FUNILO LA MULUNGU…TSOPANO

Cholinga chake ndi “kudzera ku Eklezia tsopano,” kudzera mulumikizo weniwene ndiponso osati chigulu cha anthu amene amakhala nawo pa china chake, koma miyoyo imene ili yolukana—“Kuvomereza tchimo kwa wina ndi Mnzake,” “kunyamulirana chiphinjo cha wina ndi mnzake.” Ndiponso “kukondana wina ndi mnzake.” Kuti anthu onse adziwe kuti ichi ndichochoka kumwamba (Yohane 13).

7/5/2006

Tsiku lina ndimaonera pologalamu yina yokhudza Albert Einstein, mumalonje mudali mau amene adanena chinthu china monga, “Mkamodzi kalikonse munthawi zathawi munthu amabwera ndi zimene zimaonaeka dziko ndi maso osiyana ndi kusintha dziko limene iye amakhalamo.” Ife tikufuna kuyika chowinda patsogolo pa inu. Khalani inu monga munthu amene aona dziko osati ndi maso achilengedwe, koma kudzera mu maso a Uzimu. Khalani inu olimba kuti mukhale m’modzi mw aanthu amene Aheberi 11 amayankhula. Onani masomphenya a Mulungu a pokhala pa Mulungu mwa Mzimu ndi ulemerero ochuluka. Onani chithunzi mmaso anu amalingaliro, ngati m’mene okhulupirira mubuku la Aheberi adaonera. Iwo adawona mzinda amene omanga ndi opanga wake adali Mulungu, ndipo pamenepo iwo sanakhutitsidwe ndi china chilichose.

Iwo samafuna kubwereranso kumzinda wakale. Iwo adawona chikonzero chakumwamba chilli patali, ndipo ngakhale iwo samachigwira ndi manja awo, ngakhale panthawi imeneyo sakadakhala mu mzindawu umene Mulungu adaupangira iwo, sanali kufuna kubwerera kumbuyo. “Pamenepo, Mulungu sanachite manyazi kuitanidwa Mulungu wawo ndipo iwo, anthu ake.”

Chowinda choterochi chilinso pa inu ndi ine. Onani kuzungulira dziko limene inu muli, maka maka “mpingo” umene inu muli ndiponso kulimbika kwake kudzadza inu munjira yoti mpaka inu muvomera kutaya, kapena kuyika zinthu zanu zonse pamoto m’moyo wanu kuti muonenetsetse kuti chowindachi chakwaniritsidwa mu zonse zozungulira inu. Inu muyika moyo wanu pachiswe. Inu muyika banja lanu pachiswe. Inu muyika ntchito yanu pachiswe, inu muyika chilichonse pachiswe chifukwa cha Mulungu ndi zolinga zake. Ichi chiyenera kukhala komwe likuchokera. Kuyankhula monga mwa Baibulo ichi ndicho chikhristu chenicheni chomwe chiliko. Iyi simfundo kapen alingaliro lotchuka, koma ku Aroma 4 amati, “Amene ali ndi chikhulupiriro cha Abrahamu ndi ana a Abrahamu.”

Tsononthawi kapena mpingo uliwonse umene muli, pali ponse pamene muli (dziko kapena pokhala pamene muli napo ndi mupatcha panyumba tsopano) muyenera kukhala osamalitsa kwambiri kuti musavomereze zinthu zina zomwe Mulungu sadzifuna. Musavomereze izo kuchokera paulesi, umbuli wa Mau a Mulungu, olo kapena mukusowa kwa masomphenya kapena mutchimo lomwe pamoyo wa inu nokha lakuphimbani inu kapena lakuzunzani kuti moziwone kuti ndine operewera. Musalore ena omwe ali okhutitsidwa muchilaodikeya kuti akuyendeni pansi kuti mukhale ofunda chabe osati otentha.

Mwina mwake mwagwiritsa ntchito yoti ndinu MUNTHU wamba chabe ndipo mulibe kalikonse muonetse kapena kupereka. Mwina mwake mukuganiza kuti ganizo lanu silofunika chifukwa kuli anthu ambiri anzeru ndi ophunzira kunjaku…… “Tsono inu mungadziwe chiyani?” Ndingofuna ndikulimbikitseni inu kuti aliyense amene inu muli, muli ndi kena kake koti muonetse kapena kugawa. Ngati inu munamufunsa iye kuti atsuke machimo anu, muli nacho china choti mugawe. Khumbilo lake liri kuchokera pa wangono kufikira pa wamkulu kuti munthu aliyense amudziwe iye, akhale mu uphungu ndiponso muchiyanjano ndi iye, kwa tsiku ndi tsiku.

Kamodzi kalikonse munthawi za nthawi munthu amabwera kapena anthu amalowera, amene ali kufuna, kudzaliona dziko limene amakhalamo ndi kusintha dziko lomwe lawazungulira iwo. Izo ndizo Aheberi 11. Amanena izo ndi zimene Mulungu watiyitanira aliyense wa ife kuti tikhale ngati tili akulimbika ndi akufuna ndipo muchiyanjano ndi mutu. Khalani mwa iye, ndi pamenepo padzakhala zipatso zambiri zoti tionetse. mukhonza kukhala munthu amene mungathe dziko limene mukhalamo.

Ndili ndi chiyembekezo kuti ife takonzapo kusamvetsetsa pangono kumene kumaononga chikristu icho ndi kuti kusanduka m’khristu ndi pothera nkhani. Ndipo kenako “kukhala nawo mumpingo wakukhosi kwanu pa sabata” ndikukonzanso mpakana Yesu abwerenso ndipo inu kupita kunyumba yanu pamwamba pa phiri. Ine ndikungofuna kuthetserathu maganizo amenewo chifukwa chakuti simaganizo a Mulungu. Mulungu amatcha machitidwe amenewo chipembedzo chabodza ndiponso Laodikeya amene amamusokoneza iye.

“Cholinga cha Mulungu ndi chakuti tsopano, kudzera mu mpingo, nzeru za Mulungu zidziwike ku ulamuliro ndi amaundido kumwamba...” Aefeso 3:10.

Ichi ndi cholinga cha Mulungu TSOPANO. Funilo lake ndi kupanga nzeru zake kuti zidziwike kudzera ku Mpingo. Osangoti kudzera kwa iwo okha amene amadziona kuti ndi opulumutsidwa, ndiponso osati kungodzera mwa anthu ena ochepera mphamvu amene amamvetsera ku mayankhulo patsiku lina lake la m’sabata atavala masuti ndi mataye…koma kudzera mu umoyo opangidwa, kudzera mugulu la okhulupiriia amene ali “omangidwa ndi kulukidwa pamodzi ndi minofu yogwirizana,” ndi anthu amene mphatso zawo ndi zolowerana ndi kulukidwa bwino amene ndi ziwalo za wina ndi mnzake” “mtima umodzi, malingaliro amodzi ogwirizana” Limbanani kuti mukhale ndi masophenya mu machitidwe a okhulupirira osati odzikundikira zolowa, omangiriridwa pamodzi odzipereka kudziphunzitso za atumwi, kunyema mkate chiyanjano, pemphero, tsiku ndi tsiku pachigulu kuchokera pakhomo lina kufikira pakhomo lina. “chipembezo chomangokhala nawo” chilli bwino kwa a Hindu ndi a Silamu, koma sichimene Yesu adayamba ndi kudzodza.

Cholinga chake ndi “kudzera ku Eklezia tsopano,” kudzera mulumikizo weniwene ndiponso osati chigulu cha anthu amene amakhala nawo pa china chake, koma miyoyo imene ili yolukana—“Kuvomereza tchimo kwa wina ndi Mnzake,” “kunyamulirana chiphinjo cha wina ndi mnzake.” Ndiponso “kukondana wina ndi mnzake.” Kuti anthu onse adziwe kuti ichi ndichochoka kumwamba (Yohane 13). Iye adati ichi “chidzanyazitsa maulamuliro ndi mphamvu” chifunilo cha Mulungu tsopano “Ndikudzera mu mpingo” kuti uchititse manyazi satana ndi maulamuliro ndi mphamvu zake zonse. Ndipo chifunilo chaka kutengera ndi malembo, TSOPANO ndi kudzera mu mpingo ku apanga adani ake kukhala chopondera cha miyendo yake-osati chabe pakubwera kwake kwachiwiri ndi ufumu wamphamvu wamuyaya chabe, kumene kudzakhale kumaliza kwa ntchito ya Mulungu koma TSOPANO.

Ndiponso, izi ndi zoona, ife sitikuyankhula nkhambakamwa. Ife sitikuyankhula zochita zayendera chigulu, osatinso zokhudzana ndi meleniamu ino, osatinso zokhudzana ulamuliro wa chipembedzo. Osati kufewetsa mafupa ndi minofu yathu, koma mtanda…. Tikuyankhula zokhudza anthu kuwonetsera moyo chimodzimodzi njira imene Yesu adawonetsera moyo wake, ngati Mfumu ya mafumu onse. Iye adabadwa ngati mwana wosabadwira m’banja lokwanitsa mu chodyera cha ng’ombe, amakwera bulu abwereka, ndipo adalibe cholowa (chuma) chenicheni cha iye mwini—opanda mphamvu, maphunziro, opanda “kukongola kapena ulemerero akuti wina aliyense akadakopedwera kw aiye. “Tikuyankhula zokhudza kukhala okonda anthu kuchoka okonda anthu kuchoka pansi pa mtima amene akhonza kuona m’mitima ya anthu ndikuwabweretsa iwo ku mtanda. Tikuyankhula zokhudza kuwaonetsa anthu zokhudza kubwera kwake padziko ndi umoyo wake, ndi kuwayitana iwo akhale asodzi a anthu. Kuti akhale gawo la Nyumba yake, “mokhalamo” mwake. Kuti akhale miyala ya moyo. Omwe sadakhalapo anthu, kukhala anthu.” uwu ndiye mtima wa Mulungu.

Landirani Yesu waku Nazareti ndi mfumu “osati wa dziko lino,” osati ngati ogonjetsa a Roma kapena dziko lina lirilonse lomwe timakhalamo, kapena ‘mpingo” mlandileni iye ngati mfumu yomwe idakonda, ndipo idakhululukira ndipo idapereka moyo wake……ndipo yomwe idali ndi funilo lotembenuza matebulo ndi kukwapula, ngati padali pofunika, chifukwa chachikondi cha Atate ndi Nyumba ya Atate Ake.

Yesu anali wakufuna kulifunsa dziko limene amakhalamo ndipo pakutero ndi kulisintha ilo, ndipo iye watiyitana ife kukhala chimodzimodzi iye. Uwu siuthenga ungoulutsa. Uwu ndi muyitano kuchiyero ndi kupatulitsidwa ku cholinga cha Mulungu, ndipo uwu ndi muyitano kukweza masomphenya ake mu mtima ndi miyoyo yathu. Gwadani pa maondo anu ndi mupemphere. Uwu ndi muyitano osati ongosintha dziko lowoneka chabe, komanso kusintha dziko losawoneka. “cholinga chake tsopano, ndikudzera ku Mpingo kupanga nzeru zake, nzeru zake za Mulungu ku maulamuliro ndi mphamvu” ndi kwa anthu anse.

“Tsono siyani khala la moto liyeletse milomo ndi mtima wanu, yanganani kwa Mulungu ndi kufuula “ine ndili pano nditumeni!”

<<<
jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon