Kudzadzidwa Ndi Mzimu Woyera Pamodzi!!!
4/8/2003
Lachiwiri la m’mawa a pa 5th October,1999
Panthawi yokhala pamodzi mu Africa, kuthandizira m’chichewa, kutsiyana kwa malingaliro ndi zakumitima kwa abale.
Panopa, mbale amakamba za kukhonza kumva mau a Yesu abwino wokhala ndi Yesu kuti tikakhale akumva mau ake. Izi zili ndi zambiri zochita ndi ife pokhala kachisi wa Mulungu, pa idzi makhomo aku gehena sangatsekuke.
Baibulo likutiuza zakudzazidwa ndi mzimu woyela. Mzimu wa Yehova kukhala mwa ife ndi kutidzadza mpaka pa mathero. Ili ndi lamulo la Mulungu. Izi zithandauza kuti titha kumvera lamulo kapena ayi kuti tidzazidwe ndi mzimu. Tikudziwa pokhala mkhristu, tayenera kukhala mwa Khristu, ndi kuti Khristu akhale mw aife. Amen? Choncho nkotheka kukhala mwa khristu, koma otsazazidwa ndi Khristu. Choncho nkotheka kutsamulingalira Yesu kapena kumumvela momwe tayenera kuchitira. Mwatsoka, ili ndi vuto la a Kristu ambiri lero. Koma pali vumbulutso lochokera kwa Mulungu za momwe izi zingatsithire. Njira yake ndi yokhuzana ndi kumanga mpingo bwino, “makomo a ku gehena tsangatsekuke,” tayenera kumanga miyoyo yathu kuti anthu a Mulungu, kuyamba kuchiyambi mpaka kumathero, kudzazika ndi Mzimu—osati tsogoleri awiri kapena m’modzi, koma anthu onse a Mulungu adzazidwe ndi Mzimu.
Kuzamilatu
Ndingokuyambirani chinthuzi cha mfundo imeneyi. Tiyerekeze muli ndi ndowa ya madzi. Tinene kuti pokhala ndi ndowa ya madzi kapu ya madzi ili ndi chivindikiro pamwamba pake. Kapu ili ngati munthu yemwe ali ndi Yesu mkati mwake. Kwa munthu ameneyu kukhala mukhristu, wayenera kukhala mwa Yesu. Ndiye kapu yozaza ikhale mu ndowa. Ngati munthu ali wozazidwa ndi Mzimu, adzakhaliratu mwa Khristu, ngati muli mphyeya mu kapu, idzakhala pa mwamba. Ngati sitili odzazidwa ndi Mzimu Woyera, ngati munthu, tayenera kukhala mwa Khristu ndi kupulumutsidwa, koma sitingaze mene mwa Yesu. Paulo alembera ku mpingo wa ku Agalatiya (Ch4), “Ndili mukuwawa wa kubereka mwana, pamene ndili pafupi kukhala ndi mwana. Ndikumva kuwawa kwa kubereka Yesu apangidwa.” Amalembera kwa anthu amu mpingo waku Galatiya amene adali wopulumutsidwa kale (zikunena za izi mu chapter 3:. Mudali kufooka kwakukulu mu mpingomu, choncho. Tsadali khristu wokhazikika mwa iwo. Adali ndi mphyeya mwa iwo, pweya wa dziko, koma osati khristu. Sono adayanjana pamwamba. Iwo tsadazame mu mzimu wa Khristu. Chifukwa tsadali pawokha, wozazika ndi Khristu, tsadamire mwa Khristu.
Aroma 12:1-2 akutsindika kuti mwa kudziwa zabwino, chifuniro chabwino ndi changwiro cha Mulungu kuti timumve Mulungu ngati munthu, tidzazidwe “Pantchito za dziko.” Titsakonde zomwe dziko limakonda. Titsakhale ndi malingaliro a dziko kapena kukhula monga momwe arankhulira. Tisinthe manja athu mosiyana ndi a dziko. Timwaze ndalama mosiyana ndi momwe a dziko amamwazila nthawi yawo ndi ndalama. Mulungu anati kupembedza kwithu kwa uzimu kutsakhale ngati kwa dziko mu zovuta zilizonse. Mulungu adati kuti tikhale akusandulika, ngati kuchokera ku caterpillar kupita ku butterfly, mwa mau a Mulungu. Ndiye tikhoza kumva Mulungu “Ndiye tikhoza kudziwa zabwino chifuniro chabwino ndi changwiro cha Mulungu.” Ngati tili ndi zina zamudziko mwa ife, m’malo mwa kusandulika kwa mau a Mulungu, tidzayanjana pamwamba. Ngakhale tingakhale mwa Kristu ndi ku pulumutsidwa, sitili ozama mu cholinga cha Mulungu.
Tikufuna M’modzi ndi Nzake
Cholinga cha mpingo ndi chothandiza aliyense kudzazidwa ndi Mzimu Woyera, sono tikhoza kuthandizana kuchotsa dza mudziko mu miyoyo yathu. Ku Hebrews 3 akuti, “Tayenera kuuzana ndi kuthandiza ndi kuchenjezana wina ndi mzache tsiku lililonse kuti patsakhale modzi mwa ife amene adzachite manyazi ndi kukanidwa. Baibulo likuti tiyenera kuthandizana tsiku ndi tsiku. Tichoke mumanyumba mwathu ndi kulowa mumiyoyo ya ena, mu malo ogwilila ntchito ndi mu ma nyumba mwa azizathu. Tayenera kuthandizana kuti tisakhale adzichito chito za dziko. Anthu ena mati, “ndili ndi ubale wawo ndi Mulungu wawo.” Izi sizomwe Baibulo likunena. Baibulo likuti “langidzanani wina ndi zache kuti pasadzakhale okanidwa ndi wotsalandilidwa.” Baibulo likuti ndife a nsembe awokhulupirira ndipo tayenera kuthandizana wina ndi nzake kuti tikazazidwe ndi Mzimu Woyera. Timagwiritsa ntchito mphatso zomwe zili mkati mwa ife kuthandiza ena kuti adzaze ndi Mzimu Woyera. Membala wina aliyense wa mpingo athandize membala nzake kumpingo.
Izi ndi zinthu zosiyana momwe Anthu ambiri pa dziko lapansi amangaira pamodzi cikhristu. M’mayiko ambiri, anthu amabwwera pamodzi pa tsiku la sabata ndi pa misonkhano. Momo amakhala ndi “Mumpingo yambiri padziko la pansi kulibe kuti dziko liti, Anthu amabwera pamodzi pa sabata ndikukhala mumizele. Ndiye akulu .——akulu (anthu oyera) amabwera kumbuyo kwa anthu ndi kuyambitsa mapologalamu. Koma izizi simomwe Baibulo limanenera ayi kuti cikhristu cimakhalira choncho. Tili nayo, mmayiko yosiyana siyana, momwe tamangira mpingo molakwika mudzankha zoposa tusauzande (2000) mdzaka zapitazo.
Chifukwa chiyani tamanga molakwika mpingo chonchi? Chifukwa mamangidwe ache amangidwa ngati a chipangano cha kale, momwe akulu a sembe ali momo ndipo anthu ambiri ali momo kuwonerera. A Levi (wasembe) amapeleka sembe za anthu onse. Iyeyo amakhala mu nyumba ya Mulungu wa padera dera amene amawathandiza anthu kuti amudziwe Mulungu. Ichi ndi chabwino ngati inuyo munakhalapo zaka thusauzande (2000) kumbuyoku ngati ife tifuna kukhala a Kristu osati Ayuda, ndiye timange ngati Akhristu AMEN? Tamanga molakwika chikristu mumayiko wosiyanasiyana koma, Mulungu alikubwezeretsa tsopano mpangano la tsopano Mchikristu mudziko lonse la pansi.
Ufumu wa Ansembe
Mpangano la tsopano anthu onse a Mulungu aynera kukhala a sembe kwa wina ndi mzake. Chikumbu kumbu cha Mulungu si cha kuti munthu ozozedwa modzi azilamulira mapologalamu ayi. Mawu a Mulungu akunena kuti Yesu anakwera kumwamba mwamba ndipo anapeleka zipatso pa anthu ake, anapanga ufumu wa ansembe. Iye anayika gawo limodzi la iyi mwini pa anthu ake kuti iwo ndi woona osandulika ang’ono ndi akulu.
Ndi chifukwa chake amafuna mphatso ya wina ndi mzake. Timafuna mphatso zonse Yesu. Pali mphatso zambiri—mbiri chifukwa zonse Yesu anadzithira pa banja lake (mpingo). Ichi ndi chifukwa chake Yesu anati, tonse tili a mbale wina ndi mzake sitifuna ife, mtundu modzi kapena mphatso yimodzi yizimilira patsogolo pathu nthawi zonse. Izizi sitizalora kuchitika pakati pathu. Onse amene osindidwa oona ake ndipo okhala mkati amakhala a kulimbika mmoyo wawo nthawi zonse kwa wina ndi mzake ndipo kuwonesetsa (Aheb 3:12-14) kuti onse ndi a sembe.
Mtima wa Mulungu, mpatso yanu yikale yanga komanso mpatso yanga yikhale yanu. Yesu amatero, “Musamuche wina mw ainu wamkulu, Revelande, Mbusa, kapena wasembe” ngakhale kwa ophunzira ake aja asanu ndi awiri, iye anati “inu nonse muli a mbale,” ngati chiri choona kwa Petulo ndi Yohani nditi ndi choonadi kwa ife tonse Ameni. Mphatso zimene zili mkati mwa ambale ndidzo gawo la Yesu. Ngakhale ana ali nadzo mphatso zimeneso ndi gawo la Yesu. Mphatso zonse zimafunika pa moyo wathu. Ife tonse ndife ambale. Izi ndi zomwe Baibulo limanena.
“Inde lero a mbale, ngati mumbwera pamodzi, pali wina ali mawu achiziwiso, yimbo, kapena vumbulutso,” izizi ndi zomwe kawiri kawiri mawu a Mulungu amanena ku 1 Akorinto 14, “Ngati mumbwera pamodzi, ambale, aliyense ali ndi mawu a chiziwitso, yimbo, vumbulutso kapena uneneri.”
Ngati timakhala choncho, ngakhale osakhulupirira amagwera pamaso pake ndi kulira, nanena, “Mulungu ali pakati panu.” “Ngati vumbulutso lavumbuluka kwa munthu wa chiwiri ndiye WOYAMBA ASIYE NDI KUKHALA PANSI!” Ichi chi ndi chimene chimathandauza ku 1 Akorinto 14. izi zisimaoneka kawiri kawiri ndi amanena “amakonda kukhala oyamba, amakonda kukhala olamulira komanso kuonesetsa ngati “iwo ndi auzimu eni eni. Ndi kutenga ndalama za oyera mtima.
Ife tiyenera kukhala ufumu wa a sembe. Ife tiyenera kumangilidwa wina ndi mzake tsiku liri lonse. Ngati sitimangirilana, Baibulo likuti tizaumitsidwa ndi kunamidzidwa. Chikumbu kumbu chathu chizamangiriridwa. Ife tidzazakhala kuyerekedza! Kutengeka ndi zinthu zonse zimene zimaoneka zochimwa kumoyo wanthu. Ngati sindingapeze anthu ambiri ozipeleka otsatira a Yesu kukhudziwa ndi moyo wanga tsiku ndi tsiku ndi ena Sali okhudzidwa ndi moyo wanga ndiye kuti tidzakhala ounotsidwa mitima ndipo sitidzadzidwa choonadi. Izi ndi zimene Baibulo limanena nthawi zonse. Tiyenera kukhala mu moyo pamodzi kuthandizana tsiku ndi tsiku. Ngati mukufuna kutsutsa baibulo ndi kunena kuti siloona, ndiye kuti mudzayamba chipembedzo chanu. Anthu ambiri ali mu chipembedzo chotero. Koma nonse a inu mwasonyeza pa kuzipeleka kuti muchita chilichonse cha Yesu. Choncho tiyeni tipite kukwera pamodzi ndi iye tsopano!
Tsiku Lililonse
Yesu akumanga mpingo wake umene makomo a ndende sadzaulaka. Yesu akubweletsa mphatso kuchokera kwa anthu ake ndikulora iwo kuti akhale ansembe tsopano—osati msonkhano, koma tsiku ndi tsiku. Baibulo limati ululani machimo kwa wina ndi mzake ndi kupemphererana wina ndi mzake kuti muchilitsidwe. Tadikilani kodi anthu onse a Mulungu amachita zimenezi? Ndi liti lomaliza kuwulura machimo anu kwa mbale kapena mulongo. Kodi mukufuna kuchilitsidwa? Kodi mukufuna mphamvu ya Mulungu mu moyo wanu? Baibulo limati lapani machimo anu kwa wina ndi mzake. Chifukwa chiani sitipanga? Sitipanga izi kwa nthawi zonse chifukwa timaopa. Sitipanga chifukwa cha miyambo ya anthu imene yatimeza ife. Taleka kukhala woyenerera chifukwa cha kuzikonda. Mulungu akuti kwa inu ndi ine. Titsegule mitima yathu kukhala ozichepetsa ndi wofewa. Kuwulura machimo kwa wina ndi mzake tsiku ndi tsiku ndi kupemphereeana kuti tichiritsidwe.
Iyi ndi imodzi imene timathandizira wina ndi mzake kudzazidwa ndi Mzimu Woyera. Timatsegula mitima yathu kuchengetana wina ndi mzake tsiku lililonse. Tsiku ndi tsiku kuti pasaoneke wowumitsa mitima kapena kunyengedwa. Atero Ambuye, Mulungu wanena kuti tiyenera kutsegula moyo wathu kwa wina tsiku ndi tsiku, tsiku lililonse ngati tizamanga munjira yotere yokumanirana pa Mulungu ndiye kenaka tipita ku nyumba zathu ndi kukhala mosiyana ndi mabanja. Tidzakhala osamvera Mulungu.
Mulungu walankhura momveka bwino pamene tingayendere pamodzi ndi kuthandiza wina ndi mzake kudzozedwa ndi Mzimu Woyera. Mulungu anati, “thandizanani wina ndi mzake tsiku ndi tsiku.” Mulungu anati, “Tikuika mzimu wanga ndi mphatso mkati mwa inu ndiye taya moyo wako chifukwa abale tsiku ndi tsiku.” Mulungu anati, “lapitsanani machimo anu kwa wina ndi mzake tsiku ndi tsiku.” Mulungu anati, “Tengelelani zothobwetsa ndi kukwaniritsa lamulo la Kristu.”
Muntha kuona kuti ndi chinthu chochitika tsiku ndi tsiku. Mungatenge bwanji zobvuta za munthu wina mu msonkhano kukwaniritsa lamulo la Ambuye tiyenera kutengelana zobvuta za munthu wina. Nanga zothodwa zimenezi zili kuti? Kodi zili ku misonkhano wa Mulungu? Ai, zobvuta zamoyo zimapezeka ndi ana athu, ndi akazi athu ndi amuna athunso mu zintchito zathu. Zobvuta zamoyo ndi pamene chisilamu kapena chipembedzo chonama ndi mabanja athu a thupi atida ife chifukwa choti tabwera kwa Yesu. Amaswa moyo wathu ndipo sitidziwa chimene tingachite. Tikufuna inu kuti mundithandize mabvuto anga pamene mwana ali odwala. Sindifuna kumva uthenga wako lamulungu singapite kumeneko pamene mwana wanga adwala. Sindifuna kumva nzeru wako yozama ndi kulankhura kozama ngati sungathe kundithandiza pamene ndili ndi mabvuto ndi mkazi wanga. Ndi chochitika tsiku ndi tsiku sizokhudza misonkhano ai. Kutengelana zothobwetsa tsiku ndi tsiku ndi kukwaniritsa lamulo la Kristo.
Tamanga molakwika mpingo mu mayiko ambiri kwa zakanso zambiri. Mulungu ali kuitana tsopano anthu amene ali ndi kulimbika ndi kuzichepetsa ndi kuzipeleka yekha kuti imangidwe bwino. Ngati tidzamanga nyumba ya Mulungu kusata maonekedwe amene anaikidwa. Makomo a ku Hade imene ndagwira. Mudzachita, Atero Ambuye. Tikaona monga Yesu pamene adali kuno. Yesu sanangokamba chabe ai. Anakhala moyo Yohane 1 amatero “Moyo ndipo unasanduka kuunika kwa anthu.” Ndi chonchoso mpaka lero moyo wa tsiku unasanduka kuunika kwa anthu. Ngati tikufuna anthu kuti aone chikondi cha Mulungu ndipo ngati tifuna kuti abwere kwa Yesu mmalo mwa ndalama ndi mphamvu ya chisilamu, ngati tikufuna kuona anthu ndi kunyada kwawo. Tiyenera kukhala mu moyo wa Yesu pamodzi tsiku ndi tsiku.
Mbali ya Aliyense
Talankhula zokhala ngati kapu ya madzi yodzadza ndi kulowa mwa Yesu. Tingalankhulenso za chinthu mpika wa mbatata ndinso mapika wa chimanga chosatongola umu ndi mmene tamangira mpingo kwa zaka 2000 zapitazi anthu amabwera onse pa lasabata monga anthu okhala ngati mbatata kapenanso monga chimanga mtima wa Mulungu suli mu mphaka wa mbatat kapenanso aliyense payenkha mu mphaka pamodzi kwa masiku awiri limodzi, kapena atatu pasabata. Pokhala mu nyumba mnalowa chipembedzo mopembedzelamo si mwabwino ngati sitingathe mitima yathu ndi mmene tingagwirile wina ndi mzake tsiku ndi tsiku. Msonkhano pawokha sumangitsa kuti ndi mpingo wa mbaibulo ai. Uku ndi kumene mbaibulo amati malo ophunzitsilamo mphika wa mbatata pa yekha payenkha si mpingo. Mungathe kuponya mbatata zonse kapenanso zimanga zonse mu mphika lamulungu lililonse komabe sukhala mpingo simpingo ai. Mpingo woona umafanana ndi mphika wa mbatata zosenda ndi chimanga chosendedwa ndipo simakhala zofanana. Monga zimodzi mongaso okhala amodzi mu chikhulupiriro. “Mtima umodzi moyo umodzi, onse pamodzi ndi machitidwe amodzinso. Angakhale ndife ambiri koma ndife mmodzi kubatizidwa ndi Mzimu mu thupi limodzi pamene wina sanganene kwa mzake sindifuna iwe mpaka nthawi yina sabata ya mawa.
Mphika wa mbatata yosenda kapenanso chimanga ndi moyo wanu kukhala mbali ya mbali ya ine ndi moyo wanga kukhala wa ine. Pamene til amodzi monga Yesu ndi Atate ali—pamenepo ndiye mpingo wowona ena angapulumutsidwe inde popanda moyo umenewu koma sakupindula kwa Yesu pa msonkhano. Powonetsera kudziko za mphamvu yake ndi moyo. Ndidzamanga mpingo umene makomo a ndende. Sangathe kuwononga! Pokula msinkhu, kwa ana ndi akazi anu ndinso okhala nawo pafupi ndi ena olumikizidwa ndi kulukidwa pamodzi. Umenewu ndi mpingo mu pulani ya Mulungu.
Pamene moyo wanu uli mbali ya moyo watsiku ndi tsiku pamene mphatso yanu uli mbali ya ine ndi mphatso yanga ndi mbali yanu tsiku ndi tsiku. Pamene ndiulura machimo kwa inu ndipo mukuulura machimo kwa ine ndipo tipemphererana wina ndi mzake kuti tichilitsidwe. Pamene mundidziwa ine koposa choncho mungathe kuwona kuchokera mu maso anga kuti ndawaidwa moyo ndipo muli kunditengera zothodwa—Ndi pamene mpingo udzayamba kukhala mpingo wa Yesu. Yesu anati umu ndi mmene (Asilamu, Amboni za Yehova, Amarmori ndi onse woofooka ndi othentha chabe mu chipembedzo) adzadziwa kuti chikristu ndi chochokera ndithu kumwamba. Onse adziko adzadziwa kuti tili a iye pamene tikondanilana
Mungathe kunena za mwazi wa Yesu ndi mau a Mulungu koma mpaka mutayamba kukhala ndi moyo wokondana wina ndi mzake ndiye kuti odzangokhala mau chabe. Ngati dziko lidzaona ife kukondana wina ndi mzake chifukwa choti moyo wathu wataika pothandiza wina ndi mzake ndiye kuti moyo wa Mulungu ndi mphamvu idzakhala ya mphamvu koposa. Mukumizidwa ndi mu mphamvu (ndipo tidzapachitikidwa ndi kudedwa, kunamizidwa monga mwa Yesu analankhulira!).
Atate akonda mwana ndipo tidzayamba kuoneka monga mwana kuwala monga nyenyezi zakumwamba. Mudziyikidwa pamwamba pa Phiri umene sangathe kubisika. Ameneyo ndiye Yesu ndi cholinga cha mkwatibwi wake, mpingo sitingoyenera kukhala owonera chipembedzo ndi kunena mau ena tiyenera kusiya kukhala mu mipando monga zidoli kumvetsera kwa wina ali kulankhura. Tiyenera kuti tikhudzidwe kwatunthu mu miyoyo mozama ya azanthu tsiku ndi tsiku abale pakati pa abale. Izi simsonkhano okha koma kupeleka mitulo kwa ine ndiponso ine kwa inu tsiku lililonse mu zinyumba zathu ndi muzintchito kumunda ndi kubanja athu izi zimafunika kusintha mmene mumagwilitsira nthawi yanu ndipo musinthe zinthu zimene munazitenga kuti ndi zoyambilira mu moyo wanu ndi kutero “Thangani mwapeza ufumu wa Mulungu.”
Banja Lenileni!!
Yesu anati ngati mupeleka moyo wanu ndi kukhala mkristo mudzakhala ndi amai ambiri abale ambiri ndi alongo ochuluka kuthandauza kuti mgwilizano wopambana ndi zimene baibulo limathandauza za chikristo! Mudzakhala ndi chiyanjano amene ali pafupi monga mai ndi mwana kapena mbale ndi mlongo pamodzi pafupi—pafupi molumikizana chibale. Sanati abwenzi ambiri kapena otizungulira ambiri Yesu anati mpingo ndiwo zana la mgwilizano umene uli olumikizana monga mai kwa mwana wake.
Mai wabwino amamva kulira kwa mwana wake ndipo amamva kulira kwa mwanayo pamene wabvulala kapena pamene ali ndi njala. Awa ndi kulira kosiyana amadziwa kulira kwa mwana wake molumikiza—zonse zokhudza za mwana wakeyo. Yesu anati mu mpingo wanga woona mudzakhala ndi ubale ochuluka “wolumikizana mongaamai ndi mwana mudzatha kuwona mu maso anga, ndinso ndizatha kuwona mmaso mwanu pamene mwatopa muli ndi njala, mwakwiya ndi pamene odandaula izi siza msonkhano ai sichoncho kodi? Siza lamulungu mmawa mukulalikira, sinchoncho kodi? Simsokhano wolalikidwa lamulungu mwamva kodi? Koma moyo wa tsiku ndi tsiku pamodzi monga amai ndi mwana wake.
Mai kodi angakhale ndi mwana wake lamulungu lokha basi akhoza kukhala mai oipa, sichomwecho? Chidzachitike ndi chiani ndi mwanayo? Mwanayo adzafa. Izo ndi zimene zachitika ndi akristu ambiri tamanga molakwika kwa nthawi yaitali ndi munthu olalikira ndipo ena tonse kumangomvetsera ndi kumaimba ndi kuvina ndi kupita kumudzi ndikukhala ndi moyo wosiyana chifukwa cha ichi ana ambiri afa ndipo amai ambiri asweka mitima yawo.
Cholinga cha Yesu pa mpingo wake ndi kukhala amai ambiri abale ambiri ndi alongo ochulukanso. Malo athu ndi zokhala nazo ndi nthawi ndi ndalama sizathu ayi, ifenso si a ife tokha. Tinagulidwa ndi mtengo wamkulu ndi mwazi wa Yesu ndiye timapanga chiganizo kuti tisankhalenso ndi moyo wathu pokhala mu moyo wa wina ndi mzake tsiku ndi tsiku AAH ndatopa ndikuganiza zopita kukagona Ai pita kukakumana ndi kukonda ambale ako gwira ntchito pamene kuli masana usiku ubwera ndipo palibe chochita. Ndikuganiza zochita zimene ine ndizikonda. Bweletsani mbale kwa ine ndi abale enanso ambiri chitani ndi anthu ena chabwino tiyenera kupita ku msika. Ndilibe nthawi yokhalira ndi abale kapena alongo atengeni onsewo. Ndipo chitani nonse pamodzi ndipo mumodzi. Ndipo njiramo mudztha kudziwa zosowa za zimene afuna ndi zinthu zimene zili zofunika kwa iwowo chifukwa ndinu okhuzidwa ndi moyo wanu ndipo sika ndi muzochita osati mphatso yathu yokha imene ili yokha-yokha. TONSE tili ndi mphatso ya Yesu ndikuonetsera moyo wake. mngelo anati “pitani nonse ku misika ndi kuuza wina aliyense za moyo wa TSOPANOwu umene muli nawo wa Yesu! Izi ndi zimene anthu onse adzadziwa. Pakuona kuti muli KUKONDANA WINA NDI MZAKE!” moyo unakhala (ndipo unakhala) kuunika kwa anthu.
Ngati tidikira mpaka kutha ntchito yathu yonse ithe kuti tikhale banja, sitidzakhala banja. Banja limapanga zinthu zonse pamodzi. Kuchapa zobvala zathu pamodzi ndi kupita ku msika pamodzi. Kuyenda pamodzi ndi kulankhura machimo kwa anthu za Yesu. Pamene tili tonse pamodzi timaulura machimo kwa azanthu timati, mlongo mungathe kundipemphelera? Ndili wotopa ndi ana anga ang’ono ndiponso ndakwiya ndi mwana wanga wa ng’ono dzulo. Ndafunsa Mulungu kuti andikhululukire komanso ndikufuna kuti andikhululukirenso kapena mb’ale kodi mungakhululukire di kundipemphelera ndinali ku ntchito ndipo ndinakwiya ndi wina amene amafuna kundinamiza ndipo ndinalankhura mau oipa kwa iye. Ndinapita ndikumufunsa kuti andikhululukire ndipo ndili kuwulura machimo anga pa iwe. Choonde mungathe kundikhulukira ndi kundipempherera ndikuti ndingakhale olimba zonse. Inde ilipo nthawi imene timafunika kukhala patokha ndi kupemphera mu seri ndi kukhala ndi nthawi ya wekha ndi zinthu zina. Koma pena pake tataya moyo wa Yesu umene umatikhalitsa pamodzi. Mphaka Yesu anatenga abale atatu ndi iye pamene anapita ku Geshemane mmunda uja pa nthawi yowawitsa ya moyo wake. ndi ifenso tichite choncho. Aliyense amene amati ndi wake wa iye ayenera kuyenda monga iye anayendera ndi chabwino ndi chopambana chimene chataika mu njira ya makona mu nyengo ya kutanganidwa Nu Clear. Kuzikonda ulesi ndi kunyada. Tiyeni tilengeze Yesu kuti dziko lidziwe ndikuti tikule msikhu.
Titsegule Mitima Yathu
Ichi ndicho chifungulo chenicheni. Ife tiyenera kutsegula mitima yathu ndikulora anthu ena alowe m’mitima yathu. Ichi ndi chofunikira kwambiri. Palibe njira ina yozungulira ichi. Ife tiyenera kutsegula mitima yathu kwa wina ndi mnzake kuti Yesu akhonze kulowamo ndipo abale ndi alongo athu akhonze kulowamo. “Ufumu wa Mulungu siuli pano kapena apo,” Yesu adatero “Ufumu wa Mulungu uli mwa inu.” Ngati inu ndithudi mufuna Ufumu wa Mulungu, sikungokhudza kukhulupirira zinthu zoona kapena kupita ku misonkhano. “Ufumu wa Mulungu siuli pano kapena apo; uli mwa inu.” Ichi chitanthauza kuti ine ndifuna Ufumu wa Mulungu, ndiyenera kulowa mwa inu ndi mmene Ufumu wa Mulungu uli. Ichi chitengera kulimbika mtima, kudzichepetsa ndi kumvera. AMEN? Ife tiyenera kukhala osakanizana osati osiyana. Ife tiyenera kukhala zana la amai, alongo ndi abale—osangoti zana la abwenzi abwino.
Ngati ife tidzayamba kukhala munjira iyi kwambiri ndi kwambiri tsiku lililonse pamodzi—————ngati ife tidzatuluka m’nyumba zathu ndi kulowa mumitima ndi miyoyo ya anthu ndi kuwalandila iwo m’mitima ndi miyoyo, ndiye kuti ife tidzaona mpingo moti makomo a ndende sadzaulakanso konse ayi! Ife sitidzafuna zigawo zonse zongopangilapozi za Baptist, Pentekositi kapena Nazarene. Ife sitidzafuna zigawo zonse ayi chifukwa Yesu adzadzadza ife! Ife tidzaona ulemerero wa Mulungu ukutsika mu miyoyo yathu munjira yodabwitsa. Ife sitifuna zizindikiro zonse izi tsopano.
Tsopano anthu adzadzidwa ndi mzimu Oyera onse a iwo, ndipo ife tidzamizidwa pamodzi mwa Khristu.
Ife taona zotsekeredza izi zikugwetsedwa pansi mu malo ambiri. Mpingo umene ife tili mbali uli ndi anthu ochokera kwambiri za umoyo zosiyanasiyana zambiri amene ayika mbirizo pambali chifukwa choti agwa m’chikondi ndi Yesu, pamodzi, ndipo ife tili kuthandizana wina ndi mnzake kukula kukhala ngati iye tsiku lirilonse. Khalani ndi masomphenya awa pa mzinda wanu. Yesu afuna anthu AKE kuti akhale AMODZI. Ife sitikhala amodzi chifukwa tapanga chisankho kutaya ziphunzitso zathu. Ife tidzakhala amodzi pokhapokha pamene tapanga chisankho kutaya machimo athu. Sikuti ndi aliyense AFUNA ichi—koma INU mukhonza kukhala kapena kufa chifukwa cha icho!
Ufumu Kulandidwa Zida?
Tangoyeserani padali mafumu awiri—mfumu yabwino ndi mfumu yoyipa. Mfumu yabwinoyo idali ndi mphamvu kwambiri kuposa mfumu yoipayo. Ankhondo a mfumu yabwino adali ndi zida zimene zikadagonjetsa mfumu yoipayo. Zida izi zidali za mphamvu yoposera. Mfumu yoipayo idadziwa kuti siyingaime kulimbana ndi mfumu yabwinoyo. Tsono mfumu yoipayo idaitanitsa msonkhano wa akulu ankhondo ake.
Iye adati, “ine ndili ndi njira zitatu.” Ife sitingalimbane ndi zida izi, tsono tiyeni choyamba tinyengerere gulu la nkhondo la mfumu yabwino kuti iwo safunika kuphunzira kumenya nkhondo ndi zida zao. Tiyeni tipange iwo azingokumana pamodzi ndi kungoyankhula zokhudza zida zao. Atsogoleri awo akhonza kuyankhula zokhudzana ndi kudabwitsa kwa zida zao. Iwo azimva bwino zokhudzana ndi zida, koma iwo ayiwala za mmene angadzigwiritsire ntchito izo.”
“Nayi njira yanga ya chiwiri. Ife tidzagawa gulu la nkhondo la mfumu yabwinoyo. Ife tidzazala mbeu ya chigawanikano pakati pao. Tsono kenako, mmalo mwa gulu la nkhondo limodzi, iwo adzakhala ndi timagulu tating’ono tokwana zana limodzi. Iwo sadzadziwa m’mene angamenyere nkhondo pamodzi. Ife tidzawagawa iwo ndi kuwagonjetsa iwo.”
“Nayi nira yachitatu. Ife tidzanyengerera gulu lankhondo la mfumuyi kuti alore wina aliyense kulowa nawo gululo. Ife tidawauza kuti gulu la nkhondo lalikulu ndi laulemerero ndikuti aliyense amane ali ovomera kuvala uniform akhonza kulowa nao. Ife mwachinsinsi tidzatumidza ena mwa asilikali kukalowa nawo gululo. Motero, iwo adzakhala ndi zida zamphamvu koma sadzadziwa kugwiritsa ntchito iwo adzakhala ogawikana pa wina ndi mnzake. Ndipo gulu lao lidzadzaza ndi anthu amene ali opereka ulemu kwa ine, mdani wao.” Munjira iyi, mfumu yoyipa idali ndi kuthekera kolimbana ndi mfumu yabwino.
Umu ndi mmene zachitikira mu mpingo. Nyimbo zili bwino, monga momwe tayimbira—Mwazi wa Yesu siudzataya mphamvu zake. Mau a Yesu sadzataya mphamvu zake. Dzina la Yesu silidzataya mphamvu zake. Izi ndizo zida zathu. Satana angayime kulimbana ndi Dzina, mwazi ndiponso Mau a Yesu. Koma mpingo wa Yesu wataya mphamvu zake. Mmalo mwakukhala akhulupirira a unsembe, ife tasanduka omvera ndi ochita a ndondomeko (pologramu). Ife tayiwala mmene tingagwiritsire ntchito Dzina la Yesu, Mwazi wa Yesu ndiponso Mau a Yesu. Ife tili okhutitsidwa ndikungokhala pamodzi ndi kumamvera kwa wina wake akuyankhula zokhudza zinthu izi. ife tilinso ogawikana wina ndi mnzake. Pali mazana a mipingo, wina uliwonse ndi miyambo. Ife talola migawanikano iyi kuima mnjira yathu ife tisagwirizane pamodzi ndi kumenya nkhondo ndi mdani. Ife takhalanso auchisayero. Anthu ambiri mmabwalo achipembedzo samudziwa ngakhale Yesu monga Mpulumutsi ndi Mbuye wawo. Iwo ali osokonezeka. Iwo akuganiza kuti amamudziwa Yesu, koma iwo siali choncho ngakhale pang’ono, chifukwa iwo sadapereke moonadi miyoyo yawo kwa iye.
Umboni Wa Moyo Wa Yesu
Tsono mu mnjira zonse izi mpingo watwya mphamvu zake koma Yesu adanana kuti mpingo umene iye amangaudzakhala wakutheker kugonjetsa makomo a ndende. Chimene ife takhala tikuyankhula lero ndi yankho la vuto ili. Ngati ife timanga mnjira ya Mulungu, ife tidzakhala woyera. Osati chifukwaife tili a bwino, koma chifukwa anthu ambiri akutithandia ife tsiku lililonse. Iyi ndiyo njira ya Mulungu, Ngati ife timanga mnjira imeneyi , ife tidzayanjanitsidwa mu umodzi. Ndipo ngati timanga mnjira iyi, membala aliyense adzagwiritsa mphatso yake pochitira ubwino onse. Ife sitikhala womvera chabe, ife tidzakhala asilikali, ndipo Banja la chikondi. Banja loona, kutengera kwa Yesu mu Marko 3:33-35 iyi ndiyo njira imene mpingo wa Yesu ukhonza kutengeranso mphamvu zake.
Ife tinakwera kuno mumatola mmawa uno. Oyendetsayo aamanena, mukuwawa, kuti chisilamu chakhala chikutenga mphamvu mu dziko muno. Chabwino, ine ndekha sinditsamala kuti wina ali ndi nambala yambiri. Chimene ine nditsamal ndi choti, padzakhala umboni wa Yesu khristu pa dziko ili. Umboni womwe ndi woyera, umene ndi wa mphamvu ndi umene uli ndi mphamvu yogonjetsa satana mmiyoyo ya abambo,amayi ndi ana. Ichi chikhonza kuchitika pokhapokha ngati mpingo wa Yesu ungatengeso mphamvu zake.Ife tiyenera kuthandizana wina ndi mzake. Ife tiyenera kumanga miyoyo yathu pamodzi, tsiku lililonse. Ngati ife tizakhala mnjira iyi, diye kuti dzina la Yesu lidzatengedwa mu ulemu wa pamwamba.Anthu adzayamba kunena kwa ife, “Tiudzeni ife za Yesu ameneyu amene inu mumudziwa”. Apa ndipo pothera pathu, ngati ife tidzakhala ndi kulimbika mtima kuti tiumange njira iyi. Ameni?
Chotsani Dengu Pa Chomera
Aheberi 3 amanene kuti ife tiyenera kulimbikitsana wina ndi mzake tsiku lilonso. Ife tiyenera kuchenjedzana wina ndi mzake tsiku lilonse.Ife tiyenera kuthandidzna wina ndi mzake tsiku lilonse ndi ana athu ani akazi athu ndi ntchito zathu mminad mmisika——kutithandizana winw ndi mzake siku lilonnse. Aheberi 3 amatiamapitilira kunena kuti ngati ife sitipanga achi, ndiye kiti dzinthu ziwiri zichititka. Ife tidzasanduka ouma, ndipo ife tidzaputsisidwa. Ngati inu muli ndi chikho cha madzi ndipo mukuthira madziwa pa nthaka yofewa, nthaka yofewayo imamwerera madziwo. Koma mukathira pa mwala youma madziwo amangoyenderera pa mwamba. Nthaka ndi yofewa ,mwala ndi wouma. Mwala ndi wouma sungalandire. Ngati ife sitikhalirana ndi wina ndi mzake tsiku lilonse monga Aheberi 3 afotokonzera, ife timauma. Mau a mulungu, sangalowe mmtima yathu, iwo sangalowerere. Mtima wathu watsanduka ouma.
Ife tidali chabe mdzinda wina wamtunda wokwana milingo zana limodzi kuchoka pano, pafupi ndi nyanja. Nthaka ya mfupi ndi nyanjayo ndi yofewa, chifikwa madzi nthawi zonse ali pa iyo. Kutali ndi nyanjayi, nthakayi siiyandira mvula yambiri ndi youma. Ife tiyenera kukhala mwa wina ndi mzake tsiku lililonse kapena ife tiuma. Ife sitingamve Mulungu. Ife sitingakule. Ngati inu mutenga chomera ndikuyika pansi pa dengu, chomeracho chidzafa. Chomera chimafuna kuwala. Monganso ife!n kuwerenga ma Baibulo sikokwanira. Kukhala nawo mitsonkhano pa sabata sikokwanira. Monga mbewu pansi pa dengu, ife tikhodza kufa. Timafuna kuwala. Pamodzi tikhala mnjira iyi. Ife timagawirana kuwala pa wina ndi mnzake. Popanda kuwala kumeneku, tifa. Popanda kuwala kwa wina ndi mnzake mu miyoyo athu tsiku lirilonse, ife timauma.
Chinthu chachiwiri chimene chimachitika ndichakuti, ife timaputsitsidwa. Ichi chitanthauza kuti sitidziwa kuti ife ndiouma. Ife taputsitsidwa. Ife tikuganiza kuti tili ofewa, koma ndife ouma. Ife timakonda kuyimba ndipo timakonda nthano za mBaibulo. Ife tikhozanso kukonda kuyankhula zambiri zokhudza Yesu. Koma ife tili ouma ndipo ife sitikudziwa ichi, chifukwa abale samatithandiza ife kukhala ofewa tsiku lirilonse. Ichi ndi choopsa kwambiri! Ngati munthu ali wakhungu, koma iye aganoza kuti ndi ondetsa wabwino wa basi, sichoncho?! Icho ndi choopsa!
Munjira yomweyo, ife tikhoza kuputsitsidwa. Popanda kuwala kwa anthu a Mulungu mu miyoyo yathu tsuku lirilonse, sikuti tidzangouma kokha ayi ife tidzaputsitsidwa. Ife sitidzaona mbali immene ili mwa ife imene siili ngatiYesu. Malingaliro athu adzaputsitsidwa. Awa ndi malo oipa kukhalapo. Kuwala kwa Mulungu sikungalowe, ndipo zinthu zoipazo sidzingachuluke. Ife sitidzawadziwanso kuti zinthu zoipazo zilimo, chifukwa ife taputsitsidwa. Ngati inusimukhalira tsiku liri lonse pamodzi ndi wina ndi mnzake mu njira imene Baibulo limafotokozera, ndiye kuti inu ndi ouma ndi oputsitsidwa. Ichi ndicho Baibulo linena. Mulungu sanama ayi. Aliyense amene sakumanga tsiku ndi tsiku pamodzi ndi anthu ena, ndi mau a Mulungu, amauma ndi kuputsitsidwa. Ngati ife tidzadandaulirana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku, mitima yathu iodzafewa ndipo Ife tidzamva Mulungu bwino lomwe kudzera ku abale ndi alongo, ndi ngakhale kudzera mmalemba pamaene tiwerenga. Pamene ife tikhala mnjira ya Mulungu, ife timafewa. Kuwala kwa Mulungu kulowa. Mvula ya Mulungu ibwera ndi kumaliza kudzadza ife, ndi kuchotsa mphepo zoipa mwa ife. Pali chiyembekezo chambiri ngati ife tikhala mu njira ya Mulungu! Palibe chiyembekezo ngati ife sitikhala mnjira ya Mulungu.
Ife tamanga munjira yolakwikwa kwa zaka zambiri. Mipingo yambiri kuzungulira padziko lapansi ili ngati chomera pansi padengu. Iwo akhza kumva ziphunzitso zabwino, koma iwo alibe kuwala kwambiri muniyoyo yawo. Ambiiri ndi akufa, ena ndi okhinimbira. Ife tifunika kuchotsa dengu ili pachomera. Njira yaikulu yimodzi yochitira ichi ndi kulowerana mwa pamtima ndi wina ndi mnzake, kuthandizana ndi wina ndi mnzake, kulimbikitsana wina ndi mnzake, kukondana wina ndi ,mnzake tsiku lirilonse.
Iye akumanga anthu a Mphamvu
Iye akumanga anthu kulamanda
Iwo akuyenda pamodzi ndi Mulungu
Ndipo iwo akukula ndi Dzina Lake Lopambana
Mangani Mpingo Wanu, Mbuye,
Tipangeni ife amodzi Mbuye,
Mu Ufumu wa Mwana wanu,
Mangani Mpingo Wanu Mbuye
Tipangeni ife amodzi, Mbuye,
Mu Ufumu wa Mwana Wanu.
Yendani Ulendo
Baibulo ndi loona mnjira iliyonse. Izi ndi zokhudza Yesu ndi omutsatira ake. Izi ndi nkhani za m’mene amawawidwira mtima ndi mmene amaphunzirira kudzera mmakhalidwe awo ndi Mulungu. Ife tikhonza kuphunzira kuchokera munkhani zawo, koma tikhonzanso kuphunzira: pakukumana ndi kuonana ndi Mulungu pamodzi pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mu ichi nafe tili “malembo amoyo.” Zolembedwa zonse mu dziko lapansi sizinganthe ife monga m’mene moyo wapamodzi ungatisinthire ife. Zinthu zakuya zomwe tizifuna sizidzafika pansi pa mitima yathu pamene zingawerengedwa kuchokera pa pepala chabe. Pamene tikonza zinthu pamodzi tsiku lirilonse, Yesu aliphunzitsa ife ziphunzitso zakuya zamoyo zomwe sitingaziphunzire kuchokera m’Baibulo, “ngakhale zoonadi ndi eklezia—mpingo.” “MOYO umasanduka kuunika kwa anthu.”
Moyo siunapangidwe kukhala ngati sukulu ya galamala yomwe timakaphunzirako mfundo zina ndipo kenako kukhulupirira ndondomeko ina kapena zinthu. Malo mwake Mulungu watiyitana ife kukhala amuna ndi akazi a Mulungu chimodzimodzi monga omwe adaliko pasadabwere ife—olumikizidwa kwa Mulungu yemweyo amene iwo adalumikizana naye—okhala m’chikondi chozama monga iwo adaliri. Kuti chimene tichichite kapena kuchikwanitsa, ife tiyenera osati kudziwa momwe iwo amadziwa zokha. Koma tiyenera kumva chimene iwo amamvera, Mulungu ayenera kuti—tenga paulendo onga ngati wawo. Tsono ife titenga ulendo umenewu mukugwiritsa ntchito Mau a Mulungu kumodzi ndi moyo wathu. Ife tiyenda ulendowu ndi misozi m’maso mwathu, ndikuthandizana wina ndi mnzake—mu nthawi yoipa ndi nthawi yabwino—ndi maso athu pa chiyembekezo chathu, Messiah wathu. Ife tikupita chitsogolo, kukhulupilira kuti Mulungu akhala otipatsa wathu, kutithandiza pomwe tikhala pamodzi.
Petro adakana Yesu atayenda ndi Iye kwa zaka zitatu, koma pamene iye adamva tambala atalira, zidamuswa mtima wake. Ndipo pomwepo iye adabwererapamodzi ndi mbale wake Yohane. Ichi ndi chimodzi-modzi ndi ife. Pali nthawi imene ife tidzapanga zinthu zoipa ndi nthawi pamene ifee tidzapanga zinthu zabwino. Koma chili chonse tipange, ife tiyenera kupangira pamodzi ndi maso athu pamodzi ndi Yesu ndi kulola Iye atipange ife akuya mukudalira pa Iye pamene masiku akupita. Moyoudakhala luwala kwa anthu.” Ife tiyenera kuphunzira kwambiri zakhudza Yesu kudzera mukukhala pamodzi ndi kuthandizana wina ndi mnzake—Mulungu, tithandizeni kutsegula maso athu.