake. Mphatso zimene tanenazi mu Aefeso 4:12 zimalumikiza thupi la Kristo pamodzi ndikuika mbali ili yonse pamalo ake.
Kulumikizitsidwa Ndi Kudziwa Chuphunzitso Cha Yesu
Mu Aefenso 4:13 taona kuti mphatso zimachita pamalo ali yonse—zidzatithandiza umodzi wachikhulupiriro! tawuzidwa kale mu bukhu la aefenso kugwiritsitsa umodzi wa mzimu. Mulungu akuyembekezera ife kukhala ndi umodzi wa Mzimu ndipo Mulungu watilamulira kuti tikondane wina ndi mnzake.
Mwachoncho, pali kusiyana pakati pa umodzi wa mzimu ndi umodzi wa chikhulupiriro. Popanda mphatsozi, (zonenedwa mu Aefenso 4:14) kukhala mu mgwirizano ndi malo amene timakhala, tidzakhumudwa pa zokhulupirira zathu. Ndipa mphatso imeneyi imene tili okonekeletsedwa mu umodzi wa chikhulupiriro. Popanda mphatsozi (zonenedwa mu Aefeso 4:14) kukhala mu mgwirizano ndi malo amene timakhala, tidzakhumudwa pa zokhulupirira zathu. Ndipamphatso imeneyi imene tili okonzekeletsedwa mu umodzi wa chikhulupiriro.
Umodzi wa uzimu umalumikizidwa ndi ali yense amene anagulidwa ndi mwazi wa Yesu. Timalandira ali yense ndi kukonda amene mwazi wa Yesu unamubisa iwo. Timakonda kulandira iwo munjira imene timalandilira Yesu. Umodzi wa chikhulupiriro ndi kudziwana pamodzi za chiphunzitso cha Yesu—zaubatizo, kuika dzanja, kulambira, kusonkhana pamodzi ndi mphatso ya mzimu. Mphatso imeneyi idzathandiza m’mene tingakondere wina ndi mnzake ndi m’mene utsogoleri uli, ndi m’mene m’Kristo ali, zoona zake ndithu, ngati misonkhano ilibe kulumikizitsidwa ndi mphatso zisanu. Sitingakhale ndi umodzi wa chikhulupiriro, ndipo tidzasokonezedwa kuya kwa mgwirizano.
Kudzama Kwa Chikondi
Aefenso 4:13 amanenanso kuti mphatso imatithandiza ife kukhala ndi chidziwitso cha mwana wa Mulungu, chikhumbo cha Atate ndiye kuti tidziwe zili zonse za Yesu. mawu oti, “Nzeru zonse” mu malemba awa ndi “EPIGNOSIS” ndi mau amene amati ndikhale pamodzi ndi Yesu. Mulungu anasankha mawu awa ponena kuti tiyenera kukhala ndi mgwirizano weniweni wa ukwati ndi mwana wake. Awa simau enieni a ukwati ndi mwana wake. Awa simau ochokera m’mutu ai koma ndichidziwitso cha mumtima. Ndi mau omwewa amene Maria ndi Yosefesanadziwane wina ndi mnzake mphaka Yesu atabadwa ndi mau omwewa anagwiritsidwa ntchito. pamene adam anadziwa “Eva” ndipo anakhala ndi mwana.
Choncho mphatso izi zisanu ndi kwenikweni zofunikira pa mpingo. Zimathandiza anthu a Mulungu kukhala ndi kulumikizidwa ndi Yesu ndi kuyang’ana nkhope zawo kwa iye ndi kupeza mpumulo ndi mphamvu mwa iye pamene zinthu zili zolimba. Adzaphunzira kutchula dzina la Ambuye ndipo sadzachita manyazi kapena kukhukudwa.
Mau a nyimbo ina amati, “Yesu ndiye bwenzi leni leni, machimo athu ndi zopsyinja zidzatha. Tili ndi mphotho yotitengera kwa iye mu pemphero “Mphatso zisanu izi ndi zofunikira kuthandiza anthu a Mulungu kukhala mchiyanjano ndi Kristo—mlumikizitso weniweni ndi iye kuti pamene mphepo uamkuntho ibwera osaiwala kubisala mwa Yesu. Amatembenuza nkhope zawo kwa iye ndikuona kukondwa kwa pa nkhope yake ndipo anaklwanitsa kupyola mu mphepo imeneyi. Mphatso zisanu zimene zili zoyenelera kukhala ndi nzeru zonse mulumikizo weniweni wa Yesu.
Kuimba Mu Mphepo
Aefeso 4:13 imatilonjeza kuti mphatso ndi zofunika ku munthu wangwiro kumuyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristo. Izi ndizothandauza kuti umunthu wathu uyenera kukhala ofanana naye Yesu ndikuti tisatengedwe ndi mphepo yoomba ya chiphunzitso choipa chi machitidwe. Tidzakhala otheka kuima mwamphamvu, chikondi cha Mulungu. Pamene mphepo iomba modutsa ndi kugwedeza zonse zimene zingagwedezeke, noyo wa Yesu mkati mwa ife udzakwanitsa kukula ndikukhala wamphamvu. Mulungu nthawi zina amalola kuti tigwedezeke ndikutilengera ife ku zobvuta. Atate anachita izi ndi mwana wake Yesu, ndi Paulo ndi Mtumwi wina, “anabvutika mu moyo” malemba amati, “uwu ndi mwai kuti atate apeleka ife kukhala monga iye ali. Pamene mphepo ifika ndi mafunde kuomba ndi mphepo, tisatengedwe tengedwe uku ndi uko, ai. Tidzakhala amphamvu ndi mphamvu pamene tikhala pafupi ndi Yesu ndi wina ndi mnzake.
Kulankhura Mu Chikondi
Aefeso 4:15 amati kuti tidzaphunzira kulankhula choonadi ndi chikondi. Mphatso zimenezi zimathandiza ife kuti tilankhule wina ndi mnzake mu chikondi ndimnjira yowonadi. Izi ndi chinthu chofunika mu mgwirizano wa chikondi. Kulankhula choonadi muchikondi ndi kupeza njira yokondweretsa Atate ina ndi kulankhulana bwino. Tiyenera kulankhula choonadi, koma chiyenera kubvekedwa ndi chikondi, kudekha ndi kukoma mtima, ziyenera kuonekera motere mu kudekha konse. Chikondi chathu ndi kuonetsera mu mtendere ziphatso zimathandiza ife kuti tingathe kulankhulana mu chikondi munjira imene sitingathe popanda izo.
Kuphunzira Kukhulupilira Mbuye Okondewa
Malemba amanenanso mu Aefeso 4:15 kuti mphatso zonsezi zimathandiza ife kukula kufikira kumutu amene ali Kristo, Yesu ndiye mutu wa chili chonse. Ali bwana ndi Ambuye pa panyanja ndi pamtunda. Iye ali mbuye wa mitambo imene imapeleka mvula ndi mphepo imene imaomba. Ali Mbuye wa zonse zokwawa zazing’ono ndi nyama zazikulu zomwe. Alinso wambalame za mulenga lenga, ali wa miyala yonse yokhala pamsewu. Ambuye Yesu ali mbuye wa nyenyezi zokhala mu m’mwamba ndi mwezi ndi dzuwa. Afunanso kuti akhale bwana, koma akutiitana ife kulowa mu sukulu ya Yesu kumene timaphunzira kudziwa kuti ali Ambuye. Timaphunzira kukhulupilira iye. Timaphunzira kuti ali ndi nzeru zopambana zodziwa zili zonse, ndi kuti ali ndi mphamvu zoteteza ife. Ngati sitilola iye kukhala Ambuye ndi chifukwa choti sitikhulupilira iye mokwanira kapena kuti njira zake ndi zabwino ndi chikondi chake ndi chopambana, kuti sichilephera.
Mphatso zimene zimatipangitsa ife kukula msinkhu mu ufumu wa Yesu, kuona m’mene iye ali odabwita—ali wokhulupirikira, wamphamvu, wanzeru ndi okonda. Munjir aimeneyi ndingakhulupilire iye popanga zimene iye afuna kuti tichite.
David, okondeka wa Mulungu, analemba nyimbo zambiri za chikondi kwa Atate. Atatenso analemba nyimbo ya chikondi kwa iyenso, yoti ali munthu wapamtima wa Mulungu. Cholinga chimene Mulungu ananena kuti anali wapa mtima pake chifukwa anali kudziwa Mulungu ali wabwino, wodabwitsa ndipo sanamukhumudwitse ndikumupititsa munjira yolakwika. Mulungu sanamukhumudwitse ai kapena kumuononga iye Mulungu sanamupatse mwala pamene anafuna mkate, Mulungu ali kumupatsa zonse kwa iye.
Mulungu amapeleka zinthu zambiri kwa iye ngati amayang’anira pa iye kunjira zake zonse. David amachita chili chonse chimene Atate amafunsa iye osati kuti anali omvera mouzidwa, koma anali okhulupirira chikondi cha Atate ndi anzeru kwambiri. Izi ndi zimene tonse timaphunzira ndi mphatso zimenezi. Atate ali odalilika ndi okhulupirika, ndiposno Yesu amapeleka mphatso zabwino, osati zoipa, kwa ana ake. Ndiye tingamukhulupilire iye kukhala mutu wathu, chifukwa iye ali wabwino kwa ife.
“Ndili Kufuna Iwe”
Aefenso 4:16 limati thupi lonse ndi lo “lumikizika pamodzi ndi misempha” monga momwe manja ndi miendo ili yolumikizika muthupi, mphatso zimenezi zimathandiza thupi la Kristo kubwera pamudzi kukwaniritsa kugwira ntchito ya Mulungu. Taganizani kuti thupi lamunthu silingagwire ntchito ngati manja ndi miendo zili zotayana mu malo osiyanasiyana zingakhale ziwalo zodabwitsa ndi mphamvu pazokha, koma ngati sizili zolumikizika. Kwa zina mu chikondi kulumikizika ndi mutu kuti mutu olamulire, ndiye thupi lingakhale lopanda ntchito lake.
Ndifuna kulimbikitsana inu, oyera mtima, nonse kuti muphunzire ntchito ya mphatso zimenezi ndi kuona zodabwitsa zonse zimene zikubwera ndi izo. Lolani ndi kulandira Abale ndi Alongo ochokera madera ena kukuthandizani kukhala muzodabwits zambiri zimene zimachitika pochokera mu mgwilizano wa mphatsozi. Ndiye tidzakhala odalilika kwa Yesu. Tingakhale okonda ndi nzeru monga Yesu ali. Tingakhale othekera pofikira anthu amene timakhala nawo, kopambananso kuthekera pokhala ndi mabanja, wokondana. Koposanso kuthekera pokweza chikondi, ana omvera, ndi koposera pogwiritsa ntchito mphatso mu chikondi, chifukwa talora mphatso zisanu zimenezi mu malo amene tikhale. Palibe pamalo amodzi amene (sindinaone), mwachoncho Mulungu amafuna kuti tifanane wina ndi mnzake kuchokeramudzi wina ndi wina, mzinda ndi mzinda. Akufuna kuti tikule MUKUDZADZA KWA MWANA WAKE.