Zimathandauza Chiani Kukhala Wa Nsembe

4/8/2003

Kuchita Zinthu mu njira ya Yesu

Mzuzu, Malawi, Africa, 1996

Popanda maudindo—ndife tonse Asembe.

Mu bukhu la Chibvumbulutso limati Yesu anatigula ife kukhala ufumu wa nsembe kutumikira Mulungu wathu (Chibvumbulutso 5) ngati tonse tingakhale ansembe tiyenera kudziwa kuti kukhala wansembe ndi chiani ngati tikufuna kukhala ndi mphamvu m’moyo mwathu tiyenera kukhala ndi maganizo a Mulungu pamoyo yathu. Yesu anati “pitani ndipo ndidzakhala nanu” Anatiphunzitsa, chitani chifuniro changa ndipo ndidzakupatsani inu moyo ndi mphamvu.

Chikristo chonama kwa nthawi yaitali chapondeleza anthu pansi. Zatengera anthu ochepa ena ndi kuwakweza ndikuwapanga Atsogoleri olemera ndi otchuka ndi a mphamvu, potero ndikupondereza ena pansi, ku America, India, Poland, Romania, Brazil ndi malo ozongulira kuli akhristu apa mwamba ndi apansi. Izi ndi zoipa. Yesu ananena kwa Atumwi khumi mu Mateyu 23 musamutche wina Mphunzitsi, musamutche Atate, musamutche wina mtsogoleri win aAmbuye, kapena (Rabbi) mphunzitsi kapena Mbusa kapena a Reverendi.

Pakuti muli nonse abale ndi Atate m’modzi palibe otchuka mu Chikristo choona koma Yesu yekha. Pasakhale mabwana olemekezeka amene akuchita zonse pa okha, ndalama, ndi anthu omwe pokhapo Yesu mwa anthu ake mwa Mzimu wake.

Nsembe ya Moyo

Pamene Mulungu afuna kuti ife tikhale ansembe anali ndi malingaliro mu maganizo ake. Wansembe amapeleka nsembe zauzimu kwa Mulungu. Mungathe kutero ndithu. Mulungu afuna kuti mutero. Sizaiwo utchuka okha ai ndi zawina ali yense wa ife. Nsembe ya uzimu monga Paulo ananena ndi kupeleka matupi athu monga nsembe ya moyo. Yesu amafuna lilime, maso anu ndi makutu. Amafuna maganizo anu, manja ndi mapanzi. Mungathe kupeleka ziwalo zathupi lanu monga zida za chilungamo chokha. Kapena mungapeleke ku uchimo, kuzikonda, kunyada, chilakolako ndi mantha. Koma Yesu amafuna ife kupeleka ziwalo za thupi lathu monga nsembe tsiku lililonse ndipo tidzakhala ansembe.

Ambiri amadziwa mbali iyi yoyamba ya unsembe kupeleka thupi monga nsembe. Anthu ambiri saatha izi ai, koma ambiri amadziwa zimenezi kodi mudzachita?

Kutumukira anthu ndi kuthandiza wina ndi mnzake kukhala Yesu!

Ntchito ina pambali ya unsembe mu chipangano chakale zimene anthu ambiri sadziwa ndi kutumikira anthu—osati kupeleka nsembe zopsyeleza kokha koma kutumikira anthu. Ansembe mu chipangano chakale amabweletsa Mulungu kw anthu. Tsopano, mu chipangano chatsopano ife tonse ndife ansembe ngati muli otsatira wake wa Yesu ndinu wansembe. Sitingokhala ndikuona wansembe alikuchita ntchito ya Mulungu. Ndife a nsembe mukhulupilira mumtima mwanu kuti ndinu wansembe? Bweletsani Mulungu kwa anthu. Pali njira ziwiri zomwe mungabweletsere Mulungu kwa anthu ina ndikuwauza anthu za Yesu kwa okhala nawo pafupi. Ndife tonse ansembe, choncho timabweletsa Yesu kwa okhala nawo pafupi ndi anzathu ndi mabanja awo Amen?

Wansembe amabweletsanso Yesu ku banja la Mulungu timawauza anthu ena za Yesu ndi njira zake, koma pali njira imene timabweletsa Yesu kwa anthu. Lolani ndilankhula mu zodziwika ngati muli wansembe mudzathandiza ena kukhala ngati Yesu. Ngati mungaone chithunzi cha Yesu mu mtima wanu ndi kuona kuti ali otani, ndiye yang’anani mlongo mbale amene ali ndi inu ndikaona kusiyana kwawo ndi Yesu ngati ansembe timafafanitsa kukhala otero ndi iye. Kodi Yesu ndi ozikonda? Mbale wina kapena mlongo ozikonda? Inu ndinu wansembe, athandizeni, mudzathandiza ena. Kodi Yesu amaopa? Mbale wina kapena mlongo akamaopa, athandizeni kodi Yesu amasamalila ana? Kodi anati “Bweletsani ana adze kwa ine? Ngati muona mbale, mlongo amene sakonda ana ang’ono ndi kuwasamala, ndiye thandizani kusintha ndi zimene wansembe amachita. Timathandiza aliyense kukhala monga Yesu ali ngati Yesu anakakwatira anakakhala okwiya ndi ukali kwa mkazi wake? Ngati Yesu anakakhala mkazi anakakhala okwiya kapena kuzikonda kwa mwamuna wake? Mudziwa mayankho ake ku mafunso amenewa Yesu odabwitsa mu zinthu zonse.

Inu ndinu ansembe thandizani abale ndi alongo kukhala monga Yesu analiri. Izi ndi zopweteka, izi ndi zobvuta. Chifukwa wina adzaganiza kuti muli woziyeneleza kapena oweluza chabe koma ai, inu ndinu wansembe monga wansembe monga Mulungu wakuitanilani. Sitifuna kukhala wozikonda kapena woweluza chabe. Tikufuna kukhala ozama, kuzama mu chikondi mu mtima yathu kwa aliyense. Koma tiyenenla kwafunsa kusintha kuti akhale monga Yesu—chifukwa ife ndife ansembe a chifumu.

Aliyense waife ndi wansembe wa Mulungu. Koma ndili ndi mabvuto athu ameneyonso, zilipo zinthu zimene aliyense waife sakwanitsa monga Yesu ngati ndikhulupilira kuti muli wansembe, ndiye ndiyenera kumvera kw ainu kuwona zinthu pa moyo umene sulingana ndi Yesu.

Ndikuitaneni inu monga wansembe kuona mu moyo ndi kuthandiza ena. Tili ndi kulimbika ndi kuzichepetsa pofuna anzathu kutithandiza ndikulankhula ndi moyo wathu. Mpingo sikumalo amene umapita ai mpingo ndi anthu pokhala ansembe pamodzi, umakhala mpingo pamene aliyense akuthandiza wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku kukhala monga Yesu. Simuli mpingo chifukwa muli pena ndipo mukumvera. Ndinu mpingo umatchedwa thupi la Kristo.

Ngati sitithandiza ena kukhala monga Kristo ndiye kuti sitili kumbali ya thupi lake. Tiyenera kuthandizana wina ndi mzake.

Atate, woyera Ambuye Mulungu wa mphamvu, ndi pemphero tonse pamodzi kuti mutsegule maso athu ndi ana onse kulikonse. Mulungu woyera, tionetseni kwa ife mmene tingakhalire ansembe. Tipempha inu pakulimbika, kuthandiza ndi nzeru zimene zingakhudze moyo wa ena. Tikupemphani mu kuzichepetsa ndi kulimbika polora anthu ena kulankhula ndi miyoyo yathu. Tikufunani kwambiri, tifuna kukhala mpingo wanu. Tifunanso kugwetsa makomo a ndende ndi kukondana wina ndi mzake mwa pamwamba. Mzimu woyera, thandizani ife. Phunzitsani ife njira zanu, thandizani ife kusintha mofulumira. Tikukondani koposa. Tipatseni ife nzeru yanu. Tidziwa kuti nyumba yanu imangidwa ndi nzeru, ndipo tifuna koposa. AMEN.

Kuthetsa Mabvuto

Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita mulangize pa nokha iwe ndi iye, ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe m’modzi kapena awiri kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Ndipo ngati iyee samvera iwo, uuze mpingo, ndipo ngati mpingo ngati iye samveranso mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho. Indetu ndinena kwa inu zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa kumwamba ndipo zili zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa kumwamba. Ndiponso ndinena kw ainu kuti ngati awiri a inu abvimerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wakumwamba adzawachitira. Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa ndili komweko pakati pawo. (Mateyu 18—15-20)

Anthu ambiri amene amamva vesi 20 amaganiza ndi pamene mpingo wonse ukumana ndi pamene tili okondwa kuti Yesu ali pompo. Timaimba matamando kwa Yesu, timamva bwino ndi kumva kupezeka kwakwe. Pamene zimenezi zili zoona sizimene Vesi 20 limanena ndime imeneyi. Sinena za anthu kukhala pafupi ndi kuti Yesu ali pakati pawo, koma salankhulanso za kulambira pano. Akulankhula kuthetsa mabvuto. Akuti pamene tili ansembe ndikuthandiza ena monga Yesu ali pali nthawi imene timayenera kubwela mu moyo wa aliyense. Mukaona ine kuzikonda muyenera kubwela ndi kundiuza. Pamene mlongo wina aona mlongo wina akunena za wina. Mulankhuleni za zimenezi. Mjedo ndi chimo, mjedo umaswa mtima wa Yesu. Njedo ndi mwano ndi umapweteka Yesu ndiye pamene taona kuti ndi uchimo ndipo labvulaza Yesu mu thupi lake, monga wansembe ndi thupi la Kristu. Tiyenera kuthandizana.

Yesu anati ngati pali utchimo muyenera kupita kwa iyeyo basi (ndime 15) sitifuna kuchititsa manyazi ena. Mu chikondi timafuna akhale monga Yesu, ngati ali wozikonda kapena a njedo sangathe kumva Mulungu. Pokhala ndifuna kuti amve Mulungu, Tiyenera kuthandiza ngati ali wonyada kapena kuzikweza ndi a mwano, mdiye sangakonde Mulungu kapena Anthu mwabwino. Choncho monga Ansembe tiyenera kupita kwa iwo kuti akhale monga Yesu. Koma, tiyenera kuzichepetsa. Sitikuloza chala ndi kuloza tagwira miyendo yawo ndi kuwapempha kuti apelike moyo wawo kwa Yesu. Tikufuna iwo kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu ndiye sangathe kutero ndi Mulungu ngati pali tchimo mu mitima yawo, ndiye Ambuye ndi Mphunzitsi Yesu amati tipite kwa iye yekha. Musachititse manyazi kapena kuwauza iwo akondeni. Koma pitani kwa iwo ndi muwathandize ndinu wansembe, mupite.

Ngati awiri kapena atatu ndi enanso Yesu amabwelanso, pomwepo!

Yesu amapeleka mayankho ku mabvuto pamene zinthu zabvuta. Pamene tapita kwa mbale kapena mlongo mu kuzichepetsa kuyesela kuzichepetsa ndi kunena kuti, chokani, sindifuna kumva kapena osandiweluza ine. Chotsani chitsotso mu diso lanu. Yesu amapeleka yankho pabvuto ili. Pali mbali yoti mungalakwe koma muyenerabe kupita ngati mukuganiza kuti sindinu olakwa. Yesaniso ngati mukuopa kuyesa, ndiye sindinu wansembe. Simungakondweletse Yesu ngati mpaka mutayensa. Mwina mwalakwitsadi choncho ndi bwino kutero, chifukwa adzaphunzilanso pa ichi Yesu anati ngati mukupita kwa mbale kapena mlongo ndiye samvera, tengani awiri kapena atatu kuyesela kuthandiza. Ichi sichiphunzitso cha “makhalidwe a mu mpingo” Ichi ndi chiphunzitso cha mmene tingathandizire wina ndi mzake.

Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhana mdzina langa, ndilikomweko paka ati pawo. (Mateyu 18:20)

Pamene pali awiri kapena atatu asonkhana pogwira ntchito yake, Yesu amabwera. Malembo awa sinthawi ya kulambira. Uku ndi kugwira ntchito pamodzi kuthandiza ena kukhala monga Yesu. Ngati tipita kwa mbale kapena mlongo, ndipo sakumvera chifukwa sakumvetsa kapena kufuna izi, pamene tibweletse abale awiri kapena atatu ena tonse. Ili ndi lamulo la Yesu. Sanati ngati samvera inu muiwala kapena kupemphera. Anati ngati samvera inu, tengani awiri kapena atatu alongo kapena abale, ndipo Yesu adzabweranso.

Ngati tibwera mu dzina lake pochita ntchito yake. Iye adzabwera ndi kuthandiza. Ananenanso kuti ngati iye samvelanso awiri kapena mboni zitatu. Ndipo uzani mpingo wonse. Kenanso, ichi “simakhalidwe a mu mpingo” ichi ndi kubweletsa ansembe pamodzi kuyensa kuthetsa bvuto. Zimenezi ndi zabwino.

Yesu wathu ndi wanzeru zosawelengeka. Iye ndi wauphungu wodabwitsa sichoncho kodi? Yesu anati kuti ngati pali mabvuto bweletsani ansembe kuyesa kuthandiza wina ndi mzake, tingabweletsenso anthu ena kudzathandiza, ngati ndibwera ndikuona kuti pali tchimo mu moyo ndipo simubvomeleza, poti kapena ine ndalakwitsa—kapena sindiona zinthu bwino. Pamene tibweletsa awiri kapena mbino zitatu mwina adzanena kuti ndalakwitsa. Choncho Yesu amapambana, ndi onse amakula. Izi ndi zopambana kuzidziwa ngati muli Ansembe. Zinthu siziyenda bwino nthawi zonse, koma tiyenela kukhala ndi kulimbika ndi chikondi. Tiyenera kumvera Yesu mu zimene anena nafe pamene zinthu sizili bwino. Ngati zinthu sizingayende bwino titenge anthu ena ndi kumvera pamodzi Yesu. Nthawi zina munthu m’modzi amakhoza mwinanso winayo ndi okhonza. Ndi nthawi zina onse ndi okhonza ndipo zimakhala kusamvetsana bwino. Mwinanso onse ndi olakwa, koma akamvela malamulo a Yesu pobweletsa awiri kapena atatu—ngati timvela kwa Yesu ndipo tisamalitsa—pamenepo Yesu adzabwera kudzathetsa mabvutowo ndi kutithandiza.

Chida chodabwitsa

Wamkulu wa nsembe adzathandiza ansembe onse, koma tiyenera kuchita mu njira yake osati, ulesi posalankhulitsana kwa wina ndi mzake. Tisachite mantha kubweletsa ena ndi kulankhula za izi ndipo ngati wina wabwera kudzalankhula nafe. Chifukwa ndimakonda Yesu ndi choonadi, ndipo ndaona kuti ndachimwa. Kuitana ena kuthandiza ndi kuonetsara kudabwitsa mu nzeru ya Mulungu. Ndidziwa kuti ngati awiri kapena atatu ena abwera. Yesu amabweranso.

Monga Ansembe, tiyenera kuganiza za izi ndi kuziika mu ntchito. Simasewero chabe sitikuyensa kukwanitsana wina ndi mzake pamene tikubwelera polankhulana nthawi zonse. Sikuti taikidwa ngati a polisi. Koma ndi kukondana wina ndi mzake mokwana ndi kuyensa kuthandiza. Pamene pali uchimo makutu amakhala otseka pakusamva Mulungu. Pamene pali uchimo maso amakhala osaona Mulungu ndiye monga ansembe tiyenera kuthandizana kumva Mulungu ndi kuona Mulungu pothandiza kuchotsa chimo.

Yesu anatipanga zida izi mu zoikira zida ngati sitingathese mabvuto amodzi ndi amodzi. Pamenepo anatipatsa ife zida zobweletsa ena kuthandiza kuthetsa zobvuta. Uwu ndiye ukwati weniweni ngati akazi anga ali ndi bvuto ndi ine ndipo sindikumvera, ndikudikira kuti amvera Yesu ndikubweletsa awiri kapena atatu ena. Yesu, sananene kuti zonse ndi zotero koma mu ukwati ai. Iye anati zonse ndi zoona kwa anthu onse okhulupilira. Zonse ndi zoona kwa ansembe onse. Ngati akazi anga aona uchimo paine ndipo sindikumvera ayenera kutenga awiri kapena atatu ena. Ndifuna iye atero, chifukwa ndikonda Yesu ndi zimene wina wa inu afuna? Izi ndi zolimbikitsa.

Landilani mpeni ….. muchilitsidwe.

Nthawi zonse, mpeni umapweteka, koma Yesu ndi sing’ang’a wamkulu amachotsa khasa kuti tikhale wabwino ndi mphamvu. Zimene talankhulazi ndi zopweteka pang’ono nthawi zina, koma mukamvera njira ya Yesu ndi kuzichepesa ndi kukonda ndiye adzakupangani inu a mphamvu ndi nzeru ndi wopambana. Adzachilitsa nthenda zathu zonse za mu mtima ndi thupi. Adzaika chikondi chozama mu mtima ndi kukupatsani moyo mudzakhala mitsinje ya moyo yotuphuka kuchokera mwa inu ndi Mtendere zimene zidutsa kudziwa konse. Mudzakhala ndi chimwemwe chosaneneka chodzadza cha mu ulemerero. Mudzakhala ndi mphamvu ya moyo wa ngwiro, ngati mudzachita mu njira ya Yesu ndikukhala ansembe simudzakhala anthu chabe. Mudzakhala ndi kudzadza kwa mzimu woyera ndi nzeru koma muyenera kulandira mpeni podula uchimo wonse. Muyenera kukhala okonzekera mpeni kudula chimo. Mukhale okondwa pothandizidwa, ngakhale pamene zipweteka uwu ndi maganizo a ophunzira wa Yesu.

Aliyense angathe kukhala mu chinyumba ndi kumvetsera mau onse. Koma Yesu watiitana ife kukhala ansembe ndi mafumu. Paulo anakalipira abale akwa Akorintho pamene anati “mulikuchita ngati anthu wamba monga adziko la anthu” koma Mulungu watiitana ife kuweluza angelo, watiitana ife kukhala odzadza ndi moyo ndi ulemerero ndi mphamvu monga mwana wake, Yesu. Koma tiyenera kulandira mpeni podula uchimo. Tiyenera kuthandizana pochita zimenezi kwa ife ndi mpingo, zimenezi ndi zeni-zeni zoona Mulungu anti “Yesani, ine yesani ine muona” kumvera njira ya Yesu ndi kukhala ansembe tsiku ndi tsiku. Khalani ansembe pa okuzungulilani pelekani matupi anu monga nsembe ya moyo ndi kuthandiza ena kukhala ngati Yesu ndipo Mulungu adzathira madalitso mu mtima mwanu.

Bwelani Mudzapeleke

Pali mbali ina imene pokhala wansembe uyenera kuidziwa. Iyi ndi yochepa polingana ndi zina zimene talankhula kale. Muyenera kupeleka nokha monga nsembe ya moyo ndi kubweletsa Yesu kwa anthu, kuwathandiza iwo kukhala monga Yesu analiri. Koma plai mbali ina pokhala wansembe imene imakhudza pa msonkhano kapena pokumana. Ngati simunapeleke matupi anu monga nsembe yamoyo pokonda anthu mu malo amene mukhala, ndi kuthandiza ena kukhala ofanana naye Yesu mu moyo wa tsiku ndi tsiku ndiye kuti msonkhano ulibe kanthu koma ngati mukuchita zimenezi pokhala wansembe ukunso ndi mbali yokhala wa nsembe.

Ngati Yesu adakakhala muthupi mu chipinda chino nthawi yino. Akonza kukhala phee nthawi zina koma nthawi zina Yesu amakhala ndi zofunika kulankhula. Yesu ali pompano ngati mukhulupirira kuti muli ansembe chifukwa Mulungu adatero mu mwazi wa Yesu (osati mukumva motero, nzeru kapena mphamvu) ndiye muyenera kukhala wa nsembe pa nthawi imene woyera ali pamodzinso. Ngati Yesu akhala mwa inu ndipo munabatizidwa mwa iye mu moyo ndi mzimu wake, pameneponso mungamvenso Mulungu. Monga wansembe, mudzabwera kupeleka. Bukhu la Ahebri limalankhula za izi

“Ndipo tiganizire wina ndi mzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino osaleka kusonkhana kwanthu pamodzi monga amachita ena komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyanduka.” Ahebri 10:24-25.

Taganizirani kufunika kwa kukondana ndi ntchito yabwino choncho mong wa nsembe ndi mabwera pakati pa abale ndi kuona mene tingaperekere, ndingaperekere motaninso. Muyenera kunkhala olimbika mtima Kunene zimene Yesu afuna. Osaopa kulakwitsa ngati mwalakwitsa mudzakula ndiye motero kofunika kuklhala nonse pamodzi mujsakhale anthu osafunana khalani nonse nthawi yonse pamene muyembekezera kudza patsiku la Ambuye, Monga Yesu adza posachedwa.

Osazimbaitsa, Mwamva

Yesu anakwiya, anakwiya pa zinthu zochepa. Yesu anakwiya kwa onyenga. Anakwiya kw anthu amene amayelekeza kukhala njira ina pamene mu mtima muli kusiyana njira. Yesu anakwiya pa zimenezo ndipo ali choncho mpaka lero. Tisanyenge kuti tili otere pamene sichoncho. Pamene zoona mu moyo tili mu njira yosiyana. Tiyenera kulankhula za izi ndi abale athu ndi kufuna kuthetsa mabvuto poyera ndi moona. Mulungu anati “muulure uchimo kwa wina ndi mzake” kuulura ndi kupemphera kuti tichilitsidwe. Anthu ambiri ali odwala mkati muuzimu kapena mthupi chifukwa satsegula mitima yawo ndi kunena machimo awo kwa anzawo, amaopa kuchita chomwechi. Koma mu nyumba ya Mulungu tisamaope ali chifukwa timakondana wina ndi mzake ndipo tifuna kuthandiza. Sitichita miseche sitidzakanana. Tidzathandizana wina ndi mzake, choncho tingawulure machimo athu mwaufulu. Tidzamva chisoni koma osaopa konse. Yesu adzathandiza ife ndikutitchuka ife koma ngati tinama kuti tilibe uchimo, ndiye tili achinyengo ndipo Yesu amakwiya. Yesu anakwiya, amakwiya ngati tili achinyengo sitifuna Yesu akwiye chifukw acha ife. Timachita ife? Choncho titsegule mitima yathu.

Musakwirire Luntha lanu

Yesu anakwiyanso ndi munthu wina, anakwiya kwa munthu amene anakwirira luntha lake. Ndipo Yesu anamutcha munthuyo wantchito oipa. Anamutulutsa kunja ku mdima. Chimene ndili kulankhula nanu ndi ichi, monga wansembe simuyenera kubisa luntha lanu. Mulungu anapeleka kwa wina aliyense wa inu china chake chapatali pa moyo wake. Ngati muli wa nsembe, gwilitsani ntchito chimene Mulungu anakupatsani. Munthu uyu mu fanizo limene anakwirira ndalama ali wamantha.

Yesu sanakondwere naye ai pokwririra luntha lake. Pamene oyera mtima ali pamodzi Yesu safuna kuti mungokhala, kumvetsera ai. Safuna kuti inu mukwirire chimene anaika mwa inu inu ndinu ansembe. Limbikani, mphamvu ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti mungakwanitse kulankhula mu mphatso imene anakupatsani inu, aliyense wa inu ndipo musaope monga munthu uyu mu fanizo.

Lingalirani monga mmene mungachitire ndi ena ngati muli wansembe pamodzi ndi anthu ozungulira nanu ndi okhulupirira ndi thupi lanu choncho mungathe kukhala wansembe pamene abale ali pamodzi. Muyenera kufuna kubweletsa nyimbo imene ili pamtima wanu. Aphunzitseni anzanu nyimbo imene mwaphunzira pamene mumapephera ndi Yesu m’mawa, kapena muzawelenga limodzi la Masalimo ndipo mudzafunsa Yesu kuti akupatseni mang’ombe abwino pa nyimboyo. Ndiye monga wa nsembe bwelani ndi kubweletsa woyera mtima pamodzi, ndi kuphunzitsa nyimbo imene Yesu wapeleka kwa inu. Ndiye wa nsembe muyenera kutero ngati wansembe musakwirire luntha lanu.

Mwina mbale adzabwera nalankhula za uchimo mu moyo wanu. Mumveleni iye ndipo zibweletsa misonzi mu maso mwanu. Monga nthawi imene Natani adalankhula kwa Devedi ndipo Devedi anasweka mtima, Mulungu anatuma Natani—mbale kwa inu ndipo adzanena zauchimo ndipo uzaswa mtima wanu. Mudzalankhula ndi Yesu paizi ndipo ndi kulingalira malembo ena pa izi. Kenaka mudzabweletsa abale pamodzi pa malo amodzi ndi kuwauza m’mene Yesu waphunzitsira inu. Auzeni malemba amene mwawaphunzira amene asintha moyo wanu. Auzeni m’mene munagwera ndi m’mene iwo sangagwelenso. Awonetseni zinthu zimene Mulungu waonetsa kwa inu. Ameneyo ndiye wansembe. Inu ndinu ansembe mungatenge zinthu zimene Mulungu wachita mwa inu ndi kutsegula kwa abale ndi alongo. Mulungu akufuna kuti tidzitero tonse amene. Muli wolora kutero?

Choncho tabwera pamodzi mudzina la Yesu ndikumvetsera. Koma Yesu sakhala chete kwa nthawi ngati zinthu zili chete kwa nthawi yaitali chifukwa ndi choti wina siwansembe wabwino, kapena ndikumvetsera. Koma Yesu sakhala chete kwa nthawi ngati zinthu zili chete kwa nthawi yaitali chifukwa ndi choti wina siwansembe wabwino, kapena Yesu afuna kuti inu mugawe nyimbo ndipo mukuopa. Kapenanso Yesu akufuna kuwelenga malembo amene anali apamtima wanga m’mawa uno, koma ndimaganiza Ai, sindili wabwino konse sindingathe kutero. Kenaka zii, chifukwa Yesu amafuna kugwiritsa ntchito ine koma sindinamulore ndifuna kuti ndikwilire luntha langa ngati Yesu anakakhala pano mu thupi, sanakakhala chete kwa nthawi yaitali chifukwa pali zambiri zimene Yesu amafuna kuti zichitike m’moyo mwathu. Ngati ife tili ansembeabwino, tidzamvera Yesu. Yesu adzagwiritsa ntchito aliyense wa ife. Adzakhala mwa ife kubyalera mw ansembe ake, ngati tili ofuna, muli ofuna kutero? Landilani Yesu agwiritse inu ntchito.

Akufuna kuchita zodabwitsa

Kumbukirani kuti Yesu pamene anapita ku malo ena anafuna kuchita mirakulu kumeneko, koma sanachite chifukwa anthu anali osakhulupira. Muyenera inu kukhulupira mu mtima mwanu kuti Mulungu afuna kukugwiritsirani ntchito. Muyenera kulankhula ndi Yesu pa zinthu izi. Muuzeni iye:Ndimakhulupilira ndithandizeni “kusakhulupirira” funsani iye kuti mukhale ofewa ndi ozichepesa. Funsani Yesu kuti akuthandizeni kuti mulimbike kuona mphatso yanu, funsani Yesu kuchotsa kunyada, chifukwa nthawi zina mudzakhala olakwa. Koma ndizabwino kulakwa ndipo tonse tingathandizane. Ndibwino kulakwa kusiyana ndi kukwirita luso lanu. Ngati mwalakwatsa tikhonza kukhala tonse pamodzi, koma ngati mungakwirire luso lanu. Yesu ali okwiya, ndiye funsani Yesu kuti akuthandizeni inu kuti mukhale wansembe wabwino.

Izi sizofunika kuganiza mozama kapena kulankhura bwino. Izi ndi kufunsa Yesu kuti athandize inu. Iye ndi wamoyo, akufuna kugwira ntchito yodabwitsa mu mitima kuphyola mu mitima ya ena. Koma kwa iye kuti achite mirakuli, tiyenera kukhulupilira, ndiye lankhulani ndi Yesu za zimenezi. Mwangoganiza chabe mu mutu wanu ndi kubvomeleza izo chabe. Malomwake, lankhulani ndi Yesu wa moyo pa zinthu izi ndipo adzatithandiza ife tonse, ku ulemerero wake.

Afunseni kuti akhale Ansembe

Pamene muli ansembe kwa abale anu mungathenso kuwathandiza kuphunzira kudziwa Yesu ngati ali kumbali ya chipembedzo kwina kake, apempheni kuti akhale ansembe kumene akhalako, Apempheni kugwilitsa mphatso kwa anthu amene azungulira. Asangopita ku misonkhano kwawo kukamvera chabe. Funsani iwo kuti ayang’ane kuti ayang’anire miyoyo ya zongulira iwo ndikuwathandiza kuti akhale monga Yesu. Ngati wina kulikonse achita izi. dziko lizasintha. Zimenezi ndi zamphamvu—chifukwa ndalora kuti Yesu akhale Yesu. Ngati sindingathe ansembe Yesu amakhala mu botolo kapena mu Bukhu, ngati tili ansembe ndi kufunsa wina aliyense amene abvala Yesu kukhala wa nsembe. Yesu adzaloledwa kuti akhale Yesu PALIPONSE! Midzi yathu idzasintha mizinda yathu idzasintha. Maiko ndi maiko akulu onse adzasinthika ndipo Yesu adzakhala Yesu ngati ndidzakhala ansembe! Amen?

Pamene tinadziwa Yesu zaka khumi zapitazo, taphunzira mopitilira mmene mpingo uli ndi wansembe alili, ndi mmene tingakhalire wansembe. Pamene taphunzira zinthu izi zinatitengera ife kumachitidwe odziwa kuchita ndi chipembedzo. Anthu a chipembedzo si adani athu. Ambiri ali kumeneko chifukwa ndi zimene iwo adazidziwa. Ngati atidziwa Yesu kwambiri adzakondwa kumutsata. Ndiye ndi chofunika kuti tikonde anthu ngakhale a muchipembedzo. Ife tili osamalitsa kuti tisanyade. Pamene Mulungu akupatsa ife opempha monga ife chakudya cha nyenyekwa. Tiyenera kugawa chakudya ndipo osaweluza ena pokhala alibe chakudya. Iyi ndi njira ya Yesu kugawa chakudya chimene wapeleka kw aife—osati tigawikane chifukwa cha chakudya, koma kupeleka chakudya.

Zinthu izi ndi zofunika kwambiri kukhala mu mitima ndi mmaganizo. Sitidzalora kutentha chabe kapena kunyengalera. Koma timakhulupirirra Yesu adzamanga mpingo wake, ndiye pamene tipeza anthu amene akonda Yesu mu zipemphedzo, kapena tisati chaokani, chokani mmalo mwake “mvelani Yesu ndi anthu amene muwadziwa “Timawaphunzitsa njira ya Yesu monga mmene anatiphunzitsira ife. Timawafunsa kuti aphunzitse aliyense amene amudziwa njira ya Yesu. Ngati achita motere mu mipingo adzathamangitsidwa mu chipembedzo anthu ambiri samvera Mulungu ena amamvera, komanso ena ai.

Mu mpingo woona umene Yesu akumanga, ALIYENSE amafuna kumvera Mulungu ndipo ALIYENSE amakonda Yesu. Chifukwa tonse tili ansembe ndipo timathandizana wina ndi mzake ngati wina sakonda Yesu amathawa.

Mu uneneri mu Yeremiya 31 wa mpingo wa chipangano chatsopano ndi oti, “onse adzandidziwa ine kuyambira aong’ono mpakana akulu” mu mpingo woona onse amadziwa Yesu. Mu chipembedzo chimene sichoona ndi mmene muli kutentha chabe.

Anthu amakonda dziko ndipo amakhala mu uchimo ndipo sasintha. Ndi zoipa izi ndi zobvuta kwambiri. Koma plainso anthu abwino mu chipembetso . ntchito yathu sikuti anthu achokeko. Ntchito yathu ndi kuthandiza iwo kukhala ansembe kumalo amene iwo ali. Ngati adzakhala ansembe pamalo amene ali anthu ambiri adzasintha kapena atachotsedwa.

Pamene Yesu ali——————chimo silingakhale

Ngati mbale kapena mlongo afana ndi Yesu ku chipembedzo, kapena chipembedzocho chidzasintha, kapena chidzawapha kapena kuwataya (monga momwe adachitira ndi Yesu) sitikuopa zipembedzo. Ali ngati khoka lalikulu limene lisunga nsomba zosiyana siyana. Pali nsomba zina za bwino mu khoka ndipo zina nsomba zoipa. Ntchito yathu ngati ansembe ndi kuitana nsomba zonse zabwino kuti zikhale ansembe kumene iwo akhalako.

Kodi Neneveh anasintha? Yona analabvulidwa ku kamwa kw ansomba nalowa mu mzinda oipa uja. Uchimo umalipo kumeneko koma mzinda onse anasintha kwa Mulungu ngakhale mfumu. Tiyenera kukhulupirira Mulungu kuti angapange mu chipembedzo. Tikhulupilire kuti angachite izi ku Mzuzu, ndiye ngati tili ndi abwezi kapena anthu amene timadziwa mu chipembedzo, sitimauza kuti achoke, timawauza kuti akhale ngati Yesu ndi mtima wawo yonse kulankhula mau a Mulungu kwa aliyense amene amuone kumeneko, kutaya moyo wawo, kukonda anthu osanyengelera kapena kuopa kunyengeledwa. Anthu a ku Neneve nasintha ndi moyo wathu ku chipembedzo kumene tikhale ansembe ndi kuyesa kusintha. Tidzayensa kuthandiza anthu abwino amene timawadziwa ku chipembedzo ndi kuwafunsa kuti akhale ansembe kume ali kuthandiza anthu owazungulira kusintha.

Timupempha Mulungu ndi misonzi yambiri kuti chipembedzo chisinthe Yesu analira. Anathets amisonzi ndi Yerusalemu. Anati ndinakakusunga iwe monga mmene nkhuku imasungira anapiye ake. Koma Yerusalemu sanafune ndipo anamkana iye—Anamupha. Ngati tili ansembe okhulupilika, adzatipha kapena mzinda wonse udzasintha. Koma tiyenera kukhala ansembe okhulupilika. Tiyenera kufunsa ansembe amene timawadziwa kuti akhale okhulupirika ku malo amene akhala. Ngati adzayese kuthandiza anthu amene amawadziwa, adzakhala olimba kapena kuchotsedwa koma ndiye kuti akhonza kukhala ndi okhulupirira ena amene ali ndi moyo umodzi, titayensa ndi anthu otizungulira ife. Ndizimene wansembe amachita. Tiyenera kukonda amene ali mu chipembedzo. Ndi zimene Yesu anachita. Koma tisalore kunyengedwa. Tiyenera kukhala mu choonadi ndi kufuna mu choonadicho. Ngati aliyense adzatero, pamenepo Yesu adzamanga mpingo wake.

Uwu ndi uthenga wabwino wa Yesu. Tiyenera kukhala njira yotere kwa anthu okhala nawo. Osanyengelera osakhala ozizira—-—koma tiyenera kuwakonda ndi kuthandiza iwo. Pasakhale kusiyana kukhale chifukwa wina safuna kumvera Yesu. Sitidziwa izi mpaka titayesa. Umu ndi mmene tingakhalire ndi chipembedzo. Tiyenera kutaya moyo wathu kwa iwo ndi kuchita chilichonse chimene tingapeleke mkate wa moyo ndi kufunsa iwo kuchita ndi anthu amene amawadziwa ndiye tiona ndi kuyang’anira chimene Yesuachite ndi chimenecho. Yesu anati ngati tidzachita mbali yathu. Iye adzamanga mpingo wake ndi makomo a ndende ya mtima sidzaima. Tikhononga mzinda wa Satana kuphwasula ndi kuwononga makomo onse. Timakonda anthu ndi kuwabweletsa kuchokera ku Mtima ndi ku kuwala. Sitikusiyana pa maina koma tikonda anthu—mphaka ku imfa. Timachita ntchito yawa nsembe ndipo Ambuye adzamanga mpingo wake.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon