UTSOGOLERI WA YESU
PA ANTHU AKE ONSE
Pasakhale mabwana amene amayendetsa ndi kuwongolera maganizo, ndalama, ndiponso anthu—kupatula Yesu kuzera mu Anthu ake pamodzi mwa Mzimu Wake. Onse ake, otembenuka moona ndi okhala moyo opatulitsidwa wa tsiku ndi tsiku pa wina ndi mnzake (Aheberi 3:12-14)—Onse ndi ansembe!
7/5/2006
Chikhristu chonama kwazaka zambiri chakakhira anthu pansi. Chatenga anthu ochepa ndi kuwakweza pamwamba kuwapanga ena mwa “atsogoleri” olemera ndi otchuka ndi amphamvu kwinaku chipondereza ena pansi. Mumaiko a United States, India, Poland, Brazil, Romania ndi onse padziko pano, muli “ziphona” za akhristu ndi akhristu apansi. Izi ndi zolakwika kwambiri. Yesu adati kw aophunzira ake mu Mateyu 23, “Musatche munthu phunzitsi, tate, mtsogoleri, mbuye, ‘rabbi’, m’busa pakuti muli abale ndi tate wanu m’modzi! Palibe ‘ziphona’ mu chikhristu choona kupatula Yesu yekha. Pasakhale mabwana amene amayendetsa ndi kuwongolera maganizo, ndalama, ndiponso anthu—kupatula Yesu kuzera mu Anthu ake pamodzi mwa Mzimu Wake.
Baibulo linena mu Aefeso 4 kuti pamene Yesu adapita kumwamba ndi kutumiza Mzimu Wake, Adatenga mbali za iye yekha ndikuzimwaza pa thupi la Khristu, mpingo. Yesu adatenga mphatso zonse zomwe ali nazo (ndipo Yesu adali ndi mphatso zambiri, sichoncho?), ndipo anazipereka kwa anthu ake monga thunthu. Sanatenga mphatso zomwe ali nazo ndikuziyika pa ‘abusa’ kapena pa m’modzi “munthu wa Mulungu”. Malembo anena adatenga mphatso zake zonse ndikuzipereka kwa thupi lonse Baibulo linena kuti Mzimu unayikidwa ndi kuperekedwa ngati mphatso, monga m’mene mzimu ufunira, pampingo wonse. Ngati uli nkhristu oona, ngati mwatayadi moyo wako chifukwa cha Yesu. Pamene Mzimu Woyera ukupatsa iwe mphatso yapadera.
Ndipo, mphatsoyako ndi mbali ya Yesu. Pali mitundu yambiri ya mphatso zomwe zidalembedwa m’Baibulo. Mzimu Woyera, mwachitsanzo, umapereka chifundo ngati mphatso. Mphatso ya chifundo ndi mbali ya Yesu imene iye anapeleka kwa ena. Icho ndi mphatso ta uzimu. Tonse ife tiyenera kukhala ndi chifundo, sichoncho? Koma pali chifundo chopambana chimene chili mphatso ya Mzimu Woyera. Ndipo pakuti ulamuliro onse ndi wa Yesu ndi mphatso zonse zimene zili mwa ife ndi mbali yake ya Yesu, ndiye lizipereke ku mphatso zonse zili mwa wina aliyense mwa ife chifukwa ndi Yesu adaikanso.
Munjira iyi, utsogoleri uli mwa anthu onse a Mulungu. Baibulo lititcha ife ufumu wa ansembe. Baibulo silititcha ife kuti ufumu okhala ndi ansembe, koma ufumu wa ansembe. Palibe gulu lapadera ngati a Levi aku chipangano chakale. Mu pangano la tsopano, tonse anthu a Mulungu tikuyenera kukhala ansembe kwa wina ndi mnzake. Funiro la Mulungu siloti munthu m’modzi oyera wapadera ndi amene angalalikire ayi. Baibulo linena kuti Yesu anakwera kumwamba ndi po anapereka mphatso kwa anthu ake onse. Iye adapanga ufumu wa ansembe. Iye adayika gawo lake mwa wina aliyense wa anthu ake amene ali otembenuka moona, ana ndi akulu omwe. Ichi nchifukwa chake timafuna mphatso zawina ndi m’nzake. Ife timafuna mphatso zonse za Yesu! Pali mazana a mphatso chifukwa ZONSE za Yesu zinathiridwa pa Banja Lake. Ichi ndichifukwa Yesu adati tonse tili abale pakati pa abale. Ife sitifuna munthi m’modzi ndi mphatso imodzi kuyimilira kutsogolo kwathu. Ife tisavomereze ichi ayi. Onse ake, otembenuka moona ndi okhala moyo opatulitsidwa wa tsiku ndi tsiku pa wina ndi mnzake (Aheberi 3:12–14)—Onse ndi ansembe!
Palibe ulamuliro wina wake umene uli mwa “munthu wa Mulungu” m’modzi ndi ena onse kungokhala ndi kuwonerera. Chifukwa chanjira imene anthu amangira mpingo m’zaka zoposa 1800 zapitazo, ife tachila monga ngati pali mphatso imodzi yokha basi—mphatso ya “ubusa”. (“kapena mwina wina aliyense ali ololedwa kukhala ndi “mphatso yapadera ndalama”). Koma ubusa ndi mphatso imodzi yokha! Ngati ife timanga molakwika, ife tonse tiluza ngati munthu m’modzi akankhidwira patsogolo kukhala “mbusa” ndipo ena onse azingokhala ndikumamvesela nthawi zonse, ndiye kuti palibe adzagawana nawo gawo la mphatso yawo. Iwo amangotorapo mphatso ya “abusa” ichi ndi chinthu chaching’ono komanso chachinyengo. Ngati ife tifuna kuwona ukulu wa Mulungu, ndipo ngati tifuna kuti tione miyoyo yathu ikusintha ndiponso miyoyo ya ana athu ikusintha, tikufunika ZONSE za Yesu. Mphatso zomwe onse a alongo ndi abale ali nazo ndi gawo la Yesu. Ngakhale ana lai ndi mphatso zomwe ndi gawo la yesu. Ife tonse tikufuna zonse za mphatso pa miyoyo yathu. Ife tonse ndife abale. Mtima wa Mulungu ndi oti mphatso zomwe uli nazo upatse ine ndipo zomwe ndili nazo ine ndipatse iwe. Ife tisakhalire pambali chabe ya mphatso za Yesu. Amen?
Kodi mwawona chomwe tikufunikira kulimbika mtima? Zinthu ziyenera kusintha! Simungapitilire kuchita zomwe mukuchita. Muyenera kusankha kugwiritsa ntchito mphatso yanu kwambiri ndiponso kulandira ena kuti nawonso ateronso. Mupanga chisankho kukhala omvera ndi olimbika mtima. Ngati inu mupitiliza kukhala pampando wanu kapena pansi nthawi zonse ndipo osagwiritsa ntchito mphatso yanu kwambiri ngati m’mene muliri, mphatso yanu idzapitilira kulowa pansi. “Iye amene wakhal akupasidwa chikhulupiriro kapena mphatso ayenera kuonetsa kukhulupirika.” Kodi mukukumbuka za munthu yemwe adakwirira talente yake? Yesu adati, “Iwe oyipa, watchito wa ulesi.” Icho ndi chomwe yesu anena kwa ife pamene siltipanga chomwe kuyenera kupanga. Ngati ine sindigwiritsa ntchito mphatso yanga kapena ngati simugwiritsa ntchito mphatso yanu, ife tili “oyipa ndi a ulesi”.
Bwanji ngati inuyo mutakhala othamanga wa Olympic, mwagona pa vedi ndipo wina watenga zigwe ndikukumangani? Ngakhale inu mutakhala opambana, ngati munamangidwa pa bedi minofu yanu ikakulungala ndipo mukadafa. Mphamvu zanu zonse zikadatha chifukwa mwamangidwa pa bedipo kwa miyezi ndi zaka. Kodi inu mukuwona miyambo ya anthu abale ndi kulanda Mau a Mulungu? Njira yomwe tinamangira m’zaka zoposa 1500 zapitazo mu nyumba ya Mulungu zamangirira anthu a Mulungu ambiri pa bedi!
Iwo akhala asakutha kuzuka kapena kuthamanga ndi kukwaniritsa chowinda chawo chifukwa anthu amanga molakwika, mosatsatira Mau a Mulungu. Ngati ife timanga mpingo munjira yomwe ikweza munthu ndi tizima mphatso za ena, ndife ophwanya malamulo (zigawenga) ku khoti la kumwamba chifukwa cha kuwonongeka komwe kuchitike chifukwa cha “chotupitsa chochepa muzonse” ndi mphatso zosagwiritsidwa ntchito.
Sichifukwa choti anthu ndi “oyipa” kuti tamanga molakwika. Kwambiri ndichifukwa choti sitimadziwa kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu mwa mapangidwe ake kwa zaka 1800, dziko la a khristu asokoneza zokhudzana ndikuti khristu ndu uti,…mtsogoleri ndi ndani… Kodi moyo watsiku ndi tsiku uyenera ukhale bwanji… Ndipo kodi misonkhano iyenera kuoneka bwanji. Atate athu afuna kubwezeretsa zinthu izi kwa ife pamoyo wathu tsopano. Monga m’mene Mau a Mulungu adanyalanyazilidwa munthawi ya masiku a mfumu Yoseya, ndipo chilungamo chinapezeka.
Chokwiriridwa mu zofuna za ufumu wa anthu ndi miyambo yao, tsopano chilungamo cha Mulungu, chomwe chanyalanyazidwa kwanthawi yayitali (koma nthawi zonse chilli mu Baibulo), chikhonza kumasura anthu. Mulungu asintha moyo wanu modabwitsa ndiponso kusintha ena okuzungulirani mosatila mwake.Izi ndi choonadi chopambana ndi champhamvu. Kaya ndi ochepa kapena ambiri mumzinda kapena m’mudzi.
Mulungu sali oletsedwa kupulumutsa kudzera ku ochepa kapena ambiri monga Yonatani mnzake wa Davide adanena. “iye yemwe wakhulupilidwa akuyenera kuonetsa kukhulupirika” Ife tiyenera kukhala olimbika mtima kupanga china chokhudza choonadi chomwe tinanyozera kapena osamvera kumbuyoku.