Ubatizo Wa Yesu

2003

September, 1996 Mzuzu Malawi

Kuzindikira Ubatizo

Zimene Mulungu anaika kukhala chinthu cha bwino monga mphatso chakhala chinthu chochitira nkhonkho. Monga thupi la Kristu likamakula monga ofanana ndi Yesu ndi zina. Tiyenera kudziwa kumasulira kwa kuti ubatizo ndi chiyani? Timaona mu chipangano cha tsopano mmene Yohane Mbatizi anabwera kudzawabatiza anthu kuti machimo awo akhululukidwe. Panalibe malemba mu chipangano chatsopano zoti Yohane adzabatiza anthu. Pamene Yohane anabwera anabviika anthu mu mtsinje wa Yorodani zinali zodzbwitsa kwa anthu. Chifukwa panalibe uneneri wa ubatizo ndipo panalibe wina kale amene amadziwa mpaka Yohane anabwera.

Choncho kunali kosabvuta kuti Yohane ali kulakwa chifukwa panalibe pamene Baibulo limanena kuti ndibatizidwe mu chipangano chatsopano? Koma chifukwa Yohane anali bwenzi wa Mulungu ndipo anatumidwa ndi Mulungu ndi uthenga wabwino kwa anthu anabweletsanso ubatizo kwa iwo, ndipo amabwera kuchokera kumadera ndi m’midzi kuti kudzabatizidwa. Anthu ena amumpingo mu nthawi ya Yohane anati sitifuna ubatizo utiuze kuchokera mu ubatizo. Yohane kuti tibatizidwe Yohane sanathe kuwauza kuchokera mu Baibulo chifukwa munalibe chiphunzitso mu chipangano chakale. Koma Yohane anamvetsera kwa Mulungu ndi kumva mau a Mulungu za ubatizo. Anthu ambiri ndi Afarisi anati. Ai ubatizo Baibulo limanena momveka bwino kuti anakana chifuniro cha Mulungu ku miyoyo yawo pokana ubatizo ndibwelezanso kuti mumvetse bwino Baibuli limati anthu amene anakana chifuniro cha Mulungu mu miyoyo yawo.

Mwina sitidziwa bwino ubatizo mwina kunyowa konseko sitidziwa kuti ndi chiani kwa ife. Mwina sitingadziwe za izi koma ndi zofunika kwa Mulungu mum moyo wathu. Mwina sitingadziwe kuti izi ndi chiani. Oma ndi zofunika kwa Mulungu ndiye ndizo funikanso kwa ifenso.

Kufunika Kwa Ubatizo Kwa Yesu

Mukuyangana mu chipangano chatsopano ndi chiphunzitso cha Yesu zinthu zomalizira zimene Yesu analankhura asanapite kumwamba mu mitambo zinali. Pitani ku dziko lonse ndipo pangani anthu kukhala ophunzira anga. Phunzitsani iwo mu njira zonse. Batizani iwo mu dzina la Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera.

Ngati ndikagona pakama mwina pafupi kufa ndipo ndili kukuuzani inu kumakutu anu mwana ndi mau omalizira ndithu ndipo mau omalizira amakhal ofunikira kwamabiri. Sichoncho? Mwa mau ena amenewa amene Yesu analankhula ndi kuti Akhale ophunzira anga abatizeni iwo. Aphunzitseni kuti amvere zonse zimene ndikuuzani ndi mau ofunika kwambiri kwa Yesu ndipo ayeneranso kukhala ofunikira kwa ifenso. Mau oti ubatizo mumau amu chigriki ndi ubatizo kuthandauza kumizidwa kumira. Pamene anthu anamva Yesu ali kulanhkula sanamvetsetse. “pitani akhale ophunzira anga abatizini mu chilankhuro chawo, anamva Yesu akuti . pitani akhale ophunzira anga abatizeni iwo kumizidwa mmadzi.

Ubatizo sunali mau a chipembedzo nthawi imeneyo. Pamene timamva mau oti ubatizo tsopano timaganiza kuti ndi mau chipembedzo nthawi imeneyo. Pamene anthu amachapa nsalu amaika mmadzi ndi zobvalazo zimakhala pansi pa madzi ndi kumachapa, ndipo akamatchuka ziwiya amazikanso pansi pa madzi ndimazitchuka anali mau amene analipo kale ndiye ubatizo sanali mau achipembedzo ndiye pamene Yesu amati pitani akhale ophunzira anga ndiye amatiuza momveka bwino pazimene iye amafuna kuti tidziwe.

Pali mafunso ambiri pa maganizo anthu ambiri pankhani imeneyi koma mau a Yesu ndi oti ndi ofunika tiyenera ngati sichoncho ndiye kuti sitili okonzeka kubatizidwa. Timaika manda anthu akufa ndi pamene timapeleka moyo wathu ndi pamene timauka ndi kuyenda mu moyo watsopano ubatizo ndi chikondwelero chopeleka moyo ndi kulandira moyo wa Yesu.kuikidwa mmanda pamodzi ndi Yesu ndipo zinthu izi ndi zofunika chifukwa Yesu anatero. Angabatizidwe ndi ndani? Ndi funso labwino. Peturo anati ubatizo ndi kulira kwa munthu olungama mtima kwa Mulungu. Mtima umene amafuna kukhala mwa kulira kwa Yesu kwa Mulungu kukhulupirira kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu ndi kufuna kuti machimo awo akhululukidwe ndi kuchotsedwa akhonza kubatizidwa. Munthu amene sakhulupilira Yesu salira moyo wake kwa Mulungu ndipo sanakhulupirire kuti akufuna kukhala mwa Yesu ndi mitima yawo kufikira kuthekera kwawo ndiye kuti Sali okonzeka kuti abatizidwe.

Sitingathe kumvetsetsa bwino za ubatizo ndi kusamvetsatso bwino mmene tingakhalire mwa Yesu koma kuti moyo uyenera ofuna kulondora Yesu ndi mmene tingadziwire. Tiyenera kudziwa kuti tinapachikidwa pamodzi ndi Yesu pamodzi ndi machimo anga ndi kumva kupweteka kuti tinapha mwana wa Mulungu osalakwa. Tiyenera kufuna kunena kuti, pepani, chonde tengani moyowanga Aroma 6 amanena kuti tinafa ku machimo athu tinafa naye pamodzi ndi Yesu ndi kuyenda mu moyo watsopano. Sitiyenera kukwirira munthu amene ali ndi moyo ndipo kuikidwa mmanda ndi kwa anthu akufa. ndi zoona mu mzimu tiyenera kufuna kufa ku machimo athu ngati sichoncho ndiye kuti sitili okonzeka kubatizidwa. Timaika mmanda anthu akufa ndi pamene timapeleka moyo wathu ndi pamene timauka ndi kuyenda mu moyo watsopano ubatizo ndi chikondwelero chopeleka moyo ndi kulandira moyo wa Yesu.

Monga mwa zonse zochitika muchikristo ndi nkhani ya mtima osati zochitika kunja kwa thupi. Tikuthandauza kuti zofunika kwenikweni tiyenera kuti tikonde Yesu mwana wa Mulungu ndi kupeleka moyo wathu kwa iye. Koposa mau amene amanenedwa a zaubatizo Yesu akufuna kutipatsa ife mzimu woyera ndi kukhululukidwa machimo athu. Yesu akufuna kuti tibatizidwe ndi mzimu umodzi kulowa mu thupi limodzi akufuna kuti tikhale mu mbali ta Atate, mbali ya mwana ndi mbali ya mzimu woyera. Kodi nanga tikhathe kunena zotero monga mwa chizolowezi kuti iye akwaniritse malonjezano ake?

Yankho ndi loti simau amene timalankhura ndi mtima ndi moyo umene timapeleka kwa Mulungu umene uli ofunika. Ngati tingadziwe ndi kukhulupirira ndi mtima wathu kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu ndi kuti Yesu anafa ndi kuti machimo athu okhululukidwa ndi kudziwa kuti tiyenera kukhala mwa Yesu osati mwa ife tokha ndiye timumvere ndi kupeleka miyoyo yathu kuti tibatizidwe ndiye kuti tili kumwamba ndi ngati kuti mkono wa Yesu watsitsidwa kuchokera kumwamba kufikira pa ife pamene tibatizidwa. Ubatizo ndi ofunika kwambiri pali ndi malonjezo ambiri amene ananenedwa okhunzana ndi ubatizo. Satana amatsutsa ubatizo amadana nawo.

Tinaona izi India mwa chitsanzo, munthu anganene kuti ndikhonza kukhala mkristu ndipo anzake tikunena “chabwino” “chabwino” munthu oyamba anganene tifuna kubatizidwa ndipo mpaka wina amaotcha nyumba yake satana amadana ndi ubatizo zili zonse zimene satana amadana nazo, ine timazikonda.

Ubatizo ndi malo amene Mulungu amakumana ndi munthu ndi lamo opatulika. Sichinthu chimene umangochichita. Sizingakhala ndi kukhala ndi okhulupilira ena ndi zazikulu kuposa pamenepa. Mulungu ali mu ubatizo mu kupambana koposa ndi chifukwa chake Yesu ananena ma mau ake omaliza ndi chifukwanso Peturo ananena kuyamba ku mpingo yoyamba uja “Mulungu waika Yesu, uwu amene munamupha. Kukhala Ambuye ndi Kristo chifukwa anali odulidwa mtima ananena kuti inde. Tidzachita chiani amuna inu abale? Peturo mwa Mzimu Woyera adati kuti, lowani mpingo Ai. Peturo mwa mzimu woyera anati lapani chotsani machimo anu ndipo ena onse ainu lowani mmadzi ndipo mudzalandira mphamvu ya Mzimu Woyera ndi kukjulukidwa kwa machimo anu, angakhale kuti machimo anu ndi ofiira adzayeletsedwa monga matalala ndipo mudzalandira Mzimu Woyera kukhala mkati mwa inu ndi lonjezo ili lili kwa inu ndi ana anu ndi kwa iwo amene ali kuti kw aiwo amene aitana padzina la Ambuye. Izi ndi zofunika ndithu ngati munthu wapeleka moyo wake kwa Yesu amamva chisoni ndi machimo ake ndipo amadziwa kuti Yesu amakhulukira machimo ndi kufuna kuti akhale mukuzindikira Yesu ndiye mafuna kubatizidwa.

Mu Machitidwe 8. Filipo anakumana ndi munthu pa njira ndipo anali waudindo wake ku Ethiopia anali wa nzeru ndi ophunzira ndithu. Anali kuwelenga mau a bukhu la Yesaya, Filipo anadza kwa iye nati, Kodi mukudziwa zimene muli kuwelenga? Anali kuwelenga za Mpulumutsi ndi Messiah, Yesu ndipo munthuyo anati ndidzadziwa bwanji ngati pali wina ondiuza? Ndipo Filipo anadza namuuza zonse za uthenga odabwitsa wa Mpulumutsi anamuuza za bwenzi lathu, ndinso Mfumu Yesu. Anamuuza za Yesu amene anali kuyenda panyanja. za Yesu amene anali kuimitsa namodwe kukhala bata. Anamuuza za Yesu amene anali kuukitsa akufa ndi kuwonetsa akhungu kuwona. Anamuuza za Yesu amene amatenga miyoyo yosweka ndi kuyeletsanso. Ndipo pamene munthu uyu yochokera ku Ethiopia anamva mau amenewa za odabwitsa Yesu, anati siawa madzi. Batizani ine tsopano anadziwa kuti chiphunzitso cha Yesu ndi ubatizo unali olumikizidwa ndipo sanafune kuti adikire kwa kamhpindi. “Siawa madzi” chonde letsa ine ndi chiani? Anatero. Ndipo anapita kumene kunali madzi Filipo anamuuza iye kwa Yesu ndipo anabvuuka mmadzi ali ndi chimwemwe koma kufuna kwa mtima wake unali kulumikizidwa ndi Yesu mu ubatizo.

Panalinso usunga ndende ku mzinda otchedwa Filipo kumena abale athu ena anatsekeredwa kunali chibvomelezi ndipo abale athuwa amasulidwa ndi mphamvu ya Mulungu. Wandende anaona kuti makomo anali otseguka ndipo anafuna kuzipha yekha. Abalewa anamuuza kuti apulumutsidwe angakhale kuti kunali pakati pa usiku, anafuna kuti abatizidwe nthawi yomweyo panali pakati pa usiku. Sikunali kotheka sikunali kophweka koma mtima wake unafunitsitsa Yesu kuti ayenera kubatizidwa kumizidwa ngati tili ndi maganizo a Mulungu pa ubatizo tikhala okondwa pa zimenezi monga mmene munthu wa ku Ethiopia wosunga ndende wa ku Filipo ndi zikwi zitali (3,000) za anthu aku Yerusalem, tsiku limodzi anali okondwa ndi ubatizo.

Tsopano pali kusiyana kotani ubatizo wa Yohane ndi ubatizo wa Yesu? Ubatizo wa Yohane unali okhulukira machimo (Mari) ndipo ubatizo wa Yesu unalinso wokhulukira uchimo (Machitidwe 2) patapita nthawi mu bukhu la Machitidwe a Paulo anakumana ndi anthu amene amafunika kuti abatizidwanso, chifukwa analandira uthenga wa ubatizo wa Yohane ndipo amafunika ubatizo wa Yesu. Choncho amafunika ubatizo wa Yesu ndiye kuti ubatizo sikungonyowa konkha ai. Anthu awa ndi ubatizo wa Yohane anali achite ntchito yabwino ndi asachimwenso. Ubatizo wa Yesu ndikubwera mu mzimu woyera wa Yesu ndi kukhala pamodzi ndi Yesu wa ku Nazarene. Ubatizo wa Yohane unali wa ntchito, ubatizo wa Yesu ndi wa chikhulupiriro mu mwazi wa Mpulumutsi. Ubatizo wa Yohane unali kulonjeza za kwa Mulungu ndi kumvera Mulungu ubatizo wa Yesu ndi kulira kuti tidzaziwe Yesu, ubatizo wa Yohane unali kuchita chilungamo, ubatizo wa Yesu ndi chikhulupiriro mwa Yesu kutenga machimo athu ndikusinthana ndi chilungamo ndikuchita chinthu chabwino kwa Yesu osati ntchito zimene tigwira zathu.

Atate akonde mwana wa Mulungu amene anachita pangano ndi Atate ndi kumvera iye mu zilizonse ubatizo wa Yesu ndi kulira kwithu kw a Mulungu kuti atibise ife kwa Yesu. Ichi ndi pangano lomwe Atate anachita ndi mwana linakhala pangano lathu. Osati ndi ntchito zabwino, koma chifukwa cha Yesu, uwu ndiwo uthenga wabwino, chifuwa ntchito yathu yabwino sizingathe kukondweletsa atate. Koma atate amakonda mwana ndi iye, atate amakondwera mwa iye ndiye pamene okhulupirira abisala mwa ubatizo wa Yesu, chifukwa Atate akonda mwana motero akondwera mwa iye uwu ndiwo ubatizo wa Yesu. Umene Atate anapeleka Mzimu wa mwana wake ndi kubveka ife mwana amene akondedwa uwu ndiwo uthenga wabwino.

Pali anthu amene abwera kwa ife kuti akhale mbali ya mpingo mwani sanabvikidwe mwina sanabvikidwe mwa Kristo, mwina amakhulupirira Yesu ndi mwana wa Mulungu ndi kuti ndinapeleka monga wanga kwa iye. Koma sanabatizidwe pali njira ziwiri zimene zingatsalidwe njira ina ndi ya kunja kwa thupi monga mwa lamulo ndiye kunena kuti sitingayende kuti, “tikufuna iwe ukonde Yesu, ndi kuti upeleke moyo wako kwa iye ndipo ubatizo ndiyo funika kw aYesu. Pepani, nganizirani ndi kupemphera pa zinthu izi. awa ndiyo chiphunzitso chochekera kwa Paulo, Petulo, Yohane ndi kwa Yesu.

Baibulo limati mu Kristo ndi amafuna mkaka wa uzimu wa mau a Mulungu monga mmene ana ang’ono khanda amafunira mkaka ndiye tinganene kuti sitingayende ndi iwe mpaka utabatizidwa? Kapena kuti tiyambe kuwapanga mau a Mulungu kuti tione ngati akukonda chakudyacho kapena ai izi zimatenga nthawi koma ngati akonda chakudyacho chimene sanamvepo ndikale lomwe. Ndiye kuti adzabatizidwa ngati sakonda mau a Mulungu sizithandauza kanthu ngati abatizidwa. Sitingayende ndi wina aliyense amene sakonda mau a Mulungu ndipo chonyezera ndi osati sakubatizidwa koma ngati akukonda mau a Mulungu.

Mu malembo woyera, ubatizo ndi chofunika ndithu kwa Mulungu ndi kwa wina aliyense amene adziwa Mulungu monga kwa munthu waku Ethiopia pamene anamva ubatizo anafuna kuti nthawi yomweyo monga anthu 3000 okhulupirira mu Machitidwe 2 mmene anamvera za ubatizo anachita ntahwi yomweyo wa ndende waku Filipo anachita nthawi yomweyo angakhale kunali pakati pa usiku sizinamukhudze kuti inali nthawi yanji? Zinali choncho bwanji? Zinali chonchi chifukwa onse anali okonda Mulungu pamene mukonda amuna anu kapena akazi anu ndi kukufunsani zina zake zimene akufuna kuti muwapatse ngati mukonda Yesu ndiye kuti ubatizo ndi chinthu chopambana kwa iye ndiye kuti mudzakonda kubatizidwa chifukwa Yesu amakonda ubatizo.

Zimatenga ntahwi kuti mau a Mulungu afikire anthu koma tikhala tonse pamodzi ndi kulankhura zimatengera kuti ndi ubatizo ngati sadziwa ubatizo tidzakhala nawo kwa nthawi yochepa chifukwa ngati akonda mau ndi Mulungu adzakula ndipo adzabatizidwa.

Timakula mu zinthu zambiri sinchoncho? Kuyesa kwithu sikwazinthu zimene timadzidziwa kuyesedwa ndi kwa zinthu zimene zidzasinthidwe timakhala mmalo osiyana siyana kuyesedwa kwathu ndi ngati timakonda mau a Mulungu ndikuti tili kufuna kusintha nthawi zina. Kusintha ndi kobvuta ndiye tikobvuta pafunika kufatsa ndi kukondana wina ndi mzake ngati wina sakonda mau a Mulungu ndiye bvuto ndithu. Koma akonda mau a Mulungu koma zili kwa bvuta ndiye kuti tiyenera kwathandiza.

Anthu A Mulungu Ndiwo Banja

Ngati tiyenda pamodzi ngati banja tsiku ndi tsiku ndiye kuti tidzachita zonse pamodzi ngati mpingo ndi malo ongokumana pa sabata. Mmawa tili ndi bvuto chifukwa tidzaona kuti amene Sali membara wathu kapena ai. Koma ngati ndi banja tsiku ndi tsiku, koma wina sakonda mau a Mulungu ndiye kuti adzadziwika. Tidzadziwa pakukhala kwithu kwa tsiku ndi tsiku kuti ali kukonda mau a Mulungu.

Ngati munthu adzati ndabatizidwa koma sakonda akazi awo kapena amuna awo uko ndiwo kuipa ndithu. Ngati tikhala banja tsiku ndi tsiku tidzadziwa ngati ali kukonda Yesu kapena ai. Ngati tikhala banja tsiku lirilonse tidzakhala ndi nthawi yolankhula za ubatizo. Sidzakhala uthenga wa ubatizo, udzakhala abwenzi kulankhura za ubatizo mwana wina sangathe kulankhura bwino za ubatizo asabweletsa wina amene angalankhule bwino za ubatizo. Pali mphatso zosiyana—siyana mu thupi la Kristo ndiye ena angalankhure bwino koposa ena. Pamene tikhala monga banja tingakwaniritse zinthu izi pamodzi tsiku lililonse. Zimasintha zinthu kukhala banja kusiyana ndi kuonelera chipembedzo chifukwa takhala ndi nthawi yosintha zinthu ndi kudziwana wina ndi mzake. Pamene mubwera ku nyumba ya mapemphero ndiye kuti thandauzo la mpingo lili painu. Ndiye kuti tidzakhulupilira zinthu zonse panthawi yake kuti tonse tikhalepo.

Koma ngati ife ndife banja tili ndi nthawi yokambilana za kusiyana kwithu. Chifukwa timakondana osati ndi uthenga koma kulankhulana monga banja izi zimapangitsa chisangalalo ndi ufulu. Izi ndi zimene Baibulo limati mpingo ndiyo maziko a choonadi ndi, chifukwa pamodzi monga banja tikhonza kupeza maganizo a Mulungu. Pamene mphatso zikukhalira pamodzi ndikugawana moyo wathu pamodzi. Mulungu wathu adzatithandiza kudziwa maganizo ake ku zinthu zosiyana mu dera la choonadi.

Tonse Timapeza Mayankho

Izi ndi zabwino chifukwa palibe wa ife amene ali ndi maganizo abwino. Ambiri amasiyana ophunzira bwino za mbali ina ambiri Sali ku mbali ya mpingo wa moyo. Amapita ku mpingo la Mulungu mmawa basi zathera pamenepo. Sakhala ndi nthawi yoti mphatso ina isinthe moyo, ndiye ali ndi nzeru zochepa ayi akhale ndi malingaliro okhudzana ndi zophunzira zawo. Koma maganizo awo ndi osiyana ndi anzawo ndiye ali okonza ndani? Mulungu akuti maziko a choonadi ndiwo choonadi cha mpingo wa moyo. Tonse tidzapeza mayankho mu Machitidwe 15 ophunzira sanadziwe kuti okhulupirira ayenera kudulidwa kapena ai. Ndiye amabwera pamodzi kudzithetsa bvutoli. Mmodzi anati ndili kukumbukira zimene mneneri Amosi analankhura mu malemba woyera. Anali kuchitira zinthu pamodzi monga anthu a Mulungu monganso banja la Mulungu kupeza mayankho kwa Mulungu. Anachita zonse pamodzi kupeza mayankho a Mulungu popanda otchuka okhala ndi maganizo apamwamba koma linali banja la Mulungu kugwilira ntchito pamodzi ndiye Yakobo anati. Ndi chabwino kwa ife ndi mzimu woyera kuti iyi ndilo mayankho. Mpingo ndi mizati a choonadi. Tonse tikhoza kupeza mayankho. Sipofunika kukhala wa nzeru koposa kuti mukhale kuti Mulungu akugwiritsireni ntchito mu njira imeneyi.

Ubatizo Wa Yesu—Lonjezo La Tsopano

Monga ubatizo watsopano umene Yohane amaphunzitsa Machitidwe 2. limanena kuti ubatizo wa Yesu ndi kukhulukiranso machimo kusiyana kwa ubatizo wa Yesu ndi wa Yohane ndiye kuti ubatizo wa Yesu ndi ubatizo upita ku mzimu woyera ndi kuitanira kwa Messiah.

Yohane ali kubatiza Yesu asnapachikidwe pa mtanda mwazi wa Yesu usanakhetsedwe ndiye kuti Yohane anali mu chipangano chakale anali kuchita monga mwa lamulo la Alevi. Pamene anali kubatiza unali mwazi wa ng’ombe ndi mbuzi zimene zinali kukhululukira machimo ubatizo wa Yohane unatha pamene Yesu anafa pa mtanda. Yohane anadulidwatu Ambuye Yesu asanafe pa mtanda koma pano pamene Yesu ali ndi moyo ali kubatizidwa ife ndi lonjezo latsopano.

Peturo anatero mu Machitidwe 2 kuti pangago latsopano machimo anthu akhululukidwa mu ubatizo, lapani, batizani iwo wina aliyense ndipo machimo anu adzakhululukidwa ndiye mbali yopeleka moyo wathu kwa Yesu imakhudzana ndi kukhulukidwa kwa machimo athu. Koma pali chinthu china chimene Yohane sanakatha kutipatsa ife chimene Yesu anatipatsa. Yesu amatibatizanso ife ndi Mzimu woyera “ndipo mudzalandira mphatso ya mzimu woyera” mu Machitidwe 19, amuna anali kubatizidwanso kachiwiri. Paulo amawafunsa iwo ngati analandira mzimu woyera ndiye anati sitidziwa ngati mzimu woyera unapelekedwa ndipo ndi chiani? Izi ndi zimene zinapangitse kuti Paulo awabatizidwenso. Paulo anati simungabatizidwe ndi ubatizo wa Yesu osalandira mzimu woyera muyenera kukhala ndi ubatizo olakwika. Ngati mwabatizidwa ndi ubatizo wa umaphatikizanso ndi kulandira mzimu woyera. Yohane anali kubatiza ndi madzi koma Yesu adzakubatizani ndi mzimu woyera ili ndilo lonjezo la mphamvu.

Kodi ana anga adzalangidwa ndi machimo anga?

Mzimu wa Mulungu unati mu Ezekeli 18 kuti Mulungu amationa ife payenkha ndiye kuti moyo umene umachimwa ndiyo payenkha ndiye kuti moyo umene umachimwa ndiyo udzafa. Mulungu adzaweluza munthu zina ndi zoti tili ndi temberero lochokera kwa Adamu adzaweluza nyumbayo. Uku ndiye thandauzo la malembawa mu Ezekeli 18 Mulungu akuchtsa ulemelero wake ndiye pali mtengo waukulu wopelekedwa ku nyumba yako kumachimo ako. Ana ako sadzamvera iwe ndi kukonda iwe pali kulanga pa nyumba yotere koma Ezekeli ananena kuti chilango chimene munthu amapita nacho gehena ndi la ali yense payekha payenkha.

Pali kuweluza kwa Mulungu chifukwa cha machimo anga amene angapangitse kuti ana anga akhale osasangalatsa. Pali tembelero la dziko lonse lapansi chifukwa cha machimo la Adamu ndi Eva. Mayi ali ndi ululu pakubereka kwawo tsopano, amuna ayenera kugwira ntchito yolemetsa kuti apeze chakudya ndi kugwira ntchito yolimba. Thaka imabereka minga ndi udzu, madzi a mu mtsinje amatipatsa ife matenda. Pali matemberero ambiri chifukwa cha kuchimwa kw aAdamu. Ngati ndili wakumva, padzakhala kuweluza pa banja ana anga adzakhala osakondwa chifukwa cha machimo anga umene udzapangitse kuti akhale osasangalala ndiye kuti pali kulanga ana anga adzapita ku chionongeko ndi machimo anga sadzapita ku jehena chifukwa cha machimo anga. Yesu ananena kuti pali mitundu ya nthaka zinayi. Ngati mwana wanga akonda Mulungu ndi mau ake ndi kumumvera iye. Adzapulumuka Ezekeli amanena bwino ndithu.

Ana Ndi Ubatizo

Pali nthawi pa nthawi ya umwana pamene amakhala ndi chisankho mu mtima wawo kuwulira chifukwa cha uchimo wa Adamu ndiye pamaoneka kuti ana ali ndi makhalidwe amene Sali abwino koma osati kuti Machitidwe otere adzapititsa ku jehena ai. Yesu anati mpaka mutakhala ngati mwana wang’ono sumungathe kulowa mu ufumu wa kumwamba.

Nthawi zina pamene amaloza ana ananena kuti “ufumu wa Mulungu uli otere” ana awa sanabatizidwe. Anthu amene amabatizidwa amene amanena za machimo awo. Panalibe mbiri yonena kuti ana ali kubatizidwa. Analipo ana ambiri koma palibe zonena kuti ana anali kubatizidwa. Ndingathe kudziwa chifukwa chimene ana amafuna kuti abatizidwe koma mau woyera amanena kuti ndi okhawo amene akhulupirira kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu. Amene moyo wawo wapelekedwa kwa Yesu ayenera kubatizidwa. Chifukwa choti Yesu anati ufumu uli monga ana awa ndiye tiyenera kukhulupilira kuti Mulungu adzateteza ana ang’ono. Analipo ana angono nthawi ya Yesu koma palibe mbiri yoti anabatizidwa. Choncho Yesu amateteza moyo wa ana ang’ono ndipo akakula amaganiza zoukira Yesu kapena kupeleka moyo yawo kwa iye. Ndiye chisankho chiyenera kuchitika.

Chikhulupiriro cha Ayuda unali mthunzi wa chikhulupiriro cha Akristu (Ahebri 10) mu chikhulupiriro cha chiyuda padzabwera tsiku limene limatchedwa Bar Mitzuah ndi tsiku limene munthu amakhala mnyamata. Ayuda amaphunzitsa kuti anali akapolo mu nyumba ta Atate awo mpaka atafika Bar Mitzuah pakapita Bar Mitzuah pamakhala chisankho ngati adzakhala mwa Yesu kapena mwa ine ndekha. Ana a zaka zisanu sangathe kusankha. Mwana wang’ono sangathe kuti akhale mwa Yesu kapena mwa iwo wokha koma kwa ana a zaka khumi ndi khumi ndi ziwiri akhonza kusankha kukhala pa okha kapena mwa Yesu koma osati wa zisanu chifukwa saziwa kuti Yesu ndi ndani.

Mu Machitidwe 2 limati kuti mubatizidwe muyenera kuti mulape muyenera kuti mulape kuti mubatizidwe. Simungabatizidwe ngati simungalape ndikuganiza nthawi zambiri ndi zobvuta kwa mwana wa zaka 5 (ZISANU) kuti adziwe kuti chimo ndi chiani. Mukawauza kuti anapha mwana wa Mulungu kodi adzadziwa? Sitikudziwa ngati adzadziwa? Ndi munthu yekhayo amene angadziwe kuti anapha Yesu ndi machimo ndiye angathe kubatizidwa. Yesu anati ana ali ndi Angelo amene amaima pa kupezeka kwa Mulungu Yesu mwini ndi amene analankhura ndi kuphunzitsa za izi. ndiye tiyenera kumukhulupira iye za ana athu mpaka atafika mu kukhala ndi chisankho

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon