UTSOGOLERI WA YESU
MU MOYO
Ndi moyo wopambana umene adatiitanira anthu ake kukhala pamodzi paliponse osati makonzedwe a “misonkhano”
7/5/2006
Talankhula zonsezi ndi zofunikanso kunena kuti palibe zonsezi kukwanila ngati palibe moyo wa tsiku ndi tsiku monga 1 Akorinto 12–13 pokonzekeretsa chaputala 14,” popanda moyo wa tsiku ndi tsiku izi ndi “zoopsya” sitingalankhula za “msonkhano” posiya zofunika kwambiri. Nkhani iyi ndi yayikulu. Uku ndi kupambana ndi kukula kwa moyo mwa Yesu kwa anthu ake mudziko lino, mosalumikizana, moyo wa yekha okhala ndi anthu achipembedzo ndi chofunika zokonzelathu ndi munthu oyera m’modzi yekha umakhala kwenikweni motere kuchokera muzachilendo, kupenya moipa, anthu ochimwa amagwilitsa “ufulu pa mwamba pa zofuna zawo. Moyo weniweni, 1 Akorinto 12–13 ndi choyambilira potikonzetsela mu ufulu wa mu 1 Akorinto 14.
Tiyenela kuphatikiza “zinthizi” zonse zambuyomu panthawi yomwe mtima yonse ali pamodzi monga ansembe achifumu osati ngati wowonelera monga zikhalila (Efeso 3:10) moyo wa tsiku ndi tsiku wa Machitidwe 2:42–47, 1 Akorinto 12, Aheberi 3:12–12, ndi a MAI AMBIRI (chikwi) abale ndi alongo. Yesu adati iyi ndi chikonzero Ndi moyo wopambana umene adatiitanira anthu ake kukhala pamodzi paliponse osati makonzedwe a “misonkhano” Afuna kukhala nazo zathu osati, “msonkhano” kapena kugawa nzeru, kapena kuimba chabe mtima wake uli pa munthu hiwanthunthu. Luka 9:23–27, 57–62. “Chipembedzo choona kuyambila wang’ono mpaka wamkulu” kubvala mzimu wake.
Sizongokhala pang’ono mofewa mu msonkhano wokonzedwelatu kapena osakonzedwelatu, ndi kumatiwotsogozedwa ndi Mzimu’ osati chifukwa sitidziwilatu zimene tidzachite ndiye kuti titsogozedwa ndi mzimu sinchonho. Sizotelo ai motero monga Jannes ndi Jambles. Zoyelekeza zimaonetsedwa kuchokera za maonekedwe a dziko, kuoneka ngati zoonazo.
Kusiyana kwa chipembedzo chosinthika ndi kukhala mu zenizeni wa woukawo, yesu wamoyo ndi zokokerana. Msonkhano wokonzedwanso mwamakono ndi zochitika, (ndi zoikidwa) kapena mu “nyumba” sindizo zofunika zenizeni poyelekeza ndi mwayi omwe yapatsidwa ndi ife lero.
Iye sanatitanile ife kuzatsopano ndi zosinthika mamangidwe. Watitanila ife ku moyo watsiku ndi tsiku odya pamodzi ku mtengo wa moyo, ndi odzozedwayo! Inde zimenezi zidzasintha “misonkhano” koma ichi ndi chipatso, osati polekezela, osati kungoyamba zatsopano ndi chiphunzitsp chabwino, zochita, msonkhano wa mphamvu, m’mene anthu amakhalira pamodzi mu Baibulo mulibe. Zofafanirapo, kapena chiwelenge lero chatsopano m’mayendedwe ndi zopanda thandizo kumene osati choonadi. (zimene timayenela kupeza, kufuna zimene iye afuna) ndi malo amene Yesu angakhale ndi kuchita Chibvumbulutso 1-2 popanda choletsa monga wamoyo. Mfumu yokwezedwa ndi moyo wokhawo wodzadza (monga Yesu amanenela) chauzimu moyo wa kumwamba, yolimbikitsidwa ndi mawonekedwa wapamwamba, onse pamodzi kuphatikiza choonadi cha mphamvu yosaoneka wa m’mwamba ndi choonadi ndi chikondi ndi moyo Yesu anabweletsa uwu moyo kukudzanza. “Mitsinje wa madzi a moyo” moyo kwa anthu ake kuchokera mu mlengalenga, dziko losaoneka ndi maso a munthu ndi maonekedwe a pansi pano.
Moyo wa Yesu pamodzi siza misonkhano, zimene Yesu anabweletsa ku dziko lapansi ndi uthenga wa Angelo sangakhale osazama ndi moyo osatha ndi zotele ai. Msonkhano umene anthu ambiri amachita nayo ndi umene Yesu anafera. Sinchoncho! Yesu sanabwele kudziko lapansi kubweletsa njila yatsopano ya msonkhano kapena mpingo kapena bungwe sizili choncho poyelekeza kuti mu Eklesia azindikilitse (Efeso 3:10) iye afuna kuphwanya kuononga ndi kusokoneza mdani—ndi kusintha moyo ku moyo mu chikhalidwe ndi moyo ndi nzeru ndi mphamvu za mwana. Iye akubweletsa ana ambiri ku ulemerero” osati ku chipulumutso chokha. Akumanga MPINGO wake umene makomo andende sangapambane mwa chisomo cha Yesu Kristo ndi ulamuliro wake, tikutenga ana anthu ndi akanzi omwe ndi mabanja ndi oyandikilana nawo kuchokera ku chinsiriro ndi ukapolo wa satana. Miyoyo yasintha watibweletsa ife kumalo atsopano m’mwamba pambali yake. Mphweya watsopano wopuma, maso atsopano woyang’anila, makutu atsopano womvela mtima watsopano wodziwa, ndi chikondi, kusintha uku ndi kwa zonse mu moyo, kuphatikiza “msonkhano”!
Mukaona zimenezi zimatengela kulimba mtima? Mukuona zimenezi zimatengela chikhulupiliro ndi kumvela? Mukaona zimenezi zimene zingasinthe moyo wanu ngati muyamba kukhala mu zimenezi? Simudzaulizidwa kupita pa kama! Ife ndife ansembe achifumu tsiku ndi tsiku. Ndipo msonkhano udzakhala wowonjezerapo. Inde, zochuluka kwambiri zimakhala zochokela mu moyo wa pamodzi ndiye kuti muyenela kukonza nyumba zanu ndi mzinyumba za ena. Kutenga madzi, kapena chakudya, kapena chobvala ku nyumba zawo. Mukaona kuti ali okwiya ndi mwana, aitanileni pambali ndi lankhula nawo kapena kuyenda nawo mukaona kuzikweza mwa iwo, ikani mnkhono wanu pa iwo ndi kuwafunsa kuti osamatero, mukaona kuzikonda mwa moyo wa mbale ikani mkono wanu pa iye ndi kuti choonde “muzamazikondenso” sitingotseka maso anthu mpaka msonkhano wina. Timakhala pakati pa moyo wa wina tsiku lililonse ngati Ansembe pochita ntchito ya Mulungu ndi amai ambiri, abale, alongo” Ili ndi lamulo lochokera kw aMulungu mu Ahebri 3, ndi malemba ena ambili otele.
Aheberi 3:12–14. “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa osakhulupirira, wakulekani ndi Mulungu wamoyo, komatu ndikudandaulilani nokha tsiku ndi tsiku pamene patchedwa lero kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjelero la uchimo. Pakuti takhala ife olandilana ndi Kristu ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kuitana kwathu kuchigwira kufikira chitsiliziro.
Tamvani chomwe malembowa anena ichi ndi chochoka kwa Mulungu. Mulungu wa mphamvu akunena kwa inu ndi ine kuti tiyenera, tsiku ndi tsiku, kuchenjezana ndi kuthandizana wina ndi mnzake. Ife tiyenera kukhala kumbali yawina ndi mnzake tsiku lirilonse. Mzimu Oyera unasankha kunena kuti tsiku lirilonse. Siwudanene kuti la Mulungu lirilonse.
Siudanene kuti la Mulungu ndi lachitatu lirilonse. Siudanene kuti mu misonkhano mokha ayi. Udanena kuti khalani pachilungamo mumoyo wa wina ndi mnzake tsiku lirilonse ngati ena ali kupezeka, ndipo inu simukhala nawo chifukwa cha makhalidwe a moyo wanu, kapena kudzitamandira, kapena kudzikonda, kapena chifukwa chachitsankho cha mmene mungakhalire m’moyo wanu, Mulungu akunena kuti inu mudzakhala owuma mtima ndipo opanda kuthekera kwa kumva monga iye amvera. Inu mudzapusitsidwa kuti mukudziwa chowona pamene simudziwa. Icho ndicho malembo anena mwatchutchutchu! Iye sadangoti kuti mupange ichi. Iye adanena kuti ngati simupanga ichi, chidzakupwetekani inu kwambiri. Ngati ine ndilibe abale ondiyakhula ine tsiku ndi tsiku zokhudza moyo wanga tsiku ndi tsiku ndidzakhala ndi kuuma mtima. Ine ndidzakhala ndi kupusitsidwa. Inu mukhodza kunena “koma ndimawerenga Baibulo tsiku lirilonse!” “Koma ndimapemphera tsiku lirilonse!” “Mkazi wanga ndi m’khristu ndipo ndimamuona tsiku lirilonse!” Icho sidzomwe Mulungu adanena. Inu mukhonza kuwerenga Baibulo ndi kupemphera tsiku lirilonse. Koma ngati inu simufuna kukhalilana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku, uzakhala mtima wanu ukuumira, umirabe ndipo inu mukupisitsiwa pusitsidwabe. Mulungu akunena ichi ku Ahebri 3:12–14. Kodi mumakhulupirira Baibulo? Kodi mumakhulupirira Mulungu?
Kodi adalemba Baibulo ndi ndani? Mulungu, Mulungu adanena kuti tiyenera kulowerera pa umoyo wa wina ndi m’nzake tsiku lirilonse. Ngati inu mwandiwona kuti ndazikonda ndekha, muyenera kwa ine ndikunena “Mbale, osakhala odzikonda. Zimenezo zipangitsa Yesu kukhumudwa.” Ngati inu mundiona ndikunyada chonde ndithandizeni ndipo mundikumbutse kuti Mulungu amatsutsana ndikunyada. Ine sindifuna Mulungu anditsutse! Muyenera mundithandiza ine, chifukwa ine sindingaone kapena kudziwa kuti ndikulakwa nthawi zonse.
Palibe amene angakwanitse yekha. “Limbikitsanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku kuti pasakhale wina oumitsidwa ndi kuputsitsidwa.” Ichi ndi mbali ofunikira, (ndipo ndi yomwenso siyimveredwa ndi kutsatiridwa ndi anthu pafupifupi dziko lonse), ya moyo pamodzi tsiku ndi tsiku. Iyi ndi njira imodzi ya chifungiliro imene mudakhalira wa nsembe pogwiritsa ntchito mphatso yanu, ndiponso “kazembe wa Khristu, monga ngati Mulungu adayankhula kuzera mwa inu.
Ngati inu muyika mumachitidwe zoonadi izi zimene kunthawi zonse zakhala zili mu Baibulo lanu, mudzadabwa kuona m’mene Yesu adzakhalira chifupi nanu m’zaka ziwiri zikubwerazi kuchokera pano. “Limbikitsanani wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku.” Khalani olewerana pa ana ndi banja la wina ndi mnzake ndi kutchito komwe “tsiku lirilonse” pitani komweko! Inu muyenera kuleka ndi kutuluka ‘mmalo anu abwino ndi awofuwofuwo” ndikupita komweko kumene simukadatero poyamba! Indedi, ine ndikuthandauza INU! :) Chonde, pakuti Yesu! Akuyankhula MAU. “monga a Mulungu” mu miyoyo yathu, kudzera mu machitidwe, chikondi ndi nzeru, tsiku lirilonse. “pamene mubwera pamodzi abale, aliyense ali nawo mawu a chilangizo, salima, ndi chibvumbulutso.” Pamene bvumbulutso libwera kwa wachiwiriyo, siyani oyambayo akhale pansi.” Pamene mudzayenda mu ichi, muzapeza kuti ena, amene inu mumaganiza kuti ndi a khristu sakonda Yesu monga inu mumaganizira kuti iwo ali. Inu mudzapezanso kuti ena amene mumaganiza kuti ndi ofooka, akulimbira limbira ndi kuchuluka nzeru kuposa kuganiza kwanuko. Njira ya Mulungu imaoneka poyera zinyanga, ndikupanga ofooka kukhala olimba. Ulemerero kwa Mulungu!
Chuma ichi chayikidwa kwa inu. Chiyikeni m’machitidwe chifukwa cha Yesu. Inu muyenera kutathauzira cheni cheni chomwe ukhristu uli kudzera mu zimene Yesu adanena. Inu muyenera kumvetsetsa za utsogoleri ndi mwenimweni chomwe muyenera kukhalira. Khalani moyo wanu tsiku lirilonse, pamodzi limbitsanani wina ndi mnzake, manganani wina ndi mnzake. Thandizanani kukula wina ndi mnzake ndipo kondani Yesu kwambiri mu mausana ndi mausiku amoyo wanu onse. Bwerani ndi kukumana pamodzi pamanso a Mfumu Yesu.
Baibulo ndi loona mnjira iliyonse. Izi ndi zokhudza Yesu ndi omutsatira ake. Izi ndi nkhani za m’mene amawawidwira mtima ndi mmene amaphunzirira kudzera mmakhalidwe awo ndi Mulungu. Ife tikhonza kuphunzira kuchokera munkhani zawo, koma tikhonzanso kuphunzira: pakukumana ndi kuonana ndi Mulungu pamodzi pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mu ichi nafe tili “malembo amoyo.” Zolembedwa zonse mu dziko lapansi sizinganthe ife monga m’mene moyo wapamodzi ungatisinthire ife. Zinthu zakuya zomwe tizifuna sizidzafika pansi pa mitima yathu pamene zingawerengedwa kuchokera pa pepala chabe. Pamene tikonza zinthu pamodzi tsiku lirilonse, Yesu aliphunzitsa ife ziphunzitso zakuya zamoyo zomwe sitingaziphunzire kuchokera m’Baibulo, “ngakhale zoonadi ndi eklezia—mpingo.” “MOYO umasanduka kuunika kwa anthu.”
Moyo siunapangidwe kukhala ngati sukulu ya galamala yomwe timakaphunzirako mfundo zina ndipo kenako kukhulupirira ndondomeko ina kapena zinthu. Malo mwake Mulungu watiyitana ife kukhala amuna ndi akazi a Mulungu chimodzimodzi monga omwe adaliko pasadabwere ife—olumikizidwa kwa Mulungu yemweyo amene iwo adalumikizana naye—okhala m’chikondi chozama monga iwo adaliri. Kuti chimene tichichite kapena kuchikwanitsa, ife tiyenera osati kudziwa momwe iwo amadziwa zokha. Koma tiyenera kumva chimene iwo amamvera, Mulungu ayenera kuti—tenga paulendo onga ngati wawo. Tsono ife titenga ulendo umenewu mukugwiritsa ntchito Mau a Mulungu kumodzi ndi moyo wathu. Ife tiyenda ulendowu ndi misozi m’maso mwathu, ndikuthandizana wina ndi mnzake—mu nthawi yoipa ndi nthawi yabwino—ndi maso athu pa chiyembekezo chathu, Messiah wathu. Ife tikupita chitsogolo, kukhulupilira kuti Mulungu akhala otipatsa wathu, kutithandiza pomwe tikhala pamodzi.
Ngati ife timukonda Yesu ndi kumanga munjira yoyenerera, zipata za ndende sizidzatilaka. Tchimo lidzaphwanidwa. Zofooka ndi matenda adzachilitsidwa. Machimo adzakhululukidwa. Kuleza mtima kudzatengera ambiri kukulapa. Ubale udzamangidwa kapena kubwezeretsedwa, kuposa m’mene mungalingilire mu maloto anu okoma. Mudzawala ngati nyenyezi mu mlengalenga, kuonetsera ubwino wa Mulungu. Ndipo mkwatibwi, Mpingo adzadzikhalitsa tchelu ‘Ndipo adzakhala okonzeka pamene Mkwati adzadza!! Amen.