Kudzodza Kwa Wonse Yesu Ndiye Banja

1/9/2003

Mzuzu, Malawi Afirika 1996

Kuti ukathe kuyankhula mawu a Mulungu munthu uyenera kudzodzedwa. Kodi izi ndizo inu nonsenu mumaganizira maganizo anu? Ndili ndi uthenga wabwino wochokela kwa Yesu kunza kwa inu okhudza za zimenezi. Izi zikulankhuliridwa kuchokela kwa buku la Yohane woyamba chapter 2 (okhululupira) kuti muli nako kunzodza pa inu koona osati kwachinyengo. Mzimu wa Mulungu, Yesu amene anali mphunzitsi wamkulu akhala mwa inu. Yesu ndi mphunzitsi wamkulu, wodabwitsa komanso wamphungu. Paulo adanena kuti ngati mulibe mzimu wa Yesu mwa inu ndiye kuti simuli aiye. Ngati inu muli mkhristu, ndiye kuti Yesu khristu adali munthu odzodzedwa kuposa munthu wina ali yense adakhalapo-Iyeyo akhala mwa inu. Uku ndiko kunena kuti ngati muli Mkhristu, ndinu wodzodzedwa. Alleluya!

Osakhala ndi udindo kapena dzina—Koma ntchito yochita.

Pali nthawi zina pakati pa anthu okhulupirira pamapezeka ntchito yoyenera kuchita. Pamakhala ntchito ngati kusamalira ana, kugawa chakudwa, kusamalira chuma, kusamalira amai amasiye komanso ana amasiye, kuthandiza kusamalira zinthu kapenanso nyumba za anthu, kukonza mapaipi odutsira madzi a zimbudzi, kuikira magesi, kusoka zovala kapenanso kunthandidzana kulima munda. Pali ntchito zambiri muthupi la Yesu. M’buku la Machitidwe makamaka mutu wa 6 padali ntchito yoyenera kuchitidwa. Mchitidwe amu (malembo) m’mawu a mulungu sizimanena “zokhudza kudzodza kokhala m’busa yekha ayi.” Anthu asanu ndi awiri omwe akufotokozedwa mukhaniyi adali anthu wamba chabe amene adadzadzidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera komanso nzeru. Iwo chikhalilecho adali (akutumikira) akugwira ntchito yabwino ya Yesu. Adali ndi mbiri yabwino yokhudza khalidwe lawo lodzichepesa ngati atumiki a Yesu. Koma padali ntchito yofunika kudyetsa amai amasiye. Ndi chifukwa chake mubuku la Machitidwe mutu 6 likufotokoza za kuika kwa manja osati ngati kupemphera kwa Yesu koma kugwira ntchito.

Monga molingana ndi Baibulo anthuwa sadali madikoni ngati mmene tingaganizire ambiri aife. Monga mmene iwo adalili adali oposa udikoni. Timamva tikawerenga mbuku loyamba la Timoteyo mutu wachitatu (3) timawerenga kuti dikoni ayenera kukhala mwamuna (wokwatira) wapabanja, koma monga mmene tikudziwira bwino ife tonse, anthu awa sadali okwatira kapena adali ndi ana ayi.

Tikumva nkhani inayake mmbuyomo, Paulo adapita kukaona Filipo, amene adali mmodzi wa madikoni asanu ndi awiri. Kodi mukukumbukila kuti Filipo adali ndi ana a kazi anai amene nawo amene adachitapo ulosi? Mzimu woyera umafotokoza bwino lomwe za Filipo ngati “m’modzi mwa anthu asanu ndi awiri,” osati “modzi wa madikoni asanu ndi awiri.” Kudali madikoni ambiri m’mipingo yochuluka ya m’nthawi imeneyo koma mzimu woyera siukutiuza kuti, Filipo, adali m’modzi wa madikoni asanu ndi modzi.” Koma mzimu woyera ukutiuza kuti Filipo m’modzi wa anthu asanu ndi awiri. Iyi ndi fundo yofunika kwambiri. Pali kusiyana pakati pa Dikoni ndi munthu wina amene adasankhidwa ku utumiki.

Dikoni amakhala ndi ntchito yopitilira, Koma anthu asanu ndi awiri omwe adasankhidwa mabuku la Machitidwe Atumwi mutu wa chisasnu ndi chimodzi (6) tikumva kuti adasankhidwa ku utumiki wapadera. Ndipo tonse tikuntha kuona kuti ntchito ya utumiki wawo idasintha pomwe zinthu zidayamba kusintha mu Yelusalemu. Filipo adapita ku Samaliya, Stefano adanka naralikira masunagogi kumene tikumva kuti adaponyedwa miyala naphedwa koma sitikumvanso kuti iwo adapitiriza kupereka chakudya kwa akazi amasiye. Nthawi zina timayenera kuyika manja pa anthu okhulupirira kuti Mulungu awatume ku ntchito yapaderadera, koma ngati ntchitoyo yomwe adasankhidwira yatha sapitirizanso kukhala maudindo omwe kalero adasankhidwira. Pano pali mbali yosiyana, ngakhale, thawi zina pamene Mpingo wakula kwambiri, kuti ukhale ndi madikoni ndi akulu a Mpingo. Izi zimangokhala ntchito zopitiriza-pitiriza imene imalira zinthu zambiri monga mwa udindo kuti ukathe kuthandiza munjira zambiri.

Pamene mudzatchedwa mkhristu, Yesu adzakusanjikani manja ndipo pomwepo mudzakhala wansembe. Mudzakhala olankhula koma okonda mawu a Mulungu. Pamene mpingo ukukula komanso kusintha, pamakhala ntchito yoyenera kuichita kapena kuti mpingo umasankha mwa anthu ake amene alipo ena monga awiri kapena anai amene ali odzala ndi Mzimu woyera ndi nzeru. Kapenso ngati ntchitoyo ioneka kuti ndiyaikulu amasankhirapo anthu ena asanu ndi awiri wodzala ndi mzimu woyera ndi nzeru kudzaika manja pa iwo pamodzi komanso kuwasankha iwo ku utumiki. Koma izi zimakhala choncho ngati pokhapokha pali ntchito apo bi ayi, anthuwo amakhaladi okhulupirika ndi omvera ku ntchitoyo ndipo adzakhaladi ndi udindowo, koma ngati kudzaoneka kuti sali okhulupirika pa udindowo, udindowo udzachotsedwa kwa iwo. Koma ngati alibe okhulupirika adzagwira ntchito paudindowo kufikira ntchito yomwe adasankhidwira yachitika. Pamene tikamanena za Madikoni ndi Akulu a Mpingo, iyi simakhalanso ntchito. Komanso ndi zoona kuti mwina nthawi zina zimatha kutheka kuti ngati akhala anthu osakhulupirika amatha kuwachotsa pa udindo wawonso.

Mphatso ya Mtumwi

Mtumwi Paulo adanena kuti iye ndi kapolo wosankhidwa ndi Mulungu. Sichinali kuti adali munthu wapaderadera ayinso, koma kuti Mulungu adali kufuna kuonetsera chifundo chake. Izi zidali chomwecho ndi atumwi onse. Iwo sadasankhidwe chifukwa adali anthu apaderadera ayi. Iwo adasankhidwa pa mpikisano wa chifundo cha Mulungu. Paulo adanena zimenezi kwa akhristu aku Mpingo wa ku Korinto kuti ngati sangachite ntchito yomwe Mulungu adamuitanira ndiye kuti chinthu china chake chikhodza kuchitika monga ngati matembelero. Paulo adanena kuti udindo wa mphatso ya utumwi ndiwo nthawi zonse ayenera kukhala munthu wokhulupirika ngati kapolo kuti ukathe kuwauza anthu ena za ukulu wa ulemerero wa Yesu. Choncho adakhala kapolo wa uthenga wabwino wa Yesu, ndipo m’malo mwake adapereka moyo wake pa mtengo uli wonse omwe akadayenera kupereka, kuti akathe kukwanitsa kuwauza anthu ena za uthenga wabwino wa Yesu.

Pali mphatso zambiri muthupi la Yesu khristu ndipo mphatso iliyonse ili ndi kufunikira kwake. Paulo adanena kuti mphatso zomwe aliyense adali nazo zinali zofunikira mwapadera, kuti aliyense athe kutumikira ngati wansembe kuti akathe kuwauza anthu ena za Yesu Khristu. Iye adanenanso kuti anthu ena omwe amanena za Yesu adzalandira mphoto. Koma mtumwi Paulo adanena kuti, ali otemberereka ngati sangawauze anthu ena zokhudza Yesu. Mphatso ya utumwi ndi ubwino wake ndi umodzi komanso yapaderadera komanso yosowa kwambiri. Komanso ili ndi zopereka mtengo wache zambiri, monga kulankhula kwa Paulo. Atumwi ali ngati mizati m’nyumba ya Yehova. M’buku la Aefeso mutu 3, Paulo akulankhula za zinthu ziwiri zomwe iye amayenera kuchita pa udindo wake ngati mtumwi. Adanena chinthu chimodzi pa (versi la 8) ndiko kuuza anthu ena za chuma ulemerero wa Yesu. Mundime la a Paulo akunena za chinthu chachiwiri chimene iye adaitanidwira, ndiko kuti akathe kuwafotokozera anthu momveka bwino m’mene angakhalire mu ulemerero odabwitsa wa Yesu Khristu. Iye adanena kuti adzawaphunzitsa m’mene angakhalire ndi moyo wodabwitsa wa Yesu komanso m’mene angasanthulire moyo wodabwitsawu wa Yesu m’moyo wawo.

Mubuku loyamba la ku Akorinto mutu wa 3, Paulo akudzitcha yekha womanga waluntha. Iye sadanene chinthuchi chifukwa adali onyada koma Mulungu adachiika chinthuchi m’mafupa ache. Mulungu adampatsa iye chifundo komanso kumkomera mtima pomupatula iye mwapadera kuti akhale nayo mphamvu yotha kuona zinthu zimene ena samakwanitsa kuona. Mu bukhu la Akorinto loyamba mutu wa 15: ndime ya 10, Paulo adanena kuti iye adali chigawenga koma Mulungu sadamukhululukire kokha koma adamupatsa mphatso yapadera. Yesu amapereka mphatso zambiri, zosiyanasiyana. Muzinthu zonse zomwe Yesu adali ziwalo zake zonse, adazipereka ku Thupi lake. Mukunena kwa tchutchutchu mphatso zonsezi ndi zofanana chifukwa zonsezi ndiye Yesuyo. Koma mphatso yomwe Mulungu adamupatsa Paulo idali ya utumwi. Paulo adanena kuti iye “sadali munthu oyenera kukhululukidwa machimo ake. Koma chifukwa adamukhululukira machismo ake ndikumupatsa mphatso, iye adzagwira ntchito modzipereka kwambiri ngati njira imodzi yonenera zikomo Inu Mbuye Yesu pondikhululukira machimo anga.” Mphatso imeneyi idali kuti akathe kuwafotokozera anthu ena za chuma cha mtengo wache wapatali cha Yesu.

Chifukwa kuti Paulo adali ndi mphatso yamtengo wapatali yoona zinthu zomwe anzake sankaziona, iye adafunitsitsa kuthandiza anthu onse a Mulungu kuti athe kuona m’mene angayendere pamodzi. Umu ndi m’mene mphato ya utumwi ilili, n’chifukwa chake mphatso imeneyi ili yofunika kwabasi mumpingo pa dziko lonse loti zungulira. Tayerekazani mutayika akhristu odzipereka okwana zana limodzi pamalo amodzi, onsewo adzakonda Yesu ndi mitima yawo ndipo kudzakhala kufuna kwawo kuti amumvere Yesu. Koma kopanda chiyanjano ndi mtumwi nthawi zina zimakhala zovuta kudziwa m’mene angayendere pamodzi. Angadziperekere, akhristu okondana angamavulazane wina ndi mnzake, koma mphatso yomwe Yesu amapereka kwa iwo ya utumwi imawathandiza kuti agwire ntchito limodzi.

Kuika Ziwalo Zonse Pamodzi

Tikhoza kutenga ziwalo zonse za galimoto—chowongolero, bampala, mota, chitseko—ndikuziunjika munyumba imodzi. Zonsezo zikhozao kukhala ziwalo zodabwitsa, koma m’malo mwake simungathe kuyendetsa mtunda wautali ngati zidutswa zonse za galimoto sizinaikidwe pamodzi. Zoonadi zeni zeni pa nkhaniyi ndi yakuti mukhoza kupita kuli konse ndi galimoto imeneyi. Mphatso ya utumwi ndiyo imasonkhanitsa mphatso zonse pamodzi. Mumpingo tikufuna mphatso yomwe ingapangitse kuti zidutswa za galimoto zikhale pamodzi. Izi ndi zimene Paulo amanena pa buku la Aefeso 3. Iye amawauza anthu za ukulu wa dzina la Yesu limene limathandiza kuika mpingo pamodzi. Paulo adafuna kuika mpingo pamodzi kuti itchedwe nyumba ya Mulungu. Mphatso zonse komanso akhristu onse odzipereka amafuna mphatso ya utumwi kuti iwathandize kuika nyumba pamodzi.

Mubuku la Aefeso mutu 4, Paulo adanena kuti Mulungu amapereka mphatso kwa mpingo—mtumwi, mneneri ndi mphatso zina kuti pamenepo tikakule tonse pamodzi. Imatiphunzitsa kuti tisakhalenso makanda, imatithandiza kuti tikule kufikira muuphumphu wonse wa Yesu Khristu, kutithandizira kuti tikaumbike pamodzi. Paulo adanena za kufunikira kwa mphatso ku mpingo kuthandizira anthu abwino kuti amangirirane pamodzi.

Makalata ambiri a Paulo amalankhula za ntchito zochitika zenizeni. Iye sadakambe zambiri za Yesu Khristu, koma makamaka zinalimbikitsa okhulupirira m’mene angakhalire pamodzi kwa wina ndi mzake. Iye adawaphunzitsa iwo ndi zinthu zochitika zeni zeni kuyambira ndalama, ukwati, ana ndi akazi amasiye, komanso m’mene angamangirirane mumpingo mokhudzana ndi ulamuliro. Iye adawaphunzitsa zokhudzana ndi kupembedza kwawo pamodzi, misonkhano, komanso m’mene angamangirirane pa zinthu zosowa zawo wina ndi mnzake.

Chiphunzitso cha zidutswa zabwino za galimoto (kuti m’mene zikhalire galimoto) izi ndi zimene mtumwi Paulo amachita ndi mphatso yache iye amafuna kuwaphunzitsa kuti akhale pamodzi ndi kupita kwina kwake, ifeyo sitikufuna kukhala ngati mkoko wanthochi omwe siungathe kupita kwina kuli konse. Ife tikufuna kukhala Basi ya Yesu yomwe ingakwanitse kupita kwina kulikonse. Tikufunika kumangika pamodzi kenako ndi kuphinzira m’mene tingagwirire ntchito muchikondi.

Paulo akutiuza kuti ndichinthu chabwino kukhala ndi mafunso a zinthu zochitika. Mubuku la Akorinto woyamba mutu 1, tikuwerenga za banja la Kloe lidayenda mtunda wokwana 100 milosi kuti akathe kumufunsa mafunso Paulo. Amakamufunsa za magawano chomwe iwo mu mpingo wakumeneko zokhudzana ndi mabanja, komanso chomwe iwo angachite tchimo likakhala liri pakati pawo. Chifukwa kuti mphatso yake idali ya utumwi adatha kuona chomwe iye angachite. Anthu a Mulungu adali kumufuna Paulo kuti athe kuona komanso kuwathandiza. Paulo chonsecho sadali “opsa wina aliyense ayi.” Iye adali kudziwa bwino lomwe za chifoko chake mumtima mwake, kuti tsiku lina iyenso adachitapo uchimo asadatembenuke. Koma chifukwa Mulungu adamukonda Paulo, n’chifukwa amafuna kunena “kuti zikomo” pogwiritsa ntchito mphatso yake kwa anthu a Mulungu.

Mafunso Ofunsa Zinthu Zenizeni Zokhudzana Ndi Udindo Wa Amuna Ndi Akazi

Komanso ndikadakonda amai adzivala bwino modzilemekeza, osati ndi tsitsi langale zamtengo wapatali ngati golide, kapena zovala zamtengo wapatali, akhale ndi makhalidwe abwino ovomere kwa akazi onse wopembedza Mulungu. Akazi ayenera kuphunzira mwakachetechete, koma sindilola ine akazi ayenera adzimveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyanzi, ndi chidziletso, osati ndi tsitsi loluka, ndi golide kapena ngale, kapena Malaya a mtengo wache wapatali, komatu; (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. Mkazi aphunzire akhale wachete m’kumvera konse. Koma sindiloloa ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. Adamu adali oyamba kulengedwa, pambuyo pake Eva. Adamu sindiye adayamba kunyengedwa ndi chinjoka koma mkazi ndiyo. Mkazi adapulumutsidwa mwakubala mwana ngati akhala n’chikhulupiriro, n’chikondi ndi n’chiyeretso. (1 Tim 2:9-15)

Izi zikungofanana ndi mawu omwe akupezeka m’buku loyamba la 1 Akorinto mutu 14, Paulo adalemba mawu onsewa ndi mzimu wa Mulungu. Ndiye n’chifukwa ndikufuna kuti timvetsere zomwe mzimu woyera amaganiza komanso pamene iye amalemba zinthuzi. Mzimu woyera ndi munhu amakhala ndi maganizo komanso zokhumba, monganso mene inu ndi ine tili. Inuyo mukalankhula kanthu kwa ine ndiye kuti mukulingalira zinthunzo komanso muli ndi chikhumbitso chachikulu kuposa umo mwalankhulira. N’chifukwa chake ndafuna kuti timvetsere zimene mzimu woyera amamvera komanso kulingalira chifukwa mzimu woyera ndi munthu, osati mawu okha ayi.

Mtima wake wa Mzimu Oyera umakonda mai kapena bamboo chimodzimodzi. M’bukhu la Agalatiya mutu 3, iye amanena kuti palibe mwamuna kapena mkazi tonse ndife amodzi mwa khristu. Palibe M’yuda kaya Mheleni, palibe mkazi, palibe mwamuna, palibe wakuda, kapena woyera, kapena wachikasu. Alleluya!! Koma tsopano tonse ndife a Yesu. Kodi Yesu adali ndi maonekedwe anji? Ndani akuchidziwa chinthuchi? Iye ndiye wodabwitsa! Chifukwa cha chimenechi, ndichifukwa chake tilinacho chikhulupirio mwa Yesu Khristu, tonse timavala Yesu, palibenso Myuda kapena Mheleni, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi. Izinso Mzimu Oyera adalankhula mubuku la Agalatiya mutu 3.

Malingaliro A Mtengo Wapatali Okhudza Za Ulamuliro

Pali zinthu zambiri zomwe Mzimu Oyera amaganiza zokhudzana ndi mkazi kapenanso mwamuna; zinthu zimenezi ndi zamtengo wapatali tiyenera kuzimvetsa pamodzi. Pamene tikulingalira za mwamuna kapena mkazi, tikuona kuti Atate ndi mutu wa Khristu. Khristu ndi mutu wa mwamuna. Mwamuna ndiye mutu wa mkazi. Kodi Yesu sindiyenso mutu chimodzimodzi Atate wake? Yesu adanena, “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Koma Atate ndiye wamkulu kuposa khristu, ngakhale ndiwo amodzi. Tomasi adanena ndi Yesu, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga.” Atate ndi mwana ndiwo amodzi.

Chachidziwikire kuti Yesu ndiye mutu wa mwamuna. Koma ngati tidavekedwa Yesu tili naye pamodzi Yesuyo. Apa tikuona kuti pali ulamuliro pakati pa mwamuna ndi mkazi. Mwamuna aposa mkazi chimodzimodzi Yesu ali oposa mwamuna. Pamene mwamuna ndi mkazi ndiwo amodzi mwa khristu. Choncho, kunena momveka bwino tikutathauza kuti mwamuna ndi mkazi ndiwo amodzi (ofanana). Koma ngakhale zili choncho pali ulamuliro pakati pa mwamuna ndi mkazi.

Zinthu izi ndizo za mtengo wapatali ndipo muyenera kutchereza. Mwamuna angathe kutumikira mkazi ndi mtima wanu wonse. Mwamuna ayenera kukonda mkazi kumuchengetera mozama. Mwamuna, munjira ina iliyonse ayenera kukhala kapolo kwa mkazi. Ngati chimodzimodzinso khristu adabwera kudzatumikira mpingo. Ngakhale kuti Yesu angathe kusambitsa mapazi athu ngati kapolo angachitire, komabe ali ndi ulamuliro. Chimodzimodzinso, mwamuna achengetere komanso akonde mkazi, mpakana adadziyesera yekha kapolo kwa iye munjira ina iliyonse, iye ali nawo ulamuliro pa mkazi, ndipo mkaziyo ayenera kumvera ku zimenezi.

Ngakhale kuti zili Yesu ali ndi okoma mtima kwa ife komanso kutikonda ife sindicho chifukwa kuti ife tiyiwale ulamuliro wake, kodi sichoncho? Muli dongosolo mwa Mulungu la kachitidwe kazinthu. Muli ulamuliro mwa Mulungu. Pamene Mzimu Oyera amalankhula nafe pa 1 Akorinto mutu wa 14, ndiso 1 Timoteo mutu wa 2, izi sizikutanthauza kuti amuna ndi olamulira, kulamulira mkazi ndi nkhonya ya chitsulo. Komanso mkazinso sikapolo kuti ayenera kuti adzithawira kukonda mumdima. Tiyenera tikondwerere mphatso adapereka kwa akazi athu, ngakhalebe amadzipereka pa mphatso zomwe Mulungu adawapatsa mitima mwawo. Koma akazi ayenerabe kuzindikira za ulamuliro umene Mulungu adauyika pa amuna. Choncho zinthu zonse ndi zamumtima. Zinthu zonse zotchedwa chi khristu zimakhudza mtima osati malamulo. Yesu sadatininkhe ife malamulo m’malo mwake adatipatsa ife mtima wake. Iye adatiphunzitsa ife kuganiza monga momwe iye angaganizire. Choncho cholinga chathu chachikulu ndicho kukhala ndi mtima omwe iye amafuna ife titakhalira monga mawu opezeka mabuku a 1 Akorinto 14, kudzanso 1 Timoteo 2, Baibulo sindiyo Buku la malamulo lokha komanso m’mene timapezamo moyo. Kodi zimenezi zikuoneka bwanji m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku? Muchiyanjano chomwe chilipo pakati pa mwamuna ndi mkazi, mwamuna adzadyetsa, kusamalira, komanso adzachengeta mkazi wake. Adzautaya moyo chifukwa cha mkazi munjira ina iliyonse, ngakhalenso kupitirira apo kukhala kapolo chifukwa cha Mpingo. Chimodzimodzi mkazi ayenera kukhala otchereza kwa mwamuna chifukwa ndi mtima wake. Mtima wake wa mkazi ndi kutchereza mawu onse komanso kuchita zomwe mwamuna akufuna. Ili si lamulo koma m’mene Yesu amakondera kuti ife tizikhalira m’mtima mwathu. Mukuchulukira komwe mwamuna angakhale nayo nthawi yochita zomwe tatchula pamwambapa, mochulukira mwamuna adzamvera kulankhula kwa Mulungu. Komanso mkazi akakhala ndi moyo womvera kwa mwamuna, iyenso adzakhoza kumvera kulankhula kwa Mulungu. Mawu amanena kuti, “Anthu awiri adzayenda bwanji asanapanganiretu?”

Ulamuliro Umatimasula Ife!

Zinthu zonsezi tatchulazi, ndi zofunika. Ngati mpingo uli pamodzi, komanso ngati mitima yathu ndi maganizo zili zabwino, ndipo mwamuna adzakhala wochita ulemu komanso okonda akazi onse (am’mene sadzasowa ngati mipando). Amuna adzayamba kukonda mphatso zomwe zili mwa mai ndipo iwo sadzalola kuti mphatso zomwe zili mwa iwo zikwiririke m’nthaka. Nawonso alongo adzayamba kulemekeza abale, pamene ali pachiyanjano cha oyera mtima, ndipo iwo ngati akazi adzatha kudziwa ulamuliro wa amuna osafuna kukhala pamwamba pa ulamuliro wa amuna. Paulo adanena, “Ine sindilola mkazi aphunzitse komanso akhale ndi ulamuliro pa mwamuna.” Ngakhale angathe kupereka mphatso zawo. Mwachitsanzo: Ngati mlongo wina ali ndi kanthu kena m’mtima mwake kofunika kulankhula, iye sayenera akwirire luntha lake. Iye sayenera kuti akwirire mphatso yomwe Mulungu adamupatsa mphatso yomwe ili mwa iye. Ife timafuna zonse za Yesu. Choncho ngati mlongo ali ndi kanthu komwe kakumutentha mumtima mwake kofunika kulankhulidwa, wayenera mlongoyu apemphe abale pofuna kulemekeza ulamuliro oposa wake nthawi zonse. Ngati pali mwamuna wa ulamuliro oposa wake, ayenera kumufunsa ngati koyenera kulankhula. Komanso ngati kungakhale kotheka mwamunayo angathe kufunsa mpingo ngati kuli koyenera kuti mlongoyo alankhule kapena ayi. Ngati kungakhale kuti mwamunayo aona kuti ndi kosavomereza mlongoyo kulankhula komanso mpingo wawona kuti mkaziyo asalankhule panthawiyo, iye ayenera akhale okondwa kukhala chete. Mkaziyo sayenera kuti akwiye chifukwa adakanizidwa kulankhula. Sayenera kunena taonani, “kuyambira lero sindidzalankhulanso kanthu pakati pa mpingo.”

Umu ndi m’mene amai angakhalire a Yesu kwa aliyense, komanso mwamuna pokhalabe ndi ulamuliro. Wamuna angathe kutenga mphatsoyo, koma munthu wa mkazi samadziika yekha pamwamba pa mwamuna. Pamene muwerenga ziphunzitso za mawu a Mulungu nonse pamodzi, chimene mungaone ndi chakuti Mulungu ali mtima wolunjika kwa amai. Mkazi sindiye mpando kapena gome m’chipinda. Mlongoyo ali ndi moyo mwa Yesu ndipo tiyenera kukhala omufunitsits mlongoyo. Komanso mlongoyo ayenera kumvetsetsa za ulamuliro wa Mulungu ndipo sayenera kukhala onyada. Iye ayenera kukhala odzichepetsa kuti athe kudzipereka yekha nsembe. Iyi ndi dongosolo la Angelo, dongosolo la Mulungu Atate ndi dongosolo la Yesu mwana, komanso dongosolo la mwamuna ndi mkazi. Tonse ndife amodzi, koma pali ndondomeko mwa Mulungu imene imathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino. Ndife ofanana, komanso mphatso ya mkazi ikhoza kukhla yabwino koposa poyerekeza ndi ya mwamuna wake, koma Mulungu adamupanga kukhala wa mwamuna. Ichi n’chifukwa chake pali dongosolo. Komanso mwina iye samayenera kukhala ndi ulamuliro. Koma Mulungu amasankha zinthu zimene tiyenera kuzilemekeza, choncho tonse pamodzi tiyenera kugwira ntchito yobweretsa mphatso komanso kukonda ndondomeko yomwe Mulungu waika kuti tiyende pamodzi tonse.

Kumene ndimakhala ine kuli amai ambiri omwe ali ndi mphatso. Mpingo kumeneko ndi odalitsika kwambiri chifukwa uli ndi amai olimba kwambiri mwa Yesu. Iwonso akhoza kukuuza za ndondomeko yomweyi monga ngati chinthu choyendetsa zinthu mwa dongosolo la Mulungu—chinthu ichi sichiwakanikiza iwo pansi; koma m’malo mwake chimawamasula. Pali ufulu wambiri popeleka mphatso zawo ngati nsembe m’malo mongotenga potsatira ulamuliro. Ndi chinthu chamtengo wapatali kukhala munthu wodzipereka. Akazi pa iwo okha adzakhoza kukuuzani kuti ulamuliro umawamasula m’mitima yawo ndinso umawapanga iwo kuyimba nyimbo m’kati mwawo pamene akupereka nsembe ya mphatso zawo koposa kutsatira ndondomeko. Choncho pamene sitiri kufuna kupondereza pansi mphatso zonse, mphatsozo zimabwera ngati zopereka kuchokera kwa alongo, izi ndi zoona makomo, komanso m’ziyanjano za oyeramtima. Uwu ndiwo mtima omwe Yesu amaufuna—mtima omwe iye angaudalitse.

Kodi mukukumbuka zomwe Ambuye Yesu adanena kwa Kentuliyo, Msirikari wa Chiroma? Iye adanena kwa Kentuliyoyo kuti mwa iye, adaonamo chikhulupiriro chachikulu kuposa anthu onse M’Israeli. Chikhulupiriro chomwe Yesu adali asanachionepo chidapezeka mwa munthu mwamuna amene amadziwa kukhala pansi pa ulamuliro komanso ndikukhala ndi ulamuliro. Mlonda wachiroma adanena kuti Iye angathe kunena kwa watchito wake “Pita”, ndi iye adzapita. Adzanenanso kwa waichito wina “Bwera kuno”, ndipo iye adzatero. Iye adanenso kuti ndiye munthu odziwa ulamuliro ndiko kunena kuti Pita ndinso Bwera ulamuliro wake. Yesu adanena kuiti uyu ndi munthu wachikhulupiliro Chachikulu yemwe Yesu adamuonapo chifukwa amadziwa kumvera ulamuliro. Ichi chinali chomwe chinamumasula iye, osati chomwe chingamukanikize iye pansi.

Pamene Yesu ali mutu wa Mwamuna, mwamuna amamasuka. Yesu adanena kuti ngati sitingathe kukhala kapolo wache tingathe kukhala kapolo wa tchimo. Ngati sitingathe kumulola Yesu kukhala Mbuye wathu, uchimo udzakhala mbuye wathu. Koma ngati mwana adzatiyesa ife mfulu tidzakhala mfulu ndithu. Kodi mukutha kuona zinthu izi m’moyo mwanu? Mukangomumvera Yesu, inuyo mudzamasulidwa? Koma pamene mungakhale osamvera Yesu ndi osalungama m’mtima mwanu.

Izi ndi m’mene zilili ndi mwamuna ndi mkazi. Ife tikatsalira ulamuliro wa Mulungu, sitikhalanso akapolo; ndife mfulu. Koma ngati sititsalira timakhala akapolo ku zolakwika zathu. Mkazi yemwe Sali pansi pa ulamuliro ndiye osalungama m’mtima mwake. Iye adzakhala okhumudwa ndi osakonzeka, Mulungu ndiye amapereka ulamuliro m’banja komanso m’mpingo—izi sizitanthauza kuti pali munthu wina yemwe ali wabwino kwambiri kuposa wina ayi, kapena kuwafotokozera anzakenso kuti achite chiyani powalamulira chomwe angachite. Iye amapereka ndondomeko ndi ulamuliro kuti tonse tikhale omasuka kuchikondi ndi dongosolo la Mulungu.

Kulankhula Ndi Atate Ngati Banja

Chomwe tikufuna kulankhula apa ndi m’mene tingakhalire, osati m’mene tingakhalire ndi Chiyanjano. Kuyankha mafunso amoyo watsiku ndi tsiku ndikophweka poyerekeza m’mene zingaonekere pachiyambi. Pamene tidzathe kukhala ngati banja muchoonadi pomwepo zithu zidzayamba kumveka bwino. Anthu ambiri ali okodwa pakati pa banja ndi chipembedzo ngati kabungwe. Gulu lina la anthu achabe a chipembedzo ndi banja. Pamene enanso akodwa pakati pongokhala opita kutchalitchi ndinso banja. Pamene chonsecho Mulungu akubweretsa Mpingo wake kuti ukhale ngati banja, pamenepo zinthu zimayamba kumveka bwino. Pamene tidzadziona pa ife tokha ngati banja, mayankho a mafunso ambiri omwe tingakhale nawo amayamba kupezeka. Chifukwa timayamba kukondana wina ndi mnzake mowirikiza, timagawana mbali ina iliyonse ya moyo wathu umalukika pamodzi tsiku lili lonse, amuna amadziwa kukhala bwino ndi akazi komanso akazi nawo amadziwa m’mene angakhalire ndi amuna. Ngati tingadziwe m’mene tingachitire m’makomo athu ndinso makwalala, tidzadziwa m’mene tingachitire misonkhano.

Mu zinthu zonse, tiyenera kuzindikira ndondomeko ya Mulungu, komanso tiyenera kusauzima Mzima. Tiyenera kuzindikira dongosolo, komanso sitiyenera kukwirira luntha lathu. Choncho, ngati Oyera mtima asonkhana pamodzi Mulungu amapereka pemphero mumtima wanga, ngati munthu wamwamuna ndine oyeneranso kufunsa ngati kuli koyenera kuti ndipemphere. Koma ngati amene akufuna kupemphera ndi wamkazi ndi chichidziwikire kuti ayenera apemphe kaye mwamuna ngati kuli koyenera kuti apemphere, mwamunayo naye ayenera afunse anthu onse osonkhanawo, “Kodi ndikoyenera ngati mlongoyo ayenera kupemphera?” Ngati mwamuna ndi msonkhano onse aganiza kuti ndikoyenera, mlongoyo ali pansi pa ulamuliro. Iye ndiwokutidwa ndi ulamuliro ngati timulola iye kutero, koma ngati iye angachite zinthuzi payekha, izi zidzakhala kunja kwa ulamuliro (dongosolo). Koma ngati ife tonse tingamlole kuti apemphere mlongoyo ali pansi pa ulamuliro ndipo nthawi yomweyo zinthu zili bwino. Zinthu izi nthawi ndizoona.

Tiyenera kumvetsa zinthu zina zake zokhudza pemphero. Mawu oti ‘Pemphero’ amamveka ngati achipembedzo ku makutu athu. Pamene tikhala ngati banja, mnjira yomwe tingagwirire tchito limodzi zimapangitsa kuti zinthu ziyambe kumveka bwino pakusonkhana ife. Pamene tidzakhale oyandikira kwambiri ndi Mulungu, mapemphero athu adzayamba kumveka. Mudzipembedzo zonyenga nazonso, anthu amapemphera mapemphero. Mwa Yesu, m’chikhristu, timakhala ndi chiyanjano ndi Atate athu okondedwa. Choncho, kunena kuti “Mapemphero okumana pamodzi amatanthauza chiyani?” Kodi zimatanthauza chiyani tikamanena kuti kukhala ndi banja la Mulungu pamodzi? Kodi mukutha kuona kusiyana” Wina ndi wachipembedzo, ndipo wina ndi wachiyanjano.

Sitimanena kuti “mapemphero” koma m’malo mwake timanena kuti kulankhulana ndi Atate—m’mene mwana amalankhulana ndi atate ake. Kodi mwana angakonze mnsonkhano ndi atate ake, kodi angathe kulankhulana ndi atate ake chifukwa amawakonda iwo? Tangoganizirani tiyana tating’ono titasonkhana m’kachipinda adzayenera kukonza mnsonkhano kuti akambirane ndi atate awo? Kodi adzapanga mnsonkhano ofuna kukumana ndi bambo wawoyo. Iyi sidzakhala mapemphero okumana. Koma m’malo mwake idzakhala banja kukumana pamodzi ndi atate wawo.

Tsopano ndiganiza mwayamba kuona mapemphero aumodzi amagwirira ntchito. Siziyenda zinthuzi! Zimene timachita n’chakuti ngati m’bale akufuna kulankhulana ndi atate ngati iye atha kulankhula ine ndifuna ndilankhule nawo atatewo!” Umu ndi m’mene timapempherera pamodzi pagulu. Umu ndi m’mene timalankhulirana ndi Mulungu pamodzi, pamene Mulungu akutakasa mitima yathu. Mlongo wina akhoza kufunsa m’bale wina, “Kodi chikhoza kukhala choyenera kulankhula ndi atate tsopano?” Iyeyo ali mudongosolo chifukwa ali pansi pa m’baleyo yemwe ali ndi ulamuliro pa iye. Koma izi sizitanthauza kuti mlongoyo alibe ufulu akutha kulongosola za dongosolo loyenera. Umu ndi m’mene tingamachitire tikakhala ndi mapemphero, chiphunzitso, komanso tikamafuna kuyimba nyimbo, chifukwa tili ngati banja pamodzi ndi Atate wathu.

Tikufuna tichotseretu miyambo ya anthu ndi chipembedzo-pembedzo zichoke zituluke ndipo ife tingokhala ana wina ndi mnzake. Sitikufuna kukhala achipembedzo, anthu oyera ndi Maina ndi zikhulupiriro za miyambo ya anthu. Tikufuna tikhale ana okondedwa wina ndi mnzake, komanso ndi atate tsiku ndi tsiku. Kukumana kudzadzisamalira kokha chifukwa ife ngati ana komanso banja tingathe kukumana nthawi zonse. Timalankhula ndi adadi athu nthawi zonse. Timabweretsa chiphunzitso cha Yesu Khristu kwa wina ndi mnzake nthawi zonse. Ngati zingapangike kuti takumana pamodzi muchipinda chimodzi, zimakhala zinthu zamphamvu. Komanso izi sizitanthauza kuti zikhoza kukhala zosiyana mphindi makumi atatu zikatha.

Funso Lokhudza Amai

Funso ndi ili: M’baibulo mawu a Mulungu amanena kuti pamene tisonkhana Amuna ayenera akweze manja awo mwamba, koma akazi ayi. Kodi akazinso akhoza kukwezanso manja awo mwamba? Kodi Izi zikhoza kukhala zabwino?

Funso Labwino: 1 Timoteo 2:8-9 akunena kuti “ndikufuna amuna onse kulikonse akweze manja awo kumwamba akamapemphera, popanda mkwiyo kapena kukangana kwina. Komanso ndikufuna amai adzivala modzilemekeza, ndi moyenerera osati ndi tsitsi loluka kapena dzovala za pa mwamba.

Paulo sakutanthauza kuti, amai sayenera kukweza manja awo mwamba popemphera.” Komanso sakutanthauza kuti abambo sakuyenera kuvala moyenera. Ngati m’bale angakwanitse kukweza manja, ayenera akweze manja oyera. Mawu akulu pamenepa ndi “kuyera.” Ayenera kukweza manja omwe ali odzipereka kutchito ya Mulungu komanso ofunitsitsa kumutumikira pokhapokha amai akagwiritsa udyo ulamuliro, koma ali ndi manja ofunikira motumikira Mulungu, iye wayenera kukweza manja ake mwamba. Mulungu sakutiuza kuti abambo sayenera kuvala modziyenereza komanso sakutiuza kuti iwo sioyenera kukweza manja awo mwamba popemphera; kapena kuti ndi zabwino, ngati iwo ali ndi manja oyera, m’mene zilili zovomerezeka kwa amuna onse kuvala modzilemekeza.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon