Mkwatibwi Akonzekera
2003
September 1996, Komba, ku Africa Malawi Afrika.
Posachedwapa Yesu adzabwera kwa Mkwatibwi wake okonzekayo (Chibvumbulutso 19:7) ndipo cholinga cha Atate sichoti tidzangoonera mkwati koma kukhala mkwatibwi wake, osati kungokhala mu nyumba koma kukhala nyumba. Tingathe izi pamene tikondana wina ndi mnzake ndi kusinthana moyo wathu tsiku ndi tsiku.
Timathandizana wina ndi mnzake kudziwa Yesu bwino pothandizana kutchosa uchimo, kukondana koposa ndi kusamalilana zosowa za ena koposa zosowa zathu. Ichi ndiye chiphunzitsa cha Yesu. Umu ndiye m’mene anakhalira moyo wake kwa ife, ndipo watiitana ife kukhala motero ndi wina ndi mnzake. Umu ndi mmene mkwatibwi wakonzekera kubwelanso kwa mkwati, Yesu.
Cholinga cha Atate ndi kuti tikhale okongola koposa pamene tiphunzira m’mene tingakondane wina ndi mnzake kopambana. Pamene tichotsa kuzikonda ndi kunyada zomwe zimatinyanitsa ife wina ndi mnzake ndi pamene timatsegula moyo pofunikira kwa wina pamenepo Mzimu wa Mulungu, chisomo cha Mulungu ndi chikondi cha Mulungu chidzathilidwa pa ife————ndipo tidzakhala mkwatibwi okongola okonzeka kubwera kwa mwamuna wathu, Yesu.
Uwu ndi mpingo————Wokhala motero tsiku ndi tsiku osati kuwonelera mu nyumba ya Mulungu koma kukhala malo amene Mulungu akhala nyumba zathu, kuntchito zathu ndi mpingo wathu utsakhala umodzi. Sipadzakhala zopinga mu mtima mwanga ndi wanu ndi nyumba yanga ndi yanu. Ndidzachotsa kunyada ndi kuzikonda kwanga. Ndidzachotsa ulesi ndi kusakhulupirila ndipo ndidzakonda ena monga Yesu, anaconda ine pamene aliyense atero, kuchokera wang’ono mpaka wamkulu, Yesu adzathira mafuta ochilitsa ndipo ife ndidzakhala mkwatibwi okongola.
Kuitana kwa Mulungu ku dziko la pansi
Kuitana kwa Mulungu ku dziko lonse lapansi kuti ikhale nyumba pamodzi ya Atate, mwana ndi Mzimu oyera—kukhala mkwatibwi amene wakonzekera yekha pakubwelanso kwa mkwati wake okongola, Yesu. Yohane 13:15, Aefeso 2:5, Chibvu19:7. Yesu anati umu ndi mmene anthu adzadziwire kuti munali ophunzira anga—osati kukweza mau patsikula sabata m’mawa, osati kutha kulalika bwino osatinso misonkhano—koma “mmene mukondelana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku” Izi ndi zimene anthu udzadziwa kuti ndi zakumwamba. Dziko liyenela kuona ife tikukondana. Sangaone izi kufyola mu za chipunda kamodzi pa sabata ai. Ndiponso ndi zobvuta kukondana mu chipinda. Adzaona kuti timakondana pamene timatengelana katundu, pamene tisamalilana zinthu zathu. Pamene anthu onse adzadziwa kuti muli ophunzira anga—osati pa zomwe timakhulupilira koma pamene aona kuti tili okondana. Uwu ndi kuitana kwa Mulungu lero kwa anthu ake.
Kumanga pa Thandwe
Kumanga pa thandwe ndi kuchita mau ake. Mukamva zimene Yesu anena, chitani zimenezo lero. Chitani kanthu ndithu, Lero, kusintha kwa Yesu osangoganizira chabe izi. Chitani pa ichi, osati kumva chabe ophunzira a Yesu chitani izi! Choncho abale ndi alongo khalani mpingo ku ulemerero wa Mulungu. Khalani banja pamodzi tsiku ndi tsiku. Yesu akondwera nanu.