Mipando Isanu

4/8/2003

Lachiwiri Masana Salima, Malawi October 5,1999

Mwachisomo cha Mulungu, ndifuna ndiyikize kwa inu zida zina za kuvetsetsa ndi kuzindikira makhalidwe a anthu. Tingoyezera, kwa kanyengo kamene tili nako pano ife, mipando isanu. Ndipo akukhala mipando isanu imeneyi ndi anthu asanu kuyimirira mitundu isanu ya anthu amene inu mwachidziwikire mukumane nayo pa ulendo wanu padziko lapansi.

Mipando iwiri yoyamba

Mu mpando oyamba, tili ndi osakhulupirira kapena wamafano wina wake sakhudzidwa ndi zotsata Yesu ndi pang’ono pomwe. Mwina munthu ameneyu ndi msilamu kapena Mhindu. Munthu uyu samazitcha kukhala Mkhristu .

Mu mpando wa chiwiri, ngakhale,tili ndi munthu amene amazitcha kuti amasatira Yesu, koma munthu uyu samvera Yesu. Pa misonkhano, munthu uyu amaoneka ngati okonda

Yesu, koma iye samkonda zenizeni chifukwa samvera iye. Mu Mateyo 7, Yesu adati padzakhala ambiri amene adzanene “Ambuye, ambuye padzakhala ambiri amene adzagwire ncthito yotamandika mu dzina lake, koma ku amene iye adzanena “Ndichokereni ine, ine sindikudziwani inu”

Aliyense akudziwa kuti munthu wa mpando woyamba sali owomboledwa chifukwa munthuyu sazitcha ngakhale pang’ono kuti amasatira Yesu. Ife timadziwa kuti pokhapokha ngati uli ndi mwana, siungakhale ndi Atate. Pokhapokha ngati ukhulupira mumtima wako kuti mulungu adaukitsa Yesu kwa kufa, Mwazi siudzatsuka tchimo lako. Munthu uyu sangapulumutsidwe chifukwa iye sakhulupirira mwa Yesu. Mwazi wa Yesu siutsuka machimo amunthu otereyo. Kufikira munthu wa pampando woyamba uyu atadzipereka kwa Yesu, iye sangapulumutsidwe. Iye akhoza katengedwa kukhala munthu wodabwitsa ndi tate wa bwino ndiponso wacthito wabwino, koma iye sangapulumutsidwe kopanda kuyeletsedwa ndi mwazi wa Yesu.

Kumbali yinayi, munthu wa mpando wachiwiri anena “ine ndine mkhristu” koma makhalidwe amunthu ameneyo ndi oyipa, ngakhale kuti munthu uyu akhoza kupanga ncthito zabwino zowoneka mzina la Yesu. Mu uthenga wabwino wa Luka, Yesu adati kuti pa tsiku la chiwerunzo, anthu ngati uyu adzanena, “Yesu, mudaphunzitsa makwalala athu. Mudadya magome athu. Ife tidapanga zozizitswa mu dzina lanu. Tidapereka chuma chathu kwa osauka”, koma Yesu amanena kwa anthu awa mu mateyo 7:21. “inu simudamvere ine inu simudapange funiro la atate. ine sindidakuziweni inu. Yesu akuonetsa apa kuti anthu ambiri amene mazictha a khristu ndi mpakaso amapanga nchito za mphavu mun dzina lake ali munjira ya chikulu yomwe imasogolera ku chionongeko. Anthu awa amanamizira kukhala a khristu, amanamiziran kuti ali ndi mamembala a mpingo, koma mzenizeni saali choncho.

Munthu wa mpando woyamba siali opulumusidwa chifukwa cha kusakhulupirira. Munthu mumpando wachiwiriwo siali opulumusidwa chifukwa chakusamvera, kumene Baibulo limanena kuti ndi osakhulupiriranso.

Mipando itatu inayo

Tsopano anthu amipando atatu yotsaklayo ayimirira choonadi. Otsatira a Yesu ogulidwa ndi mwazi . Atatu awa ndiwo a khristu koma ndifuna kuunika kuti pasakhale chisokonezo ndi munthu wampando wachiwiriwo.

Muli ndime zogwirizika kwambiri mu Yohane oyamba 2 imene imaonetsera ndikuzindikiritsa anthu amenewa amene tili nawo mmipando itatu yomalizayi. Yohane adati “Ndikulembera kwa inu ana ang’ono, azibambo ndi kwa inu achinyamata” Tsopano mmganizo athu a nthawi zonse mudongosolo la zinthu ndi ana ang;ono, achinyamata ndiponso azibambo sichoncho. Koma Mulungu akupereka dongosolo ili, “ana, abambo, achinyamata”

Ana, abambo, achinyamata awa ndi anthu opulumusidwa. Awa ndi anthu amene amakhulupirira kuti Yesu ndi mwana wa mulungu, ndipo machimo awo ndi wokhululukiridwa ndipo ndi osambitsidwa ndi mwazi wake. Mpando wachitatu uyimira ana, mpando wachinayi uyimira abambo ndipo mpando wachisanu uyimira achimata. Inu mukhoza kuganizira iwo monga makanda , anthu okhwima kapena akuthekera ndipo kenako chinthu chimene ndikufuna kuti ndionetsere bwinobwino ndi chakuti nthawi zina makhalidwe a ana ngakhale kuti iwo ali opulumutsidwa, amaoneka ngati makhalidwe a anthu asapulumutsidwa (ngati munthu wa mpando wa chiwiri). Koma munthu wa mpando wa chitatu (Mwana weniweni) ndi osambitsidwa ndi mwazi wa Yesu. Munthu uyu wa mpando wa chiwiri akhoza kuzitcha kuti anasambitsidwa m’mwazi wa Yesu. Munthu ameneyo akhoza ngakhale kuimba nyimbo zokhudza Mwazi Yesu kuwapulumutsa iwo , koma chifukwa munthu uyu akhoza pang’ono ndi pang’ono

Kupita mpaka kupandukako kwa Yesu, munthu uyu siotsatira wa Yesu weniweni. Aliyense amene amazitcha kuti ali mwa iye , ayenera kuyenda m’mene Yesu adayendera. Aliyense amene sadzamvera kwa Yesu adzadulidwa kuchokera pakati pa anthu “Aliyense amene ali ndi chiyembezo ichi adziyeretsa yekha monga iye ali woyera. Palibe amene adabadwadi kwa mulungu amene adzapitilira kuchimwa chifukwa mbewu ya mulungu imakhalira mwa iye, iye sangapitirire kuchimwa chifukwa iye ali obadwa mwa mulungu.

Njakata ya mpando wachiwiri/Mpando wachitatu

Nthawi zina khalidwe la munthu wa mpando wachiwiri likhonza ngakhale lukhalako labwino kuposa khalidwe la munthu wa mpando wachitatu. Koma pali chinthu china chimene muyenera kumvetsetsa chokhudzana ndi uthenga wabwino wa Yesu. Munthu wampando wachitatu ndi kufunafuna kuyeretsedwa mu Mwazi wake. Mu Aefeso I ndi Agalatiya 3 Mulungu adati kuti pamene munthu akhulupirira mu mtima mwake (osati mmutu mwake) mwa Yesu khristu kuti amapatsa munthu ameneyo MphatsoYa Mzimu oyera kuti ikhale mkati mwake. Mzimu oyera umapatsidwa kwa aliyense amene akhulupirira moona ndipo akhulupirira mwa Yesu kuchokera mu mtima

Tsopano muli mu njakata. Ngati inu mukungoweruza kudzera mumakhalidwe , ungadziwe bwanji mmene ungachitire? Nanga bwanji utakumana ndi mkhristu wa chimwana amene ali ndikhalidwe losasangalatsa , ndipo muli ndi osakhulupirira amene amazitcha m’khristu koma pa zonse mungaone , mungaone mwina ali ndi khalidwe la bwinoko? Chabwino kodi alipo wina amene adapulumutsidwa ku machimo chifukwa cha khalidwe la bwino? Kodi ichi ndicho uthega wa bwino wa Yesu? Kodi uthenga wa bwino ndiwoti kupulumusidwa ndi makhalidwe athu abwino? Ayi sichoncho! Ife tapulumutsidwa ndi mwazi wa Yesu. Ife tapulumutsidwa ku machimo athu ambuyomu, ndipo tapulumutsidwa ku machimo obwera mtsogolo ndi Mwazi wa Yesu khristu.

Tsono kenako, nchifukwa kumanenedwa mbaibulo mbuku la Agalatiya kuti aliyense amene akhala ngati wochimwa sadzalowa mu ufumu wa mulungu? Ichi chikumveka kuti chipulumutso chathu ndichokhuzidwa ndi makhalidwe athu. Koma ife timadziwa kuti ichi sichingakhale choona ife tinapulumutsidwa ndi mwazi wa Yesu, osati makhalidwe athu. Tsono keneko nchifukwa chayani Baibulo limanena kuti aliyense akhala mmachimo sangalowe mu ufumu wa mulungu ndipo sadzapita kumwamba? Nchifukwa chiyani Yesu amati, “Nkhosa ndi amene achita chifuniro changa ndi kundimvera ine, ndipo Mbuzi ndi amene sandimvera ine? Yesu adati nkhosa zikupita kumwamba ndipo Mbuzi zikupita ku Gahena. Ndipo Yesu adati mudzidziwa nkhosa kudzera mu zi ntchito zawo. Ichi chikumveka ngati tinapulumutsidwa ndi makhalidwe athu. Koma ife tidziwa izi sizoona.

Kuthana ndi njakata

Kodi uthenga ndi chiyani apa? Kodi timamveka bwanji mbali iyi ya uthenga wabwino? Chabwino ichi ndi chisisi cha uthenga wa bwino wa Yesu. Aliwonse amene amapereka mitima yawo kwa Yesu ndipo atembenuka ku machimo ndikusiya zammbuyo mwawo amapatsidwa Mphatso ya mzimu oyera. Ife timawerenga mu buku la Yohane Oyamba kuti pali zizindikiro zambiri zimene mzimu wakukhala mkati umaoneka ngati moyo wa umunthu. Pali ambiri amene adzanena “Ambuye,Ambuye” koma adzamva Yesu akuti” sindikukudziwani ndi pang’ono pomwe” Tsono ife tikudziwa kuti munthu saali mkhristu chifukwa choti munthuyo amazitcha kukhala kapena amachita zinthu zooneka zodabwitsa mzina laYesu.

Buku la Yohane Oyamba lidalembedwa mu zaka zokwana makumi asanu ndi limodzi patangotha pentekosti. Mtumwi Yohane mwina adali ndi zaka makumi asanu ndi atatu ndi mphambu zisanu kapena makumi asanu ndi anayi. Yohane adali ndi zaka zambiri kuti aganize kapena kuti apemphere zokhudzana ndi chikhristu chimaonekera. Pa nthawi imeneyi, zaka makumi asanu ndi limodzi patatha masiku a Pentekosti, padali anthu ambiri omwe adali atakula mpingo. Padali makanda atsopano obadwa amene adakula ndipo adali ndi ana awo nawonso pa nthawi imaeneyi. Tsono pamene anthu amene adakula akunena mau olondola chifukwa makolo awo adanena mawu olondola pa nthawi imeneyi, padali anthu ambiri amene “adakulira mumpingo” ndipo mwachoncho adadziwa nyimbo ndi akhonza kuomba mmanja ndi kuimba ndi kunena mawu onse olondola. Koma Yohane adadziwa kuti ngakhale ana akhonza kuoneka a khristu, iwo akhonza kukhala asanadzipereke miyoyo yawo moonadi kwa Yesu. Munthu si mu khristu chifukwa choti mmalingaliro amakhululupirira zinthu zoona. Munthu, kutengera pa Yesu, sim khristu mkhristu chifukwa chopanga zinthu zozizwa mu dzina lake. Padzakhala anthu pa tsikulo, amene adapanga zozizwa mu dzina lake, ndipo iye adzawauza iwo “Ndichokereni ine kunka kunja ku mdima. Ine sindidadziweni inu.”

Gawo la mzimu woyera

Monga ndidanena buku la Yohane Oyamba adalembedwa zaka makumi asanu ndi limodzi patatha pentekosti. Yohane amayankha ambiri mwa mafunso amenewa amene mwa chidziwikire iye adayenera kukumana nawonso.Yohane adalemba zinthu zosiyana zambiri mu buku la Yohane Oyamba zimafotokoza chimene mkhristu weniweni amaoneka ngati. Nthawi ndi nthawi iye amalongosola chimene chimaoneka ngati wina wake ali ndi umboni wa Mphatso yakukhala mkati ya mzimu oyera. Baibulo limati kuti aliyense amene ali mkhristu oona ali ndi gawo kapena gawo la malipiro otchedwa mzimu Oyera.

Pamene munthu akugula nyumba kapena galimoto, nthawi zina amapereka mbali ya malipiro kapena malipiro oyamba gawo limenelo. Kapena mbali ya malipiro oyambawo amakhala ngati chikole kuti malipiro onse adzabwera. Baibulo limati kuti Mulungu, monga mbali ya malipiro , adapereka mzimu woyera kwa aliyense okhulupirira. Ichi ndi chitsimikizo kwa ife kuti ife tidzatenga moyo kwamyaya. Ngati wina wake akusoweka mbali ya malipiro imeneyi, gawo la Mzimu woyera, ndi chidzindikiro kuti pakhala popanda pangano kapena mgwirizano pati pa munthuyo ndi Yesu.

Ichi ndi chifukwa chake Yohane, mtumwi adati kuti kusiyana kwa Mkhristu ndi osakhulupirira sikulapa kwa ngati amapanga zozizwitsa, kapena ngati amakhulupirira zinthu zolonda, koma ngati ali ndi mzimu woyera . Ndipo chimaoneka bwanji pamene munthu moonadi ali ndi mzimu woyera ? Kodi ndikupanga zozizwa ? Kodi ndikuyimba ndi kukhala nawo misonkhano ? Ayi izi siziwonetsera zimene zimathandiza ife kumvetsetsa amene ali ndi mzimu ndiponso amene alibe . Munthu wampando wachitatuwo , amene ali mwana wachikhulupiriro, akhoza akhonza kukhala kuti adanzipereka kwa Yesu kuchokera mtima, koma akhoza kuonetsa khalidwe loipa nthawi zina.

Ena anakonda kuwala

Yohane ndi Yesu anapereka kwa ife yesero lofinika kwambiri kutithandiza ife kutolapo kanthu pa chisokonezo ichi. Yesu anachiyika choncho, “Ena anakonda kuwala ndipo ena amadana ndi kuwala” (Yohane 3) Yohane adati “Ngati ife tikhonza kupitiriza kuchimwa, ndiye kuti Sitidziwa . Mulungu., ndipo ife tawonetsera kuti ife tilibe Mzimu Oyera.” (1 Yohane 1:4).

Yesu adati “Ena anakonda kuwala, ndipo ena anadana ndi kuwala.” Makhalidwe a munthu uyu opulumutsidwa akhoza kusakhala wabwino nthawi zina, koma chifukwa munthu uyu ali ndi Mzimu Oyera mmoyo wake, munthu uyu adzakonda kuwala ndi choonadi. Monga khanda lobadwa kumene, munthu uyu adzakakamira pa mkaka wa uzimu wa Mau. Pamene mudzayandikira munthu uyu ndi kunena , “khalidwe lako ku nchito, kapena ndi mkazi wako ndi losakhutitsa m’bale. Kodi ukudziwa kuti pamene uchita zinthu izi wukuwawitsa mtima anthu ambiri kuphatikizirapo Yesu?” Munthu wa mpando wa chitatu uyu akhoza kuyamba kulira ndipo nati “ukunena zoona. Ndikudziwa kuti ukunena chilungano. Mu mtima mwanga ndine odandaula mmene ndawachitira akazi anga. Zikomo pakubwera kwako kudzandiuza . Ine ndikufuna iwe undiuze zinthu zimenezi. Ndikufuna thandizo lako.” Uwu ndi umboni waukulu kuti munthu uyu ali ndi Mzimu Oyera ndipo ali oomboledwa.

Mwina makhalidwe a munthu uyu siabwino ku nyumba kapena kunchito poyamba, koma Baibolo likunena kuti ngati wina ndi opulumutsidwa, Mzimu Oyera udzadzionetsera Okha ndi chikondi pakuwala ndi choonadi. Munthu uyu adzati, “ndipempherere ine! Umufunse Yesu adzandithandize! Chonde Iwe ndithandize ine? Ndikuyitanira iwe kulankhula mau ndi nzeru za Yesu kwa ine nthawi zonse. Ndidzatsegula mtima wanga ndipo ndidzalandira kuwala ndi choonadi ndi Unsembe wake wa okhulupilira onse.”

Kodi munthu wampando wachiwiri anganene chiyani? Munthu uyu alibe Mzimu Oyera. Munthu uyu akhonza kuwoneka kuchita zozizwa mu dzina la Yesu. Munthu akhonza kuyimba ndi kuvina ndipo ngakhale kulalika, komabe alibe Mzimu Oyera. Kodi mukudziwa kuti munthu uyu alibe ndipo ndiosapulumutsidwa kwenikweni? Chifukwa pamene mupita kwa munthu uyu ndi kunena, “khalidwe lako silabwino m’mene uchitira mkazi wako,” munthu uyu amanena, “kodi ukundiweruza ine! Chotsa chipika chakocho pamaso anga! Ukhala walamulo iwe! Samala za machitidwe ako! Kodi ukuwona ngati ndiwe ndani ukandiyankhule ine choncho? Usakhudze ozozedwa wa Mulungu!” Munthu uyu siopulumutsidwa chifukwa munthu uyu sakonda kuwala. Pali umboni wa mphamvu kuti munthu uyu alibe Mzimu Oyera, chifukwa munthu uyu sakonda kuwala. Ena anakonda kuwala ndipo tsono ali opulumutsidwa. Ena anadana ndi kuwala ndipo ali osapulumutsidwa (2 Atesa. 2:10). Ena anakonda kuunika ndipo ena anadana ndi kuunika chifukwa cha zochita zawo ndi zoipa (Yohane 3:19-21).

Tsono ngati muweruza kudzera m’makhalidwe, mudzasokoneza. Nthawi zina khalidwe la anthu ampando wachiwiri ndi wachitatu limaoneka lofanana. Mu zoona, nthawi zina ampando wachiiriwu, amaoneka pa nthawi, kuti akupanga zinchito zabwino m’malo mwa Yesu. Koma Yesu mu Yohane 3, ndi Mtumwi Yohane mukukalata wa Yohane Oyamba anena khalidwe silimene munthu wungaweruzire. Inu mukhonza kumvetsetsa za amene ali ndi Mzimu. Ndipo chifunguro cha umboni chakuti Mzimu wukukhala mkati mwa munthu ndi m’mene munthuyo apangira ku kuwala.

Pangano latsopano

Ndidzapitanso kumbuyo mu Chipangano Chakale kuti ndionetsere mfundo iyi. Uneneri okhudzana ndi kubwera kwa Yesu ku Chipangano Chatsopano ukhonza kupezeka mu Yeremiya 31 ndiponso mu Ezekiele 36. Mumalo onse awa, Iye adanena chinthu chimodzi chokhudzana kubwera kwa Pangano Latsopano. Mulungu adati kuti Mupangano Lakale munthu amanena kwa mzake, “Mudziweni Ambuye!” (Ife tayetsetsa kubwezeretsa Pangano Lakalemu mpingo mfundo yolakwika).

Pangano Latsopano, kutengera kwa onse Yeremiya ndi Ezekiyele, ntchito ngati izi: “Umboni oti ndakhululukira machimo awo ndipo sindikukumbukanso zoyipanso zawo, umboni oti ndakhululukiradi machimo awo ndipo ndawapanga iwo akhristu oti ndidzayika Mzimu wanga mwa iwo ndipo ndidzapanga iwo kusunga lamulo langa.” Umboni oti munthu ndi mkhristu weniweni ndipo machimo awo ndi okhululukidwa, kutengera ndi uneneri wa zaka mazana asanu ndi limodzi pasanafike nthawi ya Yesu, ndilo kuti Yesu adzayika Mzimu wake mwa iwo ndipo Iye adzatembenuza mitima yawo yamiyala ndi kukhala mitima ya mnofu. Iye adzayika Mzimu mwa iwo ndi tsopano nkhosa zidzadziwa mau a m’busa.

Umboni wa mzimu oyera

Mkhristu, olengapo gawo la pangano latsopano, amakonda choonadi (2 Atesa. 2:10) ndipo amakonda kuunika (Yohane 3:19-21) ndipo tsopano ali “otengapo gawo la chilengedwe CHAUZIMU” (2 Petro 1:4, Aroma 6:1-14). Uwu ndiye umboni woti Mzimu umakhala mwa iwo kapena mwa wina aliyense wa ife. Ife sitiyenera mau a aliyense pakuti chifukwa akuti, “Ambuye, Ambuye! “Iyi ndi nkhani yabwino! Amafano kapena azipembedzo zonyenga sangalamulirenso Mipingo! Ife tikhonza kumvera tsopano, kuchokera mu ubale, ulamuliro oti “chotsani chotupitsa mu mkate” wapanda kukhala “moweruza!” Ngati iwo samakonda kuunika kwa kuonetsera chifukwa amakhumbitsitsa kukula mwa Yesu, koma koposa amathawa ndi kukana kutsekereza ena kudzera mkudzitchinjiriza, siali opulumutsidwa, kutengera kwa Yesu, ndipo sangatengedwe kukhala gawo la Mpingo Wake. Tsopano, kumbukirani: NDI CHIBALE CHATSIKU NDI TSIKU CHOKHA chimene mungadziwire ngati aliyense akonda kuwala ndi choonadi ndipo potere ali mwana wa Mulungu. Misonakhano yochepa pasabata sidzalola aliyense kudziwa ngati wina wake amakonda kuunika ndipo ali chabe ofooka, kapena ngati iwo amadana ndi kuunika ndipo potero siali opulumitsidwa. Ngati iwo sakonda choonadi ndi kukhumbira icho ndi mitima yawo yonse (koposa kukana mchoonadi ndi kunyada ndi kudziteteza ndi kutsatsirana kulakwa). Kenako Mzimu Oyera amanena kuti iwo siopulumutsidwa konse. Ichi ndicho chothandiza kwambiri kumvetsetsa: Ngati iwo ali opulumutsidwa, ADZAKHALA ndi Mzimu Oyera (Aroma 8:9, Agalatiya 3, Aefeso 1). Ndipo UMBONI oti iwo ali ndi Mzimu Oyera mwa iwo (ngakhale nthawi yambiri bwanji iwo akuuzani iwo “umboni” waukulu ndipo anena, “Ambuye, Ambuye! “Mateyu 7) ndi oti amakonda kumvera. Ali obadwa atsopano ndipo amakonda kuwala ndi kukonda choonadi, (2 Thess 2:10) ndipo monga makanda amakonda mkaka ndi mau a Mulungu kuchitidwa mu moyo wawo (1 Petro2).

Mu Chipangano Chatsopano sitikakamiza munthu kudziwa Mulungu. Sitinena kuti “sintha makhalidwe ako kuti ukhale Mkhristu tsopano tinganene”. “Khalidwe lako silili ngati la Yesu”. Okhulupilira wowona monga makanda akonda mkaka amati, “zoona” Mulungu andikhululukire ine mungandikhlulukirenso ine 1 Akorinto 12 ndi Aefeso 4 amati ndili kufuna kuthandizidwa kuti ndikhale monga wa Yesu. Mungandithandize chonde mundipempherere ine ndipo ngati mungawonenso ndili kuchita chomwecho chonde bwerani kwa ine ndipo ngati sindili kumveranso inu bwino, chonde tengani awirii kapena atatu bwerani ndi kulankhula ndi ine mu njira imene Ambuye ndi okondedwa Yesu anatilamulira.

Mukumbukira malembo mu Mateyu 18? Ngati mulankhula kwa mbale kapena mlongo ndipo poyamba sakumva ndi kudziwa bwino, Yesu amati tengani awiri kapena atatu kuti athandize kuti amvere. Ndiyenso ngati samveranso ndikuti sakusintha yankhulani ndi mpingo wonse. Sizimene Ambuye athu anatiphunzitsa?

Onani pa mtima, osati makhalidwe

Mtima ndi choonera kuti Mzimu Woyera uli kukhalamkati mwa munthu. Mphatso ya Mzimu Woyera uli kukhala ndi dipo limene limatipatsa cholowa chathu, ichi ndi chiweruziro chake amatero Yesu mu Yohane 3. Ichi ndi chimene chimatisiyanitsa osalakwa ku chiweruzo. Osati aliyense ndi wabwino, koma amene machimo awo akhululukidwa onse ndi kukonda “kuwunika”. Ali ndi mphatso ya Mzimu imene sanali nayo poyamba. Tsopano kuchokera pansi pa mitima yawo yowuma tsopano ndiwofewa. Pansi pa mtima Mulungu ali kuwalamulira kusunga malamulo ake. Kuchokera pansi pa mtima amasamala Yesu mau ake pa makhalidwe awo. Pansi pa mtima mau a mbusa amadziwa chifukwa ali ndi Mzimu wa Yesu nkhosa imati! ndili kufuna Yesu nditsogolereni” Mbuzi zimati ndisiyeni ndekha! Ndimachita zozizwa! Ndingapereke chuma changa kwa aumphawi. Ndimadziwa zinthu. Ndiri wabwino koposa iwe ndipo sindisamala pa zokamba zanu”.

Kuwonera pa makhalidwe sinjira yabwino ku dziwa mtima ngati khalidwe la munthu ndi loipa ndi chidziwitso choti pali bvuto. Koma ngati simungalankhule kwa iwo chifukwa sakonda kuwala ndiye kuti muli ndi bvuto lalikulu. Munthuyo ndi osapulumutsidwa ngati kumbali ina munthu ndi kutheka kuti ali choncho chifukwa choti ali khanda chabe ndipo khalidwe lokhalo ndi bvuto.

Sakudziwa za izi bwino, koma amakonda kuunika ndipo ali kufuna kuthandizidwa izi ndi zotheka kukoneka.

Tisangoona pa bvuto la khalidwe lokha . anthu ambiri ali ndi mabvuto, chifukwa mwina makolo sanawalere bwino. Enanso mwina anali ndi abwenzi amene anali ndi magulu asanakhala otsatira AYesu. Mwina asanabwere kwa Yesu anali mu uchimo waukulu (mmene ndinali ndi inu nomwe) ndiye tinabwera mu ufumu ndi mukhalidwe ambiri oipa) ndibwelezenso, nkhani kodi timakonda kuunika.

Mukumbukila chitsanzo cha malemba? Okhulupilira aku Akorinto anali akhristu oyamba kumene. Palibe amenen anali a khristu kwa zaka zoposa zitatu kapena zinayi. Anali kukhala mu mzinda yoipitsitsa otchedwa Akorintho unali ndi zoipa, monga kugonana okha-okha amuna ndi zinthu zina zambiri kulingana ndi kalata ya Paul okhupilira amenewa anali atachoka muzoipa zoipitsitsa komabe anali makandabe. Anali atapeleka miyoyo yawo kwa Yesu. Koma anali ndi zofooka ndi makhalidwe oipa choncho makhalkidwe awo sanali abwino koma mukudziwa zimene Paulo ananena pamene anakomana ndi mabvuto amenewa? Anati, ndimadziwa kuti mudzamvera.

Mukalata ya chiwiri kwa Akorintho, mu mutu 7 Paulo anati, pamene mudalandira kalata yanga yoyamba munayankha ndi mphamvu ndi kulapa kwakukulu. Munaopsedwe ndi uchimo umene unalipo mu miyoyo yawo. Munakhudzidwa ndi uchoyo ndipo mudakonzekera kuuchotsa Paulo anati ndinamuuza Taitasi kuti timadziwa

Kuti pamene mulandila kalata yanga kuti mudzalapa ndi zimene Akorinto 2:7 amanena.

Makhalidwe awo anali oipa mu mpingo wa Akorintho Paulo analemba kalata yoyamba kwa iwo ndikuthandiza za uchimo wosiyanasiyana. Koma ndithu anali woomboledwa ndipo Paulo amadziwa kuti anali opulumutsidwa ndiye anali oyera choncho ndimadziwa kuti mudzalapa ndipo ndinamuuza Taitasi kuti walapa. Choncho tsopano Taitasi wabwera kwa ine ndi kundibweretsera uthenga wachikondi ndipo chabweretsa chimwemwe mu mtima mwanga kuti mwalapa monga mmene ndinamuuzira. Aliyense amene ali ndi mzimu woyera amalandira kalata yochokera kwa mbale yomuthandiza. Amamfuna kuthandizidwa.

Uthenga wabwino ndi woti Yesu Khristu ndi oti tinatchulidwa ndi mwazi ndi kuti machimo athu onse anakhululukidwa chifukwa tinaika chikhulupiliro chathu chonse mwa Yesu monga mpulumutsi. Chitsimikizo choti tachita zimenezi kuchokera mu mtima, ndipo omwe amasindikiza za cholowa zathu, ndikuti mzimu woyera waperekedwa kwa aliyense amene ali woona mtima ngati munthu ali ndi mzimu oyera adzakonda kuwala ndi kukonda chowonadi…. Ndiye kenaka khalidwe lawo lidzasintha. Amalapa pa zimene alikuchitira ndi amuna awo kapena akazi awo ndi kusintha. Amalapa mmene amakhalira ndi ogwira nawo ntchito, kapena ana awo kapenanso ozungulira nyumba zawo ndipo makhalidwenso oipa ndi kusintha ndi kukhala akulu msinkhu.

Chikonzero cha Mulungu kuti ife tikule tsopano

Mukuwona m’mene mpingo umakhudzidwira ndi nkhaniyi? Chikonzero ndi chuma chobiisika pansi pa nthaka. Chikonzero cha Mulungu ndi choti unsembe ya okhulupilira. Pulani ya Mulungu ndi kwa anthu ake ndi kumangilirana wina ndi mzake tsiku ndi tsiku monga timakhalira moona ndi tonse pamodzi choyamba chopindulitsa ndi chakuti onse amene ali ana a Mulungu amakula ndi makhalidwe abwino. Zabwinonso zimene zimakhala poyenda pamodzi ndi Mulungu ndi choti, ngati wina sakonda kuwala, amawonekera kuti ndi onama chabe. Ngati ndi wosafuna kukonzeka, ngati sasamala pazimene Yesu ananena pa zinthu izi ngati amakwiya ndi kupsya mtima pamemepo amaonetseredwa ngati a khristu onyenga. Zimawonekera kuti sanapeleke moyo wawo kwa Yesu chifukwa alibe choonadi ndiye satha sangakhale ndi Mzimu Woyera ndiye kukhala osakonda kuwala (Yohane 3, 1 Yohane 1, 3).

Choncho ngati mpingo ndi mpingo woona, ndiye ngati ansembe tonse tidzathandiza kuti tikhale ndimakhalidwe abwino. Tidzakhala tonse kuwala ndi moyo wina ndi mzake. Tidzathandizana wina ndi mzake kuwona zinthu zimene sitingathe kuona tokha. Ngati ndili wodzikonda, sindingathe kuona kudzikonda kwanga. Kudzikonda kwanga kuli kuwawitsa Yesu. Kudzikonda kwanga kuli kuononga kuthekera kwanga kukonda Yesu. Ngati ndili ndi kudzikonda zili kuwononga kudalitsika kwanga kwa Mulungu chifukwa Mulungu safuna kudalitsa kuzikonda kwanga. Zimawononganso umboni wanga wa Yesu ngati ndili wozikonda motero cholinga cha unsembe ndikuthandizana kudziwa Mulungu bwino tsiku ndi tsiku. Mu msika, ku nyumba zathu pamalo athu mu mpingo. Ndingakule kuchoka mu mkanda la kuzikonda ndi kukhala munthu wa Mulungu.

Paulo anati, 1 Akorintho 3) kuti anthu ambiri amene anapulumuka amakhala atachoka mu lawi la moto. Anthu awa amapita kumwamba koma atadutsa mu Malawi a moto pofika kumeneko. Werengani 1 Akorintho 3 nokha. Baibulo limati anthu ena anapulumutsidwa koma atadutsa mu malawi a moto koma ichi sicholinga cha Mulungu. Sizimene Mulungu amafuna kuti ife tikalowe kumwamba. Cholinga cha Mulungu ndikuti osati kuti tikhale makanda ndi uchimo kenaka ndi kupita kumwamba. Cholinga cha Mulungu ndikuti ndife mudzi oikidwa pa mwamba pa phiri umene sungabisidwe cholinga cha Mulungu tikhale oikidwa monga mfumu pa mapiri. cholinga cha mulungu ndi choti kuti mkwatibwi amene wakonzekera kale. Cholinga cha Mulungu ndi choti ndife wowengeka, omanga banja ndi mkwatibwi omanga uchimo. Cholinga cha Mulungu ndikuti mpingo ukhale okonzeka mwana wa Mulungu pamene abweranso kwa mkwatibwi.

Aliyense ndi wololedwa kwa Mulungu kukhalamu mpingo amene akonda kuwala. Ena aife tikhonza kukhala aang`ono. Ena a ife tingakhale ndi khalidwe loipa kwa nthawi zina koma ngati tili ndi mzimu wa Mulungu ngati tili ndi akhristu osati akhristu onyenga—ndiye kuti tili kukonda kuwala. kukonda kuwala pamodzi ndi abale ndi alongo. Tidzakwanitsa kuthandizana wina ndi mzake kukula. Ndiye kuti aliyense adzakula ndi mphamvu ndi mphamvu ndi nzeru . Tingakhale okonda Yesu ndi mphamvu zambiri ndi moyo wathu. Umboni wa Yesu ukhonza kukhala wa mphamvu koposa ndi kuononga mdaniwo sipazakhala ana okha okha ndi makhalidwe oipa amene angaoneke osati ngati Yesu.

Ana ambiri ang’ono ndi a makhalidwe oipa sizakondweletsa kwa makomo a ndende. Ana ambiri ang’ono ndi amakhalidwe oipa sizodzathandiza osakhulupilira kuti atsate Yesu.

Ngati tili mpingo wa amuna ndi akazi a Mulungu amene ali okhwima ndi kumaoneka ngati Yesu ndi moyo wathu ngati mpingo ndi wopambana, nzeru, mkwatibwi wopambana wa Yesu ndi mphamvu ya Mulungu ndi khalidwe la Mulungu mu moyo wathu ndiye anthu adzakhala okondwa ndi Yesu ndipo adzafuna kubwera kuti adziwe Yesu.

Choncho lingalirani za Chikhristu chonyenga mpando wa chiwiri) ndi kuti Mkhristu weniweni (mpando wachitatu, wachinayi ndi wachisanu) Lingalirani kuti khalidwe loipa sizoti kuti ndiye sanasambitsidwe ndi mwazi wa Yesu. Nkhani yeni yeni monga mu Yobu 3, Yohane 1, 2 Atesalonika 2 ndi Petro 2 ndi yoti Mkhristu woona ali ndi Mzimu wa Mulungu. Inde makhalidwe ake angakhale oipa monga mwana pa makhalidwe ake sakhala abwino koma ngati anabadwa kachiwiri ndi Mzimu ndipo monga makanda adzakhala akumwa mkaka adzakula mu choonandi ndi kuunika. Cholinga cha mpingo ndi kuthandiza munthu ameneyo wa makhalidwe oipa amene amakonda chowonadi kuti akhale ndi nzeru ndi kulimbika mtima poopa Yesu ndi kukula msinkhu.

Choncho tiyenera kumasulira Mkhristu motere ndiponso tiyenera kukhala monga mpingo uyenera kukhalira. Kuthandizana wina ndi mzake tsiku ndi tsiku kuti wina asaumitsidwe kapena kunamizidwa ndi uchimo. Tiyenera kukhala ngati ansembe. Ndipo ana ang’ono adzakula ndi mphamvu.

Yesu adzakhala ndi umboni:—Mkwatibwi adzazidwa ndi Mzimu ndi mawonekedwe ake. Yesu adzakhala ndi mpingo umene makomo andende sadzatha kugonjetsa. Motero kukongola kwa Yesu kudzakhala kwa Isilamu onse ndi kuchita uHindu kuti onse awona kuno konse. Tisakhale makanda chabe amene amanena bwino zinthu. Koma osakhala monga Yesu ndipo Mpingo sikupeza anthu onyengezera chabe amene amakhala bwino chabe koma alibe Mzimu wa Yesu okhala mwa iwo monga munthu. Koma tikhonza kukhala opambana namwali wa Yesu uwu ndi uthenga wa bwino wa ufumu wa Mulungu.

Mphamvu chosintha, mphamvu yowonetsera

Tsopano tibwererenso ku machitidwe a mipando isanu ija, Anthu amene angakhale mu mipando wa chiwiri, wachitatu, wachinayi ndi wachisanu ali opezeka ku Bapatisiti, Nazarene, Methodis ndi ma Pentekositi mu misonkhano awo. Chifukwa tamanga molakwika mpingo ndipo anthu onsewa ali pamodzi. Mipando isanu yafanizira ija. Kuphatikizira ndi mpando wa chiwiri umene suloledwa mu mpingo ngati mamembala koma posowa chilungamo, chiyanjano mu tsiku ndi tsiku mu unsembe (monga Mulungu amafanizira ndi kulamulira) wa pa mpando wachiwiri amaloledwa (mukusamvera kwa Ambuye) 1 Akorinto 5). Monga ali oipa ndipo wa mu mpando wachitatu nthawi zone amakandira kapena osafunidwa, zoona zake ndi zoti 85% ambiri amene amaloledwa mu mpingo kuli konse ndi mpando wachiwiri kapena wachitatu. Uku ndi zomvetsa chisoni ndi zosafunikanso ngati tili kumanga mu njira ya Yesu. Posakhalitsa tidzakhala ndi Chisilamu kapena mu Hindu amene tidziganiza kuti ali chiwalo cha mpingo.

Koma chimbedzo kungokhala mwa mpingo wa chipembedzo (siumene mpingo umene mulungu amafuna kuthandinzira) umene uli ndi onse inali ya anthu pamodzi. Mukuvetsa zimenezi?

Ngati tikhala mnjira imene Yesu ananena ndi kuyamba kumanga njira imene mpingo uyenera kumangidwira, ndiye tikhonza kudziwa amene ali ongonama chabe kapena amene ali opanda mphamvu ndipo tingawathandize. Ngati mpingo ungamangidwe pozungulira mu mgwirizano mmalo mwa msonkhano wa lamulungu ndiye onse anthu amitundu inayi idzakhala ndi kulumikizidwa tsiku ndi tsiku. Onama ndi ana enieni. Atate ndi anyamata adzakhala mu mgwirizano ndi wina ndi mzake Kukonda wina, kuthandizana ndi wina zobvuta kukwaniritsa lamulo la khristu. Ngati mmenemu ndi mmene mpingo ungaonekere, ndiye muli ndi mphamvu zosintha zinthu ndi kuzionetsa poyera.

Mukukumbukira mu Machitidwe 2:42-47 kuchokera tsiku loyamba chikhristu onse ali pamodzi okhulupira ndipo anali ndi zofanana? Izi sizinali chifukwa cha “chikhalidwe” kapena zochita—zidali anthu okhala mu moyo ndi chipulumutso cha Yesu. Anthu lero amakhala kumbuyo kwa zokangana za chikhalidwe kuonetsera kuti amakonda dziko ndi zinthu za mziko ndi kufuna mulungu wa la mulungu mmawa ndi lachitatu usiku ndi magulu okumana lachisanu. Koma anthu a mulungu obadwa kuchokera ku mwamba ndi Yesu, poyamba ndi zofunika tsiku ndi tsiku ndikukhala onse pamodzi nyumba ndi nyumba. Anali onse tsiku ndi tsiku kukhala mu chiphunzitso cha Atumwi, kukhala mu chiyanjano kunyema mkate, kupemphera. Sanali ongofanana mu zinthu zina Mach 5.4.5 koma moyo watsopano kuchokera mwa iwo monga Yesu analamulira kuti zinthu zonse sizinali zawo zawo. Baibulo limati anali anthu alukana pamodzi monga mithempha ukhalira. Uwu ndiwo mpingo wa chipangano chatsopano-Tsiku lililonse. Mgwirizano wawo, aliyense wa iwo anali ndi amayi ambiri, abale, ndi alongo ngati ndi m’mene tingamangire pali mphamvu ya mulungu wosintha mphamvu yoonetsedwa ndi kuchotsa malinga a satana mu moyo wathu.

Tiyenera kumanga mu njira ya mulungu

Ngati tikumanga mu njira imene anthu anamangira ndi miyambo ya anthu pokhala ndi mmawa wa la Mulungu ndi ulaliki ndiye anthu awa amene ali mu mpando wa chiwiri umene amangosoneyeza anthu odzangowonerera chabe tsopano 1 Akorinto 5 limanena kuchotsa chotuopitsa. Baibolo limanena kuti ngati pali ojedana pakati panu, achiwerewere, odzikonda, opembedza mafano kapena anthu amene amakonda dziko lapansi tiyenera kuwachotsa mu msonkhano. Mau a Mulungu amati ngakhale osadya nawo pamodzi amene amati ndi .okhulupilira koma osakhala nawo mu njira ya Mulungu. Tisakhale nawo pamodzi kapenanso kukhala abwenzi athu. Yesu anati tiyenera kuwathamangitsa. Baibolo limati aliyense amane amati ndi mbale koma amakhala mu uchimo ayenera kuchotsedwa pakati pa msonkhano. Tsopano, mungachite bwanji zimenezi ngati ndi lamulungu mmawa. Kapena ndi moyo wokha womwe ndi wowonekera mmawa okha.

Chifukwa chiyani sikothekha kumvera malemba amene amanena kuti tikhale amodzi ndi kuchotsa chotupitsa? Chifukwa tamanga molakwika. Chifukwa mmene tamangira ndi miambo ya anthu, munthu uyu wofooka (wa mpando wa chitatu) amaoneka oipa. Ndi munthu winayo amene sanapulumutsidwe wa pa mpando (wachiwiri) amawoneka ngati ndi opambana nthawi zambiri. Nthawi zina ndi Dikoni kapena mkulu wa mpingo, kapena ndi mbusa ndipo wa mpando wa chiwiri amachita zozizwa mu dzina la Yesu la Mulungu mmawa munthu uyu ndi otsuka koma salinso mkhristu ndipo munthu wa pa mpando wa chitatu ndi ofooka. Koma munthuyu ndi opulumutsidwa ndipo munthu uyu wa chiwiri amene sachita mau ndipo sakonda kuwala. Munthu ameneyu sali opulumutsidwa ayi. Ali chotupitsa, ndipo Mulungu salikulola kuti akhale pamenepo.

Anthu ena amagwiritsa chiphunzitso cha Yesu mu mwambi wa Tirigu ndi na Msongole (Mat 13) kulola uchimo wa Mpingo, pomati tiyenera tiyenera kulola tirigu ndi na msongole kukulira pamodzi monga Yesu ananenera. Angelo ndiwo adzamalize nchito yonse ku mapeto anthawi yino. Uku ndi kulakwa kwakukuru ndikusiyanitsa ndi chimene Yesu ananena nthawi zina mmodziwa kapena mosadziwa pa zofuna zawo). Werengani Fanizo limeneli pa inu nokha, ndipo mudzaona kuti Yesu Sali kuchotsa chimene Paulo, mwa mzimu analamulidwa kuchotsa chotupitsa pakati abale Yesu sanati, “Muyenera kusunga udzu pakati pa mpingo—Yesu anati Munda ndi dziko, Yesu sanati mundawo ndi mpingo, zoona tili mu dziko lapansi koma osati mu dzikomo ai nkdipo mdani adzabyala udzu mdziko la pansi. Sitikufuna kuti tingobweretsa zinthu zina zake zosamveka ai mudziko pakuchotsa udzu kuchoka ku dziko. Ife tiyenera kukhala mchere ku dziko lapansi ndi kuunika kwa dziko lapansi ndi zimenezi anthu onse azdadziwa kuti muli ophunzira anga”! Mpingo wuyenera kukhala pamwamba pa phiri ndipo sungabisike, choncho kuti awone machitidwe anu ndi kutamanda Mulungu pa tsiku limene lilinkudza. Tiyenera kulola udzu kukula pakati pa tirigu MU DZIKO LAPANSI” Mwachoncho Yesu sanati, Munda ndi Mpingo. Udzu ndi tirigu sukulira pamodzi mu mpingo monga mwa Mulungu.

“Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse? Tsukani chotupitsa chakale kuti mukhale mtanda wa tsopano monga muli osatupa. Pakutinso Paskha cha Dumbo, kuipa mtima, koma ndi mkate osatupa wakuona mtima, ndi choonadi.

Ndinalembera inu kalata uja kuti musayanjane ndi achigololo, sikonse konse ndi achigololo adziko lino la pansi, kapena ndi osilira ndi okwatula kapena ndi opembedza mafano pakuti mukutulule mdziko lapansi. Koma tsopano ndalembera inu kuti sayanjane naye ngati wina wochedwa mbale ali wa chigololo, kapena wosilira kapena wopembedza mafano, kapena olalata kapena oledzera, kapena olanda, kungakhangale kudya naye otere iai.

Pakuti nditani nawo akunja kukaweluza iwo? Kodi amene ali mkatimu simuwaweluza ndi inu koma akunja awaweluza Mulungu? Chotsani oipayo pakati pa inu nokha (1 Akorinto 5:6-13).

Yesu sanazidzutse yekha inde munda umene Tirigu ndi Namsongole umakulira pamodzi mpa nthawi ya kutha kwa dziko lino. Si mpingo ai, monga mwa Yesu, “Munda ndi Dziko” musalore ena kudokoneza inu uthenga wa kusamvera ndi onyengelera.

Tsopano muziwoneka bwini, ngati tingayembe kumanga bwino, mu njira imene Baibolo limanena kuti mpingo uyenera kumangidwira , ndiye kuti onse anayi anthu adzakhala ndi maubwenzi abwino tsiki ndi tsiku munthu uyu wachiwiri amaoneka mngati otchuka mu msonkhano amayimba bwino ndipo amadziwa Baibolo kwambiiri siwabwino ameneyo! Koma ngati muli ndi mgwilizano wa tsiku ndi tsiku mungawone kuti amadana ndi mkazi wake. Mukapita ku nyumba yhake la chiwiri mungawone kujti ali kukalipira ana ake ndipo mukapita lachinayi madzulo kukawelenga malembo ndi iye mukapeza kulibe kuti kunyumba kulibeko. Mukafunsa mkazi wake “Ali kuti amuna anu” Ndikufuna kuwelenga naye pamodzi malembo ndipo amati, “sitikudziwa kumene apita” salinso ku offesi angochoka, amabwera mochedwa ndipo sanena kuti, ali kuti” Mungadziwe zimenezo la mulungu lokha mmawa mungawone kuti munthuyo amakonda dziko ndipo ali ndi moyo wanseri ngati Sali kunyumba yake yachinayi usiku. Sadzavala chizindikiro cholembedwa Ine ndine wonyanga ndipo ndili ndi moyo wa chinsinsi, ndiye munganene kwa iye ndinabwera ku nyumba kwanu kudzapemphera nkdi inu kudzawenga malembo dzulo madzulo ndiye inu kunalibe kumeneko. Munali kuti? Akazi anu samadziwa kumene mwapita? Munali ndi abale ena kukagawa moyo wa Yesu mu msewu?

Amayankha, “Ai sichoncho. Sizikukukhudzani ai. Ndipo mukati chabwino chifukwa chiyani mukutero? Ndingadziwe chifukwa chache. Sizikukukhudzani ai. Chotsani chisoso chanu mmaso anu. Bwanji muli oweluza ine motero ndimalamulo. Chabwino, ndamva kumene mukuchokera ndipo ndikukupemphani kuti mufewetse mitima! Mwinadi palibe chobvuta koma timangofuna kufunsa, chifukwa ndikukhuzidwa ndi mtima wanga koma simungalire kuti tilankhulanabe kuti ndidziwe? Ai samalani zanu.

Chabwino choncho ndiyenera kuchita zimene Yesu ananena kuti tizichita mu zinthu ngati izi ndipo tiganize kuyitana abale ena kuti tipitilize kulankhulana pa nkhani imeneyi aliyense amene mungaganiza amene tonse tinagulitsidwa kwa Yesu ndipo ndiwozindikira zinthu? Yesu anandilamula ine kutenga enga awiri kapena atatu ena kuti tilankhule za zinthu izi chifukwa choti ndiotsatira ake a Yesu muyenera ,kumvera Yesu pobweretsa ena awiri kapena atatu ndipo tikhale pansi ndikulankhulana za izi, akanena kuti sindifuna kuti ndilankhulane ndi ena abale awiri kapena atatu ndikuti musamale zanu osati za ine

Ndiye mumadziwa kuti ooh tili ndi mavuto akulu pano ngati sizisintha, ndiye kuti safuna kukonda kuwala kapena kukonda chowonadi, ndichitsimikizo choti ndichotupitsa chimene ndichofunika kuchoka pa mpingo ngati palibe kulapa.

Tsopano tingadziwe bwanji kuti tili ndi zobvuta m’banja? Munthu uyu anali wa mphamvu pa la mulungu mmawa ndingadziwe bwanji za munthu onyenga amene ali ndi miyoyo yiwiri? Tikadziwe ngati tingapite kwawo la chinayi madzulo. Pomaliza, timadziwa kuti mbale uyu sanali kukonda kuwala chifukwa sanali kukonda kuwala ndi mboni yoti analibe mzimu wa Yesu. Safuna kusintha, sasamalira pamaganizo athu. 1 Akorinto 5 limati ngati wina azitcha yekha mbale koma kukhala mu uchimo osadya naye, osakhala naye pamodzi ngati bwenzi ndipo achotsedwe pakati pa abale. Ngati tingamange mmene anthu amangira ndipo sitidzadziwa kuti pali vuto ndi munthu mumoyo wake ndiye chikumbumtima chake ndichoumitsidwa. Koma ngati tingamange mnjira imene Yesu ananena kuti timange potengerana zothobwitsa, wina ndi mzake tsiku ndi tsiku mwina munthu uyu adzakhala munthu wodalilika.

Wonani abale kuti kapena ukhale mwa wina wa inu mtima wiopa osakhulupilira, wakulekana ndi Mulungu wa moyo komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku pamene pachedwa lero kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjero la uchimo. Pakuti takhala wolandirana ndi khristu ngatitu tigwiritsa chiyambi chakutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro. (Aheberi 3:12-14).

Ngati tingamange mu miambo ya anthu ndi kulalikira kwa lamulungu ndingaganize kuti munthu uyu ndi mkhristu koma Mulungu akuti “Sindimudziwa iye” Tingamuthandize bwanji ku uchimo ndi kuwukira kapenanso kukonda dziko ngati sanawonekere?

Nthawi zina kulalikira kumachitika pakati pa miambo ya anthu kwa anthu amene amaganiza kuti ndi akhristu?

Ngati mungamange mnjira yabwino tsiku nkdi tsiku kuchokera mu zinyumba ndi zinyumba ndiye kuti uchimo udzawonekera ndipo tidzawona ngati ena li kukonda kuwunika ngati sakonda kuwunika ndiye timawayika kumene ayenera kukhala monga mmene Mulungu amanenera, “Achotseni pakati pa abale ndipo munthu uyu sakhalanso otchukanso ayi adzayamba kuganiza za moyo wake chifukwa sakhalanso monga mmene analiri kale ai mwaina tsopano ndi mmene angakhale mkhristu weni-weni.

Kapenanso mukumanga munjira ya Mulungu tinapeza chuma chimene siitinachidziwe ngati tili monga mmene Mulungu analamulira kukhudzidwa ndi miyoyo ya mabanja ndi zodabwitsa zizawoneka zimene siziwoneka ku magule ena kapena lamulungu mmawa. Ngati tidzakhala monga Mulungu afunira wokhala tonse ndi chikhulupiliro chimodzi tonse ngati munthu mmodzi ndipo wokhlupilira onse anali pamodzi ndipo zodabwitsa zidzakhalanso. Koma kufuna ufumu osati kukhala wodzidalira tokha kuchotsa miyolyo yathu kuchokera muthupi ndi mwazi koma mukubadwando mu mzimu.

Mbiri ya dziko yasonyeza kuti anthu amene mu mpando wa chiwiri ndamene ali atsogoleri koma ndiosapulumutsidwa! Kodi munamva za munthu wotchedwa Charles Finney? Monga munthu wa mkulu anali mtgsogoleri wa woyimba koma adazindikira kuti sadali mkhristu ndipo anabadwanso ndikukhala munthu wa Mulungu. Charles Finney anabweretsa anthu 500 000 kwa Yesu mu nthawi ya moyo wake mukudziwa kuti iye anali wodzikpereka ndi wachipembedzo mukukula kwake koma anadziwa kuti sanali mkhristu ai ndipo anasinthika mu mtima ndikukhala munthu wa Mulungu ndingatchule ambiri ena amene timawadziwa kuti ndi anthu amphamvu a Mulungu kuchokera mu mbiri anali atsogoleri mu chikhristu koma anazindikira kuti sanali akhristu ai.

Mbiri ya dziko yasonyeza kuti anthu amene mu mpando wa chiwiri ndamene ali atsogoleri koma ndiosapulumutsidwa! Kodi munamva za munthu wotchedwa Charles Finney? Monga munthu wa mkulu anali mtgsogoleri wa woyimba koma adazindikira kuti sadali mkhristu ndipo anabadwanso ndikukhala munthu wa Mulungu. Charles Finney anabweretsa anthu 500 000 kwa Yesu mu nthawi ya moyo wake mukudziwa kuti iye anali wodzikpereka ndi wachipembedzo mukukula kwake koma anadziwa kuti sanali mkhristu ai ndipo anasinthika mu mtima ndikukhala munthu wa Mulungu ndingatchule ambiri ena amene timawadziwa kuti ndi anthu amphamvu a Mulungu kuchokera mu mbiri anali atsogoleri mu chikhristu koma anazindikira kuti sanali akhristu ai.

Choncho chinthu chabwino chimene tingachite ndi munthu amene sakonda kuwala ndi kumvera zimene Yesu ananena ndi zimene Paulo ananena “pitani kwa iwo okha” ndikuyesa kuwapindula ngati apitilira mu uchimo ndipo safuna kumva ndiye tengani awiri kapena atatu ena ngati sakonda kuwunika ndi kusasamala ndiye tiyenera kumvera Mulungu ndikuwachotsa iwo mu mpingo mwina moyo wawo wungapulumutsidwe chifukwa tagwiritsa chida chimene Mulungu anatipatsa ife kuti achenjezedwe. Sitichita izi mu mkwiyo ,kapena mu kuziyenereza tokha oyera. TimachitaIzi mu kumvera Mulungu .

Timakonda iwo. Timafuna kuti asinthike mtima moona ndithu Osati kunyengedwa chabe kwa mtima. Ichi ndi chida chimene mulungu wapereka kwa ife potandiza anthu kuti azindikire amene ali mu chipembezo koma onamizidwa.

Mpaka titathandizana wina ndi mzake tsiku lililonse ndi kukhala ndi mgwirizano weni weni tsiku ndi tsiku munthu mu zochita zake zenizeni sizingatheke kudziwika baibulo limati chotupitsa pang’ono chimatupitsa mtanda wonse, choncho ngati munthu ali ndi chinsinsi cha uchimo mu umoyo wake ndipo sanathane nazo ndiye kuti anthu onse a mulungu amapwetekeka chifukwa cha chimenechi. Anthu a mulungu anagonjetsedwa Kwambriri Ai chifukwa mmodzi wa iwo (Akani) anakwirira choipa mu nyumba yake. Mulungu anachita ndi anthu ake pankhani monga mudziwira. Tiyenera kumanga mpingo mu njira imene iyenera kumangidwira kuti tisakhale ndi nyumba yoonengedwa. Pamenepo pokha pamene anthu angochokere mu mpando wachiri kufika du mpando wachisanu.

Tithandizane ena kuti akule

Tsopano palinso fundo ina imene tiyenera kuti timango bwino. Izi zimakhuzana ndi (wampondo wachitatu) munthu wofooka, amene makhalidwe ake Sali abwino koma anapulumutsidwa. Ngati tingamange mmene anthu anamangira miyambo ya anthu ndiye tingampaste uthenga kwa munthuyu. Tikuyetsesa kuti akhale mu zochita zathu. Koma ngati timange mmene anthu a dziko ndiye kuti zochita za munthuyo sizingadziwike ayi mwina ali kulira ndi chimo pamene agona usiku chifukwa mbusa amamva kulira kwa nkhosa ndipo ndi mkhristu woona okhala ndi mtima woona ndi mtima wofewa munthuyo safuna kukhala wogonjetsedwa. Ali kulankhulana ndi ndi Yesu za uchimowu, koma mu miambo ya anthu sathandizidwa ai amangomva uthenga ndipo amangoyetsa kwambiri koma nthawi zonse, uchimo umapititita kwa zaka mpaka amangosiya.

Pa dzanja lina, ngati tingamanga mnjira ya mulungu yimene iye anatiuza pali ndithu chiyembekezo. Mu nyumba ya mulunga munthu yemweyu pa nthawi yockepa pa sabata imodzi mwa mkhristu adzakhala ndi abable anayi kapena asanu amene ali kumuthandiza mu kufooka kwake. Ali kupemphera limodzi, ali kulankhula limodzi, ali kulankhula pamodzi mawu a Yesu. Ali kuulura machimo ake kwa anzake. Okhulupirira awa ali kuchengetana wina ndi mzake tsiku ndi tsiku ndi kubweretsa mphatso mu umoyo wa munthuyo. Choncho mmalo mwa kumva zowawa yekha, munthu wan’gono ameneyo ali ndi anthu amene ali okhudzidwa ndi moyo wake tsiku ndi tsiku kumuthandiza kusintha Palibe ali ndi chinsinsi mu umoyo wake kapena kutsiyanitsa moyo usadziwike ndi iwo amene amudziwa Yesu ndi kulumikizidwa kwa iye “kubatizidwa ndi mzimu umodzi, mu thupi limodzi” Timathandizana mu zofooka sathu (monga ife tili nazo) palibe otchuka. Tikuthandizana wina ndi mzake monga mbale pakati pa abale.

Choncho tiyeni tinene za munthu amene ali mkhristu kwa sabata imodzi. Ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu monga Messiah Baibulo limati machimo ake anasambitsidwa. Baibulo limati machimo ake awululika kwa iye mulungu ndi wokhulupirika ndi olungama ndi mwazi umapitirira kutitsuka. Chingachitike ndi chiyani ngati munthuyo atafa asanagonjetse uchimo mu moyo wake? Munthu uyu ndi opulumutsidwa ndi Yesu monga Paul wa Taitus ndi mwazi wa Yesu khristu munthu ndi wonulumutsidwa monga unatipulumutsa ife ku uchimo! Okhulupirira amakonda choonadi amafuna kusintha ndiye ndi opulumutsidwa, osati kungonamizira chabe. Ichi ndi chipulumutso chimene tili nacho abalendi alongo.

Uthenga wa bwino wa ufumu

Tikupatseni malembo amodzi amene amabweretsa zinthu zonsezi pamodzi mu buku la Ahebre Baibulo limati timakonzedwanso ndikukhala woyera. Ndinakonzedwanso-zinachitika pamene tinapeleka moyo wathu kwa Yesu. Kukonzedwa ndi kukhala woyera mawu oti “woyera” amatanthauza mbee ndikukhala wofunika kwa mulungu. Atate akonda mwana ndi onse amapeleka moyo kwa Yesu kuchokera mu mtima aika khristu ndi kubvala chikhristu .

Mwachocho mwana watsopano ndi mkhristu wakale onse ndi opulumutsidwa chimodzimodzi chifukwa atate anaombola mwana, Yesu ndiye pamene atate ayang’ana pansi ndi kuona anthu amene asambitsidwa ndi mwazi wa nkhosa. Angelo a imfa amapitirira ndipo sawakhudza ai mwazi wa Yesu wakhala wa thunthu kwa iye mu chionetsero cha mipando isanu amene anali mpando wachitatu, wachinayi ndi wachisanu. (Ana, atate ndi anyamata) onse ndi opulumutsidwa kwatunthu.

Ndi Yesu yekha amene ali wangwiro, mwamva? Ndiye pamene tabvala Yesu timakhala wangwiro ngati iye ali popitirira ndi chipulumutso chathu timakhala a ngwiro monga Yesu ali. Takhala a ngwiro ndi woyera ndi mmene malembo amatiphunzitsira. Ngati muli ndi mzimu mkati mwanu pamene muli opulumutsidwa kwenikweni ndiye mwakonzedwa mu ungwiro monga Yesu ali.Ndipo machimo anu akhululukidwa ndipo dipo laperekedwa pa machimo anu onse ndipo ndinu okonzedwa mu mzimu wa Yesu.

Tsopano nkhani imene tikulankhula kulumukiza ndi mpingo mu maonekedwe osati kukhala wangwiro kokha komanso kukhala woyera-chida chothandiza mu nyumba ya mulungu ngati mpingo umangidwa mu njira ya mulungu monga ngati uyenera kumangidwira ndipo ndife okhunzidwa ndi ubale wa wina ndi mzake akhale wa ngwiro monga pakuti ali kale a ngwiro pa mwazi wa Yesu koma tidzawathandiza kuti akhale chida potumikira mulungu. Tidzawapanga a mphamvu mwa khristu. Tidzawapanga kuti akhale pa ubwenzi ndi Yesu ndipo ife sitidzapedza chipulumutso chokha kwa Yesu koma Yesu adzapenzanso kanthu kwa ife! Ana ang’ono kupedza kanthu kuchokera kwa Yesu Abambo ndi anyamata adzapereka kanthu kwa Yesu! Mwana wa nkhosa wa mulungu adzapedza phindu mzowawa zake.

Mpingo omwe Yesu akumanga ndi njira ya onse amene ali wokula msinkhu. Ngati timanga ndi miambo ya anthu, anthu ambiri amakhala makanda kwa nthawi yayitali. Izi ndi zokhumudwitsa Yesu mmalo mwa chisangalalo. Tikamanga monga mwa pulani ya mulungu ndi maonekedwe ake ndipo makandawo adzasanduka Asitifano, Paulo ndi a Yohane ndipo kuyambira wang’ono mpaka wamkulu adzakahala monga Yesu pamodzi ndipo mpingo udzakhala monga mzinda oikidwa pa mwamba pa phiri umene sungabisike. Pamodzi tonse monga mwa Paulo tidzakhala malo okhalamo mulungu mwa mzimu osati kungopedza mphoto ya chipulumutso chokha, koma tsopano pomalizira

Yesu adzapedza phindu la mpingo woona! Uwu ndiwo uthenga wabwino wa ufumu. Kukonzedwa ungwiro ndi kukhala woyera.

“Mulungu ndiye kuunika ndipo mwa iye monse mulibe mdima. Tikati tiyanjane ndi iye ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi koma ngati tiyenda mkuunika monga iye ali, tiyanjana wina ndi mzake ndipo mwazi wa Yesu mwana wake utitsambitsa kutichotsa uchimo wonse”.

“Tikati kuti tilibe uchimo tizinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. Ngati tibvomereza machimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama iye kuti atikhululukire machimo athu ndi kutisambitsa kutichotsa chosalungama chiri chonse.” (1 Yohane1:5-9)

Alipo munthu amene akonda kuunika, ndipo wina amene amati alibe uchimo, koma akonda mdima kuchokera pa tsamba ili kuti mulungu amaona mosiyana.

“Ndikulemberani tiana popeza machismo akhululukidwa kwa inu mwa dzina lache. Ndikulemberani Atate, popeza mwamuzindikira amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani anyamata popeza mwamulaka oyipayo ndikulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.” (1 Yohane 2:12-13)

Ngati timanga mu njira ya mulungu idzakhala yobveka bwino kwa iwo okonda kuunika adzachoka ku mwana kukhala atate ndi ku anyamata. Uwu ndi uthenga wodabwitsa!!

 

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon