KUMANGA NDI MAPANGIDWE NDI MAMANGIDWE A
MOYO WA TSIKU NDI TSIKU PAMODZI
Kuti ikhale nyumba yabwino kuli Yesu akhalamo, nyumba ya Mulungu iyenera kumangidwa pamodzi kugwiritsa kamangidwe ndi kapangidwe ka iye. Nyumba yake ndiyopangidwa ndi anthu, miyala ya moyo wake, ndipo Ali ndi njira yomwe tingamangire miyoyo yathu pamodzi. Malembo amutcha Yesu omanga Wamkulu. Ife tiyenera kusamalitsitsa za makonzedwe a Iye.
7/5/2006
Tsopano poti tatanthauzira / fotokozera chimene chilli zomangira zabwino kumangira nyumba ya Mulungu… Nganizilani ichi: Tingoyesera tatenga miyala yonse yabwino, matabwa onse abwino, ndi zonse zabwino, zoyenera kumangira zimene Yesu wasankha za nyumba yake ndikuziunjika zonse zomangira zabwinozo pamodzi. Chingachitike nchiyani, ganizani? Nyumbayo pakadalibe, sindinamange. Nyumba ya Mulungu imafuna kupyola pa katundu womangira wabwino (Akhristu owona). Chifukwa choti uli ndi zonse zofunikira pomanga nyumba zounjikidwa pamodzi sizitanthauza kuti uli ndi nyumba yogonamo ayi. Mulu wa zinthu zomangirawo sungakupulumutse ku namodwe, ngakhale zitakhala zabwino chotani.
Kuti ikhale nyumba yabwino kuli Yesu akhalamo, nyumba ya Mulungu iyenera kumangidwa pamodzi kugwiritsa kamangidwe ndi kapangidwe ka iye. Nyumba yake ndiyopangidwa ndi anthu, miyala ya moyo wake, ndipo Ali ndi njira yomwe tingamangire miyoyo yathu pamodzi. Malembo amutcha Yesu omanga Wamkulu. Ife tiyenera kusamalitsitsa za makonzedwe a Iye.
Mulungu ali ndi anthu ambiri odabwitsa padziko lonse lapansi. Chimene chachitika muzaka 2,000 zapitazi ndi zakuti anthu amenewa amafunitsitsa kuti asinthe miyoyo yawo ndi kuti akondwetse iye, koma iwo anakhumudwitsidwa. Iwo akhala okanika kupeza kuthekera kwathuthu kwawo ndi kuti amutumikire iye bwino umakhala mtima wawo wonse, koma amalephera kawiri kawiri. Chifukwa chomwe amalepherera ndi choti tamanga molakwika. Ife sitidamange monga mwa kamangidwe, kapangidwe kamene Mulungu watipatsa. Pamene wina ayesera chinthu china, koma achiyesa munjira yolakwikiratu, iye sazapezapo phindu, ngakhale atalimbika motani. Nyumba ya Yesu imangidwa ndi kamangidwe kake, osati yathu. Ndipo kamangidwe kake ndi nyumba ina. “Zana la abambo, la amai, la abale ndi la alongo.” Kamangidwe kake ndikakuti “tivomereze machimo athu kwa wina ndi mnzake” ndipo tichiritsidwe. Kamangidwe kake ndi kakuti “tinyamulirane wina ndi mnzake zophinja zathu ndi kuti chinco tikwaniritse lamulo la khristu.” Kamangidwe kake ndi kakuti “tikhale amodzi monga iye ndi Atate ali amodzi.” Khumbilo la Mulungu kudzakhala nawo pa msonkhano kapena pamwambo, koma khumbiro lake ndi banja lomangidwa pamodzi tsiku lirilonse, lakulukana pamodzi muzigawo zonse zamoyo watsiku ndi tsiku ngati banja.
Yesu wasankha pa Nyumba yake mamangidwe omwe awoneka mofanana dziko lirilonse, osayang’anira ziyankhulo kapena miyambo. Mamangidwe awa ndi amene anthu a Mulungu amapereka miyoyo yawo kukonda ndi kutumikirana wina ndi mnzake tsiku lirilonse, monga banja, pamodzi. Mpingo woona wa yesu, omangidwa munjira yake kuti ukhale olimba, uyenera kukhala banja tsiku lirilonse. Amadyera pamodzi kuchokera kupita khomo lina, amatumikirana ndi kuthandizana wina ndi mnzake munjira zambiri tsiku ndi tsiku.
Amayankhulana za mau a Mulungu wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku kuti awathandize kukhala monga Yesu. Akawona tchimo, apita kukayenda ndi kukayankhula zokhudza tchimolo pamodzi. Sadikira “la Mulungu” kuti akamve wina akulalikira zatchimolo ayi.
Cholinga cha Mulungu (Aefeso 3:10, 1 Petro 2) ndi chakuti ife tonse tiri ansembe a tsiku ndi tsiku ndi akazembe a Mulungu kwa wina ndi mnzake ndi dzake “pamene taima tikhala pansi, ndiponso pamene tiyenda panjira.”
Tonsefe tayitanidwa kukhala ansembe a Yesu. Tonse tayitanidwa kuti tikhale ndi mawu a Mulungu ndi kuthandizana wina ndi mnzake. Ichi chitantahuza kuti ngati tiona mzanthu akudzikonda kapena kukwiya, ngati timuona akumwa, kunyada, kuzikweza komwe kumaswa mtima wa Yesu, pamenepo aliyense wa ife atengepo mbali pakuthandizana wina ndi mnzake kuti tisinthe. Izi ndizatsiku ndi tsiku. Zilibe ndi chochita ndi tsiku la Mulungu.
Mpingo woonadi wa Yesu ndiwopangidwa miyala ya moyo, ndipo mamangidwe ake a Nyumbayi ndi banja la tsiku ndi tsiku.
Sichinthu chomwe “timapita kukhala nawo”, koma ndi chinthu chomwe tiri tsiku ndi tsiku.
Kodi mukuona mmene zonse izi zalumikizana? Pokha pali ubale wa Tsiku ndi Tsiku ndi pamene ungaziwe ngati wina amakonda kuwala ndi choonadi, ndipo pamenepo ali mwana wa Mulungu. Misonkhano yochepa yam’sabata siyingathandize wina kudziwa ngati wina ali okonda kuwala ndipo koma ali ofowoka chabe, kapena ngati sakonda kuwala ndipo potero ali osapulumutsidwa. Chikonzero cha Mulungu ndi chuma mu zotengera za chikonzero cha Mulungu ndi unsembe wa okhulupirira. Chikonzero cha Mulungu pa anthu ake ndi “kulimbikitsana wina ndi mnzake tsiku ndi tsiku.” Pamene tikhaladi mzimenezi pamodzi, ubwino umodzi ngwakuti onse a ana a Mulungu amakhwimira khwimira. China mwachotsatira chakuyenda pamodzi ngati momwe Mulungu afunira ndi chakuti ngati wina sakonda kuwala, kenako amaonekera ngati ozilimbambayitsa.
Ngati ali osaweruzika, ngati sasamala za chimene Yesu anena chaokhudza zinthu izi, ngati akwiya ndi kudzitukumula, ndiye kuti aonekera ngati a Khristu oyerekezera. Chimabwera poyera kuti iwo sanapereke moona moyo wawo kwa Yesu chifukwa chilungamo chake ndi chakuti wina sangakhale ndi mzimu oyera ndikupanda kukonda kuwala (Yoh 3, 1 Yohan 1, 3).
Ngati timanga munjira iyi—kusintha kuzikonda kwithu, kapena miyoyo ya ulesi, kuphunzira moonadi mmene lingakonderane wina ndi mnzake ngati banja tsiku ndi tsiku, kutengepo mbali potumikira ndi kuthandizana wina ndi mnzake ndi mau a Mulungu tsiku lirilonse pamenepo lidzakhala nyumba imene Yesu akhoza kukhalamo ndi kuyikonda. Idzakhala nyumba yamamangidwe abwino imene idzakhala yophweka kwa Yesu ndi ife tonse kukhalamo ndi kuyipanga khomo lathu.
Yesu ananena kuti tikachita monga mwamau ake, namondwe akabwera (ndipo adzabwera), pamenepo nyumbayo idzaima. Idzaima chifukwa yamangidwa pa mwala wa “kuyika mau aku muzichitochito,” osati mukuganiza kapena mukuyimba zokhudzana ndi mau ake. Ngati ife tiyimba chabe izi, kupephera zokhudza izi ndi kuyankhula za izi osasintha njira za mmene tikhalira mukumvera mau wina ndi mnzake, pamenepo namondwe akabwera, ngakhale nyumba itakongola nzotani, idzasalazidwa ndi kuwonongedwa. Ichi ndi chimene Yesu adalonjeza mu Mateyu 7. Tsono, tsimikizani mukumanga njira yake ndipo PANGANI kanthu pazachoonadi chake. Mverani choonadicho ndipo pamenepo namondwe sadzakupwetekani inu ayi.
Munjira yomweyo mbalame yochepa kapena kalulu wang’ono abisala kunsi kwa thanthwe pamene namondwe abwera, inunso makhoza kubisala kunsi, kunthunzi wa mapiko a Yesu ngati mumanga munjira yomwe iye akuyitanirani inu kuti mumangire. Namondwe agwedeza mitengo ndi kusuntha zinthu zolemera. Zinthu ziombana ndipo mphezi ziomba. Koma ngati inu mumanga monga mwa njira ya Yesi ndi kutembenuzira nkhope zanu kwa iye namondwe akabwera, mudzakhala inu otetezedwa mu munthunzi wa mapiko ake.
Namondwe wamphamvu adzadutsa ndipo dzuwa lidzawala. Mbalame zidzayambanso kuyimba ndipo moyo udzakhalanso watsopano. Idzakhala nyumba yolimba kwambiri ya mamangidwe abwino. Pamene namondwe abwera naomba pa nyumbayi, iyo idzaima chifukwa ili ndi katundu omangira wabwino yekha, ndinso chifukwa ili ndi mamangidwe abwino. Padzakhala kuonongeka kochepa pa nyumbayi ndipo tonse tidzakhala otetezedwa. Monga mmene Atate adanenetsa chindunji za katundu ndi mamangidwe amene Nowa amayenera kugwiritsa ntchito pomanga chombo. Chonchonso Yesu ali ndi kakonzedwe pa katundu ndi mamangidwe a Nyumba yake.
Ndipo kakonzedwe kake, sikapangano latsopano munthu oyera kuyankhula kwa gulku la anthu omwe siwolumikizana “oyima pamfundo yokhala nawo mumisonkhano yotere.” Pano TSOPANO ndi mazana a amai, abambo, abale, alongo”—akulukidwa mwakuya m’chikondi “kuchokera ku ung’ono kufikira ku ukulu” waubale wa okonda kuwala.
Uwu ndiye uthenga wabwino wa Ufumu wa Yesu. Iye adati, “Atate anga ali ndi kulimbika pa nyumba yomwe ikumangidwa.” Atate akukhumbira koposa kuti timange nyumba yake mnjira yake. Mumayiko ndi mzinda yambiri, nyumba yomangidwa munjira imene Yesu afuna ndiyochepetsetsa. Pafupi—fupi mu mpingo uliwonse ndi dziko lirilonse muli anthu amene amabwera pamodzi mwa mwambo ndi khalidwe ndipo kenako kupita njira zosiyana, kukhala moyo wawo mmene chiwakondweretsera iwo eni. Mwina amachimwa mwaufulu ndi dala kapena satero konse. Komabe sinyumba ayi chifukwa sakhala ngati banja, tsiku ndi tsiku, pamodzi.
Ndi pamene miyala yonse ikakamirana pamodzi pokha, momatidwa ndi chikondi cha zichitochito ndi ndi kumangidwa ndi mamangidwe a Mulungu, pamene amasanduka malo amene iye akhonza kuwatcha nyumba. Ngakhale uli mwala wamoyo wabwino ndikuyesa kukhala moyo wachiyero, ndi iwebe mwala umodzi. Ngati utenga mwala umenewo nauyika panthaka, sudzakhalabe nyumba ya Yesu. Iye safuna miyala yapayokha yokhala munda chabe ayi. Ife tiyenera tidzipange tokha, ngakhalenso kuzikakamiza tokha, kukakamirana pamodzi ndi miyala ina. Tsiku lirilonse tiyenera kudzilamula tokha kukakamirana pamodzi ndi miyala ina, mumamangidwe a Mulungu a Nyumba——————————-—pamene “tiyimirira, tikhala pansi, pamene tiyenda mumseu” pamodzi. Kuchaya Malaya pamodzi, ndi kupita kumsika pamodzi. Pamene tigwira ntchito mminda, tiumba njerwa, tidula nkhuni, tikonza chakudyatiyeni tichite ichi pamodzi kuti ife tikhale banja limodzi mmalo mwa anthu ambiri kapena mabanja ambiri. Ndi muzochitika “zazing’ona” izi zamoyo wa tsiku ndi tsiku pamene tingalimbitse ndi kulumikidza chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi chathu pamodzi. Zochita izi zatsiku ndi tsiku, zokhalidwa pamodzi ngati Banja, ziri “mazenera a moyo” amene amalora ife kusambitsana wina ndi mnzake mmadzi a Mau, koposa.
Cha “kukhala nawo” mu miyambo yachipembezo ndi mmayimbidwe ndi mmauthenga a munthu oyera. Yesu sakumanga chilichose koma mpingo.
Yesu adanena kuti ngati mumveradi funiro langa, mudzakhala ndi mazana a atate, amai, abale ndi alongo—osati anzathu ayi, koma zana la abale a m’banja okondana kwambiri. Ichi ndicho chifunira cha Mulungu. Izi ndizo ziphunzitso za Yesu Khristu—kuti amanga nyumba yake ndi katundu omangira wabwino. Katundu oyipa Sali olandilidwa ngati safuna kusintha pakumva mau a Yesu.