KUMANGA KUTI IKHALE YA MPHAMVU
KULIMBIKA MTIMA KUTI TISINTHE
Mulungu ali ndi mamangidwe a Nyumba yake akuti timangire kuti ntchimo likhonza kuwomboledwa ndi kuphwanyika. Njira ya Mulungu “yomangira mpingo” imaloreza ubale kuti uchiritsidwe ndiponso tchimo ndi zifooka zichotsedwe. Uwu ndiwo mtima wa Mulungu kwa anthu ake kuzungulira pa dziko lonse. Ife tifuna tikuwuzeni inu m’mene anthu abwino angafikire pamphamvu zakuthekera tsopano.
7/5/2006
Pakatha zaka khumi zokhala a Khristu, anthu ambiri amuzipembedzo zowongoleredwa ndi Akulu a mpingo zamaziko ongokhala nawo pakupembedza sakhala wolimba kuposa mmene adaliri mzaka zawo zoyamba. Ichi sichabwino ayi. Ngati mwana wathu wachaka chimodzi akula kufika zaka khumi koma ali opanda mphanvu kapena nzeru koposa mmene adaliri ali ndi chaka chimodzi, ichi chingakhale chokhumudwitsa. Ngati uli ndi mwana wa zaka khumi mubanja mwanu amene adali wofooka ngati mwana wachaka chimodzi—monga tate kapena mai, ichi chikhonza kuswa mtima wanu, kodi sichingatero?
Kodi muganizapo bwanji za Atate wathu a kumwamba m’mene amamvera pamene anthu ake onse ayenera kukhala amphamvu ndi nzeru ndi “ozadzidwa ndi Mzimu Oyera ndi ozadzidwa ndi nzeru,” “ndinso oyenera kukhala aphunzitsi panthawi ngati ino” “osati makanda ayi,” ogwira ntchito ya Mulungu koma ambiri mw aife sitili amphamvu koposa makanda a chaka chimodzi? Izi ndi zoona padziko lapansi, ndipo zimaswa mtima wa Mulungu. Ife sitingayimbe nyimbo zambiri kapena “kulalika” maulaliki ambiri kuti tisinthe ichi, chifukwa ife sitimanga munjira ya Mulungu mu Nyumba yake ya Mulungu.
Mulungu ali ndi mamangidwe a Nyumba yake akuti timangire kuti ntchimo likhonza kuwomboledwa ndi kuphwanyika. Njira ya Mulungu “yomangira mpingo” imaloreza ubale kuti uchiritsidwe ndiponso tchimo ndi zifooka zichotsedwe. Uwu ndiwo mtima wa Mulungu kwa anthu ake kuzungulira pa dziko lonse. Ife tifuna tikuwuzeni inu m’mene anthu abwino angafikire pamphamvu zakuthekera tsopano.
Ife tikhonza kulola mphatso za m’thupi la Khristu kumangidwa pamodzi kukhala mokhala mwa Mulungu mozazidwa ndi ulemerero wa Mulungu. Pali njira imene Mulungu afuna ife kuti timangire kuti tithe kuwona mphamvu ya machimo ikuphwanyidwa mumoyo weniweni ndiponso ife kusiya kukhala akapolo kuzofooka zathu zonse. Chikonzero cha Mulungu ndi kumanga maubale, osati kukhala ndi mavuto ntahwi zonse. Mulungu ali ndi njira yodabwitsa yomangira nyumba yake ndi anthu odabwitsa.
Mpaka pano, chipembezo mudzikoli chamanga Nyumba ya Mulungu molakwikwa, ndi anthu ngati mabwana ndiponso anthu oyera ndi “kukhala nawo” m’misonkhano ngati matathauziro awo “a’mpingo.” Ife sitinadziwe m’mene tingamangire, koma tsopano tiyenera kuphunzira m’mene tingamangire. Mulungu adati tikhale “osamalitsa kwambiri m’mamangidwe.” Pali choonadi chapadera chomwe kwanthawi zonse chakhala chili m’Baibulo chomwe chidzasintha moyo wanu ndiponso kusintha njira yomwe Mpingo umaonetseredwa, kuti timkweze m’mwambamwamba Fumu yathu Yesu ndi kuona kuti loto lake lakwaniritsidwa.
Mulungu akufuna kumanga Nyumba yake kuti ife tonse tikhale amphamvu pamodzi. Iye akufuna kumanga Nyumba yake kuti zipata zandende zisadzaipyole. Iye akufuna kumanga Nyumba yake kuti maubale achilitsidwe. Iye akufuna kumanga nyumba yake kuti iye amasuke kuchiza matupi athu, malingaliro ndi miyoyo yathu. Iye akufuna kumanga Nyumba yake kuti ikhale ya mphamvu ndinso nzeru, ndikuti uthenga wabwino wa Yesu upite patali, mwamphamvu kuposa kale.
Kodi inu muli nako kulimbika kuti mumve zinthu izi? Kodi mumvera mau a Mulungu pamene mukumva zinthu izi? Kodi inu musintha miyoyo yanu posawerengera mtengo wake? Ngati muli nako kulimba mtima kuti mumverandipo muzipereka chonde werenganibe.