Kuyembekeza Pa Ambuye M'moyo Athu

2003

September 1996, Mlowe, Africa.

(Zogawana pa nthawi yochepa pamodzi ndi abale aku Malawi)

Pamodzi!

Tiyeni tilindire tiyamike zina lake tonse pamodzi!

Anandimva ine nandimasula ku mphamvu ya mantha!

Tiyeni tiyamike zina lake tonse pamodzi kunthawi zosatha

Nonse yimbani zomuyamika ndi kumkwezeka iye.

Mnyimbo iyi ikuchokera pa Masalimo 34. Mawu onse “pamodzi” akuyimila pakatikati ka nyimboyi. “Tiyeni tiyamike dzina lake tonse pamodzi kunthawi zonka muyaya” Tilinazo zinthu zapadera dela mnyimbo yomweyi yoyamika Yehovah, kunena za Ambuye pa kumva kulira kwathu mmapemphelo, komanso ndi Angelo ake potisamalila ife kuchokera kuzoyipa zonse ndi mantha, komanso Ambuye pokwanilitsa zokhumba zathu ndi kutipatsa ife chakudya cha tsiku ndi tsiku kuchoka ku nthaka yolengedwa ndi manja ake Yehova.

Zonse tikuonazi nzapadera dala zoyikaka ndi Yehova chonse Ambuye anapeleka kw aife kuti tipindule nazo. Mwa Ambuye wathu. Ichi ndiye chofunika pa zonse.

Moyo unasanduka kuunika kwa anthu

Ndi ganizo loyikika kwa aliyense kuti tiyenera kuyembekezera pa Ambuye kudziwa kukhala mmsinkhano ya oyela mtima a Mulungu. Ndikufunafuna nkhope ya Ambuye ndi kudziwa cholinga chaka. Ichi ndiye cholinga chake. Komabe ndikukhulupirila kuti nthawi zambiri ife sitiyembekezela pa Ambuye pa zimene timafuna kuchita mmisonkhano yathu; Mmalo mwake timamdalira Ambuye pa zokhazokha timafuna kuna kuti achite miyoyo yathu. Zinthu zambiri zimene zaphunzitsidwa kuti oyela akakhala pamodzi nkubwela ku nthawi za nthawi. Ndipo oyelawo amayenda pamodzi ndi kulingalila pamodzi. Pakakhala palibe kuyendeledwa ndi Yehova.

Ndipo oyela pamodzi tiyenda pachimene chachitika mnthawiyo tonse pamodzi. Pamene Ambuye apanga ubale wathu tonse pamodzi mwakuya. Iye amabweretsa ziphunzitso zake kuchokera kumwamba. Nthawi zina amaphunzitsa kupyolera mzopweteka ndi mukulephera kwa moyo uno. Nthawi zinanzo zimabwela mukupyolera mu chigonjetso, nthawi zinanso mzodabwitsa zake zimene amazigwiritsa ntchito potidabwitsa ife. Komanso zinthu zonsezi zimachitika pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Pamene ife tiyembekezera pa Ambuye mmoyo wa tsiku ndi tsiku tonse pamodzi mwa Ambuye.

Timalankhulana wina ndi nzake mmoyo uno wa tsiku ndi tsiku zokhuzana ndi Yesu mmoyo uno. Komanso ndikuthandizana mavuto athu pamodzi ndikuphunzira za iye nthawi zonse. Timagwilizana manja wina ndi nzake tikafooka. Chifukwa chake miyoyo yathu ngokonzeka komanso kuyembekeza pa Ambuye wathu. Zitha kuchitika kuti onse oyera akhala pamodzi, wina ayenera kuti ndiri ndi vuto, pamene wina avulala mapezanso chisangalalo cha Ambuye mkupilira kwache. Pamene oyela mtima akhala pamodzi pamenepo mlongo kapena mbale angathe kulankhula ndi kugawana chimene aphunzira ndi anzao. Mungathe kuona kuti chiphunzitsochi sichikusimikizira pa kulindira pakha ayi ndi kufunsila chochita; ngakhale zotelezi zikhoza kuchitika koma zichokera kwa Ambuye pakuyembekezera pa iye. M’ubale wathu wa tsiku ndi tsiku, pakulemekeza Mulungu ndi zinthu zochepa mu miyoyo yathu, ndi kukwezana wina ndi nzake manja athu pothandizana wina ndi mzache. Kupyolera mmoyo wa tsiku ndi tsiku chiphunzitso mmawa uno pamene ndi kuyendabe mmbali mwanjira ndi m’bale kapena mlongo, pamene tikuseka or kulira pamodzi kapena zinthu zotelezi zimabwera pakulingalira kwathu.

Ndi Chimodzimodzi Lero

M’bukhu la Yohane 1. Linena za Yesu kuti moyo unasanduka kuwala kwa pa anthu ena kuona kuchokera m’moyo otisogolera. Ndi chimodzimodzi lero. Pamene tikhala miyoyo yathu mwa Yesu ndi kuthandizana mnjira yoyenera kwa wina ndi nzake ndi mtima wathu onse. Koma makamaka tiyembekezerabe pa Ambuye ndi moyo wathu onse. Kusonkhana kwathu kumakhala chiyanjano cha wina aliyense pokondana wina ndi nzake. Kuphunzitsa kozama mmiyoyo yathu ndipo tayenera kukhala okhuzidwa ndi zotelozi. Mwa kukhala nacho chifundo. Pamenepo ndipamene tikhoza kusawana tonse pamodzi.

Zinthu izi nzofunikira kwambiri kugawana tonse. Pamodzi chifukwa ambiri a ife tiri ndi maganizo oti chiyanjano ndiye potheka pa zonse mmoyo wathu onse wa chikhristu. Kodi Yesu anali ndi chiyanjano ndi ophunzira ake sabata lili lonse? Osati lachiwiri lina lililonse usikuku? Ndi la Mulungu mmawa lina lilonse mmawa mawa sana chite chonchi. Mpaka na lero sachitabe. Ndi chimodzi modzi lero mpaka na kalekale. Amaphunzitsa ife pamene tidzuka natenga step oamene tiyenda komanso pamene tilingalila. Kusonkhana kumakhala pamene banja lili lonse pamodzi kuimilira, kukhala pansi ndi kuyenda pa njira. PAMODZI moyo unakhala kuwala kwa dziko lapansi ndi chifukwa chake pali kufunika kuti tione wina ndi nzake ndi kukondana kunja kwa “misonkhano” Timataya nthawi pa moyo owonana wina ndi nzake mu 1 Akorinto 11, mtumwi Paulo anati ngati sitingakondane ndi kunyamulana mapewa wofooka tsiku ndi tsiku ndiye kuti misonkhano imakhala wophana osati yabwino. Tiyeni tisankhe tokha mu miyoyo yathu osati mu msonkhano kapena chiphunzitso, ikhale kuunika kwa anthu.

Tifunse Atate Pamodzi

Ndinu atate okondeka, choonde lolani kuti timve ku zinthu zimene zili zoona osati zimene Satana amabweletsa ku makutu athu ndi mitima yathu. Satana ndiye tate wa mabodza ndipo amafuna kuti adzinamabe kwa ife kutiuza zonama. Tikudziwa kuti mdani wathu ndi onama ndiponso ndi wakupha amafuna njira yotiphera ife koma timadziwa kuti mumatikonda ndipo mukufuna kutipatsa zinthu zabwino kuti zitimasule ife ku nsinga. Tikufunsani Inu Atate kuti mutipatse maso amene angathe kuona zonama. Tikudziwa kuti tidzakwanitsa chifukwa muli kumbali yathu. Zikomo chifukwa cha lonjezoli zikomo chifukwa cha chiyembekezo sichidzakhumudwitsa ife. Timakhulupilira inu ndipo simudzatichititsa manyazi sitidzafa ndi mphamvu ya Yesu ndi mfumu wosatha mumafuna kuti mvula igwe ndi kuti nthaka ibale zokolora. Mumafuna kuti mitambo ibweletse dangalira pamene dzuwa liwomba mumafunanso kuti mitsinje iyende bwino kutinso ilimbe ndikupangitsa ife kudwala mumakonzanso kuti ana athu onse akule bwino ndi kukalamba ndi kuti za manja ahu zikhale zopambana kapena zolephera mumakonzanso ngati zolankhula zathu zibweletse chimwemwe kapena kukwiyitsa ena. Mumakonzanso kuti mukhale Mtendere kapena mphamvu mu mtima wanga kapena zokwiya kapenanso zolephera. Ndinu nokha amene mumakhululuka machimo anga ndi kutibweletsa kunjira yabwino uthenga wabwino ndi oti mumatikonda kwambiri pamene muli mfumu yamuyaya ndi zonse zili pansi pa ulamuliro wanu ndi uthenga wabwino kwa ife kuti ndinu odzadza ndi chifundo ndi kukoma mtima. Mfumu ya muyaya. Inde komanso bwenzi lokongolqa ndi lokondeka. Zikomo chifukwa chokhala bwenzi lathu. Mudzatitengera ife ku mbali ina ya chigonjetso….

Dzina lanu likule.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon