Kuchotsa Zipupa

4/8/2003

Mzuzu Malawi ku Afrika 1996.

Mudziko limene tikhala monganso maiko ena onse thupi la Yesu lagawidwa gawidwa zidutcha. Pali zambiri zachitikira choncho kuti thupi la Yesu liphwanyike moipa nthawi zina ndi chifukwa cha kuzikonda ndi kuziyeneleza kwa anthu ena mwananso ziphunzitso zimakahla zosiyana, ndipo anthu amagawanika chifukwa pa chiphunzitso kwa nthawi amayambana ndipo amasiyana.

Ndi cholinga chinthu ndi ntchito kwa Yesu kuti tichotse makoma amenewa ndi zotsingazi. Yesu akufuna kuti thupi lake likhale limodzi dziko lonse lapansi. Pali zina zimene zifunika kusintha kuti zimenezi zichitike, ngakhale kuzikonda ndi kunyada kuchotsedwe pa ife.tiyenela kubwela pamodzi kuti tidziwe ziphunzitso za Yesu—pamodzi, osati mosiyana tiyenera kukhala ofewa ndi ozichepetsa kuphunzira kwa wina ndi mnzake.

Mwazina zimene thupi la Yesu lagawidwa ndi kufuna kwa anthu kuika maina pa Mpingo. Pamene tiyankhana mu Baibulo lokha, pamenepo sitiona kuti mpingo woona sunakhale ndi dzina ai ndithu, Palibe mpingo wa Babatisiti mu Baibulo kapena Apostoliki kapena Mpingo wa Nazarene kulibe kumeneko. Palibenso amannoncite” kapena makalazamatiki” ulipo thupi la Yesu lokha.

Pamene muwelenga za mpingo mu Baibulo amadziwika ndi maina ambiri. Koma sizikwangwani ai, Si undindo. Mpingo angakhale mpingo wa Mulungu kwa Akorinto ungatchedwenso oyamba kubadwa ndi chimodzimodzi. Ungatchedwenso osakhidwa kapena oitanidwa. Ndi mpingo womwenso kwa Akorinto. Maina onsewa amadziwika nawo kuti anali iwo osati chizindikiro chobvalidwa. Mwa chitsanzo ngati nditanena mbale Henry chingakhale chizindikiro ndipo ndikati Henry, mbale wanga okondedwa ndiye kuti maonekedwe, osati chizindikiro. Mipingo mu Baibulo imatchedwa ndi mawonekedwe koma osati ndi zizindikiro. Palibe pamne mu Baibulo mpingo udziwika ndi chizindikiro. Mpingo wa Babatisiti ndi chizindikiro cha chipembedzo. Abale mwa Kristu ndi mawonekedwe. Babatisiti ndi chizindikiro. Izi ndi zimene zatigawa ife tonse muzidutcha—zidutcha. Chifukwa ngati muli ndi chizindikiro chosiyana ndi changa, ndizimene zatisiyanitsa ife tonse.

Simuli mphamvu mu mwazi wa Kristu? Tisiyane chifukwa cha maina chabe? Mufunanso dzina lina pambali pa dzina la Yesu? Palibe dzina lina m’mwamba kapena pansi pano limene anthu angapulumutse nalo. Sitifuna kutchedwa ma Babasititi kapena mamone kapena Apostoli kapena Asabata. Tiyenera kukhala okonda Yesu ndi okondana. Ndi zokwanira MULI mphamvu mu mwazi wa Yesu. Ndipo palibe chimene chingatilekanitse. Ngati pali kusiyana pakati pa inu ndi ine ndi chifukwa choti wina wa ife safunana kukonda ndi kumvela Yesu. Ndizimene zingatisiyanitse koma ndi zokhazo zimene zingatisiyanitse kuchokera kwa mbale. Ngatyi muli ndi chizindikiro cha Babatisiti ndi ine cha sabata ndiye pali mgawikano pakati pathu umene ukukwiitsa Yesu. Ngati tikhala moyo wathu pamodzi ndi kusamalira wina ndi mnzake popanda chizindikiro cha babatisiti kapena a sabata ndiye pamenepo pamodzi tidzaphunzira kukonda Yesu, koma ngati tili zizindikiro zosiyana sitingakhale PAMODZI.

Dzina la Mpingo Wako ndi Chiyani?

Muchifuniro cha Yesu okondedwa, sitiyenera kukhala ndi zotchinga. M’mene Paul adalankhulira. “Atembeledwe wina aliyense osakonda Ambuye” tisakhale ndi matembelero tiyenera kuchotsa zotchinga zonse zazipupa, zotchinga ndi zizindikiro ndiye ngati pali mpingo mu mzinda wanu ndi mphamvu ya mwazi wa Yesu ndiye tidzakhala a Kristo pamodzi popanda maina. Mpingo umene tili takhala kokwanira zaka makumi koma ulibe dzina. Zoona ndi zoti pamene wina atifunsa “Dzina la mpingo wanu ndi chiyani? Timati, “timakonda Yesu” ngati ali a Babatisiti ndiye palibe zipupa sanganiza za ine monga mpikisano ndipo ndimaitana kuti tidzaone Yesu tonse pamodzi popanda zizindikiro.

Pamene wina afunsa mmodzi mwa ana athu “umapita ku mpingo uti” sakwanitsa kuyankha pokhapo ponena kuti “onse amene ndimawadziwa amakonda Yesu ngati wina afunsa, mumapita kuti ku mpingo? Ana athu amati “mukuti chiani? Iwowo ali mpingo tsiku ndi tsiku sanaonelera zochitika mu mpingo. Ndife mpingo ndipo anawo amadziwa mmumtima wawo ngakhale ali ochepera msinkhu.

Ndi zofunika kuti tisakhale ndi chizindikiro mu moyo wathu. Zimafunika kuyambira ndi inu ndipo ndi onse amene mwafikire mu dziko la chipembedzo. Apempheni choonde asakhale ndi zipupa ndi zotchinga ngati muli mphamvu mwa Yesu, tisdakhale ndi zipupa, kukhala ndi maina amene mulibe mu Baibulo zimachititsa zitchinga. Anthu ena amati, koma dzina lathu lili mu Baibulo mpingo wathu amatchedwa mpingo mu Akorinto umatchedwa mpingo wa Mulungu ndiye tili ndi dzina limene lili mu Baibulo. Sikuganiza kwabwino kutero chifukwa Paulo samatchula mpingo ndi chizindikiro zimene adanena ndi zori uwu ndi mpingo umene uli wa Mulungu. Osati “Mpingo wa Mulungu mu Akorinto” koma kuti anthu a Mulungu okhala mu mzinda wa Akorinto unali mawonekedwe osati chizindikiro ndiponso anatchula anthu omwewo ndi maina ena awiri kapena atatu. Chifukwa ndi mawoonekedwe. Alipo maina ambiri a mpingo koma ngati tikhala ndi dzina limodzi ndikukhala ndi dzinalo tapondeleza pa mwazi wa Yesu chifukwa tapangitsa kuti pakhale kusiyana pakati pa ife ndi ena amaene akonda Yesu. Ngati muli ofuna, yankho labwino pamene wina afunsa inu, “Dzina la mpingo wako ndi chiani? Nenani “ndimakonda Yesu” umakonda” limeneli ndiko kuyankha kwabwino. Pamene palibe zosiyana kuti wina sakonda Yesu. Iyi ndi njira ya Mulungu ndi njira ya Baibulo. Siosiyana ndi maina. Monga ananena mtumwi, Ana ang’ono inu. Kondanani wina ndi mnzake ndizimene timapanga sititenga kunyada mu mpingo mwathu, koma kwa mwamuna wathu Yesu Amen?

Wina amene ndinamdziwa amalankhula ndi “Abusa” ndipo abusawo anakhumudwa pamene anauzidwa kuti anali mpingo. Mbusawo anali kuganiza za “mpingo” umene umapita lasabata m’mawa mu nyumba yomangidwa ndiye pamene wina afunsa inu kuti ndi mpingo uti uli? Ndipo mufunseni Mulungu kupatsa nzeru momwe mungayankhire funsolo. Pakuti pali mayankho ambiri. Mukawelenga mu chipangano cha tsopano muona kuti okhulupilira mayankha munjira mosiyana, chifukwa anali m’mene mungayankhire mafunso. Mulungu adzakuonetsani pa zimene mungayankhire. Koma mukakhala ndi chizindikiro ndipo akakufunsani “muli mu mpingo uti?” muli ndi yankho limodzi lokha—chizindikiro tsopano ngati mulibe chizindikiro mungabweretse pafupi ndi kwa Yesu powauza kwa iwo za Yesu ali ndi moyo ndi thupi lake ndi mpingo sichimene upitako, ndi chimene uli ndi Banja osati bungwe mungathe kutero pamene wina afunsa muli mu mpingo uti—pokhapo muli ndi chizindikiro chifukwa ngati sakhulupirira inu adzaganiza muli monga m’modzi amene amapita ku nyumba zomangidwa ngati musiyana mu chikhulupiriro ndi zimene amachita iwo, koma ngati mulibe dzina monga mipingo ya m’baibulo imene inalibe dzina lirilonse ndiye akafunsa dzina la mpingo munganene za banja lodabwitsa la thupi la Yesu ndi moyo wamoyo ukhala mwa anthu ake.

“Mundondomeko chikhulupiriro”—Chotchinga china

Chifukwa china chimene kuli zipembedzo ndi kuzikonda kwa anthu china ndi kusiyana kwa maonekedwe. Kusiyana kwa zotsatira mu chikhulupiriro pamene mbusa ndi munthu uja ndilankhula kale anayamba kulankhulana samadziwa zimene mnzakeyo amakhulupirira ngati munthuwo ndi abale ena adakadziwa bwino munthu winayo anakatha kulankhula zina zosiyana mukuchokera mu mgwilizano wawo. Anakatha kulankhula kubadwa kwa Yesu komanso muimfa yake ndi kuuka kwa Yesu; komanso zoti ali kubweranso kw aanthu ake. Adzayamba kuyankhula kuti Mkristu ndi ndani? Kuti ngati sungataye moyo wako kwa Yesu sungathe kumpeza iye, komanso ngati sungatenge mtanda wako sungathe kukhala ophunzira wake. Mu mgwilizano angayamba kugwira ntchito kuti mndondomeko ya chikhulupiriro ndi otani.

Muli ndi ana ndi amai? Ndondomeko ya chikhulupiriro chanu ndi yotani mu banja lanu? Pali zambiri zimene zili zofunika mu banja lanu koma mulibe mdnodomeko wa chikhulupiriro m’banja lanu. Inde zimatero koma osati motero sumaika pa chipupa koma zimakhala mu mtima wanu ndi m’mitima ya ana anu chifukwa munawaphunzitsa iwo ngati ndabwera pa nyumba yanu kudzakhala ndipo simundiuza iwe za “ndondomeko ya chikhulupiriro” ndidzaona pa nkhope yanu. Ndidzaona m’mene mumatchalira ndi akanzi ndi ana anu ndidzaonanso m’mene mumalimbikira ntchito ndipa chakudya pagome ndipo ndikakupezani kuti mwapinda mabondo anu ndi kupemphera pa mbali poterosimunaike muzipupa koma ndondomekowo ulipo ndithu.

Pamene mpingo ukhala banja ndi zofanana motere sitiika zinthu mu zipupa, koma pamene mwatidziwa ife mumaona mu mitima. Ngati wina adzakhala mbanja lathu, mpingo wathu (umene uli ndi anthu zana la anthu). Ndipo sakhulupirira zakubadwa kwa Yesu ndikuti iye ndi mwana wa Mulungu ndikuti mwazi wa Kristo ndi umene unatiombola ife kuchokera kumachimo, sitingawapatse ndondomeko ya chikhulupiriro chifukwa ndife banja silimodzi lokha monganso banja silikhala limodzi lokha koma chifukwa tili nawo mi mitima yathu, monga mmene banja lichitira. Sipapita nthawi tisanakambilane zinthu zofunika.

Bvuto lokhala ndi ndondomeko wa chikhulupiriro ndikuika pa chipupa ndi zofanana kukhala ndi dzina la mpingo. Zimamanga zipupa ndi zotchinga pakati pa anthu, ngati munthu angabwere kwa ine, nati “ndina mbabatisiti? Ine nditi, inde ndine mbabatisiti adzaganiza kuti amandidziwa, koma sandidziwa koma zimene adziwa ndi zimene mubabatisiti amachita ndiye kumaganiza kuti amandidziwa. Mwa ichi ngati ndili mkristu opanda chizindikiro ndiye sadzaopa ine chifukwa adzaganiza kuti wandidziwa kale tsopano adzalankhula kwa ine kuti ndine ndani chifukwa sindinabisare mu chizindikiro cha Babatisiti adzalankhula kwina zazinthu zina—monga mwazi wa Yesu ndipo ndingamuuze m’mene ndimakhulupirira ngati ndikulakwitsa angathe kundithandiza kusintha koma ngati ndili wa Babatisiti amanenatu kuti “chabwino” pamene tilibe zotchinga pamenepo tidzakhala ndi mulumikizo umene tingathandize wina ndi mnzake.

Kukonda anthu, koma mudane ndi zosakaniza

pamene mpingo mu Baibulo suli ndi kugawikana pa dzina posiyanitsa kudziwika ndi aKristo a mu mzinda wina pali chinthu ichi monga mwa mpingo pa wokha ndikunena ichi chifukwa ndi chofunika kukhala mu ubale ogwilizana ndi wina ndi mnzake. Mu dziko la Amerika pali kapena mitundu itatu pazochitika mu dziko la chikristu. Loyamba ndi mbali ya chipembedzo chokhala ndi chizindikiro. Alipo anthu abwino mu chipembedzo zimenezi ndi ena oipanso. Pali anthu amene anachoka mu chipembedzo koma sanathe kupeleka moyo wawo kwa okhulupirika ena ndipo pali kutayana. Amakonda Yesu ndipo amakhulupira choonadi koma amafuna anthu nthawi iliyonse. Malembo amati dandaulilanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku pamene patchedwa lero. Ndipo ngati sitidandaulilana wina ndi mnzake potchedwa lero. Ndipo ngati sitidandaulilana wina ndi mnzake potchedwa tsiku ndipo tidzaumitsidwa mtima ndi kuunitsidwa (Ahebri 3:12-13).

Pali ena amalowana mukulumikizidwa pamodzi tsiku ndi tsiku mu moyo. Sali mbali ya chipembedzo, koma amakonda anthu a chipembedzo. Amakonda tsiku ndi tsiku ndipo ali mpingo. Sangoyenda chisawawa ali amene Baibulo amati “olungamitsidwa pamodzi ndi mitchempha” pamene mbali ina yafooka, onse amafooka. Pamene mbali ina pali mdalitso, onse amakondwera amaima ndi kukhala pansi ndi kulankhula onse pamodzi. Uwu ndiwo mpingo opanda dzina ndi zinyumba zomangidwa kapena kuwonelera ndipo mamembala ake ali mu moyo kukondana wina ndi mnzake tsiku lililonse.

Ndiye magulu atatu amenewa. Ambiri amapita mumachitidwe otere nthawi zambiri. Ambiri tinaonetsedwa kwa Yesu mwa chipembedzo, ndipo zabwino zabwera kuchokera mukutero. Chifukwa ambiri ndi ofewa kuganiza kwawo amaona kuti sangathe kupitiliza mu chipembedzo. Yesu anati ndidzalavula otentha chabe mkamwa mwake. Muchipembedzo muli anthu otentha ndi ozizira. Pamene musakaniza kutentha ndi kuzizira ndipo amene amaganiza monga Yesu adzakhala ndi zobvuta pamene akhala ndi machitidwe otere. Tingakhala umasuka ndi kusatsaniza ngati ndife osalumikidwa ndi Yesu chifukwa iye sakonda kusakaniza. Ndipo timakhala ndi zobvuta. Timakonda anthu, timafuna kutumikira ndi kuthandiza ndiponso timawafunanso. Koma pamene pali kusakaniza sitidziwa tidzachitanji. Anthu ena amachoka muzimenezo. Kapenanso amachotsedwa, amachoka mokhumudwa ndipo ali paokha. Timafunsa kuti akhale ndi anzawo mofulumira mu moyo wa tsiku ndi tsiku ndikusakhala paokha nthawi yayitali. Tiyenera kupemphera zipembedzo ndi anthu apadera-dera amaene ali kumeneko, koma zipupa ziyenera kugwetsedwa ndi kutentha chabe kuyenera kutha. Malemba anati kuchotsa chotupitsa mkate. Ichi ndi cholinga chathu—kuthandiza kuchotsa chotupitsa.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon