Yesu Yekha Ndiye Bwana

4/8/2003

Mlowe, Africa 1996

Chimene chipanga Mtsogoleri?

Pali mitundu iwiri ya atsogoleri, wina ndi mtsogoleri ochokera mu mtima, kuchokera mu mulumikizo ndi Mulungu wina ndi mtsogoleri wa undindo ndi mpando ndi olemekezeka “wamkulu” Bwana olemekezeka, Yesu anati mtsogoleri utero asakhalepo. Atsogoleri a mpingo ndi amene akuyenda ndi pafupi ndi Mulungu LERO ngati mbale kapena mlongo sakuyenda pafupi ndi Mulungu lero, sayenera kuganiziridwa kukhala mtsogoleri. Ngati munthu sabata yatha samayenda ndi Mulungu koma walapa pa machimo a mu moyo ndipo akumva Mulungu, ndipo ali mtsogoleri lero koposa sabata yatha. Kukhala mtsogoleri zimachokera ubale ndi Mulungu ndi anthu a Mulungu sizichokera pa ofesi kapena undindo.1

Tili ndi atsogoleri kumene ine ndimakhala, koma kulibe “maofesara” mtsogoleri lero koma sabata in ai. Yesu anati ulamuliro yonse m’mwamba ndi pansi pano uli PAINE. Zimenezi ndi zoona, choncho, m’mene tingamvere Yesu, amene ali ndi, amene ali ndi ulamuliro. Ndi m’menenso ali ndi ulamuliro nawo—pamene akwanitsa kumva Yesu, ndi choncho. Ulamuliro wonse “kumwamba ndi pansi pano” uli pa Yesu. Iye anati munthu amene sadziwa Yesu angakhale ngati choyelekeza chabe. Munthu ameneyu amafuna adziopedwa pamene afuna zitero, ngati ali ndi mpando koma ali mtsogoleri ngati amadziwa, kukonda, ndi kumvera mutu Yesu.

Kubadwa kuchokera mu Ulesi

Pali mayambidwe ochokera mu ulesi mwa ife zimene zimapangitsa ife kubisala pansi pa nthaka ndi kulora wina atimenyere nkhondo ndi zimene akulu ndi opanda undindo zinayambira. Poyambilira pomwe mu mbiri ya mpingo kumbuyo ndithu zaka zikwi ziwiri zapitazo zaka 1800 zapitazo anthu anayamba kufuna mfumu kuti adzawalamulira. Anafuna kuti “munthu oyera” akhala mtsogoleri wa mpingo.

Mwina munthuyo analidi pafupi ndi Mulungu koma mmalo mufuna kuti aliyense akhale wansembe. Anthu a Mulungu anafuna kukhala ndi munthu mmodzi woyera kuti adzimenyera nkhondo. Anafuna kutenga munthu mmodzi ndi kumuika kukhala “mfumu wa mpingo”

Munthuyo mwina anali wabwino. Bvuto siloti munthuyu anali pa ubwenzi ndi Mulungu. Mwina munthuyu anali ndi mphamvu ndi mphatso, koma pamene ayikidwa padela monga ya padera ndikutchedwa “bwana wa mpingo” Pamanepo pali bvuto malo amenewo ndi a Yesu yekha Yesu ndi bwana wa mpingo woona. “Abusa sayenera kukhala bwana wa mpingo palibe mabwana koma Yesu.

Pali chitsanzo m’Baibulo cha mautsogoleri awiri amenewa. Samueli ndi Sauli onse adali atsogoleri a anthu a Mulungu, Israeli. Samueli adali munthu wa Mulungu amene adali ndi chikoka mu fuko chifukwa amadziwa Mulungu. Samueli adali ndi zothekera zambiri zaufumu ku Israeli—koma Samueli sadali mfumu! Komabe, Sauli adatchedwa mfumu. Israeli imafuna kukhala ndi mfumu—amafuna kukhala ndi munthu modzi kukhala bwana. Amafuna wina kuti alowe mmalo mwa Samueli ndipo amafuna “mfumu” monga mafuko onse owazungulira. Munjira ina utsogoleriwu ukhonza kuwoneka mofanafana, koma Samueli alibe “mpando” wa ulamuliro. Samueli amagwira ntchito kuchokera paubale wake ndi Mulungu, ndipo Sauli amagwira ntchito kuchokera pampando wake. Samueli adalibe ofesi, mlembi kapena malipiro (salare). Iye sadali muudindo wa mpando ngati mfumu. Samueli adali chabe munthu wa Mulungu amene amalemekezedwa ngati mfumu koma adalibe mpando kapena ofesi. Iye sadali mfumu iye sadali “mbusa”. Iye amangokonda Mulungu ndi mtima wake onse.

Ndipo chifukwa choti amamvera Mulungu, adali ndi chikoka. Adalibe mpando adali ndi chikoka. Ngati munthu moonadi adziwa Mulungu, adzathandiza anthu a Mulungu. Ngati wayitanidwa ndi Mulungu, adzakhala akuthandizila anthu. Ndibwerezanso: Munthu wa Mulungu oona alibe mpando… ali ndi chikoka. Yobtu 29, ikulongosola za munthu olemekezedwa ndi Mulungu ndi anthu, ndi woopedwa ndi odedwa ndi satana. Munthu otere safuna ofesi kapena dzina kapena malipiro. Ngati muli ngati Yesu, simudzafuna “mphamvu.”

Monga mwachitsanzo, ngati ndili m’misili, ndi mapanga zinthu ndi matabwa. Ndimapanga mpando, tebulo kapena chitseko kuchokera ku matabwa. Ngati ndili omanga, ndiye kuti ndimanga zinthu ndi njerwa. Chinachake chomwe ndipanga kuchokera ku njerwa ndi umboni oti ndine omanga. China chake dzomwe ndipanga kuchokera kuthabwa ndi umboni oti ndine m’misili. Tsopano, mu Baibulo mau awa “mbusa” (kutathauza kolakwika) koma atanthauzira kuti mphatso ya ubusa wa nkhosa, ogwira ntchito tsiku ndi tsiku pakati pa anthu a Mulungu moyendezana (mwapambali) pa mphatso zina—osati bwana kapena “olankhula wamkulu” pamsonkhano. Kodi umboni uli pati kuti ndine Mbusa weniweni? Umboni ndi wakuti ine ndimakonda anthu a Mulungu! Ndimawathandiza iwo usana ndi utsiku. Sindifuna dzina, sindifuna kukhala bwana. Ndimangokonda anthu ndi mphatso yomwe ndili nayoyi, ndikuwathandiza. Umboni waumusili ndi mpando omwe ndapanga umboni woti ndine Mbusa weniweni ndi woti ndimadyetsa anthu a Mulungu tsiku ndi tsiku, ndipo ali chifupi ndi Yesu chifukwa cha ine. Ngati ndiwona kuti m’modzi mwa anthu a Mulungu ali ndi njala, chimandiswa mtima. Ngati ndiwona kuti m’modzi mwa anthu a Mulungu ali muvuto kapena muzoopsa, mtima waubusa mkati mwanga uthamangira iwo kukawateteza. Uwu ndiye umboni oti ndine odzodzedwa wa Mulungu kukhala m’busa. Sindifuna mayina opatsidwa. Sindifuna chitupa chopachika pakhomo ndi chochokera ku Sukulu ya Baibulo. Ndifunitsa mtima okonda ndi kuchita ntchito ya Mulungu, ndipo kenako ndizabala zipatso zauzimu mumbali iliyonse yomwe iye azandipatsa ine.

Tsono, ndinu m’misili? Ndiye pangani mpando. Muli ndi mphatso ya ubusa. Ndiye kondani anthu—adyetseni, atetezeni ndipo athandizeni. Ichi ndi choona pa mphatso iliyonse! Umboni wa mphatso iliyonse uli mudzipatso zimene umabereka.

Zotsutsana za zonsezi ndi zoonanso ndithu. Ndifundo yodabwitsa kuti amafano mu sayansi ndi mankhwala ndi malonda amalamula kuti amene ali ndi maganizo ndi mtsutso ndi odzitcha okha “akatswiri” ali ndi china choti awonetse, zipatso mumiyoyo yawo, awonekera kuti ali dni ufulu wolamulira, kuphunzitsa kapena kutsutsa ena. Mudziko lachipembedzo, modabwitsa, ali ndi ungiro ochepa kuposa ngakhale zimene amafano amaonetsera. Muchipembedzo, ngakhale, anthu ali akhungu ndi wozunguzidwa kwambiri.

Mtsutso, ukatswiri, zigamulo, ndi ngakhale ubale ndi zonyoza zimayenda mophweka kuchokera kwa iwo azipatso zoyipa miyoyo yawo, m’mabanja ndi m’mabwalo awo. Zodabwitsa, koma zoona ngati inu muona chipembedzo chamunthu mosamalitsa ndi moona. Munthu amene amapanga zinthu zotere ngati bodza kapena m’nyozo kapena kukhala ngati katswiri pa njiniaring’I, zamakhwala kapena malonda akhonza kusonkhanitsa pamodzi gulu lomvera mpphweka anthu akuopa, m’mene akhonza kunderedwa pansi, kapena kuyamikiridwa mpusitsa ku—kuzipereka ku makina osabereka zipatso ndi “akatswiri” zonga zamisala koma ndi zoona. Zimachitika kunthawi zonse, chifukwa umu ndi m’mene maufumu a vuto amasungira nambala yao. Mantha ndi kuyimikira kopusitsa, mjedo, m’nyozo kapena kuyenderedwa pansi. Nchifukwa chake ziri zosadabwitsa kuti Yesu sanapange bwino mu chipembedzo chovomerezedwa kudziko lapansi cha munthawi yake. Koma, likhonza kuphunzira kwa iye ndi kusunga malembo, ndi kuyang’ana zipatso, osati kumvera—kunena kwa mfundo ndi mabanjeti, ndiponso kunena kufuna kwa yenkha kwa munthu kuti ateteze.

Pamenepo mwatengapo mfundo.: )

“Mwandikana ine”!

Izi ndi zoona kwa mphatso iliyonse koma anthu aononga kwambiri chi Kristo pofuna kukhala ndi mfumu Samuel sanali mfumu, anali munthu wa Mulungu. Sauli anali mfumu ndipo anaononga anthu a Mulungu. Mulungu anati “sanakukane iwe, Samuel, Akana Mulungu. Samueli anali wa chikoka chifukwa amadziwa Mulungu, sichifukwa choti anali pa udindo wa Ufumu.

Ndipo iwo anatengera, sanatengere? Wina wochokera dziko lina amanena akafika ku Israel, muli ndi mfumu! ‘Samueli ndi mfumu yanu”! A Israel amati “inde” tikudziwa akuoneka ngati mfumu, chifukwa ali otamandika ndi opatsidwa ulemu koma Sali mfumu. Tilibe mfumu ife, tilibe mfumu koma Mulungu. Samueli amadziwa Mulungu bwino, ndiye tikupatsa ulemu ndi kumukonda. Maiko ena maganiza kuti a Israel anali ndi mfumu, mfumu Samueli koma sanali mfumu anali munthu wa Mulungu. Analibe mpando. Mapita pano ndi uko kenako osaonekanso, ndi kubwelanso. Mafumu sapangaz zimenezo. Amuna a Mulungu amatero. A Israeli anafuna kuika wina mmalo mwa Samuel pamene anakalamba anafuna kukhala ndi Mfumu monga maiko ena onse (kapena monga zipembedo zina).

Pamene tifuna munthu wina kukhala bwana wa ife kuti atimenyere nkhondo, ndiye takana Mulungu 1 Samueli 18:7 “sanakane iwe, Samueli, andikana ine” tisayese kukhala ndi anthu okhala bwana. Tiyenera kuwakonda ma Samuel pakati pathu amene adziwa Mulungu, talemekeze ndi kuwamvera, pamene sakukhala ndi udindo kapena bwana kupatula Yesu yekha basi, timvere Yesu, kulankhula mwa Samueli, Lolani Samueli woyamba akhale pansi. Izi ndi zabwino.

Zotsatira zake

Ndikufuna kuti mumve zimene inu ngati mukhala ndi mfumu. Pamene mufuna kukhala ndi “Bwana wanu” Bwana wa mpingo. Izi ndi chipatso zochokera mwa izo

“Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweluza idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magaleta ndi akavalo ake ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake adzawaika akhale atsogoleri zikwi ndi atsogoleri makumi asanu ndipo adzaika ena ndi kulima minda ndi kutema zinthu zake ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magareta ndipo adzatenga ana anu akanzi apange zonunkhira naphikire naumbe mikate ndipo adzalanda minda yanu ndi minda ya mphesa yanu ndi minda ya azitona inde minda yoposayo, nadzaipatsa anyamata ake ndipo adzatenga limodzi la mayawo khumi la mbeu zanu ndi minda yanu ya mphesa nazaipatsa akapitawo ake ndi anyamata ake. Ndipo adzatenga akaporo, ndi azakazi anu ndi anyamata anu okongola koposa ndi abale anu nidzagwiritsa ntchito zake. Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu ndipo inu mudzakhala akaporo ake, ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha, koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo. Koma anthu anakana kumvera mau a Samueli nati Iai, koma tikufuna kukhala nayo mfumu yathu kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse kuti mfumu yathuyo ikatiweluzire ndi kutuluka kutitsogolera ndi kuponya nafe nkhondo zathu. (1 Samueli 8:11 —20)

Pamene tifuna mfumu atilamulire, pamene tifuna olemekezeka bwana mu mpingo, iye adzaba masomphenya adzaba ana athu ndi ndalama zathu ndipo tidzakhala ife otigwilitsa ntchito chabe. Zinthu izi sizabwino koma zikuchitika mu dziko lonse la chipembedzo. Kumaiko ena onse amene tapitako pamene pali bwana ndi munthu wamba, pamene pali anthu osiyana akristo. Bwana ndi munthu wamba—mitima ya anthu ndi mphatso sizimagwira ntchito. Mphatso ya chifundo ndi mphatso ya kuthandiza imachotsedwa pamene munthu mmodzi ali mtsogoleri otere osati Yesu kukhala bwana, mitima ya anthu imabedwa.

Anthu a Mulungu anali opeza bwino mu ulamuliro wa Samuel iye sanali ndi udindo, anali ndi mphatso zinali ngati zophweka kusintha kuchoka kwa Samueli kupita kwa Sauli chifukwa amaoneka ngati onse ndi mfumu. Koma ina inali mphatso ndi ina udindo, pamene pali mphatso, Anthu a Mulungu amalemera. Pamene pali udindo olamulira anthu, anthu a Mulungu amabvutika, molingana ndi mau a Mulungu. Mulungu angagwiritsidwe ntchito pa zabwino zokha. Devedi anali mfumu yabwino. Zinthu zina zabwino zingaoneke ngakhale kuti njira ndi yoipa. Koma Mulungu anati “Ndili nayo njira yabwino” njirawo ndi Samueli, osati Sauli, iye anati, Ndingachite zinthu zina zabwino ngati mukhala ndi mfumu, koma pamene mabvuto abwera mudzalira kwa ine ndipo ine sindidzayankha” Izi ndi zimene zikuchitika mu chipembedzo, chifukwa amamanga pa mphatso ya munthu kukhala mfumu. Sauli ndipo analoledwa kumuika kukhala mfumu.

Zinthu zina zabwino zikhonza kuchitika koma mu tsiku la zowawa adzalira kwa Mulungu ndipo sadzamvera iwo, ndipo zinthu zidzataikilana. Padzakhala ndale ndi mphamvu kuchitidwa ndipo padzakhala miseche ndi zamwano ndipo matemberero onse adzakhala amene Mulungu anawanena. Pamene Mulungu angathe kuchita zinthu zambiri mu zochita zilizonse. Timafuna zabwino zokha. Sizabwino zimenezi? Mulungu angadalitse chilichonse mu chifundo chabe kukoma mtima ndi kupilira. Koma tiyeni timange kuti tilandire madalitso ambiri! Tikhale ndi ma Samueli pakati pathu mmalo mwa Sauli m’modzi. AMEN?

Chinanso chimene chachitika ndi choti munthu kupita ku seminare kukatenga chizindikiro cha chipemphetso, angakhale kuti mtima ungakhale wabwino amakakamizidwa ndi udindo kukhala zimene iye saali. Angakhale ndi mabvuto nyumba mwake, ndi ukwati ndi ana ake ndi ogona nawo limodzi ndi makolo mwachoncho, chifukwa ali ndi udindo wa chipembedzo anthu amayankhana kwa iye, mmalo mokhala mbale pakati pa abale. Amachita zinthu zina munjira ina kusiyana ndi mmene amachitira kunyumba, monga kuyenera kukhala mbale pakati pa abale. Pali zina zimene zili mkato mwa ife zimene zimapangitsa ife kusafunsa moyo wa Bwana. Pamenepo atsogoleri mu mpingo asafune maudindo zimene zingaimitse zinthu zothandiza ena mu moyo wawo.

1. Mau oti ofesi amathandauza ngati ndi olemekezeka” okhalapo chilichose chokhalapo pa anthu a Mulungu kaya mu nyumba kapena munthu odziwika.

 

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon