Mzimu Wotengeka Tengeka

2003

September 1996, Mzuzu, Africa.

Malingaliro amene m’bale adagawana ndi oyera mtima mmawa wa tsiku lina pamene tidali pamodzi ku Africa.

Nditangotsegula maso anga mmawa walero. Ine ndidatsegula Baibulo langanso. Ndime yoyamba imene maso anga adaona idali ndi mau okhudzana ndi mnthunzi wa imfa, chimodzimodzi monga Masalimo 23:1 sindikadaganiza kuti ndionetsera ichi kwa inu, kupatula poti ena mwamau amenewo adali ofanana, ndipo mau oyambirira eni eniwo maso anga adaona mmawa uno adandibweretsera chikondwerero.

Kukhala Pamene Mthunzi Siungatikhudze ife

“Ngakhalebe, sipadzakhalanso zowona kwa iwo amene akhala ali m’mavuto.”

Mulungu adzachotsa zonse za zowawa ndi mavuto athu. Iye adzatsuka chikayiko chathu. Ili ndilo lonjezano lake. “Anthu akuyenda mumdima awona kuwala kwakukulu. Pa iwo akukhala mudziko la chigwa chanthunzi wa infa, kuunika kwakukulu kwaoneka.” (Yesaya 9:1-2).

Ndime iyi imapitirira kuyankhula za m’mene Mulungu adzakulitsire mitima yathu. Iye adzachulukitsa chimwemwe chathu. Iye adzatipanga ife kuti tisangalare ngati anthu akusangalalira zokolola. Iye adzatuta zothodwa zimene zili pa ife. Iye adzachotsa chitonzo zhakugonjetsedwa kwathu. Ndipo apa pali m’mene iye adzapangire, “pakuti kwa ife Mwana wamwamuna wapatsidwa, ndipo ulamuliro uzakhala pa phewa pache, ndipo adzamucha dzina lace wodabwitsa, wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate wosatha, kalonga wa Mtendere.” (Yesaya 9:6-7)

Ulamuliro wace ndi za Mtendere sizidzatha. Pa mpandowacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikitsa, ndi kuucirikiriza ndi ciweluzo ndi cilungzmo kuyambira tsopano ndi ka nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.

Dzina lake ndi Yesu: Immanueli, Mulungu ali nafe. Yesu adzabweretsa chimwemwe chachikulu. Iye adzatsuka zowawa ndipo kuunika kudzafika m’mitima mwathu. Mtima ndi malingaliro ndi mphamvu za Mulungu wamphamvu. Zonse adzakwaniritsa ichi. Anthu akuyenda mumdima (amenewo ndi fe) adzaona kuunika kwakukulu. Mlangizi wodabwitsa iye adzatithandiza ife mumayesero athu onse. Pamene tiyenda muchigwa cha mthunzi wa imfa, ife timvetsetsa kuti mthunzi siungatipweteke ife. Ndi mthunzi wa imfa chabe. Kodi mukudziwa chimene chimathamangitsa mthunzi? Kuunika kwakukulu kudzathamangitsa mthunzi uliwonse. Yesu, M’busa wathu wabwino, adzathamangitsa mithunzi yonse ya imfa m’miyoyo yathu. Nthawi zina ife timayesayesa kufufuza yankho kuchoka mmitu yathu, pamene chimene tikufunika kwenikweni kuti ife tipange ndi kutembenuza nkhope zathu kwa Yesu. Iye adzatimva kulira kwa mitima yathu ndipo adzaonjeza chimwemwe chathu, kubweretsa kuunika kwakukulu ku mitima yathu. Kwa ifde mwana watibadwira, mwana wapatsidwa ndi adzatithandiza ife ngati titembenuzira nkhope zathu kwa iye.

“Nchachikulu bwanji chikondi cha Atate chimene chidagwera pa ife, kuti ife titchedwe ana a Mulungu, pakuti ichi ndicho chimene tili! Ife tikhonza opanda nthumazi ndipo opanda manyazi pamaso pake pa kubwera kwake.” (1 Yohane 3:1,2:28) mu chiyankhulo cha chi Greek, chimanena kuti “Taonani ichi ndipo dabwani zachikondi chodabwitsa chimene Mulungu ali nacho pa ife. ichi ndi chionetsero cha “kutsegula maso athu ndi kuona mmene ukulu wa chikondi chake ulili.

Pali nyimbo yina imene nthawi zina timayimba. Imayankhula za mmene tiliri oposa agonjetsi.

Ife tili anthu a Mulungu, otchedwa ndi dzina lake.

Oyitanidwa kuchokera kumdima ndi

omasulidwa kuchoka kumnyozo

Fuko limodzi loyera—oyera mtima aliyense.

Chifukwa cha Mwazi wa Khristu, Yesu Mwana

Ndi milomo yathu tiyeni tiyimbe kuvomereza kumodzi.

Ndi mitima yathu tigwire choonadi chimodzi chokha.

Pakuti iye wafafaniza machimo athu

Watilanda ife ndipo watitcha ife ake.

Ake omwe enieni.

Timveni ife, mizimu ya kumidima

Tsono inu mudzadzidwa pamene tiyima

Ife tili anthu ake, ogulidwa ndi zipyera

Ogulira ndi mwazi wa mwana wa Nkosa.

Mwaza wa Mwana wa Nkhosa

Ichi ndi chifukwa chake pali chiyembekezo chachikulu pa tonse a ife. Ichi ndi chifukwa satana adzalephera, ndipo ichi ndichifukwa chake tili oposa agonjetsi: ife tidagulidwa ndi mwazi wa Mwana wa Nkhosa! Tsono ndi mitima yathu tiyimbe chivomerezo chimodzi. Ife tigwiritse ku choonadi chimodzi chokha. Chifukwa Yesu wathu wagonjetsa tchimo ndipo wagonjetsa imfa, satana ali ngati galu opanda mano. Yesu watikonda ife ndipo watipanga ife Ake, Ake enieni.

Ntahwi zina tiyenera kudzikumbutsa tokha za choonadi ichi. Ndi chovuta kukhala ndi tsiku pamene ife tikumbuka zinthu izi. ife tili opsa agonjetsi kudzera mwa mwana wa chikondi cha Atate.

Kutengeka ndi Zochitika

Pali njira yomutsatira Yesu imene ili yokhazikika pa momvedwe a matupi athu. Pamene mamvekedwe a matupi athu ali bwino, ife timamkonda Yesu, ife timasangalala, ndipo ife timayimba. Koma pamene ife sitimva bwino, ife sitiyimba nyimbo ndipo sitimpembedza iye. Ine ndikuganiza kuti anthu ambiri apamanga mu ubwino. Iwo amakhala ali ndi cholinga chabwino. Koma pali njira yomtsatira Yesu imene ili yamphamvu kwambiri ndipo imene siyiyelekezera kukhala yauzimu. Palinso njira ina imene ili yosakhudzikika. Ine sindikuthandauza chilichonse choipa. Ine ndingoganiza kuti nthawi zina ife sitimvetsetsa njira yeniyeni yomtsatira Yesu. Njira yeniyeni siyiyendera mmene ife tikumvera matupi mwathu. Pamene ife tikuyankhula za uzimu oyendera mamvekedwe amthupi, ife sitikutanthauza kuti wina ali ndi malingaliro oyipa kapena zolinga zoyipa. Mwina iwo sadaone nkhope ya Yesu munjira yamphamvu imene iwo tsiku lina adzayiona.

Moyo Wa Yobu

Ife tawerenga kuti Yobu adali munthu olungama kwambiri pa dziko lonse lapansi. Kuchokera mwa anthu mazikwi ndi ngakhale miyanda, Yobu adakonda Mulungu koposa wina aliyense wa anthuwa. Yobu adamvera Mulungu koposaonse mwa anthu apadziko lapansi, ndipo komabe padali njira yokuya imene iye sadamudziwire Mulungube.

Padali zinthu zambiri zoipa zimene zidamuchitikira Yobu. Iye adali ndi kuwawa mtima kwambiri ndi kuwawa kwambiri. Thanzi lake lidapitiratu. Ana ake apamwamba adafa, Chuma chake chidatengedwa.

Mkazi wake adamuuza kuti atukwane Mulungu ndipo afe. Iye adasiya osapitiriza kumkakamiza kutero. Ndipo tsono mtima wa Yobu udasweka kudzamuyendera iye, ndipo ndikhulupirira iye anthu amenewo amamkondadi Yobu. Iwo adasiya mabanja awo ndipo adakhala ndi Yobu kwamasiku asanu ndi awiri mu chete watunthu. Ndikhulupirira kuti iwo amamkonda Yobu ndipo iwo amatanthauza ubwino. Koma iwo sadamudziwe Mulungu bwino lomwe. Iwo adanena zodabwitsa zambiri, zinthu za uzimu kwa Yobu zokhudza mmene munthu wabwino amapezera zinthu zabwino nthawi zonse. Yobu adadziwa izi sizidali zoona. Iye adaonapo zoyipa zikuchitika kwa anthu abwino ndipo zabwino zikuchitiks kwa anthu oyipa. Tsono iye sadadzilandire zinthu zimene anzake amanena kwa iye.

Munjira imodzi Yobu adali ndi uzimu oyendera mamvekedwe a thupi chifukwa iye sadalore Mulungu kupanga ntchito yakuya mu mtima mwake. Iye adali okondwa kwambiri ndi mmene amamudziwira Mulungu. Iye adadziyesa yekha munthu wabwino kwambiri. Chifukwa iye adali chifupi ndi Mulungu kuposa munthu wina aliyense, iye amaganiza kuti ali chifupi kwambiri ndi Mulungu. Iye sadazindikire kuti tsamba la udzu liri pafupi ndi dzuwa kuposa nyerere. Mtengo uli pafupi ndi dzuwa kuposa tsamba la udzu. Komabe mtengo ulibe kutali kwambiri ndi dzuwa. Mtengo ndi wautali kuposa tsamba la udzu, komabe ukadalibe waung’ono kwambiri. Yobu sadamvetsetse phunziro ili. Iye adadziwa kuti iye adali chifupi ndi Mulungu maganizo a mmene iye adaliri kutali ndi Mulungube. Mtima wake sudali osweka za m’mene iye adaliri kutali ndi Mulungu. Chidatengera kuwawa kwakukulu kumeneku ndi kuonongeka kwa zinthu zonse za Yobu, munthu olungama kwambiri pa onse apadziko lapansi, kuti amvetsetse zinthu izi………….. atatha kudutsa mzowawa zimenezi, iye adati. “makutu anga amva za inu, koma tsopano ine ndikhonza kuona chimene inu muli chenicheni.” (Yobu 42:5) Yobu, munjira zina adali wa uzimu oyendera mamvedwe athupi. Yobu amapanga izi muubwino ndipo iye adali munthu wabwino. Iye sadali kunamizira kapena kuyesezera koma iye adali kutali ndi chimene Mulungu ali chenicheni.

Ngati Yobu adali wa uzimu oyendera mamvekedwe a thupi, ine ndikhonza kunena kuti tonse aife tilinso chincho. Ndi zoona ndi anthu ena amene amangomizira ukhristu. Iwo amangoyesezera chabe. Iwo amapanga nkhope zawo zioneke za uzimu. Iwo amafuna kusangalatsa anthu awaone iwo akukonda Mulungu. Koma ife kodi, mukupusa kwithu ndi kusatetezedwa kwithu ndi kunyada ndiponso kusakhwima kwithu, nthawi zina sitigweramo mu zinthu zonga zimenezi? Ichi ndicho uzimu uyendera mamvekedwe athupi. Koma pali njira yeniyeni yamukondera Yesu imene imabwera kuchokera mkudzichepesa kwakukulu, ndipo ilibe nazo ntchito kapena kusamala ngati wina akuyang’ana kapena ayi. Imachokera mu mtima. Uzimu weniweni umachokera kukusweka mtima pamaso pa Mulungu. Imachokera mu kugwa m’chikondi ndi Mulungu amene amakhululukira machimo athu. Mwina chinthu chenicheni chikhala ndi maonetsera a pankhope nachonso! Koma chimachokera mukusweka mtima osati kuchokera mmkudzionetsera. Njira yabwino yothanirana ndi uzimu oyendera mamvekedwe a thupi kuchokera mmitima yathu ndi kudzichepetsa ife tokha pamaso pa Mulungu ndi kumufunsa iye kuti atiphunzitse ife. Kumufunsa iye kuti sule ife ndi moto, kuti ife tikhonza kulira ngati Yobu, “ngakhale inu mwandilasa ine, ine ndidzakhulupirita inu!”

Vuto la uzimu oyendera mamvekedwe a thupi sioti kuti tikungoyesezera kwenikweni, koma kuti ife sitidadziwebe ntchito yakuya imene Mulungu agwira mmitima yathu, monga iye afunira. Ndi chifunika kuti ife tisaweruzane wina ndi mnzake, koma koposa kuti ife tithandizane wina ndi mnzake, koma koposa kuti ife tithandizane wina ndi mnzake kudziwa Mulungu oona. Ife tidziyike tokha pamaso pa Mulungu oona ndi kusiya iye atiotche ndi moto wake monga njira yomwe adachitira ndi Yobu. Padzakhala tsiku lakukondwa ngati ife tidziyika tokha pamaso pa Mulungu ndi kusiya iye awotche ife. Padzabwera tsiku la kukondwa ndi mphamvu. Ili lidzakhala tsiku lenileni kuchokera mkati mwakuya—osati kuti tisangalatse wina aliyense kapena kuti tidzipanga tokha kumva bwino, koma chifukwa ife taona nkhope ya Mulungu ndi mzimu wathu.

Mpingo ndi gulu la anthu amene amayenda dzanja ndi dzanja wina ndi mnzake mu chigonjetso ndi muzawawa kuti athandizane wina ndi mnzake kukhala enieni. Ndizoona mtengo uli chifupi ndi dzuwa kuposa tsamba la udzu, koma tilibe ndi ntunda waukulu ati tiyende. Mulungu adati kwa Yobu, “Kodi udali kuti pamene ine ndinkayika madziko a dziko lapansi? Kodi udali kuti pamene ndinkalamula nyanja m’mene zingapitile muukulu wake? Kodi udali kuti pamene ine ndinkalamulira kutuluka ndi kulowa kwa dzuwa? Kodi udali kuti pamene ndinkapereka kwa nyenyezi iliyonse ya mlengalenga dzina? Ndipo kodi ukuganiza kuti iwe umadziwa mmene ungandipembezere ine? Ndipo iwe uganiza kuti dzuwa kundimvera ine? Khala chete: ine ndikuphunzitsa iwe.” Ngati ife tili ndi mtima umene udzazipereka kumoto wa Mulungu, iye adzatiphunzitsa ife kudziwa, iye mu mtima wake. Ichi chimabwera ndi zowawa koma ndi chabwino kwambiri. Kodi aliyense akhonza kuyenda ulendo ndi ife?

Funso

Tsono, kodi mmapanga chiyani pamene pali nyengo patsogolo pa inu imene inu mumaona china chake chimene mumadziwa chiyenera kukhala munjira ina yake, koma chilichonse mkati mwanu chikukuwa, “ichi sichili choncho!” kodi inu mumasintha mtima wanu ndi malingaliro anu bwanji kuti mukhale munzere umodzi ndi chimene mudziwacho? Mtima wanu ndi mamvekedwe athupi lanu ali njira imodzi, koma inu mukudziwa kuti ichi sinjira imene chiyenera kukhalira. Kodi inu mumalimbana nacho bwanji ndi chikhulupiriro kuti chisinthe?

Kodi alipo wina aliyense amene adaonapo nkhondo iyi mkati mwake? Paulo adati kwa Agalatiya kuti mzimu ndi thupi zimenyana nkhondo wina ndi mnzake. Ife tiyenera kuyembekezera kuti pazakhala nkhondo mu mitima ndi malingaliro athu. Tsiku limeneli silidzabwera pamene pali nkhondo mu mitima ndi malingaliro athu. Koma Mulungu wapereka kwa ife zida za uzimu kuti togwetse zimphamvu izi. Mulungu siamapanga adani kuti athawe. Adani Mulungu amatulutsa anthu aku Iguputo kudzera mchipululu kupita ku dziko la malonjezano, padali zimphona ndi zida m’dzikolo. Kodi ichi chikumveka ngati malo a malonjezano? Kodi ichi chikumveka ngati malo osangalatsa kukhalamo————-—ndi zimphona zazikulu zamkwiyo? Koma ichi chinthu cha padera chimene Mulungu anachita. Iye amalibweretsa mu dziko lamkaka ndi uchi limene liri ndi zimphona zambiri. Kudabwitsa kw amalo amene Mulungu afuna atipatse ife, chimodzimodzi ukulu ndi ukali wa zimphona za mkatimo. Mulungu amapanga ichi ndi cholinga. Iye amapanga ichi kuti atipanga ichi ndi cholinga. Iye amapanga ichi kuti atipange ife tikhale olimba. Chifukwa iye ali ndi zinthu zapadera zotipatsa ife, iyenso amalipa ife zimphona zazikulu kuti zilimbane nafe.

Mu Yakobo 1, mmanena kuti Mulungu iye yekha amapereka mayesero kuti ife tikhonze kukula mu kupirira ndi mphamvu. Ngati ife tikula mu mphamvu kenaka tikula mu kukhwima ndi ntunthu.

Yakobo 1:2-8: “muchiyese cimwemwe cokha abale anga m’mene mukugwa mumayesero a mitundu mitundu; pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro. Koma cipiriro cikhale nayo ntchito yao ndi opanda cirema. Osasowa kanthu konse.

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru apemphe kwa Mulungu amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza. Ndipo adzamupatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro wosakayika konse. Pakuti wokayikakayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zace zonse.

Mu vesi yachiwiri ikunena kuti, “chiyeseni chachikondwerero kuti mukuyesedwa.” Ichi ndi chinsisi cha mphamvu zazikulu za Mzimu Oyera. Ngati mufuna kuona mphamvu za Mulungu mmoyo wanu, muyenera kusankha muchikondwerero pamene zovuta zibwera. Muli ndi chisankho pamene chimphona chidza kwa inu ndi lupanga lalikulu. Inu mukhonza, monga okazonda khumi aja, kunena, “ine ndimadana ndi zimphona ndipo ndili ndi mantha.” Kapena,ngati Yoswa ndi Kalebi mukhonza kunena “Zikomo chifukwa cha zimphona.”

Mulungu wathu adzatipulumutsa ku ziphona. Pamene izo zidzabwera ku moyo wanu ndi kutsutsana ndi inu, inu mukhonza kukhala ndi maganizo oyipa ndi mantha kapena mkwiyo, kapena, inu mukhonza kutenga lupanga la Mzimu, kuthokoza Mulungu chifukwa cha chimphona chimene chitsutsana nanu, ndipo ndikudula mutu wake. Pamene mayesero abwera, ndipo adzabweradi, chiyeseni chachikondwerero. Ndipo ngati inu mudzachiyesa chachikondwerero, mudzakula mu kupilira ndi pamene zimphona zitsutsana nanu, ngati muli ndi chimwemwe, chikhulupiriro ndi kulimbika mtima pakukumana nazo, zipangeni nokha kukhulupirira Mulungu mu mtima wanu kuti mupambane mchigonjetso mudzina la Yesu. Kenako mudzakula mu kupilira ndi chikhulupiriro. Ili ndi lamulo kuti tichiyesa chachimwemwe pamene chimphona chibwera. Ngati inu mukula mu chipiliro mudzakula mu kukhwima. Mudzakula mu ubwenzi ndi Mulungu ndi mu mphamvu ya Mzimu. Ngati mufuna kukula mu chikondi ndi mphamvu ya Mzimu ndiye muyenera kuvomereza nkhondo izi.

Kuthamangira ku Nkhondo

Mulungu amabweretsa, nkhondo izi kuti ife tikhonza kukhala ndi ubale ndi iye. Muli zimphona nthawi zonse mudziko la malonjezano. Monga dzikolo liriri la padera, chimodzi modzi ukulu wa ziphona. Abale, tengani malupanga anu. Alongo tengani malupanga anu ndi kuchiyesa chachimwemwe. Sankhani monga Davide, kuti ngati muzaona dzenje munthaka muli mkango, mudzadumphira mdzenjemo ndikupha mkangowo. Uwu ndiwo mtima wa munthu wamphamvu wa Mulungu. Kuona adani ndi kuthamangira kunkhondo. Davide adathamangira kwa Goliati. Yoswa ndi Kalebi, Mose, Davide, Yesu ndi aliyense wa munthu wa mphamvu wa Mulungu adathamangira ku nkhondo. Iwo adadumphira mdzenje ndi kupha mkango. Ufumu ulowedwa mokakamiza. Yesu adanena kuti kutenga motsophola kw aufumu kudzera mukukakamiza. Mulungu amayika zimphona mu dziko lonjezano chifukwa cha ife. Ndi chabwino bwino ngati izo zili kutitsutsa ife. Khalani akondwa kukhala ndi zimphona zomwe zikufuna kuzipha ife, chifukwa ife tidzawina. Zimphona zitipanga ife kukhala amphamvu ndi okhwima, izo zitipanga ife monga Yesu.

Davide adayenera kutsutsana nao mkango ndi chimbalangondo kuti apulumutse mwana wa nkhosa. Keneko, pamene adakumana ndi Goliyati, iye adali olimba mtima. Chifukwa Davide adali ndi nkhondo yaying’ono ndi mkango ndi chimbalangondo, iye sadali owopa chimphona chotchedwa Goliati ndipo adali ndi kuthekera kuchipha icho. Davide adali nako kuthekera kupulumutsa anthu a Mulungu, chifukwa tsopano adali ndi kulimbika mtima. Ichi ndi chifukwa chake Yakobo akhonza kunena kuti chiyeseni chachimwemwe pamene mukumana ndi nkhondo mu mtima ndi malingaliro anu. Pamene ubale uli ovuta kwambiri nthawi zina, pamene mayesero ali ovuta, pamene m’mimba mwathu muli mwanjala, pamene anthu adana nafe kapena atinyoza ife, pamene ife atichotsa ntchito, kapena pamene mwana afa, zonse mwa izi ndi nkhondo monga mkango ndi chimbalangondo.

Pamene nkhondo izi zibwera mumtima mwathu ndi malingaliro mwathu (ndipo izo zidzabwera) pamene Mulungu ayika chimphona mudziko la malonjezano pa ife, tichiyese chachimwemwe. Khalani okondwa ndi zazimphona. Zimphona izi zidzakuthandizani inu kukhala ndi chipiliro. Zimphona izi zidzakubweretserani watunthu mwa Yesu. Ngati ife tidzatenga malo athu ankhondo ndi kulimbana ndi mdani ameneyu ndi osathawa ndi kukabisala, Mulungu adzagwiritsa ntchito izi kutipanga ife kukhala a ufulu ndi mphamvu. Ife sitili a ufulu ndi mphamvu chifukwa Mulungu amachotsapo mavutowa. Ife tili aufulu ndi mphamvu chifukwa Mulungu amatipanga ife a akulu kuposa mavutowa. Inu muyenera kudziwa izi. iyi ndi nkhani ya Yesu mkati mwa inu. Ife sitifuna ziphona kuti zithawire kutali. Ife tifuna kudumphira mdzenje ndi kudula mutu wa chiphona. Ife sitifuna Goliati kuti adzipita, tifuna iye athamangire kwa ife kuti ife timuphe iye. Ife sitikuyesa kupewa nkhondo. Ife tigonjetsa pa nkhondoyi chifukwa ife tikufuna kukhala monga Yesu ndi ufulu mkati, ndi mitima yamphamvu ndi chikondi chakuya.

Inu mukhonza kupanga chibwana ndi pemphero la mgwirizano. Koma ngati mitima yanu ili yachidwi pa Yesu pa nkhondo, inu mudzakhala bwino bwino.

Kuonetsa pa Moyo Wa Paulo

Ife timayankhula poyamba m’mawa uno zokhudza moyo wa Paulo. Paulo adali ndi kukumana ndi Mulungu kwa padera, ndipo Mulungu adatsegula maso ake kuti aone mavumbulutso aakulu ambiri. Yesu adaoneka kwa iye ndipo adamuonetsa iye paradiso. Yesu adamuuza Paulo ziphunzitso zimene munthu sadamvepo kuyambira kale. Tsono ichi chitanthauza kuti Paulo akadakhala ndi moyo wodabwitsa sichoncho? Kodi mukuzindikira, Paulo adakhala mtumwi zaka makumi awiri asanamvetsetse ziphunzitso za mu Akorinto achiwiri 12:8. iye adapempha Mulungu katatu kuti amuchotsere zowawa zake. Mulungu adanena china chake kwa iye chimene chovuta kuchikhulupirira. Monga anzake a Yobu atatu aja, ife tifuna kukhulupirira kuti zoipa sizichitika kwa munthu wabwino. Koma Mulungu ndi wabwino. Ndipo Paulo anati “Chotsani kuwawa kwa ine ndili oputidwa ndi mtenga wa satana.” koma Mulungu anati kwa mtumiki wake Paulo, “chifukwa ndakupatsa zinthu zodabwitsa zambiri ndiye ndiyenera kuti mkati mwa mtima wako umveululu kuti usakhale onyada ndi kunyengedwa ndi zinthu zimene zapatsidwa kwa iwe.

Paulo anali odabwa ndi zimenezi Mulung ananena kuti chifukwa ali kuganiza kuti apemphera ndi kuti ululu wuchoka kwa iye. Mulungu Atate anati kwa Paulo kodi sukumbuka? Kuti mwana wanga anapachikidwa mu kufooka. Yesu anali ndi kuthekera kokhulukira uchimo mu dziko. Izi ndi choncho chifukwa anapachikidwa mu kufooka, osati kuti anali ndi mphamvu, koma chifukwa anali mu kufooka. Osati kuti sanali kumva kuwawa koma kuti ululu unali waukulu. Mmene Mulungu akufunira kuti ulemerero wake uwonekere ndi kuwonetsedwa. Chomwechonso akufuna kuti ife tinyamule imfa mu matupi athu kuti tibweletse moyo kwa anthu ena otizungulira. Pamene Mulungu amatipatsanso mphatso zodabwitsa kuti timutumikire iye. Ayeneranso kupeleka ululu mu mtima mwathu kuti tisakhale ndi kunyada kapena kunamizidwa kuti tidziwe kuti zabwino zonse zimachokera kwa iye .

Sindife eni ake amphatso zimenezi nzeru ndi bvumbulutso sizibwera kwa ife chifukwa ndife abwino. Monga Mulungu anachita ndi Yobu ndi Paulo ndi momwemo anachitira ndi mwana wake Yesu mu Yesaya 53. Anadula miyendo yathu kuchokera pansi pathu. Atate amaononga miyendo yathu ndi kuti tikwanitse kuwelama ndi lkumupembedza iye. Amachita zimenezi kuti atigwilitse ntchito kuti tisakhale wonyada. Pali mbali ya mtengo wake mu 2 Akorinto 12. “Paulo anati chifukwa choti zonse izi ndi za Yesu ndipo zimachititsa iye kukondwa ndiye ndidzakondwera ndi ululu wanga ndipo ndipo tidzakondwera mu kufooka.”

Sindidzakondwanso ndi uchimo koma ululu ndi wabwino chifukwa tikufuna cholinga cha Mulungu kuchokera mu mtima tiyenera kuti timve kupwetekeka mphamvu ya Mulungu imakhala ya ngwiro mu kufooka kwathu. Ngati tidzabvomeleze ululu ndi kulambira iyeyo. Mphamvu yake ya Umulungu idzagwira ntchito mw aife munjira zambiri mbiri modabwitsa. Ndiye timakweza manja athu kwa Mulungu ndi kunena monga Paulo ananena tigawana chiyanjano cha zowawa chake kuti tigawanenso mu mphamvu yakuuka kwa moyo wake. Uwu ndi uthenga wopambana siwaanthu ozikonda koma ndi wa anthu amene ali ozichepetsa pa maso a Mulungu. Ichi ndi chi kristu choona osati chongokhuzidwa chabe ndi maganizo athu.

Yesu ali kubwera kudzatitenga ife. Ndipo tsiku limeneli chimwemwe chidzadzaza miyoyo yathu koma pano tili ndi ntchito pokozekera mkwatibwi amenewu ndi ntchito yathu kukondana wina ndi mzake ndi kuthandizana kuti tonse monga mpingo tikonzekere kubwera kwache Yesu. Ndiye maonekedwe athu adzakhala monga Yesu pamene adzabwerere kwa mpingo wake tidzafanana naye. Tidzakhala mkwatibwi monga Yesu, Mkwatibwi amene ali wa mphamvu monga Yesu amene ali ndi chifundo ndi chikondi monga iye sizophweka ai. Koma kuyanganira maso pa Atate, monga Yesu anachitira. Ngati tiika maso athu pa iye Yesu tidzakhala mbali ya chikondwelero cha mfusulo wa mwana wa nkhosa ndipo chimwemwe chake chidzadza mitima yathu.

Miyoyo Yolumikizizana Ndi Kulukana

Tiyenera kutchura kuti kuli abale oyera mtima mu mizinda amene ali kupemphera chifukwa cha ufumu wa Mulungu kuti uwonenetsedwe pa dziko lino lapansi. Ndipo ali ozipeleka koposa mu moyo wa Yesu ndi mtima wawo yonse kufuna kaye ufumu. Monganso mutipemphelerenso ife komanso kwa iwo amene sanalambire mabondo awo kwa Balaa. Pemphelaninso iwowo chifukwa alinso mbali ya ife.

Ndizofunikanso kudziwa kuti ngati palinso china chimene tingatumikire, ndi zopezeka ndi kulukana kwa miyoyo wathu pamodzi ndi moyo wathu tsiku ndi tsiku. Zinthu zimene Yesu wawonetsera kwa ife kuno ndi kwina konse ndi zopezeka mu kugwirana mapewa ndi kuthandizana wina ndi mzake. Nthawi zimene uchimo umatchutsidwa mu miyoyo yathu nthawi imene manja athu ofooka amakwezedwa mu khosi lathu ndi nthawi imene imasonyeza mmene ife tili. Ngati pali china chimene tingapeleke, chimabwera chifukwa ena ayesetsa kuthandiza ife. Choncho, pamene mukuwelenga bukhu ili la moyo wanu. Dziwani kuti simuli kuona anthu ochepa chabe kapena zana chabe koma ochuluka amene ali kuthandiza mu msinkhu wa wina ndi mzake, ndi miyoyo yathunso. Tiyeni ife tonse pamodzi tipitilire kusintha miyoyo yathu pokweza ndi kulambira ulemerero wa Mulungu. Yesu alandire ulemerero ndi matamando!

Unsembe wa Okhulupilira

Mu thupi la kristu pali ziwalo zambiri ndipo zina ndi zowonekera kuposa zina. Koma tisachite molakwa pa mphamvu ya mphatso imene ndi yosawonekera. Mu mpingo wa mu mzinda umene inu muli mudzakhala ndi anthu amene amalankhula—lankhula koposa anzawo koma musanyoze kapena kudelera mphatso imene ili mkati mwanu angakhale kuti simulankhura—lankhula. Inu ndi ena amene amalankhula lankhula muli ndi mulingo umodzi umene umathandiza iwo kuti akhale monga ali. Mwina nonse a inu simungakhale wowonekera monga ena ali. Koma mphatso yanu ndi yofunika ndipo gwilitsani ntchito zimenezi.

Mbale kapena mlongo amene ali pano mwina sangalankhule kwambiri mu msonkhano koma ine ndekha koma alipo amene mphatso yawo ndiyopambana kundipanga ine ndekha. Koma alipo amene mphatso yawo ndi yopambana kundipanga ine kukhala chimene ine ndili komanso kulimbikitsa zinthu mu moyo kuti zichitike, koposa kulankhula mau oposa 10,000. ngati sindingathe kuthandiza aliyense kuti akhale monga Yesu mu moyo wanga, ndipo ndidzanena kuti tili kuthokonza koposa kwa Yesu kuti ali kunditumizira anthu. Amene akuthandiza kuti ndikhale monga m’mene ine ndili. Ndikunena choncho chifukwa posakhala kuti ndinu ndani mungathe kuchita posintha dziko kwa Yesu. Musaganize kuti ndinu opambana pamene muli kulankhula kwambiri pa msonkhano ena sangalankhule kwambiri koma mu njira zina ndi opambana chifukwa cha zimene ali pa miyoyo yathu zimene zili zowelengedwa kwa Mulungu.

Ndifuna kuti mudziwe m’mene wina inu anga thandizire dziko mmene mungakhalire mwa Mulungu wina ndi mzake kuthandizana kuti mukhale monga Yesu. Mulungu safuna wozipambanitsa kapena otchuka. Ali kufuna anthu amene angazichepetse kwa wina ndi mzake. Mulungu akufuna anthu amene ali ndi kuthekera kugwilitsidwa ndi iye.

Funso limafunsidwa posachedwapa

“Kukhudzana ndi zinthu zimene talankhulazi unsembe wa okhulupilira, mmene tingakhalire pafupi ndi Yesu mmene mpingo uli—kodi ndife utsalira ndi madera ena? Kodi alipo ena mu maiko amene akuzidziwa zinthu izi ndi kuyenda mu zimenezi?”

Ndifuna inu kuti mudziwe udindo wanu chifukwa ndinu oyambilira kwa anthu mu dziko ndi kuti muyende mu izi. alipo ochepa onse choonadi ichi cha Mulungu. Alipo ochepa amene amazimvetsa izi m’maiko onse choonadi ichi cha Mulungu. Mulungu wakulamulilani kuti mupite ku maiko onse ndi mau ake kumalo amene ali pafupi ndi inu. Pitani ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumu woyera wa Mulungu. (1 Akorinto 12, Machitidwe 2:42-47) Mulungu wakusankhani ngati apadera dera ndi uthenga wapadera uwu pang’ono ku India kapena Polande ndi kwina konse amene amadziwa zinthu izi zimene zili pamtima wa Mulungu. (Aefeso 3:10) Mulungu ali kunong’oneza zinthu izi mu makutu anu za mpingo kuti mukhale mu moyo uwu ndi peleka uthenga wotere. Kodi mudzapititsa uthengawu kwa onse? Uthenga wabwino wa ufumu uyenera kupita ku maiko onse. Pamene chionongeko chidzabwera! Ndili ndi chiyembekezo choti mudzalimbika ndi chikhulupiriro pochita izi.

<<<
jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon