UTSOGOLERI WA YESU

SAMUEL NDI SAULI

“kukhala mtsogoleri” kuchokera paubale ndi Mulungu ndi anthu a Mulungu siwuchokera pa mpando kapena dzina ayi.

7/5/2006

M’maiko ambiri padziko lapansi pano, tapanga kulakwitsa kwakukulu kukhudzana ndi utsogoleri pampingo. M’malo ambiri munthu amene amaphunzira Baibulo ku seminare kapena kusukulu ya Baibulo, kapena munthu odziwa zamalonda kapena kuyankhula, amapatsidwa utsogoleri kapena “ubusa” Taona ku India ndi maiko ena, nthawi zambiri, kuti munthu ali ndi njinga amenenso angawerenge amasankhidwa kukhala mtsogoleri. Iyi sinjira ya Mulungu! Utsogoleri wa Mulungu sayendera amene angawerenge, kapena amene adziwa kwambiri kapena amene ali ndi chuma kapena maphunziro, mankhwala kapena kuoneka bwino ndiponso njinga.

Ndilongosolepo pamitundu iwiri yautsogoleri yosiyana wina ndi mtsogoleri kuchokera mumtima, kuchokera paubale ndi Mulungu. Wina ndi mtsogoleri wa mpando umene ukhala ndi dzina ndipo ukhonza kutchedwa “wapampando,” bwana. Yesu adanena kuti utsogoleri wampando siuyenera. Atsogoleri a Mpingo ndi amene akuyenda chifupi ndi Mulungu LERO. Ngati m’bale kapena mlongo sayenda chifupi ndi Mulungu lero, iye sangayesedwenso mtsogoleri. Ngati munthu sabata yatha mwina sadali chifupi ndi Mulungu koma walapa machimo ake m’moyo wake ndipo tsopano akhonza kumva mau a Mulungu, ali mwa mtsogoleri sabata ino kuposa sabata yatha. “kukhala mtsogoleri” kuchokera paubale ndi Mulungu ndi anthu a Mulungu siwuchokera pa mpando kapena dzina ayi.

Tiri ndi atsogoleri ambiri mumzinda umene ndimakhala, koma tilibe “amipando” Mtsogoleri wasabata ino akhonza osakhala mtsogoleri sabata yinayo. Yesu adanena kuti ulamuliro onse wa pansi ndi kumwamba ndi wa iye. Ichi ndi choona. Tsopano, ngati tingamumvere Yesu, amene ali ndi ulamuliro momwemonso ndi m’mene munthu ali ndi ulamuliro pokhapokha ngati akhonza kumumvera Yesu, Ichi ndiye zonse. “ulamuliro onse wa padziko ndi kumwamba” uli ndi Yesu, iye adanena. Munthu amene samdziwa kapena kumumvera Yesu ali ngati “mukuyerekezera” chabe. Munthu otere akhonza kufuna kuti azimumvera monga m’mene thupi livomerezera, ngati ali ndi “mpando” koma iye ali “mtsogoleri” pokhapokha ngati adziwa, akonda, ndipo amvera Mutu, Yesu.

Pali chitsanzo m’Baibulo cha mautsogoleri awiri amenewa. Samueli ndi Sauli onse adali atsogoleri

a anthu a Mulungu, Israeli. Samueli adali munthu wa Mulungu amene adali ndi chikoka mu fuko chifukwa amadziwa Mulungu. Samueli adali ndi zothekera zambiri zaufumu ku Israeli—koma Samueli sadali mfumu! Komabe, Sauli adatchedwa mfumu. Israeli imafuna kukhala ndi mfumu—amafuna kukhala ndi munthu modzi kukhala bwana. Amafuna wina kuti alowe mmalo mwa Samueli ndipo amafuna “mfumu” monga mafuko onse owazungulira. Munjira ina utsogoleriwu ukhonza kuwoneka mofanafana, koma Samueli alibe “mpando” wa ulamuliro. Samueli amagwira ntchito kuchokera paubale wake ndi Mulungu, ndipo Sauli amagwira ntchito kuchokera pampando wake. Samueli adalibe ofesi, mlembi kapena malipiro (salare). Iye sadali muudindo wa mpando ngati mfumu. Samueli adali chabe munthu wa Mulungu amene amalemekezedwa ngati mfumu koma adalibe mpando kapena ofesi. Iye sadali mfumu iye sadali “mbusa”. Iye amangokonda Mulungu ndi mtima wake onse.

Ndipo chifukwa choti amamvera Mulungu, adali ndi chikoka. Adalibe mpando adali ndi chikoka. Ngati munthu moonadi adziwa Mulungu, adzathandiza anthu a Mulungu. Ngati wayitanidwa ndi Mulungu, adzakhala akuthandizila anthu. Ndibwerezanso: Munthu wa Mulungu oona alibe mpando… ali ndi chikoka. Yobu 29, ikulongosola za munthu olemekezedwa ndi Mulungu ndi anthu, ndi woopedwa ndi odedwa ndi satana. Munthu otere safuna ofesi kapena dzina kapena malipiro. Ngati muli ngati Yesu, simudzafuna “mphamvu.”

Monga mwachitsanzo, ngati ndili m’misili, ndi mapanga zinthu ndi matabwa. Ndimapanga mpando, tebulo kapena chitseko kuchokera ku matabwa. Ngati ndili omanga, ndiye kuti ndimanga zinthu ndi njerwa. Chinachake chomwe ndipanga kuchokera ku njerwa ndi umboni oti ndine omanga. China chake dzomwe ndipanga kuchokera kuthabwa ndi umboni oti ndine m’misili. Tsopano, mu Baibulo mau awa “mbusa” (kutathauza kolakwika) koma atanthauzira kuti mphatso ya ubusa wa nkhosa, ogwira ntchito tsiku ndi tsiku pakati pa anthu a Mulungu moyendezana (mwapambali) pa mphatso zina—osati bwana kapena “olankhula wamkulu” pamsonkhano. Kodi umboni uli pati kuti ndine Mbusa weniweni? Umboni ndi wakuti ine ndimakonda anthu a Mulungu! Ndimawathandiza iwo usana ndi utsiku. Sindifuna dzina, sindifuna kukhala bwana. Ndimangokonda anthu ndi mphatso yomwe ndili nayoyi, ndikuwathandiza. Umboni waumusili ndi mpando omwe ndapanga umboni woti ndine Mbusa weniweni ndi woti ndimadyetsa anthu a Mulungu tsiku ndi tsiku, ndipo ali chifupi ndi Yesu chifukwa cha ine. Ngati ndiwona kuti m’modzi mwa anthu a Mulungu ali ndi njala, chimandiswa mtima. Ngati ndiwona kuti m’modzi mwa anthu a Mulungu ali muvuto kapena muzoopsa, mtima waubusa mkati mwanga uthamangira iwo kukawateteza. Uwu ndiye umboni oti ndine odzodzedwa wa Mulungu kukhala m’busa. Sindifuna mayina opatsidwa. Sindifuna chitupa chopachika pakhomo ndi chochokera ku Sukulu ya Baibulo. Ndifunitsa mtima okonda ndi kuchita ntchito ya Mulungu, ndipo kenako ndizabala zipatso zauzimu mumbali iliyonse yomwe iye azandipatsa ine.

Tsono, ndinu m’misili? Ndiye pangani mpando. Muli ndi mphatso ya ubusa. Ndiye kondani anthu—adyetseni, atetezeni ndipo athandizeni. Ichi ndi choona pa mphatso iliyonse! Umboni wa mphatso iliyonse uli mudzipatso zimene umabereka.

Zotsutsana za zonsezi ndi zoonanso ndithu. Ndifundo yodabwitsa kuti amafano mu sayansi ndi mankhwala ndi malonda amalamula kuti amene ali ndi maganizo ndi mtsutso ndi odzitcha okha “akatswiri” ali ndi china choti awonetse, zipatso mumiyoyo yawo, awonekera kuti ali dni ufulu wolamulira, kuphunzitsa kapena kutsutsa ena. Mudziko lachipembedzo, modabwitsa, ali ndi ungiro ochepa kuposa ngakhale zimene amafano amaonetsera. Muchipembedzo, ngakhale, anthu ali akhungu ndi wozunguzidwa kwambiri.

Mtsutso, ukatswiri, zigamulo, ndi ngakhale ubale ndi zonyoza zimayenda mophweka kuchokera kwa iwo azipatso zoyipa miyoyo yawo, m’mabanja ndi m’mabwalo awo. Zodabwitsa, koma zoona ngati inu muona chipembedzo chamunthu mosamalitsa ndi moona. Munthu amene amapanga zinthu zotere ngati bodza kapena m’nyozo kapena kukhala ngati katswiri pa njiniaring’I, zamakhwala kapena malonda akhonza kusonkhanitsa pamodzi gulu lomvera mpphweka anthu akuopa, m’mene akhonza kunderedwa pansi, kapena kuyamikiridwa mpusitsa ku—kuzipereka ku makina osabereka zipatso ndi “akatswiri” zonga zamisala koma ndi zoona. Zimachitika kunthawi zonse, chifukwa umu ndi m’mene maufumu a vuto amasungira nambala yao. Mantha ndi kuyimikira kopusitsa, mjedo, m’nyozo kapena kuyenderedwa pansi. Nchifukwa chake ziri zosadabwitsa kuti Yesu sanapange bwino mu chipembedzo chovomerezedwa kudziko lapansi cha munthawi yake. Koma, likhonza kuphunzira kwa iye ndi kusunga malembo, ndi kuyang’ana zipatso, osati kumvera—kunena kwa mfundo ndi mabanjeti, ndiponso kunena kufuna kwa yenkha kwa munthu kuti ateteze.

(Pamenepo mwatengapo mfundo. :)

jesuslifetogether.com
chiCheŵa Languages icon
 Share icon