UTSOGOLERI WA YESU

MU MSONKHANO

Mumpingo umene Yesu amaonekela wa moyo, wochita-chita ndi wamoyo osakhala mbili yakale yoyelekeza imene iyamikilidwa ndi kuphunzitsidwa, apali ufulu.

7/5/2006

China chimene tiyenela kulimba mtima kusintha ndikukhala ndi msonkhano monga baibulo limanane mu 1 Akorinto 14: “Pamene mubwela pamodzi, abale mpingo onse uli pamodzi, zilizonse zichitike mukumanga tonse pamodzi aliyense ali ndi chimangililo, nyimbo, bvumbulutso” ngati tidzakhala motero, potero osakhulupilira adzagwetsa nkhope nanena kuti, “Mulungu ali nanu”.

Palibe bwana wina pambali pa Yesu “Musamutche wina mtsogoleri, Ambuye mphunzitsi, kapena mbusa. Ndinu nonse abale” muli ndi Yesu ndipo ndiofanana mwa inu nonse. Inde pali kusiyana kwa makulidwe, ndipo mphatso zina ndi “zoonekera” ndipo zina ai kapena zochepa kuonekera pa malongosodwe. Koma zonse zilipo ndipo zili ndi mwai. Nthawi zina timafuna chifundo cha Yesu ndipo nthawi zina timafuna kuphunzira kwa Yesu. Nthawi zina nyimbo kwa Yesu. Ndipo nthawi zina timafuna kuthandizidwa kwa Yesu pothana ndi zobvuta. Koma zonse ndi zofanana mwa Yesu chonde werengani 1 Akorinto 14:26–40. Palibe amene ali olamula, koma Yesu yekha. Timasonkhana pozindikila kukhalira pamodzi, mchikondi ndi ntchito zabwino” (Aheberi 10:24–26) Tiyenela kuganiza za pemphelo mmene tingathandizilane wina ndi mnzake pamene tili pamodzi, ndipo yense wa ife ali ndi udindo pa mau a Mulungu ndi chikondi chake. Popanda wina opambana” oikidwa kuchita kalikonse kupatula kumvela ndi kubvomereza kwa Mulungu monga wina aliyense ngati wina abweletsa chiphunzitso kuchokera kwa Yesu ndipo ena chimangiliro kapena nyimbo, kapena bvumbulutso, ngati mbale, mlongo agawa kanthu kamene Yesu waunetsela ndipo bvumbulutso lidza kwa wina okhalapo ndipo olankhulawo akhale pansi—ngati timvela malangizo a Mulungu, osati mwambo ya anthu chabe. Baibulo limanena nthawi zonse, ngati bvumbulutso lidza kwa wina okhalapo. “OYAMBA AYENELA KUKHALA PANSI” ndi zimene amanena mu 1 Akorinto 14.

Izi sizabwino kwa iwo amene amafuna kukhala otchuka ndi okonda kukhala akulu utsogolera ndipo owoneka ngati auzimu ndikumatenga ndalama za abale woyera mtima ife tatengela katundu olemela mu miambo kuchokera kwa Akatolika ndiponso kwa ma potesistant, ndi mpingo ya chipembedzo ndi ya makolo athu, akale. Mbusa kapena otsogolera zochitika amakhala patsogolo pathu kulankhula ndi ang’ono, anthu osadziwa kanthu ndipo ena onse amakhala ndi kumvetsela. Izi ndi zinthu zimene maphunzitso ake, Yesu anati, amadana nazo, ndimene zimalamulila anthu mokakamiza, koma Mulungu akuti zonsezi zisinthe, pa ubwino wa iye ndi ife.

Mwachoncho, ine ndikuganiza motele kwa inu kuti ngati tifuna kulemekeza mphatso imene ili mwa ife, ndikubweletsa mphatso zonse zili mwa anthu a Mulungu ndiye pafunika kusintha zinthu zambiri. Zopusa mmamvekedwe, mwa zina ndi mmene timakhalila mu msonkhano pamene takumana pamodzi. Pamene Yesu anali pano, iye, anthu amazungulila—Awa ndiwo anali abale, alongo Mariko 3. kukhala mozungulila iye! Zizoyenela kukhala motelo, pamene tili pamodzi ndi kumvetsera kwa iye osati munthu wamba okhala ndi mphatso zochepa ai? Zimenezi zosabvuta kwa inu zingaonekeso ngati zosafunikila, koma ndinenetsa kwa inu kuti mau oti “Pupeti” ndi “thupi” amanenedwanso choncho mu chi french.

Pamene tikhala tonse kuona ku tsogolo, zimaonetsela munthu m’modzi yekha. Sitikhalanso ofanana ai ndimakhala kapolo wa iye amene wakhala kutsogolo kwanga monga Ambuye, kapena undidziwitsa za pamseu, msilikali kapena mu kalasi kapenanso mumapemphelo. Pamene timaika mipando mmizire mmalo mwa chokala mozungulila Yesu, zimakhala ngati kuonekela kwa munthu mmodzi yekha ali owonekera izi ndi zoipa chifukwa pali mphatso zambiri mwa ife ndipo zili mbali ya Yesu. Ngati tiika anthu onse kuona patsogolo, ndiye tikukweza mphatso imodzi yokha. Kungatheke bwanji munthu modzi wonyada kulora yekha nthawi zonse kukhala patsogolo kapenanso poonekela.

umakhala mu mpingo

Mu chithunzi chili pansichi, kweni kweni chipembetso mmachitidwe owonetsela mu anthu, ndi “mipingo ya nyumba” alipo munthu wamba amene amakhala otsogolera, mwa iye onse amatsalira. Iye amayamba amamaliza amaphunzitsa kapena kugawa ntchito zina, kuphunzitsa “kupembedza” amalamulira zonse, kuyankha mafunso. Ndi kutsogolera onse Awa simau abaibulo ai 1 Akorinto 14:26 kuchepela monga mofunikila chotupitsa mu mtanda, umadzimitsa mphatso, ndi Yesu amataya umbuye mmaonetseledwe amenewa. Komanso njira zimenezo mulibe mbaibulo siziyenela kuhala choncho.

Kwa dziko lonse (kudziko lonse) chipembetso, kuphatikiza chikhalidwe cha chikristu) kupondeleza anthu mmachitidwe ndi zokozelathu zochitika sizili mu Baibulo, kapena pamtima wa Mulungu ndi maganizo ake. Yesu adalankhula mwachindunji ndi momveka, nazipatsa maina kotsutsana machitidwe odzadza ndi miambo ndi kuitanidza odzalalikila ndi ozikweza okha pa anthu a Mulungu. Ngakhale atumwi khumi ndi awili aja a mwana wa nkhosa adali abale pakati pa abale pakati pa oyela mtima osati oposa ena, monga mw aYesu mwini. Mulungu amakonda utsogoleri wa Samueli pakati pakati pa moyo wa abale osati udindo kapena kutchuka, koma chikondi ndi mphatso monga zifunikila. “Timakana Mulungu” pamene tifuna mtundu wa mtsogoleri wa Sauli, monga mwa chitsimikizo cha Samueli ndi anthu ake mwa choncho uku ndi kuitanidwa kopambana koposa miambo ya anthu zomwe zili zochokera mukuganiza za mmutu mu nthawi zino, koma mpaka titabwelelanso mu njira ya malemba, ndidzapitilabe kukhala ofunda, zotsalira za zotupitsa, monga mmene chikhalidwe cha chipembedzo chimachita.

Pano pali mbali ina tiiganizile. Timakhala nthawi yonse “muza” Yesu “kuchokela Yesu” kumvela ndi kuleza mtima ndi ufulu wa oyela mtima yonse posintha zinthu “kuchokela ndi kudzela mwa iye ndi mwa iye muli kukwanitsa zonse” zomangidwa ndi anthu “odzaonelela” ndi oyela mmodzi chikristu chamizidwa mukusapambana Yesu satha kupeza njira mwa inu, kapena kudzela mwa inu, kapena pamene sasangalala pamene anthu aumiliza anthu ndi zochita zawo” ndi mphamvu yonse yachabe. Kupatsa mantha, kutsatsa popeza mphindu la chuma pazomwe zimachitika mu chipembedzo cha anthu. Zosadabwitsa pamaoneka zimphamvu ndi mau otsulidwa pamene izi zikuchitika kwa ambiri mwa iwo ndi mwala wapangodya umene amisili omanga nyumba anaukana umenewo unakhala mwala wapa ngodya. Amisili ndiwo amene ali ndi zinthu zoonongeka, kapena amaganiza kuti ali ndi zinthu zotaika chifukwa sanathe kukwanilitsa kudalila

Yesu safuna isi ali (Mateyu 23 ndi zina zotero) zomanga anthu ndi maudindo a chipembedzo zimene zili ponse ponse lero. Ndizochititsa manyazi ndi kugonjetsedwa chifukwa mpatso zoonongedwa chabe, ndi luwi lake silimvekanso ndipo ndi zoona kuti angokhala kuti uthengawu ndi wabwino, kapena ndi wabaibulo kapena nyimbo ndi yokhudza kudzaonelera kokha, machitidwe owomiliza anthu sichipembedzo chochokera kwa iye.

Yesu Nyumba Mpingo Wamoyo!!

Ngakhale sitikhala ngati za iye sizingathe kusintha kwa ife kuti mako a kumdima sangapambane” kapena kugonjetsedwa pa moyo wa tsiku ndk tsiku (1 Akorinto 12, Machtidwe 2:42–47, Aheberi 3:12–14) Iye afuna kukhala mutu osati wa mpingo wake osati zochitika za amene asonkhana mdzina lake.

Nanga kotani mphatso zonse ndi zofanana pamalo amodzi? Ngati pali mphatso ya ubusa kukhala mozungulila ndipo wina mphatso ya uphunzitsi akhala pano ndipo ya chifundo kukhala apo. Mphatso ya kuthandiza ikhala pano ndi wina wa mphatso ya kunenela akhala apa. Zonsezi zili ndi zofanana chifukwa zili za Yesu mwini!

Monga tinanena kale, Paulo mu 1 Akorinto 14 limanena pamene “mpingowose” uli pamodzi. Ananena machitidwe a bale oyera mtima onse ali ndi ndi Yesu akhale mkati mwawo. (chapitala 12) amene amakhala pamodzi pansi pa ulamuliro ayenela kupitila kukhala ansembe pamene mpingo ukhala malo amodzi. Onse ali ndi mwayi obvomela kwa Yesu ku utsogoleri, monga ansembe woona, paliponse pamene mpingo uli pamodzi, palibe kuphangila kapena kusankhilatu wankhulu wachipembedzo mwamuna kapena mkazi kulalikila zimene zakonzedwa kale kulalikila kapena nyimbo. Ndipo machitidwe a “pamene bvumbulutso lafika kwa okhalapo, ayenela winayo kukhala pansi “ndilimene limasunga chithunzi chipangano chatsopano cha Yesu” muutsogoleri mu msonkhano mu “ufumu wa Ansembe” ndipo mphatso limatsandulidwa pa thupi la Yesu, Mpingo wake, ungagwire ntchito nthawi yonse yopelekedwa. Pamene bvumbulutso labwela kwa okhalapo, oyambayo ayenela kukhala pansi atelo Ambuye. Palibe malo opwinja wina pazochitika zilizonse, zokonzedwelatu kale makupeka nyimbo, kapena zosangalatsa, kapena muzochitika zilizonse.

Mumpingo umene Yesu amaonekela wa moyo, wochita-chita ndi wamoyo osakhala mbili yakale yoyelekeza imene iyamikilidwa ndi kuphunzitsidwa, apali ufulu. Aliyense amene ali ndi Yesu okhala mkati ndi kuchita-chita monga tsiku ndi tsiku pakatipa abale, ali ndi udindo kupeleka mphatso “mukumangilira thupi lonse” zonse Yesu anapeleka mu thupi lake, mu mphatso zonse—ndipo zifunika mu nthawi ili yonse. Ngati mnyamata atsegula pa zobvuta zake kumalo antchito ake, mphatso ya uphunzitsi, kapena kulimbikitsa, kapena ubusa kapenanso kuthandiza zikumanizana pamodzi monga bvumbulutso wofika kwa wina wa chiwili “ichi ndi :chinthunzi” cha nthawi imene mpingo wonse “ukhala pamodzi” mwa mkwatibwi. Ndipo mu “chinthunzichi” Yesu amaloledwa kukhala mutu wa modzi pa mpingo wake, osakhala mu kachisi omangidwa ndi anthu ai, utsogolezedwa ndi anthu chabe.

Munthu aliyense ukhale ndi Yesu wamoyo amakhala omasuka kuchita ndi kugwiritsidwa ndi Yesu pakubvomela pa zomwe zikuchitikazo. Zimenezo zokha ndiwo “thupi la Yesu” “msomkhano” uyenela kukhala.

Kusefukila kwa zimene zachitika kale mu tsiku lonse mu “nyumba ndi nyumba” pamodzi—mu moyo wa Yesu. Payenda kukhala malo a Yesu kulamulira ndi kutsogozedwa kudzela mwa anthu ndi mphatso NTHAWI ZONSE, mu zinyumba ndipo zotchedwa “kukumana” Anthu adzachepetsa popeleka mphatso “mu nthawiya kutumukila”—mu zonse ndi kuziowonela okha. Musalore zofanizila chabe pamene Yesu akhala mu mphatso ndi anthu ake.

Mu mtima wa “ufumu wa Ansembe” mmene Yesu kweni kweni amaonekela monga mutu wa thupi lake—ndilo phunziro lathu ndipo kukambilana kwathu sikwazibwana ndi zosapezeka mu Baibulo ai. “zamakanda chabe” ndipo aliyense amene “angatenge mbali” ndi kuchotsa umbuli ndi malingaliro kapena kuti aliyense ayenela kulankhula kanthu” ndipo ngati udalankhula mphindi mopitilila zasanu ‘sabata yapita” ndiye sikuti udzalankhulanso zotelo lero. Potelo mpingo siwaufulu otelo ai, mpingo wake ndi wa ulamuliro wa Mulungu pamene KUDZOZA ndi MPHATSO ndi MAGANIZO A LERO amalamula mu ulumikizo mu kudabwitsa ndi wosasintha njila zosakonzelathu. Munthawi (yosankonzeka) munthu mmodzi angabvomeleze Mulungu mokweza mau kwa nthawi yaitali. Koma sikhala “chomwechi” kwa nthawi zonse.

Pali ufulu ndi kumveka ku njila yake 1 Akorinto 14 sungani ndi kuzindikila kuti Paulo ananenanso mu chaputala kuti palinso kuononga kwa anthu amene samvela utsogoleri wa Yesu, kaepna kupeza mwayi kuchokela mu “ufulu” mukuzikonda, kuchitapo, ndi kusowa nzeru. Penanso, kumbukilani kuti mu malembo wonse amu 1 Akorinto 14 kuphatikiza 10 mpaka 13 pamene moyo wa Mulungu ndi oti Anthu akhala “monga mkate umodzi” kuzindikila thupi ndi kukhala pamodzi olumikizana monga dzanja ndi zala ndi mu mfundo mu malembo amenewa amu moyo wa Baibulo mu mpingo 1Akorinto 14 ziyenelanso kutsatilidwa. Pamene Bvumbulutso lili ndi ukhalapo, ndipo oimililayo akhale pansi, osati “chiwonetselo chabe ai” kapena “munthu oyela” ayendetse zochitika zonse. “Ali yemweyo dzulo, lero ndi nthawi zonse.” Kuopa, umbombo, mphamvu ndi kuzikonda kwa anthu ochepa sikungathe kuba anthu a Mulungu cholowa chawo Yesu ali ndi Moyo ndi ALANKHULA kuthyola mu “mphatso zake” monga iye afunila monga ife tili thupi lake osakhala mukuchita mu machita-chita pa tsiku lopatulika.

Inde, pangakhale “oyanganila” amene angatumikile mukuthandiza muzochitika. Ndipo, inde, pangakhale nthawi yolalika, kwa anthu osakhulupilira pabwalo monga Paulo adachitila m’malo ena monga linenela bukhu la Machitidwe, koma mosiyana ndi lero ingakhale adatumikila “polalika” padali kukambilana (Mau a chigriki amene adachitika ku Toasi) osati monga zichitikila makono ai, ndipo kulalika kotero kwa anthu osakhulupilira mu Aefeso kapena ku Anthens chisakhale chinthu chosemphana ndi monga m’mene “mpingo wonse udali pamodzi” monga m’mene osakhulupilira angakhalenso pamene Banja la Mulungu likhalila. 1 Akorinto 14: Nthawi imene mpingo wa Yesu uli pamodzi wina ndi mnzake pamalo amodzi ndi zosiyana ndi pamene wina ‘“alalikila mu mseu” kwa anthu ochuluka sukulu kucholinga cholalikila kwa anthu osatembenuka za Yesu, Machitidwe 19:8–10 kulankhula mau a Mulungu kwa ‘onse osakhulupila aku Asia. Izi ndi zosiyana pamene mpingo wonse pamodzi, woomboledwa ndi kukhala pamene akomana pamodzi monga mu 1 Akorinto 12-14 kapena Machitidwe 20. Pamene Paulo analankhula (monga mmau achigriki) ndi banja lake mpaka kutuluka kwa dzuwa mu usiku onse.

Yesu amafuna kumanga mpingo umene makomo a ndende sangathe kupambana. Mmenemo ndimo m’mene anthu onse adzaziwa kuti muli akuphunzira anga. Amafuna ife tonse kukhala malo okhalamo iye—tsiku olumikizana, kulumizika ndi kukumana pamodzi ndi “kukhalira monga mmodzi wa chikhulupiriro” ndi chikondi chenicheni cha “Amayi, mbale, mlongo” mukupambana kwa moyo umene Yesu ali ndiye anthu ake onse (kuchokela kukumphuka kwa moyo wa tsiku ndi tsiku mukulumikizika kwenikweni. Machitidwe 2:42–47, 1 Akorinto 12:13) umagwiritsidwa ndi mzimu wa Kristo mu nthawi yopezeka yonse ndizotelotu monga m’mene adali ndi ife mu nthupi pansi pano. Yesu adati, pamene ife sitimiza mzimu wake ndi zomangidwa ndi anthu, maganizo ndi miambo ndi zowonetsela, ndi kukhala moyo wa ife tokha. Iye ali ndi ufulu wozionetsela yekha mu mphatso monga m’mene adali pansi pano mthupi. M’maganizo ake tsopano ndi kudzoza, kaya ndi chokhumba chathu. Pamene bvumbulutso libwela kwa wachiwiri, wina woyamba akhale pansi.

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon