Devedi Living'isitoni Ndi Mkate Ochokera Kumwamba

4/8/2003

Chilembe, Africa 1996

Mkate wa Moyo

Mbale analankhula za Devedi Livingstoni kubweletsa mkate ku Afrika. Devedi anabweletsa ku afrika chiphunzitso cha Yesu mwana wa Mulungu. Anabweletsa uthenga mmene Yesu amakondera anthu, amafunira kukhulukira machimo athu onse ndi kubweletsa moyo wa tsopano. Tikudziwa kuti uwu ndi uthenga wabwino kwa ife. Devedi anabweletsa mkate m’mbale ndi chobvundikira, ndipo ndamva mmene mkatewo unali kukoma.

Timabwera tonse la Mulungu ndi kulankhula za mmene mkate unaliri ndi chiphunzitso choona. Mkate ndi wabwino ndithu mbali ya uthenga umene Mulungu watiitanilako ife sikungophunzitsa mmene mkate, koma zimene Baibulo amati “mafungulo a mu ufumu” ziphunzitso za Yesu mmene tingatsegulire khomo ndi ziphunzitso mmene tingachotsere chovindikira ndi kutilora ife kudya mkate umenewu.

Yesu sanangatikhululukira machimo monga zodabwitsa monga ziliri kapena kuti tiganize za chiphunzitso chake. Yesu anabwera kuti ife tikhale ndi moyo umene iye anakhalira ndi Atate—osati kudzakhala chabe, kufa ndi kupita kumwamba. Monga Baibulo linena. Anabwera kuno kuti tikhale mu “mphamvu ya moyo wagwiro” kukhala mu chiyanjano ndi moyo ndi chikondi pamodzi ndi atate ndi abale amene Yesu anachita.

Yesu amafuna ife kukhala kuthyola ziphunzitso za mkate mu mphaka, akufuna ife tidye mkate umene iye anadya ndi Atate ake.

Mkate Umodzi

Zambiri zimene chipembedzo ndi chikristo chachita kwa zaka zambiri ndikutiphunzitsa mozama za mkate. Ndi nthawi yoti tidye mkate ndi nthawi tsopano tichoke kuchokera kuphunzira ziphunzitso za mpingo ndi kukhala mpingo (Aefeso 3:10, Mateyu 16:18) Yesu sanabwere kuti tikhala ongooneka bwino. Anabwela kudzatipatsa ife moyo ochuluka—tikhale mu moyo wake tsiku lililonse wina ndi mnzake, osati kulankhula mau wake obweleka ndi kuyimba ndi kupemphera mau a chipembedzo. Anabwera kudzatipasa MOYO! “Ana ang’ono, kondani ndi mzake” uwu unali chiphunzitso cha Mulungu mutu ndi Yesu NDI Yohane ndi Paulo ndi Petro.

Timaphunzitsa za banja la Mulungu, osati chipembedzo chokaonera. Kodi ife timaonera zochitika m’banja lathu? Kapena tikhala mchikondi ndi mabanja tsiku lonse? Simungaonelere banja mukhonza kukhala banja. Baibulo limalankhula bwino za izi. simungaonelere chipembedzo choona, mukhonza kukhala mpingo woona. Banja limene mungaonere ndi losunga ana amasiye osati banja lowona. Kusunga ana amasiye kumakhala bwana wake ndipo amasonkhana onse kudzadya chakudya. Mwina amapita ndi kusewera pamodzi ndi kulandira chiphunzitso kuchokera kwa mabwana awo. Choncho limachita zambiri zimene banja limachita, koma ndi ana amasiye osati banja. Mulungu waitana ife kukhala banja tsopano ngati simuli banja, padzakhala kusintha kumene kudzakhala popeza Yesu. Pofuna kudziwa Yesu ndi kudya mkate, tiyenera kukhala mkate ndipo ngati tingakhale banja la Yesu, tiyenera kuthandizana zedi. Sitiyenera kukhala wozikonda. Tiyenera kusiya kunyada ndi kufuna kutsegula kwa anzathu za Yesu kusintha moyo wathu.

Tiyenera kukhala okhulupirika wina ndi mzake zamene tikumvera. Sitiyenera kubisa kumbuyo ka nkhope kapna chophimba koma tiyenera kutsegula miyoyo yathu ndi kulankhura pa zimene tikumva, pa izi ndi pamene Yesu adzathandiza Yesu anakwiya ndi chinyengo. Chifukwa chake sikuti anada anthu. Yesu amadziwa kuti ngati pali kunamizira kukhala njira ina pamene mu miyoyo ndi munjira ina sangathe kuchilitsa ife mkati monga m’mene ankafunira.

Yesu anamutcha satana ndi tate wa mabodza. Yesu ali okwiya ndi chinyengo ndipo Sali okondwa ndi ife. Izi ndi mbali ya banja—pokhala okhulupirika ndi wina ndi mzake. Pazimene tikumva ndi mmene tikuchitira. Koma muyenera kuzipereka, kwa wina ndi mzake kuchokera mkati, sindingakhale odandaula kapena yopambana. Ndikufuna kukhulupirira Mulungu kuti angathandize ine. Koma ndi sangozinyenga kuti angandithandize ine. Koma ndi sangozinyenga kuti zonse zili bwino pamene sizili motere. Ndiyenera kuzichepesa kupeza abale abwino ndi azilongo kulankhula pa zinthu izi chifukwa pamene awiri kapena atatu ali pamodzi Yesu amabwera kudzakhala nafe, choncho ngati ndili ofuna kutsegula pang’ono mtima wanga, udidzalora Mzimu Woyera kubwera ndikuchiritsa ndipo Yesu adzakondwa. Ngati ndimanga makoma pozungulira ine ndekha ndi kufuna kukhala wamphamvu ine ndekha, pamenepo mphamvu ya machiritso ya Yesu sidzafika.

Yesu akufuna kukhala banja limene tingatsegule miyoyo wina ndi mzake. Anatipeza ife pa malo amene tinali odzichepetsa. Yesu safuna kuti ife tikhale odandaula ndi kwidzi koma, modzichepetsa pakupempha ena kupemphera, kuthandiza ndi nzeru.

Iyi ndi njira imene banja liyenera kukhalira, koma izi sizingatheke la Mulungu m’mawa wokha. Mpingo wowona ndi banja pamodzi, monga banja lilolonse ndi banja tsiku liri lonse. Funani ndi kuyembekeza zimenezi mwa inu nokha “kwa Yesu amene akonda ine, ndidzatsegula mtima wanga kwa enanso. Ichi ndi chisankho chimene muyenera kuchita. Mungasankhe kukhala kumbuyo kwa chotchinga posatsegula moyo wanu ndi kulankhura ndi abale ndi azilongo pa zimene mukumvera. Mungasankhe kubisala kumbuyo kwa misonzi ndi zowawa kuchokera kw aanzanu. Koma mgati mungatero simudzapeza mphamvu ya machilitso ya Yesu. Adzatsenulira moyo wake kwa ife ngati tili banja Yesu adzakhala kutali mmalo mwa kusintha miyoyo yathu ndi kukhala mnjira imene afuna. Akufuna ife kugwira ntchito imeneyi pamodzi monga banja. Ndipo pamene titsegula miyoyo yathu Yesu mu mphamvu yake yonse ndi chikondi ndi ulemerero kupeza ifeyo. Koma ngati tili ndi kunyada kwambiri ndi mantha ndi zimene ena angaganize kapena kunena za ife, ndiye Yesu sadzatipeza ndikutipatsa moyo ndi mphamvu imene afuna atipatse.

Kudya mkate wokondana wina ndi mzake

Choncho tabwera mu dzina la Yesu ndi umboni wa moyo ndi mphamvu ya Mulungu, tikufunsani kudya mkate umenewu usangowelenga, ndi kukufunsani kuti mukhale mpingo ndi banja lowona, osati kuonera. Yesu afuna malo amene angakhalemo sakhala nyumba zomangidwa ndi manja a anthu. Amakhala mu banja, ndipo mubanja basi. Akufuna malo amene angakhale amene inu muli osati anthu wowerenga za mkate ndi kuwonera “mpingo” koma malo amene banja liri ndinu mpingo tsiku lirilonse.

Mzimu Woyera kudzera mwa Paulo anati masiku wonse ayenera kukhala ofanana. Zipembedzo zina ali ndi masiku apadera masiku “woyera” koma Yesu njira yake imodzi ndi kuti tsiku lirilonse ndi lofanana. Yesu ndiye sabata la mpumuro. Pamene tikhala mwa Ysu tsiku lirilonse, pameneposo tili pa mpumulo. Mulungu aitana inu kukhala banja . Tidzasankha kukhala banja? Ngati pali chokoma pakati pa inu mlongo muli mudzagwetsa kusamva nako? Mudzagwira bondo lawo ndi kupempha iwo kuti afewetse miyoyo yawo? Mudzapita ku phiri ndi kupemphera ndi misozi kwa iwo kuti afewetse mitima yawo? Mudzatsegula miyoyo yawo kwa iwo? Mudzapeleka moyo wanu kwa iwo tsiku lirilonse, kuzipeleka molimba, kupelekedwa onse atunthu ndi aphumphu mwa Kristo, ndi kulira mokweza kwa Mulungu pa mirakulu ya chikondi! Mudzapanga zimenezi kwa muombori Yesu? Safuna inu kuti mungodziwa za moyo wake. Akufuna kuti inu mukhale moyo wake.

Umenewu ndiwo uthenga wabwino wa ufumu. Muli mkuitanidwa mu moyo wake ngati mudzathawe kuchokera mu kunyada, kuzikweza ndi ku ulesi. Mulikuitanidwa kukhala Yesu, osati kungodziwa iye. Tsiku lirilonse kondanani wina ndi mzake kuchokera mu mtima ndi kukhuzidwa ndi miyoyo ya ena, kuthandizana ndi ana ang’ono kukhala monga Yesu tsiku lirilonse.

Uku ndi kuitana kwa Mulungu, uku ndi kukuitanani mkate wa chikondi pamodzi tsiku ndi tsiku ndipo Yesu adzadza miyoyo ndi kupanga inu tunthu monga m’mene sizinakhaleko pachiyambi. Adzachapa ndi kutchuka mantha anu ndi kuumitsidwa kwa mtima. Mtsinje wa Yesu udzathirira madzi, mu moyo ndi kukhala bwalo ya chonde. Chikondano ndi chikondi ndi Atate chidzakula kulirabe. Mudzaona nkhope yeniyeni ya Mulungu monga m’mene mukondana wina ndi mzake uwu ndi uthenga wabwino. Lero ngati mumvera mau ake, musaumitse miyoyo. Fewetsani pamaso pa Mulungu. Funani kuti tsiku lirilonse limene mutsegule miyoyo yanu kwa iwo wokuzungulirani ndipo simudzasiyana kuchokera kwa wina, chifukwa muchita izi kw AYesu muombori.

Mpingo monga banja

Mu mabanja ambiri muli mabanja eni eni amene anabadwa ndi mai ndi bambo amene timawatcha “Ana obvuta” Ana ena ali obvuta kuposa anzawo, koma ngati ali banja, ali banja, ndipo tidzathandiza kuthetsa mabvutowo. Sititenga ana eni—eni a mbanja ndi kupita nawo kuphiri ndi kuwasiya kumeneko. Timafunsa Mulungu mu nzeru kapena kukubweletsa kunyumba mu banja.

Pokuthandizani kuti mukhale ndi chithunzi cha mmene zingakhalire pamene mpingo uli pamodzi, taganizani mu kulingalira banja nyumba yanu, ndi ana amuna asanu akazi atatu ndi mai ndi Bambo. Kodi bambo ndi amene amalankhura munyumbamo? Ngati mmodzi mwa anayamata wa zaka khumi ndi zitatu ali ndi kanthu kolankhura, sangathe kunena kodi? Kodi amai sapeleka maganizo awo mu banja? Nanga kodi ana ochepa sangaongolere banja? Kodi pali ufulu nthawi zonse mbanja kwa mm’odzi yekha olankhura? Kodi pali mbali kwa ana ochepera kulira ndi kulankhura zofunika? Ziyeneranso kutero pamene mpingo wonse uli pamodzi, angakhale ang’ono angatsegule moyo ndi kulira pa chosowa, mwina mai angathandize kuthesa bvutolo ndikunena za mai wa uzimu, pamene mpingo uli pamodzi. Mwinanso bambo wa uzimu angathenso kuthetsa bvuto la mwanayo. Koma umu ndi mmene mpingo ungakhalire pamene ukumana pamodzi. Aliyense wa banjalo angathe kutsegula miyoyo ndi enawo a m’banjalo angathandize zosowazo. Izi simu msonkhano wokha. Pamene alongo ali kuchapa pamodzi pamene ali kuyimba nyimbo mu msonkhano onse, Bwanji sangathenso kuyimba nyimbo pamene ali kuchapa pamodzi?

Ngati mungalankhure ndi Atate pamodzi mu msonkhanowo, Ananso onse sangathe kulankhura ndi Yesu pamodzi pamene ali mkuyenda onse pamseu pamodzi siza Mulungu mmawa ndi lachitatu madzulo. Palibe zimene zingachitike mu msonkhano zimene sizingachitike pamene tili mkuyenda pa msewu pamodzi.

Sitidikira msonkhano kuwauza abale ndi alongo pazimene Yesu wationetsera lero. Sitidikira msonkhano kutsegula miyoyo ndi kufunsa kuthandizidwa ndi china chake. Tili chimodzi—modzi ali ndi bvuto angakhale ndi mwana wa ng’ono ali ndi bvuto angakhale ndi masiku apadera limene aloledwa kulankhura za bvutolo, kapena adzalankhula nthawi iliyonse chifukwa pali chikondi mbanja? Uwu ndiwo mpingo woona, pamene tsiku liri lonse tingathandizane. Palibe kusiyana pakati pa msonkhano ndi popanda misonkhano. Chifukwa timabweletsa chiphunzitso cha Yesu kwa aliyense tsiku ndi tsiku. Timalambira kuchokera pansi pa mtima ndi wina ndi mzake tsiku ndi tsiku, m’mawa ndi usiku pamene tipita kopeza chakudya, timapemphera tonse ndi kulambira pamodzi. Uwu ndiye banja la Yesu.

Penanso, pamene tikhala banja limodzi lalikulu, ngati muli kupita kumudzi ndi kumenya mkazi wanu, kapena kukhala ndi nkhanza ndi iye, Ayenera kukwanitsa kunena kwa inu. “Umu simmene njira ya Yesu pamodzi Yesu anati mwamuna ameneyu samvera kwa iye mkaziwo ayenara kupita ndikupeza awiri kapena atatu ena a mu bajja la Mulungu, ndi onse ayenera pamodzi kulankhura ndi munthu amene ali ndi nkhanza. Ndizimene anatiphunzitsa ife mu Mateyu 18, manyumba athu simalo obisalira kuchokera mu chowonadi. Sitingathe kukhala oweluza nyumba yathu ndi kukhala osasamala chiphunzitso cha Yesu. Tsopano tili tonse banja la Mulungu ndi nyumba zathu zili za ife tonse, choncho tsopano mlongo angathe kubweletsa ena kudzalankhura ndi mwamuna wake. Sitipeputsa chiphunzitso cha Yesu mu zinyumba zathu. Chiphunzitso cha Yesu sichili cha “nyumba ya mpingo” Tsopano ali pamodzi pamene tipita ku msika kapena tipita ku zinyumba kapena pamene tipita kophunzira. Tsopano chiphunzitso cha Yesu chilli mu nyengo ndi muzochitika zosiyana siyana. Tili banja limodzi tsiku lirilonse masiku onse, usiku onse.

Kumanga njira ya Yesu

Yesu anati kuti ngati mudzafika mau anga mu wochita, pamene chimphepo chibwera (ndipo adzaima) pamenepo nyumbayo idzaima. Idzaima chifukwa inamangidwa pa mwala olimba poika mau ake mu moyo osati poganiza chabe, kapena kuimba za mau ake ngati tidzaimba za izi, Pemphelani ndi kulankhula za izi ndipo tidzasinthe njira imene timakhala pomvera mau ake wina ndi mzake, pamene mphepo idzabwera, angakhale kuti nyumbayo ndi yokongola mmaonekedwe idzagwa yonse pansi. Izi ndi zimene Yesu analonjeza mu Mateyu 7, ndiye mangani mu mu njira yake, ndikuchita kanthu ndi choonadi chake. Mvekani zimenezi, ndipo mphepo sidzaonongamo.

Mu njira imene mbalame yaing’ono kapena mpira zimakhalira mu miyala pamene mphepo ya mkuntho imabwera, mungakhale mu khumbi la mapiko a Yesu ngati mudzamanga munjira imeneyi ndikuloza nkhope yanu kwa iye pamene abwera, mudzakhala mu khumbi la mapiko ake. Mphepo ya mkutho idzapita ndipo Dzuwa lowala lidzaonekera, mbalame zidzayamba kuyimbanso ndipo moyo udzakhala wa bwino ndi watsopano. Choonde mangani mu njira ya Yesu. Awa ndiwo mau a Ambuye lero.

Mmene mungadyere Mkate woonawu.

Palinso gawo lina mu Yohane 6 ananena mau amene ali olimba. Anati idyani thupi langa ndi mwazi wanga. Anayesetsa kuwauza kuti zimveke bwino. Baibulo limati anthu ambiri amene amamulonda iye anamuleka iye. Anamusiya Yesu ndi kupita kwina chifukwa sanamvetsetse ndi maganizo awo. Yesu sanawatsatire ndi kuwauza kuti anali kwa iwo kumvetsa. Anacheukira kwa ophunzira ake ndi kufunsa, “mukufuna nanaunso kukhoka ndipo Petro anatti, Ambuye Yesu, muli ndi mana moyo a moyo, sitifuna kupita kwina kuli konse. Tifuna kukhala ndithu.

Yesu anafuna anthu amutsate iye amene angathe kumva ndi mitima ndi mizimu. Yesu angaike zinthu zobvuta ndi cholinga patsogolo paife zinthu zimene sitingathe kuzidziwa—mmalo mwa kupatutsa nkhosa kuchokera ku mbuzi. Anthu amene angadziwe ndi maganizo awo koma osafuna kumva ndi mizimu yawo sangathe kumutsata iye Yesu weniweni. Yesu weniweni amapanga zinthu,zachilendo poyesa mitima yathu. Ananena ndi ife za zinthu zooneka zobvuta monga “Idyani thupi langa ndi Imwani magazi anga” zimamveka molakwika ndithu, zimene angakhale Baibulo silingabvomereze kuti ndi zabwino. Chonsecho, Yesu amayesa amene amabvetsera ndi mtima ndi amene amava ndi makutu awo. Yesu amayesa amene amakonda Mzimu wa Yesu ndi amene amakonda zakunja kokha. Pali zambiri monga izi mu zambiri mu Baibulo pamene Mulungu amasiyanitsa anthu amene amamva ndi makutu awo kuchokera kwa amene amavetsera mu mizimu yawo. Iyi ndi njira ya Mulungu, ndi imene inakhalapo muzochitika mu Yohane 6, mmene ambiri anathawa Yesu, zapitirira mu mbadwo wina uli wonse kale angakhalenso tsopano pano. Ife sindife Mulungu. Iye ndiye Mulungu. Timazipeleka ku zinthu zimene zili za Mulungu kaya sitikuzimvetsa ndi maganizo athu kapena ai. Izinso ndi zimene zili mbuku la Yobu.

Tsiku lililonse Yesu ali kulankhula mu mkuluwiko umene uli obvuta kuumvetsa, poonetsa amene amamukonda iye mu mizimu yawo, kusiyana ndi amene amagwiritsa maganizo awo kumva bwino chabe. Ngakhalenso lero iye ali kulankhula mu mkuluwiko otero umene uli obvuta kumvetsetsa, kuti aone amene angachoke ndi ena amene anganene, “Tidzapita kuti ? mwa inu muli kuwala ndi moyo” zilinso choncho lero monga zinalili kalelo.

Yesu Mkate Mwa ife

“Ngati mukonda ine, sungani malamulo anga. Ndipo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu nkhoswe yina kuti akhale ndi inu kunthawi yonse. Ndiye Mzimu wa choonadi amaene dziko lapansi silingathe kumulandira, pakuti silimuona iye, kapena kumuzindikira iye. Inu sindidzakusiya inu mukhale ana amasiye, ndidzakwa inu katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi sindiona ine, koma inu mudzandidzindikira kuti ndili ine mwa Atate wanga ndi inu mwa inu” Yohane 14:15—20.

Ndidzabwino, ndi choonadi chodabwitsa zimene Yesu sanapitilire kupita kwani apamene iye adali kuno ndi kuyimba nyimbo kw aiye ndi kuyesa kumvera ziphunzitso zimene anapeleka kwa ife ndiye tsiku lina kutsogoloku ndikubwera kwa ife. Zodabwitsa za chiphunzitso chake ndi choti adzakhala ndi ife mpaka nthawi yamalekezero a dziko ndipo sadzatisiya ife ngati a masiye. Anauza ophunzira ake kuti pameneiye adzabwera anthu sadzamuona iye koma inu. Ndipo timamuona iye osati ndi maso athuwa koma ndi maonekedwe a mzimu anati, mvelani ine ndi kukonda ine. Kondanani wina ndi mzake ndi kukhala amodzi monga ine ndi atate tili amodzi. Dziko silidzandiona ine koma inu mudzandiona ine chifukwa ine ndidzabwera ndi kukhala nyumba mwa inu. Ndakhala ndi inu, koma ndidzakhala ndi inu.

Sichiphunzitso chonyenga ichi, ichi ndi zoonadi, ali woona monga mu mpingo woona monga analili nthawi ya thupi. Zoona ndi izi Yesu anati zidzakhala bwino kuti kupita, kusiyana ndi kungoima pamene abwelanso. Awa simau wamba kapena ndi oshashalika chabe kapena chiphunzitso chopeka. Ichi ndi chenicheni. Yesu yemweyo amene anayenda panyanja ndi kuikitsa akufa ku moyonso adzabwelanso ndikukhala mkati mwa ife mu mphamvu ndi chikondi ndi ulemerero. Sadzabwera pamene diso la dziko limuona iye koma tingakonde iye ndikupeleka miyoyo yathu pachilichonse chimene tifuna pa moyo wathu, ndikukondana wina ndi mzake kuchokera pansi pa mtima, kenako Yesu yemwewu amene anayenda panyanja ndi kutidzera pa khomo lotcheka ndi kupeleka maso kwa osaona adzakhala pakati pathu mwa ife ndi kulola ife kuti tikhale pa ubwenzi ndi iye ndi atate ndi wina ndi mzake.

Anthu ena sanaone imfa asanaone Yesu asanabweranso mu mphamvu chifukwa tsiku la pentekositi linali litangodutsa masiku makumi asanu pasaka. Anabweranso kwa ife mu masiku makumi asanu. Sanabwere kudzakhala ndi ife koma kudzakhala mkati mwa ife. Ichi ndi chinsinsi chimene chinabisika kwa zaka ndi mibadwo yonse mu Akolose 1, chopambana cha nyengo chonse ndi ichi osati Kristo ndi inu, osati Kristu kungobwera chabe kwa inu (ngakhale zili choncho) koma Kristo mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero izi ndi za iwo amene adzakonda iye ndi kupeleka miyoyo yawo pa cholinga cha iye. Halleluya! Sadzatisiya ife amasiye ndipo ambiri sanalawe imfa mpaka adzabweranso mu ulemerero kukhala mkati mwathu. Izi ndi zimene Yesu ananena mu Yohane 14.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon